Ukwati ndi chinthu chopangidwa ndi Mulungu, kuti munthu asakhale yekha. Ndi ubale wapadera komanso wodabwitsa umene umafuna kudzipereka ndi kupirira. Monga ana a Mulungu tiyenera kusonyeza chikondi chake ndipo ukwati umatipatsa mwayi tsiku ndi tsiku wochisonyeza.
Tili ndi mavesi ambiri a m’Baibulo omatithandiza kukhazika bwino ukwati wathu ngati tiwatsatire. Chimodzi mwa zinthu zoyamba zimene Ambuye amatifunsa tikakwatirana, ndichokusiya abambo ndi amayi athu kuti tipange banja lathu, nyumba yathu yatsopano. Zoonadi, tiyenera kulemekeza makolo athu, koma zisankho zopangidwa tsopano ziyenera kukhala ndi mnzanu, banja lanu.
Ukwati uyenera kuperekedwa kwa Mulungu, aliyense ayenera kutenga udindo umene Mulungu wapereka mu mgwirizanowu, ndi kuika chikondi chanu m'manja mwa Mulungu, kulimbitsa chikondi chanu tsiku ndi tsiku ndi pemphero ndi mawu a Mulungu.
Ukwati ndi wa nthawi zonse, dongosolo limene Mulungu analipangira ukwati ndi la nthawi zonse, kusudzulana sikuli m'dongosolo lake, Mulungu amafuna kuti mukhale pamodzi mpaka imfa. Pali zinthu zoopsa monga kusakhulupirika kapena nkhanza, koma dongosolo loyambirira la Mulungu ndi lakuti mwamuna ndi mkazi akhale pamodzi mpaka imfa.
Komabe akunenanso za inu, kuti mwamuna aliyense azikonda mkazi wake monga momwe amadzikondera iye mwini, ndiponso kuti mkazi aliyense azilemekeza mwamuna wake.
Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo amuna ndi akazi ao azikhala okhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzaŵalanga.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.
Kodi mkazi wolemerera angathe kumpeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala ya yamtengowapatali. Mtima wa mwamuna wake umamkhulupirira, ndipo mwamunayo sadzasoŵa phindu.
Mwamuna azipereka kwa mkazi wake zomuyenerera zokhudza banja ngati mkazi wake, momwemonso mkazi azipereka kwa mwamuna wake zomuyenerera zokhudza banja ngati mwamuna wake.
Nchifukwa chake mwamuna amasiya atate ndi amai, ndipo amaphatikana ndi mkazi wake, choncho aŵiriwo amakhala thupi limodzi.
Inu amuna, muzikonda akazi anu, monga momwe Khristu adakondera Mpingo, nadzipereka chifukwa cha Mpingowo.
Inunso amuna, muzikhala moŵamvetsa bwino akazi anu. Muziŵachitira ulemu popeza kuti iwowo ndi mtundu wofookerapo, ndiponso ngolandira nanu pamodzi mphatso ya Mulungu, imene ili moyo wosatha. Muzitero, kuti pasakhale kanthu koletsa mapemphero anu.
Komabe m'maso mwa Ambuye mkazi sali kanthu popanda mwamuna, ndiponso mwamuna sali kanthu popanda mkazi.
Kuli bwino kukhala potero pa denga kupambana kukhala m'nyumba pamodzi ndi mkazi wolongolola.
Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.
Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi, Koma umu si m'mene inu mudaphunzirira za Khristu ai, ngatitu mudamva za Iyeyo, ngatinso mudaphunzitsidwa za Iye, motsata choona chimene chili mwa Yesu. Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga. Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano. Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni. Tsono lekani kunama. Aliyense azilankhula zoona zokhazokha ndi mkhristu mnzake, pakuti tonse pamodzi mogwirizana ndife ziwalo za thupi la Khristu. Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire. Musampatse mpata Satana woti akugwetseni. Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa. M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo. ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu Woyera pa kulunzana mu mtendere.
Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongola, ndiwe chiphadzuŵa. Maso ako akunga ngati nkhunda. Mkazi Wokondedwa wanga, nawenso ndiwe wokongola, wokongoladi zedi. Malo athu ogonapo ndi msipu wobiriŵira.
Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.
Ndaloŵa m'munda mwanga, iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga. Ndikukolola mure wanga ndi zokometsera chakudya. Ndikudya uchi wanga pamodzi ndi zisa zake zomwe. Ndikumwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Akazi Inu apaubwenzi, idyani ndi kumwa: Inu okondana, imwani kwambiri! Mkazi
Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima, koma kukoma kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake.
Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka, m'kati mwa nyuma yako. Ana ako adzakhala ngati tiziphukira taolivi, kuzungulira tebulo lako.
Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera.
Ndidangoti iwo aja ntaŵapitirira pang'ono, ndampeza amene mtima wanga umamkonda. Ndidamgwira, osamlola kuti achoke, mpaka nditamloŵetsa m'nyumba ya amai anga, m'chipinda cha amene adandibala.
Choncho pakali pano zilipo zinthu zitatuzi: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwa zonsezi chopambana ndi chikondi.
Tsono popeza kuti ndinu ana okondedwa a Mulungu, muziyesa kumtsanzira. Muziyesa kudziŵa kwenikweni zimene zingakondweretse Ambuye. Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muŵatsutse. Paja zimene iwo amachita mobisa, ngakhale kuzitchula komwe kumachititsa manyazi. Koma kuŵala kumaunika zinthu, ndipo zonse zimaonekera poyera. Motero chilichonse choonekera poyera, chimasanduka kuŵala. Nchifukwa chake amati, “Dzuka wam'tulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuŵalira.” Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa. Nchifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵani zimene Ambuye afuna kuti muchite. Musaledzere vinyo, kumeneko nkudzitaya, koma mudzazidwe ndi Mzimu Woyera. Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse. Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.
Munthu akangokwatira kumene, musamlembe m'gulu la ankhondo, kapena kumpatsa ntchito ina iliyonse. Papite chaka chathunthu asanachite zimenezi, kuti choncho athe kukhala kwao ndi kumakondweretsa mkazi wake amene adamkwatirayo.
Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.
Chitsulo amachinola nchitsulo chinzake, chonchonso munthu amasulidwa ndi munthu mnzake.
Uzikondwerera moyo pamodzi ndi mkazi amene umamkonda, pa masiku onse a moyo wako wopandapakewu umene Mulungu wakupatsa pansi pano. Ndi zokhazo zimene ungaziyembekeze pa moyo wako ndiponso pa ntchito zako zolemetsa zimene umazigwira pansi pano.
Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.
Muja umakhalira mtengo wa apulosi pakati pa mitengo yam'nkhalango, ndi m'mene aliri wokondedwa wanga pakati pa anyamata. Ndinkakondwa kwambiri ndikausa mumthunzi mwake, zipatso zake zinali tseketseketseke m'kamwamu.
Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, uli ngati munda wopiringidza, ngati munda wopiringidza, ngati kasupe wochingidwa.
Ndiwe wokongola zedi, ndiponso wosangalatsa, iwe wokondedwawe, namwali wokondweretsawe.
Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu a mtima wodziŵa zinthu. Ndinkayenda m'mbali mwa munda wa munthu waulesi, m'mbali mwa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru. M'minda monsemo munali mutamera minga yokhayokha, m'nthaka imeneyo munali mutamera khwisa, ndipo mpanda wake wamiyala unali utagwa. Tsono nditaona, ndidayamba kuganizirapo pa zimenezo, nditayang'ana, ndidatolapo phunziro ili: Ukati, “Taimani ndigoneko pang'ono,” kapena “Ndiwodzereko chabe,” kapena “Ndingopumulako pang'ono,” umphaŵi udzakufikira monga mbala, kusauka kudzakupeza ngati mbala yachifwamba. Wodziŵa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chokondweretsa ndi cha mtengo wapatali.
Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru.
Iye adayankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Pambuyo pake Mulungu adauza mkaziyo kuti, “Ndidzaonjeza zovuta zako pamene udzakhala ndi pathupi, udzamva zoŵaŵa pa nthaŵi yako ya kubala mwana. Udzakhumba mwamuna wako, ndipo mwamuna wakoyo adzakulamulira iwe.”
Adanditenga kupita nane ku nyumba yaphwando, mbendera yake yozika pa ine inali chikondi.
Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.
Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.
Palibe munthu amene adaona Mulungu. Koma tikamakondana, Mulungu amakhala mwa ife, ndipo chikondi chake chafika pake penipeni mwa ife.
Nkhope yachikoka ndi yonyenga, kukongola nkosakhalitsa, koma mkazi woopa Chauta ndiye woyenera kumtamanda.
Ine ndili ngati khoma, ndipo maŵere anga ali ngati nsanja zake. Tsono m'maso mwa wokondedwa wanga ndili ngati wodzetsa mtendere. Mwamuna
Ndidakakonda kuti pasakhale zokudetsani nkhaŵa. Munthu wosakwatira amangotekeseka ndi za Ambuye, kuganiza za m'mene angakondweretsere Ambuye. Koma munthu wokwatira amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mkazi wake. Motero amagwira njakata. Mkazi wosakwatiwa, kapenanso namwali, amangotekeseka ndi za Ambuye, kuti adzipereke kwa Ambuye m'thupi ndi mumzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mwamuna wake.
Motero Mulungu adalenga munthu, m'chifanizo chake, adaŵalengadi m'chifanizo cha Mulungu. Adaŵalenga wina wamwamuna wina wamkazi.
Koma ndifuna kuti mudziŵe kuti Khristu ndiye mutu wa mwamuna aliyense, mwamuna ndiye mutu wa mkazi, ndipo Mulungu ndiye mutu wa Khristu.
Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.
Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.
Wokondedwa wanga, nawenso ndiwe wokongola, wokongoladi zedi. Malo athu ogonapo ndi msipu wobiriŵira.
Adaŵadalitsa poŵauza kuti, “Mubereke ndi kuchulukana, mudzaze dziko lonse lapansi ndi kumalilamulira. Ndakupatsani ulamuliro pa nsomba, mbalame ndi nyama zonse zimene zikukhala pa dziko lapansi.”
Pali zinthu zitatu zimene zimandidabwitsa kwambiri. Pali zinthu zinai zimene sindizimvetsa konse, zinthuzo ndi izi: M'mene umaulukira mphamba mu mlengalenga, m'mene imayendera njoka pa thanthwe, m'mene chimayendera chombo pa nyanja yakuya, ndiponso m'mene mwamuna amachitira akakhala ndi namwali.
Tsono Isaki adatenga Rebeka kuti akhale mkazi wake naloŵa naye m'hema mwake. Isaki adamkonda kwambiri Rebekayo, mwakuti zimenezi zidamtonthoza pa imfa ya mai wake ija.
Choncho tsopano salinso aŵiri koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumukiza pamodzi, munthu asazilekanitse.”
Kudzikongoletsa kwanu kusangokhala kwa maonekedwe akunja pakuluka tsitsi, ndi kuvala zamakaka zagolide ndi zovala zamtengowapatali. Koma kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa moyo wam'kati, kukongola kosatha kwa mtima wofatsa ndi wachete. Moyo wotere ngwamtengowapatali pamaso pa Mulungu.
Ana ake amamnyadira nkumutchula kuti ndi wodala. Mwamuna wake nayenso amamtamanda, amati, “Inde alipo akazi ambiri olemerera kwabasi, koma kuyerekeza ndi iwe, onsewo nchabe.”
Mkazi amamangika ndi lamulo la ukwati, nthaŵi yonse pamene mwamuna wake ali moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, ali ndi ufulu kukwatiwa ndi mwamuna amene iye afuna, malinga ukwatiwo ukhale wachikhristu.
Mkazi thupi lake si lokhalira iye yekha ai, ndi lokhaliranso ndi mwamuna wake yemwe. Momwemonso mwamuna thupi lake si lokhalira iye yekha ai, ndi lokhaliranso ndi mkazi wake yemwe.
Mkazi wabwino ali ngati chisoti chaulemu kwa mwamuna wake, koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda chamafinya kwa mwamuna wake.
Wokondedwa wangayo ndi wangadi, ndipo ine ndine wake. Amadyetsa gulu lake la ziŵeto pakati pa akakombo.
Nyumba ndi chuma ndiye choloŵa chochokera kwa makolo, koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Chauta.
Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, wangoti mtima wangawu kwe! Wanditenga mtima ndi kapenyedwe ka maso ako, ndiponso ndi mphande imodzi ya mkanda wa m'khosi mwako.
Chimodzimodzinso inu azimai, muzimvera amuna anu, kuti ngati ena mwa iwo samvera mau a Mulungu, azikopeka ndi makhalidwe a akazi aonu. Sipadzafunikanso kunenerera mau,
Uzikhutira ndi mkazi wako, uzikondwa ndi mkazi wa unyamata wako. Iye uja ngwokongola ngati mbaŵala, ndi wa maonekedwe osiririka ngati mbalale. Uzikhutitsidwa ndi maŵere ake nthaŵi zonse, uzikokeka ndi chikondi chake pa moyo wako wonse.
Undimpsompsone ndi milomo yako, chifukwa chikondi chako nchoposa vinyo kukoma kwake.
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Motero Yakobe adagwira ntchito zaka zisanu ndi ziŵiri kuti akwatire Rakele, ndipo nthaŵi imeneyo idangooneka kwa iye ngati masiku oŵerengeka chabe, chifukwa choti adaamkonda kwambiri mkaziyo.
Musamakanane, koma pokhapokha mutavomerezana kutero pa kanthaŵi kuti mudzipereke ku mapemphero. Pambuyo pake mukhalenso pamodzi, kuwopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cha kulephera kudzigwira.
Wokondedwa wangayo ine ndine wake, ndipo iyeyo ndi wangawanga. Amadyetsa ziŵeto zake pakati pa akakombo. Mwamuna
Kwa anthu am'banja lamulo langa, limenetu kwenikweni ndi lochokera kwa Ambuye, ndi ili: Mkazi asalekane ndi mwamuna wake.
Umatirire mtima wako kuti musaloŵe winanso koma ine ndekha, ndipo sudzakumbatira winanso koma ine ndekha. Paja chikondi nchamphamvu ngati imfa, nsanje njaliwuma ngati manda. Chikondi chimachita kuti laŵilaŵi ngati malaŵi a moto, ndipo nchotentha koopsa.
Ngati wina aliyense saŵapatsa zofunika achibale ake, makamaka a m'banja mwake momwe, ameneyo wataya chikhulupiriro chake, ndipo kuipa kwake nkoposa kwa munthu wosakhulupirira.
Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo.
Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.
Nchifukwa chake muzilimbitsana mtima ndi kumathandizana, monga momwe mukuchitiramu.
Milomo yake njosangalatsa kwambiri, munthuyo amanditenga mtima kwabasi. Ameneyutu ndiye wokondedwa wanga, ndiponso bwenzi langa, inu akazi a ku Yerusalemu.
Mumafunsa kuti, “Chifukwa chake nchiyani?” Chifukwa chake nchakuti Chauta anali mboni ya chipangano chimene udachita ndi mkazi wako woyamba. Sudakhulupirike kwa iye, ngakhale iyeyo ndiye mnzako ndi mkazi wako potsata chipanganocho.
Mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula ya mvumbi. Kuyesa kumletsa mkazi woteroyo kuli ngati kuyesa kuletsa mphepo, kapena kuyesa kufumbata mafuta m'manja.
Pambuyo pake Chauta adati, “Sibwino kuti munthuyu akhale yekha. Ndipanga mnzake woti azimthandiza.”
Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, chikondi chako nchosangalatsa. Chikondi chako nchosangalatsa kupambana vinyo, mafuta ako ndi onunkhira bwino kupambana zonunkhira zabwino zonse.
Ngakhale madzi ochuluka sangachizimitse chikondi, ngakhale madzi a chigumula sangachikokolole. Ngakhale munthu atapereka chuma chonse cha m'nyumba chifukwa chofuna kugula chikondi, adzangonyozeka nazo kotheratu. Alongo a Mkazi