Mulungu ndi wapamwamba komanso woyenera ulemu, woyenera kutamandidwa konse. Pamaso pake, mapiri amanjenjemera, ndipo palibe wopanduka amene adzaperekedwa chilango. Dzina la Wamuyaya silitha; ali ndi mphamvu zosayerekezeka.
Chifukwa chake, konza zomwe zikuoneka zopindika mumtima mwako. Ngati pali choipa mumtima mwako, funa chikhululukiro kwa Mulungu, pakuti iye ndi wolungama komanso wachifundo. Usatsutse mawu ake kapena chifuniro chake, chifukwa sudzapila padziko lapansi ngati uchita zinthu mosemphana ndi zimene iye akufuna.
Lero ndi tsiku loyanjanirana naye, lotsegula mtima wako ndikudzitukumula pamaso pake, chifukwa mtima wodzichepetsa sudzatayidwa naye. Muzindikire m'njira zanu zonse ndipo musadzione ngati wanzeru pa maganizo anu, koma m'malo mwake, dalirani Mulungu ndipo musamadzikulitse; chifukwa, ngati simutero, moyo wanu udzawonongeka ndipo mudzapandukira amene anakulengani ndi kukupatsani moyo.
Njira za Mulungu ndi zangwiro ndipo zimatsogolera ku moyo wosatha, pomwe njira za munthu ndi zoyipa ndipo zimatsogolera ku imfa.
Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, ‘Chenjera, ndidzakuchotsa pa dziko lapansi. Ufa chaka chino chisanathe, chifukwa chakuti wakhala ukulalikira zopandukira Chauta.’ ”
Anthu osiyidwa, Mulungu amaŵapatsa malo okhalamo, am'ndende amaŵatulutsa kuti akhale pa ufulu, koma anthu oukira, amaŵapirikitsira ku nthaka yoguga.
Koma Samuele adati, “Kodi Chauta amakondwa ndi chiti: nsembe zopsereza ndi nsembe zina, kapena kumvera mau ake? Ndithu, ndi kumvera ndi kupereka nsembe kwabwino kwambiri nkumvera. Ndi kutchera khutu ndi kupereka mafuta ankhosa kwabwino kwambiri nkutchera khutu.
Kugalukira kuli ngati tchimo loombeza, kukhala wokanika kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu.”
Koma aphedwe mneneri aliyense kapena womasulira maloto aliyense amene akuuzani kuti muukire Chauta, Mulungu wanu, amene adakutulutsani ku Ejipito ndi kukuwombolani m'dziko laukapolo. Munthu wotero ndi woipa, chifukwa akufuna kukusiyitsani njira imene Chauta akufuna kuti muitsate. Aphedwe, ndipo pakutero mudzachotsa choipa chimenechi pakati panu.
“Aroni saloŵa nao m'dziko limene ndidapatsa Aisraele. Adzafa, chifukwa choti nonse aŵirinu simudamvere lamulo langa ku madzi a ku Meriba kuja.
Mukamaopa Chauta ndi kumamtumikira ndi kumamvera mau ake, osakana malamulo ake, ndiponso ngati nonsenu pamodzi ndi mfumu yanu mudzatsata Chauta, Mulungu wanu, zonse zidzakuyenderani bwino.
Koma mukapanda kumvera mau a Chauta nkumakana malamulo ake, ndiye kuti Iye adzakulangani inu ndi mfumu yanu yomwe.
Chauta akuti, “Tsoka kwa ana ondipandukira Ine! Amachita zodzikonzera okha osati zokonza Ine. Amachita chipangano chaochao, chosatsata chifuniro changa, ndipo amanka nachimwirachimwira.
Koma musagalukire Chauta. Musaope anthu a m'dzikolo chifukwa tidzaŵaononga. Iwowo alibe oŵatchinjiriza, koma ife Chauta ali nafe, musaŵaope.”
Musaiŵale m'mene mudakwiyitsira Chauta, Mulungu wanu, m'chipululu muja. Kuyambira tsiku lija mudatuluka ku Ejipito kuja, mpaka tsiku limene mudafika kuno, mwakhala mukuukira Chauta, Mulungu wanu.
Asenzetseni tchimo lao, Inu Mulungu. Upo wao woipa uŵagwetse iwo omwe, muŵachotse pamaso panu chifukwa cha zochimwa zao zambirimbiri, chifukwa akuukirani Inu.
Komabe iwo adampandukira, namkwiyitsa Mulungu. Motero Chauta adasanduka mdani wao, ndipo adamenyana nawo nkhondo.
“Akamachoka, adzaona mitembo ya anthu amene adandipandukira. Mphutsi zimene zidzaŵadya sizidzafa, ndipo moto umene udzaŵatentha sudzazima. Anthu a mitundu yonse poŵaona adzanyansidwa nawo.”
Mudzalangidwa ndi machimo anu omwe: poti mwandikana, ndidzakuimbani mlandu. Muganizire bwino za kuipa kwake kwa kundisiya Ine, Chauta, Mulungu wanu. Mulingalire kuŵaŵa kwake kwa kukhala osandiwopa,” akuterotu Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse.
Asakhale ngati makolo ao, anthu oukira ndi osamvera aja, mbadwo wa anthu amene mitima yao inali yosakhazikika, amene moyo wao unali wosakhulupirika kwa Mulungu.
Pamenepo Chauta wakhoza, chifukwa ndine ndidapandukira malamulo ake. Imvani, inu anthu a mitundu yonse, onani kuvutika kwanga. Anamwali anga ndi anyamata anga atengedwa ukapolo.
Akuzinga Yerusalemu ngati alonda a munda, chifukwa choti anthu andipandukira,” akuterotu Chauta.
Machimo anu adakulekanitsani ndi Mulungu wanu, ndipo Iye wakufulatirani chifukwa cha machimo anuwo. Choncho saamva zimene inu mumanena.
A ku Samariya adzalangidwa chifukwa choti adapandukira Mulungu wao. Adzaphedwa ndi lupanga, ana ao adzaphedwa moŵakankhanthitsa pansi. Akazi ake apathupi adzang'ambidwa.”
Ndidzaŵayeretsa pochotsa machimo ao onse ondichimwira. Ndidzaŵakhululukira zoipa zonse zimene adachita pondipandukira.
Ndikudziŵa kukanika kwanu ndiponso uchigaŵenga wanu. Ngati mugalukira Chauta, ndikadali moyo, nanji ndikadzafa, ndiye mudzaposa kugaluka kwake.
Musalole kuti wina akupusitseni mwa njira iliyonse. Pajatu lisanafike tsikulo, kudzayamba kwachitika zoti anthu ochuluka akupandukira Mulungu, ndipo kudzaoneka Munthu Woipitsitsa uja, woyenera kutayikayu.
Motero munthu wokana kumvera olamulira, akukana dongosolo limene adaliika Mulungu. Ndipo ochita zimenezi, adzadzitengera okha chilango.
Ungovomera kulakwa kwako. Vomera kuti udaukira Chauta Mulungu wako, kuti udapembedza nao milungu yachilendo patsinde pa mitengo yogudira, ndiponso kuti sudamvere mau anga,’ ” akuterotu Chauta.
Kugalukira kuli ngati tchimo loombeza, kukhala wokanika kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu.”
Koma adandipandukira, adakana kundimvera. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adasiya zonyansa zake zimene ankasangalala nazo. Palibe amene adasiya mafano a ku Ejipito. Tsono ndidaganiza zoŵaonetsa ukali ndi mkwiyo wanga ku Ejipito komwe.
Takupandukirani, takukanani, Inu Chauta, ndipo takana kukutsatani. Tapanikiza anzathu, takupandukirani Inu. Maganizo athu ndi abodza, mau athu ndi onama.
Koma Aisraele adandipandukira m'chipululumo. Sadatsate malangizo anga ndipo adakana malamulo anga, amene amakhalitsa moyo anthu oŵamvera. Anthuwo adaipitsa kotheratu masiku anga a Sabata. Motero Ine ndidaganiza zoŵalanga mwaukali m'chipululu momwemo ndi kuŵaononga kotheratu.
Adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, ndikukutuma kwa Israele, mtundu wa anthu aupandu amene andipandukira. Iwowo ndi makolo ao akhala akundichimwira mpaka lero lino.
Nthaŵi zambiri Iye ankaŵapulumutsa, koma iwo ankamuukirabe osaleka, namamira m'machimo ao,
Anthu oika mtima pa khalidwe lokonda zoipa, amadana ndi Mulungu. Anthu otere sagonjera Malamulo a Mulungu, ndipo kunena zoona, sangathedi kuŵagonjera.
Nthaŵi zonse ndakhala wokonzeka kuŵalandira mwaufulu anthu ondipandukiraŵa, amene amachita zoipa namatsata njira zao chifukwa cha kuuma mitu kwao.
“Komabe iwowo sankamvera, ndipo adakuukirani. Adaŵataya kunkhongo Malamulo anu, napha aneneri anu amene ankaŵadzudzula kuti abwerere kwa Inu. Adachita zinthu zoipitsitsa zokunyozani.
Koma inu simudafune kupita, mudaukira ulamuliro wa Chauta, Mulungu wanu.
Inu munkangodandaula m'mahema mwanu nkumati, “Chauta amadana nafe. Nchifukwa chake adatitulutsa ku dziko la Ejipito, natipereka kwa Aamori kuti atiphe.
Chauta adati, “Tamvera, iwe mlengalenga, tchera khutu, iwe dziko lapansi, Ine Chauta ndikulankhula. Ndidabereka ana ndi kuŵalera, koma andigalukira.
“Ife sitidzamvera zimene watiwuza m'dzina la Chauta.
Koma tidzachitadi zonse zimene tidalumbira. Tidzaifukizira ndithu lubani mfumukazi yakumwamba ndi kuiperekera nsembe zazakumwa, monga tinkachitira ifeyo ndi makolo athu, mafumu athu ndi akalonga athu, m'mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya mu Yerusalemu. Nthaŵi imeneyo tinali ndi chakudya chambiri, ndipo tinkakhuta, osapeza zovuta.
Pakuti Mulungu sadaŵalekerere angelo amene adachimwa aja, koma adaŵaponya m'ng'anjo yamoto, m'maenje amdima momwe ali omangidwa kudikira chiweruzo.
Koma anthuwo ankapeputsabe amithengawo, namanyoza mau a Mulungu. Ndipo ankaŵaseka aneneri ake, mpaka Chauta adakwiyira anthu ake, ndipo panalibenso mankhwala ochiritsa.
Anthu anga akuwonongeka chifukwa Ine sandidziŵa. Ndidzakukanani kuti musanditumikire ngati ansembe, chifukwa choti mwakana kuphunzitsa za Ine. Mwaiŵala malamulo a Mulungu wanu, tsono Inenso Mulungu wanu ndidzaiŵala ana anu.
Chifukwa chiyani nanga anthu ameneŵa akupitirirabe kulakwa, osabwereranso? Akangamira ndithu machimo ao, akukana kubwerera.
Koma nthaŵi zonse mtsogoleri akafa, anthuwo ankayambanso kuchita zoipa, nkusanduka oipa kupambana makolo ao, namatsata milungu ina, kumaitumikira ndi kumaigwadira. Sankaleka kuchita zimene adaazoloŵera ndiponso sankaleka kukhala ouma mitu.
Pitani ku dziko lamwanaalirenji. Koma Ine sindidzapita nanu chifukwa ndinu anthu okanika, ndipo ndingathe kukuwonongani panjira.”
“Koma anthu anga sadamvere mau anga. Israele adandinyoza.
Choncho ndidaŵasiya ndi mitima yao yosamverayo, kuti atsate zimene ankafuna.
Koma anthuwo sadamvere, sadasamaleko, ndipo adapitirira kukhala osamvera ndi mitima yao yoipa. Adayang'ana zam'mbuyo osati zakutsogolo.
Koma anthuwo sankamva, anali ouma mitu monga momwe analiri makolo ao amene sadakhulupirire Chauta Mulungu wao.
Iwowo adanyoza malamulo a Chauta ndi chipangano cha Chauta chimene Iye adachita ndi makolo ao. Adanyozanso zochenjeza za Chauta. Adatsata milungu yachabechabe, ndipo iwo omwe adasanduka achabechabe. Ankatsata zitsanzo za anthu a mitundu ina okhala nawo pafupi, ngakhale Chauta anali atalamula kuti asamachite mofanana ndi mitundu imeneyo.
Chikhalire sudamve chikhalire sudadziŵe, nkale lonse makutu ako sanali otsekuka. Chifukwa ndidaadziŵa kuti ndiwe wachiwembu, ndipo kuti chiyambire cha ubwana wako adakutchula waupandu.
“Tsoka kwa iwo pakuti andisiya Ine. Aonongeke chifukwa chakuti andipandukira. Ndimafuna kuŵapulumutsa, koma amangolankhula zabodza za Ine.
“Koma ana ao nawonso adandipandukira. Sadatsate malangizo anga, sadamvere malamulo anga, amene amakhalitsa moyo anthu oŵamvera. Ndiponso adaipitsa masiku anga a Sabata. Tsono ndidaganiza zoŵalanga mokwiya ndi kuŵalipsira m'chipululu momwemo.
Abwereranso ku machimo a makolo ao amene adakana kundimvera. Akutsata milungu ina ndi kumaipembedza. A ku Israele ndi a ku Yuda aphwanya chipangano chimene ndidapangana ndi makolo ao.
Ndikudziŵa kuti ine ndikadzafa, nonse mudzaipa ndipo mudzakana zimene ndakuuzanizi. Koma pambuyo pake kutsogoloko, mudzakomana ndi masoka, chifukwa chochita zoipa pamaso pa Chauta ndi kuputa mkwiyo wake pakuchulukitsa machimo anu. Mwakwiyitsa Chauta pochita zimene Iyeyo amakana.”
Inu simudamvere kapena kutchera khutu, ngakhale kuti Chauta sadaleke kukutumirani aneneri, atumiki ake.
Aneneriwo ankati, ‘Aliyense mwa inu akaleka makhalidwe ake oipa ndi ntchito zake zoipa, ndiye kuti mudzakhala m'dziko limene Chauta adakupatsani inu ndi makolo anu mpaka muyaya.
Anthu oipaŵa akana kumvera mau anga. Atsata milungu ina, namaitumikira nkumaipembedza. Iwowo adzakhala ngati mpango wopanda ntchitowu.
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Chifukwa chakuti wandiiŵala Ine ndi kundifulatira, uyenera kulangidwa chifukwa cha zonyansa zako ndi zigololo zako.”
Apo Chauta adayankha kuti, “Nchifukwa chakuti anthu angawo sadatsate malamulo amene ndidaŵapatsa, ndipo sadamvere mau anga ndi kuŵasamala.
Koma ankangotsata zolakwa za mitima yao yokanika. Ankapembedza Abaala monga momwe makolo ao adaŵaphunzitsira.
Pamene makolo athu anali ku Ejipito, sadasamale ntchito zanu zodabwitsa. Sadakumbukire kukula kwa chikondi chanu chosasinthika, koma adaukira Mulungu Wopambanazonse ku Nyanja Yofiira kuja.
Kuyambira masiku a makolo anu mwakhala mukuphwanya malamulo anga, simudaŵatsate konse. Ngati mubwerera kwa Ine, Inenso ndidzabwerera kwa inu. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Komabe inu mumati, ‘Kodi tingathe kubwerera bwanji?’
Ine mudandikana, mukupitirirabe kundifulatira. Motero ndidakweza mkono wanga nkukukanthani. Ndidatopa nako kukhululuka.
Mumtima mwake munthu wopusa amati, “Kulibe Mulungu.” Anthu otereŵa ndi oipa, amachita zonyansa, palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino.
Adakana kumvera, ndipo sankakumbuka zodabwitsa zimene Inu mudaazichita pakati pao. Adakhala okanika, nadzisankhira mtsogoleri woti aŵatsogolere kubwerera ku Ejipito ku dziko laukapolo lija. Koma Inu ndinu Mulungu wokhululuka, wokoma mtima, wachifundo, wosakwiya msanga, wokhala ndi chikondi chachikulu chosasinthika, motero iwowo simudaŵasiye.
Paja ine ndidaakuitanani, inu nkukana kumvera, ndidaati ndikuthandizeni, koma popanda wosamalako.
Uphungu wanga simudaulabadire, kudzudzula kwanga simudakusamale.
Ndiye inenso ndidzakusekani, mukadzagwa m'mavuto, ndidzakunyodolani, mukadzazunguzika ndi mantha,
Ambuye adati, “Anthu aŵa amati amapemphera kwa Ine, koma mau ao ndi opanda tanthauzo, ndipo mitima yao ili kutali ndi Ine. Chipembedzo chao ndi kungotsata chabe malamulo ongoŵaloŵeza pamtima, malamulo ochokera kwa anthu.
Andifulatira kotheratu. Ngakhale ndidavutikira kumaŵaphunzitsa, sadamve kapena kutolapo nzeru iliyonse.
“Koma iwowo adakana kumvera, adandifulatira ndi mtima wokanika. Adatseka makutu ao kuti asamve.
Mitima yao adaiwumitsa kwambiri, kuti asamve malamulo ndi mau amene Ine Chauta Wamphamvuzonse ndidaŵaphunzitsa ndi Mzimu wanga kudzera mwa aneneri amakedzana. Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse ndidaŵakwiyira kwambiri.
Nchifukwa chake monga momwe moto umaonongera chiputu, monga momwenso udzu wouma umapsera m'malaŵi a moto, momwemonso muzu wao udzaola, ndipo maluŵa ao adzafota ndi kuuluka ngati fumbi, chifukwa adakana malamulo a Chauta Wamphamvuzonse, adanyoza mau a Woyera uja wa Israele.
Komabe ine ndidakhala ndikutuma atumiki anga aneneri kuti adzakuuzeni kuti, ‘Musamachita zoipa zimene Ine ndimadana nazo.’
Koma makolo anuwo sadamvere, sadasamaleko nkomwe. Sadaleke kuchita zoipa zao, sadasiye kuifukizira lubani milungu ina.
Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu.
Adzakhala opanda chifundo, osapepeseka, ndi osinjirira anzao. Adzakhala osadzigwira, aukali, odana ndi zabwino,
opereka anzao kwa adani ao. Adzakhala osaopa chilichonse, odzitukumula, okonda zosangalatsa m'malo mokonda Mulungu.
Komanso inu mudachimwa koposa kupambana makolo anu: aliyense mwa inu akutsata zoipa ndi mtima wake wokanika, m'malo momandimvera Ine.
Koma Aisraele sadzakumvera, chifukwa safuna kundimvera Ine. Onsewo ngaliwuma ndi a mtima wosamvera.
“Koma iwo adzayankha kuti, ‘Zimenezo nzopanda pake. Tidzachita monga m'mene tifunira, ndipo aliyense mwa ife azidzangotsata zoipa za mtima wake wokanika.’ ”
Inde ankamudziŵa Mulungu, koma m'malo mwa kumtamanda kapena kumthokoza, maganizo ao adasanduka opanda pake, ndipo m'mitima yao yopusa mudadzaza mdima.
Iwo amadziyesa anzeru, koma chikhalirecho ndi opusa.
Adaleka kulemekeza Mulungu wosafa, nkumapembedza mafano ooneka ngati munthu amene amafa, kapena ngati mbalame ndi nyama zina, kapena zokwaŵa.
Paja Malembo akuti, “Lero lino mukamva mau a Mulungu, musaumitse mitima yanu monga muja zidaachitikira poukira Mulungu.”
Amalidziŵa lamulo la Mulungu lakuti anthu ochita zotere ndi oyenera kufa, komabe iwo omwe amachita zomwezo, ndiponso amavomerezana ndi anthu ena ozichita.
“Koma pali ena amene amangochita zoŵakomera. Kwa iwo nchimodzimodzi kupereka ng'ombe yamphongo ngati nsembe kapena kupha munthu, kupha mwanawankhosa kuti aperekere nsembe kapena kupha galu, kupereka chopereka cha chakudya kapena kupereka magazi a nkhumba, kupereka lubani ku nsembe yachikumbutso kapena kupembedza fano. Anthu ameneŵa mtima wao umakondwera nazo zonyansa zao.
Ine tsono ndidzaŵagwetsera chilango ndipo ndidzaŵachititsa mantha, chifukwa nditaŵaitana, palibe amene adandiyankha, kapena kutchera khutu pamene ndinkalankhula. Adachita zoipa pamaso panga, adasankhula kuchita zimene zimandinyansa.”
Saleka kuŵauza amene amandinyoza Ine kuti, ‘Zinthu zidzakuyenderani bwino.’ Ndipo amene amaumirira kutsata zofuna za mtima wao amaŵauza kuti, ‘Simudzaona vuto ai.’ ”
Pakuti tikamachimwirachimwira mwadala, kwina tikudziŵa choona, palibenso nsembe ina iliyonse ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.
Pamenepo chotitsalira si china ai, koma kumangodikira ndi mantha chiweruzo, ndiponso moto woopsa umene udzaononga otsutsana ndi Mulungu.
ndipo iyeyo adafuulira mneneri wa Mulungu, wochokera ku Yuda uja kuti, “Imvani mau a Chauta, akuti chifukwa choti simudamvere mau a Chauta, ndipo simudatsate lamulo lake limene adakulamulani,
koma mwabwerera, ndipo mwadya ndi kumwa madzi pa malo amene Chauta adakuuzani kuti musakadye chakudya kapena kumwako madzi, mtembo wanu sadzauika m'manda a makolo anu.”
Yesuluni, anthu ake a Chauta adakulupala, koma iwowo adamuukira, adanenepa ndi kukula thupi, ndipo adakhuta zedi, kenaka adasiya Mulungu Mlengi wao, nanyoza mtetezi ndi mpulumutsi wao.
Mafumu ao akuchita upo, olamula ao akhala pamodzi kuti apangane zoipa, zoukira Chauta ndi mfumu yake yodzozedwa.
Akuti, “Tiyeni timasule maunyolo aoŵa, tichokeretu mu ulamuliro wao.”
Anthu aipitsa dziko lapansi posatsata malamulo a Mulungu, ponyoza mau ake, ndipo pophwanya chipangano chamuyaya chimene Iye adapangana nawo.
Ndidaakuchenjezani pamene zinthu zinkakuyenderani bwino. Koma inu mudati, ‘Sitidzamvera.’ Ndi m'mene mwakhala mukuchitira kuyambira muli ana aang'ono, simudamvere mau anga.
Uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndithudi, pali Ine ndemwe, sindikondwa ndikaona munthu woipa alikufa. Ndikadakonda kuti aleke kuchimwako kuti akhale ndi moyo. Inu Aisraele, muferanji? Tembenukani, lekani zoipa zimene mukuchita.
Tsono mzimu wa Mulungu udaloŵa mwa Zekariya, mwana wa wansembe Yehoyada. Iye adaimirira pakati pa anthu naŵauza kuti, “Chauta akufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mukuchimwira malamulo a Chauta? Ndithu simudzapindula kanthu?’ ”
Kodi Inu Chauta, suja mumafuna anthu onena zoona? Inu mudaŵakantha anthuwo, koma iwo sadamve kuŵaŵa. Mudaŵatswanya, koma sadafune kutembenuka mtima. Adaumitsa mitima yao ngati mwala, adakana kwamtuwagalu kulapa.”
Ndipo Mose adati, “Ndi Chauta amene adzakupatsani madzulo nyama yoti mudye, ndi m'maŵa buledi woti nkukhuta, chifukwa choti wamva madandaulo anu onse omuŵiringulira aja. Ife ndife yani? Madandaulo anu simudaŵiringulire ife ai, koma Chauta.”
Munkachita zoipa zonsezi, mudakana kundimvera nditakulankhulani kosalekeza, ndipo simudayankhe pamene ndidakuitanani.
Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa:
maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa,
mtima wokonzekera kuchita zoipa, mapazi othamangira msangamsanga ku zoipa,
mboni yonama yolankhula mabodza, ndi munthu woutsa chidani pakati pa abale.
Dzimbiri limeneli ndi zilakolako za dama lako, poti nditakutsuka sudayere. Tsono sudzayeranso mpaka mkwiyo wanga utakwaniratu pa iwe.
Anthu anga achita machimo aŵiri: andisiya Ine kasupe wa madzi opatsa moyo, adzikumbira okha zitsime, zitsime zake zong'aluka, zosatha kusunga madzi.
Kodi ndi pati ndingakumenyeninso, popeza kuti mukupandukirapandukira? Aliyense mutu wake uli ndi mabala kale, ndipo mtima wake wafookeratu.
Anthu aipiratu monga zidachitikira ku Gibea. Nchifukwa chake Mulungu sadzaiŵala kuipa kwao, ndipo adzalanga machimo ao.
“Ndidaŵakwiyira chifukwa anali okonda chuma dziŵi. Tsono ndidaŵalanga, ndi kuŵafulatira mokwiya. Koma iwowo adakhalabe ouma mitu, ndipo adapitirira kuchita ntchito zao zoipa.
“Ndine amene ndidakusendetsani milomo m'mizinda yanu yonse. Ndine amene ndidagwetsa njala konse kumene munkakhala. Komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta.
“Ndinenso amene ndidamanga mvula patangotsala miyezi itatu kuti mukolole. Ndine amene ndinkagwetsa mvula pa mudzi wina, koma pa mudzi wina ai. Mvula inkagwa pa munda wina, koma munda wina nkumakhala gwa, chifukwa chosoŵa mvula.
Motero midzi iŵiri kapena itatu inkapita ku mudzi umodzi kuti ikamwe madzi, koma osaŵakwanira. Komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta.
Ndidzakuchotserani anthu amene amandipandukira ndi kundichimwira. Ndidzaŵatulutsa m'dziko limene akukhalamolo, koma sadzapondamo m'dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
“Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Ndidzagwetsa tsoka pa mzinda uwu pamodzi ndi pa midzi yake yonse monga ndidaanenera, chifukwa choti anthu ake ndi okanika, ndipo akukana kumvera mau anga.”
Anthu anzeru adzachita manyazi, adzatha nzeru, ndipo adzagwidwa. Akana mau a Chauta, nanga nzeru zao nzotani?
Komabe simudandimvere. Mudaputa mkwiyo wanga ndi mafano amene mudapanga ndi manja anu, motero mudadziwononga nokha,” akuterotu Chauta.
Komatu mukapanda kumvera bwino mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero lino, adzakugwerani matemberero aŵa:
Musati muumitse makosi anu monga m'mene ankachitira makolo anu, koma mudzipereke kwa Chauta, ndipo muzibwera ku Nyumba yake imene Chautayo waiyeretsa mpaka muyaya. Ndipo muzitumikira Chauta, Mulungu wanu, kuti mkwiyo wake woopsa ukuchokeni.
Ndikumtuma kwa mtundu wosasamala za Mulungu, ndipo ndikumlamula kuti apite kwa anthu amene ndaŵakwiyira, kuti akafunkhe ndi kukalanda chuma chao chonse, ndi kuŵaponderezera pansi ngati matope am'miseu.”
“Nthaŵi ikubwera pamene mudzalira kwa Chauta, koma sadzakuyankhani. Nthaŵi imeneyo adzakufulatirani chifukwa ntchito zanu nzoipa.”
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Yuda akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo anyoza malamulo a Ine Chauta, ndipo sadatsate malangizo anga. Milungu yabodza imene makolo ao ankaipembedza yaŵasokeretsa.