Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


208 Mau a m'Baibulo Okhudza Ufiti ndi Zamatsenga

208 Mau a m'Baibulo Okhudza Ufiti ndi Zamatsenga


Deuteronomo 12:3

Mukagwetse maguwa ao, ndipo miyala yao yoimiritsa, imene amaiyesa yopembedzerapo, mukaiphwanyephwanye. Mukatenthe mafano ao a Aserimu. Mukaonongenso mafano ao ofanizira milungu yao, ndipo mukafafanize ndi dzina lomwe la milunguyo konsekonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:36

Adatumikira mafano ao amene adasanduka msampha kwa iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 46:5-7

“Kodi Ine mungandifanizire ndi yani, kapena kundilinganiza ndi yani? Kodi mungandiyerekeze ndi yani, kuti Ine ndi iyeyo tikhale ofanana? Anthu ena amatsekula zikwama zao namatulutsamo golide, ndipo amayesa siliva pa masikelo. Amalemba mmisiri wosula, ndipo iye amaŵapangira milungu. Kenaka iwowo amagwada pansi, namaipembedza milunguyo. Amainyamula pa mapewa ao, naisenza. Amaikhazika pamalo pake nikhala pomwepo, ndipo singathe kusuntha pamalo pakepo. Wina aliyense akapemphera kwa milunguyo, siyankha, kapena kumpulumutsa ku mavuto ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:8

Kale simunkadziŵa Mulungu, nchifukwa chake munkatumikira zomwe sizili milungu konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 11:16

Chenjerani, musasokeretsedwe ndi kutembenukira kwa milungu ina, kuti muziipembedza ndi kuitumikira,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:13

Mumvetse zonse zimene ndakuuzanizi. Musamapemphera kwa milungu ina, ndi maina ake omwe musamaŵatchula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:22-23

Iwo amadziyesa anzeru, koma chikhalirecho ndi opusa. Adaleka kulemekeza Mulungu wosafa, nkumapembedza mafano ooneka ngati munthu amene amafa, kapena ngati mbalame ndi nyama zina, kapena zokwaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:14

Musadzapembedze mulungu wina aliyense, chifukwa Chauta amene dzina lake ndi Kansanje, ndi Mulungu wansanjedi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:20-21

Iyai, koma kuti zimene anthu akunja amapereka nsembe, amapereka kwa Satana, osati kwa Mulungu. Sindifuna kuti inu muyanjane ndi Satana. Simungathe kumwera m'chikho cha Ambuye nkumweranso m'chikho cha Satana. Simungathe kudyera pa tebulo la Ambuye nkudyeranso pa tebulo la Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:4-7

Koma mafano ao ndi asiliva ndi agolide, opangidwa ndi manja a anthu. Pakamwa ali napo, koma salankhula. Maso ali nawo, koma sapenya. Makutu ali nawo, koma saamva. Mphuno ali nazo, koma sanunkhiza. Manja ali nawo, koma akakhudza, samva kanthu. Miyendo ali nayo, koma sayenda, ndipo satulutsa ndi liwu lomwe kukhosi kwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 11:14-15

Zimenezitu si zododometsa ai, pakuti Satana yemwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati mngelo wounikira anthu. Motero si chodabwitsa ngati atumiki ake omwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati otumikira chilungamo. Potsiriza adzalandira molingana ndi zimene ankachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:3-5

“Usakhale ndi milungu ina, koma Ine ndekha. “Usadzipangire fano kapena chithunzi chilichonse chofanizira kanthu kena kalikonse kakumwamba kapena ka pa dziko lapansi, kapenanso ka m'madzi a pansi pa dziko. Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 4:23-24

Samalani bwino, musaiŵale chipangano chimene Chauta, Mulungu wanu, adachita nanu, ndipo musapange fano lofanizira chinthu chilichonse chimene Chauta, Mulungu wanu, adakuletsani. Paja Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wansanje, salola kuti wina apikisane naye. Ali ngati moto waukali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 97:7

Onse opembedza milungu yonama, amene amanyadira mafano achabechabe, amachititsidwa manyazi, pakuti milungu ina yonse imagonjera Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 42:8

Ine ndine Chauta, dzina langa nlimenelo. Ulemerero wanga sindidzapatsa wina aliyense. Mayamiko oyenera Ine, sindidzalola kuti mafano alandireko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 135:15-18

Mafano a mitundu ina ya anthu ndi asiliva ndi agolide chabe, ndi opangidwa ndi manja a anthu. Pakamwa ali napo, koma salankhula, maso ali nawo, koma sapenya. Makutu ali nawo, koma saamva, ndipo alibe mpweya m'kamwa mwao. Anthu amene amapanga mafanowo afanefane nawo, chimodzimodzi onse amene amaŵakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:8

Anthu amene amapanga mafanowo amafanafana nawo, chimodzimodzi onse amene amaŵakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 51:17-18

Anthu onse ndi opusa, alibe nzeru. Mmisiri aliyense wosula amachita manyazi ndi mafano ake. Mafano amene amapangawo ngabodza, mwa iwo mulibe konse moyo. Mafanowo ngachabechabe, oyenera kuŵaseka, ndipo pamene anthuwo adzalangidwe, mafanowo adzaonongedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 45:20

Chauta akuti, “Musonkhane pamodzi ndipo mubwere. Musendere pafupi, inu nonse amene mudapulumuka kwa anthu a mitundu ina! Ndi opanda nzeru amene amanyamula mafano amitengo, namapemphera kwa milungu imene singathe kuŵapulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 10:3-5

Ndithudi, miyambo ya anthu a mitundu inayo nzopanda pake. Iwo aja amakadula mtengo ku nkhalango, munthu waluso namausema ndi nsompho. Anthu ena amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide, kenaka nkuchikhomerera ndi misomali, kuti chisagwedezeke. Mafano aowo ali ngati kangamunthu woopsera mbalame m'munda wa minkhaka, sangathe nkulankhula komwe. Ayenera kuŵanyamula, poti sangayende okha. Musaŵaope, chifukwa sangakuchiteni choipa. Alibenso mphamvu zochitira zabwino.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Habakuku 2:18

Kodi phindu la fano nchiyani? Adalipanga ndi munthu. Ndi chifanizo chabe, ndipo nchinthu chonyenga. Munthu wopangayo amakhulupirira zimene wachita, koma mafano akewo satha nkulankhula komwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:26

“Musadye nyama yamagazi. Musamaombeza kapena kuchita zaufiti.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 10:13-14

Choncho Saulo adafa chifukwa cha kusakhulupirika kwake. Iyeyo anali wosakhulupirika kwa Chauta, poti sankamvera mau a Chauta ndiponso ankapempha nzeru kwa anthu olankhula ndi mizimu, ndipo sankafuna kuti Chauta amutsogolere. Nchifukwa chake Chautayo adamupha napereka ufumu kwa Davide mwana wa Yese.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 21:6

Pambuyo pake adapereka mwana wake wamwamuna ngati nsembe. Ankatama mizimu mopemba ndiponso ankaombeza maula, namachita zobwebwetetsa ndi zaufiti. Adachita zoipa zambiri zimene zidakwiyitsa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 5:12

Ndidzasakaza masenga anu onse, ndipo pakati panu sipadzakhalanso oombeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:18

“Munthu wamkazi wochita zaufiti, musamlole kuti akhale moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 18:10-12

Pakati panu pasadzapezeke wopereka mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pa moto ngati nsembe. Pasaoneke munthu woombeza kapena woyeseza kulosa zam'tsogolo, kapena wogwiritsa ntchito nyanga kapena zithumwa. Pasapezekenso munthu wopempha nzeru kwa mizimu ya anthu akufa. Chauta, Mulungu wanu, amadana nawo anthu ochita zoipa zimenezi. Chimene Mulungu akupirikitsira anthuŵa pamene inu mukufika ndi chifukwa chakuti anthuwo ankachita zoipa zoterezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 47:12-14

Khala nazo nyanga zako ndi matsenga ako. Wakhala ukuzigwiritsa ntchito chiyambire cha ubwana wako. Mwina mwake zingakuthandize kapena nkuwopsa nazo adani ako. Udangodzitopetsa nako kupempha malangizo ambiri. Nabwere okulangizawo kuti adzakupulumutse. Abweretu anthu amene amaphunzira zakumlengalenga, namayang'ana nyenyezi, amenenso amati mwezi ukakhala nkumalosa zimene zidzakuchitikira. “Taona, anthuwo ali ngati mapesi, adzapsa ndi moto. Sangathe kudzipulumutsa ku mphamvu ya malaŵi ake. Moto wake si woti nkuwotha kapena kusendera pafupi nawo ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 20:27

“Mwamuna kapena mkazi wolankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena munthu wanyanga, ayenera kuphedwa. Aŵaponye miyala, ndipo magazi ao akhale pa iwowo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 20:6

“Munthu akapita kwa wolankhula ndi mizimu yoipa ndi kwa wanyanga, nadziipitsa pakutsatira iwowo, ndidzamfulatira ndipo ndidzamchotsa pakati pa anthu anzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 33:6

Ndipo adapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza. Adachita zimenezi ku chigwa cha mwana wa Hinomu, ndipo ankachita zobwebwetetsa, namasamala zamalodza ndi zanyanga, nkumamvana ndi anthu olankhula ndi mizimu ndi anthu amatsenga. Adachita zoipa zambiri pamaso pa Chauta, naputa mkwiyo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-21

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:8

Koma anthu amantha, osakhulupirika, okonda zonyansa, opha anzao, ochita zadama, ochita zaufiti, opembedza mafano, ndi anthu onse onama, malo ao ndi m'nyanja yodzaza ndi moto ndi miyala ya sulufure woyaka. Imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 22:15

Koma ochita zautchisi, zaufiti, zadama, zopha anzao, zopembedza mafano, ndi okonda zabodza nkumazichita, adzakhala kunja kwa mzindawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 27:9

“Nchifukwa chake musaŵamvere aneneri anu, oombeza anu, otanthauza maloto, amaula ndi amatsenga anu, akamakuuzani kuti musadzatumikire mfumu ya ku Babiloni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:16-18

Nthaŵi ina pamene tinkapita ku malo opemphererako, tidakumana ndi kapolo wachitsikana amene adaagwidwa ndi mzimu woipa womunenetsa zakutsogolo. Ankapindulitsa mbuye wake kwambiri ndi kulosa kwakeko. Iyeyo adayamba kutitsatira Paulo ndi ife, akufuula kuti, “Anthu aŵa ndi atumiki a Mulungu Wopambanazonse, akukulalikirani njira ya chipulumutso.” Mtsikanayo adachita zimenezi masiku ambiri. Koma Paulo zimenezo zidamunyansa, choncho adatembenuka nauza mzimu woipa uja kuti, “Iwe, m'dzina la Yesu Khristu ndikukulamula kuti utuluke mwa munthuyu.” Ndipo nthaŵi yomweyo udatulukadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:31

“Musamapita kwa anthu olankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena kwa anyanga. Musaŵafunefune kuti angakuipitseni. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 41:8

Kutacha m'maŵa adavutika kwambiri, mwakuti adaitana amatsenga ake onse ndi anthu anzeru onse a ku Ejipito. Onsewo atabwera, Farao adaŵafotokozera maloto akewo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe amene adatha kuŵamasula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 28:7-9

Pamenepo Saulo adauza nduna zake kuti, “Mundifunire mkazi wolankhula ndi mizimu kuti ndipite kwa iyeyo, ndikapemphe nzeru.” Ndunazo zidamuuza kuti, “Ku Endori aliko mkazi wolankhula ndi mizimu.” Tsono Saulo adadzizimbaitsa, navala zovala zachilendo, napita. Pamodzi ndi anthu aŵiri adakafika kwa mkaziyo usiku. Ndipo adamuuza kuti, “Undifunsire zam'tsogolo kwa mizimu, makamaka undiitanire mzimu wa amene ndimtchule.” Mkaziyo adati, “Inutu mukudziŵa zimene adachita mfumu Saulo. Suja adachotsa m'dziko muno anthu olankhula ndi mizimu ndiponso oombeza? Chifukwa chiyani tsono mukunditchera msampha kuti mundiphe?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:43-45

“Mzimu woipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo opanda madzi, kufunafuna malo opumulirako, koma osaŵapeza. Ndiye umati, ‘Ndibwerera kunyumba kwanga komwe ndidatuluka kuja.’ Tsono ukafika, umapeza m'nyumba muja muli zii, mosesasesa ndi mokonza bwino. Pamenepo umakatenga mizimu ina isanu ndi iŵiri yoipa koposa uwowo, kenaka yonseyo imaloŵa nkukhazikika momwemo. Choncho mkhalidwe wotsiriza wa munthu uja umaipa koposa mkhalidwe wake woyamba. Zidzateronso ndi anthu ochimwa amakono.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 4:12

Anthu anga amapempha nzeru ku fano lamtengo, ndipo amaombeza ndi ndodo yao. Mzimu wonyansa waasokeretsa, motero posiya Mulungu wao, akhala osakhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:18-19

Ambiri amene tsopano adaayamba kukhulupirira, adabwera nkumavomera poyera ndi kuulula zoipa zimene ankachita. Ambiri amene ankakonda kuchita matsenga, adasonkhanitsa mabuku ao naŵatentha pamaso pa anthu onse. Pamene adaonkhetsa mtengo wa mabukuwo, adapeza kuti udaakwanira ngati ndalama zikwi makumi asanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 23:23

Zanyanga sizingamchite kanthu Yakobe, zamaula sizingathe kulimbana ndi Israele. Tsono anthu polankhula za Yakobe ndi za Israele adzati, ‘Onani zimene Mulungu wachita.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:25

Ndine amene ndimalepheretsa mipingu ya anthu onama, ndi kupusitsa anthu oombeza ula. Ndine amene ndimatsutsa mau a anthu anzeru, ndi kuŵaonetsa kuti nzeru zao nzopusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 18:23

Mwa iwe simudzaonekanso konse kuŵala kwa nyale. Mwa iwe simudzamvekanso konse mau a mkwati wamwamuna kapena wamkazi. Amalonda anali anthu otchuka kwambiri aja a pa dziko lapansi. Unkanyenga anthu a mitundu yonse ndi maula ako.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 9:20-21

Anthu ena onse otsala, amene sadaphedwe ndi miliri ija, sadatembenuke mtima kuti asiye ntchito za manja ao. Sadaleke kupembedza mizimu yoipa, ndi mafano agolide, asiliva, amkuŵa, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda. Anthuwo sadatembenukenso kuti aleke kupha anzao, ufiti, dama ndi kuba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:6

Inu Mulungu, mwakana anthu anu, zidzukulu za Yakobe. Dziko ladzaza ndi anthu amatsenga akuvuma, ladzazanso ndi olosa a ku Filistiya. Anthu anu akuchita nao miyambo yachilendo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 10:2

Paja mafano am'nyumba amalankhula zonama, ndipo oombeza maula amaona zabodza. Olota maloto amalota zabodza, ndipo mau ao othuzitsa mtima ndi nkhambakamwa chabe. Motero anthu amangoyenda uku ndi uku ngati nkhosa, amazunzika chifukwa chosoŵa mbusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 14:14

Koma Chauta adandiyankha kuti, “Zakuti aneneriwo amalosa m'dzina langa, ili ndi bodza. Ine sindidaŵasankhe, sindidaŵatume kapena kulankhula nawo. Iwo amakuloserani zinthu zonama zimene akuti adaziwona m'masomphenya. Amaombeza zabodza, zimene amalankhula ndi zonyenga zopeka iwo eni ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 17:17

Anthuwo adapereka ngati nsembe ana ao aamuna ndi ana ao aakazi, ndipo ankaombeza maula, namachitanso zanyanga. Adadzipereka kuti azichita zoipa zochimwira Chauta, namkwiyitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 22:28

Ndipo aneneri ake abisa zimenezi monga muja amachitira anthu popaka njereza, amaziphimba ndi zimene amaona m'maloto ao abodza ndi m'maula ao onama. Amati, ‘Ambuye Chauta akunena zakutizakuti,’ pamene Ine Chauta sindidalankhule konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 21:21

Mfumu ya ku Babiloni yaima ku njira pa mphambano ya miseu. Ikuwombeza maula ndi mivi kuti ipeze njira yoyenera kudzeramo. Ikupempha nzeru kwa milungu yake, ndipo ikuyang'ana chiŵindi cha nyama yopereka ku nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 13:6-9

Aneneriwo amalankhula zonama, ndipo amalosa zabodza. Amanena kuti, ‘Akuterotu Chauta,’ pamene Chauta sadaŵatume konse. Komabe amayembekeza kuti zimene anenazo zidzachitika. Koma Ine ndikuti, Zimene inu aneneri mukuti mudaziwona m'masomphenya nzabodza. Ndipo kulosa kwanuko nkwabodza. Mumanena kuti ‘Akuterotu Chauta,’ ngakhale Ine sindidalankhule konse.” “Tsono zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndikukutsutsani chifukwa choti mau anu ngachabe, ndipo zimene mukuti mudaziwona ngati kutulo nzabodza. Ndidzakantha aneneri onama amene amati adaona zakutizakuti ngati kutulo, amenenso kulosa kwao nkwabodza. Sadzakhala nao m'bwalo la aphungu la anthu anga. Sadzalembedwa m'kaundula wa nzika za Israele, ndipo sadzaloŵa m'dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 15:23

Kugalukira kuli ngati tchimo loombeza, kukhala wokanika kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 28:7

Pamenepo Saulo adauza nduna zake kuti, “Mundifunire mkazi wolankhula ndi mizimu kuti ndipite kwa iyeyo, ndikapemphe nzeru.” Ndunazo zidamuuza kuti, “Ku Endori aliko mkazi wolankhula ndi mizimu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 4:19

Musamale kuti mukapenya ku thambo nkuwona dzuŵa, mwezi, nyenyezi ndi zonse zakuthamboko, mtima wanu usakopeke nkuyamba kupembedza ndi kutumikira zinthu zimene Mulungu wanu wapatsa anthu ena onse a pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 23:24

Masiku amenewo Yosiya adachotsanso anthu amaula, amatsenga, milungu ya m'nyumba ndiponso mafano ena onse, kudzanso zonyansa zonse zimene zinali ku dziko la Yuda ndi ku Yerusalemu. Adachita zimenezi kuti atsate Malamulo amene adalembedwa m'buku lomwe wansembe Hilikiya adalipeza m'Nyumba ya Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:6

Chauta, Mfumu ndi Momboli wa Israele, Chauta Mphambe, akunena kuti, “Ine ndine woyamba ndi womaliza. Palibenso Mulungu wina, koma Ine ndekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 96:5

Paja milungu yonse ya mitundu ina ya anthu ndi mafano chabe. Koma Chauta ndiye adalenga zakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:17

Iwo adapereka nsembe kwa mizimu yoipa, imene siili milungu konse, milungu imene Aisraele sadaidziŵe nkale lonse, milungu yongobwera kumene, milungu imene makolo ao sankailemekeza konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 10:13

Choncho Saulo adafa chifukwa cha kusakhulupirika kwake. Iyeyo anali wosakhulupirika kwa Chauta, poti sankamvera mau a Chauta ndiponso ankapempha nzeru kwa anthu olankhula ndi mizimu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 5:26

Ndipotu muzidzanyamula Sakuti, mfumu yanu, ndi nyenyezi ija Kaiwani, mulungu wanu, mafano amene mudadzipangira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 3:2-3

anthu amphamvu ndi asilikali ankhondo, aweruzi ndi aneneri, olosa ndi akuluakulu, maduku, zigwinjiri, malamba, mabotolo a zonunkhira, zithumwa, mphete, zipini, madelesi apaphwando, makepi, miinjiro, zikwama, akalilole, zovala zabafuta, nduŵira, ndiponso nsalu zam'mapewa. M'malo mwa kununkhira padzakhala kununkha, m'malo mwa lamba adzavala chingwe, m'malo mwa tsitsi lopesa bwino adzakhala ndi mipala, m'malo mwa delesi la mtengo wapatali adzavala chiguduli, m'malo mwa kunyadira kukongola adzachita manyazi. Iwe Yerusalemu, anthu ako aamuna adzaphedwa ndi lupanga, ndipo anthu ako amphamvu adzafera ku nkhondo. Choncho pa zipata zako padzakhala kulira kokhakokha, iweyo udzasakazidwa nkukhala pansi, ukuvimvinizika pa fumbi. atsogoleri ankhondo ndi anthu olemekezeka, aphungu ndi amatsenga, ndiponso akatswiri a njirisi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:28

Anthuwo adayamba kupembedzanso Baala wa ku Peori, ndi kumadya nawo nsembe zoperekedwa kwa anthu akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 4:6

Anthu anga akuwonongeka chifukwa Ine sandidziŵa. Ndidzakukanani kuti musanditumikire ngati ansembe, chifukwa choti mwakana kuphunzitsa za Ine. Mwaiŵala malamulo a Mulungu wanu, tsono Inenso Mulungu wanu ndidzaiŵala ana anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 17:2-5

Mwina padzapezeka kuti mu mzinda wina umene Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani, muli munthu wina wamwamuna kapena wamkazi amene wachimwira Chauta, Mulungu wanu, Zimenezi zidzamthandiza kudziŵa kuti iyeyo saposa Aisraele anzake, ndiponso kuti sayenera kukhala wonyozera malamulo a Chauta mpang'ono pomwe. Motero iyeyo, pamodzi ndi zidzukulu zake zomwe, adzalamulira nthaŵi yaitali mu Israele. naphwanya chipangano chake, popembedza ndi kutumikira milungu ina, monga dzuŵa, mwezi kapena nyenyezi, zimene ndidaletsa kuti asazipembedze. Mukamva kuti chinthu chotere chachitika, mufufuze bwino nkhani imeneyo, ndipo mukapeza kuti choipa choterechi chachitikadi mu Israele, mumgwire mwamunayo kapena mkaziyo ndi kupita naye ku zipata za mzinda wanu ndipo mumphere kunja kwa mzinda pakumponya miyala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 28:3

Nthaŵi imeneyi nkuti Samuele atafa, ndipo Aisraele atalira maliro ake, namuika ku mzinda wake ku Rama. Saulo anali atachotsa anthu onse olankhula ndi mizimu ndi anthu onse oombeza maula am'dzikomo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 29:8

Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Aneneri asakunyengeni, ngakhale oombeza amene ali pakati panu, ndipo musamvere maloto ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 8:19-20

Tsono anthu akakuuzani kuti, “Kafunseni kwa olankhula ndi mizimu ndi kwa olosa amene amatulutsa liwu loti psepsepse ndi kumang'ung'udza.” Kodi anthu sayenera kupempha nzeru kwa milungu yao? Kodi sungapite kwa anthu akufa kukapemphera nzeru anthu amoyo, Tsono ndidapeza mboni zokhulupirika, wansembe Uriya ndiponso Zekariya mwana wa Yeberekiya, kuti andichitire umboni. kuti akalandireko mau enieni ndi malangizo? Iyai, amene amalankhula motero, mwa iwo mulibe konse kuŵala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 47:9

Koma m'kamphindi, tsiku limodzi, zinthu ziŵiri zonsezi zidzakugwera. Ana ako onse kukufera, iweyo kusanduka wamasiye, zonsezo zidzakugwera pamodzi, ngakhale kuti uli ndi matsenga ambiri ndi zithumwa zamphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 7:11-12

Zitatero Farao adaitana anthu ake anzeru ndi amatsenga, ndipo iwowo adachitanso zomwezo mwa matsenga ao. Adaponyanso pansi ndodo zao, ndipo zidasanduka njoka. Koma ndodo ya Aroni ija idameza ndodo zaozo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 18:14

Anthu amene mukukaŵalanda dziko limene mukakhalemolo, amatsata ndi kumvera amatsenga ndi oombeza. Koma inuyo Chauta, Mulungu wanu, sakulolani kuchita zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:19

Ambiri amene ankakonda kuchita matsenga, adasonkhanitsa mabuku ao naŵatentha pamaso pa anthu onse. Pamene adaonkhetsa mtengo wa mabukuwo, adapeza kuti udaakwanira ngati ndalama zikwi makumi asanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:22

Musakhulupirirenso munthu, poti moyo wake sukhalira kutha. Nanga iye nkumuyesanso kanthu ngati!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 23:5

Yosiya adatulutsa ansembe a mafano amene mafumu a ku Yuda adaŵakhazika kuti azipereka nsembe ku akachisi ku mizinda ya m'dziko la Yuda ndi ku malo ozungulira Yerusalemu. Adatulutsanso amene ankapereka nsembe kwa Baala, kwa dzuŵa, kwa mwezi, kwa nyenyezi ndi kwa zinthu zonse zakuthambo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 13:1-5

Mwina mneneri kapena womasulira maloto adzaoneka pakati panupo, namanena kuti adzachita chizindikiro kapena chozizwitsa, Mumuphe ndi miyala. Iye adati akusokeretseni, kuti musiyane ndi Mulungu wanu amene adakutulutsani ku dziko la Ejipito kumene mudaali kuukapolo kuja. Tsono Aisraele onse adzamva zimene zachitikazo nadzachita mantha, ndipo palibe wina pakati panu amene adzachitenso choipa choterechi. Pomakhala m'midzi imene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsaniyo, nthaŵi zina kapena mudzamva kuti anthu ena a mtundu wanu asokeretsa anthu m'mizinda yao yomwe. Akuŵapembedzetsa milungu imene inu simudaipembedzepo nkale lonse. Mbiri yoteroyo muifufuze bwino. Mukapeza kuti mbiriyo njoona, kuti chinthu choipa choterechi chidachitikadi, pompo muphe anthu onse amumzindamo pamodzi ndi zoŵeta zomwe. Muwononge mudzi umenewo kotheratu. Zinthu zonse za anthu a mu mzinda umenewo muzisonkhanitse pamodzi, ndipo muziwunjike pakati pa bwalo lalikulu la mzindawo. Tsono mutatero, muutenthe mzindawo pamodzi ndi zonse zam'menemo, kuti zikhale ngati nsembe yopsereza kwa Chauta, Mulungu wanu. Muusiye choncho kuti ukhale bwinja mpaka muyaya. Musagwireko kanthu kena kalikonse koyenera kuwonongedwa. Tsono Chauta adzaleka osakukwiyiraninso, adzakumverani chisoni ndipo adzakuchitirani chifundo, nadzakuchulukitsani monga adalonjezera makolo anu. Adzakuchitirani zimenezi mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, mukamatsata malamulo ake amene ndikukuuzani lero, ndipo mukamachita zolungama pamaso pa Chauta, Mulungu wanu. Chizindikirocho kapena chozizwitsacho chikachitikadi, iye nakuuzani kuti mupembedze ndi kutumikira milungu ina imene simudaipembedzepo nkale lonse, inu musamvere zimenezo. Chauta, Mulungu wanu, akulola zimenezo kuti akuyeseni, kuti aone ngati mumamkondadi ndi mtima wanu wonse. Mutsate Chauta, Mulungu wanu, ndi kuwopa Iye yekha. Mutsate malamulo ake ndi kumvera mau ake. Mutumikire Iye ndi kuphathana naye. Koma aphedwe mneneri aliyense kapena womasulira maloto aliyense amene akuuzani kuti muukire Chauta, Mulungu wanu, amene adakutulutsani ku Ejipito ndi kukuwombolani m'dziko laukapolo. Munthu wotero ndi woipa, chifukwa akufuna kukusiyitsani njira imene Chauta akufuna kuti muitsate. Aphedwe, ndipo pakutero mudzachotsa choipa chimenechi pakati panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:37-38

Adapereka nsembe ana ao aamuna ndi aakazi kwa mizimu yoipa. Adakhetsa magazi osachimwa, magazi a ana ao aamuna ndi aakazi, amene adaŵapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani, choncho dzikolo adaliipitsa ndi imfa zimenezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:16

Kodi Nyumba ya Mulungu nkufanana bwanji ndi mafano? Pajatu ife ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo, monga Mulungu mwini adanena kuti, “Ndidzakhazikika mwa iwo, ndi kukhala nawo. Ndidzakhala Mulungu wao, iwo adzakhala anthu angaanga.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 13:20

“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikunena kuti, Ndikuzikana zithumwa zanu zapamkono, zimene mumakolera mitima ya anthu ngati mukukola mbalame. Ndidzazithothola pa mikono yanu, kuti ndiŵapulumutse anthuwo amene mumaŵakola ngati mbalame.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:25-26

Mudzatenthe mafano ao ofanizira milungu yao. Musadzakhumbire siliva kapena golide amene iwo adapangira mafanowo. Musadzatengeko zimenezi kuti mungagwe mu msampha, popeza kuti zimenezo zimamnyansa Chauta, Mulungu wanu. Musadzaloŵe nazo m'nyumba mwanu zimenezi, kuti tsoka limene lili pa iwowo lingadzakhale pa inu. Mudzadane ndi mafanowo ndi kuŵanyoza, chifukwa Chauta adaŵatemberera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:13

Mukamafuula kufuna chithandizo, mafano anuwo akupulumutseni! Mphepo idzaiyalula milunguyo, mpweya udzaiwulutsa. Koma amene amakhulupirira Ine, adzalandira dziko lokhalamo, ndi kumapembedza pa phiri langa loyera.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 14:6

“Nchifukwa chake uŵauze Aisraele kuti Ineyo Ambuye Chauta ndikunena kuti, ‘Lapani, mulekane nawo mafano anu. Muzisiye zonyansa zanu zonse.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:14

Tsono okondedwa anga, pewani kupembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:21

Ana inu, dzisungeni bwino, osapembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:5

Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 20:7-8

Ndidaŵauza onse kuti aliyense ataye zonyansa zonse zimene ankasangalala nazo, ndipo asadziipitse ndi mafano a ku Ejipito. Ine ndine Chauta Mulungu wanu. Koma adandipandukira, adakana kundimvera. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adasiya zonyansa zake zimene ankasangalala nazo. Palibe amene adasiya mafano a ku Ejipito. Tsono ndidaganiza zoŵaonetsa ukali ndi mkwiyo wanga ku Ejipito komwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 20:31

Pamene mubwera ndi mphatso zanu, ndi kumapereka ana anu kuti akhale nsembe zopsereza, mumadziipitsa potumikira mafano anu ambirimbiri mpaka lero lino. Kodi Aisraele inu, ndingathe kukulolani bwanji kuti mulandire malangizo kwa Ine? Pali Ine ndemwe Chauta wamoyo, sindidzalola zoterezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:21-23

Inde ankamudziŵa Mulungu, koma m'malo mwa kumtamanda kapena kumthokoza, maganizo ao adasanduka opanda pake, ndipo m'mitima yao yopusa mudadzaza mdima. Iwo amadziyesa anzeru, koma chikhalirecho ndi opusa. Adaleka kulemekeza Mulungu wosafa, nkumapembedza mafano ooneka ngati munthu amene amafa, kapena ngati mbalame ndi nyama zina, kapena zokwaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:1

Mzimu Woyera akunena momveka kuti pa masiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chao. Adzamvera mizimu yonyenga ndi zophunzitsa zochokera kwa mizimu yoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:1

Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 101:3

Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chachabechabe. Ndimadana ndi zochita za anthu okusiyani, sizindikomera konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:7

Tsono muzigonjera Mulungu. Satana muzilimbana naye, ndipo adzakuthaŵani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:15

“Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:8

Chenjerani kuti wina aliyense angakusokonezeni ndi mau olongosola nzeru zapatali. Ameneŵa ndi mau onyenga chabe. Paja nzeru zimenezi zimangochokera ku miyambo ya anthu, ndi ku maganizo ao okhudza zapansipano, osati kwa Khristu ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 16:17-18

Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa, pakuti anthu otere satumikira Khristu Ambuye athu, koma amangotumikira zilakolako zao basi. Ndi mau okoma ndi oshashalika amanyenga anthu a mitima yoona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:8-9

Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye. Mulimbane naye mutakhazikika m'chikhulupiriro, podziŵa kuti akhristu anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso alikumva zoŵaŵa zomwezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:7

Mau a Chauta ngangwiro, amapatsa munthu moyo watsopano. Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika, umaŵapatsa nzeru amene alibe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:14

Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa, koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 14:9

“Ngati mneneri anyengedwa nalosa, ndine Chauta amene ndamnyenga. Ndipo ndidzamkantha ndi dzanja langa ndi kumchotsa pakati pa anthu anga Aisraele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:27

Tsono leka zoipa, ndipo chita zabwino, motero udzakhala pa mtendere mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:20

kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:22

ndipo mupewe choipa cha mtundu uliwonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 13:6-8

Iwo adabzola chilumba chonse mpaka kukafika ku mzinda wa Pafosi. Kumeneko adapezako munthu wina wamasenga, dzina lake Barayesu, Myuda amene ankadziyesa mneneri. Iyeyu ankakhala kwa bwanamkubwa Sergio Paulo, munthu wanzeru. Sergio Pauloyo adaitana Barnabasi ndi Saulo, chifukwa iye ankafunitsitsa kumva mau a Mulungu. Koma kumeneko adapezanako ndi Elimasi, wamasenga uja (Elimasi ndiye kuti Wamasenga). Iyeyo adatengana nawo, kuwopa kuti bwanamkubwa uja angakhulupirire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 47:1-3

Chauta akunena kuti, “Iwe namwali, Babiloni, tsika ndi kukhala pa fumbi. Iwe namwali, Kaldeya, khala pansi, opanda mpando waufumu. Pakuti sadzakutchulanso wofeŵa ndi wodzitekemeza. “Sunkada nako nkhaŵa konse kuipa kwako, unkaganiza kuti palibe wokupenya. Kuchenjera kwako ndi nzeru zako zidakusokeza, ndipo mumtima mwako unkaganiza kuti, ‘Ndi ineyo basi, kupatula ine palibenso wina ai.’ ” Tsoka lidzakugwera, ndipo sudzatha kuliletsa ndi matsenga ako. Chiwonongeko chidzakufikira, iwe osatha kuchithaŵa, chipasupasu chosayembekezeka konse chidzakugwera mwadzidzidzi. Khala nazo nyanga zako ndi matsenga ako. Wakhala ukuzigwiritsa ntchito chiyambire cha ubwana wako. Mwina mwake zingakuthandize kapena nkuwopsa nazo adani ako. Udangodzitopetsa nako kupempha malangizo ambiri. Nabwere okulangizawo kuti adzakupulumutse. Abweretu anthu amene amaphunzira zakumlengalenga, namayang'ana nyenyezi, amenenso amati mwezi ukakhala nkumalosa zimene zidzakuchitikira. “Taona, anthuwo ali ngati mapesi, adzapsa ndi moto. Sangathe kudzipulumutsa ku mphamvu ya malaŵi ake. Moto wake si woti nkuwotha kapena kusendera pafupi nawo ai. Ndimo m'mene adzakuthandizire anthuwo amene wakhala ukugwira nao ntchito ndi kuchita nao malonda chiyambire cha ubwana wako. Onsewo adzangomwazikana, sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.” Tenga mphero kuti upere ufa. Chotsa nsalu yako yakumaso. Kwinda zovala zako mpaka m'ntchafu, woloka mitsinje. Maliseche ako adzakhala poyera, ndipo udzachita manyazi kwambiri. Ndidzalipsira, ndipo palibe amene adzandiletsa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 81:12-13

Choncho ndidaŵasiya ndi mitima yao yosamverayo, kuti atsate zimene ankafuna. “Anthu anga akadandimvera, Aisraele akadayenda m'njira zanga,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 29:18

Chonde muchenjere kuti mwamuna kapena mkazi, ngakhale banja, kaya fuko, kungoti nonsenu amene muli pano lero lino, musapotoloke kuti muchoke kwa Chauta, Mulungu wanu, ndi kumapembedza milungu ya anthu a mitundu ina. Kuteroko kungofanafana ndi muzu umene umati ukakula, umasanduka chiphe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 2:8

Nawonso ansembe sadafunse kuti, ‘Chauta ali kuti?’ Akatswiri a malamulo sadandidziŵe. Olamulira adandipandukira. Aneneri ankalosa m'dzina la Baala, ndipo ankatsata milungu yachabechabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:31

Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:10

Apo Yesu adati, “Choka, Satana! Paja Malembo akuti, ‘Uzipembedza Ambuye, Mulungu wako, ndipo uziŵatumikira Iwo okha.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:8

Yesu Khristu ndi yemweyo dzulo, lero ndi mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:16-17

Musamanyengedwa, abale anga okondedwa. Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera Kumwamba, kwa Atate a zounikira zonse zakuthambo. Iwo sasinthika konse, ndipo kuŵala kwao sikutsitirika mpang'ono pomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:1

Agalatiya opusa inu, adakulodzani ndani? Pamene tidakulalikirani Yesu Khristu, tidamuwonetsa poyera pamaso panu ngati wopachikidwa pa mtanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:24-27

Koma Afarisi atamva zimenezi adati, “Iyai, mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipa sizichokeratu kwina, koma kwa Belezebulu, mkulu wa mizimu yoipayo.” Yesu adaadziŵa zimenezi, motero adaŵauza kuti, “Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo kutha kwake nkomweko. Ndipo anthu a m'mudzi uliwonse kapena a m'banja lililonse akayamba kuukirana, mudzi wotere kapena banja lotere silingalimbe ai. Ngati a mu ufumu wa Satana atulutsana okhaokha, ndiye kuti agaŵikana. Nanga Satanayo ufumu wake ungalimbe bwanji? Inu mukuti Ineyo ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Belezebulu, nanga ophunzira anu amaitulutsa ndi mphamvu za yani? Nchifukwa chake ophunzira anu omwewo ndi amene adzakuweruzeni kuti ndinu olakwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:19

Ndakupatsanitu mphamvu kuti muziponda njoka ndi zinkhanira, ndi kumagonjetsa mphamvu zonse za mdani uja. Palibe kanthu kamene kangakupwetekeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:14-16

“Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike. Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m'nyumbamo. Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:8

Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:17

Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:21

Musagonjere zoipazo, koma gonjetsani zoipa pakuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:2

Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:11-12

Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana. Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:14-17

Musamagwirizana ndi anthu akunja, monga ngati kuti iwo ndi inu mumafanana. Nanga kulungama kungagwirizane bwanji ndi kusalungama? Kapena kuŵala kungayanjane bwanji ndi mdima? Kodi Khristu nkuvomerezana ndi Satana? Kodi mkhristu ndi mkunja angagaŵanenso chiyani pamodzi? Kodi Nyumba ya Mulungu nkufanana bwanji ndi mafano? Pajatu ife ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo, monga Mulungu mwini adanena kuti, “Ndidzakhazikika mwa iwo, ndi kukhala nawo. Ndidzakhala Mulungu wao, iwo adzakhala anthu angaanga.” Nchifukwa chake Ambuye akuti, “Tulukani pakati pao, ndi kudzipatula. Musakhudze kanthu kosayera, ndipo ndidzakulandirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:19

Tikudziŵa kuti ndife ake a Mulungu, ndipo kuti onse odalira zapansipano ali m'manja mwa Woipa uja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:3

Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:7

Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Chauta, ngakhale adani ake omwe amakhala naye mwamtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:19-20

Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe? Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7-8

Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo. Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:13

m'menemo anthu ochimwa ndi onyenga, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanyenga ena nkumanyengedwanso iwo omwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:6

Chauta akakhala pa mbali yanga, sindichita mantha. Munthu angandichite chiyani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:1-2

Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:3-5

Musakhulupirire mafumu kapena anthu ena amene sangathe kuthandiza. Pamene mpweya wa munthu uchokeratu, munthuyo amabwerera ku dothi, zimene ankafuna kuchita, zimatha tsiku lomwelo. Ngwodala munthu amene chithandizo chake chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe, munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:1-5

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera. Satilanga moyenerera machimo athu, satibwezera molingana ndi zolakwa zathu. Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta. Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife. Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza. Amadziŵa m'mene adatipangira, amakumbukira kuti ife ndife fumbi. Kunena za munthu, masiku ake sakhalitsa, ali ngati a udzu, munthuyo amakondwa ngati duŵa lakuthengo. Koma mphepo ikaombapo, duŵalo pamakhala palibe, siliwonekanso pa malo ake. Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama. Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake. Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba, ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake. Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, ndipo usaiŵale zabwino zake zonse. Tamandani Chauta, inu angelo ake, inu amphamvu amene mumamva mau ake, amene mumachita zimene amalamula. Tamandani Chauta, inu magulu a ankhondo ake onse, atumiki ake ochita zimene Iye afuna. Tamandani Chauta, inu zolengedwa zake zonse, ku madera onse a ufumu wake. Nawenso mtima wanga, tamanda Chauta! Ndiye amene amakhululukira machimo ako onse, ndi kuchiritsa matenda ako onse. Ndiye amene amapulumutsa moyo wako ku manda. Amakuveka chikondi chake chosasinthika ndiponso chifundo chake ngati chisoti chaufumu. Ndiye amene amakupatsa zabwino nthaŵi zonse za moyo wako, choncho umakhalabe wa mphamvu zatsopano ngati mphungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 30:19-20

Tsopano ndikukupatsani mpata woti musankhe, kapena moyo kapena imfa, madalitso a Mulungu kapena matemberero ake. Zonse zakumwamba ndi zapansi zikhale mboni za zimene ndakuuzani lerozi. Tsono sankhani moyo, Tsono inuyo ndi zidzukulu zanu mudzabwerera kwa Chauta, ndipo mau ake amene ndikukupatsani leroŵa mudzaŵamvera ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. mukonde Chauta, Mulungu wanu, muzimvera mau ake ndi kukhala okhulupirika kwa Iye, kuti inu ndi zidzukulu zanu mudzakhalitsemo m'dziko limene adalonjeza kuti adzapatsa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 15:11

“Inu Chauta, kodi pali mulungu wina wofanafana nanu? Ndani amafanafana ndi Inu, amene muli aulemu chifukwa cha ungwiro wanu? Ndani amafanafana nanu, Inu amene muli oopsa chifukwa cha ntchito zanu zaulemu ndi zodabwitsa?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:10-15

Nzeru zidzaloŵa mumtima mwako, kudziŵa zinthu kudzakusangalatsa. Kuganiziratu zam'tsogolo kudzakusunga, kumvetsa zinthu kudzakuteteza. Nzeruyo idzakupulumutsa ku mayendedwe oipa, idzakuteteza kwa amtherakuŵiri, amene amasiya njira zolungama, namayenda m'njira zamdima. Iwoŵa amakondwa pochita zoipa, amasangalala ndi ntchito zosalungama. Anthu ameneŵa njira zao nzokhotakhota, makhalidwe ao ngonyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:38-39

Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1-3

Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto. “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.” Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama, ngakhale nyanja zikokome ndi kututuma. Ngakhale mapiri anjenjemere ndi kulindima kwa nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:1-3

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu. Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako. Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:4-5

Ngwodala munthu amene amadalira Chauta, munthu amene sapatukira ku mafano kapena kutsata milungu yonama. Inu Chauta, Mulungu wanga, mwatichitira zodabwitsa zambiri, mwatikonzera zabwino zambiri zakutsogolo. Palibe ndi mmodzi yemwe wotha kulingana nanu. Ndikati ndisimbe ndi kulongosola za zimenezo, sindingathe kuziŵerenga zonse chifukwa cha kuchuluka kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:33

Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:11

Okondedwa anga, popeza kuti ndinu alendo pansi pano, ndikukupemphani kuti musagonjere zilakolako zathupi zimene zimachita nkhondo ndi mzimu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:1-3

Ndimathaŵira kwa Inu Chauta, musalole kuti ndichite manyazi, koma mundipulumutse chifukwa ndinu Mulungu wolungama. Moyo wanga ukutha chifukwa cha chisoni, zaka zanganso zikutha chifukwa cha kulira kwambiri. Mphamvu zanga zatheratu chifukwa cha kulakwa kwanga, mafupa anga agooka. Adani anga onse amandinyodola, anzanga omwe amandiyesa chinthu chonyansa. Anthu odziŵana nawo amandiyesa chinthu choopsa. Anthu ondiwona mu mseu amandithaŵa. Andiiŵala kotheratu ngati munthu wakufa. Ndasanduka ngati chiŵiya chosweka. Zoonadi, ndimamva anthu ambiri akunong'onezana zoipa za ine, zoopsa zandizinga ponseponse. Amapangana zoti andiwukire, namachita upo woipa woti andiphe. Koma ndimadalira Inu Chauta, ndimati, “Inu ndinu Mulungu wanga.” Masiku anga ali m'manja mwanu. Pulumutseni kwa adani anga ndi kwa ondizunza. Yang'aneni mtumiki wanune mwa kukoma mtima kwanu, pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. Inu Chauta, musalole kuti ndichite manyazi, chifukwa ndapemphera kwa Inu. Koma anthu oipa ndiwo achite manyazi, apite ku manda kachetechete. Onse onyada ndi onama olankhula mwamwano ndi monyoza kwa anthu abwino, muŵakhalitse chete. Ndi waukulu ubwino wanu umene mwaŵasungira anthu okumverani, umene mwaŵachitira anthu othaŵira kwa Inu, aliyense waona zimenezi. Tcherani khutu kuti mundimve, fulumirani kudzandipulumutsa. Mukhale thanthwe langa lothaŵirako, ndi linga langa lolimba londipulumutsa. Mumaŵabisa pamalo pamene pali Inu, kuti muŵateteze ku ziwembu za adani ao. Mumaŵasunga bwino ndi kuŵatchinjiriza, kuti anthu angakangane nawo. Atamandike Chauta: wandiwonetsa modabwitsa chikondi chake chosasinthika, pamene ndinali mu mzinda wozingidwa ndi gulu la ankhondo. Ndidalankhula mwankhaŵa kuti, “Andipirikitsira kutali ndi Inu.” Koma Inu mudamva kupempha kwanga pamene ndidakudandaulirani kuti mundithandize. Kondani Chauta, inu nonse anthu oyera mtima. Chauta amasunga anthu okhulupirika, koma amalanga koopsa anthu odzikuza. Khalani amphamvu ndipo mulimbe mtima, inu nonse okhulupirira Chauta. Zoonadi, ndinu thanthwe langa ndi linga langa. Tsogolereni ndi kundiwongolera chifukwa Inu ndinu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:17-19

Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse. Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima. Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri. Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:1-3

Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake. Munthu woipa amaona zimenezi, ndipo amapsa nazo mtima. Amakukuta mano nazimirira. Zokhumba za munthu woipa sizidzachitika konse. Zidzukulu zake zidzakhala zamphamvu pa dziko lapansi. Ana a munthuyo adzakhala odala. Banja lake lidzakhala lachuma ndi lolemera, ndipo kulungama kwake kudzakhala kwamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:17

Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:3-5

Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo. Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:5-6

Udzipereke m'manja mwa Chauta, umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira. Adzaonetsa poyera kusalakwa kwako, ndipo kulungama kwako kudzaŵala ngati usana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:14

Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:23

Mtima wako uziwulonda bwino, pakuti m'menemo ndimo muli magwero a moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 1:10-11

Nchifukwa chake abale, chitani changu koposa kale kutsimikiza kuti Mulungu adakuitanani ndipo adakusankhani. Mukatero simudzagwa konse. Choncho adzakutsekulirani kwathunthu khomo loloŵera mu Ufumu wosatha wa Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:11

Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:10

Chauta ali ngati nsanja yolimba, munthu wokhulupirira amathaŵiramo napulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 59:1-2

Chauta si wosoŵa mphamvu, kuti angalephere kukupulumutsani, ndipo si gonthi, kuti nkupanda kumva zimene mukupempha. Timapapasapapasa ngati anthu akhungu, tili ngati anthu opanda maso. Timaphunthwa masana ngati usiku. Ndife amoyo ndithu, komabe tili ngati anthu akufa. Tonse timabangula ngati zimbalangondo, ndipo timalira modandaula ngati nkhunda. Timayembekeza kuweruza kolungama, koma sitikupeza. Timadikiranso chipulumutso, koma chili nafe kutali. Inu Chauta, takuchimwirani kwambiri. Machimo athu akutitsutsa, zolakwa zathu zili pa ife, ndipo sitingakanepo nchimodzi chomwe. Takupandukirani, takukanani, Inu Chauta, ndipo takana kukutsatani. Tapanikiza anzathu, takupandukirani Inu. Maganizo athu ndi abodza, mau athu ndi onama. Kuweruza kolungama kwalekeka, ndipo kuchita zaungwiro kwaiŵalika. Zoona sizikupezekanso m'mabwalo a milandu, ndipo chilungamo sichikutha kupezeka kumeneko. Zoona zikusoŵa kumeneko, ndipo wina aliyense akapanda kuchita nawo zoipa, amapeza mavuto.” Chauta adaziwona zimenezi ndipo zidamunyansa kuti palibe chilungamo. Chauta adaona kuti palibe munthu ndi mmodzi yemwe adadabwa kuti palibe wochitapo kanthu. Tsono adapambana ndi mphamvu zakezake, ndipo adadzilimbitsa ndi kulungama kwake. Adavala chilungamo ngati chovala chachitsulo chapachifuwa, ndipo kumutu kwake adavala chisoti chachipulumutso. Adavala kulipsira ngati mkanjo, ndipo mkwiyo udakhala ngati chofunda chake, Chauta adzalanga adani a anthu ake molingana ndi zochita zao: adzaonetsa ukali kwa omuukira, ndipo adzalipsira adani ake. Adzalanga ngakhale okhala m'maiko akutali. Motero anthu adzaopa Chauta kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe. Iyeyo adzabwera ngati mtsinje waliŵiro, wokankhidwa ndi mphepo yamkuntho. Machimo anu adakulekanitsani ndi Mulungu wanu, ndipo Iye wakufulatirani chifukwa cha machimo anuwo. Choncho saamva zimene inu mumanena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:11-12

Koma iwe, munthu wa Mulungu, uzipewe zonsezi. Uzikhala ndi mtima wofunafuna chilungamo, wolemekeza Mulungu, wokhulupirika, wachikondi, wolimbika ndi wofatsa. Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:6-7

Ndithudi, Inu mumakonda mtima woona, choncho mundiphunzitse nzeru zanu. Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzakhala woyera. Mundisambitse, ndipo ndidzayera kupambana chisanu chambee.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 84:11

Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:15

Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:22

Musamadzinyenga pakungomva chabe mau a Mulungu, koma muzichita zimene mauwo anena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:20

Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:13

Ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “Aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba adzapulumuka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:1-5

Kale inu munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu ndi machimo anu. Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite. Inu amene mtundu wanu sindinu Ayuda, kumbukirani m'mene munaliri kale. Ayuda amadzitchula oumbala, chifukwa cha mwambo umene amachita pa thupi lao, ndipo inu amakutchulani osaumbala. Tsono kumbukirani kuti nthaŵi imene ija munali opanda Khristu. Munali alendo, ndipo simunali a mtundu wa anthu osankhidwa ndi Mulungu. Munali opanda gawo pa zimene Mulungu, mwa zipangano zake, adaalonjeza anthu ake. Munkakhala pansi pano opanda chiyembekezo, opandanso Mulungu. Koma tsopano, mwa Khristu Yesu, inu amene kale lija munali kutali ndi Mulungu, mwakhala pafupi, chifukwa cha imfa ya Khristu. Khristu mwini wake ndiye mtendere wathu. Iye adasandutsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina kuti akhale amodzi. Pakupereka thupi lake, adagamula khoma la chidani limene linkatilekanitsa. Iye adathetsa Malamulo a Mose pamodzi ndi malangizo ake ndi miyambo yake. Adachita zimenezi kuti kuchokera ku mitundu iŵiri ija, alenge mtundu umodzi watsopano, wokhala mwa Iye, kuti choncho adzetse mtendere. Khristu adafa pa mtanda kuti athetse chidani, ndipo kuti mwa mtandawo aphatikize pamodzi m'thupi limodzi mitundu iŵiriyo, ndi kuiyanjanitsa ndi Mulungu. Khristu adadzalalika Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu a mitundu inanu, amene munali kutali ndi Mulungu, ndiponso kwa Ayuda, amene anali pafupi naye. Tsopano kudzera mwa Khristu ife tonse, Ayuda ndi a mitundu ina, tingathe kufika kwa Atate mwa Mzimu Woyera mmodzi yemweyo. Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu. Pa nthaŵi imeneyo, munkayenda m'zoipa potsata nzeru zapansipano, ndipo munkamvera mkulu wa aulamuliro amumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ukugwira ntchito tsopano pakati pa anthu oukira Mulungu. Ndinu omangidwa pamodzi m'nyumba yomangidwa pa maziko amene ndi atumwi ndi aneneri, ndipo Khristu Yesu mwini ndiye mwala wapangodya. Mwa Iyeyu nyumba yonse ikumangidwa molimba, ndipo ikukula kuti ikhale nyumba yopatulika ya Ambuye. Mwa Iyeyu inunso mukumangidwa pamodzi ndi ena onse, kuti mukhale nyumba yokhalamo Mulungu mwa Mzimu Woyera. Nthaŵi imene ija ifenso tonse tinali ndi moyo wonga wao, ndipo tinkatsata zilakolako za khalidwe lathu lokonda zoipa. Tinkachitanso zilizonse zimene matupi athu ndi maganizo athu ankasirira. Nchifukwa chake, mwachibadwa chathu, tinali oyenera mkwiyo wa Mulungu, monga anthu ena onse. Koma Mulungu ndi wachifundo chachikulukulu, adatikonda ndi chikondi chachikulu kopambana. Motero, pamene tinali akufa chifukwa cha machimo athu, Iye adatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu. Kukoma mtima kwa Mulungu ndi kumene kudakupulumutsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:30

Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera amene Mulungu adakusindikizani chizindikiro chake chotsimikizira kuti ndinu ake pa tsiku limene Mulunguyo adzatipulumutse kwathunthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:37

Letsani maso anga kuti asamayang'ane zachabe, mundipatse moyo monga momwe mudalonjezera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:1-2

Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe. Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha. Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi. Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse, Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:24

Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:165

Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:24

Njira yopita ku moyo imakamufikitsa ku ntchito zangwiro, kuti alewe malo a anthu akufa kunsiko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:2

Makhalidwe a munthu amakhala olungama pamaso pa mwiniwakeyo, koma Chauta ndiye amayesa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:12

Pali njira ina yooneka ngati yabwino kwa munthu, koma kopherezera kwake nku imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:30

“Munthu wosavomerezana ndi Ine, ndiye kuti ndi wotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ndiye kuti ameneyo ndi womwaza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:11-12

Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muŵatsutse. Paja zimene iwo amachita mobisa, ngakhale kuzitchula komwe kumachititsa manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 5:20

Tsoka kwa amene zoipa amaziyesa zabwino ndipo zabwino amaziyesa zoipa, amene mdima amauyesa kuŵala, ndipo kuŵala amakuyesa mdima, amene zoŵaŵa amaziyesa zozuna, ndipo zozuna amaziyesa zoŵaŵa!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 95:7-8

Pakuti ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pa busa lake, ndife nkhosa zodyera m'manja mwake. Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja, monganso tsiku lija ku Masa m'chipululu muja,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 5:30-31

M'dziko muno mwachitika chinthu chododometsa ndi choopsa. Aneneri akulosa zabodza, ndipo ansembe akuvomerezana nawo. Komabe anthu anga akukondanso zomwezo. Kodi mudzatani potsiriza?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:2

Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 99:8-9

Inu Chauta, Mulungu wathu, munkaŵayankha, munali Mulungu woŵakhululukira, komabe wolanga ntchito zao zoipa. Tamandani Chauta, Mulungu wathu, mpembedzeni ku phiri lake loyera. Chauta, Mulungu wathu, ndi woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:1

Chauta akuti, “Tsoka kwa ana ondipandukira Ine! Amachita zodzikonzera okha osati zokonza Ine. Amachita chipangano chaochao, chosatsata chifuniro changa, ndipo amanka nachimwirachimwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 13:18

Uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Tsoka kwa akazi amene amasoka zithumwa zapamkono, amenenso amasoka nsalu zakumutu za anthu a misinkhu yosiyanasiyana, kuti azikola mitima ya anthu. Kodi mufuna kukola mitima ya anthu anga, inuyo nkupulumutsa moyo wanu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 18:20-21

Pamenepo Ahabu adatumiza mau kwa onse a ku Israele, ndipo adasonkhanitsa aneneri a Baala ku Phiri la Karimele. Eliya adasendera pafupi ndi anthu onsewo, naŵafunsa kuti, “Kodi mudzakhala anthu a mitima iŵiri mpaka liti? Ngati Chauta ndiye Mulungu, mtsateni. Koma ngati Baala ndiye Mulungu, tsatani iyeyo.” Anthuwo sadamuyankhe ndi liwu limodzi lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 10:20-22

Tsiku limenelo otsalira a ku Israele, opulumuka a m'banja la Yakobe, sadzadaliranso anthu amene adaŵakantha, koma ndithu adzadalira Chauta, Woyera Uja wa Israele. Otsalira adzabwerera, otsalira a m'banja la Yakobe, adzabwereradi kwa Mulungu wamphamvu. Iwe Israele, ngakhale anthu ako achuluke ngati mchenga wakunyanja, otsalira oŵerengeka okha ndiwo adzabwerere. Chiwonongeko chalamulidwa, chidzaonetsa chilungamo chosefukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:10

Amauza oona zobisika kuti, ‘Musaonenso.’ Amauza aneneri kuti, ‘Musatiloserenso zoona. Mutiwuze zotikomera, mutilosere zam'mutu chabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:18-20

“Munthu wamkazi wochita zaufiti, musamlole kuti akhale moyo. “Aliyense wogona ndi nyama aphedwe basi. “Ngati mbala ipezeka ikuthyola nyumba ndipo ikanthidwa nkufa, asalipsire magazi chifukwa cha mbalayo. “Aliyense wopereka nsembe kwa milungu, osati kwa Chauta yekha, aphedwe ameneyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 27:15

“Atembereredwe aliyense wopanga fano losema kapena loumba, namalipembedza mobisa. Chauta amanyansidwa nacho chinthu chopanga mmisiricho.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 4:24

Paja Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wansanje, salola kuti wina apikisane naye. Ali ngati moto waukali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:16-17

Adamchititsa nsanje ndi mafano ao achilendo, ndipo zonyansa zimene adachita zidamkwiyitsa. Iwo adapereka nsembe kwa mizimu yoipa, imene siili milungu konse, milungu imene Aisraele sadaidziŵe nkale lonse, milungu yongobwera kumene, milungu imene makolo ao sankailemekeza konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:13-14

Muzigwetsa maguwa ao, muwononge miyala yao yopatulika imene adaimiritsa, ndipo mugwetse mitengo yao yopatulika yopembedzerapo. Musadzapembedze mulungu wina aliyense, chifukwa Chauta amene dzina lake ndi Kansanje, ndi Mulungu wansanjedi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:2

Chauta, Mulungu wanu, akadzapereka anthu ameneŵa kwa inu ndipo mukadzaŵagonjetsa, mudzaŵaononge onsewo. Musakayanjane nawo, kapena kuŵachitira chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:36-39

Adatumikira mafano ao amene adasanduka msampha kwa iwo. Adapereka nsembe ana ao aamuna ndi aakazi kwa mizimu yoipa. Adakhetsa magazi osachimwa, magazi a ana ao aamuna ndi aakazi, amene adaŵapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani, choncho dzikolo adaliipitsa ndi imfa zimenezo. Adadzidetsa ndi ntchito zao, nakhala osakhulupirika pa zochita zao ngati mkazi wachigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 65:3-4

Amandikwiyitsa mopanda manyazi. Amapereka nsembe zachikunja m'minda, ndipo amafukiza lubani pa maguwa anjerwa achikunja. Amakatandala ku manda, amachezera kumalo obisika usiku. Amadya nyama yankhumba, namamwa msuzi wa nyama zoperekera nsembe zachikunja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:23-25

“Pa nthaŵi imeneyo wina akadzakuuzani kuti, ‘Ali panotu Khristu uja! Uyo ali apoyo!’ musadzakhulupirire. Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu. Mvetsetsani, Ine ndiye ndakuuziranitu zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:18-23

Mkwiyo wa Mulungu ukuwoneka kuchokera Kumwamba. Amakwiyira anthu chifukwa cha kusalungama kwao konse ndi kusamchitira ulemu. Kusalungama kwaoko kumaŵalepheretsa kudziŵa zoona. Mulungu amaŵakwiyira, chifukwa zimene munthu angathe kudziŵa zokhudza Mulungu iwo akuzidziŵa bwino lomwe, popeza kuti Mulungu mwini ndiye adaŵaululira zimenezi. Uthengawu Iye adaulonjeza kale kudzera mwa aneneri ake ndipo udalembedwa m'Malembo Oyera. Pajatu chilengedwere cha dziko lapansi anthu akhala akuzindikira makhalidwe osaoneka a Mulungu, ndiye kuti mphamvu zake zosatha, ndiponso umulungu wake. Akhala akuzizindikira poona zimene Mulungu adalenga. Choncho alibe konse pozembera. Inde ankamudziŵa Mulungu, koma m'malo mwa kumtamanda kapena kumthokoza, maganizo ao adasanduka opanda pake, ndipo m'mitima yao yopusa mudadzaza mdima. Iwo amadziyesa anzeru, koma chikhalirecho ndi opusa. Adaleka kulemekeza Mulungu wosafa, nkumapembedza mafano ooneka ngati munthu amene amafa, kapena ngati mbalame ndi nyama zina, kapena zokwaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 1:6-9

Ndikudabwa kuti mukupatuka msangamsanga motere, kusiya Mulungu amene adakuitanani mwa kukoma mtima kwa Khristu, ndipo kuti mukutsata uthenga wabwino wina. Koma palibe konse uthenga wabwino wina. Pali anthu ena amene akukusokonezani, ndipo akufuna kupotoza Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Koma aliyense, kaya ndife kaya ndi mngelo wochokera Kumwamba, akakulalikirani uthenga wabwino wosiyana ndi uja tidakulalikiraniwu, ameneyo akhale wotembereredwa. Ndikubwereza kunena zimene tidaanenanso kale, kuti munthu aliyense akakulalikirani uthenga wabwino wosiyana ndi Uthenga Wabwino umene mudalandira uja, iyeyo akhale wotembereredwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:1-3

Komabe panali aneneri ena onama ngakhale pakati pa Aisraele omwe. Momwemonso pakati pa inu padzaoneka aphunzitsi onama. Iwowo adzaloŵetsa mwachinsinsi zophunzitsa zonama ndi zoononga, ngakhale kukana kumene Mbuye wao amene adaŵaombola, ndipo motero adzadziitanira chiwonongeko mwamsanga. Makamaka adzalanga anthu amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi namanyoza ulamuliro. Aphunzitsi onyenga ndi odzikuza, osasamala munthu, saopa kuchita chipongwe aulemerero a Kumwamba. Chonsecho ngakhale angelo, amene ali aakulu ndi amphamvu kuposa aphunzitsi onyengaŵa, sanyazitsa aulemererowo pamaso pa Ambuye. Koma anthu aŵa ali ngati nyama chabe, zolengedwa zopanda nzeru, zobadwira kuti zizigwidwa ndi kumaphedwa. Amanyoza mwachipongwe zinthu zosazidziŵa. Ndipo monga nyama zija, iwo omwe adzaonongedwa, nadzalangidwa molingana ndi kuipa kwao. Chimene chimaŵakomera nkumangochita zokondweretsa thupi nthaŵi yamasana. Ali ngati mathotho ndi maŵanga onyansa, chifukwa podya nanu pamodzi amakondwera kuchita zonyenga. Maso ao ndi adama, osafuna kuleka kuchimwa. Amanyengerera anthu a mtima wosakhazikika. Ali ndi mtima wozoloŵera kuumirira chuma. Anthu otembereredwa! Adasiya njira yolungama, adasokera potsata njira ya Balamu, mwana wa Beori, amene ankafunitsa kupata mphotho pochita zosalungama. Koma adadzudzulidwa chifukwa cha kulakwa kwakeko. Bulu, nyama yosalankhula, adalankhula ngati munthu, kuletsa zamisala za mneneriyo. Aphunzitsi onyengaŵa ali ngati akasupe opanda madzi, ngati nkhungu yokankhidwa ndi mphepo yamkuntho. Mulungu adaŵasungira mdima wakuda wabii. Iwowotu amalankhula mau odzitama auchitsiru, ndipo ndi zilakolako zonyansa zathupi amanyengerera anthu amene angopulumuka chatsopano pakati pa anzao oipa. Amaŵalonjeza ufulu, chonsecho eniakewo ndi akapolo a chivunde. Pajatu munthu amasanduka kapolo wa chimene chamugonjetsa. Ambiri adzatsata mkhalidwe wodzilekerera ndipo anthu adzanyoza njira ya choona chifukwa cha iwowo. Chifukwatu ngati anthu apulumuka ku zodetsa za dziko lino lapansi, pakudziŵa Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu, pambuyo pake nkugwidwanso ndi kugonjetsedwa ndi zoipa zomwezo, potsiriza adzakhala oipa koposa m'mene analiri poyamba. Kukadakhala bwino kwa iwo akadakhala osadziŵa njira ya chilungamo, koposa kuileka atadziŵa lamulo loyera limene Mulungu adaŵapatsa. Pakutero akutsimikiza kuti ngwoona mwambi uja wakuti, “Galu wabwerera ku masanzi ake,” ndi wina ujanso wakuti, “Nkhumba imene inasamba, yakunkhuliranso m'matope.” Chifukwa chokondetsa chuma, iwo adzayesa kupeza phindu pakukuuzani mau onyenga. Komatu chilango chao nchokonzeratu kale, ndipo chiwonongeko chao chikuŵadikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa