Nthawi ya Khirisimasi ndi nthawi yabwino kwambiri yoti ndiganizire za chikondi chachikulu chimene Mulungu anationetsa potumiza Mwana wake Yesu padziko lapansi. Ndi nthawi yabwino yoti ndigawane uthenga umenewu ndi chikondi chimenechi ndi anthu amene ali pafupi nane.
Ndikukumbukira kuti Khirisimasi ndi imodzi mwa maholide ofunikira kwambiri amene timakondwerera monga Akhristu, pamodzi ndi Pasika ndi Pentekosti: Kubadwa kwa Yesu Khristu ku Betelehemu. Nthawi imeneyi nthawi zambiri ndimakhala wokonzeka kumva komanso kudziwa zomwe ndili nazo ndi zomwe ndikumva, ndikuyamikira Mulungu pa zonse zomwe wandipatsa chaka chino.
Pakuti mwana wabadwira ife, mwana wamkazi wapatsidwa ife; ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzatchedwa: Wodabwitsa Wopereka Malangizo, Mulungu Wamphamvu, Atate Wamuyaya, Kalonga wa Mtendere (Yesaya 9:6).
Chaka chino Khirisimasi, lonjezo la Mulungu lindilimbikitse kukhala moyo wosiyana, kuyamika mtengo wa magazi ake pa mtanda, kukana chilichonse cha dziko, ndipo mzimu wa ubwino ndi kuwolowa manja, wodzala ndi chikondi ndipo wodzala ndi chipiriro chimene ndinalandira pa Ubatizo, zikule mu ine.
Ndikukumbukira kuti kuti ndiyime bwino pa moyo wanga, ndiyimirire patsogolo pa Mulungu.
Yesu adabadwira m'mudzi wa Betelehemu, m'dziko la Yudeya, pa nthaŵi imene Herode anali mfumu ya dzikolo. Ndiye kudaabwera akatswiri ena a nyenyezi ku Yerusalemu kuchokera kuvuma. Ataiwona nyenyeziyo, adasangalala kwabasi. Adaloŵa m'nyumba, naona mwanayo ali ndi Maria mai wake, ndipo adagwada nampembedza. Kenaka adamasula chuma chao, nampatsa mitulo ya golide, lubani ndi mafuta onunkhira a mure. Mulungu adaŵachenjeza m'maloto kuti asadzerekonso kwa Herode kuja. Motero adadzera njira ina pobwerera kwao. Atapita akatswiri a nyenyezi aja, mngelo wa Ambuye adaonekera Yosefe m'maloto. Adamuuza kuti, “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mai wake, uthaŵire ku Ejipito. Ukakhale kumeneko mpaka ndidzakuuze, popeza kuti Herode azidzafunafuna mwanayu kuti amuphe.” Apo Yosefe adadzuka usiku womwewo, nkutenga mwanayo ndi mai wake kupita ku Ejipito. Adakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira, kuti zipherezere zimene Ambuye adaalankhulitsa mneneri kuti, “Ndidaitana Mwana wanga kuti atuluke ku Ejipito.” Herode atazindikira kuti akatswiri a nyenyezi aja adampusitsa, adatuma anthu ku Betelehemu ndi ku midzi yonse yozungulira, kuti akaphe ana aamuna onse a zaka ziŵiri kapena kucheperapo. Zaka zimenezi adaaŵerengera potsata m'mene adaamvera kwa akatswiri aja za nthaŵi imene iwowo adaaiwonera nyenyeziyo. Pamenepo zidachitikadi zimene mneneri Yeremiya adaanena kuti, “Mau akumveka ku Rama, kulira ndi kubuma kwambiri: Rakele akulira ana ake. Akukana kumtonthoza, chifukwa ana ake asoŵa.” Herode atamwalira, mngelo wa Ambuye adaonekera Yosefe m'maloto ku Ejipito. Iwowo ankafunsa kuti, “Ali kuti mwana amene adabadwa kuti adzakhale Mfumu ya Ayuda? Ife tidaona nyenyezi yake ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza.”
Mngeloyo adamuuza kuti, “Musaope, Maria, Mulungu wakukomerani mtima. Mudzatenga pathupi, ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Mudzamutcha dzina lake Yesu.
Yosefe nayenso adanyamuka kuchokera ku Nazarete, mudzi wa ku Galileya. Adapita ku Yudeya, ku mudzi wa mfumu Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa anali wa m'banja ndi fuko la Davideyo. Mwanayo ankakula, nasanduka wamphamvu nkukhalanso wa nzeru zabasi. Ndipo Mulungu ankamudalitsa. Makolo a Yesu ankapita ku Yerusalemu chaka ndi chaka ku chikondwerero cha Paska. Pamene Yesu anali ndi zaka khumi ndi ziŵiri, iwo adapita kumeneko monga adaazoloŵera. Masiku a chikondwererocho atatha, adanyamuka kumabwerera kwao, mnyamata uja Yesu nkutsalira ku Yerusalemu, makolo ake osadziŵa. Iwo ankayesa kuti ali pamodzi ndi anzao aulendo, choncho adayenda ulendo wa tsiku limodzi. Tsono adayamba kumufunafuna pakati pa abale ao ndi abwenzi ao. Ataona kuti sakumpeza, adabwerera ku Yerusalemu akumufunafuna ndithu. Patapita masiku atatu, adampeza m'Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera mau ao, ndi kumaŵafunsa mafunso. Onse amene ankamva mau ake, ankadabwa ndi mayankho ake anzeru. Pamene makolo ake adamuwona, adadabwa, ndipo mai wake adamufunsa kuti, “Mwana iwe, watisautsiranji chotere? Ine ndi bambo wako tavutika nkukufunafuna.” Koma Yesu adati, “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kani simumadziŵa kuti ndiyenera kupezeka m'nyumba ya Atate anga?” Adapita kukalembedwa pamodzi ndi Maria, mkazi wake, amene anali ndi pathupi.
Pamene anali kumeneko, nthaŵi yake yoti Maria achire idakwana, ndipo adabala mwana wake wachisamba wamwamuna. Adamkulunga m'nsalu namgoneka m'chodyera cha zoŵeta, chifukwa adaasoŵa malo m'nyumba ya alendo.
Amasanjikiza tchimo pa tchimo linzake, chinyengo pa chinyengo chinzake. Amakana kundidziŵa,” akuterotu Chauta.
Mngeloyo adayankha kuti, “Mzimu Woyera adzakutsikirani, ndipo mphamvu za Mulungu Wopambanazonse zidzakuphimbani. Nchifukwa chake Mwana wodzabadwayo adzakhala Woyera, ndipo adzatchedwa Mwana wa Mulungu.
Adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu, chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo ao.” Zonsezi zidaatero kuti zipherezere zimene Ambuye adaalankhulitsa mneneri kuti, “Namwali wina wosadziŵa mwamuna adzatenga pathupi nkubala mwana wamwamuna. Mwanayo adzatchedwa dzina loti Imanuele,” ndiye kuti “Mulungu ali nafe.”
Adaloŵa m'nyumba, naona mwanayo ali ndi Maria mai wake, ndipo adagwada nampembedza. Kenaka adamasula chuma chao, nampatsa mitulo ya golide, lubani ndi mafuta onunkhira a mure.
ndipo adabala mwana wake wachisamba wamwamuna. Adamkulunga m'nsalu namgoneka m'chodyera cha zoŵeta, chifukwa adaasoŵa malo m'nyumba ya alendo.
Koma mngeloyo adaŵauza kuti, “Musaope, ndadzakuuzani uthenga wabwino, umene udzakondweretsa anthu onse kwambiri. Usiku womwe uno m'mudzi wa Davide wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.
Koma nthaŵi itakwana, Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi, adabadwa woyenera kumvera Malamulo a Mose. Adachita zimenezi kuti akaombole amene anali akapolo a Malamulowo, ndipo kuti potero tisanduke ana a Mulungu.
Zonsezi zidaatero kuti zipherezere zimene Ambuye adaalankhulitsa mneneri kuti, “Namwali wina wosadziŵa mwamuna adzatenga pathupi nkubala mwana wamwamuna. Mwanayo adzatchedwa dzina loti Imanuele,” ndiye kuti “Mulungu ali nafe.”
Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja.
Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m'manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.” Ulamuliro ndi mtendere wake zidzanka zikukulirakulira. Iye adzakhala pa mpando wa mfumu Davide, ndipo adzakhazikitsa ndi kuchirikiza ufumu wake, pochita zachilungamo ndi zangwiro kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse Chauta Wamphamvuzonse watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi.
Yosefe nayenso adanyamuka kuchokera ku Nazarete, mudzi wa ku Galileya. Adapita ku Yudeya, ku mudzi wa mfumu Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa anali wa m'banja ndi fuko la Davideyo. Mwanayo ankakula, nasanduka wamphamvu nkukhalanso wa nzeru zabasi. Ndipo Mulungu ankamudalitsa. Makolo a Yesu ankapita ku Yerusalemu chaka ndi chaka ku chikondwerero cha Paska. Pamene Yesu anali ndi zaka khumi ndi ziŵiri, iwo adapita kumeneko monga adaazoloŵera. Masiku a chikondwererocho atatha, adanyamuka kumabwerera kwao, mnyamata uja Yesu nkutsalira ku Yerusalemu, makolo ake osadziŵa. Iwo ankayesa kuti ali pamodzi ndi anzao aulendo, choncho adayenda ulendo wa tsiku limodzi. Tsono adayamba kumufunafuna pakati pa abale ao ndi abwenzi ao. Ataona kuti sakumpeza, adabwerera ku Yerusalemu akumufunafuna ndithu. Patapita masiku atatu, adampeza m'Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera mau ao, ndi kumaŵafunsa mafunso. Onse amene ankamva mau ake, ankadabwa ndi mayankho ake anzeru. Pamene makolo ake adamuwona, adadabwa, ndipo mai wake adamufunsa kuti, “Mwana iwe, watisautsiranji chotere? Ine ndi bambo wako tavutika nkukufunafuna.” Koma Yesu adati, “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kani simumadziŵa kuti ndiyenera kupezeka m'nyumba ya Atate anga?” Adapita kukalembedwa pamodzi ndi Maria, mkazi wake, amene anali ndi pathupi. Koma iwo sadamvetse zimene adaŵayankhazo. Tsono Yesu adabwerera nawo pamodzi, nafika ku Nazarete, ndipo ankaŵamvera. Mai wake ankasunga zonsezi mumtima mwake. Ndipo Yesu analikunka nakula m'nzeru ndi mu msinkhu, ndipo Mulungu ndi anthu omwe ankakondwera naye kwambiri. Pamene anali kumeneko, nthaŵi yake yoti Maria achire idakwana, ndipo adabala mwana wake wachisamba wamwamuna. Adamkulunga m'nsalu namgoneka m'chodyera cha zoŵeta, chifukwa adaasoŵa malo m'nyumba ya alendo.
Mwadzidzidzi pamodzi ndi mngeloyo padaoneka gulu lalikulu la angelo ena. Ankatamanda Mulungu ndi mau akuti, “Ulemerero kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene Iye amakondwera nawo.”
Chauta akuti, “Koma iwe Betelehemu wa ku Efurata, inde ndiwe wamng'ono pakati pa mafuko a Yuda, komabe mwa iwe ndidzatulutsa munthu amene adzakhala wolamulira Israele. Iyeyo chiyambi chake nchakalekale, cha masiku amakedzana.”
Kubadwa kwa Yesu Khristu kudaatere: amai ake Maria adaafunsidwa mbeta ndi Yosefe; koma asanaloŵane, Maria adaapezeka kuti ali ndi pathupi mwa mphamvu za Mzimu Woyera. Mwamuna wake Yosefe anali munthu wokonda chilungamo, komabe sadafune kumchititsa manyazi poyera. Nchifukwa chake adaganiza za kungothetsa mbeta ija osachitapo mlandu.
Angelowo atachoka kubwerera Kumwamba, abusa aja adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tipite ku Betelehemu, tikaone zachitikazi, zimene Ambuye atidziŵitsa.” Tsono adapita mofulumira, nakapeza Maria ndi Yosefe, atagoneka mwana wakhandayo m'chodyera cha zoŵeta chija.
Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi. Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda. Imbani nyimbo zoyamika Chauta ndi pangwe, lizani pangwe ndi nyimbo zokoma. Imbirani Chauta Mfumu, imbani molimbika ndi malipenga ndi mbetete.
Nthambi idzaphuka patsinde pa Yese, ndipo mphukira idzatuluka ku mizu yake. Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera ku banja la Davide idzakhala chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Onse adzasonkhana kwa iye, ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero. Tsiku limenelo Ambuye adzatambalitsa dzanja lake kachiŵiri kuti aombole anthu ake otsalira ku Asiriya, ku Ejipito, ku Patirosi, ku Etiopiya, ku Elamu, ku Sinara, ku Hamati ndi pa zilumba za m'nyanja yamchere. Adzakwezera mitundu ya anthu mbendera, adzasonkhanitsa otayika a ku Israele ndi obalalika a ku Yuda kuchokera ku mbali zonse zinai za dziko lapansi. Nsanje ya Efuremu idzatha, ndipo osautsa Yuda adzaonongeka. Efuremu sadzadukidwa ndi Yuda, ndipo Yuda sadzavuta Efuremu. Koma Yuda ndi Efuremu adzathira nkhondo pa Afilisti kuzambwe, ndipo onsewo pamodzi adzalanda zinthu za anthu akuvuma. Adzalimbana ndi Aedomu ndi Amowabu, ndipo Aamoni adzaŵagonjera. Ndipo Chauta adzaphwetsa kotheratu mwendo wa nyanja yofiira ya ku Ejipito. Adzatambalitsa dzanja lake ndipo adzaombetsa mphepo yotentha pa mtsinje wa Yufurate. Mtsinjewo udzagaŵikana m'timitsinje tisanu ndi tiŵiri, kuti anthu aoloke pouma. Padzakhala mseu waukulu woti ayendepo otsalira ku Asiriya aja, monga m'mene panaliri mseu waukulu woyendapo Aisraele pochoka ku Ejipito. Mzimu wa Chauta udzakhala pa Iye, mzimu wopatsa nzeru ndi kumvetsa, mzimu wopatsa uphungu ndi mphamvu, mzimu wopatsa kudziŵa zinthu ndi kuwopa Chauta.
Mudzatenga pathupi, ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Mudzamutcha dzina lake Yesu. “Adzakhala wamkulu, ndipo adzatchedwa Mwana wa Mulungu Wopambanazonse. Ambuye Mulungu adzamlonga ufumu wa kholo lake Davide, ndipo adzakhala Mfumu ya Aisraele mpaka muyaya. Ufumu wake sudzatha konse.”
Pambuyo pake abusa aja adabwerera akuyamika ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene anali atamva ndi kuziwona. Zonse zinali monga momwe mngelo uja adaaŵauzira.
Anthu amene ankayenda mumdima aona kuŵala kwakukulu. Amene ankakhala m'dziko la mdima wandiweyani, kuŵala kwaŵaonekera.
Kenaka Simeoniyo adaŵadalitsa, nauza Maria, mai wa mwanayo, kuti, “Mwanayu Mulungu wamuika kuti Aisraele ambiri adzagwe, ambirinso adzadzuke, chifukwa cha iyeyu. Adzakhala chizindikiro chochokera kwa Mulungu, chimene anthu ambiri adzatsutsana nacho, kuti choncho maganizo amene ali m'mitima ya anthu ambiri adzaonekere poyera. Ndipo inunso mai, chisoni chidzabaya mtima wanu ngati lupanga.”
Mulungu adaŵachenjeza m'maloto kuti asadzerekonso kwa Herode kuja. Motero adadzera njira ina pobwerera kwao.
Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi magazi ndi mnofu, Yesu yemwe adasanduka munthu wonga iwowo. Adachita zimenezi kuti ndi imfa yake aononge Satana amene anali ndi mphamvu yodzetsa imfa. Pakutero adafunanso kuti aŵamasule amene pa moyo wao wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa.
Imbirani Chauta nyimbo yatsopano! Imbirani Chauta, anthu a m'dziko lonse lapansi! Uzani mitundu ya anthu kuti, “Chauta ndiye Mfumu. Dziko lonse lidakhazikitsidwa molimba, silidzagwedezeka konse. Adzaweruza mitundu yonse ya anthu mwachilungamo.” Zakumwamba zisangalale, zapansi pano zikondwere, nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam'menemo. Minda zikondwe pamodzi ndi zonse zam'menemo. Mitengo yam'nkhalango idzaimba mokondwa pamaso pa Chauta, pamene zabwera kudzalamulira dziko lapansi. Adzalamulira dziko lonse mwachilungamo, adzalamulira anthu a mitundu yonse moona. Imbirani Chauta, tamandani dzina lake! Lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. Lengezani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse, simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m'maiko onse.
Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.
Pamenepo Maria adati, “Mtima wanga ukutamanda Ambuye, ndipo mzimu wanga ukukondwera mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga,
“Atamandike Ambuye, Mulungu wa Aisraele, chifukwa adadzayendera anthu ao, ndi kudzaŵaombola. Adautsa wina, wa fuko la mtumiki wake Davide, kuti akhale Mpulumutsi wathu wamphamvu. Adaalibe mwana, chifukwa Elizabeti anali wosabala, ndipo aŵiri onsewo anali okalamba. Izi ndi zomwe Iye adaaneneratu kalekale kudzera mwa aneneri ake oyera mtima.
Adakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira, kuti zipherezere zimene Ambuye adaalankhulitsa mneneri kuti, “Ndidaitana Mwana wanga kuti atuluke ku Ejipito.”
Iwe Yerusalemu dzuka, ŵala, kuŵala kwako kwayamba. Ulemerero wa Chauta wakuŵalira. Chauta akuuza Yerusalemu kuti, “Alendo adzamanganso malinga ako, ndipo mafumu ao adzakutumikira. Ndidakulanga pamene ndinali wokwiya, koma tsopano ndidzakukomera mtima ndi kukuchitira chifundo. Zipata zako zidzakhala zotsekula nthaŵi zonse. Usana ndi usiku womwe sadzazitseka, kuti choncho anthu a mitundu yonse adzabwere ndi chuma chao kwa iwe, akuyenda pa mdipiti, mafumu ao ali patsogolo. Koma maiko ndi mafumu amene sakutumikira, adzaonongekeratu. Anthu a mitundu imeneyo adzaonongeka kotheratu.” “Mitundu itatu ija ya mitengo ya paini, imene ili yabwino kwambiri m'nkhalango ya ku Lebanoni, adzabwera nayo kuti akongoletsere Nyumba yanga. Motero m'Nyumba m'mene ndimakhala Ine mudzalemekezeka. Ana a amene adaakuzunzapo adzabwera ndipo adzakugwadira kuwonetsa ulemu. Onse amene adaakunyozapo adzakuŵeramira mpaka pansi. Adzakutchula kuti Mzinda wa Chauta, ndiye kuti Ziyoni, mzinda wa Woyera uja wa Israele.” “Ngakhale anthu adakusiya nadana nawe, osadutsanso mwa iwe, ndidzakukuza mpaka muyaya, ndipo udzakhala malo a chimwemwe pa mibadwo ndi mibadwo. Monga mwana woyamwa udzadya chuma cha anthu a mitundu ina, ndipo mafumu ao omwe adzakusamala. Motero udzadziŵa kuti Ine Chauta ndine Mpulumutsi wako, ndipo kuti ndine Momboli wako, Wamphamvu uja wa Yakobe.” “Ndidzakupatsa golide m'malo mwa mkuŵa, m'malo mwa chitsulo ndidzakupatsa siliva, mkuŵa m'malo mwa mtengo, chitsulo m'malo mwa mwala. Okuyang'anira ndidzaŵasandutsa amtendere, okulamulira ndidzaŵasandutsa olungama. Ziwawa sizidzamvekanso. Dziko lako silidzaonongekanso. Ndidzakhala ngati linga lokuteteza, ndipo udzanditamanda chifukwa chokupulumutsa.” “Sipadzafikanso dzuŵa loti likuŵalire masana, kapena mwezi wokuŵalira usiku. Koma Ine Chauta ndiye ndidzakuŵalire mpaka muyaya. Ine Mulungu wako ndiye ndidzakhale ulemerero wako. Mdima udzaphimba dziko lapansi, mdima wandiweyani udzagwa pa anthu a mitundu ina. Koma iwe, Chauta adzakuŵalira, ulemerero wake udzaoneka pa iwe. Chokuunikira ngati dzuŵa sichidzaloŵanso, ndipo chokuunikira ngati mwezi sichidzazimiriranso, chifukwa ndi Chauta amene adzakhala kuŵala kwako mpaka muyaya. Choncho masiku ako olira adzatha. Anthu ako onse adzayenda m'njira zoyenera, ndipo dzikolo lidzakhala lao mpaka muyaya. Anthuwo ndidaŵaika ndine, ndidaŵalenga ndine, kuti aonetse ulemerero wanga kwa onse. Ngakhale kabanja kakang'onong'ono kadzasanduka fuko, ndipo kafuko kakang'onong'ono kadzasanduka mtundu wamphamvu. Ndidzachita zimenezi mofulumira nthaŵi yake itafika. Ine ndine Chauta.” Anthu a mitundu ina adzatsata kuŵala kwako, mafumu adzalondola kunyezimira kwako konga dzuŵa limene likutuluka kumene.
Tsono Yosefe atadzuka, adachita monga momwe mngelo wa Ambuye uja adaamuuzira. Adamtenga Maria, mkazi wake uja, koma sadamdziŵe mpaka adabala mwana wamwamuna. Pambuyo pake Yosefe adatcha mwanayo dzina loti Yesu.
Tsono mwana iwe, udzatchedwa mneneri wa Mulungu Wopambanazonse, chifukwa udzatsogola pamaso pa Ambuye, kuti ukonzeretu njira zao. Udzadziŵitsa anthu ao kuti Mulungu adzaŵapulumutsa pakuŵakhululukira machimo ao. Mulungu wathu ndi wa chifundo chachikulu, adzatitumizira kuŵala kwa dzuŵa lam'maŵa kuchokera Kumwamba. Kuŵala kwake kudzaunikira onse okhala mu mdima wabii ngati wa imfa, kudzatitsogolera pa njira ya mtendere.”
Tamandani Chauta! Tamandani Chauta inu okhala kumwamba, mtamandeni inu okhala mu mlengalenga! Inu nyama zakutchire ndi zoŵeta zonse, inu zinthu zokwaŵa ndi mbalame zouluka! Inu mafumu a pa dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse, inu akuluakulu ndi olamulira dziko lapansi! Inu anyamata pamodzi ndi anamwali, inu nkhalamba ndi ana omwe! Onsewo atamande dzina la Chauta, pakuti dzina lake lokha nlolemekezeka, ulemerero wake ndi woposa, pansi pano nkumwamba komwe. Chauta wakweza anthu ake poŵapatsa mphamvu. Walemekeza anthu ake onse oyera mtima, Aisraele amene Iye amaŵakonda. Tamandani Chauta! Mtamandeni inu angelo ake onse, mtamandeni inu magulu a ankhondo ake onse! Mtamandeni inu dzuŵa ndi mwezi, mtamandeni inu nonse nyenyezi zoŵala! Mtamandeni inu thambo lakumwambamwamba, ndi inu madzi a pamwamba pa thambo!
Nayenso mneneri Yesaya akuti, “Mmodzi mwa zidzukulu za Yese adzabwera. Iye adzadzambatuka kuti alamule anthu a mitundu ina, ndipo iwo adzaika chikhulupiriro chao pa Iyeyo.”
Ku Yerusalemuko kunali munthu wina, dzina lake Simeoni. Anali munthu wolungama ndi woopa Mulungu. Ankayembekezera nthaŵi yoti Mulungu adzapulumutse Aisraele, ndipo Mzimu Woyera anali naye. Mzimu Woyerayo adaamuululira kuti sadzafa asanaone Mpulumutsi amene Mulungu adaalonjeza. Tsiku lina Mzimu Woyera adamlamula kuti apite ku Nyumba ya Mulungu. Makolo a Yesu adaloŵanso m'Nyumbamo ndi mwana waoyo kukamchitira mwambo potsata Malamulo a Mose. Pamenepo Simeoni adalandira mwanayo m'manja mwake, nayamba kutamanda Mulungu ndi mau akuti, “Ambuye, tsopano mundilole ine mtumiki wanu, ndipite ndi mtendere, pakuti mwachitadi zija mudaalonjezazi. Motero anthu onse adapita kukalembedwa, aliyense ku mudzi kwao. Ndi maso angaŵa ndachiwonadi chipulumutso chija,
Choncho panali mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa Abrahamu mpaka pa mfumu Davide, mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa Davideyo mpaka pa nthaŵi imene Aisraele adaatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni, ndiponso mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa nthaŵi yotengedwa ukapolo kupita ku Babiloni mpaka pa nthaŵi ya Khristu, Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
Pajatu mtumiki wake uja adakula ngati chiphukira pamaso pa Mulungu, ndiponso ngati muzu m'nthaka youma. Iye analibe maonekedwe enieni kapena nkhope yabwino, kuti ife nkumamuyang'ana. Analibe kukongola koti ife nkukokeka naye.
Mafumu a ku Tarisisi ndi akuzilumba adzaipatsa mitulo, mafumu a ku Sheba ndi a ku Seba adzabwera ndi mphatso. Mafumu onse adzaigwadira ndipo mitundu yonse ya anthu idzaitumikira.
Iye adafikako nthaŵi yomweyo, nayamba kuyamika Mulungu, nkumakamba za Mwanayo ndi anthu onse amene ankayembekezera nthaŵi yoti Mulungu adzapulumutse Yerusalemu.
“ ‘Iwe Betelehemu wa m'dziko la Yuda, sindiwe wamng'ono konse pakati pa akulu olamulira Yuda. Pakuti kwa iwe kudzachokera mtsogoleri pamene adzalamulira anthu anga Aisraele.’ ”
Chauta adauza Mbuye wanga kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja, mpaka nditasandutsa adani ako kukhala ngati chopondapo mapazi ako.”
Chauta akuti, “Nayu mtumiki wanga amene ndimamchirikiza, amene ndamsankhula, amene ndimakondwera naye. Ndaika Mzimu wanga mwa iyeyo, ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo.
Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?
Mngelo uja adadza kwa iye nati, “Moni, inu amene Mulungu wakukomerani mtima kotheratu. Ambuye ali nanu.”
Adamuuza kuti, “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mai wake, ubwerere ku Israele. Aja ankafuna kumupha mwanayu adafa.” Apo Yosefe adanyamuka, nkutenga mwana uja ndi mai wake, kubwerera ku Israele.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Fuulani kwa Chauta ndi chimwemwe, inu maiko onse. Tumikirani Chauta mosangalala. Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa. Dziŵani kuti Chauta ndiye Mulungu. Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake. Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake. Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake! Paja Iye ndi wabwino. Chikondi chake nchamuyaya, kukhulupirika kwake nkosatha.
Chautayo akunena kuti, “Nchinthu chochepa kwambiri kuti ukhale mtumiki wanga, kuti udzutse mafuko a Yakobe ndi kuŵabweza kwao Aisraele amene adapulumuka. Ndidzakusandutsa kuŵala kounikira mitundu ina ya anthu, kuti chipulumutso changa chikafike mpaka ku mathero a dziko lapansi.”
Pamenepo Herode adaŵaitanira paseri akatswiri a nyenyezi aja, naŵafunsitsa za nthaŵi yeniyeni imene adaaiwonera nyenyeziyo. Kenaka adaŵatumiza ku Betelehemu nkuŵauza kuti, “Pitani, kafunsitseni za mwanayo. Mukakampeza, mudzandidziŵitse, kuti inenso ndidzapite kukampembedza.”
pakuti Iye amene ali wamphamvu wandichitira zazikulu, ndipo dzina lake nloyera. Pa nthaŵi imene Herode anali mfumu ya dziko la Yudeya, kunali wansembe wina, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya. Mkazi wake Elizabeti anali wa fuko la Aroni. Amaŵachitira chifundo anthu a mibadwo ndi mibadwo amene amamlemekeza.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Koma adadzitsitsa kotheratu pakudzitengera umphaŵi wa kapolo, ndi kukhala munthu wonga anthu onse. Ali munthu choncho adadzichepetsa, adakhala womvera mpaka imfa, imfa yake yapamtanda.
Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake!
Kudzafika mtindiri wa ngamira, ngamira zing'onozing'ono, kuchokera ku Midiyani ndi ku Efa. Onse a ku Sheba adzabwera. Adzakhala atatenga golide ndi lubani, ndipo adzatamanda Chauta mokweza mau.
“Namwali wina wosadziŵa mwamuna adzatenga pathupi nkubala mwana wamwamuna. Mwanayo adzatchedwa dzina loti Imanuele,” ndiye kuti “Mulungu ali nafe.”
Ndi maso angaŵa ndachiwonadi chipulumutso chija, chimene mudakonza kuti anthu a mitundu yonse achiwone. Mwapereka kuŵala kodzaunikira anthu a mitundu ina, kodzakhala ulemerero wa anthu anu Aisraele.”
Pambuyo pake Yesu adalankhulanso ndi Afarisi aja, adati, “Ine ndine kuŵala kounikira anthu onse. Munthu wotsata Ine, sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuŵala kotsogolera anthu ku moyo.”
Nonsenu ndinu ana a Mulungu chifukwa mumakhulupirira Khristu Yesu. Pajatu nonsenu amene mudasanduka amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, mudachita ngati kuvala moyo wa Khristu.
Masiku amenewo, Augusto, Mfumu ya ku Roma, adalamula kuti pakhale kalembera wa anthu a m'maiko ake onse. Koma mngeloyo adaŵauza kuti, “Musaope, ndadzakuuzani uthenga wabwino, umene udzakondweretsa anthu onse kwambiri. Usiku womwe uno m'mudzi wa Davide wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye. Chitsimikizo chake ndi ichi: mukapeza mwana wakhanda, wokutidwa ndi nsalu, atagona m'chodyera cha zoŵeta.” Mwadzidzidzi pamodzi ndi mngeloyo padaoneka gulu lalikulu la angelo ena. Ankatamanda Mulungu ndi mau akuti, “Ulemerero kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene Iye amakondwera nawo.” Angelowo atachoka kubwerera Kumwamba, abusa aja adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tipite ku Betelehemu, tikaone zachitikazi, zimene Ambuye atidziŵitsa.” Tsono adapita mofulumira, nakapeza Maria ndi Yosefe, atagoneka mwana wakhandayo m'chodyera cha zoŵeta chija. Pamene adamuwona, abusawo adaŵafotokozera zimene mngelo uja adaaŵauza za mwanayo. Onse amene ankamva, ankadabwa ndi zimene abusawo ankaŵasimbira. Koma Maria adasunga zonsezo namazilingalira mumtima mwake. Kalembera ameneyu anali woyamba, ndipo adachitika pamene Kwirinio anali bwanamkubwa wa dziko la Siriya. Pambuyo pake abusa aja adabwerera akuyamika ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene anali atamva ndi kuziwona. Zonse zinali monga momwe mngelo uja adaaŵauzira. Patapita masiku asanu ndi atatu, mwana uja adamuumbala namutcha dzina lake Yesu. Dzinali ndi lomwe lija limene mngelo adaatchula, Maria asanatenge pathupi. Kenaka idafika nthaŵi yoti Yosefe ndi Maria achite mwambo wakuyeretsedwa potsata Malamulo a Mose. Tsono mwanayo adapita naye ku Yerusalemu kuti akampereke kwa Ambuye. Pajatu m'Malamulo a Ambuye muli mau akuti, “Mwana aliyense wamwamuna, woyamba kubadwa, apatulidwe kuti akhale wao wa Ambuye.” Adakaperekanso nsembe potsata Malamulo a Ambuye akuti, “Apereke njiŵa ziŵiri kapena maunda aŵiri.” Ku Yerusalemuko kunali munthu wina, dzina lake Simeoni. Anali munthu wolungama ndi woopa Mulungu. Ankayembekezera nthaŵi yoti Mulungu adzapulumutse Aisraele, ndipo Mzimu Woyera anali naye. Mzimu Woyerayo adaamuululira kuti sadzafa asanaone Mpulumutsi amene Mulungu adaalonjeza. Tsiku lina Mzimu Woyera adamlamula kuti apite ku Nyumba ya Mulungu. Makolo a Yesu adaloŵanso m'Nyumbamo ndi mwana waoyo kukamchitira mwambo potsata Malamulo a Mose. Pamenepo Simeoni adalandira mwanayo m'manja mwake, nayamba kutamanda Mulungu ndi mau akuti, “Ambuye, tsopano mundilole ine mtumiki wanu, ndipite ndi mtendere, pakuti mwachitadi zija mudaalonjezazi. Motero anthu onse adapita kukalembedwa, aliyense ku mudzi kwao.
Ndithu ndidzamsandutsa mwana wanga wachisamba, adzakhala wopambana mafumu a dziko lapansi.
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera.
Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.
Wadzathandiza anthu ake Aisraele, pokumbukira chifundo chake. Izi ndi zomwe adaalonjeza kuti adzaŵachitira makolo athu akale aja, Abrahamu ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.”
Mfumu Herode atamva zimenezi, adavutika kwambiri ndipo anthu ena onse a m'Yerusalemu nawonso adavutika nazo.
Koma Inu mwandisangalatsa mtima kwambiri, kupambana anthu a zakudya ndi zakumwa zambiri!
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Kuŵala kwake kudzaunikira onse okhala mu mdima wabii ngati wa imfa, kudzatitsogolera pa njira ya mtendere.”
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
hokozani Chauta chifukwa ngwabwino, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adapha ana achisamba a ku Ejipito, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Ndipo adatulutsa Aisraele pakati pao, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambalitsa, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adagaŵa pakati Nyanja Yofiira, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adaolotsa Aisraele pakati pake, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Koma adamiza Farao ndi ankhondo ake m'Nyanja Yofiira, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adatsogolera anthu ake m'chipululu, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adapha mafumu amphamvu, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adaphanso mafumu otchuka, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adapha Sihoni, mfumu ya Aamori, pakuti chikondi chake nchamuyaya, Thokozani Mulungu wa milungu, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adapha Ogi, mfumu ya ku Basani, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Napereka dziko la mafumuwo kuti likhale choloŵa, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Choloŵa cha Israele mtumiki wake, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adatikumbukira pamene adani adatigonjetsa, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Ndipo adatipulumutsa kwa adani athu, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Amapatsa zamoyo zonse chakudya, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Thokozani Mulungu wakumwamba, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Thokozani Chauta woposa ambuye onse, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
“Ulemerero kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene Iye amakondwera nawo.”
Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.
Si kukondwetsa kwake pamene mukuwona wamthenga akuyenda m'mapiri, akubwera ndi uthenga wabwino, akulengeza za mtendere, akudzetsa chisangalalo, akulengeza za chipulumutso, akuuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wanu ndi mfumu.”
Ndipo anthu angalalike bwanji ngati palibe oŵatuma? Paja mau a Mulungu akuti, “Nchokondweretsa zedi kuwona olalika Uthenga Wabwino akufika.”
Pofuna kutsimikiza kuti ndinu ana ake, Mulungu adatitumizira Mzimu wa Mwana wake m'mitima mwathu, ndipo Mzimuyo amatinenetsa kuti, “Abba! Atate!”
Akulingalira zimenezi, mngelo wa Ambuye adamuwonekera m'maloto, namuuza kuti, “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kumtenga Maria, mkazi wakoyu. Pathupi ali napopa padachitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Uzani mitundu ya anthu kuti, “Chauta ndiye Mfumu. Dziko lonse lidakhazikitsidwa molimba, silidzagwedezeka konse. Adzaweruza mitundu yonse ya anthu mwachilungamo.”
Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo ameneŵa Iye adaŵapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu.
Tamandani Chauta! Tamandani Chauta inu okhala kumwamba, mtamandeni inu okhala mu mlengalenga! Inu nyama zakutchire ndi zoŵeta zonse, inu zinthu zokwaŵa ndi mbalame zouluka! Inu mafumu a pa dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse, inu akuluakulu ndi olamulira dziko lapansi! Inu anyamata pamodzi ndi anamwali, inu nkhalamba ndi ana omwe! Onsewo atamande dzina la Chauta, pakuti dzina lake lokha nlolemekezeka, ulemerero wake ndi woposa, pansi pano nkumwamba komwe. Chauta wakweza anthu ake poŵapatsa mphamvu. Walemekeza anthu ake onse oyera mtima, Aisraele amene Iye amaŵakonda. Tamandani Chauta! Mtamandeni inu angelo ake onse, mtamandeni inu magulu a ankhondo ake onse! Mtamandeni inu dzuŵa ndi mwezi, mtamandeni inu nonse nyenyezi zoŵala! Mtamandeni inu thambo lakumwambamwamba, ndi inu madzi a pamwamba pa thambo! Zonsezo zitamande dzina la Chauta! Paja Iye adaalamula, izo nkulengedwa.
Ndithu, Inu mumayatsa nyale ya moyo wanga. Chauta, Mulungu wanga, amandiwunikira mu mdima.
Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani. Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu. Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa. Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano.
Iwe Yerusalemu dzuka, ŵala, kuŵala kwako kwayamba. Ulemerero wa Chauta wakuŵalira. Chauta akuuza Yerusalemu kuti, “Alendo adzamanganso malinga ako, ndipo mafumu ao adzakutumikira. Ndidakulanga pamene ndinali wokwiya, koma tsopano ndidzakukomera mtima ndi kukuchitira chifundo. Zipata zako zidzakhala zotsekula nthaŵi zonse. Usana ndi usiku womwe sadzazitseka, kuti choncho anthu a mitundu yonse adzabwere ndi chuma chao kwa iwe, akuyenda pa mdipiti, mafumu ao ali patsogolo. Koma maiko ndi mafumu amene sakutumikira, adzaonongekeratu. Anthu a mitundu imeneyo adzaonongeka kotheratu.” “Mitundu itatu ija ya mitengo ya paini, imene ili yabwino kwambiri m'nkhalango ya ku Lebanoni, adzabwera nayo kuti akongoletsere Nyumba yanga. Motero m'Nyumba m'mene ndimakhala Ine mudzalemekezeka. Ana a amene adaakuzunzapo adzabwera ndipo adzakugwadira kuwonetsa ulemu. Onse amene adaakunyozapo adzakuŵeramira mpaka pansi. Adzakutchula kuti Mzinda wa Chauta, ndiye kuti Ziyoni, mzinda wa Woyera uja wa Israele.” “Ngakhale anthu adakusiya nadana nawe, osadutsanso mwa iwe, ndidzakukuza mpaka muyaya, ndipo udzakhala malo a chimwemwe pa mibadwo ndi mibadwo. Monga mwana woyamwa udzadya chuma cha anthu a mitundu ina, ndipo mafumu ao omwe adzakusamala. Motero udzadziŵa kuti Ine Chauta ndine Mpulumutsi wako, ndipo kuti ndine Momboli wako, Wamphamvu uja wa Yakobe.” “Ndidzakupatsa golide m'malo mwa mkuŵa, m'malo mwa chitsulo ndidzakupatsa siliva, mkuŵa m'malo mwa mtengo, chitsulo m'malo mwa mwala. Okuyang'anira ndidzaŵasandutsa amtendere, okulamulira ndidzaŵasandutsa olungama. Ziwawa sizidzamvekanso. Dziko lako silidzaonongekanso. Ndidzakhala ngati linga lokuteteza, ndipo udzanditamanda chifukwa chokupulumutsa.” “Sipadzafikanso dzuŵa loti likuŵalire masana, kapena mwezi wokuŵalira usiku. Koma Ine Chauta ndiye ndidzakuŵalire mpaka muyaya. Ine Mulungu wako ndiye ndidzakhale ulemerero wako. Mdima udzaphimba dziko lapansi, mdima wandiweyani udzagwa pa anthu a mitundu ina. Koma iwe, Chauta adzakuŵalira, ulemerero wake udzaoneka pa iwe.
Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
Mulungu wathu ndi wa chifundo chachikulu, adzatitumizira kuŵala kwa dzuŵa lam'maŵa kuchokera Kumwamba. Kuŵala kwake kudzaunikira onse okhala mu mdima wabii ngati wa imfa, kudzatitsogolera pa njira ya mtendere.”
Yesu Khristu, makolo ake anali Davide ndi Abrahamu. Motsatanatsatana maina a makolo ake onse ndi aŵa:
Nchifukwa chake Ambuye omwe adzakupatsani inu chizindikiro. Onani, namwali uja watenga pathupi ndipo adzabala mwana wamwamuna, mwanayo adzamutcha dzina lake Imanuele.
komabe kwanga nkukondwerera mwa Chauta, kwanga nkusangalala chifukwa cha Mulungu Mpulumutsi wanga.
Pamenepo Maria adati, “Mtima wanga ukutamanda Ambuye, ndipo mzimu wanga ukukondwera mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga, popeza kuti wayang'ana kutsika kwa mtumiki wake. Ndithu kuyambira tsopano anthu a mibadwo yonse adzanditcha wodala,
Adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu, chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo ao.”
Koma mngeloyo adaŵauza kuti, “Musaope, ndadzakuuzani uthenga wabwino, umene udzakondweretsa anthu onse kwambiri.
Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m'manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.”