Ndikudziwa kuti zinthu zimakhala zovuta munthu wamtima wako akamwalira. Ukumva chisoni chachikulu, ndipo izi ndizachibadwa. Koma usalole kuti chisonichi chikulemere kwambiri. Kumbukira kuti Mzimu Woyera, Mtonthozi wathu, ali nafe. Adzakutonthoza ndi kukupatsa mphamvu kuti upirire nthawi yovutayi.
Monga wokhulupirira, tikudziwa kuti tikachoka padziko lapansi lino, tipita kwabwino kwambiri kwa Ambuye Yesu Khristu. Anthu athu amatipatsa, koma tiyenera kukumbukira kuti ali bwino kuposa ife. Kondwera podziwa kuti miyoyo yawo yapulumutsidwa.
Tinalengedwera Mulungu. Mawu ake amatiuza kuti ngati tili ndi moyo, tili ndi moyo wa Ambuye, ndipo ngati timwalira, timwalira wa Ambuye. Kaya tili ndi moyo kapena tamwalira, ndife a Ambuye. Funa chitonthozo kwa Mulungu, ndipo upumule mwa Iye. Khulupirira kuti Mulungu ali nawe ndipo akufuna kukulimbitsa ndi kutonthoza mtima wako. Ingomulola Mulungu agwire ntchito m'moyo wako.
Yohane 11:25: Yesu anati kwa iye, “Ine ndine kuuka kwa akufa, ndi moyo; wokhulupirira Ine, angakhale atamwalira, adzakhala ndi moyo.”
Yesu adamuuza kuti, “Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso woŵapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo.
Tsopano tikuuzeni mau a Ambuye mwini. Ife amoyofe, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sikuti tidzaŵasiya kumbuyo amene adamwalira aja ai.
Kwa inetu moyo ndi Khristu amene, ndipo nayonso imfa ili ndi phindu. Koma ngati kukhalabe moyo kungandipatse mwai woti ndigwire ntchito yoonetsa zipatso, sindidziŵa kaya ndingasankhe chiti. Ndagwira njakata. Kwinaku ndikulakalaka kuti ndisiye moyo uno ndikakhale pamodzi ndi Khristu, pakuti chimenechi ndiye chondikomera koposa.
Paja ife timakhulupirira kuti Yesu adaamwalira naukanso. Motero timakhulupiriranso kuti anthu amene adamwalira akukhulupirira Yesu, iwonso Mulungu adzaŵaukitsa nkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo. Tsopano tikuuzeni mau a Ambuye mwini. Ife amoyofe, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sikuti tidzaŵasiya kumbuyo amene adamwalira aja ai. Padzakhala mfuu wa mau a mngelo wamkulu ndi wa lipenga la Mulungu. Ndipo pamenepo Ambuye mwini adzatsika kuchokera Kumwamba. Anthu amene adafa akukhulupirira Khristu, adzayamba ndiwo kuuka. Pambuyo pake ife amoyofe, otsalafe, tidzatengedwa pamodzi nawo m'mitambo kuti tikakumane ndi Ambuye mu mlengalenga. Motero tidzakhala ndi Ambuye nthaŵi zonse.
Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso. Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo Atate amakhala mwa Ine? Mau amene ndimakuuzani sachokera kwa Ine ndekha ai, koma Atate amene amakhala mwa Ine, ndiwo amagwira ntchito yao. Mundikhulupirire kuti Ine ndimakhala mwa Atate ndipo Atate amakhala mwa Ine. Kupanda apo, khulupiriranitu chifukwa cha ntchito zanga zomwezo. Ndithu ndikunenetsa kuti amene amandikhulupirira, ntchito zomwe ndimachita Ine, nayenso adzazichita. Ndipo adzachita zoposa pamenepa, chifukwa ndikupita kwa Atate. Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.” “Ngati mundikonda, muzidzatsata malamulo anga. Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthaŵi zonse. Nkhosweyo ndi Mzimu wodziŵitsa zoona. Anthu ongokonda zapansipano sangathe kumlandira ai, chifukwa samuwona kapena kumdziŵa. Koma inu mumamdziŵa, chifukwa amakhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu. Sindidzakusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ndidzabweranso kwa inu. Kwangotsala kanthaŵi pang'ono, ndipo anthu ongokonda zapansipano sadzandiwonanso, koma inu mudzandiwona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo. M'nyumba mwa Atate anga muli malo ambiri okhalamo. Kukadakhala kuti mulibe malo, ndikadakuuzani. Ndikupita kukakukonzerani malo. Tsiku limenelo mudzadziŵa kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo inu mumakhala mwa Ine, monga Ine ndimakhala mwa inu. “Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.” Yudasi, osati Iskariote uja ai, adamufunsa kuti, “Ambuye zatani kuti muziti mudzadziwonetsa kwa ife, koma osati kwa anthu onse?” Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma. “Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu. Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani. “Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa. Mwandimva ndikukuuzani kuti, ‘Ndikupita, koma ndidzabweranso kwa inu.’ Mukadandikonda, bwenzi mutakondwera kuti ndikupita kwa Atate, chifukwa Atate ngoposa Ine. Ndakuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire. Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti inunso mukakhale kumene kuli Ine. Sindilankhula nanunso zambiri tsopano ai, pakuti Satana, mfumu ya anthu ochimwa a dziko lapansi, alikudza. Iyeyo alibe mphamvu pa Ine, koma anthu onse ayenera kudziŵa kuti ndimakonda Atate, nchifukwa chake ndikuchita monga Atate adandilamulira. Tiyeni, tizipita.” Ndipo kumene ndikupita Ineko, njira yake mukuidziŵa.”
“Mtheradi ndikudziŵa kuti Momboli wanga alipo, ndipo pa nthaŵi yomaliza adzabwera kudzanditeteza. Khungu langa litatha nkuwonongeka, m'thupi langa lomweli ndidzamuwona Mulungu.
Padzakhala mfuu wa mau a mngelo wamkulu ndi wa lipenga la Mulungu. Ndipo pamenepo Ambuye mwini adzatsika kuchokera Kumwamba. Anthu amene adafa akukhulupirira Khristu, adzayamba ndiwo kuuka.
Mvetsetsani, ndikuuzeni chinsinsi. Sikuti tonse tidzamwalira, komabe tonse tidzasandulika. Zidzachitika mwadzidzidzi, pa kamphindi ngati kuphethira kwa diso, pamene lipenga lotsiriza lidzalira. Likadzaliratu lipengalo, akufa adzauka ndi matupi amene sangaole, ndipo ife tidzasandulika. Pakuti thupi lotha kuwolali liyenera kusanduka losatha kuwola, ndipo thupi lotha kufali liyenera kusanduka losatha kufa.
Tsono thupi lotha kuwolali likadzasanduka losatha kuwola, ndipo thupi lotha kufali likadzasanduka losatha kufa, pamenepo zidzachitikadi zimene Malembo adanena kuti, “Imfa yagonjetsedwa kwathunthu.” “Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, ululu wako uli kuti?” Ululu wake wa imfa ndi uchimo, ndipo chimene chimapatsa uchimo mphamvu, ndi Malamulo. Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Ndidamva mau amphamvu ochokera ku mpando wachifumu uja. Mauwo adati, “Tsopano malo okhalamo Mulungu ali pakati pa anthu. Iye adzakhala nawo pamodzi, ndipo iwo adzakhala anthu akeake. Mulungu mwini adzakhala nawo, ndipo adzakhala Mulungu wao. Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.”
“Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo.
Musadabwe nazo zimenezi, pakuti ikudza nthaŵi pamene anthu onse amene ali m'manda adzamva mau ake nadzatuluka. Anthu amene adachita zabwino, adzauka kuti akhale ndi moyo, koma amene adachita zoipa, adzauka kuti azengedwe mlandu.”
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu. Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako. Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake. Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Palibe ndi mmodzi yemwe mwa ife amene amakhala moyo chifukwa cha iye yekha, kapena kufa chifukwa cha iye yekha. Tikakhala ndi moyo, moyowo ndi wa Ambuye, tikafa, timafera Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ao a Ambuye. Paja Khristu adamwalira nakhalanso ndi moyo, kuti akhale Mbuye wa anthu akufa ndiponso wa anthu amoyo.
Anamwali adzavina mokondwa, achinyamata ndi okalamba omwe adzasangalala. Kulira kwao kuja ndidzakusandutsa chimwemwe. Ndidzaŵasangalatsa, ndidzaŵakondwetsa, nkuchotsa chisoni chao.
Paja ife timakhulupirira kuti Yesu adaamwalira naukanso. Motero timakhulupiriranso kuti anthu amene adamwalira akukhulupirira Yesu, iwonso Mulungu adzaŵaukitsa nkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo.
Chauta adzathetsa imfa mpaka muyaya, adzapukuta misozi m'maso mwa aliyense, ndipo adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi. Watero Chauta.
Pambuyo pake ife amoyofe, otsalafe, tidzatengedwa pamodzi nawo m'mitambo kuti tikakumane ndi Ambuye mu mlengalenga. Motero tidzakhala ndi Ambuye nthaŵi zonse.
Pansi pano chinthu chilichonse chili ndi nyengo yake ndi nthaŵi yake yomwe adaika Mulungu: Ndaziwona ntchito zimene Mulungu adapatsa anthu kuti azizigwira. Adapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthaŵi yake. M'mitima mwa anthu Mulungu adaikanso nzeru zotanthauzira zochitika za pa mibadwo ndi mibadwo. Komabe anthuwo sangathe kuzitulukira ntchito zonse za Mulungu kuyambira pa chiyambi mpaka pomalizira. Ndikudziŵa kuti kwa anthu palibe chabwino china choposa kukhala osangalala ndi kumadzikondweretsa nthaŵi yonse ya moyo wao. Ndi mphatso ya Mulungu kwa anthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ntchito zao zolemetsa. Ndikudziŵa kuti zimene Mulungu amazichita zimakhazikika mpaka muyaya. Palibe zimene zingathe kuwonjezedwa kapena kuchotsedwapo pa zimenezo. Mulungu adazipanga motero, kuti choncho anthu azimumvera. Zimene zilipo tsopano zidaaliponso kale. Zimene zidzakhalepo kutsogolo, zidaaliponso kale. Mulungu amabwezanso zakale zimene zidapita kuti zichitikenso. China chimene ndidachiwona pansi pano ndi ichi: Koyenera kukhala chiweruzo chabwino, komwekonso kumapezeka kuipa mtima. Koyenera kukhala chilungamo, komwekonso kumapezeka zoipa. Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Mulungu adzaŵaweruza onse, abwino ndi oipa omwe, pakuti adaika nthaŵi yochitikira chinthu chilichonse ndiponso ntchito iliyonse.” Kunena za anthu, ndinkalingaliranso kuti, “Mulungu amaŵayesa ndi cholinga choti aŵaonetse kuti iwowo sasiyana konse ndi nyama. Zimene zimachitikira anthu, zomwezonso zimachitikira nyama. Monga chinacho chimafa, chinacho chimafanso. Zonsezo zimapuma mpweya umodzimodzi, munthu saposa nyama. Zonsezi nzopandapake. pali nthaŵi yobadwa ndi nthaŵi yomwalira, pali nthaŵi yobzala ndi nthaŵi yozula zobzalazo.
Mudzati, “Mulungu wathu ndi wotere, ndi Mulungu wathu kuyambira muyaya mpaka muyaya. Iye adzakhala wotitsogolera nthaŵi zonse.”
Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso. Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo Atate amakhala mwa Ine? Mau amene ndimakuuzani sachokera kwa Ine ndekha ai, koma Atate amene amakhala mwa Ine, ndiwo amagwira ntchito yao. Mundikhulupirire kuti Ine ndimakhala mwa Atate ndipo Atate amakhala mwa Ine. Kupanda apo, khulupiriranitu chifukwa cha ntchito zanga zomwezo. Ndithu ndikunenetsa kuti amene amandikhulupirira, ntchito zomwe ndimachita Ine, nayenso adzazichita. Ndipo adzachita zoposa pamenepa, chifukwa ndikupita kwa Atate. Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.” “Ngati mundikonda, muzidzatsata malamulo anga. Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthaŵi zonse. Nkhosweyo ndi Mzimu wodziŵitsa zoona. Anthu ongokonda zapansipano sangathe kumlandira ai, chifukwa samuwona kapena kumdziŵa. Koma inu mumamdziŵa, chifukwa amakhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu. Sindidzakusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ndidzabweranso kwa inu. Kwangotsala kanthaŵi pang'ono, ndipo anthu ongokonda zapansipano sadzandiwonanso, koma inu mudzandiwona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo. M'nyumba mwa Atate anga muli malo ambiri okhalamo. Kukadakhala kuti mulibe malo, ndikadakuuzani. Ndikupita kukakukonzerani malo. Tsiku limenelo mudzadziŵa kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo inu mumakhala mwa Ine, monga Ine ndimakhala mwa inu. “Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.” Yudasi, osati Iskariote uja ai, adamufunsa kuti, “Ambuye zatani kuti muziti mudzadziwonetsa kwa ife, koma osati kwa anthu onse?” Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma. “Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu. Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani. “Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa. Mwandimva ndikukuuzani kuti, ‘Ndikupita, koma ndidzabweranso kwa inu.’ Mukadandikonda, bwenzi mutakondwera kuti ndikupita kwa Atate, chifukwa Atate ngoposa Ine. Ndakuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire. Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti inunso mukakhale kumene kuli Ine.
“Mtheradi ndikudziŵa kuti Momboli wanga alipo, ndipo pa nthaŵi yomaliza adzabwera kudzanditeteza.
Abale, tifuna kuti mudziŵeko za anthu amene adamwalira, kuti chisoni chanu chisakhale ngati cha anthu ena amene alibe chiyembekezo. Paja ife timakhulupirira kuti Yesu adaamwalira naukanso. Motero timakhulupiriranso kuti anthu amene adamwalira akukhulupirira Yesu, iwonso Mulungu adzaŵaukitsa nkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo.
Tikakhala ndi moyo, moyowo ndi wa Ambuye, tikafa, timafera Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ao a Ambuye.
Pambuyo pake ndidamva mau ochokera Kumwamba. Adati, “Lemba kuti, Ngodala anthu akufa amene kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo muno afa ali otumikira Ambuye.” Mzimu Woyera akuti, “Inde, ngodaladi. Akapumule ntchito zao zolemetsa, pakuti ntchito zaozo zimaŵatsata.”
Musachite nazo mantha zoŵaŵa zimene mukukakumana nazo. Ndithu enanu Satana adzakuponyetsani m'ndende kuti akuyeseni, ndipo mudzazunzika pa masiku khumi. Khalani okhulupirika mpaka kufa, ndipo ndidzakupatsani moyo ngati mphotho yanu.
Koma ai, Khristu adauka ndithu kwa akufa. Pakati pa onse amene adafa, ndiye woyamba kuuka. Pakuti monga imfa idadza pansi pano kudzera mwa munthu wina, momwemonso kuuka kwa akufa kudadza kudzera mwa munthu wina. Monga anthu onse amamwalira chifukwa ndi ana a Adamu, momwemonso anthu onse adzauka chifukwa cholumikizana ndi Khristu. Koma aliyense adzauka pa nthaŵi yake: woyambirira ndi Khristu, ndipo pambuyo pake, pamene Khristuyo adzabwera, nawonso amene ali ake adzauka.
Chomwecho inunso mukuvutika tsopano, koma ndidzakuwonaninso. Pamenepo mtima wanu udzakondwa, ndipo palibe munthu amene adzakulandani chimwemwe chanucho.
Adati, “M'mimba mwa amai ndidatulukamo maliseche, namonso m'manda ndidzaloŵamo maliseche, Chauta ndiye adapatsa, Chauta ndiyenso walanda. Litamandike dzina la Chauta.”
Nkhosa zanga zimamva mau anga. Ine ndimazidziŵa, ndipo zimanditsatira. Ndimazipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzatayika konse. Palibe munthu wodzazilanda m'manja mwanga. Atate anga amene adandipatsa nkhosazo amapambana onse, ndipo palibe amene angathe kuzilanda m'manja mwao.
Pambuyo pake ndidaona thambo latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Paja thambo loyamba lija ndi dziko lapansi loyamba lija zinali zitazimirira, ndipo nyanja panalibenso. Pamenepo mngelo uja adandinyamula chamumzimu nakanditula pa phiri lalikulu ndi lalitali. Adandiwonetsa Mzinda Woyera uja, Yerusalemu, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu. Unkaŵala ndi ulemerero wa Mulungu. Kuŵala kwake kunali ngati kuŵala kwa mwala wamtengowapatali, ngati mwala wambee, wonyezimira ngati galasi. Mzindawo unali ndi linga lalikulu ndi lalitali. Lingalo linali ndi zipata khumi ndi ziŵiri, pazipatapo panali angelo khumi ndi aŵiri, ndipo pa zitseko zake padaalembedwa maina a mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele. Pa mbali zonse zinai za mzindawo panali zipata zitatuzitatu: kuvuma zitatu, kumwera zitatu, kumpoto zitatu, kuzambwe zitatu. Linga la mzindawo lidaamangidwa pa maziko khumi ndi aŵiri, ndipo pamazikopo padaalembedwa maina a atumwi khumi ndi aŵiri a Mwanawankhosa uja. Mngelo amene ankalankhula naneyo anali ndi ndodo yoyesera yagolide, yoti ayesere mzinda uja, zipata zake ndi linga lake. Mzindawo unali wolingana ponseponse, m'litali mwake ndi m'mimba mwake munali chimodzimodzi. Mngelo uja adayesa chozungulira mzindawo ndi ndodo yake ija, napeza kuti kutalika kwake kunali makilomita 2,200. M'litali mwake, m'mimba mwake ndi msinkhu wake, zonse zinali zolingana. Kenaka adayesa linga la mzindawo, napeza kuti msinkhu wake unali mamita 65. Mngeloyo ankayesa ndi muyeso womwe anthu amagwiritsa ntchito. Linga la mzindawo linali la miyala yambee, ndipo mzinda weniweniwo unali wa golide wangwiro, woŵala ngati galasi. Maziko aja omwe linga la mzindawo lidaamangidwapo, adaaŵakongoletsa ndi miyala yamitundumitundu yamtengowapatali. Maziko oyamba anali a mwala wambee; achiŵiri anali a mwala wabuluu ngati thambo; achitatu anali a mwala wotuŵira; achinai anali a mwala wobiriŵira; Tsono ndidaona Mzinda Woyera, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu. Unali wokonzeka ngati mkwati wamkazi wokonzekera mwamuna wake. achisanu anali a mwala mwina mofiira mwina mwabrauni; achisanu ndi chimodzi anali a mwala wofiira; achisanu ndi chiŵiri anali a mwala wachikasu; achisanu ndi chitatu anali a mwala wobiriŵira modera; achisanu ndi chinai anali a mwala wakadzira; achikhumi anali a mwala wachisipu; achikhumi ndi chimodzi anali a mwala wabuluu ngati changululu; achikhumi ndi chiŵiri anali a mwala wofiirira. Zitseko za pa zipata khumi ndi ziŵiri zija zinali za miyala yamtengowapatali kwambiri. Chitseko chilichonse chinali cha mwala umodzi wa mtundu womwewo. Ndipo mseu wamumzindamo unali wa golide wangwiro, woonekera mpaka pansi, ngati galasi. Sindidaonenso Nyumba ya Mulungu mumzindamo, pakuti Nyumba yake ndi Ambuye Mulungu, Mphambe, mwini wake, ndiponso Mwanawankhosa uja. Palibe chifukwa choti dzuŵa kapena mwezi ziziŵala pamzindapo, pakuti ulemerero wa Mulungu ndiwo umaŵalapo, ndipo nyale yake ndi Mwanawankhosa uja. Anthu a mitundu yonse adzayenda m'kuŵala kwake kwa mzindawo, ndipo mafumu a pa dziko lonse lapansi adzabwera ndi ulemerero wao m'menemo. Zitseko za pa zipata zake zidzakhala zosatseka tsiku lonse, chifukwa kumeneko kudzakhala kulibe usiku. Ndipo m'menemo adzabwera ndi ulemerero wa anthu a mitundu yonse, pamodzi ndi chuma chao. Koma simudzaloŵa kanthu kalikonse kosayera, kapena munthu aliyense wochita zonyansa, kapenanso wabodza. Okhawo amene maina ao adalembedwa m'buku la amoyo la Mwanawankhosa uja ndiwo adzaloŵemo. Ndidamva mau amphamvu ochokera ku mpando wachifumu uja. Mauwo adati, “Tsopano malo okhalamo Mulungu ali pakati pa anthu. Iye adzakhala nawo pamodzi, ndipo iwo adzakhala anthu akeake. Mulungu mwini adzakhala nawo, ndipo adzakhala Mulungu wao. Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.” Pamenepo wokhala pampando wachifumu uja adati, “Tsopano ndisandutsa zonse kuti zikhale zatsopano.” Adanenanso kuti, “Lemba zimenezi, pakuti mau ameneŵa ndi oona ndi oyenera kuŵakhulupirira.”
Mbiri yabwino ndi yopambana mafuta onunkhira bwino amtengowapatali. Tsiku lomwalira ndi lopambana tsiku lobadwa.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Ndagwira njakata. Kwinaku ndikulakalaka kuti ndisiye moyo uno ndikakhale pamodzi ndi Khristu, pakuti chimenechi ndiye chondikomera koposa.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto. “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.” Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama,
Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.”
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu. Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liŵiro, ndasunga chikhulupiriro. Tsopano chimene chikundidikira ndi mphotho ya chilungamo imene Mulungu wandisungira. Ambuye amene ali Woweruza wolungama, ndiwo amene adzandipatsa mphothoyo pa tsiku la chiweruzo. Tsonotu sadzangopatsa ine ndekha ai, komanso ena onse amene mwachikondi akudikira kuti Ambuyewo adzabwerenso.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa. ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza. Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,” ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala. Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe. Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse. Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube. Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere. Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali.
Pansi pano chinthu chilichonse chili ndi nyengo yake ndi nthaŵi yake yomwe adaika Mulungu: Ndaziwona ntchito zimene Mulungu adapatsa anthu kuti azizigwira. Adapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthaŵi yake. M'mitima mwa anthu Mulungu adaikanso nzeru zotanthauzira zochitika za pa mibadwo ndi mibadwo. Komabe anthuwo sangathe kuzitulukira ntchito zonse za Mulungu kuyambira pa chiyambi mpaka pomalizira. Ndikudziŵa kuti kwa anthu palibe chabwino china choposa kukhala osangalala ndi kumadzikondweretsa nthaŵi yonse ya moyo wao. Ndi mphatso ya Mulungu kwa anthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ntchito zao zolemetsa. Ndikudziŵa kuti zimene Mulungu amazichita zimakhazikika mpaka muyaya. Palibe zimene zingathe kuwonjezedwa kapena kuchotsedwapo pa zimenezo. Mulungu adazipanga motero, kuti choncho anthu azimumvera. Zimene zilipo tsopano zidaaliponso kale. Zimene zidzakhalepo kutsogolo, zidaaliponso kale. Mulungu amabwezanso zakale zimene zidapita kuti zichitikenso. China chimene ndidachiwona pansi pano ndi ichi: Koyenera kukhala chiweruzo chabwino, komwekonso kumapezeka kuipa mtima. Koyenera kukhala chilungamo, komwekonso kumapezeka zoipa. Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Mulungu adzaŵaweruza onse, abwino ndi oipa omwe, pakuti adaika nthaŵi yochitikira chinthu chilichonse ndiponso ntchito iliyonse.” Kunena za anthu, ndinkalingaliranso kuti, “Mulungu amaŵayesa ndi cholinga choti aŵaonetse kuti iwowo sasiyana konse ndi nyama. Zimene zimachitikira anthu, zomwezonso zimachitikira nyama. Monga chinacho chimafa, chinacho chimafanso. Zonsezo zimapuma mpweya umodzimodzi, munthu saposa nyama. Zonsezi nzopandapake. pali nthaŵi yobadwa ndi nthaŵi yomwalira, pali nthaŵi yobzala ndi nthaŵi yozula zobzalazo. Zonse zimapita kumodzimodzi. Zonsezo nzochokera ku dothi, ndipo zimabwerera kudothi komweko. Kodi ndani angatsimikize kuti mzimu wa munthu ndiwo umakwera kumwamba, koma mpweya wa nyama umatsikira kunsi kwa nthaka? Choncho ndidaona kuti palibe chinthu chabwino kuposa kuti munthu azikondwerera ntchito yake, pakuti chake chenicheni nchimenechi. Ndani angathe kudziŵa chimene chidzamchitikire iye atafa?” Pali nthaŵi yakupha ndi nthaŵi yochiritsa, nthaŵi yogwetsa ndi nthaŵi yomanga. Pali nthaŵi yomva chisoni ndi nthaŵi yosangalala, nthaŵi yolira maliro ndi nthaŵi yovina.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.” Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
“Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, ululu wako uli kuti?” Ululu wake wa imfa ndi uchimo, ndipo chimene chimapatsa uchimo mphamvu, ndi Malamulo. Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha, chifundo chakenso nchosatha. M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano, chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri.
Anthu anu amene adafa adzakhalanso ndi moyo, matupi ao adzauka. Inu nonse amene muli m'manda, dzukani ndi kuimba mosangalala. Monga momwe mame amafeŵetsera pansi kutsitsimutsa zomera, momwemonso Chauta adzaukitsa anthu amene adafa kale.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
Yesu adamuuza kuti, “Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso woŵapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo. Ndipo aliyense amene ali ndi moyo nakhulupirira Ine, sadzafa konse. Kodi ukukhulupirira zimenezi?”
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha? Ngakhale bambo wanga ndi mai wanga andisiye ndekha, Inu Chauta mudzandisamala. Mundiwonetse njira zanu zachifundo, Inu Chauta, munditsogolere m'njira yosalala, chifukwa ndili ndi adani ambiri. Musandipereke m'manja mwa adani angawo. Mboni zonama zandiwukira, ndipo zimandiwopseza. Ndikhulupirira kuti ndidzaona ubwino wake wa Chauta m'dziko la amoyo. Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta. Pamene adani ndi amaliwongo anga andiputa kuti andiphe, adzaphunthwa ndipo adzagwa. Ngakhale gulu lankhondo lindizinge, mtima wanga sudzachita mantha konse. Ngakhale nkhondo ibuke kulimbana nane, ine sindidzaleka kukhulupirira.
Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziŵe kwenikweni ndi kufanafana naye. M'moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse. Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu. Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika. Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu. Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye. Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye. Inu amuna, muzikonda akazi anu, musamaŵavutitse ai. Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.
Ngodala anthu amene mphamvu zao nzochokera kwa Inu, amene m'mitima mwao amafunitsitsa kudzera m'miseu yopita ku Ziyoni. Akamadutsa chigwa cha Baka chopanda madzi, amachisandutsa malo a akasupe, mvula yachizimalupsa imachidzaza ndi zithaphwi. Mphamvu zao zimanka zichulukirachulukira. Mulungu wa milungu adzaoneka m'Ziyoni.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Pakuti Mwanawankhosa uja amene ali pakatikati pa mpando wachifumu, adzakhala Mbusa wao, adzaŵatsogolera ku akasupe a madzi amoyo. Ndipo Mulungu adzaŵapukuta misozi yonse m'maso.”
Thupi limene timakhalamo pansi pano lili ngati msasa chabe. Koma tikudziŵa kuti msasawu ukadzapasuka, tidzakhala ndi nyumba ina imene Mulungu adatikonzera Kumwamba. Nyumbayo ndi yosamangidwa ndi manja a anthu, ndipo ndi yamuyaya. Pakuti tonsefe tiyenera kukaimirira poyera pamaso pa Khristu kuti atiweruze. Kumeneko aliyense adzalandira zomuyenerera, molingana ndi zimene adachita pansi pano, zabwino kapena zoipa. Tsono popeza tikudziŵa kuti Ambuye ngoyenera kuŵaopa, timayesetsa kukopa anthu. Mulungu amatidziŵa kwathunthu, ndipo tikhulupirira kuti inunso mumatidziŵa kwenikweni m'mitima mwanu. Sitikuyesa kudzichitiranso umboni pamaso panu ai, koma tingofuna kukupatsani chifukwa choti muzitinyadira. Tikufuna kuti mukhale ndi kanthu koŵayankha amene angonyadira zooneka ndi maso, osati zamumtima. Ngati tidachita ngati tapenga, tidachita zimenezi kuti tilemekeze Mulungu. Koma ngati tikuchita zanzeru, tikuchita zanzeru kuti tikuthandizeni. Chikondi cha Khristu ndicho chimatiwongolera mokakamiza, popeza kuti tikudziŵa mosakayika konse kuti Munthu mmodzi adafera anthu onse, ndiye kuti pamenepo onse adafa. Iye adafera anthu onse, kuti amene ali ndi moyo, asakhalenso ndi moyo wofuna kungodzikondweretsa okha, koma azikondweretsa Iye amene adaŵafera, nauka kwa akufa chifukwa cha iwowo. Nchifukwa chake kuyambira tsopano ife sitiganiziranso za munthu aliyense potsata nzeru za anthu chabe. Ngakhale kale tinkaganiza za Khristu potsata nzeru za anthu chabe, koma tsopano sitiganizanso za Iye motero. Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano. Wochita zonsezi ndi Mulungu, amene mwa Khristu adatiyanjanitsa ndi Iye mwini, ndipo adatipatsa ntchito yolalikira anthu chiyanjanitsocho. Ndiye kuti mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, osaŵaŵerengera machimo ao. Ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiŵalalike. Nchifukwa chake tsono tikubuula ndi kulakalaka kuvala nyumba yathu yakumwambayo, Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu. Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu. kuti titaivala, tisadzapezeke amaliseche. Ife amene tili mu msasa uno timalemedwa ndipo timabuula. Sitifuna kuuvula msasawu ai, koma kwenikweni tikadakonda kuvala nyumba ija ya Kumwamba pamwamba pake, kuti chimene chili chakufa chimizidwe ndi moyo. Mulungu ndiye amene adatikonzeratu kuti tilandire zimenezi, ndipo adatipatsa Mzimu Woyera ngati chikole chake.