Ulemu ndi chinthu chomwe chingakhudze aliyense, kaya wachokera kuti, udindo wake, kapena chipembedzo chake. M’Baibulo muli mavesi omveka bwino onena za kusalemekeza ndi zotsatira zake. Deuteronomo 27:16 imati: “Wotembereredwa iye amene wanyoza atate wake kapena amake.” Ndipo anthu onse adzati, “Amen.”
Kusalemekeza si chinthu choyenera kudzitamandira nacho. M'malo mwake, ngati mumtima mwako ukusalemekeza Mulungu, makolo ako, kapena akuluakulu, uyenera kudzichepetsa pamaso pa Mulungu ndi kupempha mtima wowongoka ndi wangwiro. Umu ndi momwe ungapulumutsire moyo wako ku temberero, chifukwa Mulungu sawalekerera anthu a mitima yoipa ndi opanduka omwe sakonda kutsatira malamulo ake.
Ndikufuna kuti tiganizire za zochita zathu ndi zotsatira zake pa moyo wathu ndi wa ena. Kusalemekeza kungatitsogolere m'njira zamdima, kutali ndi choonadi ndi chilungamo. Koma kufunafuna ulemu kungatithandize kukhala moyo waukhristu ndi wachitsanzo chabwino.
Ndikukulimbikitsa kufunafuna Mulungu ndi kuphunzira Malemba, chifukwa ndi momwe tingaphunzirire kupewa kusalemekeza ndi kufunafuna moyo wopatulika ndi waulemu. Zikomo.
Nchifukwa chake Mulungu adaŵasiya kuti azingochita zonyansa zimene mitima yao inkalakalaka, mpaka kunyazitsa matupi ao.
Kodi ine sindidzachita manyazi poyenda pakati pa anthu? Ndipo iwe udzakhala mmodzi mwa zitsiru pakati pa Aisraele. Nchifukwa chake tsono, chonde, ndapota nawe, ulankhule ndi amfumu, poti iwowo sadzandikaniza kuti ndikwatiwe nawe.”
“Atembereredwe aliyense wosalemekeza atate ndi amai ake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
“Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa.
Wopondereza mmphaŵi, amachita chipongwe Mlengi wake, koma wochitira chifundo osauka, amalemekeza Mlengi wake.
Mukandipeza wolakwa, tsoka langa! Ngakhale mundipeze wosalakwa, ndigwetsabe nkhope, pakuti ndagwidwa ndi manyazi, poona mavuto angaŵa.
pakumva mau a anthu onditonza ndi onditukwana, poona mdani wanga ndi munthu wolipsira.
Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo. Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira. Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye. Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima. Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro. Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse. Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”
Ndipo mwana wamkazi wa wansembe aliyense akadziipitsa pokhala wachiwerewere, amaipitsa bambo wake. Mwanayo ayenera kumtentha pa moto.
Aliyense mwa inu aziwopa mai wake ndi bambo wake. Muzisunga masiku anga a Sabata, Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
Inu Ambuye, kunyoza kuja kumene anthu a mitundu ina adakunyozani, muŵabwezere kasanunkaŵiri.
Umphaŵi ndi manyazi zimagwera wonyozera mwambo, koma munthu womvera chidzudzulo amalemekezeka.
Kuwopa Chauta kumaphunzitsa nzeru, ndipo ndi kudzichepetsa ndi ulemu, chili patsogolo nkudzichepetsa.
Kumbukirani kuti amene akundinyozawo ndi adani anu, Inu Chauta, iwo akunyoza Wodzozedwa wanu paliponse pamene waponda.
Kapolo wochita zinthu mwanzeru adzalamula mwana wa mfulu wochita zamanyazi, kapoloyo adzagaŵana nawo choloŵa ngati mmodzi mwa abale.
Paja Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndidaalonjeza kuti anthu a pa banja lako ndi a pa banja la atate ako, azidzanditumikira nthaŵi zonse. Koma tsopano ndikuti zimenezo zithe basi! Ndidzachitira ulemu anthu ondichitira ulemu, koma anthu ondinyoza, Inenso ndidzaŵanyoza.
Maliseche ako adzakhala poyera, ndipo udzachita manyazi kwambiri. Ndidzalipsira, ndipo palibe amene adzandiletsa.”
Mbiri yabwino ndi yofunika kupambana chuma chambiri, kupeza kuyanja nkopambana siliva ndi golide.
Popeza kuti mudalandira manyazi, manyozo ndi zotukwana moŵirikiza, tsopano mudzalandira chigawo cha dziko lanu moŵirikizanso. Chimwemwe chanu chidzakhala chamuyaya.”
Paja Mulungu adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’
Makono ana aamuna akunyoza atate ao, ana aakazi akuukira amai ao. Mtengwa akulongolozana ndi mpongozi wake, nkhondo ndi anansi.
Koma amene udzachite manyazi ndiwe ndipo onse adzakunyoza kwambiri. Tsopano imwa ndiwe, mpaka kudzandira. Chikho cha chilango cha Chauta chikupeza, ndipo manyazi adzaphimba ulemerero wako.
Tsono popeza kuti iwo sadalabadireko za kumvera Mulungu, Mulunguyo adaŵasiya m'maganizo ao opusa, kotero kuti amachita zosayenera. Mitima yao idadzaza ndi zosalungama zamitundumitundu, monga kuipa, umbombo ndi dumbo. Amangolingalira za kaduka, za kupha anthu, za ndeu, za kunyenga, ndi za njiru. Amachita ugogodi, Umasimba za Mwana wake, Yesu Ambuye athu. Poyang'anira umunthu wake, kholo lake ndi Davide, amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao.
Chauta akuti, “Ndamva kunyoza kwa Amowabu, ndiponso kutukwana kwa Aamoni, m'mene anyozera anthu anga ndi m'mene adzikuzira m'dziko mwao.
Mumalinyoza pakupereka chakudya chosayenera pa guwa langa lansembe. Inu mumafunsabe kuti, kodi ife takunyozani bwanji? Mwandinyoza pakuganiza kuti tebulo la Chauta nlonyozeka.”
Udziŵe kuti pa masiku otsiriza kudzafika nthaŵi ya zovuta. Tsono iwe wakhala ukunditsatira m'zophunzitsa zanga, mayendedwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, kupirira kwanga, mazunzo anga, ndi masautso anga, monga amene adaandigwera ku Antiokeya, ku Ikonio ndi ku Listara. Ndidaazunzikadi koopsa! Koma Ambuye adandipulumutsa pa zonsezi. Onse ofuna kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi, m'menemo anthu ochimwa ndi onyenga, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanyenga ena nkumanyengedwanso iwo omwe. Koma iwe, limbika pa zimene waphunzira ndipo wadziŵa kuti nzoona, paja ukuŵadziŵa amene adakuphunzitsa. Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu. Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse. Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu. Adzakhala opanda chifundo, osapepeseka, ndi osinjirira anzao. Adzakhala osadzigwira, aukali, odana ndi zabwino, opereka anzao kwa adani ao. Adzakhala osaopa chilichonse, odzitukumula, okonda zosangalatsa m'malo mokonda Mulungu. Adzasamala maonekedwe ake okha a chipembedzo, nkumakana mphamvu zake. Anthu otere uziŵalewa.
Yesu adati, “Ine sindidagwidwe ndi mizimu yoipa. Ndimalemekeza Atate anga, koma inu mumandipeputsa.
Wina akatemberera bambo wake kapena mai wake, moyo wake udzatha ngati nyale yozima mu mdima wandiweyani.
Aliyense amene amaseka bambo ndi kumanyozera kumvera mai, makwangwala akuchigwa adzamkoloola maso, ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.
Iwe wonyadira Malamulo a Mulungu, bwanji umachititsa Mulungu manyazi pakuphwanya Malamulowo?
Kodi kapena woumba sangathe kuumba mbiya ziŵiri ndi dothi lomwelo, ina ya masiku apadera ina ya masiku onse?
Anthu ako akhala akunyoza atate ao ndi amai ao. Akhala akuzunza alendo okhala nawe, akhalanso akusautsa ana amasiye ndi akazi amasiye.
Thupi loikidwa m'manda, ndi lonyozeka ndi lofooka, koma likadzauka lidzakhala lokongola ndi lamphamvu.
Muzilemekeza anthu onse. Muzikonda akhristu anzanu. Khalani anthu oopa Mulungu. Mfumu yaikulu koposa ija muziipatsa ulemu.
Anthu adzazunzana, aliyense adzazunza mnzake. Anyamata adzachita chipongwe akuluakulu, ndipo anthu achabechabe adzanyoza olemekezeka.
Anthu amatilemekeza, komanso amatinyoza. Amatinenera zoipa, komanso zabwino. Anthu amatiyesa onyenga, komabe ndife oona.
Tsono muzipereka kwa onse zimene zikukhalira iwowo: msonkho kwa okhometsa msonkho, zolipira kwa oyenera kuŵalipira. Muzilemekeza oyenera kuŵalemekeza, ndi kuchitira ulemu oyenera kuŵachitira ulemu.
Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa: maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa,
Popeza kuti ndinu anthu a Mulungu, ndiye kuti dama kapena zonyansa, kapena masiriro oipa zisatchulidwe nkomwe pakati panu. Amatero chifukwa Mpingowo ndi thupi lake, ndipo ife ndife ziwalo zake. Paja mau a Mulungu akuti, “Nchifukwa chake mwamuna adzasiye atate ndi amai ake, nkukaphatikizana ndi mkazi wake, kuti aŵiriwo asanduke thupi limodzi.” Mau ameneŵa akutiwululira chinsinsi chozama, ndipo ndikuti chinsinsicho nchokhudza Khristu ndi Mpingo. Komabe akunenanso za inu, kuti mwamuna aliyense azikonda mkazi wake monga momwe amadzikondera iye mwini, ndiponso kuti mkazi aliyense azilemekeza mwamuna wake. Ndiponso musamalankhule zolaula, zopusa, kapena zopandapake, koma muzilankhula zoyamika Mulungu.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo. Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.
Ambuye adati, “Anthu aŵa amati amapemphera kwa Ine, koma mau ao ndi opanda tanthauzo, ndipo mitima yao ili kutali ndi Ine. Chipembedzo chao ndi kungotsata chabe malamulo ongoŵaloŵeza pamtima, malamulo ochokera kwa anthu.
Inunso amuna, muzikhala moŵamvetsa bwino akazi anu. Muziŵachitira ulemu popeza kuti iwowo ndi mtundu wofookerapo, ndiponso ngolandira nanu pamodzi mphatso ya Mulungu, imene ili moyo wosatha. Muzitero, kuti pasakhale kanthu koletsa mapemphero anu.
Munthu wabwino anzake adzamkumbukira ngati dalitso, pamene woipa, mbiri yake idzatha ngati chinthu choola.
Koma tsopano musachitenso zonsezi, monga kukalipa, kukwiya, kuipa mtima, ndi mijedu. Pakamwa panu pasamatulukenso mau otukwana kapena onyansa.
Zoonadi, onse okhulupirira Inu asaŵachititse manyazi, koma muchititse manyazi onse ochita dala zosakhulupirika.
Thaŵani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe. Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe? Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.
M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.
Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu, koma uchimo umachititsa manyazi mtundu uliwonse.
Pa zonse iwe wemwe ukhale chitsanzo cha ntchito zabwino. Zophunzitsa zako zikhale zoona, ndipo uziphunzitse mwaulemu. Mau ako akhale oona, kuti anthu asadzathe kuŵatsutsa. Motero wotsutsana nawe adzachita manyazi, atasoŵa kalikonse koipa kuti atinenere.
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
Inu Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, musalole kuti ndiŵachititse manyazi anthu okhulupirira Inu. Inu Mulungu wa Israele, musalole kuti anthu okufunafunani anyozeke chifukwa cha ine. Pakuti ndanyozedwa, nkhope yanga yagwidwa ndi manyazi chifukwa cha Inu.
Ngati wina aliyense saŵapatsa zofunika achibale ake, makamaka a m'banja mwake momwe, ameneyo wataya chikhulupiriro chake, ndipo kuipa kwake nkoposa kwa munthu wosakhulupirira.
Muzikhala ngati ana omvera, osatsatanso zimene munkalakalaka pamene munali osadziŵa. Koma monga Iye amene adakuitanani ali woyera mtima, inunso khalani oyera mtima m'makhalidwe anu onse. Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.”
Kulemekeza Chauta ndiye chiyambi cha nzeru, kudziŵa Woyera uja nkukhala womvetsa bwino zinthu.
Tsiku lonse ndimangodziwona kuti ndine munthu wopandapake. Nkhope yanga yagwa chifukwa cha manyazi, pakumva mau a anthu onditonza ndi onditukwana, poona mdani wanga ndi munthu wolipsira.
Iwe wonyadira Malamulo a Mulungu, bwanji umachititsa Mulungu manyazi pakuphwanya Malamulowo? Ndi monga Malembo anenera kuti, “Anthu akunja amanyoza Mulungu chifukwa cha inu Ayudanu.”
Mkwapulo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru, koma mwana womamlekerera amachititsa amake manyazi.
Tsoka kwa amene zoipa amaziyesa zabwino ndipo zabwino amaziyesa zoipa, amene mdima amauyesa kuŵala, ndipo kuŵala amakuyesa mdima, amene zoŵaŵa amaziyesa zozuna, ndipo zozuna amaziyesa zoŵaŵa! Tsoka kwa amene amadziwona ngati anzeru ndipo amadziyesa ochenjera!
Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse.
Munthu wonyoza malangizo amangodzinyoza yekha, koma wovomera kudzudzula amapindula nzeru yomvetsa zinthu.
Kodi inu simudziŵa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu? Ngati wina aliyense aononga nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo. Pakuti nyumba ya Mulungu ndi yopatulika, ndipo nyumbayo ndinu amene.
Amene amalalatira mmphaŵi, amanyoza Mlengi wake. Amene amakondwerera tsoka la mnzake adzalangidwa.
Tchinjirizani moyo wanga ndi kundipulumutsa. Musalole kuti andichititse manyazi, pakuti ndikuthaŵira kwa Inu.
Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.
Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma wopusa amangopitirira ndipo amanong'oneza bondo.
Mkazi wabwino ali ngati chisoti chaulemu kwa mwamuna wake, koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda chamafinya kwa mwamuna wake.
Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi.
Aliyense mwa inu adziŵe kulamula thupi lake, pakulilemekeza ndi kulisunga bwino, osalidetsa. Musamangotsata zilakolako zonyansa, monga amachitira akunja, amene sadziŵa Mulungu.
Chauta amasamalira moyo wa anthu angwiro, ndipo choloŵa chao chidzakhalapo mpaka muyaya. Pa nthaŵi ya mavuto sadzazunzika, pa nthaŵi yanjala, adzakhala nazo zakudya zochuluka.
Kupusa kumakhala mumtima mwa mwana, koma ndodo yomlangira mwanayo idzachotsa kupusako.
Chifukwa cha zimenezi Mulungu adaŵasiya kuti azitsata zilakolako zochititsa manyazi. Ngakhale akazi omwe adaleka machitidwe achibadwa pa zachikwati, namatsata machitidwe ena otsutsana ndi achibadwawo. Chimodzimodzinso amuna, adaleka machitidwe achibadwa osirira akazi, nkumakhumbana amuna okhaokha. Ankachitana zamanyazi, motero adadziitanira chilango choyenera molingana ndi zochita zao zopotokazo.
Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo amuna ndi akazi ao azikhala okhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzaŵalanga.
Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziŵa zinthu, munthu wodekha mtima ndiye womvetsa zinthu. Nchitsiru chomwe chikakhala chete, chimakhala ngati munthu wanzeru. Chikasunga pakamwa chimakhala ngati munthu wochenjera.
Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, koma muziŵalera bwino pakuŵasungitsa mwambo ndi malangizo a Ambuye.
Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake, koma mwana wopusa amanyoza amai ake.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.
Chipongwe cha osasamala za anzao chimadzetsa mkangano, koma omvera malangizo a anzao ndiwo ali ndi nzeru.
Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.
Amene amachita ndeu ndi atate ake ndi kupirikitsa amai ake, ameneyo ndi mwana wochititsa manyazi ndiponso wonyozetsa.
Munthu wonyada ndi wodzikuza amamtchula “Mnyodoli,” chifukwa amachita zinthu modzitama ndi mwachipongwe.
Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.
Amene amatsata malamulo ndiye mwana wanzeru, koma amene amayenda ndi anthu adyera, amachititsa atate ake manyazi.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Si chinthu choloŵa m'kamwa mwa munthu chimene chimamuipitsa ai, koma chotuluka m'kamwa mwake ndiye chimene chimamuipitsa.”
Zoonadi, ana ndi mphatso yochokera kwa Chauta, zidzukulu ndi mphotho yake. Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo. Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.
Munthu wachikulire usamdzudzule mokalipa, koma umchenjeze monga ngati bambo wako. Amuna achinyamata uzikhalitsana nawo ngati abale ako. Akhale mai woti anthu amamchitira umboni wakuti amachitadi ntchito zabwino. Akhale woti ankalera ana ake bwino, ankalandira bwino alendo, ankasambitsa mapazi a anthu a Mulungu, ndipo ankathandiza anthu amene anali m'mavuto. Akhalenso mai woti ankadzipereka pa ntchito zonse zabwino. Koma azimai amasiye a zaka zochepera uzikana kuŵalemba m'gulu limeneli. Pajatu zilakolako zao zikayamba kuŵavutitsa nkuŵalekanitsa ndi Khristu, amangofuna kukwatiwanso. Pamenepo amapezeka olakwa, chifukwa chosasunga lonjezo lao loyamba. Kuwonjezera pamenepo, amagwa m'chizoloŵezi cha kungokhala khale, motero amangoyendayenda ku nyumba za anthu. Tsonotu samangokhala khale chabe ai, amachitanso miseche nkumaloŵera za eni, ndi kukhala omalankhula zimene samayenera kulankhula. Nchifukwa chake nkadakonda kuti azimai amasiye a zaka zochepera azikwatiwanso, abale ana, ndipo azisamala bwino panyumba pao, kuti adani athu asapeze mpata wotisinjirira. Paja alipo kale azimai amasiye ena amene adapatukapo nkumatsata Satana. Koma ngati mai wina aliyense wachikhristu ali ndi achibale amene ali azimai amasiye, aziŵasamala iyeyo, osasenzetsa mpingo katundu wakeyo. Motero mpingo udzatha kusamala azimai amasiye opanda oŵathandiza. Akulu a mpingo otsogolera mpingo bwino, akhale oyenera kuŵalemekeza moŵirikiza, makamaka amene amagwira ntchito yolalika mau a Mulungu ndiponso yophunzitsa. Paja Malembo akuti, “Usaimange pakamwa ng'ombe imene ikupuntha tirigu.” Penanso akuti, “Wantchito ngwoyenera kulandira malipiro ake.” Usamamvere mau oneneza mkulu wa mpingo, pokhapokha ngati pali mboni ziŵiri kapena zitatu. Azimai achikulire uzikhalitsana nawo ngati amai ako, ndipo azimai a zaka zochepa uzikhalitsana nawo ngati alongo ako, m'kuyera mtima kwenikweni.
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense wopsera mtima mbale wake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu. Aliyense wonena mnzake kuti, ‘Wopandapake iwe,’ adzayenera kuzengedwera ku Bwalo Lapamwamba. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru,’ adzayenera kukaponyedwa ku moto wa Gehena.
Enanso ndi aŵa malangizo a anthu anzeru: Kukondera pozenga milandu si chinthu chabwino. Amene amauza munthu woipa kuti, “Ndiwe wosalakwa,” anthu adzamtemberera, ndipo mitundu ya anthu idzaipidwa naye. Koma aweruzi amene amalanga anthu oipa adzapeza bwino, ndipo adzakhala ndi madalitso ambiri.
Koma ndidaakulemberani kuti musamayanjane ndi munthu amene amati ndi mkhristu, pamene chikhalirecho ndi munthu wadama, kapena waumbombo, wopembedza mafano, waugogodi, chidakwa, kapena wachifwamba. Munthu wotere musamadye naye nkomwe.
Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano. Chifukwa cha zinthu zotere Mulungu amaŵakwiyira anthu osamumvera.
Bambo wa mwana waulemu adzakondwa kwambiri. Wobala mwana wanzeru adzasangalala naye. Atate ako ndi amai ako asangalale, mai amene adakubala iwe akondwe.
Tsono iwe, ukuweruziranji mbale wako? Kapena iwe winawe, ukunyozeranji mbale wako? Tonsefe tidzaima pamaso pa Mulungu kuti atiweruze. Paja Malembo akunena kuti, “Ambuye akuti, ‘Pali Ine ndemwe, anthu onse adzandigwadira ndi kuvomereza kuti ndine Mulungu.’ ” Motero aliyense mwa ife adzadzifotokozera yekha kwa Mulungu zimene adazichita.
Wolima munda wake mwakhama amapeza chakudya chambiri, koma wotsata zopanda pake ngwopanda nzeru.
Wobera atate ake kapena amai ake namanena kuti kutero sikulakwa, ameneyo ndi mnzake wa munthu woononga.
Nchifukwa chake tsono, munthu akadya mkate umenewu, kapena kumwa chikho cha Ambuyechi mosayenera, apalamula mlandu wonyoza thupi la Ambuye ndiponso magazi ao. Koma munthu aziyamba wadziwona bwino asanadyeko mkate umenewu ndi kumwa chikho chimenechi. Pakuti amene adya mkate umenewu ndi kumwa chikho chimenechi, koma osalizindikira thupi la Ambuye, akudziitanira chilango pamene akudya ndi kumwa.
Tsono popeza kuti ndinu ana okondedwa a Mulungu, muziyesa kumtsanzira. Muziyesa kudziŵa kwenikweni zimene zingakondweretse Ambuye. Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muŵatsutse. Paja zimene iwo amachita mobisa, ngakhale kuzitchula komwe kumachititsa manyazi. Koma kuŵala kumaunika zinthu, ndipo zonse zimaonekera poyera. Motero chilichonse choonekera poyera, chimasanduka kuŵala. Nchifukwa chake amati, “Dzuka wam'tulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuŵalira.” Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa. Nchifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵani zimene Ambuye afuna kuti muchite. Musaledzere vinyo, kumeneko nkudzitaya, koma mudzazidwe ndi Mzimu Woyera. Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse. Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.
Tsono munthu akadziyeretsa nkusiya zotsikazi, adzakhala ngati chiŵiya cha ntchito zolemerera. Adzakhala wopatulika ndi wofunika zedi kwa Ambuye ake, wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino. Uthaŵe zilakolako zoipa zachinyamata. Pamodzi ndi anthu onse otama Ambuye mopemba ndi mtima woyera, uzifunafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere.
Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti samkonda, koma amene amakonda mwana wake, sazengereza kumlanga.