Ndikufuna ndikuuzeni nkhani yofunika kwambiri. Munthu akamakana kumvera ndi kutsata malamulo, zimenezo zimatchedwa kupanduka. Zimaonetsa mtima wosasamala, wonyoza, komanso wopanda chifundo. Ambiri amene amachita zinthu monyadira, mwadyera, komanso osamvera akuluakulu awo, ali ndi mzimu wopanduka, womwe Mulungu sawukonda.
Ngati umati ndiwe mwana wa Atate Wathu wakumwamba, koma ukuchita zinthu zopanduka, suli paubwenzi wabwino ndi Mzimu Woyera. M'malo mwake, mizimu yoipa ndiyo ikukutsogolera. Kupanduka ndi chifukwa chachikulu chomwe anthu ambiri amathawa Mulungu. Amakana kulandira uphungu ndi kutsata malamulo ake, m'malo mwake amasankha kutsata zilakolako zawo ndi maganizo awo, akuchimwira Mulungu Wamphamvuyonse.
Wopanduka amadziona ngati wanzeru, koma sakudziwa kuti akulowera m'mavuto, kutanthauza chilango chosatha ku gehena. Buku la Deuteronomo 1:43-45 limati: "Ndinakuuzani, koma simunamvere; munapandukira lamulo la Yehova, ndipo monyadira munakwera phiri. Koma Aamori amene anakhala m’phirilo anatuluka kukakumana nanu, anakulondolani monga momwe njuchi zimachitira, ndipo anakugonjetsani ku Seiri, kufikira ku Horima. Pamenepo munabwerera ndi kulira pamaso pa Yehova, koma iye sanamvere mawu anu, kapena kukuyang’anirani.”
Kumbukirani kuti Yesu sakonda anthu opanduka. Amakukondani ndipo akufuna kukupulumutsani, koma sakonda kuti simukulapa machimo anu. Mukadali ndi nthawi yopeza chifundo cha Mulungu. Ingotsegula mtima wanu, dzichepetse pamaso pa Ambuye, pemphani chikhululukiro, ndi kuvomereza zolakwa zanu modzichepetsa. Musamadzilungamitse, ndipo landirani chilango chimene mukuyenera kuti musinthe mkati mwanu.
Yandikirani Mzimu Woyera, muuzeni kuti mukumufuna, ndipo musamakhale popanda chikondi chake changwiro. Mukatero, mudzapeza chisomo pamaso pa Mulungu ndi anthu. Pemphani chikhululukiro kwa akuluakulu anu ndi kuyambiranso moyo watsopano.
Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu.
Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.
Muchite zimenezi chifukwa mukudziŵa kuti yafika kale nthaŵi yakuti mudzuke kutulo. Pakuti chipulumutso chili pafupi tsopano kuposa pamene tidayamba kukhulupirira.
Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera.
Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje.
Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.
Motero munthu wokana kumvera olamulira, akukana dongosolo limene adaliika Mulungu. Ndipo ochita zimenezi, adzadzitengera okha chilango.
Abale, mchenjere, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woipa ndi wosakhulupirira, womlekanitsa ndi Mulungu wamoyo.
Kwenikweni muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku ikadalipo nthaŵi, imene m'mau a Mulungu imatchedwa kuti, “Lero”. Muzichita zimenezi, kuwopa kuti wina aliyense mwa inu angaumitsidwe mtima ndi chinyengo cha uchimo.
Chauta akuti, “Tsoka kwa ana ondipandukira Ine! Amachita zodzikonzera okha osati zokonza Ine. Amachita chipangano chaochao, chosatsata chifuniro changa, ndipo amanka nachimwirachimwira.
Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa,
Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai.
kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko,
dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.
Asakhale ngati makolo ao, anthu oukira ndi osamvera aja, mbadwo wa anthu amene mitima yao inali yosakhazikika, amene moyo wao unali wosakhulupirika kwa Mulungu.
Adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, ndikukutuma kwa Israele, mtundu wa anthu aupandu amene andipandukira. Iwowo ndi makolo ao akhala akundichimwira mpaka lero lino.
Anthu ake ndi okanika ndiponso achipongwe. Ndikukutuma kuti ukanene zimene Ine Ambuye Chauta ndikuŵauza.
Inu mumaŵakana anthu onse osamvera malamulo anu, zoonadi, kuchenjera kwao nkopandapake.
“Munthu wosavomerezana ndi Ine, ndiye kuti ndi wotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ndiye kuti ameneyo ndi womwaza.
Pa tchimo lao aonjezerapo upandu, akunyadira zochita zao, ndipo akuchulukitsa mau onyoza Mulungu ife tilikumva.” Mulungu amasamalira zochitika pa dziko lapansi.
Komabe ambirimbiri mwa iwo Mulungu sadakondwere nawo, kotero kuti adafera m'chipululu.
Tsono zimene zidachitikazi ndi zitsanzo zotichenjeza ife, kuti tisamasirira zoipa monga adaachitira iwowo.
Mudzalangidwa ndi machimo anu omwe: poti mwandikana, ndidzakuimbani mlandu. Muganizire bwino za kuipa kwake kwa kundisiya Ine, Chauta, Mulungu wanu. Mulingalire kuŵaŵa kwake kwa kukhala osandiwopa,” akuterotu Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse.
Chifukwa chiyani nanga anthu ameneŵa akupitirirabe kulakwa, osabwereranso? Akangamira ndithu machimo ao, akukana kubwerera.
Nchifukwa chake adaŵauza kuti akadaŵaononga, pakadapanda Mose wosankhidwa wake kuima pamaso pake, ndi kuletsa mkwiyo wake kuti usaŵaononge.
Paja Malembo akuti, “Lero lino mukamva mau a Mulungu, musaumitse mitima yanu monga muja zidaachitikira poukira Mulungu.”
Ndipo Chauta atakutumani kuchokera ku Kadesi-Baranea kuti mupite kukalandira dziko limene adakupatsanilo, inu mudakana malamulo a Chauta, Mulungu wanu, ndipo simudamkhulupirire kapena kumumvera.
Chauta adati, “Tamvera, iwe mlengalenga, tchera khutu, iwe dziko lapansi, Ine Chauta ndikulankhula. Ndidabereka ana ndi kuŵalera, koma andigalukira.
Koma mukakana ndi kumapanduka, mudzaphedwa ndi lupanga. Ine Chauta ndatero.”
Taonanitu! Mzinda umene kale udaali wokhulupirika ndi wachilungamo, tsopano ukuchita zadama. Mzinda umene kale udaali ndi anthu aungwiro, tsopano wadzaza ndi anthu opha anzao.
Iwe Yerusalemu, unali ngati siliva, koma tsopano wasanduka wopandapake. Unali ngati vinyo wabwino, koma tsopano uli ngati vinyo wosakanizika ndi madzi.
Atsogoleri ako apanduka, ndipo amagwirizana ndi mbala. Aliyense amakonda chiphuphu, ndipo amathamangira mphatso. Satchinjiriza ana amasiye, ndipo samvera madandaulo a akazi amasiye.
Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, Wamphamvu uja wa Israele, akunena kuti: “Ha! Olimbana nane ndidzaŵatha, adani anga ndidzaŵalipsira.
Ndidzatambasula dzanja langa kuti ndilimbane nawe. Ndidzasungunula machimo ako nkuŵachotsa, monga m'mene amachotsera dzimbiri ndi mankhwala.
Aweruzi ako ndidzaŵakhazikitsanso ngati pa masiku akale aja. Aphungu akonso ndidzaŵakhazikitsanso ngati poyamba paja. Pambuyo pake iweyo udzatchedwa mzinda waungwiro, mzinda wokhulupirika.”
Chauta ndi wolungama, adzaombola Ziyoni. Chauta ndi waungwiro, adzaombolanso anthu olapa amumzindamo.
Koma opanduka ndi ochimwa adzaŵaonongera pamodzi, osiya Chauta adzatheratu.
Mudzachita nayo manyazi mitengo ya thundu imene inkakusangalatsani, mudzagwetsa nkhope chifukwa cha minda imene mudaipatula.
Ng'ombe imadziŵa mwini wake, bulu amadziŵa kumene mwini wake amamdyetsera, koma Aisraele sadziŵa, anthu anga samvetsa konse.”
“Kodi inu, mukuganiza bwanji? Munthu wina anali ndi ana aamuna aŵiri. Adapita kwa woyamba, nakamuuza kuti, ‘Mwana wanga, pita ukagwire ntchito m'munda wamphesa lero.’
Iyeyo adati, ‘Toto ine.’ Koma pambuyo pake adasintha maganizo, napitadi.
Wina akakakufunsani kanthu, inu mukati, ‘Ambuye ali nawo ntchito, akangothana nawo aŵatumiza nthaŵi yomweyo.’ ”
Bambo uja adapita kwa mwana wina uja, nakamuuza mau omwe aja. Iyeyo adati, ‘Chabwino atate,’ koma sadapite.
Kodi mwa aŵiriwo, yemwe adachita zimene bambo wake ankafuna ndi uti?” Iwo adati, “Woyamba uja.” Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti okhometsa msonkho ndi akazi adama akuloŵa mu Ufumu wa Mulungu inu nkumakusiyani m'mbuyo.
“Koma iwowo adakana kumvera, adandifulatira ndi mtima wokanika. Adatseka makutu ao kuti asamve.
Chenjerani tsono kuti musakane kumvera amene akulankhula nanu. Anthu amene adakana kumvera iye uja amene adaaŵachenjeza pansi pano, sadapulumuke ku chilango ai. Nanji tsono ifeyo, tidzapulumuka bwanji ngati timufulatira wotilankhula kuchokera Kumwambaku?
Inde ankamudziŵa Mulungu, koma m'malo mwa kumtamanda kapena kumthokoza, maganizo ao adasanduka opanda pake, ndipo m'mitima yao yopusa mudadzaza mdima.
Iwo amadziyesa anzeru, koma chikhalirecho ndi opusa.
Chifukwa cha Ambuye, muzimvera akulu onse olandira ulamuliro. Ngati ndi mfumu yaikulu koposa ija, imvereni chifukwa ili ndi ulamuliro pa mafumu ena onse.
Ngati ndi nduna, zimvereni chifukwa zidachita kutumidwa ndi mfumu kuti zizilanga ochita zoipa ndi kuyamikira ochita zabwino.
Woipa mtima amangodzithaŵira popanda wina wompirikitsa, koma wochita zabwino amalimba mtima ngati mkango.
Ndipo adati, “Tsopano tiyeni timange mzinda wathu, ndipo nsanja yake italike mpaka kukafika kumwamba. Tikatero tidzatchuka ndithu, ndipo sitidzamwazikanso pa dziko lapansi.”
Tsono Chauta adatsika kudzaona mzindawo, pamodzi ndi nsanja imene anthu ankamanga.
Ndipo adati, “Tsopano anthu onseŵa ndi amodzi, ndipo akulankhula chilankhulo chimodzi. Zinthu akuchitazi ndi chiyambi chabe cha zimene adzachite. Kenaka iwoŵa adzachita chilichonse chimene afuna.
“Akamachoka, adzaona mitembo ya anthu amene adandipandukira. Mphutsi zimene zidzaŵadya sizidzafa, ndipo moto umene udzaŵatentha sudzazima. Anthu a mitundu yonse poŵaona adzanyansidwa nawo.”
Ngodala anthu ozunzidwa chifukwa cha kuchita chilungamo, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao.
“Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunyengezerani zoipa zamitundumitundu chifukwa cha Ine.
Sangalalani, kondwerani, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi m'menenso anthu ankazunzira aneneri amene analipo kale inu musanabadwe.
Tonse tidaasokera ngati nkhosa. Aliyense mwa ife ankangodziyendera. Ndipo Chauta adamsenzetsa iyeyo machimo athu.
Wolamula akakukwiyira, usachoke pa ntchito yako, pakuti kufatsa kumakonza ngakhale zolakwa zazikulu.
Nsembe imene Inu Mulungu mumailandira, ndi mtima wotswanyika. Mtima wachisoni ndi wolapa, Inu Mulungu simudzaunyoza.
Akodwe ndi kunyada kwao, chifukwa cha uchimo wa m'kamwa mwao, ndi mau a pakamwa pao. Chifukwa chakuti amatemberera ndipo amanama,
ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao.
Kusiyana kwake pakati pa ana a Mulungu ndi ana a Satana kumaoneka motere: aliyense wosachita chilungamo, ndiponso wosakonda mnzake, sali mwana wa Mulungu.
Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja, monganso tsiku lija ku Masa m'chipululu muja,
pamene makolo anu adandiputa mondiyesa ngakhale anali ataona ntchito zanga.
Mukudziŵa paja kuti mukadzipereka kuti mukhale akapolo a munthu nkumamumvera, ndiye kuti ndinu akapolo a munthu womumverayo. Tsono ngati ndinu akapolo a uchimo, mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo a Mulungu, mudzakhala olungama pamaso pake.
Koma matemberero kwa inu, mukapanda kumvera malamulo ameneŵa, nkusiya njira imene ndikukulamulani lero, kuti mutembenukire kwa milungu ina ndi kumaipembedza, milungu imene nkale lonse simudaipembedzepo.
Nthaŵi zonse ndakhala wokonzeka kuŵalandira mwaufulu anthu ondipandukiraŵa, amene amachita zoipa namatsata njira zao chifukwa cha kuuma mitu kwao.
Ndimakhala ndi nzeru za kumvetsa chifukwa cha malamulo anu. Nchifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.
Mwana wanga, uziwopa Chauta ndiponso mfumu, usagwirizane ndi anthu okonda kuŵachitira mwano.
Ameneŵa amatha kugwetsa tsoka mwadzidzidzi, ndani angadziŵe kuwopsa kwa chiwonongeko chochokera kwa aŵiriŵa?
Anthu oipa ndi osokera kuyambira ali m'mimba mwa mai ao, anthu amabodza ndi otayika kuyambira tsiku la kubadwa kwao.
Koma munthu aliyense amayesedwa ndi zinyengo pamene chilakolako cha mwiniwakeyo chimkopa ndi kumkola.
Pamenepo chilakolakocho chimachita ngati chatenga pathupi nkubala uchimo. Tsono uchimowo utakula msinkhu, umabala imfa.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Musalole kuti ine mtumiki wanu ndizichimwa dala, kulakwa koteroku ndisakutsate. Tsono ndidzakhala wangwiro wopanda mlandu wa uchimo waukulu.
Tsono mkaziyo adaona kuti mtengowo ndi wokongola, ndiponso kuti zipatso zake zingakhale zokoma kudya. Pompo adayamba kukhumbira kuti adyeko zipatsozo, adzakhale wanzeru. Motero adathyolako zipatso zina za mtengowo, naadya. Tsono zina adapatsako mwamuna wake, ndipo iyenso adadya.
Atangodya choncho, adazindikira kuti ali maliseche. Choncho adasoka masamba a mkuyu navala.
Iwo sadziŵa kanthu ndiponso alibe nzeru, amangoyenda m'chimbulimbuli. Maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Aisraele inu, aliyense mwa inu ndidzamuweruza molingana ndi ntchito zake. Lapani, tembenukani mtima, kuti machimo anu asakuwonongeni.
Pakuti tikamachimwirachimwira mwadala, kwina tikudziŵa choona, palibenso nsembe ina iliyonse ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.
Pamenepo chotitsalira si china ai, koma kumangodikira ndi mantha chiweruzo, ndiponso moto woopsa umene udzaononga otsutsana ndi Mulungu.
Chikhalire sudamve chikhalire sudadziŵe, nkale lonse makutu ako sanali otsekuka. Chifukwa ndidaadziŵa kuti ndiwe wachiwembu, ndipo kuti chiyambire cha ubwana wako adakutchula waupandu.
Simungathe kumwera m'chikho cha Ambuye nkumweranso m'chikho cha Satana. Simungathe kudyera pa tebulo la Ambuye nkudyeranso pa tebulo la Satana.
“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.
Adadzilekerera potsata zilakolako zao m'chipululu muja, adayesa Mulungu m'chipululumo.
Koma ochita zaupandu, namatsutsa zoona nkumachita zosalungama, Mulungu adzaŵakwiyira ndi kuŵazazira.
“Ndidaŵakwiyira chifukwa anali okonda chuma dziŵi. Tsono ndidaŵalanga, ndi kuŵafulatira mokwiya. Koma iwowo adakhalabe ouma mitu, ndipo adapitirira kuchita ntchito zao zoipa.
uli ndi chikhulupiriro ndiponso ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa. Ena sadamvere pamene mtima wao unkaŵatsutsa, motero chikhulupiriro chao chidaonongeka.
Inu Mulungu, anthu achipongwe andiwukira. Anthu opanda chifundo akufunafuna moyo wanga ndipo sasamala za Inu.
Koma kwa munthu woipa Mulungu amati, “Ukuvutikiranji ndi kutchula malamulo anga? Bwanji pakamwa pako pakulankhula za chipangano changa?
Iwe sufuna kulangizidwa, umaponya mau anga ku nkhongo.
Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka.
pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokutsogolera kuchita zabwino. Koma ngati ukuchita zoipa uwope, pakuti ali ndi mphamvu ndithu zokulanga. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wogwetsa mkwiyo wa Mulungu pa wochita zoipa, pomulanga.
Pajatu pamene pali kaduka ndi kudzikonda, pomweponso pali chisokonezo ndi ntchito yoipa ya mtundu uliwonse.
Zimene amachita munthu wopusa mwiniwakeyo amaziyesa zolungama, koma munthu wanzeru amamvetsera malangizo a ena.
Mdani uja adati, ‘Ndidzaŵalondola nkuŵagwira. Chuma chao ndidzachigaŵagaŵa, ndipo mtima wanga udzakhutira nacho. Ndidzasolola lupanga, ndipo ndidzaŵaononga ndi dzanja langa.’
Pa nthaŵi imeneyo ambiri adzataya chikhulupiriro chao, azidzaperekana nkumadana.
Kudzaoneka aneneri onama ambiri, amene azidzasokeza anthu ambiri.
Tsono popeza kuti zoipa zizidzachulukirachulukira, chikondi chizidzacheperachepera pakati pa anthu.
Mumtima mwake munthu wopusa amati, “Kulibe Mulungu.” Anthu otereŵa ndi oipa, amachita zonyansa, palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino.
“Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba, iwe Nthanda, mwana wa Mbandakucha? Wagwetsedwa pansi bwanji, iwe amene unkagonjetsa mitundu ya anthu?
Mumtima mwako unkati, ‘Ndidzakwera mpaka kumwamba. Ndidzakhazika mpando wanga waufumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu. Ndidzakhala pampandopo pa phiri la kumpoto kumene imasonkhanako milungu yonse.
Ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanafana naye Wopambanazonse.’
Musalole kuti wina akupusitseni mwa njira iliyonse. Pajatu lisanafike tsikulo, kudzayamba kwachitika zoti anthu ochuluka akupandukira Mulungu, ndipo kudzaoneka Munthu Woipitsitsa uja, woyenera kutayikayu.
Ameneyu ndi mdani, ndipo adzadziika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza, kotero kuti mwiniwakeyo adzadzikhazika m'Nyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.
Nanji tsono munthu wonyoza Mwana wa Mulungu, munthu woyesa chinthu chachabe magazi achipangano amene adamuyeretsa, munthu wonyoza Mzimu wotipatsa madalitso a Mulungu! Chilango cha munthu wotere chidzakhala choopsa kopambana.
Anthu oika mtima pa khalidwe lokonda zoipa, amadana ndi Mulungu. Anthu otere sagonjera Malamulo a Mulungu, ndipo kunena zoona, sangathedi kuŵagonjera.
Usachite kunyanyanso kuipa, usanyanye nawonso uchitsiru. Nanga uferenji nthaŵi yako isanakwane?
kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko,
“Koma ngati ana ake asiya lamulo langa, ndipo satsata malangizo anga,
ngati aphwanya malamulo anga, ndipo sasunga malangizo anga,
“ndidzaŵalanga ndi ndodo, chifukwa cha zolakwa zao, ndidzaŵakwapula ndi zikoti chifukwa cha machimo ao.
Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti ngati kukhulupirika kwanu sikuposa kukhulupirika kwa aphunzitsi a Malamulo ndi kwa Afarisi, simudzaloŵa konse mu Ufumu wakumwamba.
Tsono popeza kuti iwo sadalabadireko za kumvera Mulungu, Mulunguyo adaŵasiya m'maganizo ao opusa, kotero kuti amachita zosayenera.
Mitima yao idadzaza ndi zosalungama zamitundumitundu, monga kuipa, umbombo ndi dumbo. Amangolingalira za kaduka, za kupha anthu, za ndeu, za kunyenga, ndi za njiru. Amachita ugogodi,
Umasimba za Mwana wake, Yesu Ambuye athu. Poyang'anira umunthu wake, kholo lake ndi Davide,
amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao.
Ndi opusa, osakhulupirika, okhakhala moyo, ndi opanda chifundo.
Amalidziŵa lamulo la Mulungu lakuti anthu ochita zotere ndi oyenera kufa, komabe iwo omwe amachita zomwezo, ndiponso amavomerezana ndi anthu ena ozichita.
Kodi sindidana nawo anthu odana nanu, Inu Chauta? Kodi sindinyansidwa nawo anthu okuukirani?
Ndimadana nawo ndi chidani chenicheni. Ndimaŵayesa adani anga.
“ ‘Anthu aŵa amangondilemekeza ndi pakamwa chabe, koma mtima wao uli kutali ndi Ine.
Amandipembedza inde, koma kupembedza kwaoko nkopanda phindu, chifukwa zimene amaphunzitsa ngati zophunzitsa zenizeni ndi malamulo a anthu chabe.’ ”
Mulungu adapereka Malamulo kuti anthu azindikire kuchuluka kwa machimo ao. Koma pamene uchimo udachuluka, kukoma mtima kwa Mulungu kudachuluka koposa.
Chauta akuti, “Tsoka kwa ana ondipandukira Ine! Amachita zodzikonzera okha osati zokonza Ine. Amachita chipangano chaochao, chosatsata chifuniro changa, ndipo amanka nachimwirachimwira.
Amauza oona zobisika kuti, ‘Musaonenso.’ Amauza aneneri kuti, ‘Musatiloserenso zoona. Mutiwuze zotikomera, mutilosere zam'mutu chabe.
Chokani apa, osakhala pa njira. Sitifuna kumvanso za Woyera uja wa Israele.’ ”
Nchifukwa chake Woyera uja wa Israele akunena kuti, “Inu mumanyozera zimene ndimakuuzani, mumakhulupirira zopsinja anzanu ndipo mumadalira mabodza.
Nchifukwa chake tchimo lanuli lidzakhala ngati mng'ankha pa chipupa chachitali choŵinuka, chimene kugwa kwake nkwadzidzidzi.
Zidzakhala ngati kuphwanyika kwa mbiya, imene ili yotekedzekeratu, popanda ndi phale lomwe lopalira moto, kapena lotungira madzi m'chitsime.”
Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati, “Ngati mutembenuka ndi kubwerera, mudzapulumuka. Ngati mudzinga ndi kukhulupirira, mudzakhala amphamvu.” Koma inu mudakana kutero.
Mudati, “Tidzathamanga pa akavalo.” Chabwino, mudzathaŵe! Mudatinso, “Tidzakwera pa magareta aliŵiro.” Chabwino, koma okuthamangitsani adzakhalanso aliŵiro.
Anthu chikwi chimodzi mwa inu adzathaŵa poona mdani mmodzi. Asilikali asanu okha adzakwanira kukuthamangitsani. Otsalira mwa inu adzakhala ngati mtengo wa mbendera wapaphiri, ngati chizindikiro chapagomo.
Komabe Chauta akufunitsitsa kuti akukomereni mtima. Ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo, chifukwa Chauta ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!
Ndithudi, inu anthu a ku Ziyoni, okhala ku Yerusalemu, simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu, ndipo akadzangomva, pompo adzakuyankhani.
Amapita ku Ejipito kukapempha chithandizo, Ine osandifunsa. Amathaŵira kwa Farao kuti aŵatchinjirize, amakafuna malo opulumukirako ku Ejipito.
Inu anthu osakhulupirikanu, kodi simudziŵa kuti kuchita chibwenzi ndi zapansipano nkudana ndi Mulungu? Choncho munthu wofuna kukhala bwenzi la zapansipano, ameneyo amadzisandutsa mdani wa Mulungu.
Chauta amayesa anthu olungama namakondwera nawo, mtima wake umadana ndi anthu oipa okonda zachiwawa.
Kugalukira kuli ngati tchimo loombeza, kukhala wokanika kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu.”
Anthu osiyidwa, Mulungu amaŵapatsa malo okhalamo, am'ndende amaŵatulutsa kuti akhale pa ufulu, koma anthu oukira, amaŵapirikitsira ku nthaka yoguga.
Mafumu ao akuchita upo, olamula ao akhala pamodzi kuti apangane zoipa, zoukira Chauta ndi mfumu yake yodzozedwa.
“Aroni saloŵa nao m'dziko limene ndidapatsa Aisraele. Adzafa, chifukwa choti nonse aŵirinu simudamvere lamulo langa ku madzi a ku Meriba kuja.
Iye amalamula ndi mphamvu zake mpaka muyaya, maso ake amalonda mitundu ina ya anthu. Anthu oukira asadzikweze.
Mukamaopa Chauta ndi kumamtumikira ndi kumamvera mau ake, osakana malamulo ake, ndiponso ngati nonsenu pamodzi ndi mfumu yanu mudzatsata Chauta, Mulungu wanu, zonse zidzakuyenderani bwino.
Koma musagalukire Chauta. Musaope anthu a m'dzikolo chifukwa tidzaŵaononga. Iwowo alibe oŵatchinjiriza, koma ife Chauta ali nafe, musaŵaope.”
Asenzetseni tchimo lao, Inu Mulungu. Upo wao woipa uŵagwetse iwo omwe, muŵachotse pamaso panu chifukwa cha zochimwa zao zambirimbiri, chifukwa akuukirani Inu.
Koma aphedwe mneneri aliyense kapena womasulira maloto aliyense amene akuuzani kuti muukire Chauta, Mulungu wanu, amene adakutulutsani ku Ejipito ndi kukuwombolani m'dziko laukapolo. Munthu wotero ndi woipa, chifukwa akufuna kukusiyitsani njira imene Chauta akufuna kuti muitsate. Aphedwe, ndipo pakutero mudzachotsa choipa chimenechi pakati panu.
Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, ‘Chenjera, ndidzakuchotsa pa dziko lapansi. Ufa chaka chino chisanathe, chifukwa chakuti wakhala ukulalikira zopandukira Chauta.’ ”