Baibulo limatiuza nkhani zambiri zomwe zinachitika m'mawa kwambiri, zinthu zazikulu zomwe Mzimu Woyera anatilembeletsa kuti tidziwe mphamvu ya nkhondo yauzimu yomwe imachitika tikamadikira Mulungu usiku. Mulungu akutikopa chidwi chathu, akufuna kutidziwitsa kuti kupemphera usiku sikofanana ndi kupemphera masana, makamaka m'mawa kwambiri, ndipo Mawu a Mulungu amatiuza kuti timvere zimene mzimu wathu ukutiuza. Aefeso 6:18 (Buku Lopatulika) amatiuza kuti tizipemphera nthawi zonse, m'njira zosiyanasiyana, motsogozedwa ndi Mzimu Woyera, ndiponso kuti tiziyang'anira ndi mtima wonse, kupempherera oyera mtima onse. Kudikira Mulungu usiku kumatanthauza kukhala maso usiku wonse (kapena gawo lake). Kumatanthauzanso kukhala mlonda usiku. Mwachidule, kudikira Mulungu usiku kumatikumbutsa kuti tikhale maso m'dziko lino lomwe lili mu mdima wauzimu. Tikakhala ndi nkhawa, tizikhala maso usiku, kufunafuna chitonthozo cha Mulungu: "Dzuka, lira usiku, poyamba maulonda; kuthira mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye; kweza manja ako kwa Iye." (Maliro 2:19 - Buku Lopatulika)
Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”
Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye.
Muzikhala maso tsono, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse, kuti mukhale ndi mphamvu zopulumukira ku zonsezi zimene ziti zidzachitike, ndiponso kuti mukaimirire pamaso pa Mwana wa Munthu.”
Nchifukwa chake tsono tisagone tulo monga momwe amachitira anthu ena, ife tikhale maso, tikhale osaledzera.
Mtima wanga umayembekeza Chauta kupambana m'mene alonda amayembekezera mbandakucha, kupambanadi m'mene alonda amayembekezera mbandakucha.
Muchite zimenezi chifukwa mukudziŵa kuti yafika kale nthaŵi yakuti mudzuke kutulo. Pakuti chipulumutso chili pafupi tsopano kuposa pamene tidayamba kukhulupirira.
Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu.
Ngodala antchito amene mbuye wao pofika, aŵapeza ali maso. Ndithu ndikunenetsa kuti adzadzikonzekera, nadzaŵakhazika podyera, ndipo adzabwera nkumaŵatumikira.
Mverani, alonda anu akukweza mau, akuimba pamodzi mokondwa, popeza kuti akuwona chamaso Chauta akubweranso ku Ziyoni.
Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”
Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.
Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe.
Koma ife kwathu kwenikweni ndi Kumwamba, ndipo kumeneko kudzachokera Mpulumutsi amene tikumuyembekeza. Mpulumutsiyo ndi Ambuye Yesu Khristu.
Atsogoleri onse a Israele ndi akhungu, onsewo ndi opanda nzeru konse. Ali ngati agalu opanda mau, osatha kuuwa. Ntchito nkulota, kugona pansi, kukondetsa tulo.
Pomaliza Yesu adati, “Ndiyetu inu, muzikhala maso, poti simudziŵa tsiku lake kapena nthaŵi yake.”
Khala bata pamaso pa Chauta, ndipo umdikire mosadandaula. Usavutike ndi munthu amene zake zikumuyendera bwino, ndi munthu amene amatha kuchitadi zoipa zimene wakonza.
Koma iwe, uzikhala maso pa zonse, pirira pa zoŵaŵa, gwira ntchito yolalika Uthenga Wabwino. Kwaniritsa udindo wako mosamala.
Tsono ananu, khalani mwa Iye, kuti tikakhale olimba mtima Iye akadzaoneka, ndipo tisadzachite manyazi Iye akadzabweranso.
Ngodala antchitowo mbuye waoyo akadzaŵapeza ali choncho pamene iye adzafike, ngakhale pakati pa usiku kapena kuli pafupi kucha.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Abale, mchenjere, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woipa ndi wosakhulupirira, womlekanitsa ndi Mulungu wamoyo. Kwenikweni muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku ikadalipo nthaŵi, imene m'mau a Mulungu imatchedwa kuti, “Lero”. Muzichita zimenezi, kuwopa kuti wina aliyense mwa inu angaumitsidwe mtima ndi chinyengo cha uchimo.
Ngwodala munthu amene amatchera khutu kwa ine, amene amakhala pakhomo panga tsiku ndi tsiku, amene amadikira pa chitseko changa.
Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani.
Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka.
Motero chilichonse choonekera poyera, chimasanduka kuŵala. Nchifukwa chake amati, “Dzuka wam'tulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuŵalira.”
Letsani maso anga kuti asamayang'ane zachabe, mundipatse moyo monga momwe mudalonjezera.
ndipo adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukugona? Dzukani ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani.”
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo, kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi, pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe.
Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chachabechabe. Ndimadana ndi zochita za anthu okusiyani, sizindikomera konse.
Dzuka, dzuka, vala dzilimbe iwe Ziyoni. Vala zovala zako zabwino, iwe Yerusalemu, mzinda woyera. Anthu osaumbalidwa ndi onyansa pa chipembedzo sadzaloŵanso pa zipata zako.
“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba.
Tsono nditaona, ndidayamba kuganizirapo pa zimenezo, nditayang'ana, ndidatolapo phunziro ili: Ukati, “Taimani ndigoneko pang'ono,” kapena “Ndiwodzereko chabe,” kapena “Ndingopumulako pang'ono,” umphaŵi udzakufikira monga mbala, kusauka kudzakupeza ngati mbala yachifwamba.
Chimalizo cha zonse chayandikira. Nchifukwa chake khalani ochenjera ndi odziletsa, kuti muthe kupemphera.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse.
Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma wopusa amangopitirira ndipo amanong'oneza bondo.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye. Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima. Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu, chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa, chipulumutso changa, ndi linga langa. Sindidzagwedezeka konse.
“Pa nthaŵi imeneyo za Ufumu wakumwamba zidzafanafana ndi zimene zidaachitikira anamwali khumi. Iwowo adaatenga nyale zao nkumakachingamira mkwati. Pamene ankakagula, mkwati adafika. Amene anali okonzekeratu aja adaloŵa naye pamodzi m'nyumba yaphwando; pambuyo pake adatseka chitseko. “Kenaka m'mbuyomwalendo anamwali ena aja nawonso adabwera nati, ‘Bwana, Bwana, titsekulireni!’ Koma mkwatiyo adati, ‘Pepani, sindikukudziŵani!’ ” Pomaliza Yesu adati, “Ndiyetu inu, muzikhala maso, poti simudziŵa tsiku lake kapena nthaŵi yake.” “Za Ufumu wakumwamba tingazifanizirenso motere: Munthu wina ankapita pa ulendo. Asananyamuke adaitana antchito ake, naŵasiyira chuma chake. Wina adampatsa ndalama zisanu, wina ziŵiri, wina imodzi. Aliyense adampatsa molingana ndi nzeru zake, iye nkuchokapo. Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adapita nakachita nazo malonda nkupindula ndalama zinanso zisanu. Chimodzimodzinso amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adapindula ndalama zinanso ziŵiri. Koma amene adaalandira ndalama imodzi uja, adapita nakaikumbira pansi ndalama ya mbuye wake ija. “Patapita nthaŵi yaitali, mbuye wao uja adabwerako naŵaitana antchito ake aja kuti amufotokozere za zimene adaachita ndi ndalama zija. Asanu anali opusa, ndipo asanu enawo anali ochenjera. Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adabwera ndi zisanu zinanso nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama zisanu. Onani, ndidapindula zisanu zinanso: izi.’ Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’ Nayenso wantchito amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adabwera nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama ziŵiri. Onani, ndidapindula ziŵiri zinanso: izi.’ Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’ “Nayenso amene adaalandira ndalama imodzi uja adabwera nati, ‘Ambuye, ine ndinkadziŵa kuti inu ndinu munthu wankhwidzi. Mumakolola kumene simudabzale, ndipo mumasonkhanitsa dzinthu kumene simudafese mbeu. Ndiye ndinkachita mantha, choncho ndidaakaikumbira pansi ndalama yanu ija. Nayi tsono ndalama yanuyo.’ Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa ndi waulesi. Kani unkadziŵa kuti ineyo ndimakolola kumene sindidabzale, ndipo ndimasonkhanitsa dzinthu kumene sindidafese mbeu? Tsonotu udaayenera kukaiika ku banki ndalama yangayo, ine pobwera ndikadadzailandira pamodzi ndi chiwongoladzanja chake. Mlandeni ndalamayi, muipereke kwa amene ali ndi ndalama khumiyo. Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe. Asanu opusa aja adangotenga nyale zao, osatenga mafuta ena apadera.
Chauta akunena kuti, “Fuula kwambiri, usaleke, mau ako amveke ngati lipenga. Uŵauze anthu anga za kulakwa kwao, uŵauze a m'fuko la Yakobe za machimo ao.
Ndimadzuka tambala asanalire, kuti ndipemphe chithandizo. Ndimakhulupirira mau anu.
Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku.
Koma dziŵani kuti mwini nyumba akadadziŵa nthaŵi yofika mbala, bwenzi atakhala maso, osalola kuti mbala imuthyolere nyumba.
Iwo adatifera kuti tikakhale ndi moyo pamodzi naye, ngakhale pamene tili amoyo kapena titafa kale.
Ngodala amene moyo wao ulibe choŵadzudzulira, amene amayenda motsata malamulo a Chauta. Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse, musalole kuti ndisiye kumvera malamulo anu. Ndili ndi nzeru kupambana okalamba, pakuti ndimatsata malamulo anu. Ndimaletsa miyendo yanga kuti isayende m'njira yoipa iliyonse, kuti choncho ndizisunga mau anu. Sindisiyana nawo malangizo anu, pakuti Inu mudandiphunzitsa mau anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Amatsekemera kuposa uchi m'kamwa mwanga. Ndimakhala ndi nzeru za kumvetsa chifukwa cha malamulo anu. Nchifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga. mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga. Ndalumbirira, ndipo ndatsimikiza kuti ndidzamvera malangizo anu olungama. Ndazunzika koopsa, Chauta, patseni moyo, molingana ndi mau anu aja. Chauta, landirani mapemphero anga oyamika, ndipo mundiphunzitse malangizo anu. Moyo wanga uli m'zoopsa nthaŵi zonse, komabe sindiiŵala malamulo anu. Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni. Anthu oipa anditchera msampha, komabe sindisokera kuchoka m'njira ya malamulo anu. Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga. Mtima wanga muuphunzitse kuti uzikonda malamulo anu nthaŵi zonse. Ndimadana nawo anthu apaŵiripaŵiri, koma ndimakonda mau anu. Inu ndinu malo anga obisalako ndiponso chishango changa, ndimakhulupirira mau anu. Chokereni inu, anthu ochita zoipanu, kuti ine ndizitsata malamulo a Mulungu wanga. Chirikizeni molingana ndi malonjezo anu aja, kuti ndizikhala ndi moyo, ndipo anthu asandichititse manyazi, chifukwa ndine wokhulupirika. Chirikizeni kuti ndipulumuke, kuti nthaŵi zonse ndizitsata malamulo anu. Inu mumaŵakana anthu onse osamvera malamulo anu, zoonadi, kuchenjera kwao nkopandapake. Anthu onse oipa a pa dziko lapansi, mumaŵayesa ngati zakudzala, nchifukwa chake ndimakonda malamulo anu. Mutamandike, Inu Chauta, phunzitseni malamulo lanu. Thupi langa limanjenjemera chifukwa chokuwopani, ndimachita mantha ndi kuweruza kwanu. Ndachita zimene zili zolungama ndi zabwino. Musandisiye m'manja mwa ondizunza. Lonjezani kuti mudzandichitira zabwino mtumiki wanune, musalole anthu osasamala za Mulungu kuti andizunze. Maso anga atopa chifukwa cha kuyembekeza chipulumutso chanu, chifukwa cha kudikira kuti malonjezo anu olungama aja achitikedi. Komereni mtima mtumiki wanune, chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, ndipo mundiphunzitse malamulo anu. Ndine mtumiki wanu, mundipatse nzeru zomvetsa, kuti ndizidziŵa malamulo anu. Yakwana nthaŵi yakuti Inu Chauta muchitepo kanthu, popeza kuti anthu aphwanya malamulo anu. Koma ine ndimasamala malamulo anu kupambana golide, golide wosungunula bwino. Malamulo anu onse amalungamitsa mayendedwe anga. Ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga. Malamulo anu ndi abwino, nchifukwa chake ndimaŵatsata ndi mtima wanga wonse. Ndimalalika ndi mau anga malangizo onse a pakamwa panu. Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru. Ndimapuma mwaŵefuŵefu nditatsekula pakamwa, chifukwa ndimalakalaka malamulo anu. Yang'aneni, ndipo mundikomere mtima monga m'mene mumachitira ndi anthu okukondani. Chirikizani mayendedwe anga molingana ndi mau anu aja, musalole kuti tchimo lililonse lizindilamulira. Pulumutseni kwa anthu ondizunza, kuti ndizitsata malamulo anu. Yang'anireni ine mtumiki wanu ndi chikondi chanu, ndipo mundiphunzitse malamulo anu. Maso anga akudza misozi yambiri ngati mitsinje, chifukwa anthu satsata malamulo anu. Ndinu olungama Chauta, ndipo kuweruza kwanu nkolungama. Malamulo amene mwatipatsa, ndi olungama ndi okhulupirika ndithu. Changu changa chikuyaka ngati moto mumtima mwanga, chifukwa adani anga amaiŵala mau anu. Kuyenda m'njira ya malamulo anu kumandikondwetsa, kupambana kukhala ndi chuma chilichonse. Malonjezo anu ndi otsimikizika, ndipo ine mtumiki wanu ndimaŵakonda. Ine ndine wamng'ono ndi wonyozeka, komabe sindiiŵala malamulo anu. Kulungama kwanu nkwamuyaya, ndipo malamulo anu ndi oona. Mavuto andigwera pamodzi ndi zoŵaŵa zomwe, koma malamulo anu amandisangalatsa. Malamulo anu ndi olungama mpaka muyaya, patseni nzeru zomvetsa kuti ndizikhala ndi moyo. Ndikulira kwa Inu ndi mtima wanga wonse, mundiyankhe, Inu Chauta. Ndidzatsata malamulo anu. Ndikukulirirani, mundipulumutse, kuti ndizitsata malamulo anu. Ndimadzuka tambala asanalire, kuti ndipemphe chithandizo. Ndimakhulupirira mau anu. Ndimakhala maso usiku wonse, ndikusinkhasinkha za malonjezo anu. Imvani liwu langa chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. Inu Chauta, sungani moyo wanga chifukwa cha chilungamo chanu. Ndidzasinkhasinkha za malamulo anu, ndipo ndidzatsata njira zanu. Anthu ankhanza ondizunza akuyandikira. Iwo ali kutali ndi malamulo anu. Koma Inu Chauta muli pafupi, ndipo malamulo anu onse ndi oona. Poŵerenga malamulo anu ndidadziŵa kale lomwe kuti Inu mudaŵakhazikitsa mpaka muyaya. Yang'anani masautso anga, ndipo mundipulumutse, popeza kuti sindiiŵala malamulo anu. Munditchinjirize pa mlandu wanga, ndipo mundiwombole. Mundipatse moyo molingana ndi malonjezo anu aja. Chipulumutso chili kutali ndi anthu oipa, pakuti safunafuna malamulo anu. Chifundo chanu nchachikulu, Inu Chauta, mundipatse moyo molingana ndi chilungamo chanu. Anthu ondizunza ndiponso adani anga ngochuluka, koma sindisiyana nawo malamulo anu. Ndimanyansidwa ndikamayang'ana anthu osakhulupirika, chifukwa satsata malamulo anu. Onani m'mene ndimakondera malamulo anu, sungani moyo wanga chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika Ndidzakondwera ndi malamulo anu, ndipo mau anu sindidzaŵaiŵala. mau anu ndi oona okhaokha, malangizo anu onse olungama ngamuyaya. Mafumu amandizunza popanda chifukwa, koma mtima wanga umaopa mau anu. Ndimakondwa ndi mau anu monga munthu amene wapeza chuma chambiri. Ndimadana ndi anthu abodza, zoonadi, ndimanyansidwa nawo, koma ndimakonda malamulo anu. Ndimakutamandani kasanunkaŵiri pa tsiku, chifukwa cha malangizo anu olungama. Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa. Ndimakhulupirira kuti mudzandipulumutsa, Inu Chauta, ndipo ndimatsata malamulo anu. Mzimu wanga umatsata malamulo anu, pakuti ndimaŵakonda ndi mtima wanga wonse. Ndimatsata malamulo anu ndi malangizo anu, pakuti makhalidwe anga onse mukuŵaona. Kulira kwanga kumveke kwa Inu, Chauta. Mundipatse nzeru zomvetsa potsata mau anu aja. Komereni mtima ine mtumiki wanu, kuti ndikhale ndi moyo ndi kusunga mau anu. Kupempha kwanga kumveke kwa Inu. Mundipulumutse potsata malonjezo anu. Pakamwa panga padzakutamandani, chifukwa mumandiphunzitsa malamulo anu. Ndidzaimba nyimbo zoyamikira mau anu, chifukwa malamulo anu onse ndi olungama. Dzanja lanu likhale lokonzeka kundithandiza, chifukwa ndatsata malamulo anu. Ndikulakalaka nthaŵi yoti mudzandipulumutse. Inu Chauta, malamulo anu amandikondwetsa. Lolani kuti ndikhale moyo, kuti ndizikutamandani, ndipo malangizo anu azindithandiza. Ndasokera ngati nkhosa yoloŵerera, koma mundifunefune ine mtumiki wanu, pakuti sindiiŵala malamulo anu. Nyimbo yoimba pokwera ku Yerusalemu. Tsekulani maso anga kuti ndiwone zodabwitsa zochokera m'malamulo anu. Ndine munthu wongokhala nawo pa dziko lapansi, musandibisire malamulo anu. Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta, amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse,
Maso ako aziyang'ana kutsogolo molunjika, uzipenya kutsogolo osacheukacheuka. Uzisamala m'mene mukupita mapazi ako, ndipo njira zako zonse zidzakhala zosapeneketsa. Usapatukire kumanja kapena kumanzere, usayende pamene pali choipa chilichonse.
Tikudziŵa kuti Mwana wa Mulungu adafika, ndipo adatipatsa nzeru kuti timdziŵe Mulungu woona. Ndipo tili mwa Mulungu woonayo, chifukwa tili mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iyeyo ndiye Mulungu woona ndiponso moyo wosatha.
Adaŵauza kuti, “Mumtima mwanga muli chisoni chachikulu chofa nacho. Inu khalani pompano, komatu mukhale maso pamodzi nane.”
Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.
“Chenjerani kuti mitima yanu ingapusitsidwe ndi maphwando, kuledzera, ndi kudera nkhaŵa za moyo uno, kuti tsikulo lingakufikireni modzidzimutsa. Pajatu lidzaŵagwera ngati msampha anthu onse okhala pa dziko lonse lapansi. Muzikhala maso tsono, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse, kuti mukhale ndi mphamvu zopulumukira ku zonsezi zimene ziti zidzachitike, ndiponso kuti mukaimirire pamaso pa Mwana wa Munthu.”
Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka.
M'maŵa, Inu Chauta, mumamva mau anga. M'maŵa ndimapemphera kwa Inu, ndi kudikira kuti mundiyankhe.
Nchifukwa chake mtima wanu ukhale wokonzeka. Khalani tchelu. Khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa kukoma mtima kwa Mulungu pamene Yesu Khristu adzaoneke.
Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.
adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa, pakuti anthu otere satumikira Khristu Ambuye athu, koma amangotumikira zilakolako zao basi. Ndi mau okoma ndi oshashalika amanyenga anthu a mitima yoona.
“Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa. Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu?
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe. Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha. Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi. Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse, Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
pambuyo pake nkukhala wamasiye kufikira msinkhu wa zaka 84. Sankachokatu ku Nyumba ya Mulungu, ankakonda kudzatumikira Mulungu usana ndi usiku pakupemphera ndi kusala zakudya.
Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu. Kukumveka mau akuti, “Konzani njira ya Chauta m'thengo, lungamitsani mseu wa Mulungu wathu m'chipululu. Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufooka, ngakhale anyamata amaphunthwa ndi kugwa. Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe.
Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.
Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera amene Mulungu adakusindikizani chizindikiro chake chotsimikizira kuti ndinu ake pa tsiku limene Mulunguyo adzatipulumutse kwathunthu.
“Mumvetse bwino! Ndikukutumani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. Ndiye inu khalani ochenjera ngati njoka, ndi ofatsa ngati nkhunda.
Motero munthu amakhulupirira chifukwa cha zimene wamva, ndipo zimene wamvazo zimachokera ku zolalika za Khristu.
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera.
Onseŵa ankalimbikira kupemphera ndi mtima umodzi, pamodzi ndi akazi ena, ndi Maria amai ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.
“Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani.
Nchifukwa chake muzilimbitsana mtima ndi kumathandizana, monga momwe mukuchitiramu.
Kodi wina mwa inu akudwala? Aitanitse akulu a mpingo. Iwowo adzampempherere ndi kumdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye. Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo.
Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu.
Muzipemphera mosafookera, ndipo pamene mukupemphera, muzikhala tcheru ndiponso oyamika Mulungu.
Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.
Tsono choyamba ndikukupemphani kuti pakhale mapemphero opempherera anthu onse. Mapemphero ake akhale opemba, opempha ndi othokoza Mulungu.
Ifeyonso muzitipempherera kuti Mulungu atipatse mwai woti tilalike mau ake, makamaka kuti tilengeze chinsinsi chozama chokhudza Khristu. Chifukwa cha kulalika chinsinsichi ndine womangidwa m'ndende muno.
Tikamakupemphererani, nthaŵi zonse timathokoza Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi.