Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


116 Mau a m'Baibulo Okhudza Kuipa

116 Mau a m'Baibulo Okhudza Kuipa

Mawu a Mulungu m’Masalimo 5:4 amati, “Pakuti Inu simuli Mulungu wokondwera ndi zoipa; woipa sadzakhala nanu pamodzi.” Ndipo ndikukulimbikitsani kuti muzindikire kufunika koŵerenga ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu, chifukwa ndiwo chitsogozo chathu cha tsiku ndi tsiku. Ngati tikufuna moyo wabwino, tiyenera kutsatira malamulo ndi mawu amene Ambuye anatipatsa m’Baibulo.

Choncho, tisiye zoipa zonse zimene sizikondweretsa Mulungu. Tiwongolere mapazi athu ndikutsatira mawu ake kuti atitsogolere ku choonadi chake. Popeza iye amadana ndi zoipa, tiyesetse ndi mtima wonse kuti tichotse njira yachinyengo mwa ife. Tibwerere kwa Mulungu ndikulapa machimo athu.

Chifundo chake chikufuna kutipulumutsa, kutiyeretse, ndikutibwezeretsa kuti tikakhale ndi moyo wabwino, wonga fungo lokoma pamaso pake.




Masalimo 5:4

Inu sindinu Mulungu wokondwerera machimo. Simufuna zoipa pamaso panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:14

Usayende m'njira za anthu oipa, usatsate m'mapazi mwa anthu ochimwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:16-19

Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa: maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa, mtima wokonzekera kuchita zoipa, mapazi othamangira msangamsanga ku zoipa, mboni yonama yolankhula mabodza, ndi munthu woutsa chidani pakati pa abale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 7:9

Thetsani ntchito zoipa za anthu ochimwa, koma anthu ochita zabwino muŵabwezere zokoma. Inu ndinu amene mumayesa maganizo ndi mitima yomwe, Inu ndinu Mulungu wolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:14-15

Usayende m'njira za anthu oipa, usatsate m'mapazi mwa anthu ochimwa. Njira zao uzipewe, usapitemo konse. Uzilambalale, ndi kungozipitirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 2:1

Tsoka kwa anthu amene amakonzekera chiwembu, amene usiku wonse amalingalira ntchito zoipa. Akadzuka m'maŵa amakazichitadi, pakuti mphamvu zake ali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 5:20

Tsoka kwa amene zoipa amaziyesa zabwino ndipo zabwino amaziyesa zoipa, amene mdima amauyesa kuŵala, ndipo kuŵala amakuyesa mdima, amene zoŵaŵa amaziyesa zozuna, ndipo zozuna amaziyesa zoŵaŵa!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:21

Musagonjere zoipazo, koma gonjetsani zoipa pakuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 64:2

Tchinjirizeni ku upo wachiwembu wa anthu oipa, tetezeni ku chiwawa cha anthu ochita zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:17

Paja kuchita zoipa ndiye chakudya chao, kuchita ndeu ndiye chakumwa chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 5:4-5

Inu sindinu Mulungu wokondwerera machimo. Simufuna zoipa pamaso panu. Anthu onyada sangathe kuwonekera pamaso panu. Inu mumadana ndi anthu onse ochita zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 5:8

Mngeloyo adati, “Ameneyu akutanthauza kuipa konse.” Atatero adakankhira mkaziyo m'gondolo muja, nabwezera chovundikira chamtovu chija pamwamba pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:19-20

Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za kuphana, za chigololo, za chiwerewere, za kuba, maumboni onama, ndiponso zachipongwe. “Chifukwa chiyani ophunzira anu sasunga mwambo wa makolo? Sasamba m'manja moyenera akamadya chakudya.” Zimenezi ndizo zimaipitsa munthu. Koma kudya chakudya osasamba m'manja, sikungaipitse munthu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 10:15

Thetsani mphamvu za munthu woipa ndi wochimwa. Fufuzani kuipa kwake, ndipo mumlange kuti asadzabwerezenso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:29-32

Mitima yao idadzaza ndi zosalungama zamitundumitundu, monga kuipa, umbombo ndi dumbo. Amangolingalira za kaduka, za kupha anthu, za ndeu, za kunyenga, ndi za njiru. Amachita ugogodi, Umasimba za Mwana wake, Yesu Ambuye athu. Poyang'anira umunthu wake, kholo lake ndi Davide, amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao. Ndi opusa, osakhulupirika, okhakhala moyo, ndi opanda chifundo. Amalidziŵa lamulo la Mulungu lakuti anthu ochita zotere ndi oyenera kufa, komabe iwo omwe amachita zomwezo, ndiponso amavomerezana ndi anthu ena ozichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:21

Choipa chitsata mwini, anthu odana ndi munthu wa Mulungu adzalangidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:29-30

Chauta ndi linga loteteza munthu woyenda molungama, koma amaononga wochita zoipa. Chauta salola kuti munthu womukondweretsa iye, azikhala ndi njala, koma zimene woipa amazilakalaka, Mulungu amam'mana. Munthu wabwino sadzachotsedwa pamalo pake, koma woipa sadzakhazikika pa dziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 35:8

Kuipa kwanu kumangovuta anthu anzanu, chimodzimodzinso ntchito zanu zabwino zimangopindulira anzanu basi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:23

Adzaŵalanga chifukwa cha machimo ao, adzaŵaononga chifukwa cha kuipa kwao, zoonadi, Chauta, Mulungu wathu, ndiye amene adzaŵafafanize.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:5

Muchotse aphungu oipa pamaso pa mfumu, ndipo ufumu wake udzakhazikika pa chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 48:22

“Koma anthu ochimwa alibe mtendere,” akuterotu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:1-2

Usamavutika ndi anthu oipa. Usamakhumbira kukhala ngati ochita zoipa, Kanthaŵi pang'ono ndipo munthu woipa sadzakhalaponso, ngakhale muyang'ane bwino pamalo pamene analiri, simudzampezapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala pa mtendere wosaneneka. Munthu woipa amachitira upo mnzake wabwino, namamtuzulira maso mwachidani. Koma Chauta amamseka munthu woipayo, poti amaona kuti tsiku lake la kuwonongeka likubwera. Anthu oipa amasolola lupanga, ndipo amakoka mauta, kuti aphe anthu ovutika ndi osoŵa, amene amayenda molungama. Koma lupanga lao lidzalasa mitima ya eniake omwewo, ndipo mauta ao adzaŵathyokera m'manja. Nkwabwino kukhala m'chilungamo ndi kusauka, kupambana kukhala nazo zokoma zambiri zimene munthu woipa ali nazo. Pakuti Chauta adzathetsa mphamvu za anthu oipa, koma adzalimbikitsa anthu onse abwino. Chauta amasamalira moyo wa anthu angwiro, ndipo choloŵa chao chidzakhalapo mpaka muyaya. Pa nthaŵi ya mavuto sadzazunzika, pa nthaŵi yanjala, adzakhala nazo zakudya zochuluka. pakuti mosachedwa amanyala ngati udzu, ndipo amafota ngati masamba aaŵisi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 15:21

Ndidzakulanditsa kwa anthu oipa, ndipo ndidzakuwombola kwa anthu ankhanza,” akuterotu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 3:19

Koma munthu woipa ukamchenjeza kuti asiye njira zake zoipa, iye nkumapitirizabe makhalidwe ake oipawo, adzafa ali ochimwa, Koma iweyo udzapulumutsa moyo wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 59:2-4

Machimo anu adakulekanitsani ndi Mulungu wanu, ndipo Iye wakufulatirani chifukwa cha machimo anuwo. Choncho saamva zimene inu mumanena. Chauta akuuza anthu ake kuti, “Ndidzabwera ku Yerusalemu kudzapulumutsa a fuko la Yakobe amene adaleka machimo ao. “Ndipo ndidzapangana nawo chipangano chakuti, ‘Kuyambira tsopano mpaka muyaya, mzimu wanga umene uli pa iwe, ndiponso mau anga amene ndidaika m'kamwa mwako, sizidzachokeranso m'kamwa mwako kapena m'kamwa mwa ana ako kapena mwa adzukulu ako mpakampaka.’ ” Manja anu ali psuu ndi magazi a anthu amene mudapha. Mudadziipitsa ndi machimo anu ambiri. Pakamwa panu palankhula zabodza, pamanena zoipa. Palibe amene amaimba mnzake mlandu molungama, palibe wopita ku bwalo lamilandu moona. Amadalira zopanda pake, amangonena mabodza. Amangolingalira zamphulupulu, nachitadi zoipa zimene akuganiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:11

Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muŵatsutse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 6:5

Pamene Chauta adaona kuti anthu a pa dziko lapansi aipa koopsa, ndiponso kuti mitima yao inali yodzaza ndi maganizo oipa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-21

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:16

Iwo ajatu sangagone, mpaka atachita ndithu choipa. Tulo sangatiwone, mpaka atakhumudwitsapo munthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:18

mtima wokonzekera kuchita zoipa, mapazi othamangira msangamsanga ku zoipa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:1-5

Udziŵe kuti pa masiku otsiriza kudzafika nthaŵi ya zovuta. Tsono iwe wakhala ukunditsatira m'zophunzitsa zanga, mayendedwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, kupirira kwanga, mazunzo anga, ndi masautso anga, monga amene adaandigwera ku Antiokeya, ku Ikonio ndi ku Listara. Ndidaazunzikadi koopsa! Koma Ambuye adandipulumutsa pa zonsezi. Onse ofuna kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi, m'menemo anthu ochimwa ndi onyenga, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanyenga ena nkumanyengedwanso iwo omwe. Koma iwe, limbika pa zimene waphunzira ndipo wadziŵa kuti nzoona, paja ukuŵadziŵa amene adakuphunzitsa. Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu. Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse. Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu. Adzakhala opanda chifundo, osapepeseka, ndi osinjirira anzao. Adzakhala osadzigwira, aukali, odana ndi zabwino, opereka anzao kwa adani ao. Adzakhala osaopa chilichonse, odzitukumula, okonda zosangalatsa m'malo mokonda Mulungu. Adzasamala maonekedwe ake okha a chipembedzo, nkumakana mphamvu zake. Anthu otere uziŵalewa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:12

Paja Ambuye amaŵayang'anira bwino anthu olungama amatchera khutu ku mapemphero ao. Koma ochita zoipa saŵayang'ana bwino.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 17:9

Mtima wa munthu ndi chinthu chonyenga kwambiri kupambana zinthu zonse. Kuipa kwake nkosachizika. Kodi ndani angathe kuumvetsa?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:16-17

Ndani amalimba mtima kuti andimenyere nkhondo ndi anthu oipa? Ndani amaimira mbali yanga, kuti alimbane ndi anthu ochita zoipa? Chauta akadapanda kundithandiza, bwenzi posachedwa nditapita ku dziko lazii.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:12

Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:21

Zoonadi, anthu oipa chilango sichidzamuphonya, koma anthu a Mulungu adzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:8

Munthu amene amachimwa, ndi wa Satana, pakuti Satana ndi wochimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu adaoneka ndi cholinga chakuti aononge zochita za Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:17

Tsono anthu oipa adzapita ku dziko la anthu akufa, ndiye kuti anthu onse amene amakana Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:10

Mtima wa munthu woipa umalakalaka zoipa. Samva chifundo konse ndi mnzake wovutika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 11:5

Chauta amayesa anthu olungama namakondwera nawo, mtima wake umadana ndi anthu oipa okonda zachiwawa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:17-18

Chonchonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo woipa umabala zipatso zoipa. Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapena mtengo woipa kubala zipatso zabwino ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:29

Chauta amakhala kutali ndi anthu oipa mtima, koma amamva pemphero la anthu achilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 13:11

Chauta akuti, “Ndidzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha kuipa kwao, ndidzalanga oipa chifukwa cha kuchimwa kwao. Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:19-20

Usamavutika chifukwa cha anthu ochita zoipa, usachite nawo nsanje anthu oipa. chifukwa mitima yao imalingalira zandeu, ndipo pakamwa pao pamalankhula zoutsa mavuto. Pajatu munthu woipa zinthu sizidzamuyendera bwino m'tsogolo, moyo wa anthu oipa adzauzima ngati nyale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 1:5-6

Nchifukwa chake anthu ochimwa, Mulungu adzaŵazenga mlandu, adzaŵachotsa iwo pakati pa anthu ake. Paja Chauta amaŵasamalira anthu ake, koma anthu ochimwa adzaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:21

Munthu wabwino vuto silimgwera, koma woipa mavuto samchoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:7

Oipa asiye makhalidwe ao oipa, ndipo osalungama asinthe maganizo ao oipa. Abwerere kwa Chauta, kuti Iyeyo aŵachitire chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, kuti Iye aŵakhululukire machimo ao mofeŵa mtima.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:31

Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:6

Madalitso amakhala pa munthu wokondweretsa Mulungu, koma pakamwa pa munthu woipa pamabisa zandeu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:41-42

Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake kudzachotsa mu Ufumu wake anthu onse ochimwitsa anzao, ndi ena onse ochita zoipa, nadzaŵaponya m'ng'anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:12-15

Munthu wachabechabe, munthu woipa, amangoyendayenda nkumalankhula zabodza. Amatsinzinira masoŵa nkumakwekwesa pansi mapazi ake, amalozaloza ndi chala chake. Amalingalira zoipa ndi mtima wake wopotoka, amangokhalira kuvundula madzi pakati pa anthu. Nchifukwa chake tsoka lidzamgwera modzidzimutsa. Pa kamphindi kochepa adzaonongedwa, osapulumuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 14:1-3

Mumtima mwake munthu wopusa amati, “Kulibe Mulungu.” Anthu otereŵa ndi oipa, amachita zonyansa, palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino. Chauta kumwambako waŵerama, akuyang'ana anthu pansi pano, kuti aone ngati angakhalepo mmodzi wanzeru wofunitsitsa Mulungu. Koma ai, anthu onse ndi osokera, onsewo ndi oipa chimodzimodzi. Palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino, ai, palibiretu ndi mmodzi yemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:16

Koma Chauta amaŵakwiyira anthu ochita zoipa, anthuwo sadzakumbukikanso pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 32:6

Munthu wopusa amalankhula zauchitsilu, ndipo amaganiza kuchita zoipa. Amachita zoipira Mulungu, amalankhula zonyoza Mulungu. Anjala saŵapatsa chakudya, aludzu saŵapatsa chakumwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:29

Munthu wandeu amakopa mnzake, ndipo amamuyendetsa m'njira yoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 16:17-18

Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa, pakuti anthu otere satumikira Khristu Ambuye athu, koma amangotumikira zilakolako zao basi. Ndi mau okoma ndi oshashalika amanyenga anthu a mitima yoona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:6

Chifukwa cha kudzipereka ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake. Chifukwa choopa Chauta munthu amalewa zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 8:20-22

“Ndithu Mulungu sangamkane munthu wopanda cholakwa, komanso anthu olakwa Mulungu sangaŵathandize konse. Iye adzadzaza chiphwete m'kamwa mwako, ndipo udzafuula mokondwa. Amene amadana nawe adzachita manyazi, malo okhalako anthu oipa sadzaonekanso.” Yobe

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 140:1-2

Pulumutseni, Inu Chauta, kwa anthu oipa. Tchinjirizeni kwa anthu ankhanza. Makala amoto aŵagwere, aponyedwe m'maenje ozama, asatulukemonso. Musalole kuti woononga mbiri ya mnzake akhazikike m'dziko. Choipa chimlondole munthu wankhanza mpaka kumuwononga. Ndimadziŵa kuti Inu Chauta mumateteza ozunzika, mumaweruza mwachilungamo anthu osoŵa. Zoonadi, anthu ochita zabwino adzatamanda dzina lanu. Anthu amenewo adzakhala pamaso panu. Iwo amalingalira mumtima mwao kuti achite zoipa, amautsa nkhondo nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:20

Mumtima mwa anthu opangana zoipa mumakhala kunama, koma anthu olinga zabwino amakhala ndi chimwemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 59:7-8

Amathamangira kukachita zoipa, sachedwa kupha anthu osalakwa. Maganizo ao onse ali pa zoipa. Kulikonse kumene amapita amasiyako bwinja, ndiponso amaononga. Kumene kuli iwowo, anthu sapeza mtendere. Zonse zimene amachita nzopanda chilungamo. Amayenda m'njira zokhotakhota, ndipo aliyense woyenda m'njira zimenezo sadzapeza mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:1-2

Usamachitira nsanje anthu ochimwa, kapena kumalakalaka kuti uzimvana nawo, Ukataya mtima pamene upeza zovuta, ndiye kuti mphamvu zako ndi zochepa. Uŵapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe. Uŵalanditse amene akuyenda movutikira popita kukaŵapha. Ukanena kuti, “Ife sitidazidziŵe zimenezi,” kodi iye amene amayesa mtima, zimenezi saziwona? Kodi amene amayang'anira moyo wako sazidziŵa? Kodi sadzambwezera munthu potsata ntchito zake? Mwana wanga, uzidya uchi poti ndi wabwino, madzi a m'chisa cha njuchi ndi ozuna ukaŵalaŵa. Udziŵe kuti nzeru ndi yoteronso mumtima mwako. Ukaipeza, zinthu zidzakuyendera bwino m'tsogolo, ndipo chikhulupiriro chako sichidzakhala chachabe. Nyumba ya munthu wabwino usaichite zachifwamba ngati munthu woipa mtima, usachite nayo nkhondo nyumba yake. Munthu wabwino amagwa kasanunkaŵiri, koma amadzukirira ndithu, m'menemo anthu oipa tsoka limaŵagwera chonse. Usamakondwerera kugwa kwa mdani wako, mtima wako usamasangalala iyeyo akaphunthwa. Ukatero Chauta adzaziwona zimenezo nadzaipidwa nazo, kenaka adzaleka kumkwiyira mdani wakoyo. Usamavutika chifukwa cha anthu ochita zoipa, usachite nawo nsanje anthu oipa. chifukwa mitima yao imalingalira zandeu, ndipo pakamwa pao pamalankhula zoutsa mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 36:1-4

Uchimo umalankhula mu mtima wa munthu wosamvera Mulungu. Alibe mantha ndi Mulungu m'maganizo mwake. Musaleke kuŵakonda ndi chikondi chanu chosasinthika anthu okudziŵani, pitirizani kuŵachitira zokoma anthu olungama mtima. Musalole kuti mapazi a anthu odzikuza andipondereze, ndipo kuti manja a anthu oipa andipirikitse. Onani, ochita zoipa ali ngundangunda. Inu mwaŵagwetsa pansi ndipo sangathe kudzuka. Amadzinyenga m'maganizo mwake, kotero kuti tchimo lake sangathe kulizindikira ndi kudana nalo. Mau a pakamwa pake ndi oipa ndi onyenga. Sachita zanzeru kapena zabwino. Amaganiza zachiwembu akamagona usiku. Amayenda pa njira imene siili yabwino, sapewa zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:24-26

Munthu wachidani pakamwa pake pamalankhula zabwino, pamene mumtima mwake muli zonyenga. Woteroyo akamalankhula mokometsa mau, usamkhulupirire, pakuti mumtima mwake mwadzaza zoipa. Ngakhale amabisa chidani mochenjera, kuipa kwakeko kudzaoneka poyera pakati pa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 101:3-4

Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chachabechabe. Ndimadana ndi zochita za anthu okusiyani, sizindikomera konse. Ndidzakhala kutali ndi anthu a mtima woipa, sindidzalola choipa chilichonse kuloŵa mwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:16-17

Sambani, dziyeretseni, chotsani pamaso panga ntchito zanu zoipa. Inde, lekani kuchita zoipa. Phunzirani kuchita zabwino. Funafunani chilungamo, opsinjidwa muŵathandize. Tetezani ana amasiye, muŵaimirire pa milandu yao akazi amasiye.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:12

Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:5

Kulungama kwa anthu angwiro kumaŵathandiza pa moyo wao, koma kuipa mtima kumagwetsa mwiniwake yemweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:8

Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:23-24

Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga. Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:15

Chilungamo chikachitika, nzika zabwino zimakondwera, koma zimadederetsa atambwali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 3:11

Koma tsoka kwa anthu oipa! Zinthu zidzaŵaipira. Zimene akhala akuchitira anzao zomwezo zidzaŵabwerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 7:24

Koma anthuwo sadamvere, sadasamaleko, ndipo adapitirira kukhala osamvera ndi mitima yao yoipa. Adayang'ana zam'mbuyo osati zakutsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 125:5

Koma anthu amene amatsata njira zao zokhotakhota, Chauta adzaŵapirikitsira kumene kuli anthu ochita zoipa. Mtendere ukhale ndi Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:15

Ngati mumvera Chauta, adzakuyang'anirani ndipo adzayankha kupempha kwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 2:1-2

Tsoka kwa anthu amene amakonzekera chiwembu, amene usiku wonse amalingalira ntchito zoipa. Akadzuka m'maŵa amakazichitadi, pakuti mphamvu zake ali nazo. Nyamukani, chokani, ano simalo opumulirapo. Zonyansa zanu zaŵaipitsa, zadzetsapo chiwonongeko choopsa. Munthu wina atamapita uku ndi uku akulalika zabodza kuti, ‘Ndithudi mudzakhala ndi vinyo ndi zakumwa zamphamvu zambiri,’ mlaliki wotere ndi amene anthu aŵa angamkonde. “Koma inu banja lonse la Yakobe, ndidzakusonkhanitsani. Onse otsala a ku Israele ndidzaŵasonkhanitsa pamodzi ngati nkhosa m'khola, ngati gulu la zoŵeta pa busa lake. Malowo adzakhala thithithi ndi chinamtindi cha anthu.” Woŵapulumutsa adzaŵatsogolera, ndipo onse adzathyola pa chipata nathaŵa. Idzayambira ndi mfumu yao kudutsa, Chauta adzakhala patsogolo pao. Akasirira minda, amailanda. Akakhumbira nyumba, amazilanda. Amavutitsa munthu ndi banja lake, naŵatengera zonse zimene ali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:13-15

Pamene munthu akuyesedwa ndi zinyengo, asanene kuti, “Mulungu akundiika m'chinyengo.” Paja Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zinyengo, ndipo Iyeiyeyo saika munthu aliyense m'chinyengo. Koma munthu aliyense amayesedwa ndi zinyengo pamene chilakolako cha mwiniwakeyo chimkopa ndi kumkola. Pamenepo chilakolakocho chimachita ngati chatenga pathupi nkubala uchimo. Tsono uchimowo utakula msinkhu, umabala imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:12-15

Nzeruyo idzakupulumutsa ku mayendedwe oipa, idzakuteteza kwa amtherakuŵiri, amene amasiya njira zolungama, namayenda m'njira zamdima. Iwoŵa amakondwa pochita zoipa, amasangalala ndi ntchito zosalungama. Anthu ameneŵa njira zao nzokhotakhota, makhalidwe ao ngonyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:44

Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muzikonda adani anu ndipo muziŵapempherera amene amakuzunzani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:26

Maganizo a anthu oipa amamnyansa Chauta, koma mau a anthu olungama amamkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:7-8

Anthu oika mtima pa khalidwe lokonda zoipa, amadana ndi Mulungu. Anthu otere sagonjera Malamulo a Mulungu, ndipo kunena zoona, sangathedi kuŵagonjera. Ndipo anthu oika mtima pa khalidwe limenelo, sangathe kukondweretsa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 6:27-28

“Iwe Yeremiya, ndakusankha kuti ukhale choyesera zitsulo. Uŵayese anthu anga kuti uwone m'mene aliri makhalidwe ao. Onsewo ali ndi upandu wokanika, onsewo ndi akazitape, ndi olimba ngati mkuŵa ndi chitsulo. Onse amangochita zoipa zokhazokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 33:15-16

Angathe kutero ndi amene amachita zolungama ndi kulankhula zoona, amene amakana phindu lolipeza monyenga, amene amakutumula manja ake kuti angagwire chiphuphu, amene amatseka makutu kuti angamve mau opangana za kupha anzao, amene amatsinzina kuti angaone zoipa. Munthu wotere adzakhala pa malo otetezedwa. Kothaŵirako iye kudzakhala ku malinga am'matanthwe. Chakudya azidzalandira, ndipo madzi sadzamsoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:12-13

Nchifukwa chake musalole uchimo kuti ulamulire matupi anu otha kufaŵa, ndipo musagonjere zilakolako zake. Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 140:4-5

Inu Chauta, tetezeni kwa anthu oipa, tchinjirizeni kwa anthu andeu, amene amaganiza zofuna kundigwetsa. Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika, atchera ukonde wa zingwe, anditchera misampha m'mbali mwa njira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:19

Njira ya anthu oipa ili ngati mdima wandiweyani. Satha kuzindikira kuti aphunthwa pa chiyani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 3:3

Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:10-12

Paja Malembo akuti, “Palibe munthu wolungama, ai ndithu ndi mmodzi yemwe. Palibe munthu womvetsa, palibe munthu wofunadi kutumikira Mulungu. Onse asokera, onse pamodzi achimwa, palibe wochita zabwino, ai ndithu ndi mmodzi yemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:6

Chilungamo chimatchinjiriza munthu wabwino, koma tchimo limagwetsa munthu woipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:13

Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa, koma mutipulumutse kwa Woipa uja.” [Pakuti ufumu, mphamvu ndi ulemerero ndi zanu kwamuyaya. Amen.]

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:27

Onse amene ali kutali ndi Inu adzaonongeka, Inu mumaŵaononga amene ali osakhulupirika kwa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:4-5

Chauta adapanga chinthu chilichonse kuti chikhale ndi cholinga chake, ngakhale anthu oipa, kuti aone tsiku la mavuto. Munthu aliyense wodzikuza amanyansa Chauta, ndithu ameneyo sadzalephera kulangidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:21-23

“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna. Pa tsiku lachiweruzo anthu ambiri azidzanena kuti, ‘Ambuye, Ambuye, kodi suja ife tinkalalika mau a Mulungu m'dzina lanu? Suja tinkatulutsa mizimu yonyansa potchula dzina lanu? Suja tinkachita ntchito zamphamvu zambiri m'dzina lanu?’ Apo Ine ndidzaŵauza poyera kuti, ‘Sindidaakudziŵani konse. Chokani apa, anthu ochita zoipa.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:27

Anthu osoŵa chilungamo amanyansa anthu ochita chilungamo, monga momwe anthu abwino amanyansira anthu oipa mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:3

Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa wosaka, ndiponso ku mliri woopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:19

Tikudziŵa kuti ndife ake a Mulungu, ndipo kuti onse odalira zapansipano ali m'manja mwa Woipa uja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 97:10

Chauta amakonda anthu odana ndi zoipa. Iye amasunga moyo wa anthu ake oyera mtima. Amaŵapulumutsa kwa anthu oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:9

Chikondi chizikhala chopanda chiphamaso. Muzidana ndi zoipa, nkumaika mtima pa kuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:19-20

Mlandu wake ndi uwu wakuti ngakhale kuŵala kudadza pansi pano, anthu adakonda mdima, osati kuŵalako, chifukwa zochita zao zinali zoipa. adadza kwa Yesu usiku. Adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu, pakuti palibe munthu wotha kuchita zizindikiro zozizwitsa zimene Inu mukuzichita, ngati Mulungu sali naye.” Aliyense wochita zoipa, amadana ndi kuŵala. Saonekera poyera, kuwopa kuti zochita zakezo zingaonekere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:8-9

Amene amakonzekera kuchita choipa, adzatchedwa mvundulamadzi. Kukonzekera zopusa nkuchimwa, munthu wonyoza amanyansa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:17-18

Inu Chauta, musalole kuti ndichite manyazi, chifukwa ndapemphera kwa Inu. Koma anthu oipa ndiwo achite manyazi, apite ku manda kachetechete. Onse onyada ndi onama olankhula mwamwano ndi monyoza kwa anthu abwino, muŵakhalitse chete.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:4

pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokutsogolera kuchita zabwino. Koma ngati ukuchita zoipa uwope, pakuti ali ndi mphamvu ndithu zokulanga. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wogwetsa mkwiyo wa Mulungu pa wochita zoipa, pomulanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:7

Ndeu za anthu oipa zidzaŵaononga, poti amakana kuchita zolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:49-50

Zidzateronso pa kutha kwa dziko lino lapansi. Angelo adzabwera nadzachotsa anthu ochimwa pakati pa anthu olungama, Mbeu zina zidagwera pa nthaka yamiyala, pamene panalibe dothi lambiri. Zidamera msanga chifukwa nthakayo inali yosazama. nkumaŵaponya m'ng'anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 5:23-24

Amalungamitsa wolakwa chifukwa cha chiphuphu nkuipitsa mlandu wa munthu wosalakwa. Nchifukwa chake monga momwe moto umaonongera chiputu, monga momwenso udzu wouma umapsera m'malaŵi a moto, momwemonso muzu wao udzaola, ndipo maluŵa ao adzafota ndi kuuluka ngati fumbi, chifukwa adakana malamulo a Chauta Wamphamvuzonse, adanyoza mau a Woyera uja wa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:10-11

Paja mau a Mulungu akuti. “Yemwe afuna kukondwera ndi moyo, ndi kuwona masiku abwino, aletse lilime lake kulankhula zoipa, ndiponso milomo yake kunena mabodza. Alewe zoipa, azichita zabwino. Afunefune mtendere ndi kuyesetsa kuupeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:27

Musampatse mpata Satana woti akugwetseni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:29

Chauta ndi linga loteteza munthu woyenda molungama, koma amaononga wochita zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 101:4

Ndidzakhala kutali ndi anthu a mtima woipa, sindidzalola choipa chilichonse kuloŵa mwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 36:12

Onani, ochita zoipa ali ngundangunda. Inu mwaŵagwetsa pansi ndipo sangathe kudzuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:18-19

Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko, ndipo munthu wa mtima wodzikuza adzagwa. Kuli bwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu osauka, kupambana kumagaŵana chuma ndi anthu onyada.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:10

zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu, ndipangeni mtima woyera, ndipo mukonzenso mzimu wowongoka mkati mwanga. Atate wanga wakumwamba wokondedwa, ndidzichepetsa pamaso panu chifukwa ndikukusowani. Lero ndabwera kudzapempha chikhululukiro pa zoipa zanga zonse. Mundikhululukire chifukwa ndayenda m'njira yoipa ndipo mtima wanga wachita zoyipa pamaso panu. Ndikupemphani kuti mundisambitse ndi magazi anu Yesu, chifukwa ndikufuna kuti musinthe munthu wamkati wanga kukhala m'chifaniziro chanu. Mundidzaze tsiku lililonse ndi kukhalapo kwanu kotero kuti ndikhale m'chiyero chanu. Wongolereni mapazi anga ndipo mundiphunzitse chifuniro chanu chomwe chili chabwino, chokondweretsa, komanso changwiro. Ndithandizeni kuti ndisapatuke ku mawu anu nthawi iliyonse, koma kuti nthawi zonse ndizikhala kuti nditsatire malamulo ndi malangizo anu. Musandilole kutsata zilakolako za thupi langa kapena kuipa kwa mtima wanga. Khalani mwa ine Mzimu Woyera ndipo chikondi chanu chilamulire munthu wanga wonse kuti nthawi zonse ndizikhala ndi inu komanso chifukwa cha inu. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa