Ndikudziwa kuti nthawi zina mtima umangokhala chete, ngati ulibe mphamvu yokhudzidwa ndi zinthu zomwe zikuchitika pa moyo wa anthu ena, kapena ntchito zathu, kaya za Mulungu kapena za dziko. Mtima umenewu ndi wovuta, umakupangitsa kuti usamamve chisoni cha anthu ena, ngakhale akukumana ndi mavuto aakulu.
Ukakhala ndi mtima umenewu, umatha kutaya chilakolako cha zinthu zomwe unkazikonda kale, zomwe unkafuna kuchita. Umatha kungokhala chete, osafuna kuchita khama kuti ukwaniritse maloto ako. Umafika povomereza moyo wamba, osafuna kusintha kalikonse.
Koma dziwa ichi, sudzakhala ndi mtima umenewu mpaka kalekale. Yesu ali ndi mphamvu yoti akuthandize. Baibulo limatiuza kuti mwa Iye ndife opambana. Ngakhale utamva kuti suli ndi mphamvu zopitirira, Iye angakupatsenso mphamvu zoyimirira ndikupitiriza ulendo wako.
Ndikukulimbikitsa lero, muka, ukapemphere kwa Mulungu. Mukaimirire mwamphamvu pa cholinga chimene Mulungu anakupatsa. Kumbukira kuti ukhoza kuchita zonse mwa Khristu amene amakupatsa mphamvu.
Sitifuna kuti mukhale aulesi, koma kuti mutsanzire anthu amene, pakukhulupirira ndi pakupirira, akulandira zimene Mulungu adalonjeza.
Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Sindinu ozizira, sindinunso otentha. Bwenzi zili bwino mukadakhala ozizira kapena otentha. Koma popeza kuti ndinu ofunda chabe, osati otentha kapena ozizira, ndidzakusanzani.
Anthu opusa amaphedwa chifukwa cha kusokera kwao. Zitsiru zimadziwononga zokha nkudzitama kwao.
“Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu aupandu. Iwowo maso openyera ali nawo, komabe saona. Makutu omvera ali nawo, komabe saamva, chifukwa choti ngaupandu.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Paja nthaŵi imene tinali nanu pamodzi, tidaakulamulani kuti munthu wosafuna kugwira ntchito, kudyanso asadye.
Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa.
Nchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti mphatso imene Mulungu adakupatsa pamene ndidakusanjika manja, uiyatsenso ngati moto.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Paja nthaŵi imene tinali nanu pamodzi, tidaakulamulani kuti munthu wosafuna kugwira ntchito, kudyanso asadye. Tikunena zimenezi popeza kuti tikumva kuti pali ena pakati panu amene ali ndi khalidwe laulesi. Anthu ameneŵa sagwira ntchito konse, koma amangoloŵera pa za anzao. M'dzina la Ambuye Yesu Khristu tikuŵalamula ndi kuŵachenjeza anthu otere kuti azigwira ntchito mwabata, ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito.
Tsono popeza kuti zoipa zizidzachulukirachulukira, chikondi chizidzacheperachepera pakati pa anthu.
Paja Iye adadzipereka chifukwa cha ife, kuti atipulumutse ku zoipa zathu zonse, ndi kutiyeretsa kuti tikhale anthu ake achangu pa ntchito zonse zabwino.
Manja aulesi amagwetsa munthu mu umphaŵi, koma manja achangu amalemeretsa munthu. Mwana womakolola nthaŵi yachilimwe ndiye wanzeru, koma womangogona nthaŵi yokolola amachititsa manyazi.
Muziganiza za Iye amene adapirira udani waukulu chotere wochokera kwa anthu ochimwa, kuti musafookere ndi kutaya mtima.
Ukati, “Taimani ndigoneko pang'ono,” kapena “Ndiwodzereko chabe,” kapena “Ndingopumulako pang'ono,” umphaŵi udzakufikira monga mbala, kusauka kudzakupeza ngati mbala yachifwamba.
Tsono muyesetse kuchita khama kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, ndi nzeru zoona pa makhalidwe anu abwinowo. Muwonjezerepo kudziletsa pa nzeru zoonazo, kulimbika pa kudziletsa kwanu, ndiponso kupembedza Mulungu pa kulimbika kwanuko. Pa kupembedzapo muwonjezerepo chifundo chachibale, ndipo pa chifundo chachibalecho muwonjezepo chikondi. Ngati zonsezi zikhala mwa inu, nkumachuluka, simudzakhala olephera ndi opanda phindu pa nzeru zodziŵira Ambuye athu Yesu Khristu.
Muchite zimenezi chifukwa mukudziŵa kuti yafika kale nthaŵi yakuti mudzuke kutulo. Pakuti chipulumutso chili pafupi tsopano kuposa pamene tidayamba kukhulupirira.
Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa ndi waulesi. Kani unkadziŵa kuti ineyo ndimakolola kumene sindidabzale, ndipo ndimasonkhanitsa dzinthu kumene sindidafese mbeu?
Nchifukwa chake tsono tisagone tulo monga momwe amachitira anthu ena, ife tikhale maso, tikhale osaledzera.
Nchifukwa chake mtima wanu ukhale wokonzeka. Khalani tchelu. Khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa kukoma mtima kwa Mulungu pamene Yesu Khristu adzaoneke.
“Khalani okonzeka kutumikira, ndipo nyale zanu zikhale zoyaka. Khalani ngati antchito amene akudikira mbuye wao wochokera ku phwando la ukwati, kuti pamene afike ndi kugogoda, iwo amtsekulire msanga.
Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
Pita kwa nyerere, mlesi iwe. Kapenyetsetse makhalidwe ake, ukaphunzireko nzeru. Ilibe ndi mfumu yomwe, ilibe kapitao kapena wolamulira. Komabe imakonzeratu chakudya chake m'malimwe, ndipo imatuta chakudyacho m'masika.
“Za Ufumu wakumwamba tingazifanizirenso motere: Munthu wina ankapita pa ulendo. Asananyamuke adaitana antchito ake, naŵasiyira chuma chake. Wina adampatsa ndalama zisanu, wina ziŵiri, wina imodzi. Aliyense adampatsa molingana ndi nzeru zake, iye nkuchokapo. Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adapita nakachita nazo malonda nkupindula ndalama zinanso zisanu. Chimodzimodzinso amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adapindula ndalama zinanso ziŵiri. Koma amene adaalandira ndalama imodzi uja, adapita nakaikumbira pansi ndalama ya mbuye wake ija. “Patapita nthaŵi yaitali, mbuye wao uja adabwerako naŵaitana antchito ake aja kuti amufotokozere za zimene adaachita ndi ndalama zija. Asanu anali opusa, ndipo asanu enawo anali ochenjera. Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adabwera ndi zisanu zinanso nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama zisanu. Onani, ndidapindula zisanu zinanso: izi.’ Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’ Nayenso wantchito amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adabwera nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama ziŵiri. Onani, ndidapindula ziŵiri zinanso: izi.’ Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’ “Nayenso amene adaalandira ndalama imodzi uja adabwera nati, ‘Ambuye, ine ndinkadziŵa kuti inu ndinu munthu wankhwidzi. Mumakolola kumene simudabzale, ndipo mumasonkhanitsa dzinthu kumene simudafese mbeu. Ndiye ndinkachita mantha, choncho ndidaakaikumbira pansi ndalama yanu ija. Nayi tsono ndalama yanuyo.’ Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa ndi waulesi. Kani unkadziŵa kuti ineyo ndimakolola kumene sindidabzale, ndipo ndimasonkhanitsa dzinthu kumene sindidafese mbeu? Tsonotu udaayenera kukaiika ku banki ndalama yangayo, ine pobwera ndikadadzailandira pamodzi ndi chiwongoladzanja chake. Mlandeni ndalamayi, muipereke kwa amene ali ndi ndalama khumiyo. Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe. Asanu opusa aja adangotenga nyale zao, osatenga mafuta ena apadera. Tsono mtumiki wopandapakeyu kamponyeni kunja ku mdima. Kumeneko azikalira ndi kukukuta mano.’
Tiyeni tsono muzitsirize. Paja munali ndi changu pofuna kuzichita, muchitenso changu tsopano kuzitsiriza molingana ndi zimene muli nazo.
Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.
Munthu waulesi amakhumbira zinthu koma sapeza kanthu, m'menemo munthu wakhama amalemera.
Muzipemphera mosafookera, ndipo pamene mukupemphera, muzikhala tcheru ndiponso oyamika Mulungu.
Abale, mchenjere, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woipa ndi wosakhulupirira, womlekanitsa ndi Mulungu wamoyo.
Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao.
Muzikhala maso tsono, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse, kuti mukhale ndi mphamvu zopulumukira ku zonsezi zimene ziti zidzachitike, ndiponso kuti mukaimirire pamaso pa Mwana wa Munthu.”
Sikuti akuzengereza kuchita zimene adalonjeza, monga m'mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima.
Nchifukwa chake ine, womangidwa m'ndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukupemphani kuti, chifukwa Mulungu adakuitanani, muziyenda moyenerana ndi kuitanidwako.
Monga momwe mbaŵala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga umakhumbira Inu Mulungu wanga. Kunyoza kwa adani anga kumandipweteka ngati bala lofa nalo la m'thupi mwanga, akamandifunsa nthaŵi zonse kuti, “Mulungu wako ali kuti?” Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Mulungu, Mulungu wamoyo. Kodi ndidzafika liti pamaso pa Mulungu?
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiŵala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo. Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.
Ndapempha chinthu chimodzi chokha kwa Chauta, chinthu chofunika kwambiri, chakuti ndizikhala m'Nyumba ya Chauta masiku onse a moyo wanga, kuti ndizikondwera ndi kukoma kwake kwa Chauta ndi kuti ndizipembedza Iye m'Nyumba mwakemo.
Monga inu simudziŵa kuti pa mpikisano wa liŵiro onse amathamanga, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Tsono kuthamanga kwanu kukhale kwakuti nkukalandira mphothoyo. Aliyense wothamanga pa mpikisano wa liŵiro amadziletsa pa zonse. Iwowo amachita zimenezi kuti akalandire mphotho ya nkhata yamaluŵa yotha kufota. Koma mphotho imene ife tidzalandira, ndi yosafota. Nchifukwa chake ndimathamanga monga munthu wodziŵa kumene walinga. Ndiponso ndikamachita mpikisano womenyana, sindichita ngati munthu amene angomenya mophonya. Ndimazunza thupi langa ndi kuligonjetsa, kuti likhale ngati kapolo wondimvera. Ndimachita zimenezi kuwopa kuti ine ndemwe, amene ndidaitana ena ku mpikisano, ndingapezeke wosayenera kuchita nao mpikisanowo.
Nchifukwa chake, ngakhale tikhalebe kuno, kapena tikakhale kwa Ambuye, timayesetsa kuŵakondweretsa Ambuyewo.
Ngati muli okonzeka kundimvera, mudzalidyera dziko. Chauta adati, “Tamvera, iwe mlengalenga, tchera khutu, iwe dziko lapansi, Ine Chauta ndikulankhula. Ndidabereka ana ndi kuŵalera, koma andigalukira. Koma mukakana ndi kumapanduka, mudzaphedwa ndi lupanga. Ine Chauta ndatero.”
Ntchito iliyonse imene ukuti uigwire, uigwire ndi mphamvu zako zonse. Pajatu kumanda kumene ukupitako kulibe ntchito, kulibe malingaliro, kulibe nzeru, ndiponso kulibe luntha.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.
Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.
Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye.
Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.
“Pa nthaŵi imeneyo za Ufumu wakumwamba zidzafanafana ndi zimene zidaachitikira anamwali khumi. Iwowo adaatenga nyale zao nkumakachingamira mkwati. Pamene ankakagula, mkwati adafika. Amene anali okonzekeratu aja adaloŵa naye pamodzi m'nyumba yaphwando; pambuyo pake adatseka chitseko. “Kenaka m'mbuyomwalendo anamwali ena aja nawonso adabwera nati, ‘Bwana, Bwana, titsekulireni!’ Koma mkwatiyo adati, ‘Pepani, sindikukudziŵani!’ ” Pomaliza Yesu adati, “Ndiyetu inu, muzikhala maso, poti simudziŵa tsiku lake kapena nthaŵi yake.”
Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
“Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi. Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa iye, amabereka zipatso zambiri. Pajatu popanda Ine simungathe kuchita kanthu.
Usanyozere mphatso yaulere ija ili mwa iweyi, imene udailandira kudzera m'mau otchulidwa m'dzina la Mulungu, pamene gulu la akulu a Mpingo lidaakusanjika manja. Ntchito zimenezi uzizichita mosamala ndi modzipereka, kuti anthu onse aone kuti moyo wako wautumiki ukukulirakulira.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta, amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse,
Kukali usana tizigwira ntchito za Atate amene adandituma. Usiku ukudza pamene munthu sangathe kugwira ntchito.
Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Tiyesetse tsono kuloŵa mu mpumulowo, kuwopa kuti wina aliyense angakhale wosamvera monga iwo aja, nalephera kuloŵamo.
Monga makanda obadwa chatsopano amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wodyetsa mtima wanu, kuti ukukuzeni ndi kukufikitsani ku chipulumutso,
Ndikupempha Mulungu kuti kuchokera m'chuma cha ulemerero wake akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu. Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi. Ndikupempha Mulungu kuti, pamodzi ndi anthu ake onse, muthe kuzindikira kupingasa kwake ndi kutalika kwake, kukwera kwake ndi kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. Ndithu ndikupemphera kuti mudziŵe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kotheratu ndi moyo wa Mulungu mwini.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika. Musandipirikitse pamaso panu, musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine. Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu, mulimbitse mwa ine mtima womvera.
Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.
Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse, musalole kuti ndisiye kumvera malamulo anu.
Changu chochitira Nyumba yanu chandiphetsa, chipongwe cha anthu okunyozani chandigwera.
Adzasamala maonekedwe ake okha a chipembedzo, nkumakana mphamvu zake. Anthu otere uziŵalewa.
“Yesetsani kuloŵera pa khomo lophaphatiza, pakuti kunena zoona anthu ambiri adzafuna kuloŵa, koma adzalephera.
Waulesi sasoseratu pa nthaŵi yoyenera. Pa nthaŵi yokolola adzafunafuna dzinthu, koma sadzapeza kanthu.
“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.
Koma ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu opembedza kwenikweni adzapembedza Atate mwauzimu ndi moona. Atate amafuna anthu otere kuti ndiwo azimpembedza. Mulungu ndi mzimu, ndipo ompembedza Iye ayenera kumpembedza mwauzimu ndi moona.”
Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera. Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,
Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu.
Njira ya munthu waulesi ndi yoŵirira ndi minga, koma njira ya munthu wolungama imakhala ngati mseu wosalala.
Chauta akunena kuti, “Inu nonse omva ludzu, bwerani, madzi ali pano. Ndipo inu amene mulibe ndalama, bwerani mudzagule chakudya, kuti mudye. Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka, osalipira ndalama, osalipira chilichonse.
Chikondi chizikhala chopanda chiphamaso. Muzidana ndi zoipa, nkumaika mtima pa kuchita zabwino.
Ndikunenatu zimenezi kufuna kuti ndikuthandizeni, osati kuti ndikuletseni ufulu wanu ai. Makamaka ndifuna kuti muzichita zonse moyenera, ndipo kuti muzidzipereka kwathunthu potumikira Ambuye.
Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, malinga ndi chikondi chanu chosasinthika. Mufafanize machimo anga, malinga ndi chifundo chanu chachikulu. Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika. Musandipirikitse pamaso panu, musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine. Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu, mulimbitse mwa ine mtima womvera. Pamenepo ochimwa ndidzaŵaphunzitsa njira zanu, ndipo iwo adzabwerera kwa Inu. Mundikhululukire mlandu wanga wokhetsa magazi, Inu Mulungu, Mulungu Mpulumutsi wanga, ndipo ndidzakweza mau poimba za chipulumutso chanu. Ambuye, tsekulani milomo yanga, ndipo pakamwa panga padzalankhula zotamanda Inu. Si nsembe wamba imene Inu imakusangalatsani. Ndikadapereka nsembe yopsereza, sibwenzi Inu mutakondwera nayo. Nsembe imene Inu Mulungu mumailandira, ndi mtima wotswanyika. Mtima wachisoni ndi wolapa, Inu Mulungu simudzaunyoza. Muŵachitire zabwino anthu a ku Ziyoni, chifukwa cha kukoma mtima kwanu. Mumangenso kachiŵiri makoma a Yerusalemu. Pamenepo mudzakondwera ndi nsembe zoyenera, nsembe zootcha ndi zopsereza kwathunthu. Choncho adzapereka ng'ombe zamphongo pa guwa lanu lansembe. Mundisambitse kwathunthu pochotsa kulakwa kwanga, mundiyeretse mtima pochotsa machimo anga.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Mulimbitse manja ofooka, ndi kuŵapatsa mphamvu maondo olobodoka. Muuze onse a mtima wamantha kuti, “Limbani mtima, musachite mantha. Mulungu wanu akubwera kudzalipsira ndi kulanga adani anu. Akubwera kudzakupulumutsani.”
Mtima wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka, kufunitsitsa kuwona mabwalo a Chauta. Inu Mulungu wamoyo, ndikukuimbirani mwachimwemwe ndi mtima wanga wonse.
Kumeneko inu mudzafunafuna Chauta, Mulungu wathu, ndipo ngati mudzamfunafuna ndi mtima wonse ndi moyo wanu wonse, mudzampeza.
Kuyambira pa nthaŵi ya Yohane Mbatizi mpaka tsopano anthu akhala akulimbana ndi Ufumu wa Kumwamba, ndipo ochita chamuna ndiwo amene akuulanda.
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo Iye adzayandikira kwa inu. Muzisamba m'manja, inu anthu ochimwa. Chotsani maganizo onyenga m'mitima mwanu, inu anthu okayikakayika.