Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


NDIME ZA CHIYEMBEKEZO

NDIME ZA CHIYEMBEKEZO

Chiyembekezo nchofunika kwambiri pa moyo wanga. Ndilimbikitseni mtima wanu mwa Ambuye, khulupirirani kuti mudzaona maloto anu akuti akwaniritsidwa. Musalole kuti mtima wanu ulefuke, pitirizani kupita patsogolo mpaka mutakwaniritsa zomwe mukufuna. Pitirizanibe kuyesetsa, ndipo perekani zonse zomwe mukufuna m'manja mwa Atate wathu wakumwamba.

Ndili Mkristu, sindiyenera kutaya chiyembekezo choti tidzaona Ambuye wathu maso ndi maso, ndipo chifukwa cha nsembe ya Ambuye Yesu Khristu, ndapulumutsidwa ndi chisomo, ndipo tidzakhala naye kosatha. Chiyembekezo mwa Mulungu chimatimasula ku mantha a mtsogolo ndi kusatsimikizika, khulupirirani nthawi zonse Mulungu, kuti adzakupatsani mphamvu zogonjetsa mavuto aliwonse.

“Pakuti ndidziwa bwino lomwe ndikulingalira za inu,” akutero Yehova, “malingaliro a mtendere, osati a choipa, kuti ndikupatseni inu tsogolo ndi chiyembekezo.” (Yeremiya 29:11)




Maliro 3:22-23

Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha, chifundo chakenso nchosatha. M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano, chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:9

Sikuti akuzengereza kuchita zimene adalonjeza, monga m'mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 15:18-21

Basi ndinyamuka, ndipita kwa bambo wanga, ndipo ndikanena kuti: Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kutchedwanso mwana wanu. Mundilole ndisanduke mmodzi mwa antchito anu.’ Tsono Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo adayamba kuŵinya nkumanena kuti, “Munthu uyu amalandira anthu ochimwa, nkumadya nawo pamodzi.” “Choncho adanyamukadi napita kwa bambo wake. Koma akubwera patali, bambo wake adamuwona, namumvera chisoni. Adamthamangira, namkumbatira, nkumamumpsompsona. Mwanayo adati, ‘Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kuchedwanso mwana wanu.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 2:13

Ng'ambani mitima yanu, osati zovala zanu chabe.” Bwererani kwa Chauta, Mulungu wanu, poti Iye ngwokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wa chikondi chosasinthika. Nthaŵi zonse ndi wokonzeka kukhululuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:18-19

Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale. Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 7:18-19

Kodi ndani ali Mulungu ngati Inu, amene amakhululukira machimo ndi kuiŵala zolakwa za anthu anu otsala? Simusunga mkwiyo mpaka muyaya, chifukwa muli ndi chikondi chosasinthika. Mudzatichitiranso chifundo. Mudzapondereza pansi zolakwa zathu, mudzataya machimo athu onse pansi pa nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:12

Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:18

Chauta akunena kuti, “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu: chifukwa cha machimo anu mwafiira kwambiri, koma Ine ndidzakutsukani, inu nkukhala oyera kuti mbee. Mwachita kuti psuu ngati magazi, koma mudzakhala oyera ngati thonje.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:17

Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:9

Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:1

Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:8-9

Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 7:14

ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 18:32

Sindikondwera nayo imfa ya munthu wina aliyense. Nchifukwa chake lapani, kuti mukhale ndi moyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 2:25

Motero ndidzakubwezerani zonse zimene zidaonongedwa ndi dzombe, mandowa, mphutsi ndi ziwala. Limenelitu ndiye gulu lankhondo lija limene ndidatuma kudzakukanthani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:6

Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:18

“Ndidaona m'mene ankachitira, komabe ndidzaŵachiritsa. Ndidzaŵatsogolera ndi kuŵatonthoza. Anthu olira nao adzandiyamika ndi milomo yao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:6

Paja Ambuye amamlanga aliyense amene amamkonda, amakwapula mwana aliyense amene Iwo amamlandira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:1

Inu ana anga, ndikukulemberani zimenezi kuti musamachimwa. Komabe wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, ndiye Yesu Khristu amene ali wolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:20

Iye sadzatsiriza bango lothyoka, nyale yofuka sadzaizimitsa, mpaka atapambanitsa chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 24:7

Ndidzaŵapatsa mtima woti azidziŵa kuti ndine Chauta. Iwowo adzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wao, pakuti adzabwera kwa Ine ndi mtima wao wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:7

Musakumbukire machimo a unyamata wanga ndi mphulupulu zanga. Koma mundikomere mtima, Inu Chauta, chifukwa cha chikondi chanu, pakuti Inu ndinu abwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:29

Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:28

Momwemonso Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze ndi kuchotsa machimo a anthu ambiri. Adzaonekanso kachiŵiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:13-14

Koma wokhometsa msonkho uja adaima kutali, osafuna nkuyang'ana kumwamba komwe. Ankangodzigunda pa chifuwa ndi chisoni nkumanena kuti, ‘Mulungu, mundichitire chifundo ine wochimwane.’ ” Yesu popitiriza mau adati, “Kunena zoona, wokhometsa msonkhoyu adabwerera kwao ali wolungama pamaso pa Mulungu, osati Mfarisi uja ai. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo wodzichepetsa, adzamkuza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:43

Aneneri onse adamchitira umboni, ndi kunena kuti chifukwa cha dzina lake, Mulungu adzakhululukira machimo a munthu aliyense wokhulupirira Iyeyu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:11

Enanu munali otere kale, koma mudayeretsedwa, mudasanduka anthu a Mulungu, ndipo mudapezeka olungama pamaso pake. Zimenezi zidachitika m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndiponso mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 1:3

Tsono uŵauze anthuŵa kuti zimene akunena Chauta Wamphamvuzonse ndi izi, akuti, Bwererani kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:3

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:11

Mulungutu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:8

Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:1

Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:15

Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 11:29

Pakuti Mulungu sasinthanso ataitana munthu ndi kumpatsa mphatso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:27

Mbuye wake uja adamumveradi chifundo, ndipo adamkhululukira ngongole ija, namlola kuti apite.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 12:13

“Ndidachimwira Chauta.” Natani adati, “Chauta wakukhululukirani machimo anu, simufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 33:11

Uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndithudi, pali Ine ndemwe, sindikondwa ndikaona munthu woipa alikufa. Ndikadakonda kuti aleke kuchimwako kuti akhale ndi moyo. Inu Aisraele, muferanji? Tembenukani, lekani zoipa zimene mukuchita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 21:15-17

Iwo atafisula, Yesu adafunsa Simoni Petro kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi koposa m'mene amandikondera aŵa?” Iye adati, “Inde Ambuye, mukudziŵa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala anaankhosa anga.” Yesu adamufunsanso kachiŵiri kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi?” Iye adati, “Inde Ambuye, mukudziŵa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Ŵeta nkhosa zanga.” Yesu adamufunsa kachitatu kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda?” Petro adayamba kumva chisoni kuti Yesu akumufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda?” Ndipo adati, “Ambuye, mumadziŵa zonse. Mukudziŵa kuti ineyo ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala nkhosa zanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 5:32

Inetu sindidabwere kudzaitana anthu olungama, koma anthu ochimwa, kuti atembenuke mtima.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 17:30

Mulungu adaaŵalekerera anthu pa nthaŵi imene iwo anali osadziŵa, koma tsopano akuŵalamula anthu onse ponseponse kuti atembenuke mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:18

Komabe Chauta akufunitsitsa kuti akukomereni mtima. Ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo, chifukwa Chauta ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:8-9

Chauta ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika. Chauta ndi wabwino kwa onse, amachitira chifundo zamoyo zonse zimene adazilenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:13

Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:13-14

Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa ku mavuto aowo. Chauta adaŵatulutsa anthuwo mu mdima ndi m'chisoni muja, ndipo adadula maunyolo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:3-4

Ndiye amene amakhululukira machimo ako onse, ndi kuchiritsa matenda ako onse. Ndiye amene amapulumutsa moyo wako ku manda. Amakuveka chikondi chake chosasinthika ndiponso chifundo chake ngati chisoti chaufumu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:36

Monga Atate anu akumwamba ali achifundo, inunso mukhale achifundo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:2

Zinthu zonsezi ndidazilenga ndine, tsono zonsezi nzanga,” akutero Chauta. “Anthu amene ndimakondwera nawo ndi aŵa: odzichepetsa ndi olapa, ondiwopa ndi omvera mau anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:11

Maiyo adati, “Inde Ambuye, palibe.” Tsono Yesu adamuuza kuti, “Inenso sindikukuzengani mlandu. Pitani koma kuyambira tsopano musakachimwenso.”]

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:13

Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:17

Pambuyo pake akutinso, “Sindidzaŵakumbukiranso konse machimo ao ndi zolakwa zao.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:2

Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko, m'chithaphwi chamatope. Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyendetsa bwino lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 12:20

Samuele adaŵauza kuti, “Musaope. Kuchimwa mwachimwadi, komabe musaleke kutsata Chauta. Muzimtumikira ndi mtima wanu wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yona 3:1-10

Chauta adalankhula ndi Yona kachiŵiri, namuuza kuti, Mulungu adaona zimene anthuwo adachita, ndi m'mene adasiyira makhalidwe ao oipa. Choncho adakhululuka, osaŵapatsa chilango chimene adaati adzaŵapatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:13

Wobisa machimo ake sadzaona mwai, koma woulula ndi kuleka machimo, adzalandira chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:28-30

“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:13-14

Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiŵala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo. Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:10

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:7

Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:4

Nchifukwa chake pa ubatizo tidachita ngati kufa ndi kuikidwa m'manda pamodzi naye, kuti monga Khristu adauka kwa akufa ndi mphamvu ya Atate, momwemonso ife tikhale ndi moyo watsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:5

Choncho adatipulumutsa osati chifukwa cha ntchito zolungama zimene ife tidaachita, koma mwa chifundo chake pakutisambitsa. Adatisambitsa mwa Mzimu Woyera pakutibadwitsa kwatsopano ndi kutipatsa moyo watsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:5

Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:38

Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 23:43

Yesu adamuyankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino ukhala nane ku Malo a Chisangalalo, Kumwamba.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:10

Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 31:34

Nthaŵi imeneyo wina sazidzachitanso kuphunzitsa mnzake kapena mbale wake kuti adziŵe Chauta. Pakuti onsewo, ana ndi akulu omwe adzandidziŵa, Ndidzaŵakhululukira machimo ao, sindidzakumbukiranso machimo aowo,” akuterotu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1

Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:32

Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:5

Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:7

Oipa asiye makhalidwe ao oipa, ndipo osalungama asinthe maganizo ao oipa. Abwerere kwa Chauta, kuti Iyeyo aŵachitire chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, kuti Iye aŵakhululukire machimo ao mofeŵa mtima.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:14-15

“Ndithu ngati mukhululukira anthu machimo ao, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani inunso. Koma ngati simukhululukira anthu machimo ao, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:19

Tsono tembenukani mtima ndi kubwerera kwa Mulungu, kuti akufafanizireni machimo anu. Motero Ambuye adzakupatsani nthaŵi ya mpumulo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 8:12

Mwachifundo ndidzaŵakhululukira zochimwa zao, sindidzakumbukiranso machimo ao.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:31

Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:7

Popeza kuti mudalandira manyazi, manyozo ndi zotukwana moŵirikiza, tsopano mudzalandira chigawo cha dziko lanu moŵirikizanso. Chimwemwe chanu chidzakhala chamuyaya.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:16

Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 7:47

Mwakuti kunena zoona, chikondi chachikulu chimene iyeyu waonetsa, chikutsimikiza kuti Mulungu wamkhululukiradi machimo ake amene ali ochuluka. Koma munthu amene wakhululukidwa zochepa, amangokonda pang'ono.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:7

Ngodala anthu ochitira anzao chifundo, pakuti iwonso Mulungu adzaŵachitira chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 36:26

Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kuloŵetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzakuchotserani mtima wanu wouma ngati mwalawo ndi kukupatsani mtima wofeŵa ngati mnofu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:15

Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:14

Chauta amachirikiza onse ogwa m'mavuto, amakweza onse otsitsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 6:37

Onse amene Atate andipatsa, adzabwera kwa Ine. Ndipo munthu aliyense wodza kwa Ine, sindidzamkana konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:13

Ngati ndife osakhulupirika, Iye amakhalabe wokhulupirika, pakuti sangathe kudzitsutsa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 32:5

Koma ndidavomera tchimo langa kwa Inu, sindidabise kuipa kwanga. Ndidati, “Ndidzaulula machimo anga kwa Chauta,” pomwepo Inu mudakhululukiradi mlandu wa machimo anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:22

Ndachotsa zolakwa zako ngati mtambo ndiponso machimo ako ngati nkhungu. Bwerera kwa Ine poti ndakuwombola.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:15

Aŵa ndi mau otsimikizika, oyenera kuŵavomereza ndi mtima wonse, akuti Khristu Yesu adabwera pansi pano kuti adzapulumutse anthu ochimwa. Ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwa koposa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:24

Ngakhale agwe sadzapweteka, popeza kuti Chauta amamgwira dzanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:20

Mulungu adapereka Malamulo kuti anthu azindikire kuchuluka kwa machimo ao. Koma pamene uchimo udachuluka, kukoma mtima kwa Mulungu kudachuluka koposa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 12:9

koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:13-14

Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:21-22

Pamenepo Petro adadzafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi mbale wanga atamandichimwira, ndidzamkhululukire kangati? Kodi ndidzachite kufikitsa kasanunkaŵiri?” Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ndikuti kasanunkaŵiri kokha ngati, iyai, koma mpaka kasanunkaŵiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi aŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:1-2

Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, malinga ndi chikondi chanu chosasinthika. Mufafanize machimo anga, malinga ndi chifundo chanu chachikulu. Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika. Musandipirikitse pamaso panu, musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine. Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu, mulimbitse mwa ine mtima womvera. Pamenepo ochimwa ndidzaŵaphunzitsa njira zanu, ndipo iwo adzabwerera kwa Inu. Mundikhululukire mlandu wanga wokhetsa magazi, Inu Mulungu, Mulungu Mpulumutsi wanga, ndipo ndidzakweza mau poimba za chipulumutso chanu. Ambuye, tsekulani milomo yanga, ndipo pakamwa panga padzalankhula zotamanda Inu. Si nsembe wamba imene Inu imakusangalatsani. Ndikadapereka nsembe yopsereza, sibwenzi Inu mutakondwera nayo. Nsembe imene Inu Mulungu mumailandira, ndi mtima wotswanyika. Mtima wachisoni ndi wolapa, Inu Mulungu simudzaunyoza. Muŵachitire zabwino anthu a ku Ziyoni, chifukwa cha kukoma mtima kwanu. Mumangenso kachiŵiri makoma a Yerusalemu. Pamenepo mudzakondwera ndi nsembe zoyenera, nsembe zootcha ndi zopsereza kwathunthu. Choncho adzapereka ng'ombe zamphongo pa guwa lanu lansembe. Mundisambitse kwathunthu pochotsa kulakwa kwanga, mundiyeretse mtima pochotsa machimo anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:23-24

popeza kuti onse adachimwa, nalephera kufika ku ulemerero umene Mulungu adaŵakonzera. Koma mwa kukoma mtima kwake kwaulere, anthu amapezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu, chifukwa cha Khristu Yesu amene adaŵaombola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:16

Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 29:11

Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:16

Munthu wabwino amagwa kasanunkaŵiri, koma amadzukirira ndithu, m'menemo anthu oipa tsoka limaŵagwera chonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Chauta wanga wachilungamo ndi wamuyaya, Ambuye Wamkulukulu, m'dzina la Yesu ndikubwera kwa Inu, Inu nokha ndinu woyenera kutamandidwa ndi kupembedzedwa kwakukulu. Mawu anu amati: "Pakuti Ine ndikudziwa malingaliro amene ndili nawo pa inu, ati Yehova, malingaliro a mtendere, osati a choipa, kuti ndikuperekeni chiyembekezo chimene mukuchiyembekezera." Zikomo chifukwa ndimatha kupumula mwa Inu, wotetezeka komanso wodalirika ngati mkango, ngakhale pakati pa mdima wakuda kwambiri, sindidzaopa chifukwa Inu ndinu kuunika kwanga ndi mphamvu yanga. Ambuye, ndithandizeni kuti ndisaike chiyembekezo changa pa zinthu zina, koma mwa Inu nokha. Ndikukuthokozani chifukwa mwandiyesa woyera mwa chisomo chanu, ndikupemphani kuti mundithandize kuti nthawi zonse ndisunge chiyembekezo cha moyo wosatha mwa kuchisunga ndi kuchiyembekezera mumtima mwanga, kuti ndisunge ndi mantha ndi kunjenjemera chipulumutso chachikulu chimenechi chimene mwandipatsa. Ndithandizeni nthawi zonse kuti ndikhale maso pa zinthu za kumwamba osati za padziko lapansi, chifukwa nzika yanga ili kumwamba. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa