Baibulo limatiuza kuti Mulungu amaona kutali munthu wodzikuza. Kudzikuza ndi khalidwe lomwe silikondweretsa Mulungu, ndipo limapezeka mwa anthu ambiri, kumawapangitsa kudzidalira mopambanitsa ndikuganiza kuti angathe kulamulira chilichonse. Munthu wodzikuza sadziwa zolakwa zake, koma nthawi zonse amaona zolakwa za anzake, n’kunyalanyaza zake.
Njira yokha yothawa mtima umenewu womwe umawononga maganizo ndi mtima wanu, ndikuvomereza Mulungu pa chilichonse chimene muchita. Muziwerama pamaso pake ndi kuvomereza kuti mumadalira Iye, osati mphamvu kapena luso lanu. Koma chifukwa cha chikondi ndi chisomo chake. Ndikukutsimikizirani kuti mukachita izi, chikondi chake chochiritsa chidzakuphimbani, chidzasintha maganizo anu, ndi kukupangani munthu watsopano m’chifaniziro chake.
Dzipumbitsitseni pansi pa dzanja lamphamvu la Yehova, ndipo nthawi yake ikadzakwana adzakukwezani ndi kukuyikani pamalo amene anakukonzerani kuyambira kalekale.
Ngakhale Chauta ndi wamphamvu, amasamalira anthu otsika, koma anthu odzikuza amaŵadziŵira chapatali.
Munthu woipa sasamala Mulungu chifukwa cha kunyada kwake. Mumtima mwake amati, “Kulibe Mulungu.”
Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umadzikuza, koma ulemu umatsatira kudzichepetsa.
Maso odzikuza ndi mtima wonyada zimatsogolera anthu oipa ngati nyale, nchifukwa chake amachimwa.
Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru.
Kudzikuza kwa anthu kudzatha, kudzitama kwa anthu kudzaonongedwa. Chauta yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo.
Chauta, mtima wanga ndi wosadzikuza, maso anga ndi osanyada. Sinditengeka mtima ndi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa.
Ngati munthu adziyesa kanthu, pamene chikhalirecho sali kanthu konse, amangodzinyenga.
Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu.
Koma amatikomera mtima koposa. Nchifukwa chake Malembo akuti, “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma odzichepetsa amaŵakomera mtima.”
Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.”
Paja Malembo akuti, “Wofuna kunyada, anyadire Ambuye.” Pakuti munthu wovomerezeka, si amene amadzichitira yekha umboni, koma amene Ambuye amamchitira umboni.
Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi.
Mathero ake a chinthu ndi abwino kupambana chiyambi chake. Mtima wopirira ndi wopambana mtima wodzikuza. Usamafulumira kukwiya, pakuti mkwiyo umakhalira zitsiru.
Ndidakuuzani zimene Chauta adanena, koma inu simudasamale. Mudaukira Chauta, ndipo mudakaloŵa m'dziko lamapirilo, muli tumbatumba kunyada.
“Kodi iwe wanyoza ndi kulalatira yani? Kodi ndani amene wamufuulira ndi kumuyang'ana monyada? Si wina ai, koma Woyera uja wa Israele!
amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao.
Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi, pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa.
Mathero ake a chinthu ndi abwino kupambana chiyambi chake. Mtima wopirira ndi wopambana mtima wodzikuza.
Munthu wosinjirira mnzake kuseri ndidzamcheteketsa. Wooneka wonyada ndi wodzikuza sindidzamulekerera.
Chipongwe cha osasamala za anzao chimadzetsa mkangano, koma omvera malangizo a anzao ndiwo ali ndi nzeru.
Mau a pakamwa pa munthu wanzeru amakondweretsa, koma pakamwa pa chitsiru mpoononga. Chitsiru chimayamba ndi mau opusa, potsiriza zolankhula zake zimangokhala zamisala basi.
Anthu osasamala za Mulungu amandinyoza kwathunthu, komabe sindisiyana nawo malamulo anu.
Ngati wakhala ukupusa ndi kumadzikweza, kapena wakhala ukukonzekera kuchita zoipa, yamba wati chete, uziganize bwino.
Chauta akuti, “Ndidzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha kuipa kwao, ndidzalanga oipa chifukwa cha kuchimwa kwao. Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza.
“Ndikukuthira nkhondo, mzinda wachipongwewe, pakuti yakwana nthaŵi yako, lafika tsiku lako la chilango,” akutero Chauta Wamphamvuzonse.
Umakhulupirira kuti ndiwe mtsogoleri wa anthu akhungu, nyale younikira anthu amene ali mu mdima,
Kuli bwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu osauka, kupambana kumagaŵana chuma ndi anthu onyada.
Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika, atchera ukonde wa zingwe, anditchera misampha m'mbali mwa njira.
Zimene amachita munthu wopusa mwiniwakeyo amaziyesa zolungama, koma munthu wanzeru amamvetsera malangizo a ena.
Ena amaitana Mulungu koma Iye saŵayankha, chifukwa cha kunyada ndi kuipa kwa anthuwo. Ndithudi, Mulungu saamva kupempha kopanda pake, Mphambe sasamalako zimenezo.
Ukamenya munthu wonyoza anzake, adzachenjererapo. Ukadzudzula munthu womvetsa bwino zinthu, adzapindulapo nzeru.
Akodwe ndi kunyada kwao, chifukwa cha uchimo wa m'kamwa mwao, ndi mau a pakamwa pao. Chifukwa chakuti amatemberera ndipo amanama,
Mumtima mwako unkati, ‘Ndidzakwera mpaka kumwamba. Ndidzakhazika mpando wanga waufumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu. Ndidzakhala pampandopo pa phiri la kumpoto kumene imasonkhanako milungu yonse. Ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanafana naye Wopambanazonse.’
Usamakondwerera kugwa kwa mdani wako, mtima wako usamasangalala iyeyo akaphunthwa. Ukatero Chauta adzaziwona zimenezo nadzaipidwa nazo, kenaka adzaleka kumkwiyira mdani wakoyo.
Ndani mwa inu ali wanzeru ndi womvetsa zinthu? Aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru zimaongoleradi zochita zake zofatsa.
Ndimauza anthu odzitama kuti, “Musadzitame,” ndiponso anthu oipa kuti, “Musadzitukumule chifukwa cha mphamvu zanu. Musadzikuze chifukwa cha mphamvu zanu, kapena kumalankhula zamwano.”
Iye amalamula ndi mphamvu zake mpaka muyaya, maso ake amalonda mitundu ina ya anthu. Anthu oukira asadzikweze.
Nanga adakusiyanitsa ndi anthu ena ndani? Kaya uli ndi chiyaninso chimene sudachite kuchilandira? Tsono ngati udachita kuzilandira, ukunyadiranji ngati kuti sudangozilandira chabe?
Unkanyada chifukwa cha kukongola kwako, udaipitsa nzeru zako chifukwa chofuna kukhala wotchuka. Motero ndidakugwetsa pansi kuti ukhale chenjezo kwa mafumu ena.
Chauta Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku, pamene adzatsitsa onse onyada ndi odzitama, ndipo adzagonjetsa onse amphamvu.
Inu Chauta, tsekani pakamwa ponse pothyasika letsani lilime lililonse lolankhula modzikuza.
Asakhale munthu wolandiridwa mu mpingo chatsopano, kuwopa kuti angadzitukumule nkulangidwa monga momwe Satana adalangidwira.
Chauta amapasula nyumba ya munthu wonyada, koma amasamalira kadziko ka mkazi wamasiye.
Kodi iweyo ndiwe yani kuti uweruze wantchito wamwini kuti walakwa? Mbuye wake yekha ndiye aweruze ngati iye wakhoza kapena walephera pa ntchito yake. Ndipo adzakhoza, popeza kuti Ambuye angathe kumkhozetsa.
“Chenjerani, musachite ntchito zanu zabwino pamaso pa anthu ndi cholinga choti akuwoneni. Mukatero, simudzalandira mphotho kwa Atate anu amene ali Kumwamba.
Anthu onse oipa a pa dziko lapansi, mumaŵayesa ngati zakudzala, nchifukwa chake ndimakonda malamulo anu.
Ngwodala munthu amene amadalira Chauta, munthu amene sapatukira ku mafano kapena kutsata milungu yonama.
Munthu wa mtima wanzeru adzasamala malamulo, koma chitsiru chomangolongolola chidzaonongeka.
Nzoona, iwo adakadzukadi chifukwa sadakhulupirire, ndipo inu pakukhulupirira, mukukhala mu mtengo tsopano. Komatu tsono musamadzitame, makamaka muzichita mantha.
Nchifukwa chake mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthaŵi yake adzakukwezeni.
Iwo amamanga katundu wosautsa kunyamula nkusenzetsa anthu, koma iwowo samukhudzako mpang'ono pomwe.
Amalankhula modzikuza ndipo amanyadira zoipa zao. Amatswanya anthu anu, Inu Chauta, amazunza anthu anu osankhidwa.
Kuwopa Chauta kumaphunzitsa nzeru, ndipo ndi kudzichepetsa ndi ulemu, chili patsogolo nkudzichepetsa.
Chauta, mtima wanga ndi wosadzikuza, maso anga ndi osanyada. Sinditengeka mtima ndi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa. Koma ndautonthoza ndi kuukhalitsa chete mtima wanga, monga mwana amene mai wake amamtonthoza ndi bere. Momwemo mtima wanga uli phe m'kati mwanga.
Kulankhula kwa chitsiru kumamuitanira ndodo pa msana, koma mau a munthu wanzeru amamteteza.
Koma anthu ofatsa adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala pa mtendere wosaneneka.
Ndiye usachite kunkitsa nako kulungama, kapena kunkitsa nazo nzeru. Nanga ufere ziti? Usachite kunyanyanso kuipa, usanyanye nawonso uchitsiru. Nanga uferenji nthaŵi yako isanakwane?
Usamadzikuza ukakhala pamaso pa mfumu, usamakhala pa malo a anthu apamwamba. Pajatu kuli bwino kuchita kukuuza kuti, “Dzakhale pokwera pano”, koposa kuchita kukutsitsa chifukwa cha wina wokupambana. Zimene maso ako azipenya,
Aliyense aziyesa yekha ntchito zake m'mene ziliri. Ngati zili bwino, adzatha kunyadira chifukwa cha ntchito zake zokhazo, osati chifukwa zapambana ntchito za mnzake.
Anthu otsika ndi mpweya chabe, ngakhale anthu okwera ndi nthunzi chabe, onsewo ndi oluluka pa sikelo, ndi opepuka kupambana mpweya.
Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa.
Munthu woipa amachitira upo mnzake wabwino, namamtuzulira maso mwachidani. Koma Chauta amamseka munthu woipayo, poti amaona kuti tsiku lake la kuwonongeka likubwera.
Kuwopa Chauta nkudana ndi zoipa. Kunyada, kudzitama, kuchita zoipa ndi kulankhula zonyenga, zonsezo ndimadana nazo.
Ndipo inu mukudzitukumulabe! Kwenikweni mukadayenera kumva chisoni, ndi kumchotsa pakati panu munthu amene adachita zimeneziyo.
Usavutike munthu wina akamalemera, pamene chuma cha m'nyumba mwake chikukulirakulira. Chifukwa pamene munthuyu amwalira, sadzatengapo kanthu. Chuma chake sichidzapita naye limodzi.
Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu. M'thupi lathu limodzi lomweli tili ndi ziwalo zambiri, ndipo ziwalozo zili ndi ntchito zosiyanasiyana. Momwemonso ife, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, olumikizana mwa Khristu, ndipo tonse, aliyense pa mbali yake, ndife ziwalo zolumikizana.
Anthu asatinso azikutchulani atsogoleri, popeza kuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi yekha, ndiye Khristu. Pakati panupa wamkulu akhale mtumiki wanu. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.”
Ngati anthu amumvera ndi kumamtumikira, adzatsiriza masiku a moyo wao mwamtendere, adzatsiriza zaka zao mosangalala.
Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”
Iwo atemberere, koma Inu mundidalitse. Ondiputa muŵachititse manyazi, koma ine mtumiki wanu ndisangalale.
Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.
Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.
Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko, ndipo munthu wa mtima wodzikuza adzagwa. Kuli bwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu osauka, kupambana kumagaŵana chuma ndi anthu onyada.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.
Inu anthu osakhulupirikanu, kodi simudziŵa kuti kuchita chibwenzi ndi zapansipano nkudana ndi Mulungu? Choncho munthu wofuna kukhala bwenzi la zapansipano, ameneyo amadzisandutsa mdani wa Mulungu.