Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

110 Mau a M'Baibulo Okhudza Kunena Zoipa Mulungu

Nkhani ya kunyoza Mulungu yatchulidwa kambirimbiri m’Baibulo. Kuchitira mwano kapena kunyoza dzina la Mulungu si nkhani yopepuka m’Malemba. Mwachitsanzo, m’buku la Ekisodo 20:7, Mulungu anati, “Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; pakuti Yehova sadzam’leka wopanda mlandu iye amene atchula dzina lake pachabe.”

Kunyoza Mulungu kumakhudza kuyera kwake ndipo kumasonyeza kusalemekeza dzina lake. Yesu nayenso anatiphunzitsa kufunika kosamala mawu athu, poti “mawu onse achabechabe amene anthu amalankhula, adzawawerengera mlandu tsiku lachiweruzo” (Mateyu 12:36). Choncho, tiyenera kusamala kwambiri mawu athu ndikupewa mitundu yonse ya kunyoza Mulungu.

Kunyoza Mulungu n’kochititsa manyazi kwa Mulungu woyera ndipo tiyenera kupewa ngati tikufuna kukhala moyo wotsatira mfundo za m’Baibulo. Ndikukhulupirira kuti zimenezi zikukulimbikitsa kusamala mawu ako ndikufuna chisomo cha Mulungu pa chilichonse chimene umanena. Baibulo limati machimo onse adzakhululukidwa koma wonyoza Mzimu Woyera sadzakhululukidwa. Choncho usakayikire ntchito ya Mzimu Woyera chifukwa si udindo wathu kuweruza mitima ya anthu. Yesu ndiye woweruza yekha. Ndikukupempha kuti usamalire moyo wako kuti usatayike.

Tiyeni tonse tizisamala mawu athu ndikulemekeza Mulungu pa chilichonse chimene timachita kapena kunena.


Mateyu 12:31

Nchifukwa chake ndikunenetsa kuti Mulungu adzakhululukira anthu tchimo lililonse, ngakhale mau achipongwe omunyoza Iyeyo. Koma munthu wochita chipongwe Mzimu Woyera, Mulungu sadzamkhululukira.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 13:6

Tsono chidayamba kunena mau achipongwe onyoza Mulungu, dzina lake, malo ake okhalamo, ndi onse okhala Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 24:16

wonyoza dzina la Chauta ayenera kuphedwa. Mpingo wonse umponye miyala. Mlendo kapena mbadwa akangonyoza dzina la Chauta, ayenera kuphedwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 12:31-32

Nchifukwa chake ndikunenetsa kuti Mulungu adzakhululukira anthu tchimo lililonse, ngakhale mau achipongwe omunyoza Iyeyo. Koma munthu wochita chipongwe Mzimu Woyera, Mulungu sadzamkhululukira.

Chimodzimodzinso aliyense wonenera zoipa Mwana wa Munthu, Mulungu adzamkhululukira. Koma aliyense wonenera zoipa Mzimu Woyera, Mulungu sadzamkhululukira konse nthaŵi ino, ngakhalenso nthaŵi ilikudza.”

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 13:1

Pambuyo pake ndidaona chilombo chikuvuuka m'nyanja. Chinali ndi nyanga khumi ndi mitu isanu ndi iŵiri. Pa nyanga iliyonse chidaavala chisoti chaufumu, ndipo pa mutu uliwonse panali dzina lonyoza Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 17:3

Tsono mngelo uja adanditenga chamumzimu kupita nane ku chipululu. Kumeneko ndidaona mkazi atakhala pa chilombo chofiira. Pathupi ponse chilombocho chidaalembedwa maina onyozera Mulungu. Chinali ndi mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 20:7

“Usatchule pachabe dzina la Chauta, Mulungu wako, chifukwa Mulunguyo sadzamleka aliyense wotchula pachabe dzina lakelo.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 20:27

“Iwe mwana wa munthu, lankhula nawo tsono Aisraele, uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Makolo anu adandinyozanso poleka kundikhulupirira,

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 3:28-29

“Ndithu ndikunenetsa kuti anthu angathe kukhululukidwa machimo onse, ngakhalenso zonena zao zonse zomunyoza Mulunguyo.

Koma aliyense wonyoza Mzimu Woyera, sadzakhululukidwa konse. Tchimo lakelo limakhala mpaka muyaya.”

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 19:12

Musalumbire m'dzina langa monyenga ndi kumaipitsa dzina la Ine Mulungu wanu pakutero. Ine ndine Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:8

Koma tsopano musachitenso zonsezi, monga kukalipa, kukwiya, kuipa mtima, ndi mijedu. Pakamwa panu pasamatulukenso mau otukwana kapena onyansa.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 18:6

Koma pakuti iwo adaatsutsana naye ndi kumchita chipongwe, Paulo adalekana nawo pakukutumula zovala zake, naŵauza kuti, “Mwadziphetsa ndi mtima wanu. Tsono izo nzanu, ine ndilibe chifukwa. Kuyambira tsopano ndipita kwa akunja.”

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 19:37

Inu mwabwera ndi anthu aŵa kuno, ngakhale iwo sadabe za m'nyumba ya mulungu wathu wamkazi, kapena kumchita chipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 22:28

“Musanyoze Mulungu, ndipo musatemberere mtsogoleri wa anthu anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 2:24

Ndi monga Malembo anenera kuti, “Anthu akunja amanyoza Mulungu chifukwa cha inu Ayudanu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 52:5

Tsono Ine Chauta ndikunena kuti, ‘Tsopano nditani poona kuti anthu anganu adakutengani ukapolo osaperekapo kanthu? Okulamulani akufuula monyodola, ndipo angokhalira kundinyoza kosalekeza.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 2:7

Kodi si omwewo amene amalichita chipongwe dzina lolemekezekali la Khristu, limene inu mumatchulidwa?

Mutu    |  Mabaibulo
2 Petro 2:12

Koma anthu aŵa ali ngati nyama chabe, zolengedwa zopanda nzeru, zobadwira kuti zizigwidwa ndi kumaphedwa. Amanyoza mwachipongwe zinthu zosazidziŵa. Ndipo monga nyama zija, iwo omwe adzaonongedwa,

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 13:5

Chilombo chija chidaloledwa kulankhula mau onyada ndi onyoza Mulungu mwachipongwe. Ndipo chidapatsidwa mphamvu zolamulira pa miyezi 42.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 16:9

Anthu adapserera nako kutentha koopsako, ndipo adayamba kunyoza dzina la Mulungu, amene ali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi. Komabe iwo sadatembenuke mtima kuti azitamanda Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mafumu 19:6

adati, “Kauzeni mbuyanu mau a Chauta akuti, ‘Usade nawo nkhaŵa mau ondinyoza a atumiki a mfumu ya ku Asiriya.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 5:11

“Usatchule pachabe dzina la Chauta, Mulungu wako, chifukwa Chauta adzamlanga aliyense wotchula pachabe dzina lakelo.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 16:11

Adayamba kunyoza dzina la Mulungu wa Kumwamba chifukwa cha zoŵaŵa zao ndi zilonda zao. Komabe sadatembenuke mtima ndi kuleka zochita zao.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 3:28

“Ndithu ndikunenetsa kuti anthu angathe kukhululukidwa machimo onse, ngakhalenso zonena zao zonse zomunyoza Mulunguyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 23:13

Mumvetse zonse zimene ndakuuzanizi. Musamapemphera kwa milungu ina, ndi maina ake omwe musamaŵatchula.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 6:11

Tsono iwo adapangira anthu ena kuti azinena kuti, “Tidamumva akunyoza mwachipongwe Mose ndi Mulungu yemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 12:32

Chimodzimodzinso aliyense wonenera zoipa Mwana wa Munthu, Mulungu adzamkhululukira. Koma aliyense wonenera zoipa Mzimu Woyera, Mulungu sadzamkhululukira konse nthaŵi ino, ngakhalenso nthaŵi ilikudza.”

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 12:10

“Aliyense wonenera zoipa Mwana wa Munthu, Mulungu adzamkhululukira, koma wonyoza Mzimu Woyera ndi mau achipongwe, Mulungu sadzamkhululukira.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 21:10

Mupeze anthu aŵiri oipa mtima kuti adzamneneze ndi mau akuti, ‘Iwe watemberera Mulungu ndiponso mfumu.’ Tsono mumtulutsire kunja, ndipo mumponye miyala kuti afe basi.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 37:6

adati, “Kauzeni mbuyanu mau a Chauta akuti, ‘Usade nawo nkhaŵa mau ondinyoza a atumiki a mfumu ya ku Asiriya.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 3:29

Koma aliyense wonyoza Mzimu Woyera, sadzakhululukidwa konse. Tchimo lakelo limakhala mpaka muyaya.”

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 26:11

Kaŵirikaŵiri ndinkaŵalanga m'nyumba zonse zamapemphero, ndi kuyesa kuŵakakamiza kuti amnyoze Yesuyo. Ndinkaŵachitira ukali woopsa, kotero kuti ndinkaŵazunza ngakhale ku mizinda ya ku maiko achilendo.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 26:65

Apo mkulu wa ansembe uja adang'amba zovala zake nati, “Kunyoza Mulungu koopsatu kumeneku! Kodi pamenepa nkufunanso mboni zina ngati? Mwadzimvera nokha kunyoza Mulungu koopsaku.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 1:13

ngakhale kuti kale ndinkamuchita chipongwe, kumzunza ndi kumnyoza. Koma Mulungu adandichitira chifundo chifukwa ndinkazichita mosadziŵa, poti ndinali wopanda chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 74:18

Kumbukirani, Inu Chauta, kuti adani amakunyodolani, kuti anthu achipongwe amanyoza dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:20

Anthuwo amakunenani zinthu zoipa, namakuukirani ndi mtima woipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 3:8

Apo bwanji sitingonena kuti, “Tizichita zoipa kuti zabwino ziwoneke”? Alipo anthu ena amene amatisinjirira kuti timanena zotere. Iwoŵa adzalangidwa monga kuyenera.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 6:1

Onse amene ali mu ukapolo aziwona ambuye ao ngati oyenera kuŵachitira ulemu ndithu, kuti anthu anganyoze dzina la Mulungu ndiponso zimene timaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 3:2

Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 21:6

Akhale oyera pamaso pa Ine Mulungu, ndipo asachititse manyazi dzina langa. Amapereka nsembe zotentha pa moto, chakudya cha Mulungu wao, nchifukwa chake azikhala oyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 74:10

Inu Mulungu, adani athuŵa adzanyodolabe mpaka liti? Amaliwongowo adzanyozabe dzina lanu mpaka muyaya?

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 9:3

Apo aphunzitsi ena a Malamulo adayamba kudzifunsa mumtima mwao kuti, “Munthu ameneyu akuchita chipongwe Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 13:45

Pamene Ayuda aja adaona anthu ambiriwo, adachita nsanje kwambiri. Adayamba kutsutsa zimene Paulo ankanena, ndipo adamchita chipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 74:23

Musalekerere chiwawa cha amaliwongo anu, phokoso la adani anu limene likungokulirakulira nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 65:7

Ndidzaŵalanganso chifukwa cha machimo a makolo ao. Iwowo afukiza lubani pa mapiri a mafano achikunja, ndipo andinyoza Ine pa zitunda zao. Nchifukwa chake ndidzaŵalanga potsata zimene achita.”

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 1:20

Mwa iwowo wina ndi Himeneo, wina Aleksandro, anthu amene ndaŵapereka kwa Satana kuti aphunzire kusanyoza Mulungu mwachipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 27:39

Anthu amene ankadutsa pamenepo, ankamunyodola nkumapukusa mitu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 10:3

Paja munthu woipa amanyadira zokhumba za mtima wake, wokonda chuma amanyoza ndi kukana Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 73:9

Pakamwa pao pamalankhula monyoza Mulungu kumwamba, ndipo lilime lao ndi losamangika pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Petro 2:10

Makamaka adzalanga anthu amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi namanyoza ulamuliro. Aphunzitsi onyenga ndi odzikuza, osasamala munthu, saopa kuchita chipongwe aulemerero a Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 21:13

Anthu aŵiri aja adaloŵa nakhala pamaso pa Nabotiyo. Adayamba akuchita umboni pakhamu pa anthu onse kuti, “Nabotiyu adatemberera Mulungu ndiponso mfumu.” Motero anthuwo adamtulutsira kunja kwa mzinda, namponya miyala mpaka kumupha.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 15:19

Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za kuphana, za chigololo, za chiwerewere, za kuba, maumboni onama, ndiponso zachipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 43:27-28

Atate anu oyamba adachimwa, atsogoleri anu aja adandilakwira.

Mafumu anu adaipitsa malo anga opatulika. Nchifukwa chake ndidalola kuti banja la Yakobe liwonongedwe, ndidalola kuti Aisraele anyozedwe.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 44:16

pakumva mau a anthu onditonza ndi onditukwana, poona mdani wanga ndi munthu wolipsira.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 35:12

Mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndidamva mau anu onse onyoza mapiri a ku Israele. Mudanena kuti, ‘Mapiri a ku Israele asiyidwa, ndipo atipatsa kuti tiŵaononge.’

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 107:11

pakuti adaatsutsa mau a Mulungu, adaakana monyoza malangizo a Wopambanazonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 13:5-6

Chilombo chija chidaloledwa kulankhula mau onyada ndi onyoza Mulungu mwachipongwe. Ndipo chidapatsidwa mphamvu zolamulira pa miyezi 42.

Tsono chidayamba kunena mau achipongwe onyoza Mulungu, dzina lake, malo ake okhalamo, ndi onse okhala Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo
Yuda 1:15

kuti adzaweruze anthu onse. Adzagamula kuti ngolakwa onse osasamala za Mulungu, chifukwa cha ntchito zao zonse zosalungama, zimene adachita mosaopa Mulungu. Adzaŵatsutsa chifukwa cha mau onse achipongwe amene iwo, anthu ochimwa ndi onyozera za Mulungu, adanyoza nawo Ambuye.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 23:16

Chauta Wamphamvuzonse akuuza anthu kuti, “Musamvere zimene akunena aneneri, iwowo amakuloserani zonyenga. Zimene amakuuzani kuti akuziwona m'masomphenya ndi maganizo ao chabe, si zolankhula Chauta ai.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 36:20

Kodi ndi iti mwa milungu ya maikoŵa imene idapulumutsapo maiko ake kwa mfumu yathu, kuti inu muziti Chauta nkupulumutsa Yerusalemu kwa mfumu yathuyo?’ ”

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 1:30

amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 5:11

“Pali Ine ndemwe Mulungu wamoyo, ndidzakuwonongani mopanda chifundo, chifukwa choti mwaipitsa Nyumba yanga ndi mafano anu oipa ndi miyambo yanu yonyansa. Tsono Ine sindidzakulekererani, sindidzakuchitirani chisoni mpang'ono pomwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 18:21

Usatenge mwana wako aliyense kuti umpereke ngati nsembe yamoto kwa Moleki, kuti ungaipitse dzina la Mulungu wako. Ine ndine Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Numeri 15:30

Koma munthu amene achimwa dala, ngakhale akhale mbadwa kapena mlendo, wanyoza Chauta, ndipo munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mafumu 19:22

“Kodi iwe wanyoza ndi kulalatira yani? Kodi ndani amene wamufuulira ndi kumuyang'ana monyada? Si wina ai, koma Woyera uja wa Israele!

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 15:13

Chifukwa chiyani ukufuna kulimbana ndi Mulungu? Chifukwa chiyani ukumnyoza ndi pakamwa pako?

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 26:74-75

Apo Petro adayamba kulumbira nkumanena kuti, “Mulungu andilange, munthu mukunenayu ine sindimdziŵa konse.” Nthaŵi yomweyo tambala adalira.

Tsono Petro adakumbukira mau aja a Yesu akuti, “Tambala asanalire, ukhala utakana katatu kuti sundidziŵa.” Pomwepo adatuluka, nakalira misozi ndi chisoni chachikulu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 57:4

Kodi inu mukuseŵera ndi yani? Kodi mukunena yani? Mukunyoza yani? Kodi ochimwa sindinu? Onyenga sindinu?

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 12:14

Komabe, popeza kuti pochita zimenezi mwanyoza Chauta kotheratu, mwana amene akubalireniyo adzafa.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:34-37

Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muleke nkulumbira komwe. Usalumbire kuti, ‘Kumwambadi!’ Paja Kumwamba kuli mpando waufumu wa Mulungu.

Usalumbire kuti, ‘Pali dziko lapansi!’ Paja dziko lapansi ndi chopondapo mapazi ake. Usalumbire kuti, ‘Pali Yerusalemu!’ Paja Yerusalemu ndi mzinda wa Mfumu yaikulu.

Usalumbire ngakhale pa mutu wako, pakuti sungathe kusandulitsa ndi tsitsi limodzi lomwe kuti likhale loyera kapena lakuda.

Muzingoti, ‘Inde,’ kapena ‘Ai.’ Zimene muwonjezerepo nzochokera kwa Satana, Woipa uja.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 36:20

Atafika pakati pa anthu a mitundu inayo, kulikonse kumene ankapita, adaipitsa dzina langa loyera. Zidatero chifukwa anthu ponena za iwowo ankati, ‘Aŵa ndi anthu a Chauta, koma onani adachotsedwa ku dziko lake.’

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 7:30

Chauta akuti, “Anthu a ku Yuda achita zoipa Ine ndikuwona. Aimika mafano ao onyansa m'Nyumba ino imene imadziŵika ndi dzina langa, ndipo aiipitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 7:22

zigololo, masiriro, kuipa mtima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza, ndiponso kupusa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 89:51-52

Kumbukirani kuti amene akundinyozawo ndi adani anu, Inu Chauta, iwo akunyoza Wodzozedwa wanu paliponse pamene waponda.

Chauta atamandike mpaka muyaya. Inde momwemo. Inde momwemo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 65:3

Amandikwiyitsa mopanda manyazi. Amapereka nsembe zachikunja m'minda, ndipo amafukiza lubani pa maguwa anjerwa achikunja.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Atesalonika 2:4

Ameneyu ndi mdani, ndipo adzadziika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza, kotero kuti mwiniwakeyo adzadzikhazika m'Nyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 50:16-17

Koma kwa munthu woipa Mulungu amati, “Ukuvutikiranji ndi kutchula malamulo anga? Bwanji pakamwa pako pakulankhula za chipangano changa?

Iwe sufuna kulangizidwa, umaponya mau anga ku nkhongo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 23:11

“Zoonadi, aneneri ndiponso ansembe, onsewo saopa Mulungu. Ndaŵapeza akuchita zoipa ngakhale m'Nyumba mwanga,” akutero Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 5:24

Nchifukwa chake monga momwe moto umaonongera chiputu, monga momwenso udzu wouma umapsera m'malaŵi a moto, momwemonso muzu wao udzaola, ndipo maluŵa ao adzafota ndi kuuluka ngati fumbi, chifukwa adakana malamulo a Chauta Wamphamvuzonse, adanyoza mau a Woyera uja wa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 10:33

Anthu aja adamuyankha kuti, “Sitikufuna kukuponya miyala chifukwa cha ntchito yabwino ai, koma chifukwa ukunyoza Mulungu. Iwe, amene uli munthu chabe, ukudziyesa Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 32:17

Kenaka Senakeribu adalemba makalata achipongwe oputa Chauta, Mulungu wa Aisraele, adati, “Monga milungu ya mitundu ina ya anthu a m'maiko ena sidathe kuŵapulumutsa anthu ao m'manja mwanga, momwemonso Mulungu wa Hezekiya sadzatha kupulumutsa anthu ake m'manja mwanga.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 10:15

Koma Chauta akuti: “Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Kodi sowo ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Ndiye kukhala ngati kuti mkwapulo ukuzunguza munthu, kapena ndodo yanyamula munthu!”

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 66:3

“Koma pali ena amene amangochita zoŵakomera. Kwa iwo nchimodzimodzi kupereka ng'ombe yamphongo ngati nsembe kapena kupha munthu, kupha mwanawankhosa kuti aperekere nsembe kapena kupha galu, kupereka chopereka cha chakudya kapena kupereka magazi a nkhumba, kupereka lubani ku nsembe yachikumbutso kapena kupembedza fano. Anthu ameneŵa mtima wao umakondwera nazo zonyansa zao.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 31:18

Onse onyada ndi onama olankhula mwamwano ndi monyoza kwa anthu abwino, muŵakhalitse chete.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 8:12

Kodi akamachita zonyansa, amachita manyazi ngati? Iyai, sankachita manyazi mpang'ono pomwe. Sadziŵa nkugwetsa nkhope komwe. Nchifukwa chake adzagwera pakati pa anzao amene adagwa kale. Adzagweratu pa tsiku limene ndidzaŵalanga,” akutero Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 2:23-24

Iwe wonyadira Malamulo a Mulungu, bwanji umachititsa Mulungu manyazi pakuphwanya Malamulowo?

Ndi monga Malembo anenera kuti, “Anthu akunja amanyoza Mulungu chifukwa cha inu Ayudanu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 57:6

Mumatenga miyala yosalala kumadamboko, ndi kumaipembedza ngati milungu. Mumapereka chopereka cha chakumwa kwa iyo, ndi kuperekanso chopereka cha chakudya. Kodi zimenezi zingandikondweretse?

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 2:9

Akuti: Ndikudziŵa masautso anu ndiponso umphaŵi wanu, koma kwenikweni ndinu olemera. Ndikudziŵanso zomwe amakusinjirirani anthu amene amanama kuti ndi Ayuda, pamene sali Ayuda konse, koma ndi a mpingo wa Satana.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 4:14

Anthu akakuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, chifukwa ndiye kuti Mzimu wa ulemerero, Mzimu wa Mulungu, wakhazikika pa inu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 3:5

Adzasamala maonekedwe ake okha a chipembedzo, nkumakana mphamvu zake. Anthu otere uziŵalewa.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 7:51

Stefano adapitirira nati, “Ha, anthu okanika inu, mitima yanu njachikunja, makutu anu ngogontha. Nthaŵi zonse, monga ankachitira makolo anu, inunso mumakana kumvera Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 18:20-22

Koma mneneri wina aliyense woyerekeza kulankhula m'dzina langa, Ine osamulamula kuti atero, aphedwe. Ndipo ayeneranso kuphedwa mneneri wina aliyense wolankhula m'dzina la milungu ina.”

Mwina mwake munganene kuti, “Kodi munthu angadziŵe bwanji kuti mau a mneneri wakutiwakuti sakuchokera kwa Chauta?”

Munthu akati akulankhula m'dzina la Chauta, ndipo ngati zolankhula zakezo sizichitika, pomwepo dziŵani kuti si mau a Chauta amenewo. Mneneri ameneyo wongolankhula zakezake modzikhulupirira, musamuwope ai.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 23:36

Koma musanenanso kuti ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Chauta.’ Uthenga wa aliyense ndi mau a iye mwini, motero inuyo mudapotoza mau a Mulungu wamoyo, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wathu.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 9:4

Adagwa pansi namva mau akuti, “Saulo, Saulo, ukundizunziranji Ine?”

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 41:29

Ndithudi, milungu yonseyi njachabe, zochita zake si kanthu konse. Mafano ake osungunula ali ngati mphepo yachabechabe.”

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 6:10

mbala, aumbombo, zidakwa, augogodi, kapena achifwamba, ameneŵa sadzaulaŵa Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:53

Ndimapsa mtima kwambiri chifukwa cha anthu oipa amene amaphwanya malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 8:12-13

Tsono Chauta adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuwona zimene akulu a Israele akuchita mumdima muno? Aliyense akupembedza fano lakelake m'nyumbamu. Akunena kuti, ‘Chauta sakutiwona! Chauta walisiya dziko!’ ”

Chauta adandiwuzanso kuti, “Udzaŵaonanso akuchita zonyansa zina zazikulu kupambana zimenezi.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 14:14-15

Koma Chauta adandiyankha kuti, “Zakuti aneneriwo amalosa m'dzina langa, ili ndi bodza. Ine sindidaŵasankhe, sindidaŵatume kapena kulankhula nawo. Iwo amakuloserani zinthu zonama zimene akuti adaziwona m'masomphenya. Amaombeza zabodza, zimene amalankhula ndi zonyenga zopeka iwo eni ake.

Nchifukwa chake Ine Chauta ndikunena kuti aneneri ameneŵa akulosa m'dzina langa pamene sindidaŵatume. Amakuuzani kuti simudzafa pa nkhondo kapena ndi njala m'dziko lino. Koma aneneriwo ndiwo amene adzaphedwe pa nkhondo kapena kufa ndi njala.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 44:15

Tsiku lonse ndimangodziwona kuti ndine munthu wopandapake. Nkhope yanga yagwa chifukwa cha manyazi,

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:139-140

Changu changa chikuyaka ngati moto mumtima mwanga, chifukwa adani anga amaiŵala mau anu.

Kuyenda m'njira ya malamulo anu kumandikondwetsa, kupambana kukhala ndi chuma chilichonse.

Malonjezo anu ndi otsimikizika, ndipo ine mtumiki wanu ndimaŵakonda.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 13:6-9

Aneneriwo amalankhula zonama, ndipo amalosa zabodza. Amanena kuti, ‘Akuterotu Chauta,’ pamene Chauta sadaŵatume konse. Komabe amayembekeza kuti zimene anenazo zidzachitika.

Koma Ine ndikuti, Zimene inu aneneri mukuti mudaziwona m'masomphenya nzabodza. Ndipo kulosa kwanuko nkwabodza. Mumanena kuti ‘Akuterotu Chauta,’ ngakhale Ine sindidalankhule konse.”

“Tsono zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndikukutsutsani chifukwa choti mau anu ngachabe, ndipo zimene mukuti mudaziwona ngati kutulo nzabodza.

Ndidzakantha aneneri onama amene amati adaona zakutizakuti ngati kutulo, amenenso kulosa kwao nkwabodza. Sadzakhala nao m'bwalo la aphungu la anthu anga. Sadzalembedwa m'kaundula wa nzika za Israele, ndipo sadzaloŵa m'dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 12:34

Ana a njoka inu, mungathe bwanji kulankhula zabwino pamene muli oipa? Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 8:49

Yesu adati, “Ine sindidagwidwe ndi mizimu yoipa. Ndimalemekeza Atate anga, koma inu mumandipeputsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:14

Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:21-23

“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.

Pa tsiku lachiweruzo anthu ambiri azidzanena kuti, ‘Ambuye, Ambuye, kodi suja ife tinkalalika mau a Mulungu m'dzina lanu? Suja tinkatulutsa mizimu yonyansa potchula dzina lanu? Suja tinkachita ntchito zamphamvu zambiri m'dzina lanu?’

Apo Ine ndidzaŵauza poyera kuti, ‘Sindidaakudziŵani konse. Chokani apa, anthu ochita zoipa.’

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 34:14

Musadzapembedze mulungu wina aliyense, chifukwa Chauta amene dzina lake ndi Kansanje, ndi Mulungu wansanjedi.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Chauta wamphamvuyonse ndi waulemerero, ulemerero ndi ulemu zikhale kwa Inu, ndinu woyenera kulandira kutamandidwa konse, muzunguliridwa ndi ukulu ndi mphamvu, mumakhala kwamuyaya, ndinu woyera ndi wolamulira, ndinu wangwiro ndi wodabwitsa Atate wanga wokondedwa, zikomo chifukwa cha kukoma mtima kwanu kwa ine, zikomo chifukwa chondizungulira ndi chisomo chanu ndi chifundo chanu, ndikukuyamikirani chifukwa chondipatsa moyo, ndikukuyamikirani chifukwa chondiphunzitsa kudzera m'mawu anu amtengo wapatali, mmenemo ndimapeza chitsogozo choyendera molungama pamaso panu, zikomo chifukwa chondichenjeza, kundilanga ndi kundionetsa choonadi chanu. Mawu anu ndi nyali ya mapazi anga ndi kuunika kwa njira yanga, tsiku lililonse ndikufuna kusunga malamulo ndi malangizo anu, ndipatseni chilakolako cha kukhala pamaso panu kuti nthawi zonse ndikhale ndi mtima woyera pamaso panu, Yesu ndikukuyamikirani chifukwa cha Mzimu Woyera, nthawi zonse ndimalandira chitonthozo ndi chikondi chake, sindingathe kunena zoipa za iye, ndaona mphamvu yake m'moyo wanga, ndikupemphani kuti mukhululukire onse amene akukayikira chifuniro chanu, ndipo maso a kuzindikira kwawo atsegulidwe kuti miyoyo yawo ipulumutsidwe ku gehena, ndikhululukireni Ambuye chifukwa cha amene akunena zoipa za mawu anu ndi kunena chilichonse kuti awononge thupi la Khristu, chonde tikhululukireni chifukwa cha kuipa konseku ndi kutipatsa ufulu ndi chipulumutso kwa anthu anu, m'dzina la Yesu, Ameni.