Ndikufuna kukuuzani kuti kusunga mavesi a m’Baibulo ndi njira yabwino kwambiri yokuthandizani kukhala okonzeka ndi Mawu a Mulungu nthawi zonse, zivute zitani. Mukasunga mavesi amenewa, mumakhala ngati mukunyamula Baibulo mumtima mwanu.
Tangoganizani, mukuthandiza mnzanu amene akukumana ndi mavuto, ndipo mwadzidzidzi mukukumbukira vesi lonena za chikondi cha Mulungu! Kapena mwina mukudikirira kwinakwake, ndipo vesi lonena za kuleza mtima likubwera mumtima mwanu. Zimathandiza kwambiri!
Ngati tsiku lililonse mungalongosole nthawi yochepa yokumbukira mavesi a m’Baibulo, mudzapeza kuti n’kosavuta kukumbukira Mawu a Mulungu pamene mukuwafuna. Monga momwe lemba la Yoswa 1:8 limanenera, “Buku la malamulo awa lisachoke pakamwa pako, koma uziliganizire usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwa m’menemo; pakuti pamenepo uzikitsa njira yako, ndipo pamenepo uzichita mwanzeru.”
Ndi oti wanzeru akaŵamva, aonjezere kuphunzira kwake, ndipo munthu womvetsa zinthu apate luso,
Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.
Chitetezo cha nzeru chili ngati chitetezo cha ndalama. Koma kudziŵa zinthu kukuposerapo, chifukwa nzeru zimasunga moyo wa amene ali nazo.
Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
Wanzeru ukamlangiza, adzakhala wanzeru koposa. Munthu wochita chilungamo ukamuphunzitsa, adzadziŵa zambiri koposa.
Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.
Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa.
Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru.
Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Pajatu chimene chimaoneka ngati kupusa kwa Mulungu, nchanzeru kupambana nzeru za anthu. Ndipo chimene chimaoneka ngati kufooka kwa Mulungu, nchamphamvu kupambana mphamvu za anthu.
Iwo akuti, “Kodi munthu ameneyu akuti aphunzitse yani? Kodi uthengawo akuti afotokozere yani? Kodi ndife ana ongoleka kumene kuyamwa, kapena makanda ongoŵachotsa kumene kubere?
Muzichita zimene mudaphunzira ndi kulandira kwa ine, ndiponso zimene mudamva kwa ine ndi kuwonera kwa ine. Pamenepo Mulungu amene amapatsa mtendere adzakhala nanu.
Mtima wa munthu womvetsa zinthu umafunitsitsa ndithu kudziŵa zambiri, koma m'kamwa mwa anthu opusa zauchitsiru zili pha!
Lija nkale mukadayenera kukhala ophunzitsa anzanu, komabe nkofunika kuti wina akuphunzitseninso maphunziro oyamba enieni a mau a Mulungu. Nkofunikanso kukumwetsani mkaka, m'malo mwa kukupatsani chakudya cholimba. Ngati wina aliyense angomwa mkaka, ndiye kuti akali mwana wakhanda, sangathe kutsata chiphunzitso chofotokoza za chilungamo. Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima. Pakugwiritsa ntchito nzeru zao, iwoŵa adadzizoloŵeza kusiyanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa.
Mwana wanga, uchenjere ndi kalikonse kobzola pamenepa. Kulemba mabuku sikutha, ndipo kuphunzira kwambiri kumatopetsa thupi.
Choncho adauza munthu kuti, ‘Kuwopa Ambuye ndiye nzeru zimenezo, kuthaŵa zoipa ndiye luntha limenelo.’ ” Yobe
Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.
Koma mukule m'chifundo ndi m'nzeru za Yesu Khristu, Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu. Iye akhale ndi ulemerero tsopano ndi mpaka muyaya. Amen.
Pamenepo mudzatha kuyenda m'njira zimene Ambuye amafuna, ndi kuŵakondweretsa pa zonse. Pakugwira ntchito zabwino zamitundumitundu, moyo wanu udzaonetsa zipatso, ndipo mudzanka muwonjezerawonjezera nzeru zanu za kudziŵa Mulungu.
Kupata nzeru kumapambana kupata golide. Kumvetsa zinthu nkwabwino, kumapambana kukhala ndi siliva.
Malamulo a pakamwa panu amandikomera kuposa ndalama zikwizikwi zagolide ndi zasiliva.
Kodi sudziŵa? Kodi sudamve? Chauta ndiye Mulungu wachikhalire, Mlengi wa dziko lonse lapansi. Satopa kapena kufooka, palibe amene amadziŵa maganizo ake. Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu. Kukumveka mau akuti, “Konzani njira ya Chauta m'thengo, lungamitsani mseu wa Mulungu wathu m'chipululu. Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufooka, ngakhale anyamata amaphunthwa ndi kugwa. Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba.
Kunena za anthu, ndinkalingaliranso kuti, “Mulungu amaŵayesa ndi cholinga choti aŵaonetse kuti iwowo sasiyana konse ndi nyama. Zimene zimachitikira anthu, zomwezonso zimachitikira nyama. Monga chinacho chimafa, chinacho chimafanso. Zonsezo zimapuma mpweya umodzimodzi, munthu saposa nyama. Zonsezi nzopandapake.
Mau a Chauta ngangwiro, amapatsa munthu moyo watsopano. Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika, umaŵapatsa nzeru amene alibe. Malangizo a Chauta ndi olungama, amasangalatsa mtima. Malamulo a Chauta ndi olungama, amapatsa mtima womvetsa.
Munthu wanzeru ndi wamphamvu kupambana munthu wa nyonga zambiri, munthu wophunzira amaposa munthu wamphamvu.
Woyenda ndi anthu anzeru nayenso amakhala ndi nzeru, koma woyenda ndi zitsiru adzaonongeka.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu. Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.
mau anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Amatsekemera kuposa uchi m'kamwa mwanga.
Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.
Phunzirani kuchita zabwino. Funafunani chilungamo, opsinjidwa muŵathandize. Tetezani ana amasiye, muŵaimirire pa milandu yao akazi amasiye.”
Munthu wabwino amalankhula zanzeru, pakamwa pake pamatuluka zachilungamo. Malamulo a Mulungu amakhala mumtima mwake, motero sagwedezeka poyenda m'moyo uno.
Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
ndipo ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate aulemerero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatsani nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziŵe kwenikweni.
Koma nzeru zochokera Kumwamba, poyamba nzangwiro, kuwonjeza apo nzamtendere, zofatsa ndi zomvera bwino. Ndi za chifundo chambiri, ndipo zipatso zake zabwino nzochuluka. Nzeruzo sizikondera kapena kuchita chiphamaso.
Ntchito zimenezi uzizichita mosamala ndi modzipereka, kuti anthu onse aone kuti moyo wako wautumiki ukukulirakulira.
Wa mtima wanzeru amamutcha wozindikira bwino zinthu, kulankhula kwake kokometsera kumakulitsa mphamvu ya mau ake.
Sitifuna kuti mukhale aulesi, koma kuti mutsanzire anthu amene, pakukhulupirira ndi pakupirira, akulandira zimene Mulungu adalonjeza.
Pali golide ndi miyala yambirimbiri yamtengowapatali, koma mau olankhula zanzeru ali ndi mtengo woposa zonsezo.
Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga.
Abale anga, ine mwini wake sindikayika konse kuti ndinu anthu a kufuna kwabwino ndithu, ndinu anthu odziŵa zinthu, ndipo mumatha kulangizana.
Popanda uphungu zolinga zako zimalakwika, koma aphungu akachuluka, zolinga zako zimathekadi.
Ife sitidalandire mzimu wa dziko lino lapansi, koma tidalandira Mzimu Woyera wochokera kwa Mulungu, kuti adzatithandize kumvetsa zimene Mulunguyo adatipatsa mwaulere.
ndiponso kudzikuza kulikonse koletsa anthu kudziŵa Mulungu. Timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.
Landirani malangizo anga m'malo mwa siliva, funitsitsani kudziŵa zinthu, osati kuthamangira golide wabwino kwambiri. Nzerutu ndi yabwino kuposa miyala yamtengowapatali. Zonse zimene ungazilakelake sizingafanefane ndi nzeru.
Koma inu, Khristu adakudzozani ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa inu, ndipo sipafunikanso wina woti akuphunzitseni. Mzimu Woyerayo, amene mudadzozedwa naye, amakuphunzitsani zonse. Zimene amakuphunzitsani nzoona, si zonama ai. Nchifukwa chake, monga momwe adakuphunzitsirani, khalani mwa Khristu.
Maso a anthu openya sadzakhalanso otseka, ndipo makutu a anthu akumva adzakhala otchera. Anthu a mtima waphamphu adzadziŵa kuchita zinthu moganiza bwino, ndipo anthu achibwibwi adzalankhula mosadodoma ndi momveka.
Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao.
Munthu wolungama angathe kundimenya kapena kundidzudzula chifukwa andimvera chifundo, koma ndisalandire ulemu kwa anthu oipa, pakuti ndimapemphera motsutsana ndi ntchito zao zoipa.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.
Ndikutitu upemphe mtima wozindikira zinthu, ndi kupemba kuti ukhale womvetsa zinthu. Uziifunafuna nzeruyo ngati siliva, ndi kumaiwunguza ngati chuma chobisika. Ukatero, udzamvetsa za kuwopa Chauta, udzapeza nzeru za kudziŵa Mulungu.
Ngwodala munthu amene chithandizo chake chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe, munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake.
Iwe Timoteo, usunge bwino zimene adakusungitsa. Upewe nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, ndiponso maganizo otsutsana, amene anthu amanama kuti ndi nzeru zodziŵa zinthu. Anthu ena, chifukwa chovomereza nzeru zotere, adasokera nkutaya chikhulupiriro chao. Mulungu akukomere mtima.
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
Ndikukupemphani ndi mtima wanga wonse, mundikomere mtima molingana ndi malonjezo anu aja.
Pajatu chilengedwere cha dziko lapansi anthu akhala akuzindikira makhalidwe osaoneka a Mulungu, ndiye kuti mphamvu zake zosatha, ndiponso umulungu wake. Akhala akuzizindikira poona zimene Mulungu adalenga. Choncho alibe konse pozembera.
Mkwapulo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru, koma mwana womamlekerera amachititsa amake manyazi.
Paja nzeru zambiri zimadzetsa chisoni chambiri, munthu akamaonjezera nzeru, ndiye kuti akuwonjezeranso chisoni.
Munthu wopusa amakhulupirira chilichonse, koma wochenjera amayang'ana m'mene akuyendera.
Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.
Motero munthu amakhulupirira chifukwa cha zimene wamva, ndipo zimene wamvazo zimachokera ku zolalika za Khristu.
Ndimasinkhasinkha mumtima mwanga usiku. Ndimadzifunsa ndi kufufuzafufuza mumtima mwanga.
Tsono musadzinyenge. Ngati wina mwa inu adziyesa wanzeru, kunena za nzeru za masiku ano, ameneyo ayambe wakhala ngati wopusa, kuti asanduke wanzeru. Zoonadi nzeru za anthu odalira zapansipano, nzopusa pamaso pa Mulungu. Pajatu Malembo akuti, “Mulungu amakola anthu anzeru m'kuchenjera kwao.”
Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse ndi mphamvu zanu zonse.
Iye adayankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathe kukugonjetsa iwe Yoswa, nthaŵi yonse ya moyo wako. Ine ndidzakhala nawe monga momwe ndidakhalira ndi Mose, sindidzakusiya konse.
ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao.
Motero zidachitikadi zimene Malembo adaanena, kuti, “Abrahamu adakhulupirira Mulungu, nchifukwa chake Mulungu adamuwona kuti ngwolungama;” mwakuti ankatchedwa bwenzi la Mulungu.
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, ndi mtima wanga wonse. Ndidzasimba za ntchito zanu zonse zodabwitsa.
Koma Yesu adati, “Malembo akuti, “ ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mau onse olankhula Mulungu.’ ”
Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera.