Pali mavesi ena ovuta kumvetsa, koma ambiri m’Baibulo ndi osavuta. Ine ndaona kuti zonsezi ndi zoona: Baibulo ndi losavuta kumvetsa, koma nthawi zina pali zinthu zovuta… zimakhala zovutadi kupeza tanthauzo lake lenileni. Koma tati zikomo, 99% ya Mau a Mulungu ndi omveka… ndipo tiyenera kuwatsata. Baibulo limatiuza kuti Mau a Mulungu ndi omveka bwino kuti aliyense athe kuwamvetsa. Koma nthawi zina, timapeza mavesi ovuta kumvetsa. Ngakhale tili ndi mabuku ambiri otithandiza kumvetsa Baibulo, ngakhale akatswiri a maphunziro a zaumulungu amavomeleza kuti pali mavesi ena ovuta kumvetsa. Koma ndi chithandizo cha Mulungu, komanso maphunziro amene tingawapeze pa intaneti, tidzatha kumvetsa mavesi ovutawo. Mulungu adzatipatsa nzeru zomvetsa.
Palibe munthu amene adakwera kupita Kumwamba, koma Mwana wa Munthu ndiye adatsika kuchokera Kumwamba.
“Munthu wosauka uja adamwalira, angelo nkumunyamula, nakamtula m'manja mwa Abrahamu. Munthu wachuma uja nayenso adamwalira, naikidwa m'manda.
Amoyo amadziŵa kuti adzafa, koma akufa sadziŵa kanthu, ndipo alibe mphotho inanso yoonjezera. Palibe ndi mmodzi yemwe woŵakumbukira.
Pamenepo adanena mokweza mau kuti, ‘Atate Abrahamu, mundichitire chifundo. Tumani Lazaro aviike nsonga ya chala chake m'madzi kuti adzaziziritseko lilime langa, pakuti ndikuzunzika koopsa m'moto muno.’
Munthu wodalira nzeru zake zokha sangalandire zimene zimachokera kwa Mzimu wa Mulungu. Amaziyesa zopusa, ndipo sangathe kuzimvetsa, popeza kuti zimalira kukhala ndi Mzimu Woyera kuti munthu azimvetse.
Nthaŵi imeneyo anthu anali atayamba kuchuluka pa dziko lonse lapansi, ndipo adabereka ana aakazi. Anali ndi ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti. Koma anthu ena onse anali oipa pamaso pa Mulungu, ndipo kuipa kwao kudawanda ponseponse. Mulungu atayang'ana dziko lapansi, adaona kuti ndi lonyansa, chifukwa anthu onse anali oipa kwambiri. Choncho Mulungu adauza Nowa kuti, “Ndatsimikiza mu mtima kuti ndiwononge anthu onse. Ndidzaŵaononga kotheratu chifukwa dziko lonse lapansi ladzaza ndi ntchito zao zoipa. Udzipangire chombo ndipo uchipange ndi matabwa a mtengo wa mnjale. Upange zipinda m'menemo, ndipo uchimate phula kunja kwake ndi m'kati momwe. M'litali mwake mwa chombocho mukhale mamita 140. M'mimba mwake mukhale mamita 23, ndipo msinkhu wake ukhale wa mamita 13 ndi theka. Upange denga la chombocho, ndipo usiye mpata wa masentimita 50 pakati pa dengalo ndi mbali zake. Uchimange mosanjikiza, chikhale cha nyumba zitatu, ndipo m'mbali mwake mukhale chitseko. Ndidzagwetsa mvula yachigumula pa dziko lapansi, kuti iwononge zamoyo zonse. Zonse zapadziko zidzafa, koma iweyo ndidzachita nawe chipangano. Udzaloŵe m'chombomo iwe pamodzi ndi mkazi wako, ndi ana ako pamodzi ndi akazi ao. Ndipo udzatengenso nyama za mtundu uliwonse, yaimuna ndi yaikazi, kuti zisungidwe ndi moyo. Ana aamuna a Mulungu adaona kuti ana aakazi a anthu anali okongola, nayamba kukwatira amene ankaŵakonda. Mbalame za mtundu uliwonse ndi nyama zazikulu ndi zokwaŵa zomwe, zidzaloŵe m'chombo kuti zisungidwe ndi moyo. Udzatengenso zakudya za mtundu uliwonse kuti inu ndi nyamazo muzidzadya.” Motero Nowa adachitadi zonse zimene Mulungu adamlamula. Tsono Chauta adati, “Sindidzalola anthu kukhala ndi moyo mpaka muyaya, popeza kuti munthu ndi thupi limene limafa. Kuyambira tsopano adzangokhala zaka 120.” Pa masiku amenewo, ngakhale pambuyo pakenso, panali anthu amphamvu ataliatali pa dziko lapansi. Anthu ameneŵa ndi amene ankabadwa mwa akazi omwe adaakwatiwa ndi ana a Mulungu aja. Iwoŵa anali ngwazi zomveka ndiponso anthu otchuka pa masiku akalewo.
Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.
Panalibiretu wolamulira wa masiku ano wodziŵa zimenezi. Akadazidziŵa, sakadapachika Ambuye aulemerero pa mtanda.
Koma pakuti pa nyama zobzikula kapena za ziboda zogaŵikanazo, asadye izi: ngamira: imeneyi njonyansa kwa inu pa zachipembedzo, chifukwa ngakhale imabzikula, ziboda zake nzosagaŵikana. Ndipo munthu amene adyako nyamayo, achape zovala zake, komabe adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Nayenso amene anyamula nyama yakufayo, achape zovala zake, komabe adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. “Chinthu chilichonse chokwaŵa pansi nchonyansa, ndipo musadye. Chinthu chilichonse chokwaŵa ndi kumimba, ndiponso chilichonse cha miyendo inai kapena cha miyendo yambirimbiri, kungoti zonse zokwaŵa pansi, musadye poti nzonyansa kwa inu. Musadzisandutse oipitsidwa ndi chokwaŵa chilichonse, musadziipitse nazo, kuti mungasanduke oipitsidwa. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu. Tsono mudziyeretse, ndipo mukhale oyera pakuti Ine ndine woyera. Musadziipitse ndi chinthu chokwaŵa pansi chilichonse. Pakuti Ine ndine Chauta, amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito kuti ndikhale Mulungu wanu. Tsono mukhale oyera, pakuti Ine ndine woyera.” Limeneli ndilo lamulo lonena za nyama, mbalame, chamoyo chilichonse choyenda m'madzi, ndi chinthu chilichonse chokwaŵa pansi, kuti muzisiyanitsa pakati pa zonyansa ndi zosanyansa, ndiponso pakati pa zamoyo zimene mungathe kudya ndi zimene simuyenera kudya. Mbira: imeneyi njonyansa kwa inu, chifukwa ngakhale imabzikula, ziboda zake nzosagaŵikana. Kalulu: ameneyu ndi wonyansa kwa inu, chifukwa ngakhale amabzikula, ziboda zake nzosagaŵikana. Nkhumba: imeneyi njonyansa kwa inu, chifukwa ngakhale ziboda zake nzogaŵikana ndipo mapazi ake ngogaŵikananso, koma siibzikula. Nyama ya zoŵeta zimenezo musamadye, ndipo zikafa musazikhudze. Zimenezi nzonyansa kwa inu.’
Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Upange njoka yamkuŵa, ndipo uipachike pa mtengo. Aliyense wolumidwa akangoiyang'ana njokayo, adzakhala moyo.” Choncho Mose adapanga njoka yamkuŵa, naipachika pa mtengo. Ndiye ankati wina aliyense njoka ikamuluma, munthuyo akayang'ana njoka yamkuŵa ija, ankakhala moyo.
Komatu mukapanda kumvera bwino mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero lino, adzakugwerani matemberero aŵa: Chauta adzatemberera mizinda yanu ndi minda yanu. Chauta adzatemberera zokolola zanu ndiponso zokandiramo ufa wanu. Chauta adzakutembererani pokupatsani ana oŵerengeka, zokolola zochepa, ndiponso ng'ombe ndi zoŵeta zina pang'ono chabe. Chauta adzatemberera ntchito zanu zonse. Mverani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalandira madalitso onse aŵa: Mukamachita zoipa ndi kumkana Mulungu, Iye adzakutumizirani matemberero, chisokonezo ndiponso zokuvutani pa ntchito zanu zonse, mpaka mutaonongeka ndi kufa nonsenu pa kamphindi kochepa. Adzakutumizirani matenda otsatanatsatana, mpaka mutatha nonse kuti psiti m'dziko limene muli kukakhalamolo. Chauta adzakukanthani ndi nthenda zopatsana, zotupatupa ndi zamalungo. Adzakutumiziraninso kutentha koopsa ndi chilala ndiponso chinsikwi ndi chinoni zoononga mbeu zanu. Masoka amenewo adzakhala pa inu mpaka kukufetsani. Mvula sidzakugwerani ndipo nthaka yanu idzauma kuti gwa ngati chitsulo. M'malo mwa mvula, Chauta adzakugwetserani fumbi ndi mchenga, mpaka mutaonongeka nonse. Chauta adzalola kuti adani anu akugonjetseni. Pokalimbana nawo mudzadzera njira imodzi, koma poŵathaŵa mudzapanga zikuŵa zisanu ndi ziŵiri. Ndipo mafumu onse a pa dziko lapansi adzaopsedwa poona zokuchitikiranizo. Mutafa, mbalame pamodzi ndi nyama zakuthengo zidzadya mitembo yanu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzazipirikitse. Chauta adzakulangani ndi zithupsa zonga za ku Ejipito zija. Mudzakhala ndi zilonda, mphere, ndi kunyerenyesa, zonsezo zosamva mankhwala. Thupi lanu lidzakhala la mphere zokhazokha, ndipo muzidzangokandakanda, koma osachira. Chauta adzakuchititsani misala, ndipo adzakusandutsani akhungu ndi osokonezeka. Ngakhale dzuŵa lili nye, muzidzachita kufufuza njira ngati anthu akhungu. Kalikonse kamene mudzachite simudzalemera nako. Kaŵirikaŵiri azidzakupsinjani ndi kumakuberani, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzakuthandizeni. Chauta adzadalitsa mizinda yanu ndi minda yanu. Mudzafunsira mbeta mtsikana, koma ndi wina amene adzakwatirane naye. Kumanga nyumba mudzamanga ndithu, koma simudzagonamo. Munda wamphesa mudzabzala, koma mphesa zake simudzadyako. Ng'ombe zanu azidzakupherani mukupenya, koma nyama yake simudzadyako. Abulu anu azikaŵalanda mwamphamvu ndi kupita nawo kwina, inu mukupenya, ndipo sadzakubwezerani. Nkhosa zanu adzazipereka kwa adani anu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzakuthandizeni. Ana anu aamuna ndi aakazi adzatengedwa ukapolo ndi alendo, inu mukupenya. Tsiku ndi tsiku maso anu adzakhala ali psuu kuyang'anira ngati ana anuwo abwere, koma simudzaphulapo kanthu. Mtundu wachilendo udzakulandani zakumunda zanu zonse zimene mudathyoka nazo msana polima, ndipo mudzapsinjidwa ndi kuzunzika mosalekeza. Zimene mudzaziwona ndi maso zidzakupengetsani. Chauta adzabweretsa zilonda zoŵaŵa ndi zosachizika pa maondo ndi pamisongolo panu, ndipo anamkalimbwi azidzakutulukani thupi lonse, kuyambira kuphazi mpaka kumutu. Chauta adzaipirikitsira ku dziko lachilendo mfumu yanu, pamodzi ndi inu nomwe, kumene inuyo ndi makolo anu simudakhaleko nkale lonse. Kumeneko muzikatumikira milungu ina yopanga ndi mitengo ndi miyala. Ku mitundu yonse kumene Chauta adzakumwazireniko, anthu adzadabwa nanu, adzakusekani, adzakupekani nthano yokunyodolani. Mudzabzala zambiri, koma mudzakolola pang'ono chabe, chifukwa dzombe lidzadya zolima zanuzo. Minda yamphesa mudzalimadi, mpaka kuisamala bwino, koma mphesa zake simudzathyola kapena kumwako vinyo wake, chifukwa tizilombo ndito tidzadye mphesazo. Chauta adzadalitsa ana anu ndi zokolola zanu, ndi ana a zoŵeta zanu, ndipo adzakupatsani ng'ombe ndi zoŵeta zina zambiri. Mitengo ya olivi izidzamera paliponse m'dziko mwanumo, koma mafuta a olivi simudzakhala nawo, chifukwa zipatso za olivizo zidzayoyoka. Mudzabereka ana aamuna ndi aakazi ndithu, koma sadzakhala anu, chifukwa adzatengedwa ukapolo. Mitengo yanu yonse ndi dzinthu dzanu dzam'munda zidzatha ndi tizilombo. Alendo okhala m'dziko mwanu ndiwo amene azidzakwererakwerera, koma inu muzidzatsikiratsikira. Iwowo azidzakukongozani ndalama, koma inu simudzakhala nazo ndi pang'ono pomwe zoŵakongoza, ndipo potsiriza adzakulamulirani. Masoka onseŵa adzakugwerani. Adzakhala pa inu mpaka mutaonongeka, chifukwa choti simudamvere Chauta, Mulungu wanu, ndipo simudatsate malamulo ndi malangizo onse amene Iye adakupatsani. Masoka onseŵa adzakhala mboni yapadera ya chilango cha Mulungu pa inu ndi pa zidzukulu zanu mpaka muyaya. Paja Chauta adakudalitsani pa zonse, komabe inu simudamtumikire mokondwa ndi mitima yachimwemwe. Motero mudzatumikira adani odzalimbana nanu amene Chauta adzakutumizireni. Mudzamva njala ndi ludzu. Zinthu zonse zidzakusoŵani pamodzi ndi zovala zomwe. Chauta adzakuzunzani mwankhanza, mpaka mutaonongeka. Chauta adzaitanitsa mtundu wa anthu ochokera ku malekezero a dziko lapansi, kuti adzamenyane nanu. Anthu a mtundu umenewo amene inu simudziŵa chilankhulo chao, adzakuterani ngati mphungu. Chauta adzadalitsa mbeu zanu ndi chakudya chimene muchikonza kuchokera ku mbeuzo, kuti zichuluke. Anthuwo adzakhala aukali, ndipo sadzachita chifundo ndi aliyense, ngakhale akhale mwana kapena nkhalamba. Adzakudyerani ng'ombe zanu pamodzi ndi zakumunda zanu zomwe, mpaka mudzafa ndi njala. Sadzakusiyiraniko mpang'ono pomwe tirigu, vinyo, mafuta aolivi, ng'ombe kapena nkhosa, ndipo mudzafadi. Adzathira nkhondo mzinda uliwonse, m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo. Ndipo malinga ataliatali amene mukuŵakhulupirirawo adzagwa ponseponse. Adzakuzingani m'mizinda yonse ya m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsanilo. Nthaŵi imene adani anu adzazinga mizinda yanu ndi kukusautsani koopsa, mudzasoŵa chakudya kotheratu, kotero kuti muzidzadya ana anu omwe aamuna ndi aakazi, amene Chauta adakupatsani. Ngakhale munthu amene ali woleredwa bwino ndi wofatsa mtima kwambiri mwa inu, adzamana chakudya mbale wake, mkazi wake wapamtima ndi ana ake omutsalira, mwakuti sadzapatsako ndi mmodzi yemwe nyama ya ana ake amene akuŵadya, chifukwa adzakhala alibiretu chakudya pa nthaŵi imene adani anu azidzakuzingani ndi kukusautsani koopsa. Ngakhale mkazi woleredwa bwino ndi wolobodoka kotero kuti sangayese nkomwe kupondetsa pansi phazi lake, adzamana mwamuna wake wapamtima ndi ana ake onse nyama ya ana ake ongobadwa kumene, pamodzi ndi za matenda ake zomwe zochokera m'mimba mwake, popeza kuti azidzadya zimenezi yekha mobisa, chifukwa cha kusoŵeratu chakudya, nthaŵi imene adani anu adzazinga mizinda yanu ndi kukusautsani kwambiri. Muzimvera mau onse a malamulo aŵa a m'buku muno, ndipo dzina ili lodabwitsa ndi lochititsa mantha la Chauta, Mulungu wanu, muzilitamanda. Mukapanda kutero, inuyo ndi zidzukulu zanu, Chauta adzakugwetserani masautso apadera, mavuto aakulu okhalitsa ndiponso nthenda zoopsa zosamva mankhwala. Chauta adzadalitsa zochita zanu zonse. Nthenda zonse zoopsa zimene mudaopsedwa nazo muli ku Ejipito kuja, Chauta adzakugwetserani zimenezo, ndipo simudzachira. Adzakugwetseraninso nthenda zonse zamitundumitundu pamodzi ndi miliri yomwe, zimene sizidatchulidwepo m'buku la malamulo a Mulungu, ndipo mudzaonongeka. Ngakhale mudaachuluka ngati nyenyezi zakuthambo, koma amoyo mudzakhala ochepa, chifukwa choti simudamvere Chauta, Mulungu wanu. Monga momwe kudakomera Chauta kukudalitsani ndi kukuchulukitsani kuti mukhale ambiri, momwemo kudzamkomeranso kuti akuwonongeni kotheratu. Adzakuchotsani m'dziko limene mukuliloŵa kukakhalamolo. Ndipo Chauta adzakumwazani pakati pa mitundu yonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko mpaka ku malekezero ake enanso. Kumeneko muzidzapembedza milungu yamitengo ndi yamiyala, imene inu ndi makolo anu simudaidziŵe nkale lonse. Simudzapeza mtendere kwina kulikonse ndipo malo anuanu simudzaŵapeza. Mudzakhala ankhaŵa, osoŵa thandizo ndi otaya mtima, ndipo Chauta ndiye adzagwetse zimenezi pa inu. Nthaŵi zonse, moyo wanu udzakhala wopenekapeneka. Muzidzakhala amantha, usiku ndi masana womwe, ndipo muzidzangokhalira kuwopa imfa. Mitima yanu idzakhala yamantha poona kalikonse. M'maŵa mulimonse muzidzangofuna kuti kude. Madzulo aliwonse muzidzafuna kuti kuche. Ndipo Chauta adzakutumizaninso ku Ejipito m'zombo zapanyanja, ngakhale kuti ndidaalonjeza kuti simudzapitakonso. Kumeneko mudzayesayesa kudzigulitsa ngati akapolo kwa adani anu, koma palibe ndi mmodzi yemwe amene adzafune kukugulani.
Yesu adaŵayankha kuti, “Mukulakwa chifukwa simudziŵa Malembo, ngakhalenso mphamvu za Mulungu.
Yesu adaŵayankha kuti, “Si pamenepa nanga pomwe mumalakwira, chifukwa chosadziŵa Malembo ndiponso mphamvu za Mulungu?
Yefita adalumbira kwa Chauta kuti, “Mukandithandiza kugonjetsa Aamoniŵa, aliyense amene atuluke pakhomo pa nyumba yanga kudzandichingamira pobwerera, nditagonjetsa Aamoniwo, adzakhala wake wa Chauta ndipo ndidzampereka kuti akhale nsembe yopsereza.”
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Ndidzalanga Aamaleke chifukwa cha kumenyana ndi Aisraele pa njira, pamene Aisraelewo ankachokera ku Ejipito. Saulo adayankha kuti, “Iyai, inetu mau a Chauta ndidatsata, ndipo ndidapitadi kukachita zimene Chauta adandituma. Ndidagwira Agagi mfumu ya Aamaleke, ndipo ndidapha Aamaleke onse. Koma pa zofunkha anthu adatengako nkhosa ndi ng'ombe, ndi zina zabwino kwambiri, zimene zinkayenera kuwonongedwa, kuti akazipereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wanu, ku Giligala.” Koma Samuele adati, “Kodi Chauta amakondwa ndi chiti: nsembe zopsereza ndi nsembe zina, kapena kumvera mau ake? Ndithu, ndi kumvera ndi kupereka nsembe kwabwino kwambiri nkumvera. Ndi kutchera khutu ndi kupereka mafuta ankhosa kwabwino kwambiri nkutchera khutu. Kugalukira kuli ngati tchimo loombeza, kukhala wokanika kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu.” Pamenepo Saulo adauza Samuele kuti, “Ndachimwa, ndalakwira lamulo la Chauta ndiponso malangizo anu, chifukwa chakuti ndinkaopa anthu ndipo ndinkamvera mau ao. Nchifukwa chake tsono pepani, ndagwira mwendo, mundikhululukire tchimo langa, ndipo mubwerere nane pamodzi, kuti ndikampembedze Chauta.” Koma Samuele adayankha kuti, “Sindibwerera nanu, popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu yolamulira Aisraele.” Pamene Samuele ankatembenuka kuti azipita, Saulo adagwira mpendero wa mkanjo wake, ndipo mkanjowo udang'ambika. Apo Samuele adamuuza kuti, “Chauta wachita ngati kung'amba ufumu wa Israele kuchoka kwa inu lero, ndipo waupereka kwa mnzanu wabwino koposa inuyo. Mulungu Waulemerero wa Aisraele sanama kapena kusintha maganizo. Pakuti Iye si munthu, kuti athe kusintha maganizo.” Pitani tsono, mukaŵathire nkhondo Aamalekewo, mukaononge kwathunthu zinthu zao zonse. Musakasiyeko munthu ndi mmodzi yemwe, mukaphe amuna, akazi, ana ndi makanda omwe. Mukaphenso ng'ombe, nkhosa, ngamira ndi abulu onse.’ ”
Ndipo atafika pa malo opunthirapo tirigu ku Nakoni, ng'ombe zidaafuna kugwa, ndiye Uza nkutambalitsa dzanja kuti agwirire Bokosi la Mulungu lija, naligwiradi. Pamenepo Chauta adampsera mtima Uzayo, chifukwa sadasunge mwambo, ndipo Mulungu adamkantha, nafera pomwepo pafupi ndi Bokosi la Mulungulo.
Yesu adamuyankha kuti, “Zimene ndikuchitazi, sukuzidziŵa tsopano, koma udzazidziŵa m'tsogolo muno.”
Tsono iwowo akuyendabe ndi kumakamba, adangoona galeta lamoto ndi akavalo ake amoto zikuŵasiyanitsa aŵiriwo. Ndipo Eliya adakwera kumwamba m'kamvulumvulu.
Adzakhala wodala munthu amene adzatenga makanda ako ndi kuŵakankhanthitsa ku thanthwe.
Iye ankaganiza kuti abale ake adzazindikira kuti Mulungu adamuika kuti adzaŵapulumutse, koma iwo sadazindikire.
Chitsiru usamachiyankha potsata uchitsiru wake, kuwopa kuti ungafanefane nacho. Koma mwina uzichiyankha chitsiru potsata uchitsiru wake, kuwopa kuti chingamadziyese chanzeru.
Zimene zimachitikira anthu, zomwezonso zimachitikira nyama. Monga chinacho chimafa, chinacho chimafanso. Zonsezo zimapuma mpweya umodzimodzi, munthu saposa nyama. Zonsezi nzopandapake. pali nthaŵi yobadwa ndi nthaŵi yomwalira, pali nthaŵi yobzala ndi nthaŵi yozula zobzalazo. Zonse zimapita kumodzimodzi. Zonsezo nzochokera ku dothi, ndipo zimabwerera kudothi komweko.
Chaka chimene mfumu Uziya adamwalira, ndidaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu wautali ndi wokwezedwa. Mkanjo wao unali wautali kwambiri, kotero kuti udadzaza Nyumba yao yonse. Tsono anthu ameneŵa uŵaphe mtima, uŵagonthetse makutu, ndipo uŵatseke m'maso, kuti angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angamvetse ndi mitima yao, kenaka nkutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa.”
Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.
Mphamvu ya Chauta idandigwira, Mzimu wa Chauta udandinyamula nkukandikhazika pakati pa chigwa. Chigwacho chinali chodzaza ndi mafupa. Motero ndidayamba kulalika monga adandilamulira. Tsono mpweya udaloŵa mwa iwo, ndipo akufa aja adakhala ndi moyo, naimirira. Linali gulu lalikulu kwambiri la ankhondo. Kenaka Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, mafupa ameneŵa ndi Aisraele onse. Iwo amanena kuti, ‘Mafupa athu ndi ouma, chiyembekezo chathu chidataika, taonongekeratu.’ Nchifukwa chake uŵalalikire ndi kuŵauza kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Inu anthu anga, ndidzafukula manda anu, ndipo ndidzakutulutsanimo. Ndidzakubwezerani ku dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzafukula manda anu ndi kukutulutsanimo, inu anthu anga. Tsono ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo, pambuyo pake ndidzakukhazikani m'dziko lanu. Choncho mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndalankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi. Ndikutero Ine Chauta.”
Pamene Chauta adalankhula koyamba kudzera mwa Hoseya, adamuuza kuti, “Pita kakwatire mkazi wachiwerewere ndipo ubale naye ana omwe adzakhalenso achiwerewere. Pakuti anthu a m'dziko muno akhala osakhulupirika, pakusiya Ine Chauta.” Motero Hoseya adapita, nakakwatira mkazi, dzina lake Gomeri, mwana wa Dibulaimu. Mkaziyo adatenga pathupi, namubalira mwana wamwamuna.
Kodi lipenga lankhondo nkulira mu mzinda, anthu osachita mantha? Nanga tsoka likagwera mzinda, kodi si Chauta amene amachita zimenezo?
Iyai, Chauta adakuwonetsa kale, munthu iwe, chimene chili chabwino. Zimene akufuna kuti uzichita ndi izi: uzichita zolungama, uzikhala wachifundo, ndipo uziyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Lupanga iwe, dzambatuka, ukanthe mbusa wanga. Ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine. Ndikutero Chauta Wamphamvuzonse. Kantha mbusa kuti nkhosa zimwazikane. Pamenepo ndidzakantha ndi anthu wamba omwe.” Chauta Wamphamvuzonse akuti, “Mwa zigawo zitatu za anthu m'dziko monsemo ziŵiri zidzaphedwa, chidzangokhalako chigawo chimodzi chokha chamoyo. Anthu a m'chigawo chachitatuchi ndidzaŵaika pa moto, ndidzaŵayeretsa monga m'mene amayeretsera siliva. Ndidzaŵayesa monga m'mene amayesera golide. Tsono adzatama dzina langa mopemba, Ine mwiniwake nkuŵayankha. Ndidzanena kuti, ‘Ameneŵa ndi anthu anga.’ Iwowo adzati, ‘Chauta ndi Mulungu wathu.’ ”
Ngati diso lako la ku dzanja lamanja likuchimwitsa, likolowole nkulitaya. Ndi bwino koposa kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kusiyana nkuti thupi lako lonse aliponye ku Gehena. “Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, lidule nkulitaya. Ndi bwino kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kupambana kuti thupi lako lonse likaponyedwe ku Gehena.”
“Kodi mukuyesa kuti ndidadzapereka mtendere pansi pano? Sindidadzapereke mtendere ai, koma nkhondo. Inetu paja ndidadzalekanitsa mwana wamwamuna ndi bambo wake, mwana wamkazi ndi mai wake, mkazi ndi apongozi ake aakazi, mwakuti adani a munthu adzakhala a m'banja mwake omwe.
“Tsono ngati dzanja lako kapena phazi lako likuchimwitsa, lidule ndi kulitaya. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo uli woduka dzanja kapena phazi, kupambana kuti ukaponyedwe ku moto wosatha uli ndi manja onse kapena mapazi onse aŵiri. Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole ndi kulitaya. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo uli ndi diso limodzi lokha, kupambana kuti ukaponyedwe ku moto wa Gehena uli ndi maso aŵiri.”
Ndipo ndikunenetsanso kuti nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”
Tsono nthaŵi ili ngati 3 koloko, Yesu adafuula kwakukulu kuti, “Eli, Eli, lama sabakatani?” Ndiye kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?”
Iye adaŵayankha kuti, “Inuyo Mulungu adakuululirani zobisika zokhudza Ufumu wake. Koma enaŵa amene ali kunja, zonse amazimvera m'mafanizo chabe, kuti choncho, monga mau a Mulungu aja amanena, “ ‘Kuyang'ana ayang'ane ndithu, koma asapenye kanthu, ndipo kumva amve ndithu, koma asamvetse kanthu, kuti angatembenuke mtima, ndipo Mulungu angaŵakhululukire.’ ”
“Aliyense wofuna kukhala wophunzira wanga, azikonda Ine koposa atate ake ndi amai ake, mkazi wake ndi ana ake, abale ake ndi alongo ake, ndiponso koposa ngakhale moyo wake womwe.
“Simoni, Simoni, chenjera! Mulungu walola Satana kuti akupeteni nonse ngati tirigu. Koma Ine ndakupempherera, kuti usaleke kundikhulupirira. Ndipo iweyo utatembenuka mtima, ukaŵalimbitse abale akoŵa.”
Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati simudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu. Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga, ali ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. Pakuti thupi langa ndi chakudya chenicheni, ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga amakhala mwa Ine, ndipo Ine ndimakhala mwa iyeyo. Monga Atate amoyo adandituma, ndipo Ine ndili ndi moyo pokhala mwa Iwo, momwemonso aliyense wodya Ine, adzakhala ndi moyo pokhala mwa Ine. Chakudya chimene chidatsika kuchokera Kumwamba nchimenechi. Nchosiyana ndi mana aja amene makolo anu ankadya koma nkufabe. Wodya chakudya chimenechi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya.”
Munthu winanso, dzina lake Ananiya, pamodzi ndi mkazi wake Safira, adagulitsa munda wao. Pomwepo adagwa pansi ku mapazi a Petro, naafa. Pamene achinyamata aja adaloŵa, adampeza atafa kale. Adamnyamula nakamuika pafupi ndi mwamuna wake. Ndipo mpingo wonse ndi anthu onse amene adamva zimenezi, adagwidwa ndi mantha aakulu.
Koma Mulungu adasankha zimene anthu amaziyesa zopusa, kuti Iye anyazitse nazo anthu anzeru. Adasankhanso zimene anthu amaziyesa zofooka, kuti Iye anyazitse nazo anthu amphamvu. Ndipo zimene anthu amaziyesa zachabe, zonyozeka ndi zosakhala zenizeni, Mulungu adazisankha kuti athetse mphamvu zinthu zimene iwowo amayesa kuti ndiye zenizeni. Mulungu adachita zimenezi kuti pasakhale wina aliyense woti nkumadzitukumula pamaso pake.
Pakuti amene adya mkate umenewu ndi kumwa chikho chimenechi, koma osalizindikira thupi la Ambuye, akudziitanira chilango pamene akudya ndi kumwa.
Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.
Paja Iye adakupatsani mwai, osati wakungokhulupirira Khristu ai, komanso wakumva zoŵaŵa chifukwa cha Iye.
Wina aliyense asakuletseni kupata mphothoyo. Iwo aja amakonda kudziwonetsa ngati odzichepetsa, popembedza amatamanda angelo. Amaika mtima pa zimene akuti adaziwona m'masomphenya. Amadzitukumula popanda chifukwa, popeza kuti amangotsata nzeru za anthu, osakangamira Khristu amene ali mutu wa Mpingo. Komatu mwa Khristu thupi lonse limalandira mphamvu, ndi kulumikizika pamodzi mwa mfundo zake ndi mitsempha yake. Motero thupi limakula monga momwe Mulungu afuna kuti likulire.
koma zonse muziziyesa bwino, kuti muwonetsetse ngati nzoona. Musunge zimene zili zabwino,
Koma mkazi adzapulumukabe kudzera m'kubala ana, malinga akalimbikira modzichepetsa m'chikhulupiriro, m'chikondi ndi m'kuyera mtima.
Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama.
Anthu amene adataya chikhulupiriro chao, nkosatheka kuŵatsitsimutsa kuti atembenuke mtima. Iwowo kale Mulungu adaaŵaunikira, adaalaŵako mphatso yochokera Kumwamba, nkulandira nao Mzimu Woyera. Ndipo adazindikira kukoma kwa mau a Mulungu, ndi mphamvu za nthaŵi imene inalikudzafika. Tsono akamkana Mulungu tsopano, akuchita ngati kumpachika iwo omwe Mwana wa Mulungu, ndi kumnyozetsa poyera.
Mukuwonatu kuti zochita zake za munthu ndizo zimamsandutsa wolungama pamaso pa Mulungu, osati chikhulupiriro chokha.
Ndipo ali ngati mzimu choncho, adapita kukalalika kwa mizimu imene inali m'ndende. popeza kuti adzadziwonera okha makhalidwe anu aulemu ndi angwiro. Mizimuyi ndi ya anthu amene kale lija sadamvere pamene Mulungu adaadikira moleza mtima, pa nthaŵi imene Nowa ankapanga chombo. M'chombomo anthu oŵerengeka okha, asanu ndi atatu, adapulumuka ndi madzi.
Wina akaona mbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere, ndipo Mulungu adzampatsa moyo mbale wakeyo. Ndikunenatu za ochita tchimo losadzetsa imfa. Koma lilipo tchimo lina lodzetsa imfa, za tchimo limenelo sindikunena kuti apemphere ai.
Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Sindinu ozizira, sindinunso otentha. Bwenzi zili bwino mukadakhala ozizira kapena otentha. Koma popeza kuti ndinu ofunda chabe, osati otentha kapena ozizira, ndidzakusanzani.
Onse okhala pa dziko lapansi adzachipembedza, ndiye kuti aliyense amene, chilengedwere dziko lapansi, dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo la Mwanawankhosa adaphedwa uja.
Amaonetsa chikondi chake kwa anthu zikwi zambirimbiri, ndipo amaŵakhululukira mphulupulu zao, zoipa zao, ndi machimo ao. Koma sadzalekerera ochimwa, ndipo adzalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha zoipa za atate ao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai.”
‘Chauta ndi wosakwiya msanga, ndi wodzaza ndi chifundo chosasinthika, ndi wokhululukira ochimwa ndi opalamula. Koma sadzaleka kulanga ochimwa, amalanga ana a mbadwo wachitatu ndi wachinai chifukwa cha kuchimwa kwa makolo ao.’
Tiyese kuti wina ali ndi mwana wokanika ndiponso wachipongwe, mwana woti bambo ndi mai ake saŵamvera konse, ngakhale amlange chotani. Makolo ake a mwanayo amgwire ndi kupita naye kwa akuluakulu amumzinda ku chipata cha mzindawo. Akuluakulu anu ndi aweruzi anu apiteko, ndipo akayese kutalika kwake kuchokera pamalo pamene pali munthu wakufayo mpaka ku mizinda yoyandikana ndi malowo. Makolowo auze akuluakuluwo kuti, “Mwana wathu ndi wokanika ndipo ndi wachipongwe safuna kutimvera, ndi wadyera ndiponso chidakwa. Pamenepo anthu amumzindawo amuphe pakumponya miyala, motero mudzachotsa choipa pakati panu. Anthu onse a mu Israele muno akadzamva zimene zachitikazi, adzakhala ndi mantha.”
Koma anthuwo sadafune kumumvera. Choncho mlendo uja adagwira mzikazi wake uja namtulutsira kunali iwoko, iwowo nkugona naye, nachita naye zoipa usiku wonse mpaka m'maŵa. M'bandakucha adamlola kuti apite. Ndipo m'maŵa kulikucha, mkaziyo adabwera nagwa pansi pakhomo pa nyumba ya munthu uja m'mene munali mwamuna wake muja. Adakhala pamenepo ali thasa mpaka kudayera. Mwamuna wakeyo adadzuka m'maŵa, ndipo atatsekula zitseko za nyumba kuti azipita, anangoona mzikazi wake uja ali thasa pakhomo pa nyumba, manja ake ali pa chiwundo. Adamuuza kuti, “Dzuka tizipita.” Koma mkaziyo sadayankhe kanthu. Tsono adamkweza pabulu, ndipo mlendoyo adanyamuka kupita kwao. Ataloŵa m'nyumba mwake, adatenga mpeni, naduladula thupi la mkaziyo m'nthuli khumi ndi ziŵiri. Ndipo adazitumiza m'dziko lonse la Israele. Tsono mwamuna wake adanyamuka namtsatira kuti akakambe naye mofatsa, kumpempha kuti abwerere. Mwamunayo anali ndi mtumiki wake ndi abulu ake aŵiri. Ndipo adafika ku nyumba ya bambo wake wa mkaziyo. Tsono mkaziyo adamloŵetsa m'nyumba ndipo bambo wake adamlandira ndi manja aŵiri. Onse amene adaona zimenezi ankati, “Zoterezi sizinachitikepo kuyambira nthaŵi imene Aisraele adatuluka m'dziko la Ejipito mpaka lero lino. Tiziganize bwino ndipo tipangane ndi kuchitapo kanthu.”
Zidangochitika kuti tsiku lina chakumadzulo, Davide adadzuka pabedi pake, namayenda pamwamba pa denga la nyumba yake yaufumu. Ali padengapo, adaona mkazi wina akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwabasi. tsono ngati mfumu ikapse mtima, nikakufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mudapita kufupi ndi mzinda kuti mukamenye nkhondo? Kodi simunkadziŵa kuti adzakulasani kuchokera m'kati mwa linga? Kodi Abimeleki mwana wa Gideoni adamupha ndani? Kodi adamupha si mkazi, pomkunkhunizira mwalawamphero kuchokera pa linga, kotero kuti adafera ku Tebezi? Chifukwa chiyani mudakafika pafupi ndi khoma?’ Pamenepo iweyo ukanene kuti, ‘Wankhondo wanu, Uriya Muhiti uja, nayenso adaphedwa.’ ” Wamthenga uja adapita, nakafika kwa Davide, nakamuuza zonse zimene Yowabu adamuuza kuti akanene. Adauza Davide kuti, “Adani athu adaatipambana, ndipo adaatuluka kukalimbana nafe ku thengo. Koma ife tidaŵabweza mpaka ku khomo lakuchipata. Tsono anthu oponya mivi ankalasa ankhondo anu kuchokera m'linga. Ndipo ankhondo ena mwa ankhondo a inu mfumu adaphedwa. Wankhondo wanu uja, Uriya Muhiti, nayenso adaphedwa.” Apo Davide adauza wamthenga uja kuti, “Kamuuze Yowabu kuti, ‘Zimenezi usavutike nazo, poti wakufa sadziŵika. Ulimbike polimbana ndi mzindawo, ndi kuugonjetsa.’ Choncho ukamlimbitse mtima Yowabuyo.” Pamene mkazi wa Uriya adamva kuti mwamuna wake Uriya adaphedwa, adalira, kulira mwamuna wake. Mkaziyo atatha kulira malirowo, Davide adatuma munthu nakamtenga, nkubwera naye kunyumba kwa mfumu, ndipo Davide adamukwatira. Mkaziyo adambalira mwana wamwamuna. Koma zimene adachita Davidezi zidaipira Chauta. Pomwepo Davide adatuma munthu kuti akafunsitse za mkaziyo. Ndipo munthuyo adamuuza kuti, “Mkazi ujatu ndi Bateseba, mwana wa Eliyamu, mwamuna wake ndi Uriya Muhiti.” Apo Davide adatuma amithenga kuti akamtenge mkaziyo. Iwo adabwera naye kwa Davide, ndipo Davideyo adagona naye. Nthaŵi imeneyo nkuti mkaziyo atangomaliza kusamba. Pambuyo pake mkazi uja adabwerera kunyumba kwake. Kenaka ataona kuti waima, adatumiza mau kwa Davide kukamuuza kuti, “Inetu ndi mommuja, sindili bwino!”
Tsiku lina akazi aŵiri adama adadza kwa Solomoni naimirira pamaso pake. Mkazi woyamba adati, “Inu mbuyanga, ine ndi mnzangayu timakhala nyumba imodzi. Tsono ine ndidaona mwana, mnzangayu ali m'nyumba momwemo. Tsiku lachitatu lake, ine nditachira kale, mnzangayu nayenso adaona mwana. Ndipo ifeyo tinali tokha, panalibe munthu wina aliyense m'nyumbamo, koma aŵiri tokhafe. Koma mwana wa mnzangayu adafa usiku, chifukwa adaamugonera. Anthu nsembe ankatsirirabe ku akachisi osiyanasiyana, chifukwa choti nthaŵi imeneyo anali asanammangire nyumba Chauta. Tsono iyeyu adadzuka pakati pa usiku, natenga mwana wanga kumimba kwanga namgoneka kumimba kwake, ndipo adagoneka mwana wake wakufayo kumimba kwanga. Nthaŵiyo nkuti mdzakazi wanune ndili m'tulo. M'maŵa nditadzuka kuti ndiyamwitse mwana wanga, ndidaona kuti ngwakufa. Koma nditayang'anitsitsa, ndidaona kuti si mwana wanga ai.” Koma mkazi wina uja adamdula pakamwa nati, “Iyai, mwana wamoyoyu ndiye wanga, wako ndi wakufayu.” Mkazi woyamba uja adati, “Iyai, mwana wakufayu ngwako, koma wamoyoyu ngwanga.” Adaatero kulankhula kwake azimaiwo pamaso pa mfumu. Tsono mfumu idati, “Wina akuti, ‘Mwana wamoyoyu ngwanga,’ winanso akuti, ‘Iyai, mwana wako ngwakufayu, wanga ngwamoyoyu.’ ” Ndiye mfumuyo idati, “Patseni lupanga.” Adabwera nalo lupanga kwa mfumu. Tsono mfumu idagamula kuti, “Mduleni pakati mwana wamoyoyu, aliyense mwa azimai aŵiriŵa mumpatse chigawo chimodzi.” Pomwepo mai amene anali mwini wake wa mwana wamoyoyo adagwidwa ndi chisoni chachikulu mu mtima chifukwa cha mwanayo. Choncho adauza mfumuyo kuti, “Pepani, mbuyanga, ingompatsani iyeyu mwana wamoyoyu, musamuphe, ndakupembani.” Koma mai wina uja adati, “Iyai asapatse ine kapena iwe, amdule pakati basi!” Tsono mfumu idayankha kuti, “Perekani mwana wamoyoyu kwa mai woyamba uja, musamuphe ai. Ameneyu ndiye mai wake wa mwanayu.” Ndipo Aisraele onse adamva za m'mene mfumu idagamulira mlanduwo. Motero anthu adayamba kulemekeza Solomoni, chifukwa adaona kuti anali ndi nzeru za Mulungu zoweruza mwachilungamo.
Kuchokera kumeneko Elisa adapita ku Betele. Ndipo pamene anali pa njira, anyamata ena amumzindamo adatuluka nayamba kumseka kuti, “Choka apa, chidazi! Choka apa, chidazi!” Tsono Elisayo adatembenuka, ndipo ataŵaona anyamatawo, adaŵatemberera m'dzina la Chauta. Pompo padatuluka zimbalangondo ziŵiri zazikazi kuchokera kuthengo, nkuphapo anyamata 42.
“Munthu wobadwa mwa mkazi amakhala masiku oŵerengeka, komanso masiku ake ndi amavuto okhaokha. Koma munthu akafa, kutha kwake nkomweko. Kodi munthuyo akafa, amapita kuti? Monga madzi amaphwa m'nyanja, monganso mtsinje umaphwa nuuma, momwemonso munthu amagona pansi osadzukanso. Mpaka zamumlengalenga zidzatha, iyeyo sadzadzuka. Palibe aliyense angamdzutse kutulo kwake. Ha! Achikhala mudaangondibisa ku manda, kuti ndisaoneke mpaka mkwiyo wanu utapita. Achikhala mudaangondiikira nthaŵi, kuti pambuyo pake mundikumbukirenso. Kodi munthu atafa, nkudzakhalanso ndi moyo? Koma masiku onse a moyo wanga wovutikawu, ndidzadikira mpaka kumasulidwa kwanga kutafika. Inu mudzandiitana, ine nkukuyankhani. Mudzafunitsitsanso kuwona ine, ntchito ya manja anune. Nthaŵiyo mudzayang'ana mayendedwe anga onse, koma simudzalondoloza machimo anga. Zolakwa zanga zidzakhululukidwa, Inu mudzafafaniza machimo anga onse. “Komabe monga phiri limagwa nkuswekasweka, ndipo thanthwe limasendezeka kuchoka pamalo pake, monganso madzi oyenda amaperesa miyala, ndipo madzi othamanga amakokolola nthaka, momwemonso Inu mumaononga chiyembekezo cha munthu. Amaphuka ngati duŵa, kenaka nkufota. Sakhalitsa, amathaŵa ngati mthunzi.
Anthu oipa ndi osokera kuyambira ali m'mimba mwa mai ao, anthu amabodza ndi otayika kuyambira tsiku la kubadwa kwao.
Pamene paja ndinkavutika ndi maganizo, ndi kumamva cholasa mumtimamu, ndinali wopusa wosamvetsa kanthu, ndinali ngati chilombo kwa Inu.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.
Zonse nzopanda phindu, akutero Mlaliki. Zonse nzachabechabe! Ndithudi zonse nzopandapake. Kodi munthu amapindulanji ndi ntchito zonse zolemetsa zimene amazigwira pansi pano?
Angathe kulanga mwankhalwe, komabe adzaonetsa chifundo, chifukwa chikondi chao nchochuluka. Savutitsa mwadala, sakonda kusautsa munthu aliyense.
Tsoka kwa inu amene mumalilakalaka tsiku la Chauta! Kodi tsiku limenelo lidzakupinduliraninji inuyo? Kudzakhalatu mdima, osati kuŵala ai. Kudzakhala monga m'mene kumachitira munthu akamathaŵa mkango, ndipo akumana ndi chimbalangondo, kapena monga munthu woti wakaloŵa m'nyumba, atsamira chipupa ndi dzanja lake, njoka nkumuluma. “Namwali Israele wagwa chonse osati nkudzukanso ai. Wagwa ndi kuiŵalika pa dziko lake, popanda wina womdzutsa.” Kodi suja tsiku la Chauta ndi mdima wokhawokha osati kuŵala, kodi suja lili ngati usiku wabii wopanda mpoti mbee pomwe!
“Panali munthu wina wachuma, amene ankavala zovala zamtengowapatali, ndipo ankasangalala ndi kudyerera masiku onse. Tsono mbuye wakeyo adamuitana, namufunsa kuti, ‘Nchiyani chimene ndikumva za iwe? Undifotokozere za ukapitao wako, pakuti sungakhalenso kapitao ai.’ Panalinso munthu wina, dzina lake Lazaro, amene ankadzagona pa khomo la munthu wachuma uja. Iyeyu anali ndi zilonda m'thupi lonse. Ankalakalaka kudya nyenyeswa zimene zinkagwa pansi kuchokera pa tebulo la wachuma uja. Koma si pokhapo, ngakhale agalu ankabwera kumadzanyambita zilonda zake. “Munthu wosauka uja adamwalira, angelo nkumunyamula, nakamtula m'manja mwa Abrahamu. Munthu wachuma uja nayenso adamwalira, naikidwa m'manda. Pamene ankazunzika ku Malo a anthu akufa, wachuma uja adayang'ana kumwamba naona Abrahamu ali patali, ndi Lazaro ali pambali pakepa. Pamenepo adanena mokweza mau kuti, ‘Atate Abrahamu, mundichitire chifundo. Tumani Lazaro aviike nsonga ya chala chake m'madzi kuti adzaziziritseko lilime langa, pakuti ndikuzunzika koopsa m'moto muno.’ Koma Abrahamu adati, ‘Mwana wanga, kumbukira kuti udalaandiriratu zokondweretsa ukadali ndi moyo, pamene Lazaro adaalandira zoŵaŵa. Koma tsopano iye akusangalala kuno, pamene iwe ukuzunzika kwambiri. Ndiponso pakati pa ife ndi inu pali chiphompho, kotero kuti ofuna kuchoka kuno kuwolokera kwanuko, sangathe ai. Chimodzimodzinso kuchoka kwanuko kuwolokera kuno.’ “Apo wachuma uja adati, ‘Ndipotu ndikukupemphani atate, kuti mumtume Lazaroyo apite ku nyumba ya bambo wanga. Kumeneko ndili ndi abale anga asanu. Akaŵachenjeze, kuwopa kuti iwonso angabwere ku malo ano amazunzo.’ Koma Abrahamu adati, ‘Iwo ali ndi mabuku a Mose ndi a aneneri. Amvere zam'menemo.’ Apo kapitaoyo adayamba kuganiza mumtima mwake kuti, ‘Ndichite chiyani, popeza kuti mbuye wanga akundilanda ukapitao? Kulima, ai, ndilibe mphamvu. Kupemphapempha, ainso, kukundichititsa manyazi. Iye adati, ‘Iyai, atate Abrahamu, koma wina atauka kwa akufa nkupita kwa iwo, apo adzatembenuka mtima.’ Koma Abrahamu adamuuza kuti, ‘Ngatitu iwo samvera Mose ndi aneneri, sangathekenso ngakhale wina auke kwa akufa.’ ”
Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha. Mulungu adatuma Mwana wakeyo pansi pano, osati kuti adzazenge anthu mlandu, koma kuti adzaŵapulumutse. “Munthu wokhulupirira Mwanayo, sazengedwa mlandu. Koma wosakhulupirira, wazengedwa kale, chifukwa sadakhulupirire Mwana mmodzi yekha uja wa Mulungu.
Kochokera mwa kholo limodzi Iye adalenga mitundu yonse ya anthu, kuti ikhale pa dziko lonse lapansi. Adakonzeratu nthaŵi ya moyo wao, ndiponso malire a pokhala pao.
Ngakhale anawo asanabadwe, ndiye kuti tsono asanachite chilichonse chabwino kapena choipa, Mulungu adaafunabe kuti cholinga chake chosankhira munthu aliyense chipitirire. Izi adachita osati chifukwa cha ntchito za munthu koma chifukwa chakuti Mulungu adamuitana munthuyo. Motero Mulungu adauza Rebeka kuti, “Wamkuluyu adzatumikira wamng'onoyu.” Paja Malembo akuti, “Yakobe ndidaamukonda, koma Esau ndidaadana naye.”
Chuma cha Mulungu nchachikulu zedi. Nzeru zake ndi kudziŵa kwake nzozama kwambiri. Ndani angamvetse maweruzidwe ake, ndipo njira zake ndani angazitulukire? Ndi monga mau a Mulungu anenera kuti, “Ndani amadziŵa maganizo a Chauta, ndani angamupatse malangizo? Ndani adaayamba waperekapo kanthu kwa Mulungu, kuti Mulunguyo amubwezereko kanthu?” Paja zinthu zonse nzochokera kwa Iye, nzolengedwa ndi Iye ndipo zimalinga kwa Iye. Ulemerero ukhale wake mpaka muyaya. Amen.
Koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Maso a munthu sanaziwone, makutu a munthu sanazimve, mtima wa munthu sunaganizepo konse zimene Mulungu adaŵakonzera amene amamkonda.”
Ngati Yesu sadauke kwa akufa, nanga amafunanji anthu amene amabatizidwa m'malo mwa amene adafa? Ngati akufa sauka konse, nanga chifukwa chiyani anthu amabatizidwa m'malo mwao?
Motero palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakati pa akapolo ndi mfulu, kapenanso pakati pa amuna ndi akazi, pakuti nonsenu ndinu amodzi mwa Khristu Yesu.
Mulungu asanalenge dziko lapansi, adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi opanda cholakwa pamaso pake.
Zoonadi, zonse ndikuziwona kuti nzosapindulitsa poziyerekeza ndi phindu lopambana la kudziŵa Khristu Yesu, amene ndi Ambuye anga. Chifukwa cha Khristuyo ndidalolera kutaya zonse, nkumaziyesa zinyalala, kuti potero phindu langa likhale Khristu, Iye ndi ine tikhale amodzi. Sindiyesanso pandekha kukhala wolungama pakutsata Malamulo, koma ndizikhala ndi chilungamo chopezeka pakukhulupirira Khristu, chilungamo chochokera kwa Mulungu, chochilandira pakukhulupirira.
Kudakomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristuyo. Tikulembera inu osankhidwa ndi Mulungu okhala ku Kolose, abale athu okhulupirika mwa Khristu. Mulungu Atate athu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.
Pamene anthu azikati, “Pali mtendere, tili pabwino”, pamenepo chiwonongeko chidzaŵagwera modzidzimutsa. Chidzaŵadzidzimutsa monga momwe zoŵaŵa zimamchitira mkazi pa nthaŵi yoti achire; ndipo sadzatha konse kuchizemba.
Ndithudi, chinsinsi cha chipembedzo chathu nchachikulu: “Iye uja adaonekera ali ndi thupi la munthu, Mzimu Woyera adamchitira umboni kuti ndi wolungama, angelo adamuwona, adalalikidwa pakati pa anthu a mitundu yonse, anthu a pa dziko lonse lapansi adamkhulupirira, Iyeyo adatengedwa kunka kumwamba mu ulemerero.”
Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.
Paja pali anthu ambiri osaweruzika, makamaka pakati pa gulu la anthu ochokera ku Chiyuda. Anthu ameneŵa amalankhula nkhani zopanda pake nkumasokeretsa anzao. Nkofunika kuŵakhalitsa chete, chifukwa akusokoneza mabanja ena athunthu pakuŵaphunzitsa zimene sayenera kuŵaphunzitsa. Amangochita zimenezi ndi cholinga choipa, chofuna kupata ndalama.
Pajatu munthu wotsata Malamulo onse, akangophonyapo ngakhale pa mfundo imodzi yokha, ndiye kuti wachimwira Malamulo onsewo.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Motero aliyense amene adzapambane, adzamuvekanso zovala zoyera. Dzina lake sindidzalifafaniza m'buku la amoyo, ndipo ndidzamchitira umboni pamaso pa Atate anga, ndi pamaso pa angelo ao.
Pambuyo pake ndidaona mpando wachifumu woyera, waukulu, ndiponso amene amakhalapo. Dziko lapansi ndi thambo zidathaŵa pamaso pake, ndipo sizidapezekenso konse. Ndidaonanso anthu akufa, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja, ndipo mabuku adafutukulidwa. Adafutukula buku linanso, limene lili buku la amoyo. Tsono anthu akufawo adaweruzidwa poyang'anira ntchito zao monga momwe zidaalembedwera m'mabukumo. Pamenepo nyanja idapereka onse amene adaferamo. Imfa ndi Malo a anthu akufa zidaperekanso akufa ake, ndipo aliyense adaweruzidwa potsata ntchito zake. Kenaka Imfa ija ndi Malo a anthu akufa aja zidaponyedwa m'nyanja yamoto. Nyanja yamoto imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri. Aliyense wopezeka kuti dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo lija, adaponyedwa m'nyanja yamotoyo.
Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.”
Ine Yohane, ndikuchenjeza aliyense womva mau a m'buku lino oneneratu zam'tsogolo. Wina akadzaonjezerapo kanthu pa mau ameneŵa, Mulungu adzamuwonjezera miliri ija yalembedwa m'buku munoyi. Ndipo wina akadzachotsapo kanthu pa mau a m'buku lino loneneratu zam'tsogolo, Mulungu adzamchotsera gawo lake la zipatso za mtengo wopatsa moyo uja, ndi malo ake omwe mu Mzinda Woyera uja, monga zalembedwera m'buku muno.