Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


103 Mau a m'Baibulo Okhudza Mkwiyo

103 Mau a m'Baibulo Okhudza Mkwiyo

Ndikufuna ndikuuzeni nkhani ya mkwiyo. Mkwiyo ndi chida cha mdani wathu kuti atichititse tichinjirize Mulungu. Tikalola mkwiyo kutilamulire, sitidzathawa mavuto ake. Ngakhale Mulungu wakwiya kale ndi anthu, nthawi zonse amatipatsa mwayi woti tiyanjane naye.

Mkwiyo umatibweretsera mavuto ambiri, osati kungotaya madalitso a Mulungu okha, koma umatibweretseranso chisoni chamumtima. Kaya tikwiya pa zifukwa zomveka kapena ayi, lemba la Efeso 4:26-27 limatiuza kuti, “Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyo, ndipo musampatse mmalo Mdyerekezi.”

N’zomveka kukwiya ngati tawona zosalungama kapena zamwano zokhudza Mulungu, koma Ambuye amatiuza mu Aroma 12 kuti, “Kubwezera ndi kwanga; Ine ndidzabwezera.”

Kukhala paubwenzi ndi Mzimu Woyera n’kofunika kwambiri kuti tizitha kulamulira maganizo athu. Tiyeni tipemphe Mzimu Woyera kuti zipatso zake zilamule mitima yathu, kutilimbitsa mkati mwathu.




Masalimo 37:8

Lewa kupsa mtima ndi kukwiya. Usachite zimenezi, pakuti sudzapindula nazo kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:19

Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:26

Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:32

Munthu wosapsa mtima msanga amapambana wankhondo, amene amadzigwira mtima amapambana msilikali wogonjetsa mzinda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:8

Koma tsopano musachitenso zonsezi, monga kukalipa, kukwiya, kuipa mtima, ndi mijedu. Pakamwa panu pasamatulukenso mau otukwana kapena onyansa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:9

Usamafulumira kukwiya, pakuti mkwiyo umakhalira zitsiru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:8

Chauta ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:18

Munthu wopsa mtima msanga amautsa mkangano, koma munthu woleza mtima amabweretsa mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:1

Kuyankha kofatsa kumazimitsa mkwiyo, koma mau ozaza amakolezera ukali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 4:6-7

Apo Chauta adafunsa Kainiyo kuti, “Kodi wakwiyiranji chotere? Chifukwa chiyani nkhope yako yagwa? Ukadachita zabwino, ndikadakondwera nawe. Koma chifukwa choti wachita zoipa, tchimo lakukhalirira pa khomo ngati chilombo cholusa. Likulakalaka kuti likugwire, koma iweyo uligonjetse tchimolo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:24

Usachite naye chibwenzi munthu wopsa mtima msanga, ndipo usamayenda naye munthu waukali,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:19

Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:6

Adayenda pamaso pa Mose nanena mokweza kuti, “Chauta, Chauta, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndiponso wokhulupirika kwa anthu ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:11

Nzeru zimapatsa munthu mtima wosakwiya msanga, ulemerero wake wagona pa kusalabadako za chipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:11

Wopusa amaonetsa mkwiyo wake, koma munthu wanzeru amadzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:31

Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:22

Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense wopsera mtima mbale wake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu. Aliyense wonena mnzake kuti, ‘Wopandapake iwe,’ adzayenera kuzengedwera ku Bwalo Lapamwamba. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru,’ adzayenera kukaponyedwa ku moto wa Gehena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 7:11

Mulungu ndiye muweruzi wolungama, amalanga anthu oipa nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 14:18

‘Chauta ndi wosakwiya msanga, ndi wodzaza ndi chifundo chosasinthika, ndi wokhululukira ochimwa ndi opalamula. Koma sadzaleka kulanga ochimwa, amalanga ana a mbadwo wachitatu ndi wachinai chifukwa cha kuchimwa kwa makolo ao.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 9:8

Ngakhale ku phiri la Horebu kuja, mudakwiyitsa Chauta, kukwiya kwake koti akadakuwonongani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:35

Kulipsira nkwanga, kubwezera zoyenerera nkwanganso, nthaŵi yoti agwe idzakwana. Tsiku la masoka ao layandikira, chiwonongeko chao chikudza mofulumira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:41

kuti ndidzanola lupanga langa lochezimira, ndipo ndidzaona kuti chilungamo chichitike. Adani anga ndidzaŵabwezera chilango, amene amadana nane ndidzaŵalanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:38

Komabe pakuti Mulungu ngwachifundo, adaŵakhululukira machimo ao, ndipo sadaŵaononge. Kaŵirikaŵiri ankadziletsa kukwiya, sadalole kuti mkwiyo wake wonse uyake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 85:3

Mudaleka ndithu ukali wanu woopsa, mudaletsa mkwiyo wanu woyaka moto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:8

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima, ndi wosakwiya msanga, ndipo chikondi chake chosasinthika nchachikulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:29

Wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri, koma wofulumira kupsa mtima amaonetsa uchitsiru wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:19

Munthu wa ukali woopsa adzalandira chilango chomuyenerera, pakuti ukamlekerera wotereyu, zidzaipa koposa kale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:3

Nchaulemu kwa munthu kumalewa mikangano, koma aliyense wopusa amakonda kulongolola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:19

Kuli bwino kukhala ku chipululu kupambana kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wopsa mtima msanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:24-25

Usachite naye chibwenzi munthu wopsa mtima msanga, ndipo usamayenda naye munthu waukali, kuwopa kuti ungadzaphunzireko mayendedwe ake, ndi kukodwa mu msampha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:4

Mkwiyo umadzetsa nkhanza, kupsa mtima kumachititsa zoopsa, koma nsanje imabweretsa zoipa zopambana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:22

Munthu wamangaŵa amautsa mikangano, munthu wokalipakalipa amabweretsa zolakwa zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 13:13

Tsono ndidzagwedeza mlengalenga, ndipo dziko lapansi lidzachoka pa maziko ake. Zonsezi zidzachitika chifukwa cha ukali wa Ine Chauta Wamphamvuzonse pa tsiku la mkwiyo wanga woopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 34:2

Pakuti Chauta waŵakwiyira anthu a mitundu yonse, waŵapsera mtima magulu ao onse ankhondo, watsimikiza kuti adzaonongedwa, waŵapereka kuti aphedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 48:9

“Kuti anthu alemekeze dzina langa ndikuchedwetsa mkwiyo wanga. Kuti anthu aone ulemerero wanga ndikukulezera ukali wanga, kuti ndisakuwononge kotheratu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:8

Ndidaakufulatira pa mphindi yaing'ono ndili wokwiya zedi, koma ndidzakuwonetsa chikondi changa mpaka muyaya,” akuterotu Chauta, Momboli wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:16

“Ndine amene ndidalenga anthu anga ndi kuŵapatsa mpweya wa moyo, motero sindidzapitirira kukangana nawo kapena kuŵakwiyira mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 63:3

“Ndapondereza ndekha anthu a mitundu ina ngati mphesa, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adadzandithandiza. Ndidaŵapondereza ndili wokwiya, magazi ao nkufalikira pa zovala zanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 3:12

Pita ukalalike kumpoto uthenga uwu wakuti, “ ‘Israele wosakhulupirikawe, bwerera,’ akuterotu Chauta. ‘Ukali wanga sudzapitirira, poti ndine wachifundo. Sindidzakukwiyira mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 10:24

Langizeni, Inu Chauta, koma mwachilungamo. Musandikwiyire kuti mungandiwononge.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 30:24

Mkwiyo wa Chauta sudzachoka mpaka utatsiriza kuchita zonse zimene mtima wa Chautayo ukufuna. Mudzamvetsa zimenezi masiku akubwerawo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 51:45

Tulukani m'Babiloni, inu anthu anga! Fulumirani, pulumutsani moyo wanu! Thaŵani mkwiyo woopsa wa Chauta!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Maliro 3:66

Inu Chauta, muŵapirikitse mwaukali, muŵaonongeretu pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 7:8

Posachedwapa ndidzakukwiyirani, ndipo ukali wanga udzathera pa inu. Ndidzagamula mlandu wanu potsata makhalidwe anu, ndipo ndidzakulangani chifukwa cha zonyansa zanu zochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:42

Pamenepo ndidzaleka, ukali wanga udzatha, ndipo sindidzakuchitiranso nsanje. Ndidzakhala phee, osachitanso ukali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 25:17

Ndidzaŵalipsira koopsa ndi kuŵalanga mwaukali kwambiri. Ndikadzaŵalanga choncho, adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 38:18-19

Pa nthaŵi imeneyo, pamene Gogi adzabwera kudzalimbana ndi dziko la Israele, mkwiyo wanga udzayaka zedi. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanga woyakawo, ndikulumbira kuti kudzachita chivomezi chachikulu m'dziko lonse la Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 11:9

Sindidzalekerera kuti mkwiyo wanga ukulangitse, sindidzamuwononganso Efuremu, pakuti Ine ndine Mulungu osati munthu. Ine, Woyera uja, ndili nawe, ndipo sindidzabwera kudzakuwononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 2:13

Ng'ambani mitima yanu, osati zovala zanu chabe.” Bwererani kwa Chauta, Mulungu wanu, poti Iye ngwokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wa chikondi chosasinthika. Nthaŵi zonse ndi wokonzeka kukhululuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yona 4:2

Tsono adapemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, nzimenezitu zimene ndinkaopa ndili kwathu. Nchifukwa chake ndidaayesetsa kuthaŵira ku Tarisisi. Ndidaadziŵa kuti Inu ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo, woleza mtima ndi wa chikondi chosasinthika, ndiponso wokhululukira machimo nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nahumu 1:2-3

Chauta ndi Mulungu wansanje ndiponso wolipsira. Chauta amalanga, ndipo ndi wamkali. Chauta amalipsira amaliwongo ake amakwiyira adani ake. Chauta ndi wamphamvu zedi. Ndi wosakwiya msanga, komabe sadzalola kuti munthu wochimwa akhale wosalangidwa. Pamene amayenda pamachitika kamvulumvulu ndi mphepo yamkuntho, mitambo ndiye fumbi limene mapazi ake amachititsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zefaniya 2:3

Funafunani Chauta, inu nonse odzichepetsa, inu amene mumamvera malamulo ake. Chitani zolungama, khalani odzichepetsa. Mwina mwake mudzatha kupulumuka pa tsiku la mkwiyo wa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zefaniya 3:8

Chauta akunena kuti, “Nchifukwa chake mundidikire, mudikire tsiku limene ndidzakuimbeni mlandu. Pakuti ndatsimikiza zosonkhanitsa mitundu ya anthu pamodzi ndi maufumu onse, kuti ndiŵaonetse kusakondwa kwanga amve ululu wa ukali wanga. Dziko lonse lapansi lidzapserera ndi moto waukali wa mkwiyo wanga.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 1:15

Ndaŵakwiyira kwambiri anthu a mitundu ina amene ali pa mtendere. Pamene ndinkakwiyira anthu anga motsinira, mpamene anthu enawo ankakakatira kuzunza anthu anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:44

Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muzikonda adani anu ndipo muziŵapempherera amene amakuzunzani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:12-13

Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nayamba kutulutsa onse amene ankachita malonda m'menemo. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama, ndiponso mipando ya ogulitsa nkhunda. Adaŵauza kuti, “Malembo akuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo.’ Koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:33

“Njoka inu, ana a mamba, mudzachipeŵa bwanji chilango cha ku Gehena?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 3:5

Pamenepo Yesu mtima wake udamuŵaŵa, poona kuti anali anthu okanika chotero, ndipo adaŵayang'ana ndi mkwiyo. Tsono adalamula munthuyo kuti, “Tambalitsa dzanja lako.” Iye adalitambalitsa, ndipo dzanja lakelo lidakhalanso bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:28-29

Muziŵafunira madalitso amene amakutembererani, muziŵapempherera amene amakuvutitsani. Ngati munthu akumenya pa tsaya, uperekere linalonso. Ndipo munthu akakulanda mwinjiro wako, umlole atenge ndi mkanjo womwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:54-55

Ophunzira ake, Yakobe ndi Yohane ataona zimenezi adati, “Ambuye, bwanji tiitane moto kuchokera Kumwamba kuti udzaŵapsereze anthu ameneŵa?” Koma Yesu adacheuka nadzudzula ophunzirawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 2:15-16

Apo Yesu adapanga mkwapulo wazingwe nayamba kuŵatulutsira onse kunja, pamodzi ndi nkhosa ndi ng'ombe zao zomwe. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama aja, naŵamwazira ndalama zao. Ndipo adalamula ogulitsa nkhunda aja kuti, “Izi zitulutseni muno. Nyumba ya Atate anga musaisandutse nyumba yochitiramo malonda.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:18

Mkwiyo wa Mulungu ukuwoneka kuchokera Kumwamba. Amakwiyira anthu chifukwa cha kusalungama kwao konse ndi kusamchitira ulemu. Kusalungama kwaoko kumaŵalepheretsa kudziŵa zoona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:5

Koma chifukwa ndiwe wa mtima wokanika ndi wosafuna kutembenuka, ukudzisungira chilango cha Mulungu. Chilangocho chidzakugwera pa tsiku limene adzaonetse mkwiyo wake ndiponso kuweruza kwake kolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:9

Ndiye popeza kuti tsopano chifukwa cha magazi ake tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa pamenepo ku mkwiyo wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:21

Musagonjere zoipazo, koma gonjetsani zoipa pakuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:4

pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokutsogolera kuchita zabwino. Koma ngati ukuchita zoipa uwope, pakuti ali ndi mphamvu ndithu zokulanga. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wogwetsa mkwiyo wa Mulungu pa wochita zoipa, pomulanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:5

Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 12:20

Ndikuwopa kuti ndikadzabwera kwanuko, mwina nkudzakupezani muli osiyana ndi m'mene ndikadafunira. Ndikuwopa kuti mwina inunso nkudzandipeza ine wosiyana ndi m'mene mukadafunira. Ndikuwopanso kuti mwina ine nkudzapeza kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusinjirirana, ugogodi, kudzitukumula, ndiponso chisokonezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-21

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:6

Munthu wina aliyense asakupusitseni ndi mau onyenga, pakuti zinthu zotere ndizo zimadzetsa ukali wa Mulungu pa anthu omupandukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:6-8

Chifukwa cha zinthu zotere Mulungu amaŵakwiyira anthu osamumvera. Inunso kale makhalidwe anu anali omwewo, munkachita zomwezo. Koma tsopano musachitenso zonsezi, monga kukalipa, kukwiya, kuipa mtima, ndi mijedu. Pakamwa panu pasamatulukenso mau otukwana kapena onyansa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:9

Paja Mulungu sadatisankhe kuti tidzaone mkwiyo wake, koma kuti tidzalandire chipulumutso kwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 2:8

Ndikufuna kuti paliponse amuna popemphera azikweza manja ao kwa Mulungu momchitira ulemu, mopanda mkwiyo kapena kukangana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:24

Ndipo mtumiki wa Ambuye asamakhala wokanganakangana ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa onse, mphunzitsi wokhoza, munthu wodziŵa kupirira mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 1:7

Woyang'anira mpingo azikhala wosapalamula konse, chifukwa ali ngati kapitao m'banja la Mulungu. Asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena chidakwa, kapena wandeu, kapenanso wokonda kudya phindu la ndalama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 3:10-11

Tsono ndidaukwiyira mbadwowo, ndipo ndidati, ‘Nthaŵi zonse amasokera mumtima mwao, sanaphunzirebe njira zanga.’ Motero ndili wokwiya ndidalumbira kuti, ‘Sadzaloŵa konse mu mpumulo umene ndidaŵakonzera.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:7

Nchifukwa chake Mulungu adaikanso tsiku lina, lotchedwa kuti “Lero”. Patapita nthaŵi yaitali Mulungu adalankhula za tsiku lomweli kudzera mwa Davide ponena mau aja tatchula kaleŵa, akuti, “Lero, mukamva mau a Mulungu, musaumitse mitima yanu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:30-31

Paja tikumdziŵa kale amene adati, “Kulipsira nkwanga, ndidzakhaulitsa ndine.” Adatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.” Kugwa m'manja mwa Mulungu wamoyo ndi chinthu choopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:29

Paja Mulungu wathu ndi moto wopsereza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:19-20

Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso. Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu. Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:1-2

Kodi nkhondo zimachokera kuti? Kukangana pakati panu kumachokera kuti? Kodi suja zimachokera ku zilakolako zanu zathupi, zimene zimachita nkhondo mwa inu? Mudzichepetse pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani. Abale, musamasinjirirana. Wosinjirira mbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo a Mulungu. Koma ukaweruza Malamulo a Mulungu, ndiye kuti sukuchita zimene Malamulowo akunena, ukudziyesa woweruza. Mulungu yekha ndiye wopanga Malamulo ndiponso woweruza. Ndiyenso wotha kupulumutsa ndi kuwononga. Nanga iwe ndiwe yani kuti uziweruza mnzako? Onani tsono, inu amene mukuti, “Lero kapena maŵa tipita ku mzinda wakutiwakuti, ndipo tikachitako malonda chaka chimodzi kuti tikaphe ndalama,” m'menemo inuyo zamaŵa simukuzidziŵa. Kodi moyo wanu ngwotani? Pajatu inu muli ngati utsi chabe, umene umangooneka pa kanthaŵi, posachedwa nkuzimirira. Kwenikweni muyenera kumanena kuti, “Ambuye akalola, tikakhala ndi moyo, tidzachita chakutichakuti.” Koma monga zilirimu, mumanyada ndi kudzitama. Kunyada konse kotere nkoipa. Munthu akadziŵa zabwino zimene ayenera kuchita, napanda kuzichita, ndiye kuti wachimwa. Mumalakalaka zinthu, koma zimakusoŵani, nchifukwa chake mumapha munthu. Mumasirira zinthu, koma simungathe kuzipeza, nchifukwa chake mumamenyana, nkumachita nkhondo. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:1

Nchifukwa chake tayani choipa chonse, kunyenga konse, chiphamaso, kaduka ndi masinjiriro onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:23

Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sadabwezere chipongwe. Pamene ankazunzika, Iye sadaopseze, koma adapereka zonse kwa Mulungu amene amaweruza molungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:9

Anthu okuchitani choipa, osaŵabwezera choipa, okuchitani chipongwe osaŵabwezera chipongwe. Koma inu muziŵadalitsa, pakuti inuyo Mulungu adakuitanirani mkhalidwe wotere, kuti mulandire madalitso ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:8

Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:8

Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:9

Ndiye kuti pamene anthu osamala za Mulungu akuyesedwa, Iye amadziŵa kuŵapulumutsa kwake. Koma amadziŵanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:9

Sikuti akuzengereza kuchita zimene adalonjeza, monga m'mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:15

Aliyense wodana ndi mnzake, ndi wopha anthu. Ndipo mukudziŵa kuti aliyense wopha anthu, alibe moyo wosatha mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:18

Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:16

Wina akaona mbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere, ndipo Mulungu adzampatsa moyo mbale wakeyo. Ndikunenatu za ochita tchimo losadzetsa imfa. Koma lilipo tchimo lina lodzetsa imfa, za tchimo limenelo sindikunena kuti apemphere ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 6:16-17

Iwowo ankafuulira mapiri ndi matanthwewo kuti, “Tigwereni ndi kutivundikira, kuti wokhala pa mpando wachifumu uja angatiwone, ndipo kuti tipulumuke ku chilango cha Mwanawankhosayo. Lafikadi tsiku loopsa la mkwiyo wao, ndipo angathe kulimbapo ndani?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 11:18

Anthu akunja adakalipa, koma yafika nthaŵi yoonetsa mkwiyo wanu, ndiye kuti nthaŵi yoweruza anthu akufa. Yafika nthaŵi yoti mupereke mphotho kwa atumiki anu, aneneri, ndi kwa anthu anu, ndiye kuti onse, ang'onoang'ono ndi akuluakulu, amene amaopa dzina lanu. Yafika nthaŵi yoti muŵaononge amene akuwononga dziko lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 14:10

nayenso adzamwako vinyo wa ukali wa Mulungu. Vinyo wake adzathiridwa, popanda kanthu kochepetsa mphamvu yake, m'chikho cha mkwiyo wa Mulungu. Munthuyo adzazunzidwa ndi moto ndi miyala yasulufure yoyaka. Zimenezi zidzachitikira pamaso pa angelo a Mulungu, ndi Mwanawankhosa uja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 14:19

Pamenepo mngelo uja adakayambadi ntchitoyo ndi chikwakwa chake, nadula mphesa zonse za pa dziko lapansi, nkuziponya m'chopondera mphesa cha ukali woopsa wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 15:1

Pambuyo pake ndidaona Kumwamba chizindikiro china chachikulu ndi chododometsa: angelo asanu ndi aŵiri okhala ndi miliri isanu ndi iŵiri. Miliriyo ndi yotsiriza, pakuti ukali wa Mulungu uthera pa imeneyi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 15:7

Chimodzi mwa Zamoyo zinai zija chidapereka mikhate isanu ndi iŵiri yagolide kwa angelo asanu ndi aŵiri aja. Mikhateyo inali yodzaza ndi ukali wa Mulungu amene ali ndi moyo mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 16:1

Pambuyo pake ndidamva mau amphamvu ochokera m'Malo Opatulika aja. Adauza angelo asanu ndi aŵiri aja kuti, “Pitani, kathireni pa dziko lapansi ukali wa Mulungu, umene uli m'mikhate isanu ndi iŵiri ija.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 16:19

Mzinda waukulu uja udagaŵika patatu, ndipo mizinda ya m'maiko ena onse idagwa. Mulungu adakumbukira Babiloni wamkulu uja, ndipo adamumwetsa chikho cha vinyo wa mkwiyo wake waukali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 19:15

M'kamwa mwake munali lupanga lakuthwa lotulukira kunja, loti adzalangire mitundu ya anthu. Adzaŵalamulira ndi ndodo yachitsulo, ndipo m'chopondera mphesa adzaponda mphesa za vinyo wa mkwiyo waukali wa Mulungu Mphambe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:15

Aliyense wopezeka kuti dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo lija, adaponyedwa m'nyanja yamotoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:8

Koma anthu amantha, osakhulupirika, okonda zonyansa, opha anzao, ochita zadama, ochita zaufiti, opembedza mafano, ndi anthu onse onama, malo ao ndi m'nyanja yodzaza ndi moto ndi miyala ya sulufure woyaka. Imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 22:12

Yesu akuti, “Mvetsetsani, ndikubwera posachedwa. Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense molingana ndi zimene adachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, ulemerero ndi ulemu zikhale zanu! Mulungu wanga wakumwamba, ndikubwerera kwa Inu chifukwa ndikudziwa kuti ndikufunika kukhalapo kwanu kulamulira moyo wanga kuti mtima wanga udzazidwe ndi kubwezeretsedwa ndi kumasulidwa. M'dzina la Yesu, ndikupemphani kuti mundithandize kuganiza ndi kuzindikira mwanzeru zinthu, osachita zinthu mopupuluma ndi mosasamala, koma kudzera mu mpanda wa Mzimu Woyera wanu ndiphunzire kulamulira maganizo ndi malingaliro anga. Mundidziwitse tanthauzo la mawu anu akuti: "Mayankho ofatsa amathetsa mkwiyo; koma mawu okalipa amayatsa ukali." Ndikudziwa kuti ndawaletsa anthu ondizungulira powamenya ndi mawu anga, ndikuwapweteka, ndipo zotsatira zake ndikuwononga moyo wanga ndi wa banja langa. Ndidziwitseni kuyenda mogwirizana ndi zomwe zili m'mawu mwanu kuti kukhalapo kwanu kukhale patsogolo pa chilichonse. Ndithandizeni kudikira ndi kutseka mipata yonse ya mdani, mundidziwitse kuti mkwiyo umangondipangitsa kukhala ndi khoma lolekanitsa ndi anthu ondizungulira komanso kufesa mkwiyo, ukali ndi chisoni. Ndikutsutsa mkwiyo, ukali ndi kupsa mtima. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa