Pa moyo wanga, ndidzakumana ndi zinthu zosangalatsa, komanso zinthu zomwe zidzandibweretsera chisoni ndi mphwayi. Yesu, munthu wangwiro komanso wabwino kwambiri amene anakhalapo padziko lapansi, anakumananso ndi mavuto ambiri: anabeledwa, anapsinjidwa, anakana ndi kunyozedwa. Komabe, palibe chilichonse mwa izi chomwe chinasintha chikondi chake pa anthu. M'malo motittemberera, anatikonda ndi chikondi chosatha ndipo anapempha Atate kuti atikhululukire machimo athu.
Ndikofunika kukumbukira kuti anthu ambiri adzayesa kukupwetekani ndi kukuvutitsani, komanso kukusetsani, maloto anu kapena ntchito zanu. Nthawi zina mungafooke mtima ndi kufuna kungotayika chifukwa cha manyazi. Komabe, ndikukulemberani izi lero kuti ndikulimbikitseni. Ngakhale ena angakusekeni, ndikofunika kwambiri kudziwa zomwe Mulungu amaganiza za inu. Kwa iye, ndinu cholengedwa chodabwitsa, ndipo Mawu ake amati: "Ndithudi adzaseka onyoza, koma odzichepetsa adzawapatsa chisomo." (Miyambo 3:34).
Musadandaule ndi zomwe ena akunena kapena kuchita. Mulungu sadzamasula wolakwa. Khulupirirani Mawu ake, pumulani mwa Iye ndipo mulole dzanja lake lamphamvu likutetezeni ku onse akuzunzani. Musagonje ku chiwembu cha mdani chokuopsezani; kumbukirani kuti zonse mukhoza mwa Khristu amene akukupatsani mphamvu, ndipo m'dzina lake muli opambana.
“Kodi anthu osachangamukanu, mudzakondwerabe kupusaku mpaka liti? Kodi anthu onyodola, adzakhalabe akunyodola mpaka liti? Nanga opusa adzakana kuphunzira zanzeru mpaka liti? Musamale kudzudzula kwangaku, ine ndikuuzani maganizo anga, ndi kukudziŵitsani mau anga.
“Kodi anthu osachangamukanu, mudzakondwerabe kupusaku mpaka liti? Kodi anthu onyodola, adzakhalabe akunyodola mpaka liti? Nanga opusa adzakana kuphunzira zanzeru mpaka liti?
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.
Inu Chauta, mwandipusitsa ine, ndipo ndapusadi. Inu ndinu amphamvu kuposa ine, ndipo mwandipambana. Aliyense akundiseka tsiku lonse, aliyense akundinyodola kosalekeza.
Pamene anthuwo adamva za kuuka kwa akufa, ena adangoseka. Koma ena adati, “Bwanji mudzatiwuzenso zimenezi tsiku lina.”
Choyamba mumvetse izi: pa masiku otsiriza kudzafika anthu olalata, otsata zilakolako zao zoipa.
Woyesa kukonza munthu wonyoza, amangonyozekerapo, wodzudzula munthu woipa, amangopwetekerapo. Wonyoza usamdzudzule, angadane nawe. Koma ukadzudzula munthu wanzeru, adzakukonda.
Munthu wa mtima wanzeru adzasamala malamulo, koma chitsiru chomangolongolola chidzaonongeka.
Pamene Paulo ankadziteteza ku zomnenezazo, Fesito adanena mokweza mau kuti, “Misalatu imeneyi, iwe Paulo! Kuphunziritsa kwako kukukupengetsa.”
Pamene Yesu ankapita ku Yerusalemu, adaŵatengera pambali ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja. Pa njira adaŵauza kuti, “Tilitu pa ulendo wopita ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Iwo akamuweruza ndi kugamula kuti aphedwe, ndipo akampereka kwa anthu akunja. Amenewo akamchita chipongwe, akamkwapula, nkumupachika pa mtanda; koma mkucha wake Iye adzauka kwa akufa.”
Yesu adatengera ophunzira ake pambali, naŵauza kuti, “Tilitu pa ulendo wopita ku Yerusalemu, ndipo zonse zidzachitika zimene aneneri adalemba zokhudza Mwana wa Munthu.
“Koma tsopano akundiyesa chinthu chochiseka, anthu amene ali ana kwa ine, anthu oti ndi atate ao omwe sindikadaŵayesa oyenera kuti athandizane ndi agalu kuŵeta nkhosa zanga.
Tsono anthu amene ankalonda Yesu aja adayamba kumseka ndi kumammenya. Adammanga nsalu m'maso nkumamufunsa kuti, “Lota, wakumenya ndani?” Ndipo adamnenanso mau ena ambiri achipongwe.
Wonyoza anzake amafunafuna nzeru osaipeza, koma munthu womvetsa amadziŵa bwino zinthu msanga.
Herode pamodzi ndi asilikali ake adayamba kumseka Yesu ndi kumamnyoza. Adamuveka chovala chachifumu, namubwezera kwa Pilato.
Nawonso akulu a ansembe ankamuseka, nkumauzana ndi aphunzitsi a Malamulo kuti, “Adapulumutsa anthu ena, koma akulephera kudzipulumutsa Iye yemwe! Uja ankati ndi Mpulumutsi wolonjezedwayu, Mfumu ya Aisraele, atatsikatu tsopano pamtandapa, kuti tiwone ndi kumkhulupirira!” Ndiponso amene adaŵapachika pamodzi naye aja ankamunyoza.
Anthu ena onse adaimirira pomwepo nkumaonerera. Komanso akulu a Ayuda ankamunyodola nkumanena kuti, “Adapulumutsa ena, adzipulumutse yekha ngati ndiyedi Mpulumutsi uja amene Mulungu adamsankha.”
Ukamenya munthu wonyoza anzake, adzachenjererapo. Ukadzudzula munthu womvetsa bwino zinthu, adzapindulapo nzeru.
Munthu wonyada ndi wodzikuza amamtchula “Mnyodoli,” chifukwa amachita zinthu modzitama ndi mwachipongwe.
Amene amalalatira mmphaŵi, amanyoza Mlengi wake. Amene amakondwerera tsoka la mnzake adzalangidwa.
Aliyense amene amaseka bambo ndi kumanyozera kumvera mai, makwangwala akuchigwa adzamkoloola maso, ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.
Mboni yachabe imanyoza chilungamo, pakamwa pa anthu oipa pamalikwira tchimo. Zakonzeka kale kuti mlandu uŵagwere anthu onyoza, mkwapulo ndi wokonzakonza kuti akwapulire pamsana pa zitsiru.
Kuseka kwa zitsiru kuli ngati kuthetheka kwa moto kunsi kwa mbiya. Zimenezinso nzachabechabe.
Koma ankhanza adzatheratu, oseka anzao adzazimirira, ndipo opendekera ku zoipa adzaonongedwa.
Tsono inu musanyozere mau ameneŵa. Mukatero, maunyolo anu adzakuthinani koposa. Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, andiwuza kuti, “Ndagamula kuti ndidzaononga dziko lonse.”
Paja adakuuzani kuti, “Pa masiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, otsata zilakolako zao zoipa.”
Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu,
“ ‘Mvetsani inu anthu onyoza, zizwani ndipo muwonongeke, pakuti pa nthaŵi ya moyo wanu Ine ndidzachita chinthu chimene simungakhulupirire konse, ngakhale wina akuuzeni.’ ”
Munthu woipa amachitira upo mnzake wabwino, namamtuzulira maso mwachidani. Koma Chauta amamseka munthu woipayo, poti amaona kuti tsiku lake la kuwonongeka likubwera.
Pamene ndidadzilanga posala zakudya, anthu adandinyoza. Pamene ndidavala chiguduli kuwonetsa chisoni, ndidasanduka chinthu choŵaseketsa. Anthu okhala pa chipata amandinena, ndipo zidakwa zimandiimba nyimbo.
Pa nthaŵi yaitali, anthu olemera akhala akutinyodola, anthu onyada akhala akutinyoza.
Ulemu woulandira chitsiru uli ngati chisanu chambee chomagwa nthaŵi yachilimwe, kapena mvula yomagwa nthaŵi yokolola.
Mkwapulo ndi wokwapulira kavalo, chitsulo ncha m'kamwa mwa bulu, chonchonso ndodo ndi yoyenerera zitsiru.
Chitsiru usamachiyankha potsata uchitsiru wake, kuwopa kuti ungafanefane nacho. Koma mwina uzichiyankha chitsiru potsata uchitsiru wake, kuwopa kuti chingamadziyese chanzeru.
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense wopsera mtima mbale wake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu. Aliyense wonena mnzake kuti, ‘Wopandapake iwe,’ adzayenera kuzengedwera ku Bwalo Lapamwamba. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru,’ adzayenera kukaponyedwa ku moto wa Gehena.
Adaluka nsangamutu yaminga naiika pamutu pake, ndipo adamgwiritsa ndodo m'dzanja lake lamanja. Kenaka adayamba kumgwadira, namaseŵera naye mwachipongwe nkumanena kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda.”
Yesu adayang'ana ophunzira ake amene adaamzungulira naŵauza kuti, “Nkwapatali kwambiri kwa anthu achuma kuti akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”
“Ndinu odala anthu akamadana nanu, akamakusalani ndi kukuchitani chipongwe, ndipo akamaipitsa dzina lanu chifukwa cha Ine Mwana wa Munthu.
Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai.
Tsono iwe, ukuweruziranji mbale wako? Kapena iwe winawe, ukunyozeranji mbale wako? Tonsefe tidzaima pamaso pa Mulungu kuti atiweruze.
Mau onena za imfa ya Khristu pa mtanda ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akutayika, koma kwa ife amene tili pa njira ya chipulumutso, mauwo ndi mphamvu ya Mulungu.
Ife ndife opusa chifukwa cha Khristu, koma inu ndinu anzeru mwa Khristu. Ife ndife ofooka, koma inu ndinu amphamvu. Inu mumalandira ulemu, koma ife timanyozedwa.
Tsono popeza kuti chimene timalalika ndi chakuti Khristu adauka kwa akufa, bwanji ena mwa inu akunena kuti, “Anthu akufa sadzaukanso?” Ngati akufa sadzauka, ndiye kuti Khristunso sadauke. Tsono ngati Khristu sadauke, kulalika kwathu nkwachabe, ndipo chikhulupiriro chanu nchachabenso.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo. Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.
M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.
Nthaŵi zonse mau anu akhale okoma, opindulitsa ena, kuti potero mudziŵe m'mene muyenera kuyankhira munthu aliyense.
Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso. Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu. Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu.
Abale, musamasinjirirana. Wosinjirira mbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo a Mulungu. Koma ukaweruza Malamulo a Mulungu, ndiye kuti sukuchita zimene Malamulowo akunena, ukudziyesa woweruza. Mulungu yekha ndiye wopanga Malamulo ndiponso woweruza. Ndiyenso wotha kupulumutsa ndi kuwononga. Nanga iwe ndiwe yani kuti uziweruza mnzako?
Amene amatuma chitsiru kukanena uthenga, amachita ngati kudzidula mapazi ndipo amadziitanira mavuto.
Amene amanka nachita ugogodi, amaulula zinsinsi. Nchifukwa chake usamagwirizane naye wolankhula zopusayo.
Inu mwatisandutsa anthu onyozeka kwa anzathu oyandikana nafe, anthu otizungulira amatiseka ndi kutinyodola. Inu mwatisandutsa anthu oŵanyodola pakati pa anthu a mitundu ina, anthu omangosekedwa pakati pa anzathu.
Akodwe ndi kunyada kwao, chifukwa cha uchimo wa m'kamwa mwao, ndi mau a pakamwa pao. Chifukwa chakuti amatemberera ndipo amanama,
Pamene ndidavala chiguduli kuwonetsa chisoni, ndidasanduka chinthu choŵaseketsa. Anthu okhala pa chipata amandinena, ndipo zidakwa zimandiimba nyimbo.
Anthu osasamala za Mulungu amandinyoza kwathunthu, komabe sindisiyana nawo malamulo anu.
Usamkonzekere chiwembu mnzako, amene amakhala nawe pafupi mokudalira. Khalidwe la kudzipereka ndi kukhulupirika zisakuthaŵe, makhalidwe ameneŵa uziyenda nawo ngati mkanda wam'khosi, uŵalembe mumtima mwako. Usamakangane ndi munthu popanda chifukwa pamene iyeyo sadakuchite choipa chilichonse.
Wofulumira kulankhula, zonena zake zimalasa ngati mpeni, koma mau a munthu wanzeru amachiza anzake.
Mau a chitsiru amautsa mkangano, ndipo pakamwa pake pamaitana mkwapulo. Pakamwa pa chitsiru ndipo pamabweretsa chiwonongeko chake. Mau ake ali ngati msampha wodzikolera mwiniwakeyo.
Usamakondwerera kugwa kwa mdani wako, mtima wako usamasangalala iyeyo akaphunthwa. Ukatero Chauta adzaziwona zimenezo nadzaipidwa nazo, kenaka adzaleka kumkwiyira mdani wakoyo.
Mau a pakamwa pa munthu wanzeru amakondweretsa, koma pakamwa pa chitsiru mpoononga. Chitsiru chimayamba ndi mau opusa, potsiriza zolankhula zake zimangokhala zamisala basi.
Tsoka kwa ufumu wonyada wa zidakwa za ku Efuremu! Tsoka kwa ulemerero wake umene wayamba kufota ngati duŵa, mzinda uja uli kumtunda kwa chigwa chachonde, umene amanyadira anthu oledzera vinyo. Akuyesa kumatiphunzitsa pang'onopang'ono lemba ndi lemba, mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro. Zonsezo akungoti apa pang'ono, apa pang'ono.” Ndithudi, Mulungu adzakuphunzitsani kudzera mwa anthu a chilankhulo chachilendo, anthu a chilankhulo chamtundu. Adaakuuzani kuti, “Malo opumulira ndi ano, otopa apumule, malo ousira ndi ano,” koma inu simudamvere. Nchifukwa chake Chauta adzakuphunzitsani pang'onopang'ono, lemba ndi lemba, mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro, kuti mudzakhumudwe poyenda. Mudzapweteka, mudzakodwa mu msampha, ndipo adzakutengani ku ukapolo. Tsopano mverani zimene Chauta akukuuzani, inu anthu achipongwe, amene mumalamulira anthu ake kuno ku Yerusalemu. Inu mumanena kuti “Ife tidachita chipangano ndi imfa, ndipo manda satiwopsa ai. Chiwonongeko chikamadzafika, sichidzatikhudza konse. Inu mumakhulupirira mabodza ngati kothaŵira, ndipo mumadalira kunama kuti kukhale kopulumukira.” Tsopano zimene akunena Ambuye Chauta nzakuti, “Ku Ziyoni ndikuika maziko a mwala wotsimikizika, mwala wapangodya wamtengowapatali wopanga maziko amphamvu. Pamwalapo palembedwa kuti, ‘Wokhulupirira sadzagwedezeka.’ Chilungamo ndicho chidzakhala ngati chingwe choyesera maziko ake, ndipo ungwiro udzakhala ngati choongolera chake. Koma matalala adzaononga mabodza amene mumaŵakhulupirira, ndipo chigumula chidzamiza malo anu opulumukirapo.” Chipangano chimene mudachita ndi imfa chidzatha, kotero kuti manda adzayamba kukuwopsani. Chiwonongeko chikamadzafika, chidzakugonjetsani. Nthaŵi iliyonse imene chizidzaoneka, chizidzakukanthani. Chizidzafika m'maŵa mulimonse, usana ndi usiku. Tsono anthu akadzamvetsa uthenga umenewu, adzaopsedwa kwambiri. Ambuye ali naye wina wamphamvu ndi wanyonga. Iyeyo adzabwera ngati mkuntho wamatalala ndi namondwe woononga, ngati chigumula chamadzi chokokolola zonse, ndipo adzaŵagwetsa pansi mwankhanza.
Ataseŵera naye mwachipongwe choncho, adamuvula chovala chija namuvekanso zovala zake. Kenaka adamtenga, nkupita naye kuti akampachike pa mtanda.
amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao.
mbala, aumbombo, zidakwa, augogodi, kapena achifwamba, ameneŵa sadzaulaŵa Ufumu wa Mulungu.
Koma ngati muyamba kulumana ndi kukadzulana, muchenjere kuti mungaonongane kotheratu.
Chimodzimodzinso lilime: ndi kachiwalo kakang'ono, komabe limadzitama kuti nkuchita zazikulu. Tangoganizani kukula kwake kwa nkhalango imene ingayatsidwe ndi kalilaŵi kakang'ono ka moto. Tsonotu lilime limatentha ngati moto. Chifukwa chokhala pakati pa ziwalo zathu limawanditsa zoipa m'thupi monse. Limaipitsa khalidwe lonse la munthu. Limayatsa moto moyo wathu wonse kuyambira pobadwa mpaka imfa; ndipo moto wake ngwochokera ku Gehena.
Zoonadi, munthu woipa amalingalira zoipa zokhazokha nthaŵi zonse, ntchito yake ndi kunyenga ndi kuvutitsa anthu ena basi.
Paja Iye amachitira chifundo anthu ozunzika, salephera kumva kulira kwao ndipo amalanga anthu oŵazunzawo.
Anthu oipa amasolola lupanga, ndipo amakoka mauta, kuti aphe anthu ovutika ndi osoŵa, amene amayenda molungama.
Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika, atchera ukonde wa zingwe, anditchera misampha m'mbali mwa njira.
Ndiye inenso ndidzakusekani, mukadzagwa m'mavuto, ndidzakunyodolani, mukadzazunguzika ndi mantha,
Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi, pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa.
Usamasamala zonse zokamba anthu, mwinamwina udzamva wantchito wako akukutukwana. Mumtima mwako ukudziŵa kuti iweyonso udatukwanapo anthu ena.
Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula. Mwakuti chifukwa cha mau ako omwe mlandu udzakukomera kapena kukuipira.”
Ndipo Iye adaŵauza kuti, “Inu mumadziwonetsa olungama pamaso pa anthu, koma Mulungu amaidziŵa mitima yanu. Pajatu zimene anthu amaziyesa zamtengowapatali, m'maso mwa Mulungu zimaoneka zonyansa.
Nchifukwa chake Mulungu adaŵasiya kuti azingochita zonyansa zimene mitima yao inkalakalaka, mpaka kunyazitsa matupi ao. Adasiya zoona za Mulungu namatsata zabodza. Adayamba kupembedza ndi kutumikira zolengedwa m'malo mwa kupembedza ndi kutumikira Mlengi mwini, amene ali woyenera kumlemekeza mpaka muyaya. Amen.
Popeza kuti ndinu anthu a Mulungu, ndiye kuti dama kapena zonyansa, kapena masiriro oipa zisatchulidwe nkomwe pakati panu. Amatero chifukwa Mpingowo ndi thupi lake, ndipo ife ndife ziwalo zake. Paja mau a Mulungu akuti, “Nchifukwa chake mwamuna adzasiye atate ndi amai ake, nkukaphatikizana ndi mkazi wake, kuti aŵiriwo asanduke thupi limodzi.” Mau ameneŵa akutiwululira chinsinsi chozama, ndipo ndikuti chinsinsicho nchokhudza Khristu ndi Mpingo. Komabe akunenanso za inu, kuti mwamuna aliyense azikonda mkazi wake monga momwe amadzikondera iye mwini, ndiponso kuti mkazi aliyense azilemekeza mwamuna wake. Ndiponso musamalankhule zolaula, zopusa, kapena zopandapake, koma muzilankhula zoyamika Mulungu.
Koma tsopano musachitenso zonsezi, monga kukalipa, kukwiya, kuipa mtima, ndi mijedu. Pakamwa panu pasamatulukenso mau otukwana kapena onyansa.
Munthu wotere ndi wodzitukumula ndi kunyada, sadziŵa kanthu. Mtima wake ngwodwala, wongofuna zotsutsanatsutsana ndi kukangana pa mau chabe. Zimenezi zimabweretsa kaduka, kusamvana, kusinjirirana, kuganizirana zoipa,
Koma amatikomera mtima koposa. Nchifukwa chake Malembo akuti, “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma odzichepetsa amaŵakomera mtima.”
Anthu okuchitani choipa, osaŵabwezera choipa, okuchitani chipongwe osaŵabwezera chipongwe. Koma inu muziŵadalitsa, pakuti inuyo Mulungu adakuitanirani mkhalidwe wotere, kuti mulandire madalitso ake.
Kodi nonsenu mudzaukira munthu mpaka liti, kuti mumgwetse pansi ngati khoma lopendekeka, ngati mpanda wogwedezeka?
Ndili ndi tsoka lalikulu, chifukwa ndimakhala pakati pa anthu onga mbuli za ku Meseki ndi Kedara. Ndakhala nthaŵi yaitali pakati pa anthu odana ndi mtendere. Ine ndimafuna mtendere, koma ndikalankhula za mtendere, iwo amafuna nkhondo.
Moto umazima pakasoŵa nkhuni, chonchonso kumene kulibe kazitape, kulibenso ndeu. Monga momwe aliri makala pa moto wonyeka ndiponso nkhuni pa moto woyaka, ndimonso amakhalira munthu wandeu poutsa mikangano. Mau a kazitape ali ngati zakudya zokoma, zimene zimatsikira m'mimba msanga.
Munthu wochenjera amachita zonse mwanzeru, koma wopusa amaonetsa poyera uchitsiru wake.
Onse onyada ndi onama olankhula mwamwano ndi monyoza kwa anthu abwino, muŵakhalitse chete.
“Mverani, inu amene mukudziŵa chilungamo, inu amene mukusunga malamulo anga mumtima mwanu. Musachite mantha anthu akamakudzudzulani, musataye mtima akamakulalatirani.
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu woipa osalimbana naye. Ngati munthu akumenya pa tsaya la ku dzanja lamanja, upereke linalonso.
Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.
Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse.
Tsono musadzinyenge. Ngati wina mwa inu adziyesa wanzeru, kunena za nzeru za masiku ano, ameneyo ayambe wakhala ngati wopusa, kuti asanduke wanzeru. Zoonadi nzeru za anthu odalira zapansipano, nzopusa pamaso pa Mulungu. Pajatu Malembo akuti, “Mulungu amakola anthu anzeru m'kuchenjera kwao.”
Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa. Nchifukwa chake tsono, nthaŵi zonse tikapeza mpata, tizichitira anthu onse zabwino, makamaka abale athu achikhristu. Onani malemba akuluakulu amene ndikulemba ndi dzanja langalanga tsopano. Onse amene afuna kuti akome pamaso pa anthu, akukukakamizani kuti muumbalidwe. Ali ndi cholinga chimodzi chokha, chakuti asazunzidwe chifukwa cha mtanda wa Khristu. Pakuti ngakhale iwo omwe amene amaumbalidwa satsata Malamulo, komabe amafuna kuti inu muumbalidwe, kuti athe kunyadira kuumbalidwa kwanuko. Koma ine sindinganyadire kanthu kena kalikonse, koma mtanda wa Ambuye athu Yesu Khristu basi. Popeza kuti Iye adafa pa mtanda, tsopano zapansipano kwa ine zili ngati zakufa, ndipo inenso kwa zapansipano, ndili ngati wopachikidwa. Kuumbalidwa si kanthu, kusaumbalidwa si kanthunso, chachikulu nchakuti Mulungu apatse munthu moyo watsopano. Mulungu aŵapatse mtendere, ndipo aŵachitire chifundo anthu a Mulungu onse amene amatsata njira imeneyi. Kuyambira tsopano asandivutenso munthu wina aliyense, pakuti zipsera zimene ine ndili nazo pa thupi langa, zikutsimikiza kuti ndine wakewake wa Yesu. Abale, Ambuye athu Yesu Khristu akudalitseni inu nonse. Amen. Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.
Pali golide ndi miyala yambirimbiri yamtengowapatali, koma mau olankhula zanzeru ali ndi mtengo woposa zonsezo.