Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


MAVESI ODALITSA

MAVESI ODALITSA

Pali anthu apadera amene Mulungu waika pa moyo wako, ndi anthu odalitsidwa ndi okondedwa, amene tikuwadalitsa m'dzina la Yesu. M'Baibulo muli mavesi ambiri oti tithokoze ndi kudalitsa miyoyo imeneyi.

Sitimadalitsa anthu okhawo, koma mabanja athu, dziko lathu, ndi abale athu mwa Khristu. “Yehova akudalitse, nakusunge; Yehova akuunikire nkhope yake pa iwe, nakuchitire chifundo; Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatsenso mtendere.” (Numeri 6:24-26)

Timadalitsanso abusa athu amene Mulungu amawagwiritsa ntchito. “Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungama; Mudzam'zungulira ndi chiyanjo chanu ngati ndi chishango.” (Salimo 5:12)

Sitiyenera kudalitsa okhawo atichitira zabwino, chifukwa Mulungu watilamula kuti tizidalitsa ngakhale atichitira zoipa. “Dalitsani iwo akutikuzunzani; dalitsani, musatemberere.” (Aroma 12:14)




Eksodo 23:11

Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri mudzaipumuze mindayo. Anthu osauka a mtundu wanu ndiwo adzadye zomera m'mindamo, ndipo nyama zakuthengo zidzadya zotsala. Muzidzachita chimodzimodzi ndi minda yamphesa ndi yaolivi yomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:4

Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:8

Musakhale ndi ngongole ina iliyonse kwa munthu wina aliyense, koma kukondana kokha. Wokonda mnzake, watsata zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:31

Wopondereza mmphaŵi, amachita chipongwe Mlengi wake, koma wochitira chifundo osauka, amalemekeza Mlengi wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:27

Iye adayankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:12

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:13

Pakuti ntchito imeneyi ikuŵatsimikizira kuti chifundo chanu nchoona, iwo adzatamanda Mulungu chifukwa cha kumvera kwanu povomereza Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Adzatero chifukwanso cha ufulu wanu poŵagaŵirako iwowo ndi anthu ena onse zinthu zimene muli nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 24:1

Dziko lapansi ndi zonse zam'menemo ndi za Chauta, dziko lonse lapansi pamodzi ndi anthu onse okhalamo ndi ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:21

Yesu adamuuza kuti, “Ngati ufuna kukhala wabwino kotheratu, pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:22

Mmphaŵi usamubere, chifukwa choti iyeyo ndi wosauka. Anthu ozunzika usaŵapondereze pa bwalo la milandu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 58:7

Anthu anjala muziŵagaŵirako chakudya chanu, osoŵa pokhala muziŵapatsako malo. Mukaona wausiŵa, mpatseni chovala, musalephere kuthandiza amene ali abale anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:9

Yesu popitiriza mau adati, “Ndipo Ine ndikukuuzani kuti mudzipezere abwenzi ndi chuma chonyengachi. Apo chumacho chikadzakutherani, Mulungu adzakulandirani ku nyumba zamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:9

Amapereka chithandizo mwaufulu, amaoloŵa manja kwa anthu osauka. Chilungamo chake chidzakhala chamuyaya, adzakhala wamphamvu ndipo anthu adzampatsa ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:34-35

Panalibe munthu wosoŵa kanthu pakati pao, chifukwa onse amene anali ndi minda kapena nyumba, ankazigulitsa, namabwera ndi ndalama zake kudzazipereka kwa atumwi. Ndipo ndalamazo ankagaŵira munthu aliyense malinga ndi kusoŵa kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:15-16

Mwachitsanzo: mbale wina kapena mlongo ali ndi usiŵa, ndipo masiku onse alibe chakudya chokwanira. Tsono wina mwa inu angoŵauza kuti. “Pitani ndi mtendere, mukafundidwe ndipo mukakhute”, koma osaŵapatsa zimene akusoŵazo, pamenepo phindu lake nchiyani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:30

Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akatenga zinthu zako, usamlamule kuti abweze.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:3

Ndipo ngakhale nditagaŵira amphaŵi chuma changa chonse, kapena kupereka thupi langa kuti anthu alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ndiye kuti changa palibe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 15:7-8

Pakati pa abale anu pakakhala wina wosauka m'midzi yanu, m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo, musadzaume mtima, ndipo musadzaume manja. Makamaka muzidzamchitira chifundo ndi kumkongoza monga momwe angafunire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:33-34

Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupatse amphaŵi. Mudzipezere matumba a ndalama amene safwifwa, ndi kudziwunjikira chuma chokhalitsa Kumwamba; kumeneko mbala sizingafikeko, ndipo njenjete sizingachiwononge. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:26

Tsiku lathunthu anthu oipa amasirira zinthu, koma omvera Mulungu amapatsa ndipo alibe kaliwumira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:17-19

Anthu amene ali olemera pa zinthu zapansipano, uŵalamule kuti asanyade kapena kudalira chuma chimene sichidziŵika ngati chidzakhalitsa. Koma azidalira Mulungu amene amatipatsa zonse moolowa manja kuti tisangalale nazo. Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao. Pakutero adzadziwunjikira chuma chokoma ndi chokhalitsa chimene chidzaŵathandize kutsogoloko, kuti akalandire moyo umene uli moyo weniweni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:20

Koma makamaka, monga mau a Mulungu akunenera, “Ngati mdani wako wamva njala, iwe umpatse chakudya. Ngati wamva ludzu, iwe umpatse madzi akumwa. Ukatero udzamchititsa manyazi kwambiri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 15:11

Nthaŵi zonse padzakhala Aisraele ena osauka, osoŵa zinthu. Motero ndikukulamulani kuti otereŵa muzidzaŵachitira chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 17:13-14

Koma Eliya adauza maiyo kuti, “Musade nkhaŵa. Pitani, mukachite monga mwaneneramo. Koma poyamba mutapeko kaufa pang'ono, mundiphikire kakeke, mubwere nako kuno. Pambuyo pake mukaphikenso kuti mudye inuyo ndi mwana wanu. Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Ufa umene uli m'mbiyawo sudzatha, mafutanso amene ali m'nsupawo sadzatha, mpaka tsiku limene Chauta adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:28

Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:10

Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:48

Koma wantchito amene sadziŵa zimene mbuye wake amafuna, tsono nkumachita zoyenera kumlanga nazo, adzamkwapula pang'ono. Aliyense amene adalandira zambiri, adzayenera kubweza zambiri. Ndipo amene adamsungiza zambiri, adzamlamula kuti abweze zochuluka koposa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:4

Ngakhale nthaŵi ya mdima, munthu wochita chilungamo ayenda m'kuŵala, chifukwa ngwokoma mtima, wachifundo ndi woongoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:1

Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:10

Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziŵeto zake, koma munthu woipa mtima chifundo chake nchankhwidzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:13

Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 13:34

Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:27

Inde unali ufulu kuchita zimenezi, komanso unali udindo wao kuthandiza osaukawo. Ayuda adagaŵana madalitso ao achikhristu ndi anthu a mitundu ina, choncho iwowo ayeneranso kuthandiza Ayudawo pa zosoŵa zao za moyo wathupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:29

Wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri, koma wofulumira kupsa mtima amaonetsa uchitsiru wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:41

Popereka zachifundo kwa amphaŵi, muzipereka zimene zili m'kati, ndiye pamenepo zanu zonse zidzakhala zoyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 58:11

Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:9

Uzilemekeza nacho Chauta chuma chako chonse, uzimuyamika nazo zokolola zako zonse zam'minda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:10

Musakolole mphesa zonse m'munda wanu wamphesa, ndipo musatolenso mphesa zakugwa m'munda mwanumo. Zimenezo musiyire anthu osauka ndiponso alendo, Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 24:19

Mukamakolola dzinthu m'minda mwanu, zina pang'ono nkuiŵalika, musabwerere kukatenga zoiŵalikazo. Zimenezo muzisiyire alendo okhala nanu, ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:22

Pamene Yesu adamva zimenezi, adamuuza kuti, “Ukusoŵabe chinthu chimodzi: kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:16

Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 82:3

Inu tetezani anthu ofooka ndi amasiye mwachilungamo. Weruzani molungama ozunzika ndi amphaŵi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:22

Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake choloŵa, koma chuma cha munthu woipa amachilandira ndi anthu abwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:39

Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:2

Pa tsiku loyamba la sabata, aliyense mwa inu azipatulapo kanthu, potsata momwe wapezera. Zimene wapatulazo azisunge kunyumba, kuti pasakakhalenso kusonkhasonkha ine ndikabwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 29:12

Zidatero chifukwa choti ndinkapulumutsa amphaŵi olira, ndinkalanditsa ana amasiye opanda woŵathandiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:11

Inu okondedwa, ngati Mulungu adatikonda kwambiri chotere, ifenso tiyenera kumakondana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:5

Atate a ana amasiye ndiponso mtetezi wa azimai amasiye, ndi Mulungu amene amakhala m'malo ake oyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:8

Tsono mumachita bwino ngati mumatsatadi lamulo lachifumu lija limene limapezeka m'Malembo, lonena kuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:6-7

Nkhanitu ndi iyi: wobzala pang'ono, adzakololanso pang'ono, wobzala zochuluka, adzakololanso zochuluka. Aliyense apereke monga momwe adatsimikiziratu mumtima mwake, osati ndi chisoni kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:13

Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:5

Munthu amene amakongoza mosafuna phindu, amene amayendetsa ntchito zake mwachilungamo, zinthu zimamuyendera bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:27

Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 15:10

Dzampatseni mwaufulu mosaŵinya, ndipo Chauta adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:18

Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 41:1

Ngwodala munthu amene amaganizirako za amphaŵi, popeza kuti Chauta adzapulumutsa munthu wotere pa tsiku lamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:25

“Mukakongoza ndalama munthu wina aliyense waumphaŵi pakati panupo, musamachita monga momwe amachitira anthu okongoza, musamuumirize kupereka chiwongoladzanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 25:35

“Mbale wako akakhala wosauka, ndipo sangathe kudzisamala, iweyo umthandize. Uzikhala naye monga ngati mlendo, ndiponso monga ngati munthu wokhala nao kanthaŵi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:35

M'maŵa mwake adatulutsa ndalama ziŵiri zasiliva, nazipereka kwa mwini nyumba ya alendoyo. Adamuuza kuti, ‘Msamalireni bwino, ndipo mukamwazanso ndalama zina, ndidzakubwezerani pobwera.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:21

Amene amanyoza mnzake ngwochimwa, koma ngwodala amene amachitira chifundo amphaŵi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:1-4

“Chenjerani, musachite ntchito zanu zabwino pamaso pa anthu ndi cholinga choti akuwoneni. Mukatero, simudzalandira mphotho kwa Atate anu amene ali Kumwamba. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwechonso pansi pano. Mutipatse ife lero chakudya chathu chamasikuwonse. Mutikhululukire ife machimo athu, monga ifenso takhululukira otilakwira. Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa, koma mutipulumutse kwa Woipa uja.” [Pakuti ufumu, mphamvu ndi ulemerero ndi zanu kwamuyaya. Amen.] “Ndithu ngati mukhululukira anthu machimo ao, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani inunso. Koma ngati simukhululukira anthu machimo ao, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu. “Pamene mukusala zakudya, musamaonetsa nkhope zachisoni monga amachitira anthu achiphamaso aja. Iwo amaipitsa nkhope kuti anthu aone kuti akusala zakudya. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma iwe, pamene ukusala zakudya, samba m'maso nkudzola mafuta kumutu, kuti anthu asadziŵe kuti ukusala zakudya. Koma Atate ako amene ali osaoneka ndiwo adziŵe. Ndipo Atate akowo amene amaona zobisika, adzakupatsa mphotho. “Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba. “Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko. “Maso ndiwo nyale zounikira thupi la munthu. Ngati maso ako ali bwino, m'thupi mwako monse mumakhala kuŵala. Koma ngati maso ako sali bwino, m'thupi mwako monse mumakhala mdima. Tsono ngati kuŵala kumene kuli mwa iwe kusanduka mdima, mdima wakewo ndi wochita kuti goo! “Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma. “Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena mudzamwanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji. Kodi suja moyo umaposa chakudya? Kodi suja thupi limaposa zovala? Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame? Ndani mwa inu ndi maganizo ankhaŵa angathe kuwonjezera ngakhale tsiku limodzi pa moyo wake? “Ndipo mumaderanji nkhaŵa ndi zovala? Onani maluŵa akuthengo m'mene amakulira. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu ai. Komatu kunena zoona, ngakhale mfumu Solomoni yemwe, mu ulemerero wake wonse, sankavala zokongola kulingana ndi limodzi lomwe mwa maluŵa ameneŵa. Koma iwe ukamapereka zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziŵe zimene dzanja lako lamanja likuchita. Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu? “Nchifukwa chake musamada nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Tidzadyanji? Tidzamwanji? Tidzavalanji?’ Paja zimenezi amazifunafuna ndi anthu akunja. Atate anu akumwamba amadziŵa kuti mukuzisoŵa zonsezi. Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso. Motero musadere nkhaŵa zamaŵa. Zamaŵa nzamaŵa. Tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira. Ukatero, zachifundo zakozo zidzakhala zodziŵa iwe wekha. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 3:11

Iye adati, “Amene ali ndi miinjiro iŵiri, apatseko mnzake amene alibe. Ndipo amene ali nacho chakudya, achitenso chimodzimodzi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 58:10

mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:25

Munthu wa mtima waufulu adzalemera, wothandiza anzake nayenso adzalandira thandizo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:38

Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:40

Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:16

Musanyozere kumachita zachifundo ndi kumathandizana, chifukwa nsembe zotere zimakondweretsa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:17

Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:42

Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akafuna kubwereka kanthu kwa iwe, usamkanize.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 20:35

Pa zonse ndakuwonetsani kuti pakugwira ntchito kolimba motere, tiyenera kuthandiza ofooka. Kumbukirani mau aja a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupatsa kumadalitsa munthu koposa kulandira.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:10

Nchifukwa chake tsono, nthaŵi zonse tikapeza mpata, tizichitira anthu onse zabwino, makamaka abale athu achikhristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:9

Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsidwa, poti amagaŵana chakudya chake ndi anthu osauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:17

Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 32:8

Koma munthu wa mtima wabwino amalingalira zabwino, ndipo amalimbikira kuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 8:12

Malinga munthu akakhala ndi changu cha kupereka, Mulungu amalandira mokondwa zimene munthuyo ali nazo, ndipo samkakamiza kuti apereke zimene alibe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:2

Musanyozere kumalandira bwino alendo m'nyumba mwanu. Pali ena amene kale adaalandira bwino alendo, ndipo mosazindikira adaalandira angelo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:10

Mulungu amene amapatsa mbeu kwa wobzala, ndiponso chakudya choti adye, adzakupatsani mbeu zoti mubzale, ndipo adzazichulukitsa. Adzachulukitsanso zipatso zake za chifundo chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:19

Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye adayamba kutikonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:17

Phunzirani kuchita zabwino. Funafunani chilungamo, opsinjidwa muŵathandize. Tetezani ana amasiye, muŵaimirire pa milandu yao akazi amasiye.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:24

Wina amatha kupatsako anzake zinthu mwaufulu, komabe amanka nalemereralemerera. Wina nkukhala wakaligwiritsa, nakhalabe wosauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:21

Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:26

Nthaŵi zonse munthu wolungama amapatsa mosaumira, ndipo amakongoza mwaufulu, ana ake amakhala madalitso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 19:8

Koma Zakeyo adaimirira nauza Ambuye kuti, “Ambuye, ndithudi ndidzapereka hafu la chuma changa kwa amphaŵi. Ndipo ngati ndidalandira kanthu kwa munthu aliyense monyenga, ndidzamubwezera kanai.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:18

Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 8:2

Anthu a m'mipingoyo adayesedwa kwambiri ndi masautso, komabe adakondwa kwakukulu, kotero kuti adapereka moolowa manja kwenikweni, ngakhale anali amphaŵi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:13

Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:27

Amene amapatsa osauka sadzasoŵa kanthu koma amene amatsinzina dala kuti asaŵapenye, adzatembereredwa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:2

Aliyense mwa ife azikondweretsa mnzake, ndi kumchitira zabwino, kuti alimbikitse chikhulupiriro chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:27

Usaleke kumchitira zabwino woyenera kuzilandira, pamene uli nazo mphamvu zochitira choncho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:8

Muzikachiritsa odwala, muzikaukitsa akufa, muzikachotsa khate, muzikatulutsa mizimu yoipa. Mwalandira mwaulere, kaperekeni mwaulere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:19

Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 29:14

“Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndi ayani kuti tingathe kupereka mwaufulu motere? Paja zinthu zonse zimachokera kwa Inu ndipo zimene tikupereka kwa Inu nzanu zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 16:17

Ndipo pobwera pamaso pa Chauta, asamadzakhale chimanjamanja, koma munthu aliyense azidzabwera ndi mphatso monga momwe angathere, molingana ndi madalitso amene Chauta, Mulungu wanu, adampatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 31:16-18

“Ngati amphaŵi ndidaŵamana zimene ankakhumba, kapena kuŵagwiritsa mwala mwankhanza akazi amasiye, ngati chakudya ndidadya ndekha, ana amasiye osachilaŵa, pakuti anawo ndidaŵalera ngati bambo wao ndi kuŵasamalira bwino chibadwire chao,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:21

Munthu woipa amakonda ngongole koma satha kubweza, koma munthu wabwino ali ndi mtima wokoma ndi wopatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:45

Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagaŵira onse, malinga ndi kusoŵa kwa aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:10

Adangopempha chokhachi kuti tisaleke kukumbukira anthu ao aumphaŵi. Ndipotu chimenechi ndicho ndakhala ndikuchita moikapo mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:13-14

Koma iwe ukamakonza phwando, uziitana amphaŵi, otsimphina, opunduka ndi akhungu. Apo udzakhala wodala, chifukwa iwo alibe kanthu koti nkukubwezera. Mulungu ndiye adzakubwezera, pamene anthu olungama adzauka kwa akufa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:7

Ngodala anthu ochitira anzao chifundo, pakuti iwonso Mulungu adzaŵachitira chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye, inu ndinu Alfa ndi Omega! Atate, Mlengi wa thambo ndi dziko lapansi, ndinu woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi chitsiriziro. Ndikubwera kwa inu kudzera mwa Ambuye wanga Yesu Khristu, ndikupempha kuti muteteze ndi kulimbitsa moyo wa mnzanga, mupatseni nzeru ndi luntha kuti asankhe zinthu zabwino, kuti ayende m'cholinga chimene munamupangira. Mulimbitseni, mutsitsimutseni mphamvu zake ndipo molimbikira mulimbitse chikhulupiriro chake, kotero kuti kukhalapo kwa Mzimu Woyera wanu kukhale patsogolo pa moyo wake ndi banja lake. Mawu anu amati: "Pakuti adzatumiza angelo ake kukutetezani m'njira zako zonse." Ambuye, pitirizani kumupatsa zonse zomfunika, mupatseni nzeru ndi kulimba mtima kuti agonjetse mantha ake ndipo athe kupambana mavuto aliwonse omwe akukumana nawo. Ndikulengeza kuti mukupita patsogolo pake ngati chimphona champhamvu, mukulimbana nkhondo zake zonse. Mumuteteze ku ziwembu zonse ndi misampha ya mdani. Zikomo, Ambuye, ulemerero ndi ulemu zonse zikhale kwa inu. M'dzina la Yesu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa