Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


MAVESI OKHUDZA MALO A MOYO

MAVESI OKHUDZA MALO A MOYO

Moyoyo wanga, taganizirani izi: timadutsa nthawi zosiyanasiyana m'miyoyo yathu. Nthawi zina tili ndi thanzi labwino, nthawi zina timadwala. Tili achinyamata, tili ndi mphamvu zambiri, timaganiza kuti tingathe kuchita chilichonse, koma nthawi zina timapuma chifukwa tilibe ndalama zokwanira. Tikakula, tikapeza ntchito yabwino, ndalama zimabwera, koma nthawi yoti tikhale ndi banja lathu komanso anzathu imachepa, ndipo maloto athu amakhala ngati akutali kwambiri. Kenako, tikakalamba, titasunga ndalama pang'ono, nthawi yambiri ilipo, koma mphamvu zathu zimachepa. Chifukwa chake, tiyeni tisangalale ndi nthawi iliyonse popanda kulakalaka zomwe sitingathe kuzikwanitsa. Mulungu watipatsa zonse zomwe tikufunikira pano ndi tsopano. Monga momwe lemba limatiuza, "Musadere nkhawa ndi za mawa; pakuti mawa adzadzikhalira ndi nkhawa zake. Zokwanira tsiku ndi zoipa zake." (Mateyu 6:34)




Levitiko 19:32

“Muzikhala mwaulemu pamaso pa munthu waimvi. Wokalamba muzimchitira ulemu, ndipo pakutero mudzaopa Mulungu wanu. Ine ndine Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 25:8

Adamwalira ali nkhalamba yotheratu, atagonera zaka zochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 32:7

Ndinkati ayambe ndi akuluakulu aja kulankhula, chifukwa amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:25

Chiyambire unyamata wanga mpaka ukalamba wanga uno, sindidaonepo munthu wabwino atasiyidwa ndi Mulungu, kapena ana ake akupempha chakudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 46:3-4

“Mundimvere, inu zidzukulu za Yakobe, inu nonse otsala a m'nyumba ya Israele. Ndakhala ndikukusamalani chibadwire chanu, ndidakunyamulani kuyambira m'mimba mwa amai anu. Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja, mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu. Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani. Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:22

Umvere atate ako amene adakubala, ndipo usamanyoza amai ako atakalamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:1

Mwana wanzeru amamvera malangizo a atate ake, koma wonyoza samvetsera akamamdzudzula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Rute 4:15

Mwanayo adzakupatsani moyo watsopano ndipo adzakuchirikizani mu ukalamba wanu. Inde wakubalirani mwana mpongozi wanu amene amakukondani, amene wakuwonetsani kuti akupambana ana aamuna asanu ndi aŵiri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 46:4

Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja, mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu. Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani. Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:1-2

Munthu wachikulire usamdzudzule mokalipa, koma umchenjeze monga ngati bambo wako. Amuna achinyamata uzikhalitsana nawo ngati abale ako. Akhale mai woti anthu amamchitira umboni wakuti amachitadi ntchito zabwino. Akhale woti ankalera ana ake bwino, ankalandira bwino alendo, ankasambitsa mapazi a anthu a Mulungu, ndipo ankathandiza anthu amene anali m'mavuto. Akhalenso mai woti ankadzipereka pa ntchito zonse zabwino. Koma azimai amasiye a zaka zochepera uzikana kuŵalemba m'gulu limeneli. Pajatu zilakolako zao zikayamba kuŵavutitsa nkuŵalekanitsa ndi Khristu, amangofuna kukwatiwanso. Pamenepo amapezeka olakwa, chifukwa chosasunga lonjezo lao loyamba. Kuwonjezera pamenepo, amagwa m'chizoloŵezi cha kungokhala khale, motero amangoyendayenda ku nyumba za anthu. Tsonotu samangokhala khale chabe ai, amachitanso miseche nkumaloŵera za eni, ndi kukhala omalankhula zimene samayenera kulankhula. Nchifukwa chake nkadakonda kuti azimai amasiye a zaka zochepera azikwatiwanso, abale ana, ndipo azisamala bwino panyumba pao, kuti adani athu asapeze mpata wotisinjirira. Paja alipo kale azimai amasiye ena amene adapatukapo nkumatsata Satana. Koma ngati mai wina aliyense wachikhristu ali ndi achibale amene ali azimai amasiye, aziŵasamala iyeyo, osasenzetsa mpingo katundu wakeyo. Motero mpingo udzatha kusamala azimai amasiye opanda oŵathandiza. Akulu a mpingo otsogolera mpingo bwino, akhale oyenera kuŵalemekeza moŵirikiza, makamaka amene amagwira ntchito yolalika mau a Mulungu ndiponso yophunzitsa. Paja Malembo akuti, “Usaimange pakamwa ng'ombe imene ikupuntha tirigu.” Penanso akuti, “Wantchito ngwoyenera kulandira malipiro ake.” Usamamvere mau oneneza mkulu wa mpingo, pokhapokha ngati pali mboni ziŵiri kapena zitatu. Azimai achikulire uzikhalitsana nawo ngati amai ako, ndipo azimai a zaka zochepa uzikhalitsana nawo ngati alongo ako, m'kuyera mtima kwenikweni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:29-31

Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu. Kukumveka mau akuti, “Konzani njira ya Chauta m'thengo, lungamitsani mseu wa Mulungu wathu m'chipululu. Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufooka, ngakhale anyamata amaphunthwa ndi kugwa. Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:5-6

Adapereka mau odzichitira umboni kwa Yakobe, adakhazikitsa malamulo ake mu Israele. Adalamula makolo athu kuti aziŵaphunzitsa ana ao malamulowo. Adalola kukwiya, osadziletsa, sadaŵapulumutse ku imfa, koma adapereka moyo wao ku miliri. Adapha ana achisamba onse a Aejipito, ana oyamba a mphamvu zao, m'zithando za zidzukulu za Hamu. Tsono Mulungu adaŵatulutsa anthu ake ngati nkhosa, naŵatsogolera m'chipululu ngati zoŵeta. Adaŵatsogolera bwino lomwe kotero kuti sanalikuwopa, koma nyanja idamiza adani ao. Adaŵafikitsa ku dziko lake loyera, ku dziko lamapiri limene adaŵagonjetsera ndi dzanja lake lamphamvu. Adapirikitsa mitundu ina ya anthu, kuŵachotsa m'njira. Adagaŵagaŵa dziko la anthuwo kuti likhale la anthu ake, adakhazikitsa mafuko a Israele m'midzi ya anthuwo. Komabe Aisraele adamuputa ndi kumuukira Mulungu Wopambanazonse, sadasunge malamulo ake, koma iwo adakhala okanika ndi osakhulupirika monga makolo ao. Adapotoka ngati uta wosakhulupirika. Iwo adakwiyitsa Mulungu ndi akachisi ao opembedzerako mafano ku mapiri. Adamupsetsa mtima chifukwa cha mafano ao osemawo. Pamene Mulungu adamva zimenezi, adakwiya kwambiri, ndipo adakana Aisraele kotheratu. Motero mbadwo wakutsogolo wa ana amene sanabadwebe, udzaŵadziŵa, ndipo nawonso udzafotokozera ana ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 12:26-27

Ana anu azidzakufunsani kuti, ‘Kodi mwambo umenewu umatanthauza chiyani?’ Pamenepo inu muzidzayankha kuti, ‘Ndi nsembe ya Paska ya Chauta, chifukwa chakuti adapitirira nyumba za Aisraele ku Ejipito; pamene ankapha Aejipito, nyumba zathu adazisiya.’ ” Atamva zimenezi, anthu adaŵerama pansi, napembedza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 12:1

Uzikumbukanso Mlengi wako pa masiku a unyamata wako, masiku oipa asanafike, zisanafikenso zaka zoti uzidzati, “Moyowu wandikola.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:31

Imvi zili ngati chisoti chaufumu chopatsa ulemerero, munthu amazipata akakhala ndi moyo wautali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 12:6-7

Apo mfumu Rehobowamu adapempha nzeru kwa madoda amene ankakhala ndi bambo wake Solomoni ndi kumamlangiza akali moyo. Adaŵafunsa kuti, “Kodi mungandilangize zotani, kuti ndiŵayankhe anthu ameneŵa?” Madodawo adamuuza kuti, “Mukamatumikira bwino anthu ameneŵa nkukhaladi mtumiki wao, muzilankhula nawo mau abwino, ndipo iwowo adzakutumikirani mpaka muyaya.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:12

“Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 32:9

Sikuti ukalamba wokha ndiwo umasandutsa anthu kuti akhale anzeru, si kukhwima kokha kumene kumachititsa kuti anthu azimvetsa zimene zili zoyenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 92:14-15

Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba, nthaŵi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriŵira, imaonetsa kuti Chauta ndi wolungama. Iye ndiye thanthwe langa mwa Iye mulibe chokhota.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:7

Muzikumbukira atsogoleri anu amene ankakulalikirani mau a Mulungu. Muzilingalira za moyo wao ndi m'mene adafera, ndipo muzitsanzira chikhulupiriro chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:8

Ngati wina aliyense saŵapatsa zofunika achibale ake, makamaka a m'banja mwake momwe, ameneyo wataya chikhulupiriro chake, ndipo kuipa kwake nkoposa kwa munthu wosakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:24

Bambo wa mwana waulemu adzakondwa kwambiri. Wobala mwana wanzeru adzasangalala naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:29

Kukongola kwa achinyamata kwagona pa nyonga zao, koma ulemerero wa nkhalamba wagona pa imvi zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:20

Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake, koma mwana wopusa amanyoza amai ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 12:12

Inde anthu okalamba ali ndi nzeru, anthu amvulazakale ndi omvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:19

lemekeza atate ako ndi amai ako, ndiponso konda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 27:16

“Atembereredwe aliyense wosalemekeza atate ndi amai ake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:9

Musanditaye nthaŵi ya ukalamba wanga, musandisiye ndekha pamene mphamvu zanga zatha,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:7

Inunso amuna, muzikhala moŵamvetsa bwino akazi anu. Muziŵachitira ulemu popeza kuti iwowo ndi mtundu wofookerapo, ndiponso ngolandira nanu pamodzi mphatso ya Mulungu, imene ili moyo wosatha. Muzitero, kuti pasakhale kanthu koletsa mapemphero anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:1-3

Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera. Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana. Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga. Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji. Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu. Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu. Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana. Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani. Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu. Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima. Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo. Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira. Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye. Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima. Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro. Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse. Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:5

Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:3-4

Zoonadi, ana ndi mphatso yochokera kwa Chauta, zidzukulu ndi mphotho yake. Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 92:12-14

Anthu okondweretsa Mulungu zinthu zimaŵayendera bwino ngati mitengo ya mgwalangwa, amakula ngati mikungudza ya ku Lebanoni. Ali ngati mitengo yookedwa m'Nyumba ya Chauta, yokondwa m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu. Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba, nthaŵi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriŵira,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:10

Usamafunsa kuti, “Chifukwa chiyani masiku amakedzana anali abwino kupambana masiku ano?” Limeneli si funso lanzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:2-3

Uuze amuna achikulire kuti azikhala osaledzera, ochita zachiukulu, a maganizo anzeru, olimba pa chikhulupiriro, pa chikondi ndi pa kusatepatepa. Chimodzimodzinso azimai achikulire, uŵauze kuti azikhala ndi makhalidwe oyenera azimai oyera mtima. Asakhale osinjirira anzao kapena akapolo a zoledzeretsa. Akhale alangizi abwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 12:8

Koma Rehobowamu adanyozera zimene madoda aja adaamlangiza, nakapempha nzeru kwa achinyamata anzake, amene adaakula naye pamodzi namamtumikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:20

Mwana wanga, uzitsata malamulo a atate ako, usasiye zimene adakuphunzitsa amai ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:6

Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:7

Kumbukirani zakale, lingalirani zamakedzana ndithu, funsani atate anu, akuuzani zimene zidachitika. Funsani akuluakulu, akufotokozerani zakalezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:12-13

Abale, tikukupemphani kuti muziŵalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene Ambuye adaŵaika kuti azikutsogolerani ndi kumakulangizani. Mwa chikondi muziŵachitira ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yao. Muzikhalitsana ndi mtendere pakati panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:17

Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga, ndipo ndikulalikabe ntchito zanu zodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:20

Uzimvera malangizo ndi kuvomera mwambo, kuti ukhale ndi nzeru m'tsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:7

Munthu wabwino anzake adzamkumbukira ngati dalitso, pamene woipa, mbiri yake idzatha ngati chinthu choola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:17

Akulu a mpingo otsogolera mpingo bwino, akhale oyenera kuŵalemekeza moŵirikiza, makamaka amene amagwira ntchito yolalika mau a Mulungu ndiponso yophunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:1

Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake, koma mwana wopusa amanyoza amai ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:1-2

Ana inu, mverani malangizo a atate anu, tcherani khutu, kuti mupate nzeru zodziŵira zinthu. Mwana wanga, umvere ndi kuvomera zimene ndikunena. Ukatero, zaka za moyo wako zidzachuluka. Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru. Ndakutsogolera pa njira za moyo wolungama. Ukamayenda, mapazi ako sazidzaombana. Ukamathamanga, sudzakhumudwa ai. Uŵasamale zedi, pakuti moyo wako wagona pamenepo. Usayende m'njira za anthu oipa, usatsate m'mapazi mwa anthu ochimwa. Njira zao uzipewe, usapitemo konse. Uzilambalale, ndi kungozipitirira. Iwo ajatu sangagone, mpaka atachita ndithu choipa. Tulo sangatiwone, mpaka atakhumudwitsapo munthu. Paja kuchita zoipa ndiye chakudya chao, kuchita ndeu ndiye chakumwa chao. Koma njira ya anthu okondweretsa Mulungu, ili ngati kuŵala kwa mbandakucha, kumene kumanka kukukulirakulira mpaka dzuŵa litafika pamutu. Njira ya anthu oipa ili ngati mdima wandiweyani. Satha kuzindikira kuti aphunthwa pa chiyani. Ine ndikukupatsani malamulo abwino, musasiye zimene ndikukuphunzitsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 5:26

Udzafika ku manda utakalamba, monga m'mene zokolola zimachera pa nyengo yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 29:8-9

anyamata akandiwona ankapatuka, ndipo madoda ankadzambatuka nkukhala chilili. Akalonga ankakhala chete, atangoti pakamwa gwirire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:1-2

Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa, koma mtima wako usunge malamulo anga. Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo. Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye. Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo. Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu. Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha. Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika. Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 92:14

Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba, nthaŵi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriŵira,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:20

Mudzanditsitsimutsanso Inu amene mwandiwonetsa mavuto ambiri oŵaŵa, mudzanditulutsanso m'dzenje lozama la pansi pa nthaka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 90:10

Zaka za moyo wathu nzokwanira makumi asanu ndi aŵiri, tikakhala amphamvu, ndiye makumi asanu ndi atatu. Koma zaka zonsezo ndi za nkhaŵa ndi mavuto. Zakazo zimatha msanga, ife nkumapita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:16

Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:12

Munthu asakupeputse poona kuti ndiwe wachinyamata, koma ukhale chitsanzo kwa akhristu onse pa mau, pa mayendedwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 42:16-17

Pambuyo pake Yobe adakhala ndi moyo zaka 140. Tsono adaona ana ake ndi zidzukulu zake mpaka mbadwo wachinai. Potsiriza Yobe adamwalira, ali nkhalamba ya masiku ochuluka zedi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:18

Choncho Inu Mulungu, musandisiye ndekha ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbu, mpaka nditalalika mphamvu zanu kwa mibadwo yonse yakutsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:17

Aliyense amene amaseka bambo ndi kumanyozera kumvera mai, makwangwala akuchigwa adzamkoloola maso, ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:33

Kuwopa Chauta kumaphunzitsa nzeru, ndipo ndi kudzichepetsa ndi ulemu, chili patsogolo nkudzichepetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:6

Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba, ulemerero wa ana ndi atate ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:4

Paja Mulungu adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 15:15

Tsono iwe udzakhala ndi moyo nthaŵi yaitali ndipo udzafa mwamtendere. Udzaikidwa m'manda utakalamba kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:4-7

Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa. Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:17

Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:23

Mwamuna wake ndi wodziŵika ndithu ku mabwalo, akakhala pakati pa akuluakulu a dziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:8-9

Mwana wanga, umvere zimene bambo wako akukulangiza, usakane zimene mai wako akukuphunzitsa. Zili ngati nsangamutu yokongola yamaluŵa pamutu pako, zili ngati mkanda wa m'khosi mwako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 12:2

Tsopano mfumu ndiyo izikutsogolerani. Ine nkukalamba kuno, kumutuku imvi zati mbuu, ndipo ana anga muli nawo pamodzi. Ndakhala ndikukutsogolerani kuyambira ndili mnyamata mpaka pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 3:5

Anthu adzazunzana, aliyense adzazunza mnzake. Anyamata adzachita chipongwe akuluakulu, ndipo anthu achabechabe adzanyoza olemekezeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:25

Ku Yerusalemuko kunali munthu wina, dzina lake Simeoni. Anali munthu wolungama ndi woopa Mulungu. Ankayembekezera nthaŵi yoti Mulungu adzapulumutse Aisraele, ndipo Mzimu Woyera anali naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 14:10-11

Kalebe adapitiriranso kunena kuti, “Koma tsopano, papita zaka 45 Chauta atauza kale Mose zimenezi. Taonani, ndili ndi zaka 85 tsopano, komabe ndikadali ndi mphamvu lero, monga ndidaaliri muja, pamene Mose adandituma. Ndikadali wamphamvu, mwakuti ndingathe kumenya nkhondo ndithu, ndiponso ndingathe kuchita zina zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 12:13-14

Ndiye mfumuyo idaŵayankha anthuwo mwankhanza. Idanyozera malangizo a madoda aja, nilankhula nawo anthuwo potsata malangizo a anyamata anzake, nkunena kuti, “Bambo wanga ankakusenzetsani goli lolemetsa, koma ine ndidzaonjezerapo. Bambo wanga ankakukwapulani ndi zikoti wamba, koma ine ndidzakukwapulani ndi mikwapulo yachitsulo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:4

Sitidzabisira ana ao, koma tidzafotokozera mbadwo wakutsogolo ntchito zotamandika za Chauta, tidzaŵasimbira mphamvu zake ndi zodabwitsa zimene wakhala akuchita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:17

“ ‘Mulungu akuti, Pa masiku otsiriza ndidzaika Mzimu wanga mwa anthu onse, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi azidzalalika za Mulungu. Anyamata anu azidzaona zinthu m'masomphenya, ndipo nkhalamba zanu zizidzalota maloto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 19:26-27

Pamene Yesu adaona amai ake ndi wophunzira uja amene Iye ankamukonda kwambiri, akuimirira pafupi, adauza amai ake kuti, “Mai, nayu mwana wanu.” Adauzanso wophunzirayo kuti, “Naŵa amai ako.” Ndipo kuyambira pamenepo wophunzirayo adaŵatenga amaiwo kumakaŵasamala kwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:5

Ndimakumbukira chikhulupiriro chako chosanyenga. Chikhulupiriro chimenechi adaayamba ndi agogo ako aLoisi kukhala nacho. Amai ako aYunisi anali nachonso, ndipo tsopano sindikukayika konse kuti iwenso uli nacho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 12:13

“Koma Mulungu ali ndi nzeru ndi mphamvu zopambana. Ali ndi uphungu wabwino, ndi kumvetsa zinthu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:15

Zimene amachita munthu wopusa mwiniwakeyo amaziyesa zolungama, koma munthu wanzeru amamvetsera malangizo a ena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:28

Usasendeze malire akalekale amene makolo ako adaŵaika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:9

Tinali nawo azibambo athu apansipano amene ankatilanga, ndipo tinkaŵalemekeza. Kwenikweni tsono tikadayenera kugonjera Mulungu, Atate a mizimu, kuti tikhale ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 4:9

Mukhale tcheru, ndipo musadzaiŵale zonse zimene mudaziwona. Zimenezo zisachoke m'mitima mwanu pa moyo wanu wonse. Muzizifotokoza kwa ana anu ndi kwa zidzukulu zanu zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:5-6

Inu Ambuye, ndinu amene ndimakukhulupirirani, Inu Chauta, ndinu amene ndimakudalirani kuyambira ubwana wanga. Inu mwakhala wondichirikiza kuyambira pa nthaŵi imene ndidabadwa. Inu ndinu amene mudanditulutsa m'mimba mwa mai wanga. Ndimatamanda Inu nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:14

Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa, koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:4

Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 21:2

Choncho Sarayo adatenga pathupi, nabalira Abrahamu mwana wamwamuna pamene Abrahamuyo anali nkhalamba. Mwana ameneyu adabadwa pa nthaŵi yeniyeni imene Mulungu adaanena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 48:9

Yosefe adayankha kuti “Ameneŵa ndi ana anga amene Mulungu adandipatsa ku Ejipito kuno.” Apo Yakobe adati, “Chonde abwere kuno anawo kuti ndiŵadalitse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:6

Aŵiri onsewo anali olungama pamaso pa Mulungu, ndipo ankatsata mokhulupirika malamulo ndi malangizo onse a Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 42:10

Choncho Yobe ataŵapempherera abwenzi ake aja, Chauta adambwezera chuma chake. Adampatsa moŵirikiza kuposa zimene adaali nazo kale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 17:1

Abramu ali wa zaka 99, Chauta adamuwonekera namuuza kuti, “Ine ndine Mulungu Mphambe. Tsono uzindimvera nthaŵi zonse, ndipo uzichita zolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:3-4

Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 45:9

Tsopano fulumirani, bwererani kwa bambo wanga, mukamuuze kuti mwana wanu Yosefe akunena kuti, ‘Mulungu wandikuza mpaka kukhala wolamulira Ejipito yense, tsono bwerani kuno, musachedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:36-37

Kunalinso mneneri wina wamkazi, dzina lake Anna, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere. Anali wokalamba kwambiri. Anali atakhala pa banja zaka zisanu ndi ziŵiri zokha, pambuyo pake nkukhala wamasiye kufikira msinkhu wa zaka 84. Sankachokatu ku Nyumba ya Mulungu, ankakonda kudzatumikira Mulungu usana ndi usiku pakupemphera ndi kusala zakudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:10

Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:1-5

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera. Satilanga moyenerera machimo athu, satibwezera molingana ndi zolakwa zathu. Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta. Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife. Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza. Amadziŵa m'mene adatipangira, amakumbukira kuti ife ndife fumbi. Kunena za munthu, masiku ake sakhalitsa, ali ngati a udzu, munthuyo amakondwa ngati duŵa lakuthengo. Koma mphepo ikaombapo, duŵalo pamakhala palibe, siliwonekanso pa malo ake. Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama. Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake. Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba, ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake. Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, ndipo usaiŵale zabwino zake zonse. Tamandani Chauta, inu angelo ake, inu amphamvu amene mumamva mau ake, amene mumachita zimene amalamula. Tamandani Chauta, inu magulu a ankhondo ake onse, atumiki ake ochita zimene Iye afuna. Tamandani Chauta, inu zolengedwa zake zonse, ku madera onse a ufumu wake. Nawenso mtima wanga, tamanda Chauta! Ndiye amene amakhululukira machimo ako onse, ndi kuchiritsa matenda ako onse. Ndiye amene amapulumutsa moyo wako ku manda. Amakuveka chikondi chake chosasinthika ndiponso chifundo chake ngati chisoti chaufumu. Ndiye amene amakupatsa zabwino nthaŵi zonse za moyo wako, choncho umakhalabe wa mphamvu zatsopano ngati mphungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:8

Pakamwa panga pakutamanda Inu, pakulalika ulemerero wanu tsiku lonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 9:10

Kulemekeza Chauta ndiye chiyambi cha nzeru, kudziŵa Woyera uja nkukhala womvetsa bwino zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:26

Munthu woopa Chauta ali ndi chikhulupiriro cholimba, ndipo ana ake adzakhala napo pothaŵira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 4:13

Mnyamata wosauka ndi wanzeru ali bwino kupambana mfumu yokalamba ndi yopusa, imene siikumvanso malangizo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:2

Aliyense mwa ife azikondweretsa mnzake, ndi kumchitira zabwino, kuti alimbikitse chikhulupiriro chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 12:9

koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Zikomo Ambuye chifukwa ndinu wochiritsa wanga, wopereka wanga, ndi wolinda wanga, ndinu amene mumalowerera nkhondo zanga ndi kunditsogolera kuchokera ku ulemerero kupita ku ulemerero. M'dzina lamphamvu la Yesu ndikufikira kwa inu Mulungu wanga, kuti munditsogolere pa gawo lililonse la moyo wanga kudzera mwa Mzimu wanu wabwino. Ndikudziwa kuti chikondi chanu ndi chifuniro chanu n'chabwino kuposa moyo, chifukwa chake ngakhale ndili wamng'ono ndikufuna kukupatsani zonse zomwe ndili nazo kuti mudzidziwitse mwa ine ndipo monga woumba mbiya muumbe mtima wanga. Mzimu Woyera ndikupemphani kuti mundithandize kukondweretsa Mulungu ndi zochita zanga, maganizo anga ndi zolinga zanga kuti zonse zomwe ndingachite m'moyo uno zomwe zatsala patsogolo zikhale za ulemerero wanu osati za kuonekera kwa anthu. Ndilengeza mwazi wa Khristu pa thupi langa ndi mtima wanga, ndilengeza kuti palibe mliri udzakhudza nyumba yanga, ndilengeza kuti zabwino ndi chifundo cha Ambuye zinditsata tsiku lililonse la moyo wanga. Mawu anu amati: "Munthu ali ngati udzu, masiku ake ali ngati maluwa a kuthengo." Mulungu wa chipulumutso changa ndikupemphani kuti masiku anga adzazidwe ndi mtendere wanu ndi chikondi chanu, munditsukire ndi hisopo ndipo muone ngati pali njira yoipa mwa ine ndipo mundilanditse ku kuchita zoipa. M'dzina la Yesu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa