Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani.
Ndipo adaona ngati timalaŵi ta moto tooneka ngati malilime tikugaŵikana nkukhala pa iwo, aliyense kakekake. Paja iye anali mneneri, ndipo ankadziŵa zimene Mulungu adamlonjeza molumbira zakuti mmodzi mwa zidzukulu zake ndiye adzaloŵe ufumu wake. Ndiye kuti Davideyo adaaoneratu zimenezi, zakuti Khristu adzauka kwa akufa, ndipo pamenepo adanena mau aja akuti, “ ‘Iye sadasiyidwe ku Malo a anthu akufa, ndipo thupi lake silidaole.’ Yesu yemweyo Mulungu adamuukitsadi kwa akufa, ndipo tonsefe ndife mboni za zimenezi. Iye adakwezedwa kukakhala ku dzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera, amene Atate adaalonjeza. Ndipo zimene mukuwona ndi kumvazi ndiye mphatso yake imene watitumizira. Pajatu Davide sadakwere kupita Kumwamba, koma iye yemwe adati, “ ‘Ambuye adauza Mbuye wanga kuti, Khala ku dzanja langa lamanja mpaka ndisandutse adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’ “Tsono Aisraele onse adziŵe ndithu kuti Yesu uja inu mudampachika pamtandayu, Mulungu adamsankhula kuti akhale Ambuye ndi Mpulumutsi.” Pamene anthu aja anamva zimenezi, zidaŵalasa mtima, ndipo adafunsa Petro ndi atumwi ena aja kuti, “Abale, tsono ifeyo tichite chiyani?” Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Paja zimene Mulungu adalonjeza zija, adalonjezera inuyo, ana anu ndiponso anthu onse okhala kutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaŵaitana.” Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankaŵalankhulitsira.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
Mzimu wa Chauta udzakhala pa Iye, mzimu wopatsa nzeru ndi kumvetsa, mzimu wopatsa uphungu ndi mphamvu, mzimu wopatsa kudziŵa zinthu ndi kuwopa Chauta.
Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene aŵapempha.”
Tsono tikamati, “Ambuye,” tikunena Mzimu Woyera. Ndipo kumene kuli Mzimu wa Ambuye, kuli ufulu.
Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Ndidzaika mzimu wanga mwa inu, ndipo ndidzakutsatitsani malangizo anga, ndi kukusungitsani malamulo anga mosamala kwambiri.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka.
Koma akadzafika Mzimu wodziŵitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ai, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziŵitsani zinthu zam'tsogolo. Adzandilemekeza, pakuti adzatenga zochokera kwa Ine nadzakudziŵitsani.
Ndipo sindidzaleka kukondwa podziŵa kuti chifukwa cha mapemphero anu ndiponso chithandizo cha Mzimu wopatsidwa ndi Yesu Khristu ndidzamasulidwa.
Mboni za zimenezi ndi ifeyo ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu adampereka ngati mphatso kwa anthu omvera Iye.”
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”
Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu.
Kudzera mwa Iye mumakhulupirira Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa, namupatsa ulemerero. Ndipo choncho chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu zili mwa Mulungu.
Pakuti khalidwelo limalakalaka zotsutsana ndi zimene Mzimu Woyera afuna, ndipo zimene Mzimu Woyera afuna zimatsutsana ndi zimene khalidwe lokonda zoipalo limafuna. Ziŵirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mufuna kuchita.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso.
“Ngati mundikonda, muzidzatsata malamulo anga. Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthaŵi zonse. Nkhosweyo ndi Mzimu wodziŵitsa zoona. Anthu ongokonda zapansipano sangathe kumlandira ai, chifukwa samuwona kapena kumdziŵa. Koma inu mumamdziŵa, chifukwa amakhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu.
Ndikupempha Mulungu kuti kuchokera m'chuma cha ulemerero wake akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu. Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi.
Ifeyo Mulungu adatiwululira zimenezi mwa Mzimu Woyera. Pajatu Mzimuyo amadziŵa zinthu zonse kotheratu, ngakhalenso maganizo ozama a Mulungu.
Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka. Ndipo Mulungu amene amayang'ana za m'kati mwa mitima ya anthu, amadziŵa zimene Mzimu Woyera afuna, pakuti Mzimuyo amapempherera anthu a Mulungu monga momwe Mulungu afunira.
Kodi za munthu angazidziŵe ndani, osakhala mzimu wa mwiniwake yemweyo umene uli mwa iyeyo? Momwemonso palibe munthu amene angadziŵe za Mulungu, koma Mzimu wa Mulungu Mwini.
ndipo ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate aulemerero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatsani nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziŵe kwenikweni.
Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse.
Tsono iye adandiwuza kuti ndidziŵitse Zerubabele uthenga wa Chauta wakuti, “Inde udzapambana, koma osati ndi nkhondo kapena ndi mphamvu, koma ndi mzimu wanga.
Phunzitseni, kuti ndizichita zofuna Inu, pakuti ndinu Mulungu wanga. Mzimu wanu wabwino unditsogolere pa njira yanu yosalala.
Kodi inu simudziŵa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu?
Tikudziŵa kuti timakhala mwa Mulungu, ndipo Iyenso amakhala mwa ife, chifukwa adatipatsa Mzimu wake Woyera.
Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe? Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.
Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.
Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankaŵalankhulitsira.
Koma akadzafika Mzimu wodziŵitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ai, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziŵitsani zinthu zam'tsogolo.
Munthu wotsata malamulo a Mulungu, amakhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu amakhala mwa iye. Chifukwa cha Mzimu Woyera amene adatipatsa, timadziŵa kuti Mulungu amakhaladi mwa ife.
Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lopendekera ku zoipa. Mumalamulidwa ndi Mzimu Woyera, ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu sali wake wa Khristu.
Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza. Mzimu Woyerayo ndiye chikole chotsimikizira kuti tidzalandiradi madalitso onse amene Mulungu adalonjeza kupatsa anthu ake, ndipo kuti Mulungu adzapulumutsa kwathunthu anthu amene adaŵaombola kuti akhale ake enieni. Cholinga cha zonsezi ndi chakuti tilemekeze ulemerero wake.
Paja Malembo akuti, ‘Munthu wokhulupirira Ine, mtima wake udzakhala ngati gwelo la mitsinje ya madzi opatsa moyo.’ ” (Pakutero Yesu ankanena za Mzimu Woyera amene anthu okhulupirira Iye analikudzalandira. Nthaŵi imeneyo nkuti Mzimu Woyera asanafike, chifukwa Yesu anali asanalandire ulemerero wake.)
Petro akulankhulabe, Mzimu Woyera adaŵatsikira anthu onse amene ankamva mauwo. Ndipo okhulupirira achiyuda amene adaaperekeza Petro, adadabwa kuti Mulungu adapereka mphatso ya Mzimu Woyera ndi kwa anthu akunja omwe. Pakuti adaŵamva akulankhula zilankhulo zosadziŵika ndi kutamanda ukulu wa Mulungu. Tsono Petro adati, “Anthu aŵa alandira Mzimu Woyera monga ife. Nanga alipo amene angaŵaletse kubatizidwa ndi madzi?”
natisindikiza chizindikiro chake, ndi kuika Mzimu Woyera m'mitima mwathu ngati chikole.
Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera amene Mulungu adakusindikizani chizindikiro chake chotsimikizira kuti ndinu ake pa tsiku limene Mulunguyo adzatipulumutse kwathunthu.
Ife sitidalandire mzimu wa dziko lino lapansi, koma tidalandira Mzimu Woyera wochokera kwa Mulungu, kuti adzatithandize kumvetsa zimene Mulunguyo adatipatsa mwaulere. Timalankhula zimenezi osati ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za anthu, koma ndi mau amene Mzimu Woyera amatiphunzitsa. Timaphunzitsa zoona zauzimu kwa anthu amene ali naye Mzimu Woyera.
Pofuna kutsimikiza kuti ndinu ana ake, Mulungu adatitumizira Mzimu wa Mwana wake m'mitima mwathu, ndipo Mzimuyo amatinenetsa kuti, “Abba! Atate!”
ndipo adaŵafunsa kuti, “Kodi mudalandira Mzimu Woyera pamene mudakhulupirira?” Iwo adati, “Nkumva komwe sitinamve kuti kuli Mzimu Woyera.”
Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati munthu sabadwa m'madzi ndi mwa Mzimu Woyera, sangathe kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu. Chobadwa mwa munthu ndi thupi chabe, koma chobadwa mwa Mzimu Woyera ndi mzimu.
“ ‘Mulungu akuti, Pa masiku otsiriza ndidzaika Mzimu wanga mwa anthu onse, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi azidzalalika za Mulungu. Anyamata anu azidzaona zinthu m'masomphenya, ndipo nkhalamba zanu zizidzalota maloto. Ndithu, pa masiku amenewo ndidzaika Mzimu wanga ngakhale mwa akapolo anga aamuna ndi aakazi, ndipo azidzalalika za Mulungu.
Ndikupempha Mulungu kuti kuchokera m'chuma cha ulemerero wake akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu.
Mulungu yemwe ankachitira umboni pakuchita zizindikiro, zinthu zozizwitsa ndi ntchito zamphamvu zamitundumitundu, ndi pakuŵagaŵira mphatso za Mzimu Woyera monga momwe Iye ankafunira.
“Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa,
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Nkhosweyo ndi Mzimu wodziŵitsa zoona. Anthu ongokonda zapansipano sangathe kumlandira ai, chifukwa samuwona kapena kumdziŵa. Koma inu mumamdziŵa, chifukwa amakhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu.
Iwowo atafika, adayamba kupempherera okhulupirira aja kuti alandire Mzimu Woyera. Nthaŵiyo nkuti Mzimu Woyera asanafike pa wina aliyense mwa iwo. Onsewo anali atangobatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu. Tsono Petro ndi Yohane adaŵasanjika manja, ndipo adalandira Mzimu Woyera.
Khristu adachita zimenezi, kuti dalitso limene Mulungu adaalonjeza Abrahamu, lipatsidwe kwa anthu a mitundu yonse kudzera mwa Khristu Yesu, ndipo kuti pakukhulupirira tilandire Mzimu Woyera amene Mulungu adaatilonjeza.
Mulungu adaŵaululira kuti ntchito yaoyi sankaigwira chifukwa cha eniakewo, koma chifukwa cha inu, pamene iwo ankanena zoonazi zimene mwamva tsopano. Olalika Uthenga Wabwino adakuuzani zoonazi mwa mphamvu ya Mzimu Woyera wotumidwa kuchokera Kumwamba. Angelo omwe amalakalaka kuwona nao zinthuzo.
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!” Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu.
Tsopano kudzera mwa Khristu ife tonse, Ayuda ndi a mitundu ina, tingathe kufika kwa Atate mwa Mzimu Woyera mmodzi yemweyo.
Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.”
Choncho adatipulumutsa osati chifukwa cha ntchito zolungama zimene ife tidaachita, koma mwa chifundo chake pakutisambitsa. Adatisambitsa mwa Mzimu Woyera pakutibadwitsa kwatsopano ndi kutipatsa moyo watsopano.
Motero munthu wokana mau ameneŵa, sakukana munthu chabe ai, koma akukana Mulungu amene amakupatsani Mzimu wake Woyera.