Mnzanga, uli ngati mwala wamtengo wapatali m'manja mwa Mulungu. Uli wolimba mtima, wogwira ntchito, ndipo wokhoza zinthu zambiri. Mulungu amakukonda ndipo anakulenga ndi cholinga chokongola. Tsiku lililonse yesetsa kuchita zabwino zomwe ungathe ndipo khalidwe lako lilemekeze Mulungu.
Ndikudziwa kuti pali mavuto ndi zinthu zovuta zomwe umakumana nazo, koma kumbukira kuti Yehova adzakulanditsa ku zonsezo. Menya nkhondo zako tsiku lililonse, koma pogwadira pamaso pa Mulungu ndipo Iye adzakutsogolera ndi kukupatsa chipambano.
Iwe, yang'ana kwambiri kukongola kwa mkati, osati kwa kunja. Mulungu amaona kukongola kwa mkati, kukongola kosatha komwe kumachokera mu mzimu wodekha pamaso pa Mulungu. Umenewu ndiye uli ndi mtengo wapatali pamaso pa Mulungu.
Nthawi zonse lankhula ndi nzeru zochokera kwa Mulungu, ndipo uphunzitse ndi chikondi. Khala munthu wanzeru pomanga banja lako, osachita ngati chitsiru chimene chimagwetsa nyumba yake ndi manja ake.
Pitiriza kupita patsogolo tsiku lililonse. Mulungu ali nawe, usakayike zimenezo. Ndi chithandizo cha Atate wako wakumwamba, udzakhala munthu wotsanzira kulikonse kumene upita. Nthawi zonse mufufuze Mlengi wako ndipo uzisinkhasinkha zabwino zake tsiku lililonse. “Kukongola kumanamiza, ndipo mawonekedwe amakhala opanda pake; koma mkazi woopa Yehova ndiye woyenera kutamandidwa.” (Miyambo 31:30)
Kudzikongoletsa kwanu kusangokhala kwa maonekedwe akunja pakuluka tsitsi, ndi kuvala zamakaka zagolide ndi zovala zamtengowapatali. Koma kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa moyo wam'kati, kukongola kosatha kwa mtima wofatsa ndi wachete. Moyo wotere ngwamtengowapatali pamaso pa Mulungu.
Nkhope yachikoka ndi yonyenga, kukongola nkosakhalitsa, koma mkazi woopa Chauta ndiye woyenera kumtamanda.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Mfumu idzakukonda chifukwa cha kukongola kwako. Umuŵeramire popeza kuti ndiye mbuyako.
Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku.
Momwe chimaonekera chipini chagolide chikakhala pa mpuno wa nkhumba, ndi momwenso kumakhalira kukongola kwa mkazi wam'kamwa.
Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite.
Koma Chauta adauza Samuele kuti, “Usayang'ane maonekedwe ake, ngakhale kutalika kwa msinkhu wake, poti ndamkana ameneyo. Chauta sapenya monga m'mene apenyera anthu. Anthu amapenya zakunja, koma Chauta amapenya zamumtima.”
Motero Mulungu adalenga munthu, m'chifanizo chake, adaŵalengadi m'chifanizo cha Mulungu. Adaŵalenga wina wamwamuna wina wamkazi.
Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongola, ndiwe chiphadzuŵa. Maso ako akunga ngati nkhunda. Mkazi
Ndiwe wokongola, iwe wokondedwa wanga! Ndithuditu, ndiwe wokongoladi! Kumbuyo kwa nsalu yako yakumutuyo maso ako akuwoneka oŵala ngati nkhunda. Tsitsi lako likuchita pekupeku ngati mbuzi zoti zikutsetsereka pa mapiri a ku Giliyadi.
Udzakhala ngati chisoti chaufumu chokongola m'manja mwa Chauta, ngati nsangamutu yaulemerero m'manja mwa Mulungu wako.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Pamene anali pafupi kuwoloka malire a Ejipito, adauza mkazi wake Sarai kuti, “Ndikudziŵa kuti iwetu ndiwe mkazi wokongola.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
M'dziko monsemo munalibe akazi okongola ngati ana a Yobe. Bambo wao adaŵapatsa choloŵa chimodzimodzi ngati alongo ao.
Paja Chauta amakondwera ndi anthu ake, amaŵalemekeza anthu odzichepetsa poŵagonjetsera adani ao.
Munthuyo anali Nabala, wa fuko la Kalebe, ndipo mkazi wake anali Abigaile. Mkaziyo anali wanzeru ndi wokongola, koma mwamuna wakeyo anali wouma mtima ndi wankhanza. Anali wa fuko la Kalebe.
Ndiwe wokongola zedi, ndiponso wosangalatsa, iwe wokondedwawe, namwali wokondweretsawe.
Anali namwali wosadziŵa mwamuna aliyense, wokongola kwambiri. Iye adatsikira kuchitsime kuja, natunga madzi mu mtsuko, nkutulukako.
Wokondedwa wanga akulankhula nkumandiwuza kuti: Mwamuna “Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga, tiye tizipita.
Ndani uyu wooneka ngati mbandakuchayu, wokongola ngati mwezi, woŵala ngati dzuŵa, wochititsa mantha ngati gulu la ankhondo mbendera zili m'manja?
Mumameretsa udzu kuti ng'ombe zidye, ndi zomera kuti munthu azilima ndi kupeza chakudya m'nthaka. Amapezamo vinyo wosangalatsa mtima wake, mafuta odzola kuti thupi lake lisisire, ndiponso buledi kuti ampatse mphamvu.
Dzuka, iwe mphepo yakumpoto, bwera kuno, iwe mphepo yakumwera. Uuzire pa munda wanga kuti fungo lake lokoma likwanire ponseponse. Wokondedwa wanga aloŵe m'munda mwake, adye zipatso zake zokoma.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Ndapempha chinthu chimodzi chokha kwa Chauta, chinthu chofunika kwambiri, chakuti ndizikhala m'Nyumba ya Chauta masiku onse a moyo wanga, kuti ndizikondwera ndi kukoma kwake kwa Chauta ndi kuti ndizipembedza Iye m'Nyumba mwakemo.
Iwe wokongola koposa akazi onsewe, ngati sukukudziŵa, uzingotsata m'makwalala a msambi wa ziŵeto, uzidyetsa mbuzi zako pambali pa mahema a abusawo.
Iwe namwali wachifumu, mapazi ako ngokongola m'nsapato wavalazo. Ntchafu zako nzoulungika bwino ngati miyala yamtengowapatali, yosemedwa ndi mmisiri waluso.
koma kuti kwa mkazi nchaulemu? Mulungu adapatsa mkazi tsitsi lalitali loti aziphimbira mutu wake.
Adapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthaŵi yake. M'mitima mwa anthu Mulungu adaikanso nzeru zotanthauzira zochitika za pa mibadwo ndi mibadwo. Komabe anthuwo sangathe kuzitulukira ntchito zonse za Mulungu kuyambira pa chiyambi mpaka pomalizira.
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
ndi chuma chao chamitundumitundu. Mwana wamkazi wa mfumu ali m'chipinda mwake, wadzikongoletsa kwambiri, wavala zovala zoluka ndi thonje lagolide. Akupita naye kwa mfumu atavala zovala zamaluŵa, pamodzi ndi anamwali anzake omperekeza.
Chimodzimodzinso inu azimai, muzimvera amuna anu, kuti ngati ena mwa iwo samvera mau a Mulungu, azikopeka ndi makhalidwe a akazi aonu. Sipadzafunikanso kunenerera mau, Paja mau a Mulungu akuti. “Yemwe afuna kukondwera ndi moyo, ndi kuwona masiku abwino, aletse lilime lake kulankhula zoipa, ndiponso milomo yake kunena mabodza. Alewe zoipa, azichita zabwino. Afunefune mtendere ndi kuyesetsa kuupeza. Paja Ambuye amaŵayang'anira bwino anthu olungama amatchera khutu ku mapemphero ao. Koma ochita zoipa saŵayang'ana bwino.” Ndani angakuchiteni choipa ngati muchita changu pa zabwino? Koma ngakhale mumve zoŵaŵa chifukwa cha chilungamo, mudzakhala odala ndithu. Musachite mantha ndi anthu, kapena kuvutika mu mtima, koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza. Khalani ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, kotero kuti anthu ena akamasinjirira mayendedwe anu abwino pamene mukutsata Khristu, achite manyazi ndi chipongwe chao. Nkwabwino kumva zoŵaŵa chifukwa chochita zabwino, ngati Mulungu wafuna choncho, koposa kumva zoŵaŵa chifukwa chochita zoipa. Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo. Ndipo ali ngati mzimu choncho, adapita kukalalika kwa mizimu imene inali m'ndende. popeza kuti adzadziwonera okha makhalidwe anu aulemu ndi angwiro.
Mkazi wabwino ali ngati chisoti chaulemu kwa mwamuna wake, koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda chamafinya kwa mwamuna wake.
Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, wangoti mtima wangawu kwe! Wanditenga mtima ndi kapenyedwe ka maso ako, ndiponso ndi mphande imodzi ya mkanda wa m'khosi mwako.
Iwe nkhunda yanga, yokhala m'ming'alu yam'matanthwe, yobisala m'phiri lotsetsereka, ntaonako nkhope yako, ntamvako liwu lako. Paja liwu lako nlomveka bwino, ndipo nkhope yako ndi yokongola.
Umatirire mtima wako kuti musaloŵe winanso koma ine ndekha, ndipo sudzakumbatira winanso koma ine ndekha. Paja chikondi nchamphamvu ngati imfa, nsanje njaliwuma ngati manda. Chikondi chimachita kuti laŵilaŵi ngati malaŵi a moto, ndipo nchotentha koopsa.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga. Inu Chauta, Mulungu wanga, ndinu aakulu kwambiri. Mumavala ulemu ndi ufumu. Inu mumatumphutsa akasupe m'zigwa, mitsinje imayenda pakati pa mapiri. Imapatsa nyama zonse zakuthengo madzi akumwa, mbidzi zimapherapo ludzu. Mbalame zimamanga zisa pafupi ndi mitsinjeyo, zimaimba m'nthambi za mitengo. Inu mumathirira mapiri ndi madzi ochokera ku malo anu akumwamba. Dziko lapansi ladzaza ndi madalitso anu. Mumameretsa udzu kuti ng'ombe zidye, ndi zomera kuti munthu azilima ndi kupeza chakudya m'nthaka. Amapezamo vinyo wosangalatsa mtima wake, mafuta odzola kuti thupi lake lisisire, ndiponso buledi kuti ampatse mphamvu. Mitengo ya Chauta amaithirira ndi madzi ambiri, mikungudza ya ku Lebanoni imene adaibzala. Mbalame zimamanga zisa m'menemo, dokowe amamanga chisa m'mikungudzamo. M'mapiri aatali ndimo m'mene mumakhala mbalale, m'matanthwe ndimo m'mene mumathaŵira mbira. Inu mudapanga mwezi kuti uzisiyanitsa nyengo, ndipo dzuŵa limadziŵa nthaŵi yake yoloŵera. Mumadzifunditsa ndi kuŵala ngati chovala, mwatambasula mlengalenga ngati hema.
Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongola ngati Tiriza, wa maonekedwe abwino ngati Yerusalemu, ndiwe wochititsa mantha ngati gulu la ankhondo mbendera zili m'manja.
Khristu ali ngati thupi limodzi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha.
Chauta, mtima wanga ndi wosadzikuza, maso anga ndi osanyada. Sinditengeka mtima ndi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa. Koma ndautonthoza ndi kuukhalitsa chete mtima wanga, monga mwana amene mai wake amamtonthoza ndi bere. Momwemo mtima wanga uli phe m'kati mwanga.
Ndiyetu mudamlenga mochepera pang'ono kwa Mulungu amene, mudampatsa ulemerero ndi ulemu wachifumu.
Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo.
Wokondedwa wangayo ngwokongola, ndiponso wathanzi, wodziŵika zedi pakati pa amuna zikwi khumi.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
Yakobe ankakonda Rakele, ndipo adati, “Ndidzakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi ziŵiri chifukwa cha mwana wanu Rakele.”
Monga momwe nkhope imaonekera m'madzi, momwemonso mtima wa munthu umadziŵika ndi zochita zake.
“Ndipo mumaderanji nkhaŵa ndi zovala? Onani maluŵa akuthengo m'mene amakulira. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu ai. Komatu kunena zoona, ngakhale mfumu Solomoni yemwe, mu ulemerero wake wonse, sankavala zokongola kulingana ndi limodzi lomwe mwa maluŵa ameneŵa.
Khosi lako lili ngati nsanja ya Davide, yomangidwa bwino ndipo yosalala. Mkanda wako wam'khosi, ngati zishango 1,000 zokoloŵeka kuzungulira nsanjayo.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Amadzuka usikusiku nkuyamba kukonzera chakudya anthu a pabanja pake, ndi kuŵagaŵira ntchito adzakazi ake.
Khosi lako lili see ngati nsanja ya mnyanga wanjovu. Maso ako ali ngati maiŵe a ku Hesiboni, amene ali pafupi ndi chipata cha ku Batirabimu. Mphuno yako ikuwoneka ngati nsanja ya ku Lebanoni, yoyang'ana ku Damasiko.
Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali.
Tsono adani anga adzabwezedwa m'mbuyo pa tsiku lomwe ndidzaitana Mulungu. Ndikudziŵa kuti Mulungu ali pa mbali yanga.
Motero amagwira njakata. Mkazi wosakwatiwa, kapenanso namwali, amangotekeseka ndi za Ambuye, kuti adzipereke kwa Ambuye m'thupi ndi mumzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mwamuna wake.
Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake, udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo. Kukhulupirika kwake kumateteza monga chishango ndi lihawo.
Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndakupembani, chikondichi musachigwedeze kapena kuchiwutsa mpaka pamene chifunire ichocho. Akazi
Pembedzani Chauta waulemerero ndi woyera, njenjemerani pamaso pake, inu anthu onse a pa dziko lapansi.
Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.
Choncho Potifara adaika m'manja mwa Yosefe zake zonse, kotero kuti sankalabadiranso kanthu kalikonse, koma chakudya chokha chimene ankadya. Yosefe anali wa maonekedwe abwino ndi wokongola.
Mwadzidzidzi Yesu adakumana nawo nati, “Monitu azimai!” Iwo adadza pafupi, nkugwira mapazi ake, nampembedza.
Mumakonda chilungamo ndipo mumadana ndi zoipa. Nchifukwa chake Mulungu, Mulungu wanu, wakusankhani. Wakudzozani ndi kukusangalatsani kupambana anzanu ena onse.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Milomo yake njosangalatsa kwambiri, munthuyo amanditenga mtima kwabasi. Ameneyutu ndiye wokondedwa wanga, ndiponso bwenzi langa, inu akazi a ku Yerusalemu.
Mikuyu ikubereka zipatso, mipesa ikuyamba maluŵa. Mitengoyo ikutulutsa fungo lokoma. Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga, tiye tizipita.
Yakobe adauza Labani kuti, “Tsopano nthaŵi yatha. Patseni mwana wanuyu kuti ndimkwatire.”
Wokondedwa wanga ndikumuwona ngati chipukutu cha maluŵa ofiira a m'munda wamphesa wa ku Engedi. Mwamuna
Maŵere ako ali ngati mbaŵala ziŵiri, ngati mphoyo zamapasa zimene zikudya pakati pa akakombo.
Koma ife kwathu kwenikweni ndi Kumwamba, ndipo kumeneko kudzachokera Mpulumutsi amene tikumuyembekeza. Mpulumutsiyo ndi Ambuye Yesu Khristu.
Munthu wamba, wodzigwirira ntchito napeza zofunika, ali pabwino kuposa wongodzikuza, pamene alibe nchakudya chomwe.
Usandipenyetsetse, pakuti maso ako amanditenga mtima. Tsitsi lako likuchita pekupeku ngati mbuzi, zoti zikutsetsereka pa mapiri a ku Giliyadi.
Pajatu mtumiki wake uja adakula ngati chiphukira pamaso pa Mulungu, ndiponso ngati muzu m'nthaka youma. Iye analibe maonekedwe enieni kapena nkhope yabwino, kuti ife nkumamuyang'ana. Analibe kukongola koti ife nkukokeka naye.
Inunso amuna, muzikhala moŵamvetsa bwino akazi anu. Muziŵachitira ulemu popeza kuti iwowo ndi mtundu wofookerapo, ndiponso ngolandira nanu pamodzi mphatso ya Mulungu, imene ili moyo wosatha. Muzitero, kuti pasakhale kanthu koletsa mapemphero anu.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Idzakhala madalitso ngati mvula yogwa pa minda ngati mvula yowaza pa nthaka! Pa masiku ake chilungamo chidzakula, mtendere udzachuluka, mpaka mwezi utaleka kuŵala!
Ndimadziŵa kuti Inu Chauta mumateteza ozunzika, mumaweruza mwachilungamo anthu osoŵa.
Mtima wa mwamuna wake umamkhulupirira, ndipo mwamunayo sadzasoŵa phindu. Masiku onse a moyo wake, mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino osati zoipa.
Tiye tichokeko ku Lebanoni, iwe mkazi wanga. Tiye tichoke ku Lebanoni kuno, utsagane ndi ine. Utsikepo pa nsonga ya phiri la Amana, pa nsonga ya phiri la Seniri ndi la Heremoni. Uchokemo m'mapanga a mikango, uchokeko ku ngaka za akambuku.
Pali golide ndi miyala yambirimbiri yamtengowapatali, koma mau olankhula zanzeru ali ndi mtengo woposa zonsezo.
Mchombo wako uli ngati chikho choulungika, chimene nthaŵi zonse nchodzaza ndi vinyo wabwino. Pamimba pako mponing'a ngati mtolo wa tirigu wozingidwa ndi akakombo.
Tamandani Chauta, pakuti ngwabwino. Muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti nlokoma kwambiri.
Tsono Isaki adatenga Rebeka kuti akhale mkazi wake naloŵa naye m'hema mwake. Isaki adamkonda kwambiri Rebekayo, mwakuti zimenezi zidamtonthoza pa imfa ya mai wake ija.
Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, chikondi chako nchosangalatsa. Chikondi chako nchosangalatsa kupambana vinyo, mafuta ako ndi onunkhira bwino kupambana zonunkhira zabwino zonse.
Iwe Yerusalemu, ndidadinda chithunzi chako pa zikhatho zanga, zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse.
Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu?
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Pamene wokondedwa wanga adangoti pisu dzanja pa chiboo chapachitseko, mtima wanga udachita kuti phwii!
Abramu ataoloka malire kuloŵa mu Ejipito, Aejipito adaonadi kuti mkazi wake ndi wokongola kwambiri. Akalonga a mfumu ya ku Ejipito atamuwona mkaziyo, adakauza Farao za kukongola kwake. Pomwepo anthu aja adamtenga mkaziyo kukamuika ku nyumba ya mfumu.
Amapezamo vinyo wosangalatsa mtima wake, mafuta odzola kuti thupi lake lisisire, ndiponso buledi kuti ampatse mphamvu.
Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.
Nanga ndili ndi yani kumwamba kupatula Inu? Pansi pano palibe kanthu kena kamene ndimafuna, koma Inu nokha. Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Wokondedwa wanga ali ngati mphoyo, kapena mwanawambaŵala. Si uyo waimirira apoyo, kuseri kwa khoma lathulo, akusuzumira m'mawindo, akuyang'anira pa made a mawindo.
Nkhaŵa ya munthu imakhala ngati katundu wolemera mumtima mwake, koma mau abwino amamsangalatsa.
Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo. Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Milomo yako ili ngati mbota yofiira, ndipo pakamwa pako mpokongola zedi. Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yakumutuyo, masaya ako, akuwoneka ngati mabandu a makangaza.
Mwana wanga, umvere zimene bambo wako akukulangiza, usakane zimene mai wako akukuphunzitsa. Zili ngati nsangamutu yokongola yamaluŵa pamutu pako, zili ngati mkanda wa m'khosi mwako.
Usiku uliwonse ndili gone pabedi panga ndinkangomufunafuna amene mtima wanga umamkonda. Ndidamufunafuna koma osampeza. Ndidamuitana, koma iye osandiyankha.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.
Malo amene mumakhalamo, Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndi okoma kwambiri. Kukhala tsiku limodzi m'mabwalo anu nkwabwino kwambiri kupambana kukhala masiku ambiri kwina kulikonse. Nkadakonda kukhala wapakhomo wa Nyumba ya Mulungu wanga kupambana kukhala m'nyumba za anthu oipa. Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama. Inu Chauta Wamphamvuzonse, ngwodala munthu woika chikhulupiriro chake pa Inu. Mtima wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka, kufunitsitsa kuwona mabwalo a Chauta. Inu Mulungu wamoyo, ndikukuimbirani mwachimwemwe ndi mtima wanga wonse.
Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, uli ngati munda wopiringidza, ngati munda wopiringidza, ngati kasupe wochingidwa.
Wantchito usamsinjirire kwa mbuyake, kuti angakutemberere, ndipo iweyo ungapezeke kuti ndiwe wolakwa.
Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.
Mutu wako uli bwinobwino neng'a, ngati phiri la Karimele, ndipo tsitsi lako lalitali lili chezichezi. Kukongola kwake kumatha kudolola ndi mfumu yomwe.
Ngakhale nthaŵi ya mdima, munthu wochita chilungamo ayenda m'kuŵala, chifukwa ngwokoma mtima, wachifundo ndi woongoka.
Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza, Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate. Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye. Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo, kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi, pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe. Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu. Chimodzimodzi inunso muzikondwa, ndi kusangalala nane pamodzi. Ngati Ambuye Yesu alola, ndikhulupirira kuti ndidzatha kutuma Timoteo kwanuko msanga, kuti mtima wanga ukhale pansi nditamva za kumeneko. Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi.
Atamandike Chauta: wandiwonetsa modabwitsa chikondi chake chosasinthika, pamene ndinali mu mzinda wozingidwa ndi gulu la ankhondo.
Amene ali ake a Khristu Yesu, adalipachika pa mtanda khalidwe lao lokonda zoipa, pamodzi ndi zokhumba zake ndi zilakolako zake.
Wokondedwa wanga watsikira kumunda kwakeku, ku timinda ta mbeu zokometsera chakudya. Akukadyetsa ziŵeto zake ku minda ndiponso akukathyola akakombo.