Mtima wanga, ukakhala wodzala ndi mkwiyo, umaona moyo uli mdima. Koma iwe sukugonja ndi malingaliro oipa amenewa, ukutha kuona zinthu zabwino zomwe moyo ukupereka ndi kuyamikira madalitso a Mulungu. Mkwiyo umatiletsa kuona bwino ndi kusangalala mokwanira, umatibera mtendere ndi chimwemwe chathu.
Kukhala opanda mkwiyo ndiye chinthu chabwino kwambiri, chifukwa mkwiyo umangobweretsa kuvutika ndi kulephera kupita patsogolo. Ndikulimbikitsa kuti ulankhule ndi Mulungu, umuuze zomwe zikukuvutitsa, umupemphe kuti akukonzenso ndi kukutsogolera m’chifuniro chake changwino.
Ambuye ali ndi mapulani akuluakulu pa moyo wako! Monga mmene lemba la Ahebri 12:15 limatiuza, "Yang'anirani kuti pasakhale wina amene alephere kulandira chisomo cha Mulungu; kuti pasakhale mizu ya mkwiyo imene idzabuke ndi kubweretsa mavuto, ndi kuipitsa ambiri."
Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake.
Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse.
Pakuti ndakuwona kuti ndiwe wodzaza ndi ndulu yoŵaŵa, ndiponso ndiwe womangidwa ndi maunyolo a zoipa.”
Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.
Pamene paja ndinkavutika ndi maganizo, ndi kumamva cholasa mumtimamu,
ndinali wopusa wosamvetsa kanthu, ndinali ngati chilombo kwa Inu.
“Nchifukwa chake sindidzatseka pakamwa. Ndiyenera kulankhula, chifukwa kukhosi kwanga kuli nthumanzi. Ndiyenera kudandaula, chifukwa mumtima mwanga muli zoŵaŵa.
Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse.
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Mwana wopusa amamvetsa chisoni atate ake, ndipo amapweteka mtima wa amai ake amene adambala.
Davide adavutika koopsa, pakuti anthu ankakamba zoti amponye miyala, chifukwa cha chisoni chao pokumbukira ana ao aamuna ndi aakazi. Koma Davide adapeza mphamvu mwa Chauta, Mulungu wake.
Iwe ukungodzipweteka ndi mkwiyo wako. Kodi dziko lapansi lidzasanduka bwinja chifukwa choti iweyo uli wokwiya? Kodi thanthwe nkudzachotsedwa pamalo pake, kuti likukondweretse iweyo?
Esau atamva zimenezi, adalira kwambiri ndi mtima woŵaŵa, ndipo adati, “Bambo, pepani inenso mundidalitseko.”
Mtima wa munthu umatha kupirira matenda, koma munthu akataya mtima, ndani angathe kumlimbitsanso?
Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”
“Ndithudi, ndatopa nawo moyo wanga, choncho ndidzalankhula zodandaula zanga momasuka. Ndidzaulula zoŵaŵa zonse zamumtima.
Koma ngati muli ndi mtima wakaduka ndi wodzikonda, musamanyada ndi kutsutsana ndi choona pakunena mabodza.
M'kamwa mwao m'moopsa ngati manda apululu, ndi lilime lao amalankhula zonyenga, pamilomo pao pamatuluka mau aululu, ululu wake wonga wa mamba.
M'kamwa mwao m'modzaza ndi matemberero, mumatuluka mau oŵaŵa.
Nchifukwa chake tembenuka mtima, uleke choipa chakochi. Pempha Ambuye kuti mwina mwake nkukukhululukira maganizo a mumtima mwakoŵa.
Pakuti ndakuwona kuti ndiwe wodzaza ndi ndulu yoŵaŵa, ndiponso ndiwe womangidwa ndi maunyolo a zoipa.”
Anthu okuchitani choipa, osaŵabwezera choipa, okuchitani chipongwe osaŵabwezera chipongwe. Koma inu muziŵadalitsa, pakuti inuyo Mulungu adakuitanirani mkhalidwe wotere, kuti mulandire madalitso ake.
Mzimu wa Mulungu udandikweza ndi kundinyamula, ndipo ndidachokapo ndili ndi mtima woŵaŵa ndi wonyuka. Mphamvu za Chauta zidandiloŵa dzolimba.
“Ndithu ngati mukhululukira anthu machimo ao, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani inunso.
Koma ngati simukhululukira anthu machimo ao, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.
Chimene ndidamvera zoŵaŵa nkuti ndipeze bwino. Mwapulumutsa moyo wanga ku manda, mwataya machimo anga onse kumbuyo kwanu.
Hanayo ankavutika kwambiri mumtima mwake, ndipo adapemphera kwa Chauta, akulira ndi mtima woŵaŵa.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
Moyo wanga ukutha chifukwa cha chisoni, zaka zanganso zikutha chifukwa cha kulira kwambiri. Mphamvu zanga zatheratu chifukwa cha kulakwa kwanga, mafupa anga agooka.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.
Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu.
“Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?”
Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Mukakhululukira munthu, inenso ndimkhululukira. Ngati ine ndakhululukira, patakhala kanthu koti ndakhululukira, ndiye kuti ndakhululukira chifukwa cha inu pamaso pa Khristu.
Cholinga chake nkuti Satana asatichenjerere, paja tikudziŵa njira zake.
Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire.
Musampatse mpata Satana woti akugwetseni.
Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
Musadandaule monga momwe adaadandaulira ena mwa iwo: paja adaphedwa ndi mngelo wodzetsa imfa.
Paja tikumdziŵa kale amene adati, “Kulipsira nkwanga, ndidzakhaulitsa ndine.” Adatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.”
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muzikonda adani anu ndipo muziŵapempherera amene amakuzunzani.
Nkhaŵa ya munthu imakhala ngati katundu wolemera mumtima mwake, koma mau abwino amamsangalatsa.
Mundimvere, ndipo mundiyankhe. Mtima wanga suli m'malo chifukwa cha mavuto anga.
Mnzanga adatambasula dzanja lake kuti amenye abwenzi ake, adaphwanya chipangano chake.
Mau ake anali osalala kupambana batala, komabe mumtima mwake munali zankhondo. Mau ake anali ofeŵa kupambana mafuta, komabe anali ndi malupanga osololasolola.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Koma Inu Mulungu mudzaŵaponya adani anga m'dzenje lozama lachiwonongeko. Anthu okhetsa magazi ndi onyenga sadzafika ngakhale theka la masiku ao. Koma ine ndidzadalira Inu.
Ndikuda nkhaŵa chifukwa adani anga akundifuulira, anthu oipa akundipsinja. Akundivutitsa kwambiri, akundikwiyira kosalekeza.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.
Onetsetsani kuti wina aliyense mnzake akamchita choipa, asabwezere choipacho. Koma nthaŵi zonse muziyesetsa kuchitira zabwino anzanu ndi anthu ena onse.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino.
Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Ndipo mtumiki wa Ambuye asamakhala wokanganakangana ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa onse, mphunzitsi wokhoza, munthu wodziŵa kupirira mavuto.
Akhale wofatsa polangiza otsutsana naye. Mwina Mulungu angaŵapatse mwai woti atembenuke ndi kuzindikira choona.
Pamenepo nzeru zao zidzabweramo, ndipo adzapulumuka mu msampha wa Satana, amene adaaŵagwira kuti azichita zofuna zake.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Chirikizeni molingana ndi malonjezo anu aja, kuti ndizikhala ndi moyo, ndipo anthu asandichititse manyazi, chifukwa ndine wokhulupirika.
Amoyo, amoyo okha, ndiwo amakutamandani, monga m'mene ndikuchitira ine tsopanomu. Atate amauza ana ao za kukhulupirika kwanu.
Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso.
kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko,
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Koma adani anga ondifunira zoipa, amati, “Kodi munthu ameneyu adzafa liti, kuti aiŵalike?”
Amene amabwera kudzandiwona, ndi wosakhulupirika, mumtima mwake amaganiza zoipa za ine, ndipo akatuluka, amakaziwanditsa.
Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.
Usamavutika ndi anthu oipa. Usamakhumbira kukhala ngati ochita zoipa,
Kanthaŵi pang'ono ndipo munthu woipa sadzakhalaponso, ngakhale muyang'ane bwino pamalo pamene analiri, simudzampezapo.
Koma anthu ofatsa adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala pa mtendere wosaneneka.
Munthu woipa amachitira upo mnzake wabwino, namamtuzulira maso mwachidani.
Koma Chauta amamseka munthu woipayo, poti amaona kuti tsiku lake la kuwonongeka likubwera.
Anthu oipa amasolola lupanga, ndipo amakoka mauta, kuti aphe anthu ovutika ndi osoŵa, amene amayenda molungama.
Koma lupanga lao lidzalasa mitima ya eniake omwewo, ndipo mauta ao adzaŵathyokera m'manja.
Nkwabwino kukhala m'chilungamo ndi kusauka, kupambana kukhala nazo zokoma zambiri zimene munthu woipa ali nazo.
Pakuti Chauta adzathetsa mphamvu za anthu oipa, koma adzalimbikitsa anthu onse abwino.
Chauta amasamalira moyo wa anthu angwiro, ndipo choloŵa chao chidzakhalapo mpaka muyaya.
Pa nthaŵi ya mavuto sadzazunzika, pa nthaŵi yanjala, adzakhala nazo zakudya zochuluka.
pakuti mosachedwa amanyala ngati udzu, ndipo amafota ngati masamba aaŵisi.
Pamenepo Petro adadzafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi mbale wanga atamandichimwira, ndidzamkhululukire kangati? Kodi ndidzachite kufikitsa kasanunkaŵiri?”
Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ndikuti kasanunkaŵiri kokha ngati, iyai, koma mpaka kasanunkaŵiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi aŵiri.
Aliyense wodana ndi mnzake, ndi wopha anthu. Ndipo mukudziŵa kuti aliyense wopha anthu, alibe moyo wosatha mumtima mwake.
Kodi nkhondo zimachokera kuti? Kukangana pakati panu kumachokera kuti? Kodi suja zimachokera ku zilakolako zanu zathupi, zimene zimachita nkhondo mwa inu?
Mudzichepetse pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.
Abale, musamasinjirirana. Wosinjirira mbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo a Mulungu. Koma ukaweruza Malamulo a Mulungu, ndiye kuti sukuchita zimene Malamulowo akunena, ukudziyesa woweruza.
Mulungu yekha ndiye wopanga Malamulo ndiponso woweruza. Ndiyenso wotha kupulumutsa ndi kuwononga. Nanga iwe ndiwe yani kuti uziweruza mnzako?
Onani tsono, inu amene mukuti, “Lero kapena maŵa tipita ku mzinda wakutiwakuti, ndipo tikachitako malonda chaka chimodzi kuti tikaphe ndalama,”
m'menemo inuyo zamaŵa simukuzidziŵa. Kodi moyo wanu ngwotani? Pajatu inu muli ngati utsi chabe, umene umangooneka pa kanthaŵi, posachedwa nkuzimirira.
Kwenikweni muyenera kumanena kuti, “Ambuye akalola, tikakhala ndi moyo, tidzachita chakutichakuti.”
Koma monga zilirimu, mumanyada ndi kudzitama. Kunyada konse kotere nkoipa.
Munthu akadziŵa zabwino zimene ayenera kuchita, napanda kuzichita, ndiye kuti wachimwa.
Mumalakalaka zinthu, koma zimakusoŵani, nchifukwa chake mumapha munthu. Mumasirira zinthu, koma simungathe kuzipeza, nchifukwa chake mumamenyana, nkumachita nkhondo. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu.
Ndipo ngakhale mupemphe, simulandira, chifukwa mumapempha molakwa. Zimene mumapempha, mumafuna kungozimwazira pa zokukondweretsani basi.
Kuli bwino kudyera masamba pali chikondi, kupambana kudyera nyama ya ng'ombe yonenepa pali chidani.
Koma ochita zaupandu, namatsutsa zoona nkumachita zosalungama, Mulungu adzaŵakwiyira ndi kuŵazazira.
Amene ali ake a Khristu Yesu, adalipachika pa mtanda khalidwe lao lokonda zoipa, pamodzi ndi zokhumba zake ndi zilakolako zake.
Paja ukakuntha mkaka, mafuta amapangika. Ukapsinya mphuno, magazi amatuluka, ndipo ukautsa mkwiyo, mikangano imaoneka.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
“Musamaweruza anthu ena kuti ndi olakwa, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni.
Kapena atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka?
Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha?
Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.
“Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri.
Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.
“Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa.
Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu?
Chonchonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo woipa umabala zipatso zoipa.
Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapena mtengo woipa kubala zipatso zabwino ai.
Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula nkuuponya pa moto.
M'mene inu mumaweruzira ena, ndi m'menenso Mulungu adzakuweruzirani inuyo. Ndipo muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.
Imvani mau anga, Inu Mulungu, pamene ndikukudandaulirani. Tetezani moyo wanga kwa mdani woopsa.
Chauta adalitse anthu ake mtendere ndi chimwemwe zikhale nao, anthu akondwere chifukwa cha Chauta
Tchinjirizeni ku upo wachiwembu wa anthu oipa, tetezeni ku chiwawa cha anthu ochita zoipa.
Iwo amanola lilime lao ngati lupanga, amaponya mau obaya ngati mivi.
Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.
Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa.
Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu.
Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Pansi pano chinthu chilichonse chili ndi nyengo yake ndi nthaŵi yake yomwe adaika Mulungu:
Ndaziwona ntchito zimene Mulungu adapatsa anthu kuti azizigwira.
Adapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthaŵi yake. M'mitima mwa anthu Mulungu adaikanso nzeru zotanthauzira zochitika za pa mibadwo ndi mibadwo. Komabe anthuwo sangathe kuzitulukira ntchito zonse za Mulungu kuyambira pa chiyambi mpaka pomalizira.
Ndikudziŵa kuti kwa anthu palibe chabwino china choposa kukhala osangalala ndi kumadzikondweretsa nthaŵi yonse ya moyo wao.
Ndi mphatso ya Mulungu kwa anthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ntchito zao zolemetsa.
Ndikudziŵa kuti zimene Mulungu amazichita zimakhazikika mpaka muyaya. Palibe zimene zingathe kuwonjezedwa kapena kuchotsedwapo pa zimenezo. Mulungu adazipanga motero, kuti choncho anthu azimumvera.
Zimene zilipo tsopano zidaaliponso kale. Zimene zidzakhalepo kutsogolo, zidaaliponso kale. Mulungu amabwezanso zakale zimene zidapita kuti zichitikenso.
China chimene ndidachiwona pansi pano ndi ichi: Koyenera kukhala chiweruzo chabwino, komwekonso kumapezeka kuipa mtima. Koyenera kukhala chilungamo, komwekonso kumapezeka zoipa.
Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Mulungu adzaŵaweruza onse, abwino ndi oipa omwe, pakuti adaika nthaŵi yochitikira chinthu chilichonse ndiponso ntchito iliyonse.”
Kunena za anthu, ndinkalingaliranso kuti, “Mulungu amaŵayesa ndi cholinga choti aŵaonetse kuti iwowo sasiyana konse ndi nyama.
Zimene zimachitikira anthu, zomwezonso zimachitikira nyama. Monga chinacho chimafa, chinacho chimafanso. Zonsezo zimapuma mpweya umodzimodzi, munthu saposa nyama. Zonsezi nzopandapake.
pali nthaŵi yobadwa ndi nthaŵi yomwalira, pali nthaŵi yobzala ndi nthaŵi yozula zobzalazo.
Zonse zimapita kumodzimodzi. Zonsezo nzochokera ku dothi, ndipo zimabwerera kudothi komweko.
Kodi ndani angatsimikize kuti mzimu wa munthu ndiwo umakwera kumwamba, koma mpweya wa nyama umatsikira kunsi kwa nthaka?
Choncho ndidaona kuti palibe chinthu chabwino kuposa kuti munthu azikondwerera ntchito yake, pakuti chake chenicheni nchimenechi. Ndani angathe kudziŵa chimene chidzamchitikire iye atafa?”
Pali nthaŵi yakupha ndi nthaŵi yochiritsa, nthaŵi yogwetsa ndi nthaŵi yomanga.
Pali nthaŵi yomva chisoni ndi nthaŵi yosangalala, nthaŵi yolira maliro ndi nthaŵi yovina.
Pali nthaŵi yokhala malo amodzi ndi nthaŵi yotalikirana, nthaŵi yokumbatirana ndi nthaŵi yoleka zokumbatiranazo.
Pali nthaŵi yofunafuna ndi nthaŵi yotaya, nthaŵi yosunga ndi nthaŵi yomwaza.
Pali nthaŵi yong'amba ndi nthaŵi yosoka, nthaŵi yokhala chete ndi nthaŵi yolankhula.
Pali nthaŵi yokondana ndi nthaŵi yodana, nthaŵi ya nkhondo ndi nthaŵi ya mtendere.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu,
akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
Inu Chauta, mukadaŵerengera machimo, ndani akadakhala chilili opanda mlandu, Ambuye?
Koma inu mumakhululukira, nchifukwa chake timakulemekezani.
Abale, mchenjere, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woipa ndi wosakhulupirira, womlekanitsa ndi Mulungu wamoyo.
Kwenikweni muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku ikadalipo nthaŵi, imene m'mau a Mulungu imatchedwa kuti, “Lero”. Muzichita zimenezi, kuwopa kuti wina aliyense mwa inu angaumitsidwe mtima ndi chinyengo cha uchimo.
Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso.
Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe?
Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, ndipo usaiŵale zabwino zake zonse.
Tamandani Chauta, inu angelo ake, inu amphamvu amene mumamva mau ake, amene mumachita zimene amalamula.
Tamandani Chauta, inu magulu a ankhondo ake onse, atumiki ake ochita zimene Iye afuna.
Tamandani Chauta, inu zolengedwa zake zonse, ku madera onse a ufumu wake. Nawenso mtima wanga, tamanda Chauta!
Ndiye amene amakhululukira machimo ako onse, ndi kuchiritsa matenda ako onse.
Ndiye amene amapulumutsa moyo wako ku manda. Amakuveka chikondi chake chosasinthika ndiponso chifundo chake ngati chisoti chaufumu.
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga.
Inu Aisraele, ndinu mboni zanga, ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani, kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina, ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina.
Chauta ndi Ineyo, mpulumutsi wanu ndine ndekha.
Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta.
Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.”
Chauta, Momboli wanu, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babiloni, kuti ndikupulumutseni. Ndidzagwetsa zipata za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira.
Ine ndine Chauta, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israele. Ine ndekha ndine mfumu yanu.”
Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu.
Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale.
Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale.
Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu.
Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.
Ndipo anthu angalalike bwanji ngati palibe oŵatuma? Paja mau a Mulungu akuti, “Nchokondweretsa zedi kuwona olalika Uthenga Wabwino akufika.”
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo.
Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.