Ndikufuna tikambirane za nkhani yofunika kwambiri, nkhani ya mgwirizano. Tonse tikudziwa kuti nthawi zina pamakhala kusamvana, mwina chifukwa cha maganizo osiyana, kapena zinthu zina zosafunika kwenikweni. Koma Baibulo limatiphunzitsa njira ina yoonera nkhaniyi.
M’buku la 1 Akorinto 1:10, mtumwi Paulo akutilimbikitsa kuti tigwirizane, tipewe mikangano yosafunikira. Akutikumbutsa kuti mwa Khristu sitiyenera kukhala ogawanika, koma tiyenera kukhala ogwirizana pacholinga chimodzi, m’chikondi chimodzi. Chifukwa mgwirizanowu ndi momwe mphamvu ya uthenga wabwino imaonekera, ndi momwe mpingo umalimbikira. Mulungu akutiitana kuti tisiye kusiyana maganizo, ndipo tifunafune mtendere pakati pathu.
Aefeso 4:3, imatilimbikitsa “kusunga umodzi wa Mzimu m’chomangira cha mtendere.” Mgwirizano ndi wofunika kwambiri kuti mpingo ugwire ntchito yake padziko lapansi, kuti tikakhale mboni zoona za chikondi ndi chisomo cha Mulungu. Sitingathe kukana kuti kusamvana kulipo m’dziko lathu lino, koma monga otsatira a Khristu, tili ndi udindo wofunafuna mgwirizano m’zonse zomwe timachita ndi zomwe timalankhula.
Tikamaganizira za kusamvana, tizikumbukira mawu a wamasalmo m’Masalmo 133:1, “Taonani, kuli kwabwino ndi kokoma chotani nanga, abale kukhala pamodzi m’chigwirizano!”
Adachita zimenezi kuti pasakhale kugaŵikana m'thupi, koma kuti ziwalo zonse zizisamalirana.
Abale, ndikukupemphani m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu, kuti muzivomerezana pa zimene munena. Pasakhale kupatulana pakati panu, koma muzimvana kwenikweni pokhala a mtima umodzi ndi a maganizo amodzi.
ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu Woyera pa kulunzana mu mtendere. Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera amene Mulungu adakusindikizani chizindikiro chake chotsimikizira kuti ndinu ake pa tsiku limene Mulunguyo adzatipulumutse kwathunthu. Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse. Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso. Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu Woyera mmodzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene Mulungu adakuitanirani. Pali Mbuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi. Pali Mulungu mmodzi amene ali Atate a anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse, amagwira ntchito kudzera mwa onse, ndipo ali mwa onse.
popeza kuti mukudalirabe zapansipano. Pakati panu pali kaduka ndi kukangana. Nanga zimenezi sizikutsimikiza kuti mukudalirabe zapansipano, ndipo kuti mumachita monga momwe amachitira anthu odalira zapansipanozo? Mumangoti ali apa, “Ine ndine wa Paulo,” ali apa, “Ine ndine wa Apolo.” Kodi mukamatero simukuchita ngati anthu odalira zapansipano?
Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa,
Koma ngati muyamba kulumana ndi kukadzulana, muchenjere kuti mungaonongane kotheratu.
Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi. Ndilibenso wina wonga amene ali ndi mtima wosamala za inu kwenikweni. Paja ena onse amangofuna zokomera iwo okha, osati zokomera Yesu Khristu. Koma mukudziŵa kuti mkhalidwe wa Timoteo ndi wotsimikizika kale kuti ngwabwino. Mukudziŵanso kuti adagwira mogwirizana nane ntchito yofalitsa Uthenga Wabwino, monga mwana ndi bambo wake. Ndikuyembekeza tsono kumtumiza kwa inu msanga, nditadziŵa za m'mene ziyendere zanga. Koma ndikhulupirira kuti, Ambuye akalola, inenso ndidzafika kwanuko msanga. Ndaganiza kuti nkofunikadi kuti ndikutumizireni mbale wathu uja, Epafrodito. Mudaamtuma kuti adzandithandize pa zosoŵa zanga, ndipo wagwiradi ntchito ndi kumenya nkhondo yachikhristu pamodzi ndi ine. Tsonotu akukulakalakani nonsenu, ndipo ndi wokhumudwa podziŵa kuti inu mudamva zoti iye ankadwala. Nzoonadi adaadwala zedi mpaka pafupi kufa. Mwai kuti Mulungu adamchitira chifundo. Ndipotu sadangochitira chifundo iye yekhayu, komanso ineyo, kuti chisoni changa chisakhale chosanjikizana. Nchifukwa chake ndikufunitsitsa ndithu kumtumiza kwa inu, kuti podzamuwonanso mudzasangalale, kutinso nkhaŵa yanga ichepeko. Mlandireni mwachikhristu ndi chimwemwe chachikulu. Anthu otere muziŵachitira ulemu. Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo.
popeza kuti mukudalirabe zapansipano. Pakati panu pali kaduka ndi kukangana. Nanga zimenezi sizikutsimikiza kuti mukudalirabe zapansipano, ndipo kuti mumachita monga momwe amachitira anthu odalira zapansipanozo?
Anthuwo adachita kuchoka pakati pathu, komabe sanali a gulu lathu kwenikweni. Pakuti akadakhala a gulu lathu, bwenzi akali nafebe. Koma adatichokera, kuti aonekere poyera kuti panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene anali wa gulu lathu.
Adachita zimenezi kuti pasakhale kugaŵikana m'thupi, koma kuti ziwalo zonse zizisamalirana. Chiwalo chimodzi chikamamva kuŵaŵa, ziwalo zonse zimamvanso kuŵaŵa. Chiwalo chimodzi chikamalandira ulemu, ziwalo zonse zimakondwa nao.
Pajatu pamene pali kaduka ndi kudzikonda, pomweponso pali chisokonezo ndi ntchito yoipa ya mtundu uliwonse. Koma nzeru zochokera Kumwamba, poyamba nzangwiro, kuwonjeza apo nzamtendere, zofatsa ndi zomvera bwino. Ndi za chifundo chambiri, ndipo zipatso zake zabwino nzochuluka. Nzeruzo sizikondera kapena kuchita chiphamaso.
Afarisi ena adati, “Munthu amene uja ngwosachokera kwa Mulungu, chifukwa satsata lamulo lokhudza tsiku la Sabata.” Koma ena adati, “Kodi inu, munthu wochimwa nkuchita zizindikiro zozizwitsa zotere?” Choncho panali kutsutsana.
Koma anthu amumzindamo adagaŵikana, ena anali mbali ya Ayuda, ena anali mbali ya atumwi.
Yesu adaadziŵa zimenezi, motero adaŵauza kuti, “Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo kutha kwake nkomweko. Ndipo anthu a m'mudzi uliwonse kapena a m'banja lililonse akayamba kuukirana, mudzi wotere kapena banja lotere silingalimbe ai.
Munthu woipa mtima amafalitsa mkangano, kazitape amadanitsa anthu okhala pa chibwenzibwenzi.
Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu. Motero potsiriza, tonse tidzafika ku umodzi umene umapezeka pakukhulupirira, ndiponso pakudziŵa Mwana wa Mulungu. Pamenepo tidzakhwima ndithu, ndi kufika pa msinkhu wathunthu wa Khristu.
Choyamba, ndikumva kuti mukamasonkhana mu mpingo, mumapatulana. Ndipo ndikhulupirira kuti zimenezi kwinaku nzoona.
Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.
Paja adakuuzani kuti, “Pa masiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, otsata zilakolako zao zoipa.” Anthu ameneŵa ndi oyambitsa mipatuko. Amangotsata zapansipano, ndipo mumtima mwao alibe Mzimu Woyera.
Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere.
Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo sungalimbe. Ndipo anthu a m'banja limodzi akayamba kugaŵikana, banja lotere silingalimbe. Tsono ngati a mu ufumu wa Satana aukirana okhaokha nagaŵikana, Satanayo sangalimbe, ndiye kuti watha basi.
Mau otsiriza ndi aŵa: nonse mukhale a mtima umodzi, ndi omverana chisoni. Muzikondana nawo abale. Mukhale a mtima wachifundo ndi odzichepetsa.
Ndiye kuti munthu uyu ife tampeza kuti ngwovutitsa kwabasi. Wakhala akuutsa chipolowe pakati pa Ayuda pa dziko lonse lapansi, ndiponso ndi mtsogoleri wa gulu lopatulika la Anazarete.
kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko,
Uzikana matsutsano opusa ndi opanda nzeru, paja ukudziŵa kuti zotere zimautsa mikangano. Ndipo mtumiki wa Ambuye asamakhala wokanganakangana ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa onse, mphunzitsi wokhoza, munthu wodziŵa kupirira mavuto.
Ndikuŵapempherera kuti iwo onse akhale amodzi. Monga Inu Atate mumakhala mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife. Motero anthu onse adzakhulupirira kuti mudandituma.
Mulungu safuna chisokonezo ai, koma mtendere. Monga zimachitikira m'mipingo yonse ya anthu a Mulungu,
Chokha chakuti mumaimbana milandu inu nokhanokha, chatsimikiza kale kuti mwalephereratu. Bwanji osangopirira pamene ena akulakwirani? Bwanji osangolola kuti inuyo akubereni?
Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake.
Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.
Khristu mwini wake ndiye mtendere wathu. Iye adasandutsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina kuti akhale amodzi. Pakupereka thupi lake, adagamula khoma la chidani limene linkatilekanitsa. Iye adathetsa Malamulo a Mose pamodzi ndi malangizo ake ndi miyambo yake. Adachita zimenezi kuti kuchokera ku mitundu iŵiri ija, alenge mtundu umodzi watsopano, wokhala mwa Iye, kuti choncho adzetse mtendere. Khristu adafa pa mtanda kuti athetse chidani, ndipo kuti mwa mtandawo aphatikize pamodzi m'thupi limodzi mitundu iŵiriyo, ndi kuiyanjanitsa ndi Mulungu.
Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino,
Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.
Mlandireni bwino munthu amene chikhulupiriro chake nchofooka, koma osati kuti mutsutsane naye pa maganizo ake.
M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.
Abale, zimene ndanenazi nzokhudza ine ndi Apolo. Ndifuna kuti zimenezi zikuphunzitseni tanthauzo la mau aja akuti, “Musapitirire zimene Malembo akunena.” Nchifukwa chake musamanyadira wina, ndi kupeputsa mnzake.
Tsono iwe, ukuweruziranji mbale wako? Kapena iwe winawe, ukunyozeranji mbale wako? Tonsefe tidzaima pamaso pa Mulungu kuti atiweruze.
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
Wina akamanena kuti, “Ndimakonda Mulungu”, komabe nkumadana ndi mbale wake, ndi wonama ameneyo. Pakuti munthu wosakonda mbale wake amene wamuwona, sangathe kukonda Mulungu amene sadamuwone. Lamulo limene Iye adatipatsa ndi lakuti, wokonda Mulungu azikondanso mbale wake.
Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka. Poyenderana, muzisamalirana bwino mosadandaula.
Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu, akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa. Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.
Ndikufuna kuti zimenezi ziŵalimbitse mtima, ndipo azilunzana pamodzi m'chikondi, azikhala odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu. Motero adzatha kudziŵa mozama chinsinsi cha Mulungu chonena za Khristu.
Abale musamanenerana zoipa pakati panu, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Onani, woweruza waima pa khomo.
“Mbale wako akakuchimwira, pita ukamdzudzule muli aŵiri nokha. Akakumvera, wamkonza mbale wakoyo. Koma akapanda kukumvera, utengerepo wina mmodzi kapena ena aŵiri, kuti mau onse akatsimikizike ndi mboni ziŵiri kapena zitatu. Akapanda kuŵamvera iwowo, ukauze Mpingo. Ndipo akapanda kumveranso ndi Mpingo womwe, umuyese munthu wakunja kapena wokhometsa msonkho.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Nchifukwa chake ine, womangidwa m'ndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukupemphani kuti, chifukwa Mulungu adakuitanani, muziyenda moyenerana ndi kuitanidwako. Iye amene adaatsika, ndi yemweyo amene adakwera, nabzola Kumwamba konse, kuti zinthu zonse zikhale zodzaza ndi Iye. Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu. Motero potsiriza, tonse tidzafika ku umodzi umene umapezeka pakukhulupirira, ndiponso pakudziŵa Mwana wa Mulungu. Pamenepo tidzakhwima ndithu, ndi kufika pa msinkhu wathunthu wa Khristu. Sitidzakhalanso ngati ana akhanda ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, ndiponso otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya zophunzitsa za anthu onyenga amene amasokeretsa anthu ndi kuchenjera kwao Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu, umene umalamula thupi lonse, ndi kulilumikiza pamodzi ndi mfundo zake zonse. Motero chiwalo chilichonse chimagwira ntchito yake moyenera, ndipo thupi lonse limakula ndi kudzilimbitsa ndi chikondi. Tsono m'dzina la Ambuye ndikukuuzani, ndipo ndikunenetsa, kuti musayendenso monga amachitira akunja potsata maganizo ao achabe. Nzeru zao zidachita chidima, sangalandire nao konse moyo wa Mulungu chifukwa cha umbuli umene udadza mwa iwo kaamba ka kuuma mtima kwao. Mitima yao idaludzulala ndipo adangodzipereka ku zonyansa, kuti azichita zoipa zilizonse mosadziletsa. Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi,
Nchifukwa chake muzilimbitsana mtima ndi kumathandizana, monga momwe mukuchitiramu.
Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.
Tsono tiyeni tileke kumaweruzana. Makamaka mutsimikize kuti musachite kanthu kalikonse kophunthwitsa mbale wanu, kapena komchimwitsa.
Choyamba, ndikumva kuti mukamasonkhana mu mpingo, mumapatulana. Ndipo ndikhulupirira kuti zimenezi kwinaku nzoona. Nkofunika ndithu kuti pakhale kusiyana maganizo pakati panu, kuti amene ali okhoza pakati panu adziŵike.
Komabe panali aneneri ena onama ngakhale pakati pa Aisraele omwe. Momwemonso pakati pa inu padzaoneka aphunzitsi onama. Iwowo adzaloŵetsa mwachinsinsi zophunzitsa zonama ndi zoononga, ngakhale kukana kumene Mbuye wao amene adaŵaombola, ndipo motero adzadziitanira chiwonongeko mwamsanga.
Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi.
Motero palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakati pa akapolo ndi mfulu, kapenanso pakati pa amuna ndi akazi, pakuti nonsenu ndinu amodzi mwa Khristu Yesu.
Khristu ali ngati thupi limodzi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha.
Kodi Khristu wagaŵika? Kodi adakuferani pa mtanda ndi Paulo? Kodi mudabatizidwa m'dzina la Paulo?
Ndine mfulu, osati kapolo wa munthu wina aliyense ai, komabe ndidadzisandutsa kapolo wa anthu onse, kuti ndikope anthu ambiri. Ngakhaletu ena sandiyesa mtumwi, koma kwa inu ndine mtumwi ndithu, pakuti moyo wanu wachikhristu ndi umboni wakuti ndinedi mtumwi. Kwa Ayuda ndidakhala ngati Myuda, kuti ndiŵakope. Ngakhale ineyo sindilamulidwa ndi Malamulo a Mose, komabe kwa Ayuda amene ali olamulidwa ndi Malamulowo, ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ndiŵakope. Kwa amene alibe Malamulo a Mose, ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ndiŵakope. Sindiye kuti ndilibe Malamulo a Mulungu ai, popeza kuti ndili nawo malamulo a Khristu. Kwa amene ali ndi chikhulupiriro chofooka, ndidakhala ngati wa chikhulupiriro chofooka, kuti ndiŵakope ofookawo. Kwa anthu onse ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ngati nkotheka ndikope ena mwa iwo. Zonsezi ndimazichita chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti inenso ndilandire nao madalitso a Uthengawo.
Koma ngati wakunja uja afuna kuleka mkhristu, amuleke. Zikatero, ndiye kuti mkhristu wamwamunayo kapena wamkaziyo ali ndi ufulu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale ndi moyo wamtendere.
Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe? Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.
Tsono lekani kunama. Aliyense azilankhula zoona zokhazokha ndi mkhristu mnzake, pakuti tonse pamodzi mogwirizana ndife ziwalo za thupi la Khristu.
Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu. Wina amakhulupirira kuti palibe choletsa kudya chakudya chilichonse. Koma wina, amene chikhulupiriro chake nchofooka, amadya zamasamba zokha. Chakudya chisakuwonongetseni ntchito ya Mulungu. Zakudya zonse nzololedwa kuzidya, koma nkulakwa kudya chinthu chimene chingachimwitse anzathu. Nkwabwino kusadya nyama, kusamwa vinyo, ndiponso kusachita kanthu kalikonse kamene kangachimwitse mbale wako.
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi. Paja Malamulo onse a Mulungu amaundidwa mkota pa lamulo limodzi lija lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.
Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.
Angathe kupezeka munthu wophunzitsa zosiyana ndi zimenezi, wosavomereza mau oona a Ambuye athu Yesu Khristu ndi chiphunzitso chogwirizana ndi moyo wolemekeza Mulungu. Munthu wotere ndi wodzitukumula ndi kunyada, sadziŵa kanthu. Mtima wake ngwodwala, wongofuna zotsutsanatsutsana ndi kukangana pa mau chabe. Zimenezi zimabweretsa kaduka, kusamvana, kusinjirirana, kuganizirana zoipa, kupsetsana mtima kosalekeza pakati pa anthu amene nzeru zao zidaonongekeratu ndipo sazindikiranso choona. Iwo amayesa kuti kupembedza Mulungu ndi njira yopatira chuma.
Abale, tsopano tikukulamulani m'dzina la Ambuye Yesu Khristu kuti muziŵapewa abale onse a makhalidwe aulesi, osafuna kutsata mwambo umene tidaŵapatsa.
Paja Khristu adandituma, osati kuti ndizibatiza ai, koma kuti ndizilalika Uthenga Wabwino. Ndipo ndiyenera kumaulalika mosagwiritsa ntchito luso lake la ulaliki, kuwopa kuti mtanda wa Khristu ungatheretu mphamvu.
Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu. Pa nthaŵi imeneyo, munkayenda m'zoipa potsata nzeru zapansipano, ndipo munkamvera mkulu wa aulamuliro amumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ukugwira ntchito tsopano pakati pa anthu oukira Mulungu. Ndinu omangidwa pamodzi m'nyumba yomangidwa pa maziko amene ndi atumwi ndi aneneri, ndipo Khristu Yesu mwini ndiye mwala wapangodya. Mwa Iyeyu nyumba yonse ikumangidwa molimba, ndipo ikukula kuti ikhale nyumba yopatulika ya Ambuye. Mwa Iyeyu inunso mukumangidwa pamodzi ndi ena onse, kuti mukhale nyumba yokhalamo Mulungu mwa Mzimu Woyera.
Mwa chikondi muziŵachitira ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yao. Muzikhalitsana ndi mtendere pakati panu.
Nchifukwa chake tsono, nthaŵi zonse tikapeza mpata, tizichitira anthu onse zabwino, makamaka abale athu achikhristu.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu, tiziŵalezera mtima anthu ofooka, osamangodzikondweretsa tokha. Akutinso, “Inu anthu a mitundu ina, kondwani pamodzi ndi anthu ake a Mulungu.” Ndiponso akuti, “Inu nonse a mitundu ina, tamandani Ambuye, anthu a mitundu yonse amtamande.” Nayenso mneneri Yesaya akuti, “Mmodzi mwa zidzukulu za Yese adzabwera. Iye adzadzambatuka kuti alamule anthu a mitundu ina, ndipo iwo adzaika chikhulupiriro chao pa Iyeyo.” Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Abale anga, ine mwini wake sindikayika konse kuti ndinu anthu a kufuna kwabwino ndithu, ndinu anthu odziŵa zinthu, ndipo mumatha kulangizana. Komabe m'kalata ino zina ndakulemberani mopanda mantha konse, kuti ndikukumbutseni zimenezo. Ndalemba motere popeza kuti Mulungu adandikomera mtima pakundipatula kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu a mitundu ina. Adandipatsa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu ngati wansembe, kuti anthuwo akhale ngati nsembe yokomera Iye ndi yoperekedwa mwa Mzimu Woyera. Tsono pokhala ndine wake wa Khristu Yesu, ndikunyadira ntchito imene ndikugwirira Mulungu. Sindidzalimba mtima kulankhula za kanthu kena ai, koma zokhazo zimene ndimachita kudzera mwa Khristu, kuti ndithandize anthu a mitundu ina kumvera. Zimenezi ndidazichita ndi mau anga ndi ntchito zanga, ndi zizindikiro ndi zozizwitsa zamphamvu zochitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Motero Uthenga Wabwino wonena za Khristu ndidaulalika kwathunthu ku Yerusalemu ndi ku dziko lozungulira mpaka ku Iliriko. Aliyense mwa ife azikondweretsa mnzake, ndi kumchitira zabwino, kuti alimbikitse chikhulupiriro chake.
Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.”
Koma ngati muli ndi mtima wakaduka ndi wodzikonda, musamanyada ndi kutsutsana ndi choona pakunena mabodza. Nzeru zotere si zochokera Kumwamba, koma ndi nzapansipano, ndi za anthu chabe, ndiponso nzochokera ku mizimu yoipa.
Wochita zonsezi ndi Mulungu, amene mwa Khristu adatiyanjanitsa ndi Iye mwini, ndipo adatipatsa ntchito yolalikira anthu chiyanjanitsocho. Ndiye kuti mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, osaŵaŵerengera machimo ao. Ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiŵalalike.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza. Mulungu alandire ulemuwo mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibadwo yonse mpaka muyaya. Amen.
Nthaŵi zonse ndimayamika Mulungu wanga chifukwa cha inu, popeza kuti adakukomerani mtima mwa Khristu Yesu. Zoonadi mwa Khristu mwakhala anthu olemera pa zonse, makamaka pa kulankhula ndi pa kudziŵa zinthu,
Gulu lonse la okhulupirira linali la mtima umodzi, ndi la maganizo amodzi. Panalibe munthu amene ankati, “Zimene ndiri nazo nzangazanga,” koma aliyense ankapereka zake zonse kuti zikhale za onse.
Komabe ife ndife okhaokha ogwira ntchito ya Mulungu, inuyo ndinu munda wa Mulungu, ndinunso nyumba ya Mulungu.
Kunena za kukondana pakati pa akhristu, nkosafunikira kuti ndichite kukulemberani, popeza kuti ndi Mulungu mwini amene adakuphunzitsani za m'mene muyenera kukonderana.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Tikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto. Mulungu adakupatulani mwa Khristu Yesu, ndipo adakuitanani kuti mukhale anthu akeake, pamodzi ndi anthu onse amene ponseponse amatama dzina la Ambuye Yesu Khristu mopemba. Iye ndiye Mbuye wathu ndi Mbuye waonso.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Choncho pakali pano zilipo zinthu zitatuzi: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwa zonsezi chopambana ndi chikondi.
Tamva kuti anthu ena ochokera m'gulu lathu akhala akukuvutani ndi kukusokonezani maganizo. Amenewo sitidaŵatume ndife ai. Tsono titasonkhana, tavomerezana kusankha anthu ndi kuŵatuma kwa inu. Adzabwera pamodzi ndi okondedwa athu Barnabasi ndi Paulo.
Cholinga changa pokupatsa malangizo ameneŵa, nchakuti pakhale chikondi chochokera mu mtima woyera, mu mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndiponso m'chikhulupiriro chopanda chiphamaso.
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Yuwodiyayo ndi Sintikeyo ndaŵapemba, chonde akhale omvana, popeza kuti ndi abale mwa Ambuye. Mulungu Atate athu alemekezedwe mpaka muyaya. Amen. M'dzina la Khristu Yesu mundiperekereko moni kwa aliyense wamumpingo. Akukupatsani moni abale amene ndili nawo pamodzi kuno. Akukupatsani moni anthu onse a Mulungu amene ali kuno, makamakanso ogwira ntchito ku nyumba ya Mfumu ya ku Roma. Ambuye Yesu Khristu akudalitseni. Ndiponso iwe, mnzanga weniweni pa ntchito yathuyi, bwanji uŵathandize azimaiŵa. Paja ameneŵa pofalitsa Uthenga Wabwino akhala akugwira ntchito kolimba pamodzi ndi ine ndi Klemensi ndi antchito anzanga ena onse, amene maina ao ngolembedwa m'buku la amoyo.
Akhale wofatsa polangiza otsutsana naye. Mwina Mulungu angaŵapatse mwai woti atembenuke ndi kuzindikira choona.
Chikondi chimene ndikunenachi nchakuti tikhale omvera malamulo a Mulungu. Lamulo limene ndikukulemberanilo, monga mudamva kuyambira pa chiyambi, ndi lakuti moyo wanu uzikhala wachikondi.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.