Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -


NDIME ZA KUSALA

NDIME ZA KUSALA

Kusala kudya kumatithandiza kukula monga ana a Mulungu, kumatiyandikitsa kwa Mulungu ndikulimbitsa ubale wathu ndi Atate wakumwamba. Tisamasale kudya chifukwa cha phindu lathu lokha, koma kuti tiwongolere moyo wathu mwa Mulungu. Kusala kudya ndi chinthu chodzipereka, ndi pamene timasankha kunyalanyaza njala yathupi kwakanthawi ndikutenga nthawi imeneyo kudyetsa ndikulimbitsa mzimu. Ndi nthawi yofunafuna Mulungu mwapadera. N’chifukwa chake n’kofunika kuti usale kudya pamalo abata kumene ungalankhule ndi Mulungu pawekha.

Danieli 9:3 Ndinatembenuzira nkhope yanga kwa Ambere Mulungu, kufunafuna pemphero ndi mapembedzero, ndi kusala kudya, ndi ziguduli, ndi phulusa.




Mateyu 6:16-18

“Pamene mukusala zakudya, musamaonetsa nkhope zachisoni monga amachitira anthu achiphamaso aja. Iwo amaipitsa nkhope kuti anthu aone kuti akusala zakudya. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma iwe, pamene ukusala zakudya, samba m'maso nkudzola mafuta kumutu, kuti anthu asadziŵe kuti ukusala zakudya. Koma Atate ako amene ali osaoneka ndiwo adziŵe. Ndipo Atate akowo amene amaona zobisika, adzakupatsa mphotho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 58:6-7

“Kusala koona kumene ndimafuna ndi uku: masulani maunyolo ozunzira anzanu, masulani nsinga za goli la kuweruza mokondera. Opsinjidwa muŵapatse ufulu, muthetse ukapolo uliwonse. Anthu anjala muziŵagaŵirako chakudya chanu, osoŵa pokhala muziŵapatsako malo. Mukaona wausiŵa, mpatseni chovala, musalephere kuthandiza amene ali abale anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 2:12-13

Koma Chauta akunena kuti, “Ngakhale tsopano bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse, mukusala zakudya, mukukhetsa misozi ndi kulira mwachisoni. Ng'ambani mitima yanu, osati zovala zanu chabe.” Bwererani kwa Chauta, Mulungu wanu, poti Iye ngwokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wa chikondi chosasinthika. Nthaŵi zonse ndi wokonzeka kukhululuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:2

Pa masiku makumi anai Yesu adasala zakudya usana ndi usiku, ndipo pambuyo pake adamva njala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 13:2-3

Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.” “Pambuyo pake adaŵapatsa oweruza kufikira nthaŵi ya mneneri Samuele. Kenaka anthu adapempha kuti aŵapatse mfumu, ndipo Mulungu adaŵapatsa Saulo, mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, iye nkuŵalamulira pa zaka makumi anai. Pambuyo pake Mulungu adamchotsa Sauloyo, naika Davide kuti akhale mfumu yao. Za iyeyu Mulungu adanena kuti, ‘Ndapeza Davide, mwana wa Yese, ndiye munthu wanga wapamtima, amene adzachita zonse zimene Ine ndifuna.’ Mwa zidzukulu za Davideyo Mulungu adasankha Yesu kuti akhale Mpulumutsi wa Aisraele, monga momwe adaalonjezera kale. Iyeyo asanayambe ntchito, Yohane ankalalikira Aisraele onse kuti atembenuke mtima ndi kubatizidwa. Pamene Yohane anali pafupi kutsiriza ntchito yake, adafunsa anthu kuti, ‘Kodi inu mumayesa kuti ine ndine yani? Inetu sindine amene mukumuyembekezayo ai. Koma pakubwera wina pambuyo panga amene ine sindili woyenera ngakhale kumvula nsapato zake.’ “Ine abale, zidzukulu za Abrahamu, ndi ena nonse oopa Mulungu, uthenga wa chipulumutsowu Mulungu watumizira ife. Anthu okhala ku Yerusalemu ndi akulu ao sadamzindikire Yesu, ndipo sadamvetse mau a aneneri amene amaŵerengedwa tsiku la Sabata lililonse. Komabe pakumzenga mlandu Yesuyo kuti aphedwe, adachitadi zimene aneneri adaaneneratu. Ngakhale sadapeze konse chifukwa chomuphera, komabe adapempha Pilato kuti Yesuyo aphedwe. Ndipo atachita zonse zimene zidalembedwa za Iye, adamtsitsapo pa mtanda paja namuika m'manda. Tsono atasala zakudya ndi kupemphera adaŵasanjika manja naŵatuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 8:21-23

Ku mtsinje wa Ahavako, ndidalengeza kuti anthu onse asale zakudya, adzichepetse pamaso pa Mulungu wathu ndi kumpempha kuti atitsogolere ife ndi ana athu, ndiponso kuti ateteze katundu wathu pa ulendo wathu. Ndinali ndi manyazi kupempha mfumu kuti itipatse gulu la asilikali, ena oyenda pansi ndi ena okwera pa akavalo, oti atiteteze kwa adani athu pa njira. Tinali titauza mfumuyo kuti, “Mulungu wathu amaŵadalitsa onse okhulupirira Iye, koma amaŵakwiyira amene salabadako za Iye.” Choncho tidasala zakudya ndi kupemphera kwa Mulungu wathu kuti atiteteze, ndipo Iye adamva kupempha kwathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 20:3-4

Pamenepo Yehosafati adachita mantha, ndipo adaganiza zopempha nzeru kwa Chauta, nalengeza kuti anthu onse a ku dziko la Yuda asale zakudya. Motero mudakhala bata mu ufumu wonse wa Yehosafati, pakuti Mulungu adampatsa mtendere ku maiko onse omzungulira. Choncho Yehosafati adayamba kulamulira Yuda. Anali wa zaka 35 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 25 ku Yerusalemu. Mai wake anali Azuba, mwana wa Sili. Yehosafati ankayenda motsata chitsanzo chabwino cha Asa atate ake. Sadapatuke pa zimenezo. Ankachita zolungama pamaso pa Chauta. Komabe akachisi opembedzerako mafano sadaŵaononge. Anthu anali asanapereke mitima yao kwa Mulungu wa makolo ao. Tsono ntchito zonse zimene adachita Yehosafati kuyambira poyamba mpaka potsiriza, zidalembedwa m'buku la mbiri ya Yehu, mwana wa Hanani, limene lili chigawo cha buku lokamba za mafumu a Aisraele. Zitapita zimenezi, Yehosafati mfumu ya ku Yuda, adagwirizana ndi Ahaziya mfumu ya ku Israele, amene ankachita zoipa kwambiri. Adagwirizana naye pomanga zombo zomapita ku Tarisisi ndipo zombozo ankazimangira ku Eziyoni-Gebere. Tsono Eliyezere mwana wa Dodavahu wa ku Maresa, adalosa zoipira Yehosafati adati, “Chifukwa chakuti mwagwirizana ndi Ahaziya, Chauta adzaononga zimene mwapangazo.” Ndipo zombozo zidaonongekadi zosakafika ku Tarisisi. Ayuda onse adasonkhana kuti adzapemphe chithandizo kwa Chauta. Anthu onse a ku mizinda yonse ya ku Yuda adabwera kudzapempha chithandizo kwa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 1:4

Pamene ndidamva mau ameneŵa, ndidakhala pansi nkuyamba kulira, ndipo ndidalira masiku angapo. Ndinkasala chakudya, ndi kumapemphera kwa Mulungu wakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:1-2

Yesu, ali wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, adabwerako ku mtsinje wa Yordani kuja. Mzimu Woyerayo ankamutsogolera m'chipululu Paja Malembo akuti, “ ‘Mulungu adzalamula angelo ake kuti akusamaleni.’ Ndiponso, “ ‘Iwo adzakunyamulani m'manja mwao, kuti mapazi anu angapweteke pa miyala.’ ” Koma Yesu adati, “Malembo akuti, ‘Usaŵayese Ambuye, Mulungu wako.’ ” Tsono Satana atatha kumuyesa mwa zonsezi, adalekana naye, kudikira nthaŵi ina. Yesu adabwereranso ku Galileya ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Mbiri yake idawanda kuzungulira dziko lonselo. Ankaphunzitsa m'nyumba zao zamapemphero, ndipo anthu onse ankamutamanda. Nthaŵi ina Yesu adafika ku Nazarete kumene adaaleredwa. Ndipo pa tsiku la Sabata adaloŵa m'nyumba yamapemphero, monga adaazoloŵera, naimirira kuti aŵerenge mau. Adampatsa buku la mneneri Yesaya. Tsono Iye adafutukula bukulo, napeza pamene padalembedwa kuti, “Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa, ndi kukalalika za nthaŵi imene Ambuye adzapulumutsa anthu ao.” masiku makumi anai, ndipo kumeneko Satana ankamuyesa. Yesu sankadya kanthu masiku amenewo, ndipo pamene masikuwo adatha, adamva njala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:28

Tsono Mose adakhala pamodzi ndi Chauta kumeneko masiku makumi anai, usana ndi usiku, osadya kanthu. Ndipo Chautayo adalemba pa miyala iŵiri ija mau onse a chipanganocho, ndiye kuti Malamulo Khumi aja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 14:23

Pa mpingo uliwonse adakhazika akulu a mpingo. Ndipo pakupemphera ndi kusala zakudya adaŵapereka kwa Ambuye amene anali atamkhulupirira tsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 35:13-14

Koma ine pamene adani anga analikudwala, ndidavala chiguduli kuwonetsa chisoni. Ndidadzilanga posala zakudya. Ndidapemphera nditaŵeramitsa mutu wanga pa chifuŵa, monga ngati ndikuchitira chisoni bwenzi langa kapena mbale wanga. Ndinkayenda khumakhuma ngati munthu wolira maliro a mai wake, nditaŵerama ndi kumalira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 21:27-29

Ahabu atamva mau amenewo, adang'amba zovala zake, navala ziguduli. Adasala zakudya nagona pa zigudulizo, ndipo adayamba kuyenda modzichepetsa. Apo Chauta adauza Eliya wa ku Tisibe kuti, “Kodi waona m'mene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga? Popeza kuti wadzichepetsa pamaso panga, sindidzamlanga ndi zonse zija iyeyo ali moyo. Koma ndidzalanga banja lake, kuyambira mwana wake.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:14-15

Pambuyo pake ophunzira a Yohane Mbatizi adabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Kodi bwanji ife ndi Afarisi timasala zakudya kaŵirikaŵiri, pamene ophunzira anu sasala nkomwe?” Yesu adati, “Kani anzake a mkwati angathe kumasala zakudya pamene mkwati ali nao pomwepo? Chosatheka! Koma idzafika nthaŵi pamene adzaŵachotsera mkwatiyo. Pamenepo ndiye azidzasala zakudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 58:3-5

Anthu akufunsa kuti, “Kodi tizisaliranji zakudya, pamene Inu Chauta simulabadako? Kodi tivutikirenji nkudzichepetsa, pamene Inu simusamalako?” Chauta akunena kuti, “Kunena zoona, tsiku limene mumasala zakudya lija, mumafunafuna zimene zingakupatseni phindu, mumazunza antchito anu onse. Mumati uku mukusala zakudya, uku mukukangana ndi kumenyana, mpaka kutchayana ndi nkhonya zopwetekana. Kodi mukuyesa kuti Ine nkumvera mapemphero anu, chifukwa cha kusala zakudya kotereku. Kodi kusala kumene ndimafuna Ine nkumeneku, kungokhala tsiku loti munthu adzichepetse basi? Inu mumaŵerama pansi ngati udzu, mumayala ziguduli nkuthirapo phulusa kuti mugonepo. Kodi ndiye mumati kusala kumeneku, tsiku lokondwetsa Chauta?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 9:1-2

Tsono tsiku la 24 la mwezi womwewo, Aisraele onse adasonkhana kuti asale chakudya, kuvala chiguduli ndi kudzithira dothi pa mutu. Mudachita zizindikiro ndi zodabwitsa pamaso pa Farao, antchito ake onse, ndi anthu onse okhala m'dziko mwake, popeza kuti mudaadziŵa kuti iwowo adazunza makolo athu. Nchifukwa chake mbiri yanu idakula monga momwe iliri mpaka lero lino. Mudagaŵa nyanja pakati, anthu anu akupenya, kotero kuti iwowo adaoloka pakati pa nyanja pali pouma. Kenaka mudaŵamiza m'nyanja adani amene ankaŵalondola, monga momwe umachitira mwala m'madzi ozama. Munkaŵatsogolera masana ndi mtambo, ndipo usiku munkaŵaunikira ndi moto njira imene ankayendamo. Mudatsika pa phiri la Sinai, ndipo mudalankhula nawo kuchokera kumwamba. Mudaŵapatsa malangizo olungama, malamulo oona, zophunzitsa zabwino ndiponso mau aluntha. Mudaŵadziŵitsa kuti tsiku lanu la Sabata ndi lopatulika, ndipo mudaŵapatsa malamulo, malangizo, ndiponso mau anu, kudzera mwa Mose mtumiki wanu. Mudaŵapatsa buledi wochokera kumwamba kuti adye. Mudaŵapatsa madzi otuluka m'thanthwe, kuti aphere ludzu. Mudaŵauza kuti apite kukalanda dziko limene Inu mudaalonjeza kuti mudzaŵapatsa. “Koma makolo athu adadzitukumula nakhala okanika ndipo sadamvere malamulo anu. Adakana kumvera, ndipo sankakumbuka zodabwitsa zimene Inu mudaazichita pakati pao. Adakhala okanika, nadzisankhira mtsogoleri woti aŵatsogolere kubwerera ku Ejipito ku dziko laukapolo lija. Koma Inu ndinu Mulungu wokhululuka, wokoma mtima, wachifundo, wosakwiya msanga, wokhala ndi chikondi chachikulu chosasinthika, motero iwowo simudaŵasiye. Ngakhale pamene adadzipangira fano la mwanawang'ombe, namanena kuti, ‘Uyu ndiye Mulungu wathu amene adatitulutsa ku dziko la Ejipito,’ ndipo ngakhale adachita zinthu zoipitsitsa zokunyozani, Inu amene muli ndi chifundo chachikulu, simudaŵasiye m'chipululu iwowo. Mtambo umene unkaŵatsogolera poyenda m'njira masana sudaŵachokere, ndipo moto umene unkaŵaunikira njira poyenda usiku sudaŵasiye. Aisraele atadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina, adaimirira, nayamba kuulula machimo ao ndi zolakwa za makolo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 7:5

“Funsa anthu onse a m'dziko ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala zakudya ndi kulira pa mwezi wachisanu ndi pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri zaka makumi asanu ndi aŵiri zapitazi, kodi munkalemekezadi Ine pochita zimenezo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 7:6

Choncho adasonkhana ku Mizipa, natunga madzi ndi kuŵathira pansi pamaso pa Chauta mopepesera, ndipo adasala chakudya tsiku limenelo, namanena kuti, “Tidachimwira Chauta.” Nku Mizipako kumene Samuele ankaweruza milandu ya Aisraele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:5

Musamakanane, koma pokhapokha mutavomerezana kutero pa kanthaŵi kuti mudzipereke ku mapemphero. Pambuyo pake mukhalenso pamodzi, kuwopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cha kulephera kudzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 17:21

“Koma mzimu wa mtundu umenewu, pokhapokha mutayamba mwapemphera ndi kusala zakudya mpamene mungautulutse.”]

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 69:10

Pamene ndidadzilanga posala zakudya, anthu adandinyoza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 12:16

Nchifukwa chake Davide adapempherera mwanayo kwa Mulungu. Adaleka kudya, nakaloŵa m'nyumba, nkukagona pansi usiku wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 1:14

Lamulani kuti anthu asale zakudya. Itanitsani msonkhano waulemu. Akulu ndi onse okhala m'dziko asonkhane ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu, ndipo iwowo alire kwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 20:26

Tsono Aisraele onse, ndiye kuti gulu lonse la ankhondo, adapita ku Betele ndi kukalira kumeneko. Adakhala pansi pamaso pa Chauta, nasala chakudya tsiku limenelo mpaka madzulo, ndipo adapereka nsembe zopsereza ndi zamtendere pamaso pa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 109:24

Maondo anga afooka chifukwa chosala zakudya, thupi langa laonda ndi mutu womwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 19:8

Eliya uja adadzuka, nadya nkumwera. Motero adapeza mphamvu zoyendera. Adayenda masiku makumi anai usana ndi usiku mpaka adakafika ku Sinai, phiri la Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:30-31

Kornelio adati, “Dzana ilo, ndinkapemphera m'nyumba mwanga, nthaŵi ngati yomwe ino ya 3 koloko dzuŵa litapendeka. Mwadzidzidzi kutsogolo kwangaku kudaimirira munthu wovala zovala zonyezimira. Adandiwuza kuti, ‘Kornelio, Mulungu wamva pemphero lako, ndipo wakumbukira ntchito zako zachifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yona 3:5

Anthu a ku Ninive adakhulupirira Mulungu. Adalengeza kuti aliyense, wamkulu ndi wamng'ono yemwe, asale zakudya, ndipo avale chiguduli.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:18

kuti anthu asadziŵe kuti ukusala zakudya. Koma Atate ako amene ali osaoneka ndiwo adziŵe. Ndipo Atate akowo amene amaona zobisika, adzakupatsa mphotho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 14:12

Ngakhale asale zakudya, Ine sindidzamva kulira kwao. Ndipo ngakhale apereke nsembe zopsereza ndi chopereka cha chakudya, sindidzazilandira. Koma ndidzaŵaononga ndi nkhondo, njala ndi mliri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 8:19

Kusala zakudya pa mwezi wachinai, wachisanu, wachisanu ndi chiŵiri ndi wakhumi, kudzakhala nthaŵi yachimwemwe ndi yachisangalalo ku banja la Yuda. Muzikonda zoona ndiponso mtendere.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 35:13

Koma ine pamene adani anga analikudwala, ndidavala chiguduli kuwonetsa chisoni. Ndidadzilanga posala zakudya. Ndidapemphera nditaŵeramitsa mutu wanga pa chifuŵa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 2:15-16

Lizani lipenga ku Ziyoni. Lengezani mwambo wa kusala zakudya. Muitanitse msonkhano waukulu. Sonkhanitsani anthu pamodzi, muŵauze kuti adziyeretse. Sonkhanitsani akuluakulu, sonkhanitsani ana, sonkhanitsani ndi oyamwa omwe. Lamulani kuti nawonso akwati achoke m'chipinda mwao, abwere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 9:27

Ndimazunza thupi langa ndi kuligonjetsa, kuti likhale ngati kapolo wondimvera. Ndimachita zimenezi kuwopa kuti ine ndemwe, amene ndidaitana ena ku mpikisano, ndingapezeke wosayenera kuchita nao mpikisanowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 1:4-6

Pamene ndidamva mau ameneŵa, ndidakhala pansi nkuyamba kulira, ndipo ndidalira masiku angapo. Ndinkasala chakudya, ndi kumapemphera kwa Mulungu wakumwamba. Ndidati, “Inu Chauta, Mulungu wakumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, mumasunga chipangano. Mumaonetsa chikondi chosasinthika kwa anthu amene amakukondani ndi kutsata malamulo anu. Tsekulani maso ndipo tcherani khutu, kuti mumve pemphero la mtumiki wanune, limene ndikupereka tsopano kwa Inu usana ndi usiku, kupempherera Aisraele atumiki anu. Ndikuvomera machimo amene ife Aisraele tidakuchimwirani. Zoonadi, ine pamodzi ndi banja la makolo anga, tidakuchimwirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 1:7-8

Zimenezi zinkachitika chaka ndi chaka. Nthaŵi zonse akamapita ku nyumba ya Chauta, mkazi mnzakeyo ankamputa. Nchifukwa chake Hana ankangolira, ndipo sankafuna ndi kudya komwe. Mwina Elikana mwamuna wake ankamufunsa kuti, “Hana, kodi watani apa ukulira ndi kuwoneka wachisoni ndiponso sukufuna kudya? Kodi kwa iwe ineyo sindikuposa ana aamuna khumi?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 13:2

Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:37

pambuyo pake nkukhala wamasiye kufikira msinkhu wa zaka 84. Sankachokatu ku Nyumba ya Mulungu, ankakonda kudzatumikira Mulungu usana ndi usiku pakupemphera ndi kusala zakudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 8:23

Choncho tidasala zakudya ndi kupemphera kwa Mulungu wathu kuti atiteteze, ndipo Iye adamva kupempha kwathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 21:9

M'makalatamo adalembamo kuti, “Lalikani kuti anthu asale zakudya, ndipo Naboti amuike pa malo aulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 1:12

Ndipo anthuwo adabuma maliro. Adalira ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Saulo ndi Yonatani mwana wake. Adaliranso chifukwa cha Aisraele, anthu a Chauta, chifukwa choti anali ataphedwa ku nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 20:26-28

Tsono Aisraele onse, ndiye kuti gulu lonse la ankhondo, adapita ku Betele ndi kukalira kumeneko. Adakhala pansi pamaso pa Chauta, nasala chakudya tsiku limenelo mpaka madzulo, ndipo adapereka nsembe zopsereza ndi zamtendere pamaso pa Chauta. Bokosi lachipangano la Chauta linali kumeneko masiku amenewo. Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni, ndiye ankayang'anira bokosilo masiku amenewo. Choncho Aisraele adafunsa Chauta kuti, “Kodi tipitenso kukamenyana nawo nkhondo Abenjamini, abale athu, kapena tingoleka?” Chauta adayankha kuti, “Pitaninso, pakuti maŵa ndidzaŵapereka m'manja mwanu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 1:14-15

Lamulani kuti anthu asale zakudya. Itanitsani msonkhano waulemu. Akulu ndi onse okhala m'dziko asonkhane ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu, ndipo iwowo alire kwa Iye. Kalanga ine! Tsiku loopsa layandikira, tsiku la Chauta, likubwera ndi chiwonongeko chochokera kwa Mphambe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 5:35

Koma idzafika nthaŵi pamene adzaŵachotsera mkwatiyo. Pamenepo ndiye azidzasala zakudya.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 58:1-9

Chauta akunena kuti, “Fuula kwambiri, usaleke, mau ako amveke ngati lipenga. Uŵauze anthu anga za kulakwa kwao, uŵauze a m'fuko la Yakobe za machimo ao. mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana. Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa. Anthu anu adzamanganso nyumba zimene zakhala mabwinja nthaŵi yaitali. Adzamanganso pa maziko akalekale. Apo mudzatchedwa anthu okonza makoma, omanganso nyumba zamabwinja, kuti anthu azikhalamo.” Chauta akunena kuti, “Muzidziletsa kuchita zanuzanu pa Sabata, osagwira ntchito zanu pa tsiku langa loyera. Tsiku la Sabatali muzilitcha kuti chinthu chosangalatsa, tsiku loyera la Chauta muzilitcha kuti chinthu cholemekezeka. Muzililemekeza pakusayendayenda, poleka kugwira ntchito zanu ndiponso posakamba nkhani zachabe. Mukatero ndiye kuti mudzakondwa mwa Ine, Chauta, ndipo ndidzakukwezani ndi kukupambanitsani pa dziko lonse lapansi. Mudzadyerera dziko limene ndidapatsa Yakobe kholo lanu. Ine Chauta ndalankhula zimenezi ndi pakamwa panga.” Masiku onse iwo amaoneka ngati akufuna kuchita zimene Ine ndifuna. Amangonena kuti afuna kumvera malamulo a Mulungu wao. Amandipempha kuti ndigamule mlandu wao mwachilungamo, ndipo amakondwera kukhala pafupi ndi Mulungu wao.” Anthu akufunsa kuti, “Kodi tizisaliranji zakudya, pamene Inu Chauta simulabadako? Kodi tivutikirenji nkudzichepetsa, pamene Inu simusamalako?” Chauta akunena kuti, “Kunena zoona, tsiku limene mumasala zakudya lija, mumafunafuna zimene zingakupatseni phindu, mumazunza antchito anu onse. Mumati uku mukusala zakudya, uku mukukangana ndi kumenyana, mpaka kutchayana ndi nkhonya zopwetekana. Kodi mukuyesa kuti Ine nkumvera mapemphero anu, chifukwa cha kusala zakudya kotereku. Kodi kusala kumene ndimafuna Ine nkumeneku, kungokhala tsiku loti munthu adzichepetse basi? Inu mumaŵerama pansi ngati udzu, mumayala ziguduli nkuthirapo phulusa kuti mugonepo. Kodi ndiye mumati kusala kumeneku, tsiku lokondwetsa Chauta? “Kusala koona kumene ndimafuna ndi uku: masulani maunyolo ozunzira anzanu, masulani nsinga za goli la kuweruza mokondera. Opsinjidwa muŵapatse ufulu, muthetse ukapolo uliwonse. Anthu anjala muziŵagaŵirako chakudya chanu, osoŵa pokhala muziŵapatsako malo. Mukaona wausiŵa, mpatseni chovala, musalephere kuthandiza amene ali abale anu. “Mukatero, mudzaŵala ngati mbandakucha, ndipo mabala anu adzapola msanga. Ine, kulungama kwanu, ndidzakutsogolerani, ndipo ulemerero wanga udzakutchinjirizani kumbuyo kwanu. “Mukamapemphera ndidzakumverani, ndipo mukandiitana ndidzakuyankhani. Mukaleka kuzunza anzanu, mukasiya kulozana chala, mukaleka kunena zoipa za anzanu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:1-4

Zitatha izi, Mzimu Woyera adatsogolera Yesu kupita ku chipululu kuti Satana akamuyese. Apo Yesu adati, “Choka, Satana! Paja Malembo akuti, ‘Uzipembedza Ambuye, Mulungu wako, ndipo uziŵatumikira Iwo okha.’ ” Pamenepo Satana adamsiya, angelo nkubwera kumadzamutumikira Yesuyo. Yesu atamva kuti Yohane adamponya m'ndende, adabwerera ku Galileya. Adachokako ku Nazarete, nakakhala ku Kapernao, mzinda wina wa m'mbali mwa nyanja ku dera la Zebuloni ndi Nafutali. Zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri Yesaya adaanena kuti, “Iwe dziko la Zebuloni ndi iwe dziko la Nafutali, ku njira yakunyanja, patsidya pa Yordani, iwe Galileya, dziko la anthu akunja! Anthu okhala mu mdima aona kuŵala kwakukulu. Anthu okhala m'dziko la mdima wabii wa imfa, kuŵala kwaŵaonekera.” Kuyambira nthaŵi imeneyo Yesu adayamba kulalika kuti, “Tembenukani mtima, chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira.” Yesu akuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, adaona anthu aŵiri pachibale pao: Simoni wotchedwa Petro, ndi mbale wake Andrea, akuponya khoka m'nyanjamo, popeza kuti anali asodzi. Yesu adaŵauza kuti, “Inu, munditsate, ndikakusandutseni asodzi a anthu.” Pa masiku makumi anai Yesu adasala zakudya usana ndi usiku, ndipo pambuyo pake adamva njala. Pomwepo iwo adasiya makoka ao, namamtsatadi. Atapitirira pamenepo, Yesu adaona enanso aŵiri pachibale pao: Yakobe ndi Yohane, ana a Zebedeo. Iwo anali m'chombo pamodzi ndi bambo waoyo, akukonza makoka ao, Yesu nkuŵaitana. Pomwepo iwowo adasiya chombo chao ndi bambo wao uja, namatsata Yesu. Yesu adayendera dziko lonse la Galileya akuphunzitsa m'nyumba zamapemphero ndi kulalika Uthenga Wabwino wonena za ufumu wakumwamba. Ankachiritsanso nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi. Mbiri yake idabuka m'dziko lonse la Siriya, kotero kuti anthu ankabwera kwa Iye ndi odwala onse ovutika ndi nthenda ndi zoŵaŵa zosiyanasiyana, ogwidwa ndi mizimu yoipa, akhunyu ndi opunduka, Iye nkumaŵachiritsa. Anthu ambirimbiri ankamutsata kuchokera ku Galileya, ku dera lotchedwa Mizinda Khumi, ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi kutsidya kwa mtsinje wa Yordani. Tsono Woyesa uja adadza namuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, lamulani miyala ili apayi kuti isanduke chakudya.” Koma Yesu adati, “Malembo akuti, “ ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mau onse olankhula Mulungu.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 7:14

ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 27:33-34

Kuli pafupi kucha, Paulo adaŵapempha onse aja kuti adyeko kanthu. Adaŵauza kuti, “Mwakhala masiku khumi ndi anai tsopano mitima ili m'malere, nthaŵi yonseyi osadya kapena kulaŵa kanthu. Ndikukupemphani tsono mudye kanthu kuti mupulumuke. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene adzataye ngakhale tsitsi limodzi la kumutu kwake.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:15

Yesu adati, “Kani anzake a mkwati angathe kumasala zakudya pamene mkwati ali nao pomwepo? Chosatheka! Koma idzafika nthaŵi pamene adzaŵachotsera mkwatiyo. Pamenepo ndiye azidzasala zakudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 36:9

Pa mwezi wachisanu ndi chinai wa chaka chachisanu cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, anthu onse a ku Yerusalemu ndi onse amene adaabwera kumeneko kuchokera ku mizinda ya Yuda, adapangana za kusala chakudya kuti apepese Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 2:15

Lizani lipenga ku Ziyoni. Lengezani mwambo wa kusala zakudya. Muitanitse msonkhano waukulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yona 3:6-9

Mfumu ya ku Ninive itamva zimenezo, idatsika pa mpando wake waufumu, nivula mkanjo wake. Idavala chiguduli, nikakhala nao pa dzala. Tsono mfumuyo idalengeza ku Ninive, kuti, “Nali lamulo lochokera kwa mfumu ndi akalonga ake: ‘Munthu aliyense asadye kanthu, ndiponso ziŵeto zonse zikuluzikulu ndi zing'onozing'ono zomwe zisadye kanthu. Zisadyetu kanthu, nkumwa madzi komwe zisamwe. Anthu avale ziguduli, nyamanso aziveke ziguduli. Anthuwo azifuula kwa Mulungu ndi mphamvu zao zonse. Ndithu aliyense asiye makhalidwe ake oipa ndi ntchito zake zankhanza. Nkudziŵanji, mwina Mulungu nkutikhululukira, naleka kutikwiyira, ifeyo osaonongeka.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 10:6

Pambuyo pake Ezara adachokako ku Nyumba ya Mulungu napita ku chipinda cha Yehohanani, mwana wa Eliyasibu, kumene adakachezera usikuwo. Sadadye buledi kapena kumwa madzi. Nthaŵi yonseyo adakhalira kulira chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu obwerako ku ukapolo aja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 31:13

Pambuyo pake adatenga mafupa ao naŵakwirira patsinde pa mtengo wa mbwemba ku Yabesi, ndipo adasala zakudya masiku asanu ndi aŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 9:1-3

Tsono tsiku la 24 la mwezi womwewo, Aisraele onse adasonkhana kuti asale chakudya, kuvala chiguduli ndi kudzithira dothi pa mutu. Mudachita zizindikiro ndi zodabwitsa pamaso pa Farao, antchito ake onse, ndi anthu onse okhala m'dziko mwake, popeza kuti mudaadziŵa kuti iwowo adazunza makolo athu. Nchifukwa chake mbiri yanu idakula monga momwe iliri mpaka lero lino. Mudagaŵa nyanja pakati, anthu anu akupenya, kotero kuti iwowo adaoloka pakati pa nyanja pali pouma. Kenaka mudaŵamiza m'nyanja adani amene ankaŵalondola, monga momwe umachitira mwala m'madzi ozama. Munkaŵatsogolera masana ndi mtambo, ndipo usiku munkaŵaunikira ndi moto njira imene ankayendamo. Mudatsika pa phiri la Sinai, ndipo mudalankhula nawo kuchokera kumwamba. Mudaŵapatsa malangizo olungama, malamulo oona, zophunzitsa zabwino ndiponso mau aluntha. Mudaŵadziŵitsa kuti tsiku lanu la Sabata ndi lopatulika, ndipo mudaŵapatsa malamulo, malangizo, ndiponso mau anu, kudzera mwa Mose mtumiki wanu. Mudaŵapatsa buledi wochokera kumwamba kuti adye. Mudaŵapatsa madzi otuluka m'thanthwe, kuti aphere ludzu. Mudaŵauza kuti apite kukalanda dziko limene Inu mudaalonjeza kuti mudzaŵapatsa. “Koma makolo athu adadzitukumula nakhala okanika ndipo sadamvere malamulo anu. Adakana kumvera, ndipo sankakumbuka zodabwitsa zimene Inu mudaazichita pakati pao. Adakhala okanika, nadzisankhira mtsogoleri woti aŵatsogolere kubwerera ku Ejipito ku dziko laukapolo lija. Koma Inu ndinu Mulungu wokhululuka, wokoma mtima, wachifundo, wosakwiya msanga, wokhala ndi chikondi chachikulu chosasinthika, motero iwowo simudaŵasiye. Ngakhale pamene adadzipangira fano la mwanawang'ombe, namanena kuti, ‘Uyu ndiye Mulungu wathu amene adatitulutsa ku dziko la Ejipito,’ ndipo ngakhale adachita zinthu zoipitsitsa zokunyozani, Inu amene muli ndi chifundo chachikulu, simudaŵasiye m'chipululu iwowo. Mtambo umene unkaŵatsogolera poyenda m'njira masana sudaŵachokere, ndipo moto umene unkaŵaunikira njira poyenda usiku sudaŵasiye. Aisraele atadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina, adaimirira, nayamba kuulula machimo ao ndi zolakwa za makolo ao. Inu mudaŵapatsa mzimu wanu wabwino kuti aziŵalangiza. Simudaŵamane chakudya cha mana chija, ndipo mudaŵapatsa madzi akumwa, kuti aphe ludzu lao. Mudaŵasunga zaka makumi anai m'chipululu ndipo nthaŵi yonseyo sankasoŵa kanthu. Zovala zao sizidathe, mapazi aonso sadatupe. Mudaŵapatsa mphamvu zogonjetsera maiko ndiponso mitundu ya anthu. Mudaŵagaŵiranso maiko achilendo, ndipo choncho adalanda dziko la Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani. Mudachulukitsa zidzukulu zao ngati nyenyezi zamumlengalenga. Mudaŵaloŵetsa m'dziko limene mudaauza makolo ao kuti adzalilandira nkukhala lao. Choncho zidzukulu zaozo zidaloŵamo ndi kukhazikika m'menemo, ndipo Inu mukuŵatsogolera, mudagonjetsa Akanani, nzika za m'dzikomo. Akananiwo, ndiye kuti mafumu ao ndi anthu onse am'dzikomo, mudaŵapereka kwa anthu anu, kuti achite nawo monga angafunire. Motero adagonjetsa mizinda yamalinga nalanda dziko lachonde, nyumba zodzaza ndi zinthu zabwino, zitsime zokumbakumba, minda yamphesa, minda yaolivi ndiponso mitengo yazipatso yochuluka kwambiri. Choncho iwowo ankadya, namakhuta, mpaka kumanenepa, ndipo ankakondwa chifukwa cha ubwino wanu, Inu Chauta. “Komabe iwowo sankamvera, ndipo adakuukirani. Adaŵataya kunkhongo Malamulo anu, napha aneneri anu amene ankaŵadzudzula kuti abwerere kwa Inu. Adachita zinthu zoipitsitsa zokunyozani. Nchifukwa chake Inu mudaŵapereka kwa adani ao amene ankaŵavuta. Pa nthaŵi imene anali m'mavutoyo, ankalira kwa Inu, ndipo Inu munkaŵamvera muli Kumwambako. Chifukwa cha chifundo chanu chachikulu, mudaŵapatsa atsogoleri amene ankaŵapulumutsa kwa adani ao. Koma atakhala pa mtendere, adayambanso kuchimwa pamaso panu, ndipo mudaŵaperekanso kwa adani ao, kotero kuti adani aowo ankaŵalamulira. Komabe pamene ankabwerera ndi kumalira Inu, Inuyo munkaŵamvera muli Kumwambako. Motero nthaŵi zambiri munkaŵapulumutsa chifukwa cha chifundo chanu. Zoonadi Inu mudaŵachenjeza kuti ayambenso kutsata Malamulo anu. Koma iwo ankadzitukumula, ndipo sankamvera malamulo anu. Adachimwira malangizo anu opatsa moyo kwa anthu oŵasunga. Ankakufulatirani namaumitsa mitu yao, osafuna kumvera. Anthuwo adaimirira pomwepo, ndipo adamva mau a m'buku la Malamulo a Chauta akuŵaŵerenga nthaŵi yokwanira maora atatu. Pa maora atatu enanso, anthuwo ankaulula machimo ao namapembedza Chauta, Mulungu wao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 11:27

Ndidagwira ntchito zolemetsa, ndipo kaŵirikaŵiri sindidalaŵe tulo. Ndidamva njala ndi ludzu, kaŵirikaŵiri osaona chakudya, ndipo kusoŵa zovala ndi kuzizidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 9:9

Ndipo adakhala masiku atatu osatha kupenya ndiponso osadya kapena kumwa kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 9:9

Ine ndidakwera phiri kukalandira miyala iŵiri imene padalembedwapo chipangano chimene Chauta adachita nanu. Ndidakhala kumeneko masiku makumi anai, usana ndi usiku, ndipo sindidadye kapena kumwa kanthu kalikonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 20:26-27

Tsono Aisraele onse, ndiye kuti gulu lonse la ankhondo, adapita ku Betele ndi kukalira kumeneko. Adakhala pansi pamaso pa Chauta, nasala chakudya tsiku limenelo mpaka madzulo, ndipo adapereka nsembe zopsereza ndi zamtendere pamaso pa Chauta. Bokosi lachipangano la Chauta linali kumeneko masiku amenewo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 14:24

Koma ankhondo a Aisraele adavutika tsiku limene lija, pakuti Saulo adaŵaopseza pakunena kuti, “Atembereredwe amene adye kanthu kusanade, ndisanalipsire adani anga.” Motero panalibe ndi mmodzi yemwe amene adalaŵa chakudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:16

“Pamene mukusala zakudya, musamaonetsa nkhope zachisoni monga amachitira anthu achiphamaso aja. Iwo amaipitsa nkhope kuti anthu aone kuti akusala zakudya. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:12

Ine ndimasala zakudya kaŵiri pa mlungu, ndipo ndimapereka chachikhumi pa zonse zimene ndimapata.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 109:21-24

Koma Inu Mulungu, Ambuye anga, munditchinjirize malinga ndi ulemerero wa dzina lanu, mundipulumutse chifukwa chikondi chanu chosasinthika ndi chabwino. Pakuti ine ndine wosauka ndi wosoŵa, ndipo mtima wanga ukuŵaŵa kwambiri. Ndazimirira ngati mthunzi wamadzulo, ndapirikitsidwa ngati dzombe. Maondo anga afooka chifukwa chosala zakudya, thupi langa laonda ndi mutu womwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 8:21

Ku mtsinje wa Ahavako, ndidalengeza kuti anthu onse asale zakudya, adzichepetse pamaso pa Mulungu wathu ndi kumpempha kuti atitsogolere ife ndi ana athu, ndiponso kuti ateteze katundu wathu pa ulendo wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yona 3:8

Anthu avale ziguduli, nyamanso aziveke ziguduli. Anthuwo azifuula kwa Mulungu ndi mphamvu zao zonse. Ndithu aliyense asiye makhalidwe ake oipa ndi ntchito zake zankhanza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 24:18

Mose adakaloŵa mumtambomo mpaka kukafika pamwamba pa phiri. Adakhala kumeneko masiku makumi anai, usana ndi usiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 21:12

anthuwo adalengeza za kusala zakudya, ndipo adamuika Naboti pa malo aulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:14-17

Pambuyo pake ophunzira a Yohane Mbatizi adabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Kodi bwanji ife ndi Afarisi timasala zakudya kaŵirikaŵiri, pamene ophunzira anu sasala nkomwe?” Yesu adati, “Kani anzake a mkwati angathe kumasala zakudya pamene mkwati ali nao pomwepo? Chosatheka! Koma idzafika nthaŵi pamene adzaŵachotsera mkwatiyo. Pamenepo ndiye azidzasala zakudya. Munthu satenga chigamba cha nsalu yatsopano, nkuchisokerera pa chovala chakale. Chigamba chotere chimakoka nkunyotsolako chovalacho, ndiye kung'ambika kwake kumakhala kwakukulu koposa kale. Ndiponso munthu sathira vinyo watsopano m'matumba achikopa akale. Chifukwa akatero, matumbawo amaphulika, vinyoyo natayika, matumbawo nkutha ntchito. Koma vinyo watsopano amamuthira m'matumba atsopanonso. Apo zonse ziŵiri zimasungika bwino.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 20:3

Pamenepo Yehosafati adachita mantha, ndipo adaganiza zopempha nzeru kwa Chauta, nalengeza kuti anthu onse a ku dziko la Yuda asale zakudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 7:6-8

Choncho adasonkhana ku Mizipa, natunga madzi ndi kuŵathira pansi pamaso pa Chauta mopepesera, ndipo adasala chakudya tsiku limenelo, namanena kuti, “Tidachimwira Chauta.” Nku Mizipako kumene Samuele ankaweruza milandu ya Aisraele. Afilisti atamva kuti Aisraele adasonkhana ku Mizipa, akalonga a Afilisti adapita kuti akachite nawo nkhondo. Aisraele atamva zimenezi, adachita nawo mantha Afilistiwo, ndipo adauza Samuele kuti, “Musaleke kutidandaulira kwa Chauta, Mulungu wathu, kuti atipulumutse kwa Afilistiŵa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 2:18

Apo chikondi cha Chauta chidayaka ngati moto chifukwa cha dziko lake, ndipo adaŵachitira chifundo anthu ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 9:5

Tsono itakwana nthaŵi ya nsembe yamadzulo, ndidadzidzimuka mumtima mwanga nkuimirira, zovala zanga zong'ambika zija zikali m'thupi. Ndidagwada nkukweza manja anga kwa Chauta, Mulungu wanga,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:30

Kornelio adati, “Dzana ilo, ndinkapemphera m'nyumba mwanga, nthaŵi ngati yomwe ino ya 3 koloko dzuŵa litapendeka. Mwadzidzidzi kutsogolo kwangaku kudaimirira munthu wovala zovala zonyezimira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 13:8-9

Koma mneneri wa Mulungu uja adauza mfumu kuti, “Ngakhale mundipatse theka la chuma chanu, sindikadya chakudya chilichonse kapena kumwa madzi kuno. Pakuti Chauta adandilamula kuti, ‘Usakadye chakudya chilichonse, kapena kumwa madzi, kapenanso kudzera njira yomwe udaadzera kale pobwera.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 42:1-2

Monga momwe mbaŵala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga umakhumbira Inu Mulungu wanga. Kunyoza kwa adani anga kumandipweteka ngati bala lofa nalo la m'thupi mwanga, akamandifunsa nthaŵi zonse kuti, “Mulungu wako ali kuti?” Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Mulungu, Mulungu wamoyo. Kodi ndidzafika liti pamaso pa Mulungu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 8:15-23

Anthu onsewo ndidaŵasonkhanitsa ku mtsinje umene umafika mpaka ku mudzi wa Ahava, ndipo kumeneko tidagona m'zithando masiku atatu. Pamene ndinkayang'ana anthu ndi ansembe, ndidapeza kuti ana a Levi palibe. Tsono ndidaitana atsogoleri aŵa, Eliyezere, Ariyele, Semaya, Elinatani, Yaribu, Elinatani, Natani, Zekariya ndi Mesulamu, pamodzi ndi aphunzitsi aŵiri, Yoyaribu ndi Elinatani. Ndipo ndidaŵatuma kwa Ido, mtsogoleri wa malo otchedwa Kasifiya. Ndidaŵauza zoti akanene kwa Ido ndi kwa abale ake, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ku Kasifiyako, kuti atitumizire anthu odzatumikira ku Nyumba ya Mulungu wathu. Chifukwa cha kutikomera mtima Mulungu wathu, Ido adatitumizira munthu wanzeru, mwana wa fuko la Mahili, mwana wa Levi, mwana wa Israele, dzina lake Serebiya, pamodzi ndi ana ake aamuna ndi achibale ake, anthu 18 pamodzi. Adatitumiziranso Hasabiya ndi Yeshaiya wa fuko la Merari, kudzanso achibale ake ndiponso ana ao, anthu makumi aŵiri. Geresomo, wa fuko la Finehasi. Daniele, wa fuko la Itamara. Panalinso atumiki a ku Nyumba ya Mulungu okwanira 220, amene Davide ndi nduna zake adaaŵasankha kuti azitumikira Alevi. Anthu onseŵa adalembedwa potsata maina ao. Ku mtsinje wa Ahavako, ndidalengeza kuti anthu onse asale zakudya, adzichepetse pamaso pa Mulungu wathu ndi kumpempha kuti atitsogolere ife ndi ana athu, ndiponso kuti ateteze katundu wathu pa ulendo wathu. Ndinali ndi manyazi kupempha mfumu kuti itipatse gulu la asilikali, ena oyenda pansi ndi ena okwera pa akavalo, oti atiteteze kwa adani athu pa njira. Tinali titauza mfumuyo kuti, “Mulungu wathu amaŵadalitsa onse okhulupirira Iye, koma amaŵakwiyira amene salabadako za Iye.” Choncho tidasala zakudya ndi kupemphera kwa Mulungu wathu kuti atiteteze, ndipo Iye adamva kupempha kwathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:1-11

Zitatha izi, Mzimu Woyera adatsogolera Yesu kupita ku chipululu kuti Satana akamuyese. Apo Yesu adati, “Choka, Satana! Paja Malembo akuti, ‘Uzipembedza Ambuye, Mulungu wako, ndipo uziŵatumikira Iwo okha.’ ” Pamenepo Satana adamsiya, angelo nkubwera kumadzamutumikira Yesuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 5:33-35

Anthu ena adauza Yesu kuti, “Ophunzira a Yohane amasala zakudya kaŵirikaŵiri nkumapemphera, chimodzimodzinso ophunzira a Afarisi. Koma ophunzira anu amangodya ndi kumwa.” Yesu adati, “Kani anzake a mkwati angathe kumasala zakudya pamene mkwati ali nao pomwepo? Chosatheka! Koma idzafika nthaŵi pamene adzaŵachotsera mkwatiyo. Pamenepo ndiye azidzasala zakudya.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 20:27-28

Bokosi lachipangano la Chauta linali kumeneko masiku amenewo. Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni, ndiye ankayang'anira bokosilo masiku amenewo. Choncho Aisraele adafunsa Chauta kuti, “Kodi tipitenso kukamenyana nawo nkhondo Abenjamini, abale athu, kapena tingoleka?” Chauta adayankha kuti, “Pitaninso, pakuti maŵa ndidzaŵapereka m'manja mwanu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 12:15-23

Pompo Natani adabwerera kunyumba kwake. Motero Chauta adalanga mwana amene mkazi wa Uriya adabalira Davide, ndipo adadwala kwambiri. Nchifukwa chake Davide adapempherera mwanayo kwa Mulungu. Adaleka kudya, nakaloŵa m'nyumba, nkukagona pansi usiku wonse. Akuluakulu a ku nyumba ya mfumu adadzaima pambali pake kuti amuutse. Koma iye adakana kuuka, ndipo sadadye nawo chakudya anthuwo. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, mwanayo adamwalira. Atumiki a Davide adaopa kukamuuza kuti mwanayo wafa. Adati, “Pamene mwanayo anali moyo, tinkalankhula naye Davide, koma sankatimvera. Tsono tingathe kukamuuza bwanji lero kuti mwana wafa? Mwina nkudzipweteka.” Koma pamene Davide adaona kuti atumiki ake akunong'onezana, adadziŵa kuti mwana uja wafa. Choncho adafunsa atumiki ake aja kuti, “Kodi mwana uja watisiya?” Atumikiwo adati, “Inde, watisiyadi.” Wolemerayo anali ndi nkhosa zambiri ndi ng'ombenso zambiri. Apo Davide adadzuka pansi paja, ndipo adakasamba, nadzola mafuta, nkusintha zovala zake. Tsono adakaloŵa m'nyumba ya Chauta, nakapembedza. Pambuyo pake adapita kunyumba kwake, naitanitsa chakudya. Ndipo anthu atabwera nacho, iye adadya. Tsono atumiki ake aja adamufunsa kuti, “Tatifotokozerani, kodi zimene mwachitazi nzotani? Pamene mwana uja anali moyo, inu munkakana kudya. Koma pamene adamwalira, inu mudadzuka, nkuyamba kudya.” Davide adati, “Pamene mwanayo anali moyo, ndinkakana zakudya ndipo ndinkalira, poti ndinkati, ‘Sizidziŵika, mwina kapena Chauta nkundikomera mtima, kuti mwanayo akhale moyo?’ Koma tsopano mwanayo wafa. Nanga ndizikaniranjinso zakudya? Kodi ndingathe kumbwezanso? Ine ndidzapitadi kumene kuli iyeko, koma iyeyo sadzabwereranso kwa ine.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 1:13-14

Inu ansembe, valani ziguduli mudzigunde pa chifuwa chifukwa cha chisoni. Lirani, inu otumikira ku guwa. Tiyeni, mufunde ziguduli usiku wonse, inu atumiki a Mulungu wanga. Pakuti chopereka cha chakudya ndi chakumwa sizidzaonekanso ku Nyumba ya Mulungu wanu. Lamulani kuti anthu asale zakudya. Itanitsani msonkhano waulemu. Akulu ndi onse okhala m'dziko asonkhane ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu, ndipo iwowo alire kwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 69:10-11

Pamene ndidadzilanga posala zakudya, anthu adandinyoza. Pamene ndidavala chiguduli kuwonetsa chisoni, ndidasanduka chinthu choŵaseketsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 58:10-11

mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana. Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:6

Koma iwe, pamene ukuti upemphere, loŵa m'chipinda chako, tseka chitseko, ndipo upemphere kwa Atate ako amene ali osaoneka. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 8:15

Anthu onsewo ndidaŵasonkhanitsa ku mtsinje umene umafika mpaka ku mudzi wa Ahava, ndipo kumeneko tidagona m'zithando masiku atatu. Pamene ndinkayang'ana anthu ndi ansembe, ndidapeza kuti ana a Levi palibe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 30:7-8

Pamenepo Davide adauza wansembe Abiyatara, mwana wa Ahimeleki, kuti, “Undipatse efodi ija.” Abiyatara adampatsa. Tsono Davide adapempha nzeru kwa Chauta nati, “Kodi ndilitsatire gulu lankhondo la Aamaleke? Kodi ndidzaŵapambana?” Chauta adamuyankha kuti, “Litsatire, pakuti udzalipambana ndithu ndipo udzaŵapulumutsa akapolowo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 63:1-5

Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi. Iwo adzaperekedwa kuti akaphedwe ku nkhondo, motero adzasanduka chakudya cha nkhandwe. Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu. Onse olumbirira Iye, adzamtamanda, koma pakamwa pa anthu abodza padzatsekedwa. Ndikukhumbira kukuwonani m'malo anu oyera ndi kuwona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu. Ndidzakutamandani chifukwa chikondi chanu nchabwino kupambana moyo. Choncho ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga. Ndidzakweza manja anga kwa Inu mopemphera. Mudzandikhutitsa ndi zonona, ndipo ndidzakutamandani ndi mau osangalala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yona 4:2

Tsono adapemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, nzimenezitu zimene ndinkaopa ndili kwathu. Nchifukwa chake ndidaayesetsa kuthaŵira ku Tarisisi. Ndidaadziŵa kuti Inu ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo, woleza mtima ndi wa chikondi chosasinthika, ndiponso wokhululukira machimo nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 84:2

Mtima wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka, kufunitsitsa kuwona mabwalo a Chauta. Inu Mulungu wamoyo, ndikukuimbirani mwachimwemwe ndi mtima wanga wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:8-9

Athokoze Chauta chifukwa cha chikondi chake chosasinthika, chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse. Chauta amapha ludzu la munthu womva ludzu, amamudyetsa zinthu zabwino munthu womva njala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:36-37

Kunalinso mneneri wina wamkazi, dzina lake Anna, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere. Anali wokalamba kwambiri. Anali atakhala pa banja zaka zisanu ndi ziŵiri zokha, pambuyo pake nkukhala wamasiye kufikira msinkhu wa zaka 84. Sankachokatu ku Nyumba ya Mulungu, ankakonda kudzatumikira Mulungu usana ndi usiku pakupemphera ndi kusala zakudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 8:10

Tsono Nehemiya adapitiriza nati, “Kazipitani, mukachite phwando ku nyumba, kenaka muŵapatseko anzanu amene sadakonze kanthu. Pakuti lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wathu. Tsono musakhale ndi chisoni, popeza kuti chimwemwe chimene Chauta amakupatsani, chimakulimbikitsani.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 2:18-19

Apo chikondi cha Chauta chidayaka ngati moto chifukwa cha dziko lake, ndipo adaŵachitira chifundo anthu ake. Chauta adaŵayankha anthu ake kuti, “Ndikutumizirani tirigu, vinyo ndi mafuta, ndipo mudzakhuta ndithu. Sindidzalolanso kuti akunja akunyozeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 13:1-3

Mu mpingo wa ku Antiokeya munali alaliki ndi aphunzitsi aŵa: Barnabasi, Simeoni (wotchedwa Wakuda), Lusio wa ku Kirene, Manaene (amene adaaleredwa pamodzi ndi bwanamkubwa Herode), ndiponso Saulo. nati, “Iwe mwana wa Satana, mdani wa chilungamo, wa mtima wa kunyenga kulikonse ndi kuchenjeretsa kwamtundumtundu, udzaleka liti kupotoza njira zolungama za Ambuye? Ona dzanja la Ambuye likukantha tsopano apa. Ukhala wakhungu osaonanso dzuŵa pa kanthaŵi.” Nthaŵi yomweyo khungu ndi mdima zidamgweradi, ndipo adayamba kufunafuna anthu oti amgwire dzanja ndi kumtsogolera. Pamene bwanamkubwa uja adaona zimene zidachitikazo, adakhulupirira. Adaadabwa nazo zimene iwo adaaphunzitsa za Ambuye. Paulo ndi anzake adayenda m'chombo kuchokera ku Pafosi kukafika ku Perga m'dera la Pamfiliya. Koma Yohane adaŵasiya nabwerera ku Yerusalemu. Kuchokera ku Perga iwo adapitirira nakafika ku Antiokeya m'dera la Pisidiya. Pa tsiku la Sabata adaloŵa m'nyumba yamapempherero ya Ayuda, nakhala pansi. Ataŵerengedwa mau a m'buku la Malamulo a Mose ndi m'buku la aneneri, akulu a nyumba yamapemphero ija adaŵatumira mau oŵauza kuti, “Abale, ngati muli ndi mau olimbikitsa nawo anthuŵa, nenani.” Apo Paulo adaimirira nakweza dzanja kuti anthu akhale chete, ndipo adayamba kulankhula. Adati, “Inu Aisraele, ndi ena nonse oopa Mulungu, mverani. Mulungu wa mtundu wathu wa Aisraele, adasankha makolo athu, ndipo adaŵakuza pamene anali alendo ku dziko la Ejipito. Adaŵatulutsa m'dzikomo ndi dzanja lake lamphamvu, adaŵasamalabe mopirira m'chipululu zaka makumi anai. Iye adaononga mitundu isanu ndi iŵiri ya anthu m'dziko la Kanani, napereka dziko lao kwa Aisraele kuti likhale laolao. Zonsezi zidatenga zaka ngati 450. Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.” “Pambuyo pake adaŵapatsa oweruza kufikira nthaŵi ya mneneri Samuele. Kenaka anthu adapempha kuti aŵapatse mfumu, ndipo Mulungu adaŵapatsa Saulo, mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, iye nkuŵalamulira pa zaka makumi anai. Pambuyo pake Mulungu adamchotsa Sauloyo, naika Davide kuti akhale mfumu yao. Za iyeyu Mulungu adanena kuti, ‘Ndapeza Davide, mwana wa Yese, ndiye munthu wanga wapamtima, amene adzachita zonse zimene Ine ndifuna.’ Mwa zidzukulu za Davideyo Mulungu adasankha Yesu kuti akhale Mpulumutsi wa Aisraele, monga momwe adaalonjezera kale. Iyeyo asanayambe ntchito, Yohane ankalalikira Aisraele onse kuti atembenuke mtima ndi kubatizidwa. Pamene Yohane anali pafupi kutsiriza ntchito yake, adafunsa anthu kuti, ‘Kodi inu mumayesa kuti ine ndine yani? Inetu sindine amene mukumuyembekezayo ai. Koma pakubwera wina pambuyo panga amene ine sindili woyenera ngakhale kumvula nsapato zake.’ “Ine abale, zidzukulu za Abrahamu, ndi ena nonse oopa Mulungu, uthenga wa chipulumutsowu Mulungu watumizira ife. Anthu okhala ku Yerusalemu ndi akulu ao sadamzindikire Yesu, ndipo sadamvetse mau a aneneri amene amaŵerengedwa tsiku la Sabata lililonse. Komabe pakumzenga mlandu Yesuyo kuti aphedwe, adachitadi zimene aneneri adaaneneratu. Ngakhale sadapeze konse chifukwa chomuphera, komabe adapempha Pilato kuti Yesuyo aphedwe. Ndipo atachita zonse zimene zidalembedwa za Iye, adamtsitsapo pa mtanda paja namuika m'manda. Tsono atasala zakudya ndi kupemphera adaŵasanjika manja naŵatuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 58:13-14

Chauta akunena kuti, “Muzidziletsa kuchita zanuzanu pa Sabata, osagwira ntchito zanu pa tsiku langa loyera. Tsiku la Sabatali muzilitcha kuti chinthu chosangalatsa, tsiku loyera la Chauta muzilitcha kuti chinthu cholemekezeka. Muzililemekeza pakusayendayenda, poleka kugwira ntchito zanu ndiponso posakamba nkhani zachabe. Mukatero ndiye kuti mudzakondwa mwa Ine, Chauta, ndipo ndidzakukwezani ndi kukupambanitsani pa dziko lonse lapansi. Mudzadyerera dziko limene ndidapatsa Yakobe kholo lanu. Ine Chauta ndalankhula zimenezi ndi pakamwa panga.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 20:1-30

Nthaŵi ina, Amowabu, Aamoni ndi Ameuni ena adabwera kudzamenyana nkhondo ndi Yehosafati. Pajatu pamene Aisraele ankachoka ku Ejipito, simudalole kuti aŵathire nkhondo Aamoni, Amowabu ndi anthu a ku phiri la Seiri. Onsewo adaŵaleka osaŵaononga. Koma tsopano chimene akutibwezera nkudzatipirikitsa m'dziko limene Inu mudatipatsa kuti likhale choloŵa chathu. Inu Mulungu wathu, monga simuŵalanga iwoŵa? Ife tilibe mphamvu zoti nkulimbana nacho chinamtindi chikudzatithira nkhondocho. Tikusoŵa chochita, maso athu ali pa Inu.” Nthaŵi imeneyo nkuti anthu onse a dziko la Yuda ataimirira pamaso pa Chauta, pamodzi ndi akazi ao ndi ana ao ndi ang'onoang'ono omwe. Ndipo mumsonkhanomo mzimu wa Chauta udatsikira Yehaziele, mwana wa Zekariya, mwana wa Benaya, mwana wa Yeiyele, mwana wa Mataniya, mlevi, mmodzi mwa ana a Asafu. Iyeyo adati, “Mverani Ayuda nonsenu, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu, ndi inunso mfumu Yehosafati. Chauta akukuuzani kuti, ‘Musaope, ndipo musataye nacho mtima chinamtindi cha anthuchi, pakuti nkhondo si yanu, nja Mulungu. Maŵa mupite mukamenyane nawo nkhondo. Adzabwera ndipo adzadzera cha ku chikwera cha Zizi. Mudzaŵapeza pafupi ndi chigwa cha kuvuma kwa chipululu cha Yeruwele. Sikudzafunika kuti mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale m'malo mwanu, mungoima, ndipo muwonerere Chauta akukumenyerani nkhondo, inu anthu a ku Yuda ndi inu anthu a mu Yerusalemu.’ Musaope ndipo musataye mtima, mutuluke maŵa mukalimbane nawo, Chauta adzakhala nanu.” Apo Yehosafati adazyolikitsa nkhope yake pansi, ndipo anthu onse a ku Yuda ndi anthu onse a ku Yerusalemu adagwa pansi pamaso pa Chauta nampembedza. Kenaka Alevi, ana a Kohati ndi ana a Kora, adaimirira kuti atamande Chauta, Mulungu wa Aisraele, mokweza kwambiri. Anthu ena adadzauza Yehosafati kuti “Chinamtindi cha anthu chikudzamenyana nanu nkhondo, kuchokera ku Edomu patsidya pa nyanja. Anthuwo ali ku Hazazoni-Tamara,” (ndiye kuti Engedi). Tsono anthuwo adadzuka m'mamaŵa nakaloŵa m'chipululu cha ku Tekowa. Pamene ankatuluka, Yehosafati adaima nati, “Tamverani inu anthu a ku Yuda ndi inu okhala mu Yerusalemu. Khulupirirani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalimbika, khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzapambana.” Tsono ataŵafunsa anthuwo, adasankha ena oti aziimbira Chauta ndi kumtamanda, oimbawo atavala zovala zoyera, akutsogolera gulu lankhondo namanena kuti, “Thokozani Chauta, pakuti chikondi chake chosasinthika chimakhala mpaka muyaya.” Iwo aja atayamba kuimba ndi kutamanda, Chauta adaŵatchera msampha Aamoni, Amowabu ndiponso anthu a ku phiri la Seiri, amene adaadzalimbana ndi anthu a ku Yuda, kotero kuti adaŵagonjetsa onse. Aamoni ndi Amowabu adaukira anthu okhala ku phiri la Seiri, naŵaononga kotheratu. Ndipo ataononga anthu onse a ku Seiri aja, adayamba kumaphana okhaokha. Pambuyo pake anthu a ku Yuda atafika ku nsanja yakuchipululu, adapenya kumene kunali chinamtindi cha anthu chija. Adangoona mitembo yokhayokha ili pansi ngundangunda. Panalibe ndi mmodzi yemwe wopulumuka. Tsono Yehosafati ndi anthu ake atadzafunkha za anthuwo, adapeza ng'ombe zambirimbiri, katundu, zovala ndiponso zinthu zamtengowapatali. Adatenga zinthu zochuluka, mpaka kuzilephera. Adafunkha zinthuzo masiku atatu, chifukwa zinali zambirimbiri. Pa tsiku lachinai lake, adasonkhana ku chigwa cha Beraka, ndipo kumeneko adatamanda Chauta. Nchifukwa chake malowo amatchedwa chigwa cha Beraka mpaka lero lino. Tsono onsewo a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu adabwerera mokondwa ku Yerusalemu, Yehosafati akuŵatsogolera, pakuti Chauta adaŵakondweretsa poŵagonjetsera adani ao. Anthuwo adafika ku Yerusalemu, ku Nyumba ya Chauta, akuimba azeze, apangwe ndiponso malipenga. Ndipo maufumu onse a m'maiko achilendowo adachita mantha kwambiri, atamva kuti Chauta ndiye adathira nkhondo pa adani a Aisraele. Pamenepo Yehosafati adachita mantha, ndipo adaganiza zopempha nzeru kwa Chauta, nalengeza kuti anthu onse a ku dziko la Yuda asale zakudya. Motero mudakhala bata mu ufumu wonse wa Yehosafati, pakuti Mulungu adampatsa mtendere ku maiko onse omzungulira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 21:27

Ahabu atamva mau amenewo, adang'amba zovala zake, navala ziguduli. Adasala zakudya nagona pa zigudulizo, ndipo adayamba kuyenda modzichepetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 20:18-26

Aisraele adanyamuka napita ku Betele kukafunsa kwa Mulungu kuti, “Ndani mwa ife amene ayambe kukamenyana nkhondo ndi Abenjamini?” Chauta adayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo limene liyambe.” Tsono Aisraele adadzuka m'maŵa nakamanga zithando zao moyang'anana ndi Gibea. Atsogoleri a anthu onse ndi a mafuko onse a Aisraele adabwera ku msonkhano wa anthu a Mulungu. Onse pamodzi analipo 400,000 oyenda pansi omenya nkhondo ndi lupanga. Aisraele adapita kukamenyana nkhondo ndi Abenjamini, nakhazika ankhondo ao kuyang'ana mzinda wa Gibea. Nawonso Abenjamini adatuluka ku Gibea ndipo tsiku limenelo adapha Aisraele 22,000. Koma Aisraelewo adalimbitsana mtima ndipo adakhazika ankhondo ao kachiŵiri pa malo omwe aja pamene adaaŵakhazika tsiku loyamba lija. Tsono Aisraelewo adapita kukalira pamaso pa Chauta mpaka madzulo. Adakafunsa Chauta kuti, “Kodi tipitenso kachiŵiri kukamenyana nawo nkhondo Abenjamini, abale athu?” Chauta adayankha kuti, “Inde pitani mukamenyane nawo.” Choncho Aisraele adafika pafupi, kuti akalimbane ndi Abenjamini tsiku lachiŵiri lake. Abenjamini adatulukanso mu mzinda wa Gibea, kukalimbana nawo tsiku lachiŵirilo, ndipo adapha ankhondo a Aisraele 18,000. Tsono Aisraele onse, ndiye kuti gulu lonse la ankhondo, adapita ku Betele ndi kukalira kumeneko. Adakhala pansi pamaso pa Chauta, nasala chakudya tsiku limenelo mpaka madzulo, ndipo adapereka nsembe zopsereza ndi zamtendere pamaso pa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:2-4

Pa masiku makumi anai Yesu adasala zakudya usana ndi usiku, ndipo pambuyo pake adamva njala. Pomwepo iwo adasiya makoka ao, namamtsatadi. Atapitirira pamenepo, Yesu adaona enanso aŵiri pachibale pao: Yakobe ndi Yohane, ana a Zebedeo. Iwo anali m'chombo pamodzi ndi bambo waoyo, akukonza makoka ao, Yesu nkuŵaitana. Pomwepo iwowo adasiya chombo chao ndi bambo wao uja, namatsata Yesu. Yesu adayendera dziko lonse la Galileya akuphunzitsa m'nyumba zamapemphero ndi kulalika Uthenga Wabwino wonena za ufumu wakumwamba. Ankachiritsanso nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi. Mbiri yake idabuka m'dziko lonse la Siriya, kotero kuti anthu ankabwera kwa Iye ndi odwala onse ovutika ndi nthenda ndi zoŵaŵa zosiyanasiyana, ogwidwa ndi mizimu yoipa, akhunyu ndi opunduka, Iye nkumaŵachiritsa. Anthu ambirimbiri ankamutsata kuchokera ku Galileya, ku dera lotchedwa Mizinda Khumi, ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi kutsidya kwa mtsinje wa Yordani. Tsono Woyesa uja adadza namuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, lamulani miyala ili apayi kuti isanduke chakudya.” Koma Yesu adati, “Malembo akuti, “ ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mau onse olankhula Mulungu.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 1:14-16

Lamulani kuti anthu asale zakudya. Itanitsani msonkhano waulemu. Akulu ndi onse okhala m'dziko asonkhane ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu, ndipo iwowo alire kwa Iye. Kalanga ine! Tsiku loopsa layandikira, tsiku la Chauta, likubwera ndi chiwonongeko chochokera kwa Mphambe. Chakudya chathu chikutha ife tikuwona. Mulibenso chimwemwe ndi chisangalalo m'Nyumba ya Mulungu wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 9:3

Anthuwo adaimirira pomwepo, ndipo adamva mau a m'buku la Malamulo a Chauta akuŵaŵerenga nthaŵi yokwanira maora atatu. Pa maora atatu enanso, anthuwo ankaulula machimo ao namapembedza Chauta, Mulungu wao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 12:15-16

Pompo Natani adabwerera kunyumba kwake. Motero Chauta adalanga mwana amene mkazi wa Uriya adabalira Davide, ndipo adadwala kwambiri. Nchifukwa chake Davide adapempherera mwanayo kwa Mulungu. Adaleka kudya, nakaloŵa m'nyumba, nkukagona pansi usiku wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:2

masiku makumi anai, ndipo kumeneko Satana ankamuyesa. Yesu sankadya kanthu masiku amenewo, ndipo pamene masikuwo adatha, adamva njala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:17

Koma iwe, pamene ukusala zakudya, samba m'maso nkudzola mafuta kumutu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 9:18-19

Pompo m'maso mwake mudachoka zinthu zonga mamba a nsomba, ndipo adayambanso kupenya. Adaimirira nabatizidwa, ndipo atadya chakudya, adapezanso mphamvu. Saulo adakhala masiku angapo limodzi ndi ophunzira a ku Damasiko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 10:6-8

Pambuyo pake Ezara adachokako ku Nyumba ya Mulungu napita ku chipinda cha Yehohanani, mwana wa Eliyasibu, kumene adakachezera usikuwo. Sadadye buledi kapena kumwa madzi. Nthaŵi yonseyo adakhalira kulira chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu obwerako ku ukapolo aja. Tsono anthu adalengeza m'dziko lonse la Yuda ndi mu mzinda wa Yerusalemu, kwa onse ochokera ku ukapolo aja, kuti asonkhane ku Yerusalemu. Adanena kuti, “Wina aliyense akapanda kufika asanathe masiku atatu, ndiye kuti potsata lamulo la atsogoleri ndi la akulu, adzayenera kumlanda katundu wake yense, ndipo adzachotsedwe m'gulu la anthu obwerako ku ukapolo aja.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 2:12

Koma Chauta akunena kuti, “Ngakhale tsopano bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse, mukusala zakudya, mukukhetsa misozi ndi kulira mwachisoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 9:25-27

Aliyense wothamanga pa mpikisano wa liŵiro amadziletsa pa zonse. Iwowo amachita zimenezi kuti akalandire mphotho ya nkhata yamaluŵa yotha kufota. Koma mphotho imene ife tidzalandira, ndi yosafota. Nchifukwa chake ndimathamanga monga munthu wodziŵa kumene walinga. Ndiponso ndikamachita mpikisano womenyana, sindichita ngati munthu amene angomenya mophonya. Ndimazunza thupi langa ndi kuligonjetsa, kuti likhale ngati kapolo wondimvera. Ndimachita zimenezi kuwopa kuti ine ndemwe, amene ndidaitana ena ku mpikisano, ndingapezeke wosayenera kuchita nao mpikisanowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:8

Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino. Ngwodala munthu wothaŵira kwa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 63:1

Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 5:33

Anthu ena adauza Yesu kuti, “Ophunzira a Yohane amasala zakudya kaŵirikaŵiri nkumapemphera, chimodzimodzinso ophunzira a Afarisi. Koma ophunzira anu amangodya ndi kumwa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Mulungu Wakuombola! Lero ndikukuimbirani ndi kufuna nkhope yanu kuti ndikupatseni ulemerero ndi ulemu. Ndimadzera kwa inu kudzera mwa Ambuye wanga Yesu Khristu, inu nokha ndinu woyenera ulemerero ndi ulemu. Ambuye, zikomo chifukwa cha chida champhamvu chauzimu ichi chomwe ndi kusala kudya ndi kupemphera, kuti kudzera mu kulira kumeneku kwa inu, maunyolo, zomangira, ndi zomangira zoipa ziyambe kumasulidwa pa moyo wanga. Mzimu Woyera ndithandizeni kukhala ndi moyo wosala kudya ndi kupemphera, womwe umadalira kukhalapo kwanu kokha ndi mtima wofunitsitsa kudzipatula kwa inu, mundiphunzitse kumizidwa mu chiyanjano chozama nanu, kufunafuna malangizo anu ndi chifuniro chanu changwiro pa moyo wanga m'malo obisikawo kudzera mu kusala kudya ndi kupemphera. Ndipatseni mphamvu kuti ndigonjetse zofooka za thupi langa, ndikuletsa chakudya chakuthupi, kuti ndidzaze ndi chauzimu chokha. Mu mawu anu mukuti: "Ndinatembenuzira nkhope yanga kwa Mulungu Ambuye kuti ndimufunefune m'pemphero ndi m'mapembedzero, m'kusala kudya, m'zifuwa ndi m'phulusa." Ndinatembenuzira nkhope yanga kwa Mulungu Ambuye kuti ndimufunefune m'pemphero ndi m'mapembedzero, m'kusala kudya, m'zifuwa ndi m'phulusa. Mzimu Woyera, kuti kudzera mu kusala kudya kumeneku mphamvu yanu iwonekere m'moyo wanga ndipo nditha kugonjetsa chilichonse ndi mapulani onse a mdani motsutsana ndi ine ndi banja langa. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa