Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

122 Mau a m'Baibulo Okhudza Chilungamo

Mwambi 17:15 umati: “Wokhululukira woipa ndi wotsutsa wolungama, onse awiri ndi onyansa kwa Ambuye.” Mulungu amadana ndi onse okhululukira ochimwa ndi otsutsa olungama ndipo amatiwonetsa kuti chilungamo chake sichikhala ndi tsankho kapena ziphuphu, koma chimafuna nthawi zonse chilungamo ndi chiweruzo choyenera, chifukwa Iye ndi wolungama m'njira zake zonse.

Mu buku la Yesaya 1:17, Mulungu akutiitana kuti tichite motsutsana ndi chisalungamo: “Phunzirani kuchita zabwino; funani chiweruzo; tsimikizirani woponderezedwa; weruzani mlandu wa mwana wamasiye; tetezani mkazi wamasiye.” Mawu awa akutilimbikitsa kukhala anthu osintha zinthu ndi kulimbana ndi chisalungamo m'njira zonse, osati m'mawu okha, komanso m'machitidwe athu. Chisalungamo ndi vuto lomwe limakhudza anthu ambiri padziko lonse lapansi, motero tiyenera kupemphera kwa Mulungu kuti atichotse ku machimo onse ndi chisalungamo.

Mu buku la Mika 6:8, tikukumbutsidwa kuti: “Iye wakudziwitsa, iwe munthu, chokoma; ndipo Yehova afunanji ndi iwe, koma kuchita chilungamo, ndi kukonda chifundo, ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?” Monga Akhristu, ndi udindo wathu kutsatira chitsanzo cha Yesu ndi kudzipereka kukhala zida za chilungamo m'dziko lomwe nthawi zambiri limasowa chilungamo.

Ndikofunika kukumbukira kuti chilungamo sichili m'manja mwathu, koma m'manja mwa Mulungu. Tiyenera kudalira ulamuliro wake ndi kufunafuna chitsogozo chake polimbana ndi chisalungamo.


2 Petro 2:9

Ndiye kuti pamene anthu osamala za Mulungu akuyesedwa, Iye amadziŵa kuŵapulumutsa kwake. Koma amadziŵanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 17:15

Woweruza munthu woipa mtima kuti ndi wosalakwa, amanyansa Chauta, nayenso wopasa mlandu munthu wosalakwa amaipira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Mika 6:8

Iyai, Chauta adakuwonetsa kale, munthu iwe, chimene chili chabwino. Zimene akufuna kuti uzichita ndi izi: uzichita zolungama, uzikhala wachifundo, ndipo uziyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 19:35

“Musamaweruza milandu molakwa, ndipo muyeso wanu woyesera utali wa zinthu, kulemera kwa zinthu kapena kuchuluka kwa zinthu, usamakhala wonyenga.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 1:17

Phunzirani kuchita zabwino. Funafunani chilungamo, opsinjidwa muŵathandize. Tetezani ana amasiye, muŵaimirire pa milandu yao akazi amasiye.”

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 21:15

Chilungamo chikachitika, nzika zabwino zimakondwera, koma zimadederetsa atambwali.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 11:1

Muyeso wonyenga umanyansa Chauta, koma muyeso wachilungamo umamkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Amosi 5:24

Koma kuweruza kwanu kwangwiro kuziyenda kosalekeza ngati madzi, kulungama kwanu kukhale ngati mtsinje wosaphwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 12:22

Pakamwa pabodza pamamnyansa Chauta. Koma anthu ochita zinthu mokhulupirika amamkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 10:1-2

Tsoka kwa amene amapanga malamulo opanda chilungamo, ndi kwa alembi amene amalemba zongovutitsa anzao.

Ine ndidakantha mafumu a anthu opembedza mafano, amene mafano ao ndi aakulu kupambana a ku Yerusalemu ndi a ku Samariya.

Ndiye ndingalephere kuwononga Yerusalemu pamodzi ndi mafano ake omwe, monga momwe ndidachitira Samariya ndi mafano ake?”

Ambuye atamaliza ntchito yao yolanga onse pa phiri la Ziyoni ndiponso ku Yerusalemu, adzalanganso mfumu ya ku Asiriya, chifukwa cha kudzitama kwake ndi kunyada kwake.

Pakuti mfumuyo ikuti, “Ndachita zimenezi ndi mphamvu zanga ndiponso ndi nzeru zanga, pakuti kumvetsa nkwanga. Ndachotsa malire a mitundu ya anthu, ndipo ndafunkha chuma chao. Ndaŵatsitsa amene anali pa mipando yaufumu.

Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu, monga momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame. Monga momwe anthu amatolera mazira osiyidwa, ndimo m'mene Ine ndidasonkhanitsira dziko lonse lapansi. Ndipo panalibe mbalame ndi imodzi yomwe yoti mapiko phephere-phephere, kapena yoti kukamwa yasa kapena yolira kuti psepsepse.”

Koma Chauta akuti: “Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Kodi sowo ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Ndiye kukhala ngati kuti mkwapulo ukuzunguza munthu, kapena ndodo yanyamula munthu!”

Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adzatumiza matenda oondetsa kwa ankhondo amphamvu a mfumu ya ku Asiriya. Ndipo mfumuyo kunyada kwake kudzapsa ndi moto wosazimika.

Mulungu, Kuŵala kwa Israele, adzakhala ngati moto. Mulungu, Woyera Uja wa Israele, adzakhala ngati malaŵi a moto. Motowo udzaŵatentha ndi kuŵapsereza ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi.

Adzaononga nkhalango yaikulu ndi nthaka yachonde. Zidzaonongeka m'kati ndi kunja kwake, ndipo zidzakhala ngati munthu wodwala amene akuwonda.

Mitengo yotsalira yam'nkhalangomo idzakhala yochepa kwambiri, yoti ndi mwana yemwe nkuiŵerenga.

Pakutero amapotoza malamulo poweruza amphaŵi mosalungama. Amaŵalanda zoŵayenerera anthu anga osauka, amafunkha za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye!

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 6:16-19

Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa:

maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa,

mtima wokonzekera kuchita zoipa, mapazi othamangira msangamsanga ku zoipa,

mboni yonama yolankhula mabodza, ndi munthu woutsa chidani pakati pa abale.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 82:3-4

Inu tetezani anthu ofooka ndi amasiye mwachilungamo. Weruzani molungama ozunzika ndi amphaŵi.

“Landitsani ofooka ndi osoŵa. Apulumutseni kwa anthu oipa.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 43:1

Inu Mulungu, onetsani kuti ine ndine wosalakwa, munditchinjirize pa mlandu wanga kwa anthu osasamala za Mulungu. Mundipulumutse kwa anthu onyenga ndi opanda chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 29:7

Munthu wokoma mtima amasamalira zoyenerera osauka, koma munthu woipa salabadako za zimenezo.

Mutu    |  Mabaibulo
Nehemiya 4:4-5

Pamenepo ndidayamba kupemphera, ndidati, “Inu Mulungu wathu, imvani m'mene akutinyozera. Mau ao otonza aŵabwerere, anthu ameneŵa alandidwe zao zonse, ndipo atengedwe ukapolo ku dziko lachilendo.

Musaŵakhululukire cholakwa chao, musafafanize tchimo lao, popeza kuti aputa ukali wanu pamaso pa amisiri omanga.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:27-29

Tsono leka zoipa, ndipo chita zabwino, motero udzakhala pa mtendere mpaka muyaya.

Chauta amakonda chilungamo, sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika. Iye adzawasunga mpaka muyaya, koma adzaononga ana a anthu oipa.

Anthu a Mulungu adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala m'menemo mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 12:5

Chifukwa choti osauka alandidwa zao ndipo osoŵa akudandaula, Chauta akunena kuti, “Ndichitapo kanthu tsopano, ndiŵapulumutsa monga momwe akufuniramo.”

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 31:8-9

Munthu wosalankhula umlankhulire ndiwe. Anthu osiyidwa uŵalankhulire pa zoŵayenerera.

Uzilankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uziteteza amphaŵi ndi osauka.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Atesalonika 1:6-7

Paja Mulungu mwa chilungamo chake, adzaŵalanga ndi masautso anthu amene amakusautsani inu.

Koma inu amene mukusauka tsopano, adzakupatsani mpumulo pamodzi ndi ife tomwe. Adzachita zimenezi, Ambuye Yesu akadzabwera kuchokera Kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 18:20

Kondwerani inu, Dziko la Kumwamba, chifukwa cha kuwonongeka kwake. Kondwerani inu, anthu a Mulungu, inu atumwi, ndi inunso aneneri. Pakuti Mulungu pakuulanga mzindawo, wautsutsa kuti ndi wolakwa pa zimene udakuchitani.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 4:14

Aleksandro, mmisiri wa zosulasula uja adandichita zoipa kwambiri. Ambuye adzamlanga molingana ndi zimene adachita.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 16:19

Asadzachite zinthu mopanda chilungamo kapena kuweruza milandu mokondera. Asadzalandire chiphuphu, chifukwa ziphuphu zimadetsa m'maso ngakhale anthu anzeru ndipo zimalakwitsa anthu olungama poweruza.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 61:8

“Ine Chauta ndimakonda chilungamo, ndimadana ndi zakuba ndi zoipa. Anthu anga ndidzaŵapatsa mphotho mokhulupirika, ndidzapangana nawo chipangano chosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 19:5

Mboni yonama sidzalephera kulangidwa, wolankhula mabodza sadzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 22:3

Chautatu akuti uziweruza molungama ndi mosakondera. Munthu amene adambera zake uzimpulumutsa kwa womsautsa. Usavutitse mlendo, mwana wamasiye kapena mkazi wamasiye. Usakhetse magazi a anthu osachimwa pa malo ano.

Mutu    |  Mabaibulo
Amosi 5:11-12

Mumapondereza anthu osauka ndi kuŵabera pa msonkho. Nchifukwa chake ngakhale mwamanga nyumba za miyala yosema, simudzakhalamo. Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa, simudzamumwa vinyo wake.

Ine ndikudziŵa kuchuluka kwa zolakwa zanu ndi kukula kwa machimo anu. Inu mumazunza anthu ochita chilungamo, mumalandira ziphuphu ndiponso mumapotoza milandu ya anthu osauka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 10:17-18

Chauta, mumamva zimene odzichepetsa amapempha. Mudzalimbitsa mitima yao, mudzaŵatchera khutu.

Potero mudzaŵateteza amasiye ndi opsinjidwa, kuti anthu amene ali a pansi pano, asadzathe kuwopsezanso.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:1-2

Usamavutika ndi anthu oipa. Usamakhumbira kukhala ngati ochita zoipa,

Kanthaŵi pang'ono ndipo munthu woipa sadzakhalaponso, ngakhale muyang'ane bwino pamalo pamene analiri, simudzampezapo.

Koma anthu ofatsa adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala pa mtendere wosaneneka.

Munthu woipa amachitira upo mnzake wabwino, namamtuzulira maso mwachidani.

Koma Chauta amamseka munthu woipayo, poti amaona kuti tsiku lake la kuwonongeka likubwera.

Anthu oipa amasolola lupanga, ndipo amakoka mauta, kuti aphe anthu ovutika ndi osoŵa, amene amayenda molungama.

Koma lupanga lao lidzalasa mitima ya eniake omwewo, ndipo mauta ao adzaŵathyokera m'manja.

Nkwabwino kukhala m'chilungamo ndi kusauka, kupambana kukhala nazo zokoma zambiri zimene munthu woipa ali nazo.

Pakuti Chauta adzathetsa mphamvu za anthu oipa, koma adzalimbikitsa anthu onse abwino.

Chauta amasamalira moyo wa anthu angwiro, ndipo choloŵa chao chidzakhalapo mpaka muyaya.

Pa nthaŵi ya mavuto sadzazunzika, pa nthaŵi yanjala, adzakhala nazo zakudya zochuluka.

pakuti mosachedwa amanyala ngati udzu, ndipo amafota ngati masamba aaŵisi.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 16:20

Mukonde osati china ai, koma chilungamo chokha basi, kuti mudzalandiredi dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani ngati choloŵa chanu, ndi kukhazikikamo.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 4:6

Pa zimenezi munthu asachimwire mbale wake kapena kumpezera. Monga tidakuuzani kale monenetsa, Ambuye adzalanga anthu onse ochita zotere.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 26:10-11

Munthu woipa mukamchitira zabwino, saphunzira zachilungamo. Amachita zoipa m'dziko lachilungamoli, ndipo amalephera kuzindikira ukulu wa Chauta.

Inu Chauta, mwasamula dzanja lanu kuti muŵalange, koma iwo sakuliwona. Anthuwo achite manyazi poona m'mene mumakondera anthu anu, ndipo moto umene mwasonkhera adani anu, uŵapsereze.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 23:6-7

“Ngati mmodzi mwa anthu ako osauka aimbidwa mlandu, umuweruze molungama ndithu.

Ulewe zabodza, zosinjirira. Usaphe munthu wosalakwa ndi wosapalamula, chifukwa Ine sindidzakhululukira wochimwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 20:16

“Usachite umboni womnamizira mnzako.”

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 28:5

Anthu oipa samvetsa kuti chilungamo nchiyani, koma amene amatsata kufuna kwa Chauta amachimvetsa kwathunthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 22:21-22

“Musazunze mlendo kapena kumkhalitsa m'phanthi, poti paja inunso munali alendo ku dziko la Ejipito.

Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye.

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 3:16-17

China chimene ndidachiwona pansi pano ndi ichi: Koyenera kukhala chiweruzo chabwino, komwekonso kumapezeka kuipa mtima. Koyenera kukhala chilungamo, komwekonso kumapezeka zoipa.

Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Mulungu adzaŵaweruza onse, abwino ndi oipa omwe, pakuti adaika nthaŵi yochitikira chinthu chilichonse ndiponso ntchito iliyonse.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 101:5

Munthu wosinjirira mnzake kuseri ndidzamcheteketsa. Wooneka wonyada ndi wodzikuza sindidzamulekerera.

Mutu    |  Mabaibulo
Amosi 2:6-7

Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Israele akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo amagulitsa anthu achilungamo ndi siliva, amagulitsa anthu osauka ndi nsapato.

Anthu osauka iwo amaŵadyera masuku pa mutu, anthu ozunzika iwo safuna kuŵayang'ana. Bambo ndi mwana amakagona ndi mdzakazi mmodzimmodzi, mwakuti amanyoza dzina langa loyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Malaki 3:5

Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsono ndidzakufikani pafupi kuti ndikuzengeni mlandu. Mosataya nthaŵi ndidzanena mau otsutsa mfiti, anthu achigololo, a umboni wonama, odyerera antchito ao, ovutitsa akazi ndi ana amasiye, ochita alendo zosalungama ndipo onse amene sandiwopa Ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 14:5

Mboni yokhulupirika siinama, koma mboni yonyenga imalankhula zabodza.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 28:21

Kuchita tsankho si kwabwino, komabe ena amaweruza mokondera chifukwa cha kachidutswa ka buledi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 9:24

Koma ngati wina afuna kunyadira, anyadire ichi chakuti amamvetsa za Ine, ndipo amandidziŵa. Amadziŵa kuti Ine ndine Chauta wokonda chifundo, chilungamo, ndi ungwiro pa dziko lapansi. Ndithudi, pazimenezi ndipo pali mtima wanga.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 29:21

Mulungu adzalanga anthu osinjirira anzao, ndiponso ophophonyetsa anthu ozengedwa mlandu. Adzalanganso amene amapereka umboni wonama, kuti anzao osalakwa asaweruzidwe molungama.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 146:7-9

Amachitira anthu opsinjidwa zolungama, amaŵapatsa chakudya anthu anjala. Chauta amamasula am'ndende.

Chauta amatsekula maso a anthu osapenya, Chauta amakweza anthu otsitsidwa. Chauta amakonda anthu ochita chilungamo.

Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 58:1-2

Kodi mumagamuladi molungama, inu akuluakulu oweruza? Kodi mumaweruzadi anthu mwachilungamo?

Munthu wangwiro adzakondwera poona kulipsirako. Adzasamba mapazi ake m'magazi a anthu oipawo.

Motero anthu adzati, “Zoona, olungama amalandiradi mphotho. Alipodi Mulungu amene amaweruza pa dziko lapansi.”

Iyai, mitima yanu imangolingalira zoipa, kuweruza kwanu kosalungama kumadzetsa chiwawa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 29:4

Mfumu imalimbitsa dziko pakuweruza molungama, koma imene imaumiriza anthu kuti aipatse ziphuphu, imaononga dziko.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 58:6-7

“Kusala koona kumene ndimafuna ndi uku: masulani maunyolo ozunzira anzanu, masulani nsinga za goli la kuweruza mokondera. Opsinjidwa muŵapatse ufulu, muthetse ukapolo uliwonse.

Anthu anjala muziŵagaŵirako chakudya chanu, osoŵa pokhala muziŵapatsako malo. Mukaona wausiŵa, mpatseni chovala, musalephere kuthandiza amene ali abale anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 24:14-15

Wantchito wolembedwa amene ali mmphaŵi ndi wosoŵa, musamamdyerera, ngakhale akhale mnansi wanu kapena mlendo wokhala mumzinda mwanu m'dziko lanulo.

Tsiku lililonse dzuŵa lisanaloŵe, muzimlipira malipiro a tsikulo. Ndalamazo akuzisoŵa iyeyo ndipo akuŵerengera zomwezo. Mukapanda kumlipira, adzakulirirani kwa Mulungu ndipo mudzatsutsidwa kuti ndinu ochimwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 1:21

Taonanitu! Mzinda umene kale udaali wokhulupirika ndi wachilungamo, tsopano ukuchita zadama. Mzinda umene kale udaali ndi anthu aungwiro, tsopano wadzaza ndi anthu opha anzao.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 22:22-23

Mmphaŵi usamubere, chifukwa choti iyeyo ndi wosauka. Anthu ozunzika usaŵapondereze pa bwalo la milandu.

Pakuti Chauta adzaŵateteza pa mlandu wao, ndipo adzaŵalanda moyo amene amalanda zinthu zao.

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 5:15-16

Koma Mulungu amateteza amphaŵi kwa adani oŵasinjirira, amapulumutsa osauka kwa anthu ofuna kuŵapanikiza.

Choncho amphaŵi amaŵalimbitsa mtima, koma anthu oipa amaŵatseka pakamwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 5:20

Tsoka kwa amene zoipa amaziyesa zabwino ndipo zabwino amaziyesa zoipa, amene mdima amauyesa kuŵala, ndipo kuŵala amakuyesa mdima, amene zoŵaŵa amaziyesa zozuna, ndipo zozuna amaziyesa zoŵaŵa!

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 14:31

Wopondereza mmphaŵi, amachita chipongwe Mlengi wake, koma wochitira chifundo osauka, amalemekeza Mlengi wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 11:42

“Muli ndi tsoka, inu Afarisi, chifukwa mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, cha timbeu tokometsera chakudya, ndiponso cha mbeu zakudimba za mtundu uliwonse. Koma simulabadako kuchita chilungamo, kapena kukonda Mulungu. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo.

Mutu    |  Mabaibulo
Amosi 8:4-6

Amosi adati, “Imvani izi, inu amene mumapondereza osoŵa, amene mufuna kuwononga anthu osauka am'dzikomu.

Inu mumadzifunsa kuti, ‘Kodi chikondwerero cha kukhala kwa mwezi chidzatha liti, kuti tigulitse dzinthu? Kodi tsiku lopumula la Sabata litha liti kuti tigulitsenso tirigu, kutinso tipeze mpata wochepetsera miyeso ndi kukweza mitengo, ndiponso kuti tichenjeretse anthu ndi masikelo onama,

kuti osauka tiŵagule ndi siliva, amphaŵi tiŵagule ndi nkhwaŵiro, kutinso tigulitse ndi mungu womwe wa tirigu?’ ”

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 23:1-3

“Usachite umboni wonama. Munthu wolakwa usamthandize pakumchitira umboni wonama.

“Muzibzala mbeu zaka zisanu ndi chimodzi m'munda mwanu, ndi kumakolola mbeuzo.

Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri mudzaipumuze mindayo. Anthu osauka a mtundu wanu ndiwo adzadye zomera m'mindamo, ndipo nyama zakuthengo zidzadya zotsala. Muzidzachita chimodzimodzi ndi minda yamphesa ndi yaolivi yomwe.

“Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri musamagwira ntchito, kuti ng'ombe zanu zipume pamodzi ndi abulu anu omwe, kutinso akapolo anu ndi alendo omwe apezenso mphamvu.

Mumvetse zonse zimene ndakuuzanizi. Musamapemphera kwa milungu ina, ndi maina ake omwe musamaŵatchula.

“Muzikhala ndi tsiku lachikondwerero katatu pa chaka, kuti mundilemekeze Ine.

Muzikhala ndi tsiku la chikondwerero cha Buledi Wosatupitsa. Monga ndidakulamulirani, muzidya Buledi Wosatupitsa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, pa nthaŵi yake, chifukwa mudatuluka ku Ejipito mwezi umenewo. Munthu asadzaonekere pamaso panga ali chimanjamanja.

Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha Masika pokolola mbeu zoyamba zochokera ku zobzala zanu. Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha kututa zokolola zonse pakutha pa chaka, pamene muika m'nkhokwe dzinthu dzanu dzonse.

Anthu aamuna onse aziwonekera pamaso pa Ine Chauta pa masiku atatu ameneŵa.

“Mukamapereka magazi a nyama ngati nsembe kwa Ine, musapereke pamodzi ndi buledi wofufumitsa, ndipo mafuta a nyama yopereka pa tsiku langa lachikondwerero asakhale mpaka m'maŵa.

“Muzibwera ndi zokolola zoyamba zabwino kwambiri za kumunda kwanu ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu. “Musamaphika kamwanakanyama mu mkaka wa make.

Ngakhale anthu ambiri akamachita choipa, usamavomerezana nawo. Ndipo usamapereka umboni wopotoza chiweruzo m'bwalo lamilandu, kuti ukondweretse anthu ambiri.

“Ndikutuma mngelo wanga patsogolo panu, kuti akutchinjirizeni pa njira ndi kukufikitsani ku malo amene ndakukonzerani.

Mumvere iyeyo, ndipo mumvetse zimene akunena. Musamchite zaupandu, chifukwa sadzakhululukira tchimo lotere. Iye akuchita zimenezi m'dzina langa.

Koma mukamvera iyeyo ndi kuchita zonse zimene ndinena, Ineyo ndidzadana ndi adani anu, ndipo onse amene atsutsana nanu ndidzalimbana nawo.

“Mngelo wanga adzapita patsogolo panu, ndipo adzakuloŵetsani m'dziko la Aamori, Ahiti, Aperizi, Akanani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzaŵaononga onsewo.

Tsono musagwadire milungu yao kapena kuipembedza. Musamachita nao zimene amachita anthu amenewo. Mukaonongeretu milungu yao, ndiponso mukaphwanye miyala yao yopembedzerapo.

Muzipembedza Chauta, Mulungu wanu, tsono ndidzakudalitsani pokupatsani chakudya ndi madzi, ndipo ndidzakuchiritsani matenda onse.

Palibe mkazi amene adzapititse padera m'dziko mwanumo, ndipo wosabala sadzaoneka. Ndidzakupatsani moyo wautali.

Anthu onse olimbana nanu ndidzaŵachititsa mantha kuti andiwope Ine. Ndidzadzetsa chisokonezo pakati pa anthu amene mukumenyana nawo. Ndipo adani anu onse ndidzaŵathamangitsa liŵiro lamtondowadooka.

Ndidzapirikitsa Ahivi, Akanani ndi Ahiti, inu musanafike, ndipo adzathaŵa monga ngati ndaŵatumira mavu.

Sindidzaŵapirikitsa chaka chimodzinchimodzi, kuti dzikolo lingadzakhale lopanda anthu ndi kukusiyirani nyama zakuthengo zokhazokha.

Munthu wosauka ukamuweruza, usaweruze mokondera.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 19:15

“Musamaweruza mopanda chilungamo. Musachite tsankho pakati pa anthu osoŵa ndi anthu otchuka, koma muziweruza mnzanu mwachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 30:18

Komabe Chauta akufunitsitsa kuti akukomereni mtima. Ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo, chifukwa Chauta ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 17:11

Munthu wopeza chuma pobera anthu ena, ali ngati nkhwali yokonkhomola mazira amene sidaikire. Masiku asanachuluke, chumacho chimamthera, potsiriza amasanduka ngati chitsilu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 4:1

Ndidaonanso kuzunza kulikonse kochitika pansi pano. Ndipo ndidaona ozunzidwa akulira misozi, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti aŵatonthoze. Panalibe oŵatonthoza chifukwa ozunzawo anali ndi mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 23:23

“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, ndi cha timbeu tokometsera chakudya, koma simusamala zazikulu zenizeni pa Malamulo a Mulungu, monga kuweruza molungama, kuchita zachifundo, ndi kukhala okhulupirika. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 20:23

Miyeso yosintha imanyansa Chauta, masikelo onyenga ndi oipanso.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 22:22-23

Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye.

Mukamaŵazunza, Ine ndidzaŵamva iwowo akamalira kwa Ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 59:14-15

Kuweruza kolungama kwalekeka, ndipo kuchita zaungwiro kwaiŵalika. Zoona sizikupezekanso m'mabwalo a milandu, ndipo chilungamo sichikutha kupezeka kumeneko.

Zoona zikusoŵa kumeneko, ndipo wina aliyense akapanda kuchita nawo zoipa, amapeza mavuto.” Chauta adaziwona zimenezi ndipo zidamunyansa kuti palibe chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:19

Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 27:19

“Atembereredwe aliyense woweruza mopotoza milandu ya alendo, ya ana amasiye, ndi ya akazi amasiye.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 3:14-15

Chauta akuŵaimba mlandu akuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake. Akuŵazenga kuti, “Ndinu amene mwaononga munda wanga wamphesa. Nyumba zanu zadzaza ndi zinthu zolanda kwa amphaŵi.

Mukuŵapsinjiranji anthu anga? Chifukwa chiyani mukuŵadyera masuku pamutu amphaŵi?” Akutero Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 18:5

Si kwabwino pa mlandu kukondera munthu woipa, kapena kupondereza munthu wosalakwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 9:7-9

Koma Chauta amakhala pa mpando wake waufumu nthaŵi zonse, adakhazika mpando wake kuti aziweruza.

Iye amaweruza dziko lapansi molungama, amagamula milandu ya anthu mosakondera.

Kwa Chauta ndiye kothaŵirako anthu opsinjidwa, ndiyenso kopulumukira pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:6

Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 5:26-29

Paja mwa anthu anga muli ena achifwamba, amene amalalira anzao monga m'mene amachitira otchera mbalame. Amatcha misampha nakola anthu.

Nyumba zao nzodzaza ndi chuma chochipeza mwachinyengo, ngati chitatanga chodzaza ndi mbalame. Nchifukwa chake adasanduka otchuka ndi olemera.

Adanenepa nkukhala a matupi osalala. Ntchito zao zoipa nzopanda malire, saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye, kuti iyende bwino, ndipo sateteza amphaŵi.

Chauta akuti, “Ndiye ndingapande kuŵalanga chifukwa cha zimenezi? Monga ndisaulipsire mtundu wochita zotere?”

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 24:24-25

Amene amauza munthu woipa kuti, “Ndiwe wosalakwa,” anthu adzamtemberera, ndipo mitundu ya anthu idzaipidwa naye.

Koma aweruzi amene amalanga anthu oipa adzapeza bwino, ndipo adzakhala ndi madalitso ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Habakuku 1:3-4

Chifukwa chiyani mukufuna kuti ndiziwona mavuto otereŵa. Chifukwa chiyani mukulekerera zoipa? Ponseponse ndikuwona chiwonongeko ndiponso nkhondo. Pali ndeu ndi kukangana kwambiri.

Ndiye kuti malamulo atha mphamvu. Chilungamo sichikugwira ntchito. Anthu oipa akupambana anthu abwino, motero chilungamo chalephereka.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 2:11

Pajatu Mulungu alibe tsankho.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 82:2

Akuti, “Mudzakhalabe mukuweruza mopanda chilungamo mpaka liti? Bwanji mukupitirizabe kumakondera anthu oipa?

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 18:7-8

Nanga Mulungu, angaleke kuŵaweruzira mlandu wao osankhidwa ake, amene amamdandaulira usana ndi usiku? Kodi adzangoŵalekerera?

Iyai, kunena zoona adzaŵaweruzira mlandu wao msanga. Komabe Mwana wa Munthu pobwera, kodi adzapezadi chikhulupiriro pansi pano?”

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 3:17

Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake?

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 22:16

Amene amapondereza osauka kuti aonjezere pa chuma chake, kapena amene amangopatsa zinthu olemera okha, adzasanduka wosauka.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 23:8

Usalandire chiphuphu poti chimadetsa m'maso anthu oweruza, ndipo motero mlandu umaipira anthu osalakwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 94:20-21

Kodi angathe kugwirizana nanu olamulira oipa, amene amapotoza malamulo anu olungama?

Amagwirizana kuti aononge anthu osalakwa, nagamula kuti opanda mlandu aphedwe.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 21:16

Ahabu atangomva kuti Naboti wafa, adanyamuka napita ku munda wamphesa wa Naboti Myezireele, nautenga kuti ukhale wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 5:8

Ukamaona anthu osauka akuzunzika m'dziko, ndiponso anthu ena akupsinja anzao ndi kuŵalanda ufulu wao mwankhanza, usadabwe nazo zimenezo. Paja woyang'anira wokulapo ali naye wina wamkulu kwambiri amene amamuyang'anira. Ndipo palinso akuluakulu enanso oyang'anira iwowo.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 17:23

Munthu woipa amalandira chiphuphu cham'seri, ndipo amapotoza chigamulo cha mlandu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 25:35-36

Paja Ine ndidaali ndi njala, inu nkundipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu nkundipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu nkundilandira kunyumba kwanu.

Ndidaali wamaliseche, inu nkundiveka. Ndinkadwala, inu nkumadzandizonda. Ndidaali m'ndende, inu nkumadzandichezetsa.’

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 22:13

“Tsoka kwa munthu womanga nyumba yake mopanda chilungamo, womanga zipinda zake monyenga, pogwiritsa ntchito anthu, koma osaŵapatsa malipiro a ntchito yao.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 12:15

Atatero adauza anthu aja kuti, “Chenjerani, ndipo mupewe khumbo lililonse lofuna zambiri. Pajatu ngakhale munthu akhale ndi chuma chochuluka chotani, chumacho sichingatchinjirize moyo wake.”

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 13:23

M'tsala la munthu wosauka mumalola chakudya chambiri, koma anthu opanda chilungamo amalanda chakudyacho.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 10:3

Kodi mudzatani pa tsiku lachilango pofika namondwe wochokera kutali? Kodi mudzathaŵira kwa yani kuti akuthandizeni? Nanga chuma chanu mudzachisiya kuti?

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 5:1-4

Mverani tsono, inu anthu achumanu. Lirani ndi kufuula chifukwa cha zovuta zimene zikudzakugwerani.

Abale, kumbukirani chitsanzo cha aneneri amene adalankhula m'dzina la Ambuye. Iwo adamva zoŵaŵa, komabe adapirira.

Anthu amene timaŵatchula odala, ndi amene anali olimbika. Mudamva za kulimbika kwa Yobe, ndipo mudaona m'mene Ambuye adamchitira potsiriza, pakuti Ambuye ngachifundo ndi okoma mtima.

Koma koposa zonse abale anga, musamalumbira. Musalumbire potchula Kumwamba, kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. Pofuna kutsimikiza kanthu, muzingoti, “Inde”. Pofuna kukana kanthu, muzingoti, “Ai”. Muzitero, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni kuti ndinu opalamula.

Kodi wina mwa inu ali m'mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu.

Kodi wina mwa inu akudwala? Aitanitse akulu a mpingo. Iwowo adzampempherere ndi kumdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye.

Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo.

Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.

Eliya anali munthu monga ife tomwe. Iye uja adaapemphera kolimba kuti mvula isagwe, ndipo mvula siidagwedi pa zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi.

Atapempheranso, mvula idagwa, nthaka nkuyambanso kumeretsa mbeu zake.

Abale anga, wina mwa inu akasokera pa kusiya choona, mnzake nkumubweza,

Chuma chanu chaola, ndipo njenjete zadya zovala zanu.

dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa.

Golide wanu ndi siliva zachita dzimbiri, ndipo dzimbirilo lidzakhala mboni yokutsutsani. Lidzaononga thupi lanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano amene ali otsiriza.

Antchito okolola m'minda mwanu simudaŵalipire. Ndalama zamalipirozo zikulira mokutsutsani. Ndipo kufuula kwa okololawo kwamveka m'makutu a Chauta Mphambe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 35:10

Ndidzasangalala ndi mtima wonse ndi kunena kuti. “Ndani angafanefane ndi Inu Chauta, Inu amene mumapulumutsa munthu wofooka kwa munthu wopambana pa mphamvu, Inu amene mumapulumutsa munthu wofooka ndi wosoŵa kwa munthu wolanda zinthu zake?”

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 22:21

“Musazunze mlendo kapena kumkhalitsa m'phanthi, poti paja inunso munali alendo ku dziko la Ejipito.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 3:23

popeza kuti onse adachimwa, nalephera kufika ku ulemerero umene Mulungu adaŵakonzera.

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 27:8-9

Nanga chiyembekezo cha munthu wopanda Mulungu nchiyani pamene aphedwa, pamene Mulungu amchotsera moyo wake?

Kodi Mulungu angamve kulira kwa munthu wotere, pamene zovuta zimgwera?

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:12

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:25

Chauta amapasula nyumba ya munthu wonyada, koma amasamalira kadziko ka mkazi wamasiye.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:28

Chauta amakonda chilungamo, sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika. Iye adzawasunga mpaka muyaya, koma adzaononga ana a anthu oipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 7:7

Ndithudi kuzunza ena kumamsandutsa munthu wanzeru kuti akhale wopusa, ndipo kulandira chiphuphu kumaononga mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 22:28

Paja anthu odzichepetsa Inu mumaŵapulumutsa, koma anthu odzikuza mumaŵatsitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 5:8-9

“Achikhala ndinali ine, ndikadatembenukira kwa Mulungu, ndikadapereka mlandu wanga kwa Iye.

Ntchito zake ndi zazikulu ndi zosamvetseka. Zodabwitsa zimene amachita ndi zosaŵerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 21:3

Kuchita zolungama ndi zokhulupirika kumakondweretsa Chauta koposa kupereka nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 33:15

Angathe kutero ndi amene amachita zolungama ndi kulankhula zoona, amene amakana phindu lolipeza monyenga, amene amakutumula manja ake kuti angagwire chiphuphu, amene amatseka makutu kuti angamve mau opangana za kupha anzao, amene amatsinzina kuti angaone zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 24:2-4

Anthu ena amasendeza malire, kuti akuze dziko lao, amalanda ziŵeto namakazidyetsa ku mabusa ao.

Ngakhale mai wake adzamuiŵala, koma mphutsi zidzasangalala pomudya. Momwemonso woipayo adzathyoka ngati mtengo.

“Zidzatero chifukwa choti adaŵachita nkhanza akazi amasiye, akazi opanda ana sadaŵachite zabwino.

Koma Mulungu amaononga anthu amphamvu. Anthuwo ngakhale atakhazikika, moyo wao ndi wosatsimikizika.

Mulungu angathe kumtchinjiriza munthu woipa ndi kumpatsa mtendere, koma amakhala akupenyetsetsa njira zake.

Woipayo amamkweza pa kanthaŵi kochepa, koma posachedwa saonekanso. Monga ena onse nayenso amafota ngati udzu, amagwa ngati ngala za tirigu akazidula.

Ndani angathe kukana kuti si momwemo? Kodi wina anganditsutse kuti mau angaŵa si oona?” Bilidadi

Amalanda abulu a ana amasiye, amalandanso ng'ombe za akazi amasiye, kuti zikhale chikole.

Amapatutsa anthu osauka m'miseu, ndipo amapirikitsa amphaŵi onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 16:8

Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono uli ndi chilungamo kupambana kukhala ndi chuma chambirimbiri ulibe chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 15:15

Ine ndidati, “Inu Chauta, mumadziŵa zonse. Mundikumbukire ndipo mundithandize. Mundilipsirire anthu ondizunza. Mundilezere mtima, musandilande moyo. Onani mavuto amene ndikupeza chifukwa cha Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 140:12

Ndimadziŵa kuti Inu Chauta mumateteza ozunzika, mumaweruza mwachilungamo anthu osoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 8:9

Zonsezi ndidaziwona pamene ndinkalingalira mumtima mwanga zonse zimene zimachitika pansi pano. Nthaŵi zonse pali ena amene amalamulira anzao mwankhanza.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 3:10-11

Pamenepo anthu aja adafunsa Yohane kuti, “Tsono ife tizichita zabwino zanji?”

Iye adati, “Amene ali ndi miinjiro iŵiri, apatseko mnzake amene alibe. Ndipo amene ali nacho chakudya, achitenso chimodzimodzi.”

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 28:27

Amene amapatsa osauka sadzasoŵa kanthu koma amene amatsinzina dala kuti asaŵapenye, adzatembereredwa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 34:12

Ndithudi, Mulungu sangachite choipa, Mphambe sangaweruze mosalungama.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 7:11

Mulungu ndiye muweruzi wolungama, amalanga anthu oipa nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 29:27

Anthu osoŵa chilungamo amanyansa anthu ochita chilungamo, monga momwe anthu abwino amanyansira anthu oipa mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 6:31

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:3

Muzikumbukira am'ndende, ngati kuti mukuzunzikira nawo limodzi m'ndendemo. Muzikumbukira ovutitsidwa, pakuti inunso muli ndi thupi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 61:1-2

Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.

Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali.

Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse.

Wandituma kukalengeza za nthaŵi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 11:4

Pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu chuma sichithandiza konse, koma chilungamo ndiye chimapulumutsa ku imfa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 9:9

Kwa Chauta ndiye kothaŵirako anthu opsinjidwa, ndiyenso kopulumukira pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 23:9

“Musazunze mlendo. Inu nomwe mukudziŵa m'mene amamvera mlendo, poti paja inunso munali alendo ku Ejipito kuja.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 32:7

Munthu wachabechabe njira zake nzoipa. Amalingalira zaupandu kuti aŵachite chiwembu anthu osauka pakuŵanamizira, ngakhale pamene osaukawo ali osalakwa konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 13:10

Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Wamkulu ndi woopsa Inu Ambuye wanga, muli ndi mphamvu, wokwera ndi wolungama m'njira zanu zonse, ndinu wolungama, maganizo anu odzala ndi nzeru alipo, ndinu nokha amene mumadziwa kulemera kwa mtima ndi kuona ngati pali njira yoipa m'moyo wanga, pamaso panu ndilipo, ndilibe kanthu kobisira pamaso panu, mumandidziwa bwino, mwaona kugona kwanga ndi kudzuka kwanga, mwandiyang'anitsitsa, ndikupemphani mundipatse mtima woyera ndi kukonzanso mzimu wolungama mkati mwanga, kuti ndizitha kuyenda m'chilungamo chanu nthawi zonse ndipo kuti njira yanga isapezeke yoipa ndi yachinyengo, ndikonzeni, ndikufuna kuti ntchito zanga zonse zizioneke chikondi chanu, ndithandizeni kukonda mnzanga ndi kusakhala wosalungama ndi wina aliyense, koma ndikufuna kuyenda m'chilungamo chanu, chikondi ndi ubwino. Ndimakulambirani Ambuye wanga, ikani mwa ine mantha chifukwa cha kukhalapo kwanu, tsogolerani mapazi anga nthawi zonse, m'dzina la Yesu, Ameni.