Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

112 Mau a m'Baibulo Okhudza Mikangano

Ndikufuna kukuuzani kuti Mulungu amafuna tonse timachite zabwino, mitima yathu ikhale yoyera ndi yowongoka pamaso pake. Tonse tili ndi maganizo ndi zokhumba zomwe nthawi zina zimatipangitsa kuchita zinthu zosakondweretsa Mulungu.

Komabe, sitingalole kuti uchimo utilamulire n’kutipangitsa kukangana. Tiyenera kusamala kwambiri ndi zochita zathu za tsiku ndi tsiku, n’kupempha Mulungu kuti Mzimu Woyera utitsogolere. Ukamachita zimenezi, udzakhala mfulu ndipo sudzakhala ndi mkangano ndi ena.

Baibulo, pa 2 Timoteo 2:14, limatiuza kuti tisamakangane, pakuti palibe phindu lake, koma limangowononga okhululukira. Mkanganowo suthandiza, sumanga chilichonse chabwino.

N’chifukwa chake tiyenera kuyeretsa mitima yathu, n’kupempha Yesu kuti atipatse mzimu wamtendere, womwe umalimbikitsa ndi kudalitsa ena, m’malo mowapweteka.


Genesis 13:7-8

Motero padaauka ndeu pakati pa abusa a Abramu ndi abusa a Loti. Nthaŵi imeneyo nkuti Akanani ndi Aperizi akadalipo m'dzikomo.

Tsono Abramu adauza Loti kuti, “Ifetu ndife abale, choncho pasakhale kukangana pakati pa iwe ndi ine, ndipo abusa ako sayenera kumakangana ndi abusa anga.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 18:6

Mau a chitsiru amautsa mkangano, ndipo pakamwa pake pamaitana mkwapulo.

Mutu    |  Mabaibulo
Tito 3:9

Koma upewe kufufuzafufuza zopusa, kumaŵerengaŵerenga ndondomeko za maina a makolo, mikangano, ndi mitsutso pa za Malamulo a Mose. Zimenezi nzosathandiza, zilibe phindu konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 20:3

Nchaulemu kwa munthu kumalewa mikangano, koma aliyense wopusa amakonda kulongolola.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 30:33

Paja ukakuntha mkaka, mafuta amapangika. Ukapsinya mphuno, magazi amatuluka, ndipo ukautsa mkwiyo, mikangano imaoneka.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 3:16

Pajatu pamene pali kaduka ndi kudzikonda, pomweponso pali chisokonezo ndi ntchito yoipa ya mtundu uliwonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 120:7

Ine ndimafuna mtendere, koma ndikalankhula za mtendere, iwo amafuna nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:15

Koma ngati muyamba kulumana ndi kukadzulana, muchenjere kuti mungaonongane kotheratu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:18

Munthu wopsa mtima msanga amautsa mkangano, koma munthu woleza mtima amabweretsa mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 18:19

Mnzako ukamthandiza amakhala ngati mzinda wolimba, koma kukangana naye kumakutsekera thandizo lililonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 14:19

Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 19:13

Mwana wopusa ndi tsoka kwa atate ake, mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula ya mvumbi.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 2:14-15

Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo,

kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi,

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 4:1-2

Kodi nkhondo zimachokera kuti? Kukangana pakati panu kumachokera kuti? Kodi suja zimachokera ku zilakolako zanu zathupi, zimene zimachita nkhondo mwa inu?

Mudzichepetse pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

Abale, musamasinjirirana. Wosinjirira mbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo a Mulungu. Koma ukaweruza Malamulo a Mulungu, ndiye kuti sukuchita zimene Malamulowo akunena, ukudziyesa woweruza.

Mulungu yekha ndiye wopanga Malamulo ndiponso woweruza. Ndiyenso wotha kupulumutsa ndi kuwononga. Nanga iwe ndiwe yani kuti uziweruza mnzako?

Onani tsono, inu amene mukuti, “Lero kapena maŵa tipita ku mzinda wakutiwakuti, ndipo tikachitako malonda chaka chimodzi kuti tikaphe ndalama,”

m'menemo inuyo zamaŵa simukuzidziŵa. Kodi moyo wanu ngwotani? Pajatu inu muli ngati utsi chabe, umene umangooneka pa kanthaŵi, posachedwa nkuzimirira.

Kwenikweni muyenera kumanena kuti, “Ambuye akalola, tikakhala ndi moyo, tidzachita chakutichakuti.”

Koma monga zilirimu, mumanyada ndi kudzitama. Kunyada konse kotere nkoipa.

Munthu akadziŵa zabwino zimene ayenera kuchita, napanda kuzichita, ndiye kuti wachimwa.

Mumalakalaka zinthu, koma zimakusoŵani, nchifukwa chake mumapha munthu. Mumasirira zinthu, koma simungathe kuzipeza, nchifukwa chake mumamenyana, nkumachita nkhondo. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:9

Ngodala anthu odzetsa mtendere, pakuti Mulungu adzaŵatcha ana ake.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 2:24-26

Ndipo mtumiki wa Ambuye asamakhala wokanganakangana ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa onse, mphunzitsi wokhoza, munthu wodziŵa kupirira mavuto.

Akhale wofatsa polangiza otsutsana naye. Mwina Mulungu angaŵapatse mwai woti atembenuke ndi kuzindikira choona.

Pamenepo nzeru zao zidzabweramo, ndipo adzapulumuka mu msampha wa Satana, amene adaaŵagwira kuti azichita zofuna zake.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:3

Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 1:10

Abale, ndikukupemphani m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu, kuti muzivomerezana pa zimene munena. Pasakhale kupatulana pakati panu, koma muzimvana kwenikweni pokhala a mtima umodzi ndi a maganizo amodzi.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 13:10

Chipongwe cha osasamala za anzao chimadzetsa mkangano, koma omvera malangizo a anzao ndiwo ali ndi nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:2-3

Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi,

Koma umu si m'mene inu mudaphunzirira za Khristu ai,

ngatitu mudamva za Iyeyo, ngatinso mudaphunzitsidwa za Iye, motsata choona chimene chili mwa Yesu.

Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga.

Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano.

Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni.

Tsono lekani kunama. Aliyense azilankhula zoona zokhazokha ndi mkhristu mnzake, pakuti tonse pamodzi mogwirizana ndife ziwalo za thupi la Khristu.

Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire.

Musampatse mpata Satana woti akugwetseni.

Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa.

M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.

ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu Woyera pa kulunzana mu mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 3:8-9

Mau otsiriza ndi aŵa: nonse mukhale a mtima umodzi, ndi omverana chisoni. Muzikondana nawo abale. Mukhale a mtima wachifundo ndi odzichepetsa.

Anthu okuchitani choipa, osaŵabwezera choipa, okuchitani chipongwe osaŵabwezera chipongwe. Koma inu muziŵadalitsa, pakuti inuyo Mulungu adakuitanirani mkhalidwe wotere, kuti mulandire madalitso ake.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 22:10

Mukampirikitsa wonyoza, kukangana kudzatha, ndipo ndeu ndi zonyoza zidzalekeka.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 26:20-21

Moto umazima pakasoŵa nkhuni, chonchonso kumene kulibe kazitape, kulibenso ndeu.

Monga momwe aliri makala pa moto wonyeka ndiponso nkhuni pa moto woyaka, ndimonso amakhalira munthu wandeu poutsa mikangano.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 4:1

Kodi nkhondo zimachokera kuti? Kukangana pakati panu kumachokera kuti? Kodi suja zimachokera ku zilakolako zanu zathupi, zimene zimachita nkhondo mwa inu?

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 3:3

popeza kuti mukudalirabe zapansipano. Pakati panu pali kaduka ndi kukangana. Nanga zimenezi sizikutsimikiza kuti mukudalirabe zapansipano, ndipo kuti mumachita monga momwe amachitira anthu odalira zapansipanozo?

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 17:19

Wokonda zolakwa amakonda mkangano. Wokonda kulankhula zonyada amadziitanira chiwonongeko.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 58:4

Mumati uku mukusala zakudya, uku mukukangana ndi kumenyana, mpaka kutchayana ndi nkhonya zopwetekana. Kodi mukuyesa kuti Ine nkumvera mapemphero anu, chifukwa cha kusala zakudya kotereku.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:18

Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 2:14

Uziŵakumbutsa zimenezi anthu, ndipo uŵachenjeze kolimba pamaso pa Mulungu kuti asamakangana pa za mau. Kutero kulibe phindu, koma kumangotayikitsa anthu amene akumva kukanganako.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 2:23-24

Uzikana matsutsano opusa ndi opanda nzeru, paja ukudziŵa kuti zotere zimautsa mikangano.

Ndipo mtumiki wa Ambuye asamakhala wokanganakangana ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa onse, mphunzitsi wokhoza, munthu wodziŵa kupirira mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 26:21

Monga momwe aliri makala pa moto wonyeka ndiponso nkhuni pa moto woyaka, ndimonso amakhalira munthu wandeu poutsa mikangano.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 133:1

Ati kukoma ndi kukondweretsa ati, anthu akakhala amodzi mwaubale!

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 17:14

Chiyambi cha mkangano chili ngati kukhamulira madzi, ndiye uzichokapo ndeu isanabuke.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 10:12

Chidani chimautsa mikangano, koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:31

Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 6:3-5

Angathe kupezeka munthu wophunzitsa zosiyana ndi zimenezi, wosavomereza mau oona a Ambuye athu Yesu Khristu ndi chiphunzitso chogwirizana ndi moyo wolemekeza Mulungu.

Munthu wotere ndi wodzitukumula ndi kunyada, sadziŵa kanthu. Mtima wake ngwodwala, wongofuna zotsutsanatsutsana ndi kukangana pa mau chabe. Zimenezi zimabweretsa kaduka, kusamvana, kusinjirirana, kuganizirana zoipa,

kupsetsana mtima kosalekeza pakati pa anthu amene nzeru zao zidaonongekeratu ndipo sazindikiranso choona. Iwo amayesa kuti kupembedza Mulungu ndi njira yopatira chuma.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 16:17

Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa,

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 18:15-17

“Mbale wako akakuchimwira, pita ukamdzudzule muli aŵiri nokha. Akakumvera, wamkonza mbale wakoyo.

Koma akapanda kukumvera, utengerepo wina mmodzi kapena ena aŵiri, kuti mau onse akatsimikizike ndi mboni ziŵiri kapena zitatu.

Akapanda kuŵamvera iwowo, ukauze Mpingo. Ndipo akapanda kumveranso ndi Mpingo womwe, umuyese munthu wakunja kapena wokhometsa msonkho.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:10

Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:14

Lewa zoipa, ndipo uchite zabwino. Funafuna mtendere ndi kuulondola.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:13

Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:1

Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 28:25

Munthu waumbombo amautsa mkangano, koma wokhulupirira Chauta adzalemera.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 2:1

Nchifukwa chake tayani choipa chonse, kunyenga konse, chiphamaso, kaduka ndi masinjiriro onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 12:14

Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 26:17

Amene angoloŵerera ndeu ya eniake, ali ngati munthu wombwandira galu wongodziyendera.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 12:25

Yesu adaadziŵa zimenezi, motero adaŵauza kuti, “Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo kutha kwake nkomweko. Ndipo anthu a m'mudzi uliwonse kapena a m'banja lililonse akayamba kuukirana, mudzi wotere kapena banja lotere silingalimbe ai.

Mutu    |  Mabaibulo
Tito 1:10-11

Paja pali anthu ambiri osaweruzika, makamaka pakati pa gulu la anthu ochokera ku Chiyuda. Anthu ameneŵa amalankhula nkhani zopanda pake nkumasokeretsa anzao.

Nkofunika kuŵakhalitsa chete, chifukwa akusokoneza mabanja ena athunthu pakuŵaphunzitsa zimene sayenera kuŵaphunzitsa. Amangochita zimenezi ndi cholinga choipa, chofuna kupata ndalama.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 16:17-18

Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa,

pakuti anthu otere satumikira Khristu Ambuye athu, koma amangotumikira zilakolako zao basi. Ndi mau okoma ndi oshashalika amanyenga anthu a mitima yoona.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:1-2

Usamavutika ndi anthu oipa. Usamakhumbira kukhala ngati ochita zoipa,

Kanthaŵi pang'ono ndipo munthu woipa sadzakhalaponso, ngakhale muyang'ane bwino pamalo pamene analiri, simudzampezapo.

Koma anthu ofatsa adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala pa mtendere wosaneneka.

Munthu woipa amachitira upo mnzake wabwino, namamtuzulira maso mwachidani.

Koma Chauta amamseka munthu woipayo, poti amaona kuti tsiku lake la kuwonongeka likubwera.

Anthu oipa amasolola lupanga, ndipo amakoka mauta, kuti aphe anthu ovutika ndi osoŵa, amene amayenda molungama.

Koma lupanga lao lidzalasa mitima ya eniake omwewo, ndipo mauta ao adzaŵathyokera m'manja.

Nkwabwino kukhala m'chilungamo ndi kusauka, kupambana kukhala nazo zokoma zambiri zimene munthu woipa ali nazo.

Pakuti Chauta adzathetsa mphamvu za anthu oipa, koma adzalimbikitsa anthu onse abwino.

Chauta amasamalira moyo wa anthu angwiro, ndipo choloŵa chao chidzakhalapo mpaka muyaya.

Pa nthaŵi ya mavuto sadzazunzika, pa nthaŵi yanjala, adzakhala nazo zakudya zochuluka.

pakuti mosachedwa amanyala ngati udzu, ndipo amafota ngati masamba aaŵisi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:19-20

Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso.

Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu.

Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 19:19

Munthu wa ukali woopsa adzalandira chilango chomuyenerera, pakuti ukamlekerera wotereyu, zidzaipa koposa kale.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 12:20

Ndikuwopa kuti ndikadzabwera kwanuko, mwina nkudzakupezani muli osiyana ndi m'mene ndikadafunira. Ndikuwopa kuti mwina inunso nkudzandipeza ine wosiyana ndi m'mene mukadafunira. Ndikuwopanso kuti mwina ine nkudzapeza kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusinjirirana, ugogodi, kudzitukumula, ndiponso chisokonezo.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:1-5

“Musamaweruza anthu ena kuti ndi olakwa, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni.

Kapena atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka?

Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha?

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.

“Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri.

Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.

“Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa.

Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu?

Chonchonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo woipa umabala zipatso zoipa.

Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapena mtengo woipa kubala zipatso zabwino ai.

Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula nkuuponya pa moto.

M'mene inu mumaweruzira ena, ndi m'menenso Mulungu adzakuweruzirani inuyo. Ndipo muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.

Choncho mudzaŵadziŵira zochita zao.

“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.

Pa tsiku lachiweruzo anthu ambiri azidzanena kuti, ‘Ambuye, Ambuye, kodi suja ife tinkalalika mau a Mulungu m'dzina lanu? Suja tinkatulutsa mizimu yonyansa potchula dzina lanu? Suja tinkachita ntchito zamphamvu zambiri m'dzina lanu?’

Apo Ine ndidzaŵauza poyera kuti, ‘Sindidaakudziŵani konse. Chokani apa, anthu ochita zoipa.’

“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe.

Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba.

Koma aliyense wongomva mau angaŵa, osaŵagwiritsa ntchito, ali ngati munthu wopusa amene adaamanga nyumba yake pa mchenga.

Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo, ndipo idagwa. Kugwa kwake kunali koopsa.”

Yesu atatsiriza kunena zimenezi, anthu onse aja adadabwa ndi kaphunzitsidwe kake,

chifukwa ankaŵaphunzitsa monga munthu waulamuliro osati monga m'mene ankachitira aphunzitsi a Malamulo.

Umaoneranji kachitsotso kamene kali m'maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe?

Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, ‘Taima ntakuchotsa kachitsotso kali m'maso mwakoka,’ pamene m'maso mwako momwe muli chimtengo?

Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m'maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m'maso mwa mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 14:13

Tsono tiyeni tileke kumaweruzana. Makamaka mutsimikize kuti musachite kanthu kalikonse kophunthwitsa mbale wanu, kapena komchimwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 6:16-19

Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa:

maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa,

mtima wokonzekera kuchita zoipa, mapazi othamangira msangamsanga ku zoipa,

mboni yonama yolankhula mabodza, ndi munthu woutsa chidani pakati pa abale.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 3:14-16

Koma ngati muli ndi mtima wakaduka ndi wodzikonda, musamanyada ndi kutsutsana ndi choona pakunena mabodza.

Nzeru zotere si zochokera Kumwamba, koma ndi nzapansipano, ndi za anthu chabe, ndiponso nzochokera ku mizimu yoipa.

Pajatu pamene pali kaduka ndi kudzikonda, pomweponso pali chisokonezo ndi ntchito yoipa ya mtundu uliwonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:20

kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko,

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 6:1-8

Ngati wina ali ndi mlandu ndi mkhristu mnzake, angathe bwanji kukauzengetsa kwa oweruza amene ali akunja, osati kwa akhristu anzake?

mbala, aumbombo, zidakwa, augogodi, kapena achifwamba, ameneŵa sadzaulaŵa Ufumu wa Mulungu.

Enanu munali otere kale, koma mudayeretsedwa, mudasanduka anthu a Mulungu, ndipo mudapezeka olungama pamaso pake. Zimenezi zidachitika m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndiponso mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

Zinthu zonse nzololedwa kwa ine, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwadi kwa ine, koma sindingalole kuti chilichonse chindigonjetse.

Chakudya, kwake nkuloŵa m'mimba, ndipo mimba, kwake nkulandira chakudya. Koma Mulungu adzaononga ziŵiri zonsezo. Thupi la munthu si lochitira dama, koma ndi la Ambuye, ndipo Ambuye ndiwo mwiniwake thupilo.

Mulungu adaukitsa Ambuye kwa akufa, ndipo mwa mphamvu yake adzatiwukitsa ifenso.

Kodi inu simudziŵa kuti matupi anu ndi ziwalo za Khristu? Monga tsono ine nkutenga ziwalo za Khristu nkuzisandutsa ziwalo za mkazi wadama? Chosatheka!

Kaya simudziŵa kuti munthu amene amadzipereka kwa mkazi wadama, iyeyo ndi mkaziyo amasanduka thupi limodzi? Paja Malembo akuti, “Aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi.”

Koma amene amadzipereka kwa Ambuye, iyeyo ndi Ambuye amakhala mzimu umodzi.

Thaŵani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe.

Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso.

Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe?

Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.

Kodi simukudziŵa kuti tidzaweruza angelo? Nanji zinthu za moyo wapansipano?

Tsono ngati muli ndi milandu pa zinthu zotere, bwanji mumaika anthu amene mpingo suŵayesa kanthu kuti aiweruze?

Ndikunena zimenezi kuti ndikuchititseni manyazi. Kodi mwa inu palibe ndi mmodzi yemwe wanzeru, amene angathe kuweruza mlandu pakati pa akhristu anzake?

Bwanji mkhristu akuimba mlandu mkhristu mnzake, mlanduwo nkuupereka kwa anthu akunja kuti auzenge?

Chokha chakuti mumaimbana milandu inu nokhanokha, chatsimikiza kale kuti mwalephereratu. Bwanji osangopirira pamene ena akulakwirani? Bwanji osangolola kuti inuyo akubereni?

Koma inuyo ndi amene mukulakwira ena, ndipo mukuŵabera, ngakhale iwowo ndi akhristu anzanu!

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:2

Yuwodiyayo ndi Sintikeyo ndaŵapemba, chonde akhale omvana, popeza kuti ndi abale mwa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 6:4

Munthu wotere ndi wodzitukumula ndi kunyada, sadziŵa kanthu. Mtima wake ngwodwala, wongofuna zotsutsanatsutsana ndi kukangana pa mau chabe. Zimenezi zimabweretsa kaduka, kusamvana, kusinjirirana, kuganizirana zoipa,

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:165

Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 29:22

Munthu wamangaŵa amautsa mikangano, munthu wokalipakalipa amabweretsa zolakwa zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 4:8

Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:5-6

Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu,

akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 5:18-19

Wochita zonsezi ndi Mulungu, amene mwa Khristu adatiyanjanitsa ndi Iye mwini, ndipo adatipatsa ntchito yolalikira anthu chiyanjanitsocho.

Ndiye kuti mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, osaŵaŵerengera machimo ao. Ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiŵalalike.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 3:17

Koma nzeru zochokera Kumwamba, poyamba nzangwiro, kuwonjeza apo nzamtendere, zofatsa ndi zomvera bwino. Ndi za chifundo chambiri, ndipo zipatso zake zabwino nzochuluka. Nzeruzo sizikondera kapena kuchita chiphamaso.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 1:1-2

Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu,

koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 5:15-16

Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru.

Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 12:15

Zimene amachita munthu wopusa mwiniwakeyo amaziyesa zolungama, koma munthu wanzeru amamvetsera malangizo a ena.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:26

Tisakhale odzitukumula, oputana, kapena ochitirana dumbo.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:23-24

“Nchifukwa chake ngati wabwera ndi chopereka chako ku guwa, nthaŵi yomweyo nkukumbukira kuti mnzako wina ali nawe nkanthu,

siya chopereka chakocho kuguwa komweko, ndipo pita, kayambe wayanjana naye mnzakoyo. Pambuyo pake ndiye ubwere kudzapereka chopereka chako chija.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:20

Wina akamanena kuti, “Ndimakonda Mulungu”, komabe nkumadana ndi mbale wake, ndi wonama ameneyo. Pakuti munthu wosakonda mbale wake amene wamuwona, sangathe kukonda Mulungu amene sadamuwone.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:1

Kuyankha kofatsa kumazimitsa mkwiyo, koma mau ozaza amakolezera ukali.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 4:6

Nthaŵi zonse mau anu akhale okoma, opindulitsa ena, kuti potero mudziŵe m'mene muyenera kuyankhira munthu aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 16:19

Anthu onse adaimva mbiri ya kumvera kwanu. Tsono ine ndikunyadira inuyo, koma ndifuna kuti mukhale anzeru pa zabwino, ndi othaŵa zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 10:24-25

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino.

Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:30

Usamakangane ndi munthu popanda chifukwa pamene iyeyo sadakuchite choipa chilichonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 3:13

Ndani mwa inu ali wanzeru ndi womvetsa zinthu? Aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru zimaongoleradi zochita zake zofatsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:2

Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 18:21-22

Pamenepo Petro adadzafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi mbale wanga atamandichimwira, ndidzamkhululukire kangati? Kodi ndidzachite kufikitsa kasanunkaŵiri?”

Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ndikuti kasanunkaŵiri kokha ngati, iyai, koma mpaka kasanunkaŵiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi aŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:1

Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 19:11

Nzeru zimapatsa munthu mtima wosakwiya msanga, ulemerero wake wagona pa kusalabadako za chipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:31-32

Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse.

Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 14:33

Mulungu safuna chisokonezo ai, koma mtendere. Monga zimachitikira m'mipingo yonse ya anthu a Mulungu,

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 2:1-2

Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni.

Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza,

Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate.

Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera.

Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.

Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo,

kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi,

pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe.

Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu.

Chimodzimodzi inunso muzikondwa, ndi kusangalala nane pamodzi.

Ngati Ambuye Yesu alola, ndikhulupirira kuti ndidzatha kutuma Timoteo kwanuko msanga, kuti mtima wanga ukhale pansi nditamva za kumeneko.

Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 3:10-11

Paja mau a Mulungu akuti. “Yemwe afuna kukondwera ndi moyo, ndi kuwona masiku abwino, aletse lilime lake kulankhula zoipa, ndiponso milomo yake kunena mabodza.

Alewe zoipa, azichita zabwino. Afunefune mtendere ndi kuyesetsa kuupeza.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 4:2-3

Mumalakalaka zinthu, koma zimakusoŵani, nchifukwa chake mumapha munthu. Mumasirira zinthu, koma simungathe kuzipeza, nchifukwa chake mumamenyana, nkumachita nkhondo. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu.

Ndipo ngakhale mupemphe, simulandira, chifukwa mumapempha molakwa. Zimene mumapempha, mumafuna kungozimwazira pa zokukondweretsani basi.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:22

Popanda uphungu zolinga zako zimalakwika, koma aphungu akachuluka, zolinga zako zimathekadi.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 11:20

Mumangolekerera munthu akakuyesani akapolo, kapena akadya chuma chanu, kapena akakunyengani, kapena akakunyozani, kapena akakumenyani kumaso.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:15-16

Koma ngati muyamba kulumana ndi kukadzulana, muchenjere kuti mungaonongane kotheratu.

Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:14-15

Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.

Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 18:35

“Inunsotu Atate anga akumwamba adzakuchitani zomwezo, aliyense mwa inu akapanda kukhululukira mbale wake ndi mtima wonse.”

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 1:5

Cholinga changa pokupatsa malangizo ameneŵa, nchakuti pakhale chikondi chochokera mu mtima woyera, mu mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndiponso m'chikhulupiriro chopanda chiphamaso.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:10-11

Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu.

Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 1:11

Pakuti ena a m'banja la Koloe andifotokozera kuti pali kukangana pakati panu, abale anga.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 28:10

Amene amasokeza anthu olungama kuti azitsata njira yoipa, adzagwa m'dzenje lake lomwe. Koma anthu amene alibe cholakwa adzalandira choloŵa chabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 1:7

Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 14:19-20

Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.

Wina amakhulupirira kuti palibe choletsa kudya chakudya chilichonse. Koma wina, amene chikhulupiriro chake nchofooka, amadya zamasamba zokha.

Chakudya chisakuwonongetseni ntchito ya Mulungu. Zakudya zonse nzololedwa kuzidya, koma nkulakwa kudya chinthu chimene chingachimwitse anzathu.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:27

Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino,

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:37

Upenye munthu wopanda cholakwa ndi wolungama, ndipo udzapeza kuti munthu wamtendere ali ndi zidzukulu zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:5

Ngodala anthu ofatsa, pakuti Mulungu adzaŵapatsa dziko la pansi pano kuti likhale lao.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 12:18

Wofulumira kulankhula, zonena zake zimalasa ngati mpeni, koma mau a munthu wanzeru amachiza anzake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 85:10

Chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika zidzakumana. Chilungamo ndi mtendere zidzagwirizana.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 13:11

Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 16:7

Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Chauta, ngakhale adani ake omwe amakhala naye mwamtendere.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:1-2

Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu.

ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziŵe kwenikweni ndi kufanafana naye.

M'moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse.

Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.

Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.

Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.

Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.

Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.

Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.

Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye.

Inu amuna, muzikonda akazi anu, musamaŵavutitse ai.

Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 1:29-31

Mitima yao idadzaza ndi zosalungama zamitundumitundu, monga kuipa, umbombo ndi dumbo. Amangolingalira za kaduka, za kupha anthu, za ndeu, za kunyenga, ndi za njiru. Amachita ugogodi,

Umasimba za Mwana wake, Yesu Ambuye athu. Poyang'anira umunthu wake, kholo lake ndi Davide,

amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao.

Ndi opusa, osakhulupirika, okhakhala moyo, ndi opanda chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 133:1-3

Ati kukoma ndi kukondweretsa ati, anthu akakhala amodzi mwaubale!

Ndi ngati mafuta amtengowapatali oŵathira pa mutu, otsikira ku ndevu, ku ndevu za Aroni, oyenderera mpaka ku khosi la mkanjo wake.

Ndi ngati mame a ku Heremoni, omatsikira ku mapiri a Ziyoni. Ku Ziyoni Chauta amaperekako madalitso, ndiye kuti moyo wamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 2:12

Samalani mayendedwe anu pakati pa akunja, kuti ngakhale azikusinjirirani kuti ndinu anthu ochita zoipa, komabe aziwona ntchito zanu zabwino. Apo adzalemekeza Mulungu pa tsiku limene Iye adzaŵayendere.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:19-21

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa,

Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai.

kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko,

dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:4-6

Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu Woyera mmodzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene Mulungu adakuitanirani.

Pali Mbuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi.

Pali Mulungu mmodzi amene ali Atate a anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse, amagwira ntchito kudzera mwa onse, ndipo ali mwa onse.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Woyera ndi Wokwezeka Mulungu wanga, woyenera ulemerero ndi kukwezedwa konse. Zinthu zazikulu mwachita pa moyo wanga, tsiku lililonse mumandikhazika mwatsopano, mumandiyenga, ndipo mumandipatsa mtima wolungama. Ambuye, tsiku lililonse ndimakufunani, ndipo mu mtima mwanga muli chikhumbo chachikulu chokhala moyera pamaso panu. Nthawi ino ndikupemphani mundisanthule ndi kuchotsa chilichonse chomwe sichikukondweretsani chifukwa sindikufuna kukulephani. Ndikupempha chikhululukiro pa zolakwa zanga, ngati nthawi ina ndakhala munthu wobweretsa ndewu pakati pa abale anga ndikupempha chikhululukiro. Mundimasule ku ndewu, kunena zinthu zomwe sizikukondweretsani, kunena zoyipa za mnzanga, mundimasule ku kuyambitsa mkangano ndi kukhala munthu woyipa. Ndikufuna kukhala mwa inu ndipo monga momwe Mawu anu amanenera m'buku la Miyambo kuti ulemu wa munthu ndi kusiya mkangano; koma chitsiru chilichonse chimadzilowetsa mmenemo. Mtima wanga, malingaliro anga, ndi maganizo anga zili pamaso panu, mundipange monga inu. M'dzina la Yesu, zikomo chifukwa cha zonse Ambuye. Ameni.