Mtima wanga ukufuna kuti mukachoke kuno, muzipita bwino pa zonse, ndipo mukhale ndi thanzi labwino, monga momwe mukupitira patsogolo mwauzimu. Ndikukhulupirira kuti Mulungu adzakudalitsani pa ulendo wanu.
Mau ambiri ochokera m'Baibulo angatilimbikitse, monga momwe lemba la 3 Yohane 1:2 limatiuza. Mulungu ali ndi malonjezo ambiri kwa ife, ndipo ndikukhulupirira kuti mudzapeza mphamvu ndi chiyembekezo mwa Iye pamene mukupitiriza ulendo wanu.
Zikomo kwambiri chifukwa chobwera, ndipo Mulungu akudalitseni.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Chauta adaonekera Abrahamu ku mitengo ya thundu ya ku Mamure ija. Abrahamuyo atakhala pa khomo la hema lake nthaŵi yamasana kutatentha, Chauta adati, “Ndikukulonjeza kuti pakapita miyezi isanu ndi inai ndidzabweranso, ndipo mkazi wako adzakhala ali ndi mwana wamwamuna.” Sara ankangomvetsera ali kuseri kwa chitseko cha hema. Abrahamu pamodzi ndi Sara anali nkhalamba zokhazokha, ndipo nthaŵi imeneyo nkuti Sara ataleka kusamba monga amachitira akazi. Motero Sara adangoseka, namati, “Ha, monga ndakalambira inemu, kodi nkuthekanso kuti ndikondwe ndi mwamuna wanga? Komanso mwamuna wanga ndi wokalamba zedi.” Chauta adafunsa Abrahamu kuti, “Chifukwa chiyani Sara amaseka ndi kunena kuti, ‘Ine monga ndakalambiramu kungatheke bwanji kukhala ndi mwana?’ Kodi chilipo china choti chingakanike Chauta? Tsono pa nthaŵi yake, ndidzachitadi zimene ndalonjezazi, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.” Apo Sara adakana chifukwa cha mantha, adati, “Sindidaseke.” Koma Iye adati, “Inde, unaseka.” Tsono anthuwo adachoka, nafika pamalo pamene anali kupenya Sodomu. Abrahamu adapita nawo limodzi, naŵalozera njira. Ndipo Chauta adanena mwa Iye yekha kuti, “Abrahamuyu sindingamubisire chomwe ndikuti ndichite. Zidzukulu zake zidzakhala mtundu waukulu wamphamvu. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadalitsidwa chifukwa cha iye. Ndamsankha iyeyu kuti alamule ana ake ndi mabanja ake akutsogolo kuti azidzamvera mau anga, pochita zabwino ndi zolungama. Choncho ndidzachita zonse zimene ndidamlonjeza.” mwadzidzidzi adangoona anthu atatu ataimirira potero. Atangoŵaona, adanyamuka mwamsanga kukaŵalonjera. Adaŵeramitsa mutu, Tsono Chauta adauza Abrahamu kuti, “Pali zolakwa zoopsa zokhudza Sodomu ndi Gomora, ndipo tchimo lao ndi lalikulu kwambiri. Choncho ndikuti nditsikireko kuti ndikaone ngati zolakwa zimene ndamvazo ndi zoona. Ngati si choncho, ndidzadziŵa.” Anthu aja adachoka, napita ku Sodomu, koma Abrahamu adatsarira ndi Chauta. Apo Abrahamu adayandikira kwa Chauta namufunsa kuti, “Kodi monga mudzaonongadi anthu osachimwa pamodzi ndi ochimwa? Nanga patakhala kuti pali anthu 50 osachimwa mumzindamo, kodi mudzaonongabe mzinda wonse? Kodi simudzauleka kuti musunge anthu 50 amenewo? Ndithu simudzaononga anthu osachimwa pamodzi ndi ochimwa. Chimenechi nchosatheka ndipo simungachite. Mukadatero bwenzi anthu osachimwa akulangidwira kumodzi ndi ochima. Kutalitali, Inu simungachite zotere! Kodi Muweruzi wa dziko lonse lapansi nkupanda chilungamo?” Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 50 osachimwa m'Sodomu, ndidzauleka mzinda wonsewo osauwononga, chifukwa cha anthu 50 amenewo.” Abrahamu adalankhulanso, adati, “Chonde, ndalimba mtima pakulankhula nanu chotere, Ambuye. Inetu ndine munthu chabe pamaso panu. Nanga pa chiŵerengero cha 50 pakangopereŵera anthu asanu okha, bwanji? Kodi mudzaononga mzindawo popeza kuti asoŵa asanu okha?” Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 45 olungama, sindidzaononga mzindawo.” Abrahamu adafunsanso kuti, “Nanga pakapezeka anthu olungama 40 okha?” Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 40, sindidzauwononga.” nati, “Mbuyanga, ngati ndapeza kuyanja pamaso panu, chonde musapitirire pakhomo pa mtumiki wanu.
“Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa.
Wokondedwa, ndimapemphera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndipo kuti moyo wako wathupi ukhale wolimba, monga momwe uliri moyo wako wauzimu.
Inu Chauta, mumadalitsa munthu wochita chilungamo. Kukoma mtima kwanu kuli ngati chishango chomuteteza.
Mlendo amene akhala nanu, akhale ngati mbadwa pakati panu, ndipo mumkonde monga momwe mumadzikondera inu nomwe. Pajatu inunso mudaali alendo m'dziko la Ejipito. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
Tsono muŵakonde anthu achilendowo, chifukwa paja inunso mudaali alendo ku Ejipito.
Kumindako Yonatani adauza Davide kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akhale mboni. Nditaŵafunsa abambo anga nthaŵi yonga yomwe ino maŵa, ngakhale mkucha, ndipo ndikapeza kuti akufuna kukuchitira chinthu chabwino, ndidzatumiza mau kuti udziŵe. Koma akakafunitsitsa kukuchita choipa, Chauta adzandilange kwambiri ndikapanda kukuululira ndi kukuthandiza kuti upulumuke. Chauta akhale nawe, monga momwe adakhalira ndi abambo anga. Ndikakhala ndili moyobe, udzandiwonetse kukoma mtima konga kwa Chauta. Koma ndikafa, usadzaleke kuchitira chifundo banja langa mpaka muyaya. Pamene Chauta adzaŵatha adani onse a Davide pa dziko lapansi,
Mukamulonjere motere: mukati mbuye wathu akuti, ‘Mtendere ukhale ndi inu ndi banja lanu ndi zinthu zonse zimene muli nazo.
Davide adamuuza kuti, “Usaope. Ndifuna kukuchitira chifundo chifukwa cha Yonatani bambo wako, ndipo ndidzakubwezera dera lonse la Saulo mbuyako. Udzadya nane pamodzi masiku onse.”
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Mulungu wopatsa mtendere, adaukitsa kwa akufa Ambuye athu Yesu, amene ndiye Mbusa wamkulu wa nkhosa, chifukwa cha imfa yake yotsimikizira Chipangano chamuyaya. Mulunguyo akupatseni zabwino zonse zimene mukusoŵa kuti muzichita zimene Iye afuna. Ndipo mwa Yesu Khristu achite mwa ife zomkondweretsa, Khristuyo akhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.
Apo mfumu idayankha kuti, “Kimuhamu ndiwoloka naye limodzi, ndipo ndidzamchitira chilichonse chimene chikukomereni inu. Ndipo zonse zimene mufuna kuti ndikuchitireni, ndidzakuchitirani.”
Atatero adagona tulo patsinde pa kamtengo ka tsache pomwepo. Mwadzidzidzi mngelo adamkhudza namuuza kuti, “Dzuka, udye.” Eliya atapenya, adangoona kuti kumutu kwake kuli buledi wootcha pa makala, ndiponso mkhate wa madzi. Adadya, namwera, nkugonanso. Mngelo wa Chauta uja adabweranso kachiŵiri, namkhudza nati, “Dzuka, udye kuti ulendowu ungakukanike.”
Ngwodala munthu amene amaganizirako za amphaŵi, popeza kuti Chauta adzapulumutsa munthu wotere pa tsiku lamavuto. Koma Inu Chauta, mundikomere mtima, mundichiritse kuti ndiŵalange anthuwo. Mukatero ndidzadziŵa kuti mumakondwera nane, chifukwa mdani wanga sadandipambane. Inu mwandichirikiza chifukwa cha kukhulupirika kwanga, mwandikhazika pamaso panu mpaka muyaya. Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele, kuyambira muyaya mpaka muyaya. Inde momwemo. Inde momwemo. Chauta adzamteteza ndi kumsunga ndi moyo. Adzatchedwa wodala pa dziko. Chauta sadzampereka kwa adani ake, kuti amchite zimene iwo akufuna. Chauta adzamthandiza munthuyo akamadwala. Adzamchiritsa matenda ake onse.
Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni. Chauta akuyang'aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima. Chauta akuyang'aneni mwachifundo, ndipo akupatseni mtendere.”
Anthu osiyidwa, Mulungu amaŵapatsa malo okhalamo, am'ndende amaŵatulutsa kuti akhale pa ufulu, koma anthu oukira, amaŵapirikitsira ku nthaka yoguga.
Inu tetezani anthu ofooka ndi amasiye mwachilungamo. Weruzani molungama ozunzika ndi amphaŵi. “Landitsani ofooka ndi osoŵa. Apulumutseni kwa anthu oipa.”
Pali abwenzi ena amene chibwenzi chao nchachiphamaso chabe, koma pali ena amene amakukangamira koposa mbale yemwe.
Kunyumba kwa mnzako uzipitako kamodzikamodzi, kuwopa kuti angatope nawe, nkuyamba kudana nawe.
Anthu anjala muziŵagaŵirako chakudya chanu, osoŵa pokhala muziŵapatsako malo. Mukaona wausiŵa, mpatseni chovala, musalephere kuthandiza amene ali abale anu.
Ankateteza anthu otsika ndi osauka, ndipo zonse zinkamuyendera bwino. Kodi zimenezi sizidaonetse kuti ankandidziŵa?” Akuterotu Chauta.
Zotayika ndidzazifunafuna, zosokera ndidzazibweza, zopweteka ndidzazimanga mabala ake. Zofooka ndidzazilimbikitsa, koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaŵeta nkhosa zanga mwachilungamo.”
Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akafuna kubwereka kanthu kwa iwe, usamkanize.”
Ndipo aliyense wopatsa ngakhale chikho cha madzi ozizira kwa mmodzi mwa ophunzira angaŵa, chifukwa chakuti ndi wophunzira wanga, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.”
Paja Ine ndidaali ndi njala, inu nkundipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu nkundipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu nkundilandira kunyumba kwanu. Ndidaali wamaliseche, inu nkundiveka. Ndinkadwala, inu nkumadzandizonda. Ndidaali m'ndende, inu nkumadzandichezetsa.’ Apo olungama aja adzati, ‘Ambuye, ndi liti tidaakuwonani muli ndi njala, ife nkukupatsani chakudya, kapena muli ndi ludzu, ife nkukupatsani chakumwa? Ndi liti tidaakuwonani muli mlendo, ife nkukulandirani kunyumba kwathu, kapena muli wamaliseche, ife nkukuvekani? Ndi liti tidaamvapo kuti mukudwala kapena kuti muli m'ndende, ife nkudzakuchezetsani?’ Koma asanu ochenjera aja adaatenga mafuta ena apadera m'nsupa zao. Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’
Lamulo lachiŵiri lake ndi ili, ‘Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.’ Palibe lamulo lina loposa malamulo ameneŵa.”
Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, adafikanso pamalo pomwepo. Pamene adaona munthu uja, adamumvera chisoni. Adabwera kwa wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa mabala ake, nkuŵamanga. Atatero adamkweza pa bulu wake, nkupita naye ku nyumba ya alendo, namsamalira bwino. M'maŵa mwake adatulutsa ndalama ziŵiri zasiliva, nazipereka kwa mwini nyumba ya alendoyo. Adamuuza kuti, ‘Msamalireni bwino, ndipo mukamwazanso ndalama zina, ndidzakubwezerani pobwera.’ ”
Yesu adauzanso Mfarisi uja amene adaamuitana kudzadya naye kuti, “Ukamakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamaitana abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anzako achuma, chifukwa mwina iwonso adzakuitanako, motero udzalandiriratu mphotho yako. Koma iwe ukamakonza phwando, uziitana amphaŵi, otsimphina, opunduka ndi akhungu. Apo udzakhala wodala, chifukwa iwo alibe kanthu koti nkukubwezera. Mulungu ndiye adzakubwezera, pamene anthu olungama adzauka kwa akufa.”
Tsono ngati Ine Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu ndakusambitsani mapazi anu, ndiye kuti inunso muyenera kumasambitsana mapazi. Ndakupatsani chitsanzo, kuti inunso muzichita monga momwe Ine ndakuchitirani inu.
Ku Yopa kunali wophunzira wina wamkazi, dzina lake Tabita (pa Chigriki amati Dorika). Iyeyu ankachita ntchito zabwino zambiri ndi kumathandiza osauka. Masiku amenewo maiyo adaadwala, nkumwalira. Anthu adatsuka maliro, nakagoneka mtembo m'chipinda cham'mwamba. Ku Yopa kunali kufupi ndi ku Lida, choncho pamene ophunzira adamva kuti Petro ali ku Lida, adatuma anthu aŵiri kuti akamuuze kuti, “Chonde, mubwere kwathu kuno msanga.” Tsono Petro adanyamuka napita nawo. Pamene iye adafika, adamperekeza ku chipinda cham'mwamba chija. Akazi onse amasiye adangoti kwete m'mbali mwakemu, akungolira, nkumamuwonetsa malaya ndi zovala zina zimene Dorika ankasoka ali nawo pamodzi.
Ku Kesareya kunali munthu wina, dzina lake Kornelio. Iyeyu anali mkulu wa asilikali 100 achiroma, a m'gulu lotchedwa “Gulu la ku Italiya.” Ali pamenepo, adamva njala, namafuna kudya. Koma pamene anthu ankakonza chakudya, iye adachita ngati wakomoka. Adaona kuthambo kutatsekuka, chinthu china chikutsikira pansi chooneka ngati chinsalu chachikulu chomangidwa pa nsonga zake zinai. M'menemo munali nyama zamitundumitundu, ndi zokwaŵa, ndiponso mbalame zamumlengalenga. Tsono Petro adamva mau akuti, “Petro dzuka, ipha udye.” Koma Petro adati, “Iyai, pepani Ambuye, ine sindinadyepo ndi kale lonse chinthu chosayera kapena chonyansa.” Kenaka Petro adamvanso kachiŵiri mau akuti, “Zimene Mulungu waziyeretsa, iwe usati nzosayera.” Zimenezi zidachitika katatu, ndipo pompo chinthu chija chidatengedwa kupitanso kumwamba. Petro adayamba kusinkhasinkha za tanthauzo la zimene adaaziwona m'masomphenya zija. Nthaŵi yomweyo anthu amene Kornelio adaaŵatuma aja, ankafunsa za nyumba ya Simoni, ndipo tsopano adaadzaima pa khomo. Adaitana nkufunsa kuti, “Kodi kuli mlendo kuno, dzina lake Simoni, wotchedwanso Petro?” Pamene Petro ankalingalirabe za zimene adaaziwona m'masomphenya zija, Mzimu Woyera adamuuza kuti, “Iwe, anthu atatu akukufuna. Anali munthu wotsata zachipembedzo, ndipo iye pamodzi ndi banja lake lonse ankaopa Mulungu. Ankathandiza kwambiri Ayuda osauka, ndipo ankapemphera Mulungu nthaŵi ndi nthaŵi.
Iye ndi a m'banja mwake atabatizidwa, iyeyo adatipempha kuti, “Ngati mwandiwonadi kuti ndine munthu wokhulupirira Ambuye, dzaloŵeni m'nyumba mwanga, mudzakhale nafe.” Mwakuti adatikakamiza ndithu, ife nkukaloŵadi.
Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa.
Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu, tiziŵalezera mtima anthu ofooka, osamangodzikondweretsa tokha. Akutinso, “Inu anthu a mitundu ina, kondwani pamodzi ndi anthu ake a Mulungu.” Ndiponso akuti, “Inu nonse a mitundu ina, tamandani Ambuye, anthu a mitundu yonse amtamande.” Nayenso mneneri Yesaya akuti, “Mmodzi mwa zidzukulu za Yese adzabwera. Iye adzadzambatuka kuti alamule anthu a mitundu ina, ndipo iwo adzaika chikhulupiriro chao pa Iyeyo.” Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Abale anga, ine mwini wake sindikayika konse kuti ndinu anthu a kufuna kwabwino ndithu, ndinu anthu odziŵa zinthu, ndipo mumatha kulangizana. Komabe m'kalata ino zina ndakulemberani mopanda mantha konse, kuti ndikukumbutseni zimenezo. Ndalemba motere popeza kuti Mulungu adandikomera mtima pakundipatula kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu a mitundu ina. Adandipatsa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu ngati wansembe, kuti anthuwo akhale ngati nsembe yokomera Iye ndi yoperekedwa mwa Mzimu Woyera. Tsono pokhala ndine wake wa Khristu Yesu, ndikunyadira ntchito imene ndikugwirira Mulungu. Sindidzalimba mtima kulankhula za kanthu kena ai, koma zokhazo zimene ndimachita kudzera mwa Khristu, kuti ndithandize anthu a mitundu ina kumvera. Zimenezi ndidazichita ndi mau anga ndi ntchito zanga, ndi zizindikiro ndi zozizwitsa zamphamvu zochitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Motero Uthenga Wabwino wonena za Khristu ndidaulalika kwathunthu ku Yerusalemu ndi ku dziko lozungulira mpaka ku Iliriko. Aliyense mwa ife azikondweretsa mnzake, ndi kumchitira zabwino, kuti alimbikitse chikhulupiriro chake.
Adachita zimenezi kuti pasakhale kugaŵikana m'thupi, koma kuti ziwalo zonse zizisamalirana. Chiwalo chimodzi chikamamva kuŵaŵa, ziwalo zonse zimamvanso kuŵaŵa. Chiwalo chimodzi chikamalandira ulemu, ziwalo zonse zimakondwa nao.
Zoonadi ntchito imeneyi yomwe mukuchitira anthu a Mulungu, siingoŵathandiza pa zosoŵa zao, komanso chotsatira chake china nchakuti anthu ochuluka adzathokoza Mulungu kwambiri. Pakuti ntchito imeneyi ikuŵatsimikizira kuti chifundo chanu nchoona, iwo adzatamanda Mulungu chifukwa cha kumvera kwanu povomereza Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Adzatero chifukwanso cha ufulu wanu poŵagaŵirako iwowo ndi anthu ena onse zinthu zimene muli nazo.
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
Nchifukwa chake tsono, nthaŵi zonse tikapeza mpata, tizichitira anthu onse zabwino, makamaka abale athu achikhristu.
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.
Abale, tikukupemphani kuti anthu amene amangokhala osafuna kugwira ntchito muziŵadzudzula, anthu otaya mtima muziŵalimbikitsa. Anthu ofooka muziŵathandiza, anthu onsewo muziŵalezera mtima.
Akhale mai woti anthu amamchitira umboni wakuti amachitadi ntchito zabwino. Akhale woti ankalera ana ake bwino, ankalandira bwino alendo, ankasambitsa mapazi a anthu a Mulungu, ndipo ankathandiza anthu amene anali m'mavuto. Akhalenso mai woti ankadzipereka pa ntchito zonse zabwino.
Anthu athunso aziphunzira kudzipereka pa ntchito zabwino, kuti azithandiza pamene pali kusoŵa kwenikweni. Azitero kuti moyo wao usakhale wopanda phindu.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Pitirizani kukondana monga abale. Ife tili ndi guwa, ndipo ansembe otumikira m'chihema chachipembedzo cha Ayuda saloledwa kudyako zoperekedwa pamenepo. Mkulu wa ansembe wachiyuda amaloŵa ndi magazi a nyama ku Malo Opatulika kuti magaziwo akhale nsembe yopepesera machimo. Koma nyama yeniyeniyo amaiwotchera kunja kwa misasa. Chifukwa cha chimenechi, Yesu nayenso adafera kunja kwa mzinda, kuti pakutero ayeretse anthu ndi magazi ake. Tiyeni tsono tipite kwa Iye kunja kwa misasa kuti tikanyozekere naye limodzi. Paja ife tilibe mzinda wokhazikika pansi pano, tikufunafuna wina umene ulikudza. Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera. Musanyozere kumachita zachifundo ndi kumathandizana, chifukwa nsembe zotere zimakondweretsa Mulungu. Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe. Muzitipempherera ifeyo, pakuti sitipeneka konse kuti tili ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndipo tatsimikiza kuchita zonse mwachilungamo. Ndikukupemphani makamaka kuti mupemphere kuti Mulungu andibwezere kwa inu msanga. Musanyozere kumalandira bwino alendo m'nyumba mwanu. Pali ena amene kale adaalandira bwino alendo, ndipo mosazindikira adaalandira angelo.
Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi.
Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake? Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.
Chauta adzaona kuti cholinga chake pa ine chichitikedi. Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
Usaleke kumchitira zabwino woyenera kuzilandira, pamene uli nazo mphamvu zochitira choncho. Usamuuze mnzakoyo kuti, “Pita, ukachite kubweranso, ndidzakupatsa maŵa,” pamene uli nazo tsopano lino.
Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.
Pansi pano chinthu chilichonse chili ndi nyengo yake ndi nthaŵi yake yomwe adaika Mulungu:
Aŵiriwo akagwa, wina adzautsa mnzake. Koma tsoka amene ali yekha: akagwa, ndiye kuti zavuta, chifukwa palibe wina womuutsa.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Pamene adaona makamu a anthu, adaŵamvera chifundo, chifukwa iwo anali olema ndi ovutika ngati nkhosa zopanda mbusa.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Iye sadzatsiriza bango lothyoka, nyale yofuka sadzaizimitsa, mpaka atapambanitsa chilungamo.
“Mbale wako akakuchimwira, pita ukamdzudzule muli aŵiri nokha. Akakumvera, wamkonza mbale wakoyo. Koma akapanda kukumvera, utengerepo wina mmodzi kapena ena aŵiri, kuti mau onse akatsimikizike ndi mboni ziŵiri kapena zitatu. Akapanda kuŵamvera iwowo, ukauze Mpingo. Ndipo akapanda kumveranso ndi Mpingo womwe, umuyese munthu wakunja kapena wokhometsa msonkho.
“Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa,
Lamulo langa ndi lakuti muzikondana monga momwe Ine ndakukonderani. Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagaŵana zinthu zao. Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagaŵira onse, malinga ndi kusoŵa kwa aliyense.
Gulu lonse la okhulupirira linali la mtima umodzi, ndi la maganizo amodzi. Panalibe munthu amene ankati, “Zimene ndiri nazo nzangazanga,” koma aliyense ankapereka zake zonse kuti zikhale za onse. Atumwi ankachita umboni ndi mphamvu yaikulu kuti Ambuye Yesu adaukadi kwa akufa, ndipo onse Mulungu ankaŵakomera mtima kwambiri. Panalibe munthu wosoŵa kanthu pakati pao, chifukwa onse amene anali ndi minda kapena nyumba, ankazigulitsa, namabwera ndi ndalama zake kudzazipereka kwa atumwi. Ndipo ndalamazo ankagaŵira munthu aliyense malinga ndi kusoŵa kwake.
Ndikupereka m'manja mwanu Febe, mlongo wathu, amene ali mtumiki wa mpingo wa ku Kenkrea. Moni kwa Apelesi, mkhristu wolimba uja. Moni kwa a m'banja la Aristobulo. Moni kwa Herodiono, Myuda mnzanga. Moni kwa akhristu a m'banja la Narkiso. Moni kwa Trifena ndi Trifosa, amene amagwira mwamphamvu ntchito ya Ambuye. Moni kwa Perisi, wokondedwa uja, amene wachita zambiri pogwirira Ambuye ntchito. Moni kwa Rufu, wotchuka pa ntchito ya Ambuye. Moninso kwa mai wake amene ali ngati mai wanganso. Moni kwa Asinkrito, Filegoni, Heremesi, Patrobasi, Herimasi ndi abale onse amene ali nawo pamodzi. Moni kwa Filologo ndi Juliya, kwa Nereo ndi mlongo wake, kwa Olimpasi ndi kwa anthu onse a Mulungu amene ali nawo pamodzi. Mupatsane moni mwa chikondi choona. Mipingo yonse yachikhristu ikukupatsani moni. Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa, pakuti anthu otere satumikira Khristu Ambuye athu, koma amangotumikira zilakolako zao basi. Ndi mau okoma ndi oshashalika amanyenga anthu a mitima yoona. Anthu onse adaimva mbiri ya kumvera kwanu. Tsono ine ndikunyadira inuyo, koma ndifuna kuti mukhale anzeru pa zabwino, ndi othaŵa zoipa. Mlandireni m'dzina la Ambuye, monga momwe anthu a Mulungu ayenera kulandirirana. Mumthandize monga momwe angasoŵere chithandizo chanu, pakuti iyeyo adathandiza anthu ambiri, ine ndemwenso adandithandizako.
Popanda wina aliyense woŵakakamiza adatipempha, natiwumiriza kuti tiŵapatse mwai woti nawonso athandize anthu a Mulungu a ku Yudeya.
Aliyense apereke monga momwe adatsimikiziratu mumtima mwake, osati ndi chisoni kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwa.
Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani. Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu. Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa. Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano.
Inu Afilipi, mukudziŵa inu nomwe kuti pamene ndidachoka ku Masedoniya, masiku oyamba aja akulalika Uthenga Wabwino, panalibe mpingo wina wogwirizana nane pa zoyenera kulipira kapena kulandira, koma inu nokha. Pamene ndinali ku Tesalonika, mudatumiza kangapo zondithandiza pa zosoŵa zanga.
Timathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu nonse ndi kumakutchulani m'mapemphero athu. Timakumbukira kosalekeza pamaso pa Mulungu Atate athu za m'mene mumatsimikizira chikhulupiriro chanu mwa ntchito zanu, za m'mene chikondi chanu chimakuthandizirani kugwira ntchito kolimba, ndiponso za m'mene mumachitira khama poyembekeza Ambuye athu Yesu Khristu.
Tiyenera kuthokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale. Nkoyeneradi kutero, chifukwa chikhulupiriro chanu chikunka chikukulirakulira kwambiri pamodzi ndi kukondana kwanu pakati pa inu nonse.
Kwenikweni muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku ikadalipo nthaŵi, imene m'mau a Mulungu imatchedwa kuti, “Lero”. Muzichita zimenezi, kuwopa kuti wina aliyense mwa inu angaumitsidwe mtima ndi chinyengo cha uchimo.
Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.
Wopondereza mmphaŵi, amachita chipongwe Mlengi wake, koma wochitira chifundo osauka, amalemekeza Mlengi wake.
Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.
mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’
Tsono Yesu adafunsa katswiri wa Malamulo uja kuti, “Inu pamenepa mukuganiza bwanji? Mwa anthu atatuŵa, ndani adakhala ngati mnzake wa munthu uja achifwamba adaamugwirayu?” Iye adati, “Amene adamchitira chifundo uja.” Apo Yesu adamuuza kuti, “Pitani tsono, nanunso muzikachita chimodzimodzi.”
Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana. Mukamakondana, anthu onse adzadziŵa kuti ndinudi ophunzira anga.”
Ku Yopa kunali wophunzira wina wamkazi, dzina lake Tabita (pa Chigriki amati Dorika). Iyeyu ankachita ntchito zabwino zambiri ndi kumathandiza osauka.
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.
Mayendedwe anu pakati pa anthu akunja azikhala anzeru, ndipo muzichita changu, osataya nthaŵi pachabe.
Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao.
Paja Iye adadzipereka chifukwa cha ife, kuti atipulumutse ku zoipa zathu zonse, ndi kutiyeretsa kuti tikhale anthu ake achangu pa ntchito zonse zabwino.
Musanyozere kumachita zachifundo ndi kumathandizana, chifukwa nsembe zotere zimakondweretsa Mulungu.
Mwachitsanzo: mbale wina kapena mlongo ali ndi usiŵa, ndipo masiku onse alibe chakudya chokwanira. Tsono wina mwa inu angoŵauza kuti. “Pitani ndi mtendere, mukafundidwe ndipo mukakhute”, koma osaŵapatsa zimene akusoŵazo, pamenepo phindu lake nchiyani?
Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.
Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.
Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la atate ako. Usachite kupita ku nyumba ya mbale wake, ukakhala pa mavuto. Mnzako wokhala naye pafupi amaposa mbale wako wokhala kutali.
Paja Ine ndidaali ndi njala, inu nkundipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu nkundipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu nkundilandira kunyumba kwanu.
Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.