Mtima wanga, dziwani kuti dyera ndi chinthu chomwe chimatigwira tonse, mosasamala kanthu za msinkhu wathu, kapena kuti ndife ndani.
M’Baibulo, muli nkhani zambiri zomwe zimatithandiza kuzindikira kuopsa kwa dyera. M’buku la Mlaliki, Mfumu Solomoni inalankhula za kufupika kwa moyo ndi kupanda pake kwa chuma ndi ulemerero wa dziko lapansi. Iye amatilimbikitsa kuyika chiyembekezo chathu mwa Mulungu, chifukwa zonse zomwe tili nazo ndi zomwe tinakwanitsa zidzatha.
Yesu, m’Chipangano Chatsopano, anatiphunzitsa kufunika koika maganizo athu pa zinthu zosatha, osati kufuna kuvomerezedwa ndi anthu. Mawu ake amatipatsa njira yopezera cholinga chenicheni cha moyo wathu, moyo wodzaza ndi chikondi cha Mulungu ndi cha anansi athu.
Dyera limatiletsa kukhala odzichepetsa ndipo limatipangitsa kufuna kudzikweza tokha, kuiwala chikondi ndi chifuniro cha Mulungu. Tiyeni tichenjere zimenezi.
Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi.
Chuma chochipeza mofulumira chidzanka chitha pang'onopang'ono, koma chochipeza pang'onopang'ono chidzanka chichulukirachulukira.
Nkhope yachikoka ndi yonyenga, kukongola nkosakhalitsa, koma mkazi woopa Chauta ndiye woyenera kumtamanda.
Anthu okonda ndalama sakhutitsidwa nazo ndalamazo. Chimodzimodzinso anthu okonda chuma, sakhutitsidwa nalo phindu. Zimenezinso nzachabechabe.
Choncho muchotseretu zokusautsani mu mtima mwanu, mupewe zokupwetekani m'thupi mwanu. Pajatu unyamata ndi ubwana, zonse nzopandapake.
Musalole kuti ndikhale wabodza kapena wonama. Ndisakhale mmphaŵi kapena khumutcha. Muzindidyetsa chakudya chondiyenera,
“Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba. “Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.
Tsono ndidazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.
Kudzikongoletsa kwanu kusangokhala kwa maonekedwe akunja pakuluka tsitsi, ndi kuvala zamakaka zagolide ndi zovala zamtengowapatali. Koma kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa moyo wam'kati, kukongola kosatha kwa mtima wofatsa ndi wachete. Moyo wotere ngwamtengowapatali pamaso pa Mulungu.
Anthu inu, mudzaleka liti kunyoza ulemu wanga? Bwanji mukukondabe zinthu zachabechabe? Bwanji mukulakalakabe zinthu zonama?
chifukwa cha zoipa zake ndi za Ela mwana wake, zimene onse aŵiriwo adaachita. Iwo adachimwitsa anthu a ku Israele, naputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa Aisraele, chifukwa cha mafano ao.
Momwe chimaonekera chipini chagolide chikakhala pa mpuno wa nkhumba, ndi momwenso kumakhalira kukongola kwa mkazi wam'kamwa.
Iwowo adanyoza malamulo a Chauta ndi chipangano cha Chauta chimene Iye adachita ndi makolo ao. Adanyozanso zochenjeza za Chauta. Adatsata milungu yachabechabe, ndipo iwo omwe adasanduka achabechabe. Ankatsata zitsanzo za anthu a mitundu ina okhala nawo pafupi, ngakhale Chauta anali atalamula kuti asamachite mofanana ndi mitundu imeneyo.
Ndatopa nawo moyo wanga, sindingakonde kukhala moyo nthaŵi zonse. Ingondisiyani, poti moyo wanga uli ngati mpweya chabe.
“Onani, mwandipatsa masiku ochepa chabe, nthaŵi ya moyo wanga siili kanthu pamaso panu. Ndithudi, munthu aliyense ndi mpweya chabe.
Nanga ndiye kuti munthu angapindulenji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake? Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake?
Asadzinyenge pokhulupirira zinthu zoipa zachabe, poti zinthu zachabezo ndizo zidzakhale malipiro ake.
Inu mumalanga munthu pakumdzudzula chifukwa cha uchimo wake. Mumaonongeratu zimene iye amazikonda, monga m'mene chimachitira chifukufuku. Zoonadi, munthu aliyense ndi mpweya chabe.
Nzoonadi, kupembedza Mulungu kumapindulitsa kwambiri, malinga munthu akakhutira ndi zimene ali nazo. Sitidatenge kanthu poloŵa m'dziko lino lapansi, ndipo sitingathenso kutenga kanthu potulukamo.
Anthu otsika ndi mpweya chabe, ngakhale anthu okwera ndi nthunzi chabe, onsewo ndi oluluka pa sikelo, ndi opepuka kupambana mpweya.
Choncho Mulungu adadula masiku ao kuti azimirire ngati mpweya, adadula zaka zao kuti zithere m'zoopsa.
Chauta akunena kuti, “Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake, munthu wamphamvu asanyadire mphamvu zake, ndipo munthu wolemera asanyadire chuma chake. Koma ngati wina afuna kunyadira, anyadire ichi chakuti amamvetsa za Ine, ndipo amandidziŵa. Amadziŵa kuti Ine ndine Chauta wokonda chifundo, chilungamo, ndi ungwiro pa dziko lapansi. Ndithudi, pazimenezi ndipo pali mtima wanga.”
Letsani maso anga kuti asamayang'ane zachabe, mundipatse moyo monga momwe mudalonjezera.
Kudzikuza kwa anthu kudzatha, kudzitama kwa anthu kudzaonongedwa. Chauta yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo.
Atatero adauza anthu aja kuti, “Chenjerani, ndipo mupewe khumbo lililonse lofuna zambiri. Pajatu ngakhale munthu akhale ndi chuma chochuluka chotani, chumacho sichingatchinjirize moyo wake.”
Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo.
Landitseni kwa adani ankhalwe, mundipulumutse m'manja mwa akunja, amene amalankhula zabodza, ndipo amalumbira zonama.
Kudamveka mau akuti, “Lengeza.” Ine ndidafunsa kuti, “Kodi ndilengeze chiyani?” Mau aja adati, “Ulengeze kuti anthu onse ali ngati udzu. Kukongola kwao kuli ngati maluŵa akuthengo. Udzu umauma, maluŵa amafota, Chauta akaziwuzira mpweya wake. Ndithudi anthu sasiyana ndi udzu. Udzu umauma, maluŵa amafota, koma mau a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.”
Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu.
Zonse nzopanda phindu, akutero Mlaliki. Zonse nzachabechabe! Ndithudi zonse nzopandapake.
Zonse zochitika pansi pano ndaziwona. Zonsezo nzopandapake, ndipo kuzifunafuna nkungodzivuta chabe.
Nthaŵi zina mumtima mwangamu ndinkati, “Ah! Tsopano ndiyesepo zokondweretsa, ndidzisangalatse.” Koma ai, zimenezinso zinali zopanda phindu.
Ngati munthu adziyesa kanthu, pamene chikhalirecho sali kanthu konse, amangodzinyenga.
Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Kani zimene zimagwera chitsiru nanenso zidzandigwera zomwezo! Nanga tsono ineyo nzeru zambiri chotere nzanji?” Pamenepo ndidaona kuti zimenezinso nzopanda phindu!
Tsono ndidayamba kulingalira zonse zimene ndidazichita, ntchito zolemetsa zonse zimene ndidazigwira, nkuwona kuti zonsezo zinali zopanda phindu. Kunali kungodzivuta chabe. Ndithu panalibe choti nkupindulapo pa dziko lapansi.
Motero moyo wanga ndidaipidwa nawo, chifukwa chakuti zonse zochitika pansi pano zimandimvetsa chisoni. Ndithudi, zonsezo nzopandapake, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.
Kuli bwino kumangopenya zinthu ndi maso kupambana kumazilakalaka chamumtima. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.
Tsoka kwa amene amadzikokera machimo ambiri ndi kunama kwao, amene amalephera kudzimasula ku machimo awo.
Koma Chauta adauza Samuele kuti, “Usayang'ane maonekedwe ake, ngakhale kutalika kwa msinkhu wake, poti ndamkana ameneyo. Chauta sapenya monga m'mene apenyera anthu. Anthu amapenya zakunja, koma Chauta amapenya zamumtima.”
Mu mzinda wachisokonezo uja zonse zaonongedwa, nyumba iliyonse yatsekedwa, kotero kuti palibe wotha kuloŵamo.
Mulungu adzalanga anthu osinjirira anzao, ndiponso ophophonyetsa anthu ozengedwa mlandu. Adzalanganso amene amapereka umboni wonama, kuti anzao osalakwa asaweruzidwe molungama.
Paja mau a Mulungu amanena kuti, “Anthu onse ali ngati udzu, ulemerero wao uli ngati duŵa lakuthengo. Udzu umauma, ndipo duŵa limathothoka, koma mau a Ambuye ngokhala mpaka muyaya.” Mau ameneŵa ndi Uthenga Wabwino umene walalikidwa kwa inu.
Inuyo sindinu kanthu konse, ndipo zochita zanu nzopandapake. Amene amakupembedzaniyo amandinyansa.
Ndithudi, milungu yonseyi njachabe, zochita zake si kanthu konse. Mafano ake osungunula ali ngati mphepo yachabechabe.”
Anthu omvera khalidwe loipalo, amaika mtima pa zilakolako zathupi. Koma anthu omvera Mzimu Woyera, amaika mtima pa zimene Mzimu Woyerayo afuna. Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.
Kupembedza pa magomo sikuthandiza, kuchita maphwando pa mapiri kulibenso ntchito. Zoonadi, mwa Chauta, Mulungu wathu ndiye muli chipulumutso cha Israele.
Zimene zimachitikira anthu, zomwezonso zimachitikira nyama. Monga chinacho chimafa, chinacho chimafanso. Zonsezo zimapuma mpweya umodzimodzi, munthu saposa nyama. Zonsezi nzopandapake. pali nthaŵi yobadwa ndi nthaŵi yomwalira, pali nthaŵi yobzala ndi nthaŵi yozula zobzalazo. Zonse zimapita kumodzimodzi. Zonsezo nzochokera ku dothi, ndipo zimabwerera kudothi komweko.
Ndithudi, miyambo ya anthu a mitundu inayo nzopanda pake. Iwo aja amakadula mtengo ku nkhalango, munthu waluso namausema ndi nsompho.
Mafanowo ngachabechabe, ayenera kuŵaseka, ndipo pamene anthuwo adzalangidwe, mafanowo adzaonongeka.
Mafanowo ngachabechabe, oyenera kuŵaseka, ndipo pamene anthuwo adzalangidwe, mafanowo adzaonongedwa.
Zaka za moyo wathu nzokwanira makumi asanu ndi aŵiri, tikakhala amphamvu, ndiye makumi asanu ndi atatu. Koma zaka zonsezo ndi za nkhaŵa ndi mavuto. Zakazo zimatha msanga, ife nkumapita.
Nanga adakusiyanitsa ndi anthu ena ndani? Kaya uli ndi chiyaninso chimene sudachite kuchilandira? Tsono ngati udachita kuzilandira, ukunyadiranji ngati kuti sudangozilandira chabe?
Zinthu zimene aneneri ako adakuwonera m'masomphenya zinali zabodza ndi zonyenga. Iwo sadaonetse uchimo wako, kuti ukhalenso pabwino. Mau amene adakutengeraniwo anali abodza ndi osokeretsa.
Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.
Inde ankamudziŵa Mulungu, koma m'malo mwa kumtamanda kapena kumthokoza, maganizo ao adasanduka opanda pake, ndipo m'mitima yao yopusa mudadzaza mdima. Iwo amadziyesa anzeru, koma chikhalirecho ndi opusa.
Monga momwe munthu adabadwira m'mimba mwa mai wake opanda kanthu, chonchonso adzapita maliseche. Pa zonse zimene adakhetsera thukuta, palibe nchimodzi chomwe chimene adzatenge m'manja mwake.
Wina amadziyesa wolemera, m'menemo alibe nkanthu komwe. Wina amadziyesa wosauka, m'menemo ali nchuma chochuluka.
Nanga ndiye kuti munthu wapindulanji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake kapena kuuwononga?
Iye akukufunsani kuti, “Kodi makolo anu adandipeza ncholakwa chanji kuti andithaŵe? Adatsata milungu yachabechabe, iwonso nkusanduka achabechabe.
m'menemo inuyo zamaŵa simukuzidziŵa. Kodi moyo wanu ngwotani? Pajatu inu muli ngati utsi chabe, umene umangooneka pa kanthaŵi, posachedwa nkuzimirira.
Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa.
Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru.
Tsono m'dzina la Ambuye ndikukuuzani, ndipo ndikunenetsa, kuti musayendenso monga amachitira akunja potsata maganizo ao achabe. Nzeru zao zidachita chidima, sangalandire nao konse moyo wa Mulungu chifukwa cha umbuli umene udadza mwa iwo kaamba ka kuuma mtima kwao.
Kuseka kwa zitsiru kuli ngati kuthetheka kwa moto kunsi kwa mbiya. Zimenezinso nzachabechabe.
Zoonadi, aliyense atha kuwona kuti ngakhale anthu anzeru amafa. Chimodzimodzi, anthu opusa ndi opulukira ayenera kufa ndi kusiyira ena chuma chao. Manda ao ndiye kwao mpaka muyaya, ndi malo odzakhalako pa mibadwo yonse, ngakhale akadali moyo ankatcha maiko maina ao. Ngakhale munthu akhale wolemera chotani, komabe adzafa chabe ngati nyama zakuthengo.
“Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza.
Mukamafuula kufuna chithandizo, mafano anuwo akupulumutseni! Mphepo idzaiyalula milunguyo, mpweya udzaiwulutsa. Koma amene amakhulupirira Ine, adzalandira dziko lokhalamo, ndi kumapembedza pa phiri langa loyera.”
Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.
Paja Malembo akuti, “Wofuna kunyada, anyadire Ambuye.” Pakuti munthu wovomerezeka, si amene amadzichitira yekha umboni, koma amene Ambuye amamchitira umboni.
Mau akachuluka, zopandapake zimachulukanso. Nanga munthu apindulapo chiyani? Ndani amadziŵa zomkomera munthu kwenikweni pa nthaŵi yochepa imene munthuyo ali ndi moyo? Moyo wake ndi wa masiku ochepa, ndi wopandapake, umangopitirira ngati mthunzi. Ndani angathe kumufotokozera munthuyo zimene zidzachitike pansi pano iyeyo atafa?
Koma amatikomera mtima koposa. Nchifukwa chake Malembo akuti, “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma odzichepetsa amaŵakomera mtima.”
Nchifukwa chake amavala kunyada ngati mkanda wam'khosi. Amavala nkhanza ngati malaya. Maso ao ndi otupa ndi kunenepa. Mitima yao ndi yodzaza ndi maganizo ofuna kuchita zoipa.
Koma chifukwa cha Khristu, zomwe kale ndinkaziyesa zaphindu, tsopano ndikuziwona kuti nzosapindula. Zoonadi, zonse ndikuziwona kuti nzosapindulitsa poziyerekeza ndi phindu lopambana la kudziŵa Khristu Yesu, amene ndi Ambuye anga. Chifukwa cha Khristuyo ndidalolera kutaya zonse, nkumaziyesa zinyalala, kuti potero phindu langa likhale Khristu,
Pali chinthu china chachabechabe chimene chimachitika pansi pano. Chinthucho ndi ichi: mwina anthu abwino amalangidwa ngati ochita zoipa, pamene oipa amalandira zabwino ngati kuti ndi anthu abwino. Ndikuti zimenezinso nzachabechabe. Nchifukwa chake ndikuti munthu azikondwerera moyo, pakuti munthu alibe chinthu chinanso chabwino pansi pano choposa kudya, kumwa ndi kumadzikondweretsa. Akamatero, munthuyo adzakhala ndi chimwemwe pa ntchito yake masiku onse a moyo wake, amene Mulungu wampatsa pansi pano.
Kuwopa Chauta kumaphunzitsa nzeru, ndipo ndi kudzichepetsa ndi ulemu, chili patsogolo nkudzichepetsa.
Chauta akapanda kumanga nawo nyumba, omanga nyumbayo angogwira ntchito pachabe. Chauta akapanda kulonda nawo mzinda, mlonda angochezera pachabe.
Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.”
Ndidaonanso pansi pano kuti opambana pa kuthamanga si aliŵiro okhaokha, opambana pa nkhondo si amphamvu okhaokha, ndiponso okhala ndi chakudya si anzeru okhaokha. Olemera si odziŵa zambiri okhaokha, ndipo si anthu aluso okhaokha amene anzao amaŵakomera mtima. Onsewo mwai umangoŵagwera pa nthaŵi yake. Kungoti munthu saidziŵa nthaŵi yake. Monga momwe nsomba zimagwidwira mu ukonde, monga momwenso mbalame zimakodwera mu msampha, anthunso nchimodzimodzi. Amachita ngati kukodwa mu msampha pa nthaŵi yoipa, pamene tsoka laŵagwera mwadzidzidzi.
Maso odzikuza ndi mtima wonyada zimatsogolera anthu oipa ngati nyale, nchifukwa chake amachimwa.
Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya.
Kudzikuza kwa anthu kudzatha, kudzitama kwao konse kudzaonongedwa. Chauta yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Usavutike munthu wina akamalemera, pamene chuma cha m'nyumba mwake chikukulirakulira. Chifukwa pamene munthuyu amwalira, sadzatengapo kanthu. Chuma chake sichidzapita naye limodzi.
Mitundu ya anthu ili ngati kadontho ka madzi mu mtsuko, ilinso ngati fumbi chabe pa sikelo. M'manja mwa Chauta zilumba nzopepuka ngati fumbi. Nkhalango ya ku Lebanoni siingakwanitse nkhuni zosonkhera moto, nyama zam'menemo sizingakwanire kuperekera nsembe yootcha. Mitundu yonse ya anthu si kanthu konse pamaso pa Chauta, Iye amaziyesa zachabe ndi zopandapake.
Musalole kuti ndikhale wabodza kapena wonama. Ndisakhale mmphaŵi kapena khumutcha. Muzindidyetsa chakudya chondiyenera, kuwopa kuti ndikakhuta kwambiri, ndingayambe kukukanani nkumanena kuti, “Chauta ndiye yaninso?” Kuwopanso kuti ndikakhala mmphaŵi, ndingayambe kuba, potero nkuipitsa dzina la Mulungu wanga.
Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera Kumwamba, kwa Atate a zounikira zonse zakuthambo. Iwo sasinthika konse, ndipo kuŵala kwao sikutsitirika mpang'ono pomwe.
“Muwoneni munthu amene sadafune kudalira Mulungu, koma adakhulupirira chuma chake chochuluka, nalimbikira kuchita zoipa.”
Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo adatipatsa madalitso aakulu ndi amtengowapatali amene Iye adatilonjeza. Adatero kuti mulandireko moyo wake wa Mulungu, mutapulumuka ku chivunde chimene chili pa dziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoipa.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade.
Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.
Koma ndidati, “Ndagwira ntchito yopanda phindu. Ndangoononga mphamvu zanga pachabe.” Komabe zondiyenerera zili m'manja mwa Chauta, mphotho yanga ili m'manja mwa Mulungu wanga.
Ndazindikira kuti zabwino zonse zili ndi malire, koma malamulo anu alibe konse malire.
“Palibe wantchito amene angathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkunyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.”
“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna. Pa tsiku lachiweruzo anthu ambiri azidzanena kuti, ‘Ambuye, Ambuye, kodi suja ife tinkalalika mau a Mulungu m'dzina lanu? Suja tinkatulutsa mizimu yonyansa potchula dzina lanu? Suja tinkachita ntchito zamphamvu zambiri m'dzina lanu?’ Apo Ine ndidzaŵauza poyera kuti, ‘Sindidaakudziŵani konse. Chokani apa, anthu ochita zoipa.’
Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu. Adzakhala opanda chifundo, osapepeseka, ndi osinjirira anzao. Adzakhala osadzigwira, aukali, odana ndi zabwino, opereka anzao kwa adani ao. Adzakhala osaopa chilichonse, odzitukumula, okonda zosangalatsa m'malo mokonda Mulungu.
Mfumu ikhoza kulamulira anthu osaŵerengeka, komabe itamwalira, palibe aliyense amene adzayamikire zomwe mfumuyo idachita. Ndithudi, zimenezinso nzopandapake, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.
Ndikudziŵa kuti mwa ine simukhala kanthu kabwino. Ndikamati, “ine”, ndikunena khalidwe langa lokonda zoipa. Ngakhale ndimafuna kuchita zabwino, komabe sindizichita.
Kunena za munthu, masiku ake sakhalitsa, ali ngati a udzu, munthuyo amakondwa ngati duŵa lakuthengo. Koma mphepo ikaombapo, duŵalo pamakhala palibe, siliwonekanso pa malo ake.
Basi, zonse zamveka. Mfundo yeniyeni ya zonsezi ndi iyi: Uzimvera Mulungu, ndipo uzitsata malamulo ake, pakuti umenewu ndiwo udindo wake wonse wa munthu. Pajatu Mulungu adzaweruza zonse zimene timachita, zabwino kapena zoipa, ngakhale ndi zam'chinsinsi zomwe.