M'mavesi osiyanasiyana a m'Baibulo, tikulimbikitsidwa kuti tisamachite miseche. Mwachitsanzo, mu bukhu la Aefeso 4:29, limatiuza kuti, "Mawu alionse oipa asatuluke m'kamwa mwanu, koma oti angakhoze kulimbikitsa ena, malinga ndi chifuniro chawo, kuti apereke chisomo kwa iwo akumva."
Mulungu akufuna kuti mawu athu akhale olimbikitsa ndi omanga, osati owononga. Tikamanena miseche, sitikungowononga mbiri ya munthu wina, koma tikuwononganso yathu, chifukwa mawu athu amasonyeza umunthu wathu ndi makhalidwe athu.
Baibulo limatilangizanso kufunika kwa chilungamo ndi choonadi. Mu Levitiko 19:16 limati, "Usamanene miseche pakati pa anthu a mtundu wako; usaime moyo wa mnansi wako: Ine ndine Yehova."
Ndikufuna kukuuzani kuti Baibulo limatiuza kuti tisamale ndi mawu athu ndikupewa miseche. M'malo moipitsa ndi kuwononga mbiri ya ena, tiyenera kukhala anthu olankhula zoona, chilungamo, ndi mawu olimbikitsa.
Motsatira mfundo izi za m'Baibulo, tidzathandiza kumanga dziko lomwe miseche siilipo, komanso lomwe ulemu ndi choonadi zimalamulira. Zikomo.
Abale, musamasinjirirana. Wosinjirira mbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo a Mulungu. Koma ukaweruza Malamulo a Mulungu, ndiye kuti sukuchita zimene Malamulowo akunena, ukudziyesa woweruza.
Wantchito usamsinjirire kwa mbuyake, kuti angakutemberere, ndipo iweyo ungapezeke kuti ndiwe wolakwa.
Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa: maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa, mtima wokonzekera kuchita zoipa, mapazi othamangira msangamsanga ku zoipa, mboni yonama yolankhula mabodza, ndi munthu woutsa chidani pakati pa abale.
Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula.
Khalani ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, kotero kuti anthu ena akamasinjirira mayendedwe anu abwino pamene mukutsata Khristu, achite manyazi ndi chipongwe chao.
Munthu wosinjirira mnzake kuseri ndidzamcheteketsa. Wooneka wonyada ndi wodzikuza sindidzamulekerera.
Mwa iwe muli ena ochita ugogodi kuti aphe anzao. Mulinso ena odyera zansembe pa zitunda zachipembedzo. Muli anthu enanso ochita zonyansa.
Paja mau a Mulungu akuti. “Yemwe afuna kukondwera ndi moyo, ndi kuwona masiku abwino, aletse lilime lake kulankhula zoipa, ndiponso milomo yake kunena mabodza.
Ndikuwopa kuti ndikadzabwera kwanuko, mwina nkudzakupezani muli osiyana ndi m'mene ndikadafunira. Ndikuwopa kuti mwina inunso nkudzandipeza ine wosiyana ndi m'mene mukadafunira. Ndikuwopanso kuti mwina ine nkudzapeza kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusinjirirana, ugogodi, kudzitukumula, ndiponso chisokonezo.
M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.
Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za chiwerewere, za kuba, za kuphana, zigololo, masiriro, kuipa mtima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza, ndiponso kupusa. Zoipa zonsezi zimachokera m'kati mwa munthu, ndipo ndizo zimamuipitsa.”
Pakamwa pabodza pamamnyansa Chauta. Koma anthu ochita zinthu mokhulupirika amamkondweretsa.
Koma tsopano musachitenso zonsezi, monga kukalipa, kukwiya, kuipa mtima, ndi mijedu. Pakamwa panu pasamatulukenso mau otukwana kapena onyansa.
Chimodzimodzinso azimai achikulire, uŵauze kuti azikhala ndi makhalidwe oyenera azimai oyera mtima. Asakhale osinjirira anzao kapena akapolo a zoledzeretsa. Akhale alangizi abwino,
Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse.
Nchifukwa chake tayani choipa chonse, kunyenga konse, chiphamaso, kaduka ndi masinjiriro onse.
Inu Chauta, kodi ndani angathe kukhala m'Nyumba mwanu? Ndani angathe kukhala pa phiri lanu loyera? Ndi munthu amene amayenda mosalakwa, amene amachita zolungama nthaŵi zonse, amene amalankhula zinthu ndi mtima woona. Ndi amene sasinjirira ndipo sachita anzake zoipa, kapena kumafalitsa mbiri yoipa ya anzake.
Musamangoyendayenda uku ndi uku kumachita ukazitape pakati pa anthu a mtundu wanu. Musachite kanthu kalikonse kamene kangathe kudzetsa imfa ya munthu wina. Ine ndine Chauta.
Munthu woipa mtima amafalitsa mkangano, kazitape amadanitsa anthu okhala pa chibwenzibwenzi.
Samalani mayendedwe anu pakati pa akunja, kuti ngakhale azikusinjirirani kuti ndinu anthu ochita zoipa, komabe aziwona ntchito zanu zabwino. Apo adzalemekeza Mulungu pa tsiku limene Iye adzaŵayendere.
Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula. Mwakuti chifukwa cha mau ako omwe mlandu udzakukomera kapena kukuipira.”
Mitima yao idadzaza ndi zosalungama zamitundumitundu, monga kuipa, umbombo ndi dumbo. Amangolingalira za kaduka, za kupha anthu, za ndeu, za kunyenga, ndi za njiru. Amachita ugogodi, Umasimba za Mwana wake, Yesu Ambuye athu. Poyang'anira umunthu wake, kholo lake ndi Davide, amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao.
Ndimalirira Chauta m'mavuto anga kuti andiyankhe. Ndimati, “Pulumutseni, Inu Chauta, kwa anthu onama ndi kwa anthu onyenga.”
Amene amanka nachita ukazitape, amaulula zinsinsi. Koma wa mtima wokhulupirika, amasunga pakamwa pake.
“Aliyense achenjere ndi mnzake, asakhulupirire ngakhale mbale wake. Zoona, aliyense amafuna kulanda malo a mbale wake. Aliyense amachitira mnzake ugogodi. Aliyense amanyenga mnzake, ndipo sanena zoona. Pakamwa pao adapazoloŵeza kulankhula zonama. Amakonda zoipa kwambiri, kotero kuti sangathenso kulapa. Amasanjikiza tchimo pa tchimo linzake, chinyengo pa chinyengo chinzake. Amakana kundidziŵa,” akuterotu Chauta.
Anthu akamatilalatira, timangoŵayankha moleza. Tasanduka onyozeka, ngati zinyatsi za dziko lapansi, ndipo mpaka tsopano anthu onse akutiyesa zinyalala.
Uŵauze kuti asamakamba zoipa za wina aliyense, apewe kukangana, akhale ofatsa, ndipo nthaŵi zonse akhale aulemu kwa anthu onse.
“Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunyengezerani zoipa zamitundumitundu chifukwa cha Ine.
Munthu wochitira mnzake umboni wonama, amapweteka mnzakeyo ngati chibonga kapena lupanga kapena muvi wakuthwa.
Suwopa kulankhula zoipa pakamwa pako, lilime lako limapeka mabodza. Mulungu akuŵala atakhala m'Ziyoni, mzinda wake wokongola kotheratu. “Umakhala pansi nkumachitira mbale wako miseche, inde, umasinjirira mbale wako weniweni.
Onse onyada ndi onama olankhula mwamwano ndi monyoza kwa anthu abwino, muŵakhalitse chete.
Ndimati, “Pulumutseni, Inu Chauta, kwa anthu onama ndi kwa anthu onyenga.” Mulungu adzakuchitani chiyani, anthu onyenganu? Kodi adzakupatsani chilango cha mtundu wanji?
Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake. Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.”
Tsonotu lilime limatentha ngati moto. Chifukwa chokhala pakati pa ziwalo zathu limawanditsa zoipa m'thupi monse. Limaipitsa khalidwe lonse la munthu. Limayatsa moto moyo wathu wonse kuyambira pobadwa mpaka imfa; ndipo moto wake ngwochokera ku Gehena.
Tsiku lonse umakhalira kusinkhasinkha za kuwononga ena, lilime lako lili ngati lumo lakuthwa, ntchito yako nkunyenga. Umakonda zoipa kupambana zabwino, umakonda kunama kupambana kulankhula zoona. Umakonda kulankhula mau ovutitsa ena, iwe wabodzawe.
Munthu woyenda mwaungwiro, amayenda mosatekeseka. Koma woyenda njira zoipa, adzadziŵika.
Wina akamanena kuti, “Ndimakonda Mulungu”, komabe nkumadana ndi mbale wake, ndi wonama ameneyo. Pakuti munthu wosakonda mbale wake amene wamuwona, sangathe kukonda Mulungu amene sadamuwone.
Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere.
Kuwonjezera pamenepo, amagwa m'chizoloŵezi cha kungokhala khale, motero amangoyendayenda ku nyumba za anthu. Tsonotu samangokhala khale chabe ai, amachitanso miseche nkumaloŵera za eni, ndi kukhala omalankhula zimene samayenera kulankhula.
Ndidati, “Ndidzasamala zochita zanga, kuti ndisachimwe polankhula. Ndidzatseka pakamwa panga nthaŵi zonse pamene anthu oipa ali nane.”
Ngati wina akudziyesa woika mtima pa zopembedza Mulungu, koma nkukhala wosasunga pakamwa, chipembedzo chakecho nchopanda pake, ndipo amangodzinyenga.
pakuti anthu oipa ndi onama amakamba zondiwukira, amalankhula zondinamizira. Zimenezi zikhale chilango chochokera kwa Chauta kugwera ondineneza. Ziŵagwere amene amalankhula zoipira moyo wanga. Koma Inu Mulungu, Ambuye anga, munditchinjirize malinga ndi ulemerero wa dzina lanu, mundipulumutse chifukwa chikondi chanu chosasinthika ndi chabwino. Pakuti ine ndine wosauka ndi wosoŵa, ndipo mtima wanga ukuŵaŵa kwambiri. Ndazimirira ngati mthunzi wamadzulo, ndapirikitsidwa ngati dzombe. Maondo anga afooka chifukwa chosala zakudya, thupi langa laonda ndi mutu womwe. Ondineneza amandinyodola, akandiwona amapukusa mitu yao. Thandizeni Chauta, Mulungu wanga. Pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. Adani adziŵe kuti limeneli ndi dzanja lanu londipulumutsa, Inu Chauta, ndinu amene mwachita zimenezi. Iwo atemberere, koma Inu mundidalitse. Ondiputa muŵachititse manyazi, koma ine mtumiki wanu ndisangalale. Ondineneza akhale onyozeka, manyazi ao aŵakute ngati chovala. Ponseponse amandilankhula mau achidani, amandinena popanda chifukwa.
Koma zotuluka m'kamwa mwa munthu zimachokera mu mtima, ndipo zimenezi ndizo zimamuipitsa. Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za kuphana, za chigololo, za chiwerewere, za kuba, maumboni onama, ndiponso zachipongwe.
Mau ake anali osalala kupambana batala, komabe mumtima mwake munali zankhondo. Mau ake anali ofeŵa kupambana mafuta, komabe anali ndi malupanga osololasolola.
Nthaŵi zonse mau anu akhale okoma, opindulitsa ena, kuti potero mudziŵe m'mene muyenera kuyankhira munthu aliyense.
Anthu osasamala za Mulungu amandisinjirira, komabe ndimatsata malamulo anu ndi mtima wanga wonse.
Zimene umanena zingathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo, munthu wolankhulalankhula adzapeza bwino kapena tsoka.
Munthu wosalabadirako za Mulungu amaononga mnzake ndi pakamwa pake; munthu wochita chilungamo amapulumuka chifukwa cha kudziŵa zinthu.
Ndiponso musamalankhule zolaula, zopusa, kapena zopandapake, koma muzilankhula zoyamika Mulungu.
Mbiri yabwino ndi yofunika kupambana chuma chambiri, kupeza kuyanja nkopambana siliva ndi golide.
Pakamwa pomwe pamatuluka mayamiko pomweponso pamatuluka matemberero. Abale anga, zoterezi siziyenera kumachitika.
Amene amanka nachita ugogodi, amaulula zinsinsi. Nchifukwa chake usamagwirizane naye wolankhula zopusayo.
Ulewe zabodza, zosinjirira. Usaphe munthu wosalakwa ndi wosapalamula, chifukwa Ine sindidzakhululukira wochimwa.
Akadakhala mdani wanga wondinyozayo, ndikadatha kupirira. Akadakhala mdani wanga wondichita chipongweyo, ndikadangobisala basi. Koma iweyo mnzanga, mnzanga woyenda naye, bwenzi langa wozoloŵerana naye, ndi amene ukuchita zimenezi. Tinkakambirana nkhani zokoma tili aŵiri, tinkapembedza limodzi m'Nyumba ya Mulungu.
Tsono lekani kunama. Aliyense azilankhula zoona zokhazokha ndi mkhristu mnzake, pakuti tonse pamodzi mogwirizana ndife ziwalo za thupi la Khristu.
Nchifukwa chake zonse zimene mwalankhula pa mdima, zidzamveka poyera, ndipo zonse zimene mwanong'oneza anthu m'kati mwa nyumba, adzazilengeza pa bwalo.”
Pakamwa pa wochita chilungamo pamatuluka zanzeru, koma lilime lokhota adzalidula. Anthu omvera Mulungu amadziŵa zoyenera kulankhula, koma pakamwa pa anthu oipa pamatuluka zosayenera.
Kudzudzula munthu poyera nkwabwino kupambana kubisa chikondi chimene uli nacho. Amene amakukonda, ngakhale akupweteke, chikondi chake chimakhalapobe, mdani wako ngakhale akumpsompsone, nkunyenga chabe kumeneko.
Munthu wachidani pakamwa pake pamalankhula zabwino, pamene mumtima mwake muli zonyenga. Woteroyo akamalankhula mokometsa mau, usamkhulupirire, pakuti mumtima mwake mwadzaza zoipa. Ngakhale amabisa chidani mochenjera, kuipa kwakeko kudzaoneka poyera pakati pa anthu.
Ankakonda kutemberera, choncho matemberero amgwere. Sadakonde kudalitsa anthu ena, choncho madalitso akhale kutali ndi iye. Kutemberera anzake kunali ngati chovala chake, motero matemberero amgwere ngati mvula. Akhale ngati mafuta oloŵa m'mafupa mwake.
Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa, pakuti anthu otere satumikira Khristu Ambuye athu, koma amangotumikira zilakolako zao basi. Ndi mau okoma ndi oshashalika amanyenga anthu a mitima yoona.
Inu Chauta, tsekani pakamwa ponse pothyasika letsani lilime lililonse lolankhula modzikuza. Paja anthu amenewo amanena kuti, “Tidzapambana ndi mau athu, pakamwa tili napo, nanga angatigonjetse ndani?”
Munthu wachabechabe, munthu woipa, amangoyendayenda nkumalankhula zabodza. Amatsinzinira masoŵa nkumakwekwesa pansi mapazi ake, amalozaloza ndi chala chake. Amalingalira zoipa ndi mtima wake wopotoka, amangokhalira kuvundula madzi pakati pa anthu. Nchifukwa chake tsoka lidzamgwera modzidzimutsa. Pa kamphindi kochepa adzaonongedwa, osapulumuka konse.
Pakati panu pasakhale ndi mmodzi yemwe wogwa m'mavuto chifukwa choti wapha munthu, kapena waba, kapena wachita choipa, kapena waloŵerera za eniake.
Pakamwa pake pamangolankhula zotemberera, zonyenga ndi zoopseza. M'kamwa mwake mumatuluka zovutitsa ena ndiponso zoipa zokhazokha.
Munthu wabwino amaganizira za m'mene ayankhire, koma pakamwa pa munthu woipa pamatuluka mau oipa okhaokha.
Chuma chomachipeza monyenga chimangoti wuzi ngati nthunzi, ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa.
Musandichotsere kumodzi ndi anthu oipa, anthu amene amachita zonyenga, amene amalankhula zamtendere ndi anzao, koma mitima yao ndi yodzaza ndi chidani.
Abale musamanenerana zoipa pakati panu, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Onani, woweruza waima pa khomo.
Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.
Ana a njoka inu, mungathe bwanji kulankhula zabwino pamene muli oipa? Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.
Tsono woweruza enawe, kaya ndiwe yani, ulibe pozembera. Pakutitu pamene ukuweruza mnzako, ukudzitsutsa wekha, popeza kuti iweyo woweruzawe umachita zokhazokhazo.
Koma nzeru zochokera Kumwamba, poyamba nzangwiro, kuwonjeza apo nzamtendere, zofatsa ndi zomvera bwino. Ndi za chifundo chambiri, ndipo zipatso zake zabwino nzochuluka. Nzeruzo sizikondera kapena kuchita chiphamaso. Ndipo chilungamo ndiye chipatso cha mbeu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.
Zoonadi, munthu woipa amalingalira zoipa zokhazokha nthaŵi zonse, ntchito yake ndi kunyenga ndi kuvutitsa anthu ena basi. Amakumba mbuna kuti ikhale yozama, koma amagwamo ndiye yemwe. Choipa chitsata mwini, chiwawa chimabwerera pa mwini wake.
Munthu wachifundo amadzipindulira zabwino, koma munthu wankhwidzi amadzipweteka yekha.
Pakamwa pako pasakuchimwitse, kuti choncho usayenerenso kukauza wansembe wa Mulungu kuti, “Ai, ndinkangonena!” Chifukwa chiyani ufuna kuputa Mulungu? Kodi ukufuna kuti aononge zimene wazigwirira ntchito?
Koma Yesu adati, “Iyai, odala ndi anthu amene amamva mau a Mulungu naŵagwiritsa ntchito.”
Koma Mulungu adzakutswanya kosalekeza, adzakugwira ndi kukutulutsira kunja kwa nyumba yako. Adzakuzula m'dziko la anthu amoyo.
Monga munthu wopenga amene amangoponya nsakali zamoto, kapena mivi yoopsa, ndimonso amakhalira munthu wonyenga mnzake, amene amati, “Ai, ndi zoseka chabe!”
“Aliyense wonenera zoipa Mwana wa Munthu, Mulungu adzamkhululukira, koma wonyoza Mzimu Woyera ndi mau achipongwe, Mulungu sadzamkhululukira.
Ndi amene amanyoza munthu womkana Mulungu, koma amalemekeza anthu omvera Chauta. Ndi amene amachitadi zimene walonjeza, ngakhale zikhale zoŵaŵa chotani.