Buku la Aefeso limandiphunzitsa kuti ndisamanene mawu alionse oipa, koma mawu anga onse akhale opatsa mphamvu kwa anthu ondizungulira, kuti ndiwadalitse pamavuto alionse amene akukumana nawo.
Lilime langa linalengedwa kuti likhale chitoliro cha madalitso chimene Mulungu amafuna kugwiritsa ntchito pofalitsa uthenga ndi kumanga anthu ambiri. Ndiye chifukwa chake, ndikofunikira kwambiri kuchotsa chilichonse chimene sichichokera kwa Mulungu ndipo sichithandiza pakumanga.
Ndiyenera kusamala kwambiri ndi mawu anga, chifukwa ndidzaweruzidwa malinga ndi zimene ndimanena. Ndiyenera kukhala wofulumira kudalitsa m'malo motemberera mnzanga kapena kufalitsa miseche, chifukwa miseche siyabwino pamaso pa Mulungu.
Ndiyenera kuyesetsa kukhala wolankhula wamawu a Mulungu mwachangu, kuti chisomo chake ndi chifundo chake zikhale nane nthawi zonse. Ndikumbukire kusunga lilime langa ku zoipa ndi milomo yanga kuti isanene bodza, chifukwa munthu woipa amabweretsa ndewu zoopsa, koma woteteza mnzake amapulumutsa moyo.
Amene amanka nachita ukazitape, amaulula zinsinsi. Koma wa mtima wokhulupirika, amasunga pakamwa pake.
Munthu woipa mtima amafalitsa mkangano, kazitape amadanitsa anthu okhala pa chibwenzibwenzi.
M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.
Musamangoyendayenda uku ndi uku kumachita ukazitape pakati pa anthu a mtundu wanu. Musachite kanthu kalikonse kamene kangathe kudzetsa imfa ya munthu wina. Ine ndine Chauta.
Munthu wosalabadirako za Mulungu amaononga mnzake ndi pakamwa pake; munthu wochita chilungamo amapulumuka chifukwa cha kudziŵa zinthu.
“Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunyengezerani zoipa zamitundumitundu chifukwa cha Ine.
Amene amanka nachita ugogodi, amaulula zinsinsi. Nchifukwa chake usamagwirizane naye wolankhula zopusayo.
Ndi munthu amene amayenda mosalakwa, amene amachita zolungama nthaŵi zonse, amene amalankhula zinthu ndi mtima woona.
Ndi amene sasinjirira ndipo sachita anzake zoipa, kapena kumafalitsa mbiri yoipa ya anzake.
Nchifukwa chake tayani choipa chonse, kunyenga konse, chiphamaso, kaduka ndi masinjiriro onse.
Uŵauze kuti asamakamba zoipa za wina aliyense, apewe kukangana, akhale ofatsa, ndipo nthaŵi zonse akhale aulemu kwa anthu onse.
Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula.
Chimodzimodzinso lilime: ndi kachiwalo kakang'ono, komabe limadzitama kuti nkuchita zazikulu. Tangoganizani kukula kwake kwa nkhalango imene ingayatsidwe ndi kalilaŵi kakang'ono ka moto.
Tsonotu lilime limatentha ngati moto. Chifukwa chokhala pakati pa ziwalo zathu limawanditsa zoipa m'thupi monse. Limaipitsa khalidwe lonse la munthu. Limayatsa moto moyo wathu wonse kuyambira pobadwa mpaka imfa; ndipo moto wake ngwochokera ku Gehena.
Abale, musamasinjirirana. Wosinjirira mbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo a Mulungu. Koma ukaweruza Malamulo a Mulungu, ndiye kuti sukuchita zimene Malamulowo akunena, ukudziyesa woweruza.
Ngati wina akudziyesa woika mtima pa zopembedza Mulungu, koma nkukhala wosasunga pakamwa, chipembedzo chakecho nchopanda pake, ndipo amangodzinyenga.
Ndiponso musamalankhule zolaula, zopusa, kapena zopandapake, koma muzilankhula zoyamika Mulungu.
Mitima yao idadzaza ndi zosalungama zamitundumitundu, monga kuipa, umbombo ndi dumbo. Amangolingalira za kaduka, za kupha anthu, za ndeu, za kunyenga, ndi za njiru. Amachita ugogodi,
Umasimba za Mwana wake, Yesu Ambuye athu. Poyang'anira umunthu wake, kholo lake ndi Davide,
amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao.
Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa:
maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa,
mtima wokonzekera kuchita zoipa, mapazi othamangira msangamsanga ku zoipa,
mboni yonama yolankhula mabodza, ndi munthu woutsa chidani pakati pa abale.
Kuwonjezera pamenepo, amagwa m'chizoloŵezi cha kungokhala khale, motero amangoyendayenda ku nyumba za anthu. Tsonotu samangokhala khale chabe ai, amachitanso miseche nkumaloŵera za eni, ndi kukhala omalankhula zimene samayenera kulankhula.
Inu Chauta, kodi ndani angathe kukhala m'Nyumba mwanu? Ndani angathe kukhala pa phiri lanu loyera?
Ndi munthu amene amayenda mosalakwa, amene amachita zolungama nthaŵi zonse, amene amalankhula zinthu ndi mtima woona.
Ndi amene sasinjirira ndipo sachita anzake zoipa, kapena kumafalitsa mbiri yoipa ya anzake.
Amene amabwera kudzandiwona, ndi wosakhulupirika, mumtima mwake amaganiza zoipa za ine, ndipo akatuluka, amakaziwanditsa.
Koma tsopano musachitenso zonsezi, monga kukalipa, kukwiya, kuipa mtima, ndi mijedu. Pakamwa panu pasamatulukenso mau otukwana kapena onyansa.
“Mbale wako akakuchimwira, pita ukamdzudzule muli aŵiri nokha. Akakumvera, wamkonza mbale wakoyo.
Tsono woweruza enawe, kaya ndiwe yani, ulibe pozembera. Pakutitu pamene ukuweruza mnzako, ukudzitsutsa wekha, popeza kuti iweyo woweruzawe umachita zokhazokhazo.
Yesetsani kukhala ndi moyo wabata. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kumagwira ntchito ndi manja ake. Chitani zimenezi, monga tidakulangizirani muja,
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
Wokhululukira cholakwa amafunafuna chikondi, koma wosunga nkhani kukhosi amapha chibwenzi.
Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.
Wofulumira kulankhula, zonena zake zimalasa ngati mpeni, koma mau a munthu wanzeru amachiza anzake.
Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse.
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Munthu wosinjirira mnzake kuseri ndidzamcheteketsa. Wooneka wonyada ndi wodzikuza sindidzamulekerera.
Ndikuwopa kuti ndikadzabwera kwanuko, mwina nkudzakupezani muli osiyana ndi m'mene ndikadafunira. Ndikuwopa kuti mwina inunso nkudzandipeza ine wosiyana ndi m'mene mukadafunira. Ndikuwopanso kuti mwina ine nkudzapeza kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusinjirirana, ugogodi, kudzitukumula, ndiponso chisokonezo.
Paja mau a Mulungu akuti. “Yemwe afuna kukondwera ndi moyo, ndi kuwona masiku abwino, aletse lilime lake kulankhula zoipa, ndiponso milomo yake kunena mabodza.
Nthaŵi zonse mau anu akhale okoma, opindulitsa ena, kuti potero mudziŵe m'mene muyenera kuyankhira munthu aliyense.
Wina akamanena kuti, “Ndimakonda Mulungu”, komabe nkumadana ndi mbale wake, ndi wonama ameneyo. Pakuti munthu wosakonda mbale wake amene wamuwona, sangathe kukonda Mulungu amene sadamuwone.
Nchifukwa chake zonse zimene mwalankhula pa mdima, zidzamveka poyera, ndipo zonse zimene mwanong'oneza anthu m'kati mwa nyumba, adzazilengeza pa bwalo.”
Tsiku lonse umakhalira kusinkhasinkha za kuwononga ena, lilime lako lili ngati lumo lakuthwa, ntchito yako nkunyenga.
Umakonda zoipa kupambana zabwino, umakonda kunama kupambana kulankhula zoona.
Umakonda kulankhula mau ovutitsa ena, iwe wabodzawe.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza.
Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.
Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona.
Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.
Paja Malamulo onse a Mulungu amaundidwa mkota pa lamulo limodzi lija lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Koma ngati muyamba kulumana ndi kukadzulana, muchenjere kuti mungaonongane kotheratu.
Zimene umanena zingathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo, munthu wolankhulalankhula adzapeza bwino kapena tsoka.
Tsono tiyeni tileke kumaweruzana. Makamaka mutsimikize kuti musachite kanthu kalikonse kophunthwitsa mbale wanu, kapena komchimwitsa.
Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera.
“Musamaweruza anthu ena kuti ndi olakwa, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni.
Kapena atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka?
Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha?
Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.
“Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri.
Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.
“Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa.
Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu?
Chonchonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo woipa umabala zipatso zoipa.
Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapena mtengo woipa kubala zipatso zabwino ai.
Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula nkuuponya pa moto.
M'mene inu mumaweruzira ena, ndi m'menenso Mulungu adzakuweruzirani inuyo. Ndipo muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.
Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa,
Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai.
kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko,
dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.
Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa.
Nchifukwa chake muzilimbitsana mtima ndi kumathandizana, monga momwe mukuchitiramu.
“Musamaweruza anthu ena kuti ngolakwa, ndipo Mulungu sadzakuweruzani. Musamaimba ena mlandu, ndipo Mulungu sadzakuimbani mlandu. Muzikhululukira ena, ndipo Mulungu adzakukhululukirani.
Paja tonsefe timalakwa pa zinthu zambiri. Ngati alipo amene salakwa pakulankhula, ndiye kuti ndi wangwirodi ameneyo, mwakuti angathe kulamuliranso thupi lake lonse.
Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi,
Koma umu si m'mene inu mudaphunzirira za Khristu ai,
ngatitu mudamva za Iyeyo, ngatinso mudaphunzitsidwa za Iye, motsata choona chimene chili mwa Yesu.
Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga.
Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano.
Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni.
Tsono lekani kunama. Aliyense azilankhula zoona zokhazokha ndi mkhristu mnzake, pakuti tonse pamodzi mogwirizana ndife ziwalo za thupi la Khristu.
Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire.
Musampatse mpata Satana woti akugwetseni.
Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa.
M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.
ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu Woyera pa kulunzana mu mtendere.
“Umakhala pansi nkumachitira mbale wako miseche, inde, umasinjirira mbale wako weniweni.
Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.
Monga munthu wopenga amene amangoponya nsakali zamoto, kapena mivi yoopsa,
ndimonso amakhalira munthu wonyenga mnzake, amene amati, “Ai, ndi zoseka chabe!”
Abale musamanenerana zoipa pakati panu, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Onani, woweruza waima pa khomo.
Munthu wabwino amaganizira za m'mene ayankhire, koma pakamwa pa munthu woipa pamatuluka mau oipa okhaokha.
Ana a njoka inu, mungathe bwanji kulankhula zabwino pamene muli oipa? Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.
Pakamwa pabodza pamamnyansa Chauta. Koma anthu ochita zinthu mokhulupirika amamkondweretsa.
Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo,
kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi,
Aliyense mwa ife azikondweretsa mnzake, ndi kumchitira zabwino, kuti alimbikitse chikhulupiriro chake.
Koma nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, uzipewe, pakuti anthu olankhula zotere adzanka nanyozeranyozera Mulungu.
Pakati panu pasakhale ndi mmodzi yemwe wogwa m'mavuto chifukwa choti wapha munthu, kapena waba, kapena wachita choipa, kapena waloŵerera za eniake.
Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.
Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense wopsera mtima mbale wake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu. Aliyense wonena mnzake kuti, ‘Wopandapake iwe,’ adzayenera kuzengedwera ku Bwalo Lapamwamba. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru,’ adzayenera kukaponyedwa ku moto wa Gehena.
Tchinjirizeni ku upo wachiwembu wa anthu oipa, tetezeni ku chiwawa cha anthu ochita zoipa.
Iwo amanola lilime lao ngati lupanga, amaponya mau obaya ngati mivi.
Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake. Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.”
Musamauzana mabodza, pakuti mwachita ngati mwavula moyo wanu wakale, pamodzi ndi zochitachita zake zoipa,
Tsono popeza kuti ndinu ana okondedwa a Mulungu, muziyesa kumtsanzira.
Muziyesa kudziŵa kwenikweni zimene zingakondweretse Ambuye.
Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muŵatsutse.
Paja zimene iwo amachita mobisa, ngakhale kuzitchula komwe kumachititsa manyazi.
Koma kuŵala kumaunika zinthu, ndipo zonse zimaonekera poyera.
Motero chilichonse choonekera poyera, chimasanduka kuŵala. Nchifukwa chake amati, “Dzuka wam'tulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuŵalira.”
Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru.
Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa.
Nchifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵani zimene Ambuye afuna kuti muchite.
Musaledzere vinyo, kumeneko nkudzitaya, koma mudzazidwe ndi Mzimu Woyera.
Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse.
Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.
Monga munthu wopenga amene amangoponya nsakali zamoto, kapena mivi yoopsa,
ndimonso amakhalira munthu wonyenga mnzake, amene amati, “Ai, ndi zoseka chabe!”
Monga imachitira mpheta yokhalira kuuluka, monga amachitira namzeze kumangoti zwezwezwe, ndimonso limachitira temberero lopanda chifukwa, silitha.
Moto umazima pakasoŵa nkhuni, chonchonso kumene kulibe kazitape, kulibenso ndeu.
Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana.
Mukamakondana, anthu onse adzadziŵa kuti ndinudi ophunzira anga.”
Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu.
Tsono muzilankhula ndi kuchita zinthu monga anthu oti Mulungu adzaŵaweruza potsata lamulo loŵapatsa ufulu.
Paja munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso Mulungu adzamuweruza mopanda chifundo. Koma wochita chifundo alibe chifukwa choopera chiweruzo cha Mulungu.
Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru.
Munthu wotere ndi wodzitukumula ndi kunyada, sadziŵa kanthu. Mtima wake ngwodwala, wongofuna zotsutsanatsutsana ndi kukangana pa mau chabe. Zimenezi zimabweretsa kaduka, kusamvana, kusinjirirana, kuganizirana zoipa,
Munthu wochitira mnzake umboni wonama, amapweteka mnzakeyo ngati chibonga kapena lupanga kapena muvi wakuthwa.
Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.