Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

128 Mau a m'Baibulo Oletsa Kuipitsa

Ndikufuna ndikuuzeni kuti Mulungu amafuna kuti tonse timupatse miyoyo yathu. Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti si chimene chimalowa mkamwa chimene chimadetsa munthu, koma chimene chimatuluka mumtima mwake.

Masiku ano, tikudziwa bwino kuti dziko lapansi laipa kwambiri, kuipa ndi chiwerewere zikuchulukirachulukira. Pachifukwa ichi, tiyenera kusamala kuti tisachite zinthu zomwe sizikondweretsa Ambuye wathu.

Muyenera kudziwa kuti mtima wa munthu ungadetsedwe ndi zinthu zosiyanasiyana zomwe zimakhudza makhalidwe athu, malingaliro athu ndi momwe timamvera. Zinthu monga nsanje, mkwiyo, maganizo oipa, kudzikuza, dyera, umbombo, bodza, ndi zina zambiri, zingawononge mitima yathu mosavuta ndikutipatutsa kutali ndi Mulungu wathu.

Kumbukirani kuti kudetsedwa kwa mtima kungawonekere m'njira zosiyanasiyana, monga kusakhululukira anthu otilakwira, kufuna chuma ndi mphamvu, kusasamala anthu ovutika, kufuna kubwezera, kusamvera mawu a Mulungu, komanso ulesi wotsatira chifuniro chake.

Lero, ndikukupemphani mwachikondi kuti musankhe kukhala moyo woyera wokondweretsa Mulungu. Pitani kwa Mulungu ndipo tulutsani chilichonse chomwe chikukudetsani ndikukupangitsani kukhala kutali ndi iye. Ngakhale machimo anu atakhala ofiira ngati nsalu yofiira, magazi a Yesu adzawachapa oyera ngati ubweya. Dzukani, yendani m'chiyero kuti moyo wanu upulumuke.


Machitidwe a Atumwi 15:20

Koma tiŵalembere kalata kuŵauza kuti asamadye zimene zili zosayera chifukwa zidaperekedwa kwa mafano. Alewe dama, ndipo asamadye nyama zochita kupotola, alewenso magazi.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 7:1

Tsono, inu okondedwa, popeza kuti tili ndi malonjezo ameneŵa, tiyeni tidzichotsere zinthu zonse zodetsa thupi lathu kapena mtima wathu. Ndipo pakuwopa Mulungu tiziyesetsa ndithu kukhala oyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 1:16

Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.”

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 20:3

Munthu ameneyo ndidzamfulatira, ndipo ndidzamchotsa pakati pa anthu anzake, chifukwa wapereka ana ake kwa Moleki ndi kuipitsa malo anga oyera, ndiponso waipitsa dzina langa loyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 20:7

Ndidaŵauza onse kuti aliyense ataye zonyansa zonse zimene ankasangalala nazo, ndipo asadziipitse ndi mafano a ku Ejipito. Ine ndine Chauta Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:2

Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 20:18

“Ndidalamula ana ao m'chipululu kuti asatsate malangizo a makolo ao, asamvere malamulo ao, kapena kudziipitsa ndi mafano ao.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 6:17

Nchifukwa chake Ambuye akuti, “Tulukani pakati pao, ndi kudzipatula. Musakhudze kanthu kosayera, ndipo ndidzakulandirani.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 4:4

Inu anthu osakhulupirikanu, kodi simudziŵa kuti kuchita chibwenzi ndi zapansipano nkudana ndi Mulungu? Choncho munthu wofuna kukhala bwenzi la zapansipano, ameneyo amadzisandutsa mdani wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:21

Nchifukwa chake siyani chizoloŵezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muŵalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m'mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:19-21

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa,

Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai.

kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko,

dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 7:20-23

Adatinso, “Zimene zimatuluka mwa munthu, ndizo zimamuipitsa.

Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za chiwerewere, za kuba, za kuphana,

zigololo, masiriro, kuipa mtima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza, ndiponso kupusa.

Zoipa zonsezi zimachokera m'kati mwa munthu, ndipo ndizo zimamuipitsa.”

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 6:19-20

Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso.

Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe?

Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 5:22

ndipo mupewe choipa cha mtundu uliwonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:8

Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 1:9

Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 2:15-17

Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye.

Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi.

Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 4:8

Yandikirani kwa Mulungu, ndipo Iye adzayandikira kwa inu. Muzisamba m'manja, inu anthu ochimwa. Chotsani maganizo onyenga m'mitima mwanu, inu anthu okayikakayika.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 5:11

Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muŵatsutse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 1:16

Sambani, dziyeretseni, chotsani pamaso panga ntchito zanu zoipa. Inde, lekani kuchita zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Tito 2:14

Paja Iye adadzipereka chifukwa cha ife, kuti atipulumutse ku zoipa zathu zonse, ndi kutiyeretsa kuti tikhale anthu ake achangu pa ntchito zonse zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 4:23

Mtima wako uziwulonda bwino, pakuti m'menemo ndimo muli magwero a moyo.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 2:22

Uthaŵe zilakolako zoipa zachinyamata. Pamodzi ndi anthu onse otama Ambuye mopemba ndi mtima woyera, uzifunafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:8

Ngodala anthu oyera mtima, pakuti adzaona Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 22:16

Nanga tsono ukuchedweranji? Dzuka ndi kutama dzina lake mopemba, ubatizidwe ndi kusambitsidwa kuti machimo ako achoke.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 1:18

Chauta akunena kuti, “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu: chifukwa cha machimo anu mwafiira kwambiri, koma Ine ndidzakutsukani, inu nkukhala oyera kuti mbee. Mwachita kuti psuu ngati magazi, koma mudzakhala oyera ngati thonje.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 13:14

Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Petro 2:20

Chifukwatu ngati anthu apulumuka ku zodetsa za dziko lino lapansi, pakudziŵa Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu, pambuyo pake nkugwidwanso ndi kugonjetsedwa ndi zoipa zomwezo, potsiriza adzakhala oipa koposa m'mene analiri poyamba.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 24:3-4

Ndani angayenere kukwera phiri la Chauta? Ndani angaime m'malo ake oyera?

Ndi amene amachita zabwino ndi manja ake, ndipo amaganiza zabwino mumtima mwake. Ndi amene salingalira zonama, ndipo salumbira monyenga.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 5:11

Koma ndidaakulemberani kuti musamayanjane ndi munthu amene amati ndi mkhristu, pamene chikhalirecho ndi munthu wadama, kapena waumbombo, wopembedza mafano, waugogodi, chidakwa, kapena wachifwamba. Munthu wotere musamadye naye nkomwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 18:20

Usagone ndi mkazi wa mnzako ndi kudziipitsa naye.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 18:25

Dziko lidaipa kotero kuti ndidalanga tchimo lake, ndipo dzikolo lidasanza anthu ake okhalamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 18:27

Pajatu anthu am'dzikomo amene adaalipo inu musanafike, ankachita zonyansa zonsezi, kotero kuti dziko lidaipitsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:9

Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 19:29

“Musaipitse mwana wanu wamkazi pakumsandutsa mkazi wachiwerewere kuti dziko lingasanduke la anthu adama ndi loipa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 19:31

“Musamapita kwa anthu olankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena kwa anyanga. Musaŵafunefune kuti angakuipitseni. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 10:13

Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 106:38

Adakhetsa magazi osachimwa, magazi a ana ao aamuna ndi aakazi, amene adaŵapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani, choncho dzikolo adaliipitsa ndi imfa zimenezo.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:5

Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 59:3

Manja anu ali psuu ndi magazi a anthu amene mudapha. Mudadziipitsa ndi machimo anu ambiri. Pakamwa panu palankhula zabodza, pamanena zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 2:7

Ndidakufikitsani ku dziko lachonde kuti mudye zipatso zake ndi zabwino zake zina. Koma mutangoloŵa m'dzikolo, mudaliipitsa, dziko limene ndidakupatsani mudalisandutsa lonyansa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 2:11

Okondedwa anga, popeza kuti ndinu alendo pansi pano, ndikukupemphani kuti musagonjere zilakolako zathupi zimene zimachita nkhondo ndi mzimu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:22-24

Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga.

Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano.

Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 3:9

Dama la Israele linali lochititsa manyazi, kotero kuti potsiriza pake adaipitsa dziko. Adachita chigololo popembedza mafano amiyala ndi amitengo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 32:34

Adaika mafano ao onyansa m'Nyumba imene imadziŵika ndi dzina langa, ndipo adaiipitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 12:14

Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 6:27-28

Kodi munthu angathe kufukata moto, zovala zake osapsa?

Kodi munthu angathe kuponda makala amoto, mapazi ake osapserera?

Mutu    |  Mabaibulo
Maliro 4:14

Ankangoyendayenda m'miseu ngati akhungu, zovala zao zili magazi psu, mwakuti palibe munthu woti nkuzikhudza.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 4:12

Munthu asakupeputse poona kuti ndiwe wachinyamata, koma ukhale chitsanzo kwa akhristu onse pa mau, pa mayendedwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 23:38

Adachitanso izi: adaipitsa malo anga ondipembedzera, ndipo adanyoza masiku anga a Sabata.

Mutu    |  Mabaibulo
Hoseya 5:3

“Aefuremu ndikuŵadziŵa, Aisraele ndi osabisika kwa Ine. Aefuremu akhala osakhulupirika, Aisraele adziipitsa.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:27

Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Mika 2:10

Nyamukani, chokani, ano simalo opumulirapo. Zonyansa zanu zaŵaipitsa, zadzetsapo chiwonongeko choopsa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 15:33

Musadzinyenge. “Paja kuyanjana ndi anthu ochimwa kumaononga khalidwe.”

Mutu    |  Mabaibulo
Zefaniya 3:1

Tsoka kwa Yerusalemu, mzinda wopanduka, wonyansa ndi wankhanza.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 52:11

Nyamukani, nyamukani, chokaniko msanga ku Babiloniko, musakhudze kanthu konyansa pa chipembedzo. Tulukanimo ndipo mudziyeretse, inu amene mukunyamula ziŵiya zopatulikira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Zefaniya 3:4

Aneneri ake anali achabechabe, anthu osakhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 15:11

Si chinthu choloŵa m'kamwa mwa munthu chimene chimamuipitsa ai, koma chotuluka m'kamwa mwake ndiye chimene chimamuipitsa.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 17:15-16

Sindikupempha kuti muŵachotse pansi pano ai, koma kuti muŵatchinjirize kwa Woipa uja.

Iwo sali a dziko lapansi, monga Inenso sindili wa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:11

“Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunyengezerani zoipa zamitundumitundu chifukwa cha Ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 15:18

Koma zotuluka m'kamwa mwa munthu zimachokera mu mtima, ndipo zimenezi ndizo zimamuipitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 15:20

Zimenezi ndizo zimaipitsa munthu. Koma kudya chakudya osasamba m'manja, sikungaipitse munthu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 6:12-13

Nchifukwa chake musalole uchimo kuti ulamulire matupi anu otha kufaŵa, ndipo musagonjere zilakolako zake.

Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:16

Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 5:3

Popeza kuti ndinu anthu a Mulungu, ndiye kuti dama kapena zonyansa, kapena masiriro oipa zisatchulidwe nkomwe pakati panu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:4

Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo amuna ndi akazi ao azikhala okhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzaŵalanga.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 3:3

Munthu aliyense amene ali ndi chiyembekezo chimenechi pa Khristu, amadzisandutsa woyera monga momwe Khristuyo ali woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 4:3-4

Chimene Mulungu akufuna ndi ichi: mukhale oyera mtima, ndiye kuti muzipewa dama.

Aliyense mwa inu adziŵe kulamula thupi lake, pakulilemekeza ndi kulisunga bwino, osalidetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 5:8

Uzilambalala kutali ndi mkazi wotere, usamafika kufupi ndi khomo la nyumba yake.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:13

Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa, koma mutipulumutse kwa Woipa uja.” [Pakuti ufumu, mphamvu ndi ulemerero ndi zanu kwamuyaya. Amen.]

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 3:16-17

Kodi inu simudziŵa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu?

Ngati wina aliyense aononga nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo. Pakuti nyumba ya Mulungu ndi yopatulika, ndipo nyumbayo ndinu amene.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 51:10

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 5:17

Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:6-8

Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.

Anthu oika mtima pa khalidwe lokonda zoipa, amadana ndi Mulungu. Anthu otere sagonjera Malamulo a Mulungu, ndipo kunena zoona, sangathedi kuŵagonjera.

Ndipo anthu oika mtima pa khalidwe limenelo, sangathe kukondweretsa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:29

M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 2:15

kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi,

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 3:15-16

koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.

Khalani ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, kotero kuti anthu ena akamasinjirira mayendedwe anu abwino pamene mukutsata Khristu, achite manyazi ndi chipongwe chao.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 23:31-32

Usatengeke mtima ndi kufiira kwa vinyo, pamene akututuma m'chikho namakoma poloŵa ku m'mero.

Potsiriza pake amaluma ngati njoka, ndipo amanjenjedula ngati mphiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 14:13

Tsono tiyeni tileke kumaweruzana. Makamaka mutsimikize kuti musachite kanthu kalikonse kophunthwitsa mbale wanu, kapena komchimwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 8:9

Komabe chenjerani kuti ufulu wanuwu pochita zinthu, ungaphunthwitse ena amene chikhulupiriro chao nchosalimba kwenikweni.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 101:3

Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chachabechabe. Ndimadana ndi zochita za anthu okusiyani, sizindikomera konse.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 5:18

Tikudziŵa kuti aliyense amene ali mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamsunga, ndipo Woipa uja sangamkhudze.

Mutu    |  Mabaibulo
Tito 2:12

Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wolungama ndi wolemekeza Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 13:20

Woyenda ndi anthu anzeru nayenso amakhala ndi nzeru, koma woyenda ndi zitsiru adzaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 3:5

Adzasamala maonekedwe ake okha a chipembedzo, nkumakana mphamvu zake. Anthu otere uziŵalewa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:37

Letsani maso anga kuti asamayang'ane zachabe, mundipatse moyo monga momwe mudalonjezera.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 4:7

Paja Mulungu sadatiitane kuti tizichita zonyansa, koma kuti tikhale oyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 14:16

Munthu wanzeru ngwochenjera, ndipo amalewa choipa, koma chitsiru chimadudukira zinthu mosasamalako.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 26:41

Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:8

Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:2

Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 3:9

Aliyense amene ali mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira, popeza kuti umulungu wake wa Mulunguyo uli mwa iye. Sangathe kumachimwirachimwira, chifukwa ndi mwana wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 7:18

Ndikudziŵa kuti mwa ine simukhala kanthu kabwino. Ndikamati, “ine”, ndikunena khalidwe langa lokonda zoipa. Ngakhale ndimafuna kuchita zabwino, komabe sindizichita.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 9:27

Ndimazunza thupi langa ndi kuligonjetsa, kuti likhale ngati kapolo wondimvera. Ndimachita zimenezi kuwopa kuti ine ndemwe, amene ndidaitana ena ku mpikisano, ndingapezeke wosayenera kuchita nao mpikisanowo.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Petro 3:14

Choncho inu okondedwa, popeza kuti mukudikira zimenezi, muzichita changu kuti Ambuye adzakupezeni muli opanda banga kapena chilema ndiponso muli pa mtendere ndi Ambuyewo.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 4:15

Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 6:11

Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 16:17

Mseu wa munthu wolungama umapewa zoipa. Munthu wopenyetsetsa kumene akupita amasunga moyo wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 13:13

Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:4

Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Petro 1:4

Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo adatipatsa madalitso aakulu ndi amtengowapatali amene Iye adatilonjeza. Adatero kuti mulandireko moyo wake wa Mulungu, mutapulumuka ku chivunde chimene chili pa dziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 10:22

Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:27

Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino,

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 6:19

Ndikukupherani fanizo la ukapololi kuti mungalephere kumvetsa bwino zimenezi. Kale munkadzipereka kuti mukhale akapolo a zonyansa ndi zosalongosoka zonkirankira. Chonchonso tsopano mudzipereke kuti musanduke atumiki a Mulungu ochita zachilungamo, kuti mukhale oyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 6:18

Thaŵani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 11:2

Nsanje imene ndikukuchitirani ndi yonga ya Mulungu. Pakuti ndidakupalitsani ubwenzi ndi mwamuna mmodzi yekha, ngati namwali wangwiro ndi woyera mtima, kuti mukhale akeake a Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 5:6

Nchifukwa chake tsono tisagone tulo monga momwe amachitira anthu ena, ife tikhale maso, tikhale osaledzera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:11

Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:29-30

Ngati diso lako la ku dzanja lamanja likuchimwitsa, likolowole nkulitaya. Ndi bwino koposa kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kusiyana nkuti thupi lako lonse aliponye ku Gehena.

“Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao.

Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, lidule nkulitaya. Ndi bwino kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kupambana kuti thupi lako lonse likaponyedwe ku Gehena.”

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 5:5

Mudziŵe ichi, kuti munthu aliyense wadama, kapena wochita zonyansa, kapena wa masiriro oipa (pakuti wa masiriro oipa ali ngati wopembedza fano) sadzaloŵa nao mu Ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 4:3-4

Paja kale mudakhala mukutaya nthaŵi yochuluka pakuchita zinthu zimene akunja amazikonda. Munkatsata zonyansa, zilakolako zoipa, kuledzera, dyera, maphokoso apamoŵa, ndi kupembedza mafano konyansa.

Anthu akunja amadabwa tsopano poona kuti mwaleka kuthamangira nao zoipitsitsa zimene iwo amachita mosadziletsa konse. Nchifukwa chake amalalata.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 3:10-12

Pakamwa pomwe pamatuluka mayamiko pomweponso pamatuluka matemberero. Abale anga, zoterezi siziyenera kumachitika.

Kodi kasupe amatulutsa madzi omweka ndi oŵaŵa pa dzenje limodzimodzi?

Abale anga, kodi mkuyu ungathe kubala zipatso za olivi, kapena mpesa kubala nkhuyu? Momwemonso kasupe wa madzi amchere sangathe kupereka madzi omweka.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 1:10

Mwana wanga, anthu oipa akafuna kukukopa, usamaŵamvera.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 2:6

Munthu akamati amakhala mwa Mulungu, zochita zake zizilingana ndi zimene Yesu ankachita.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 141:4

Musalole kuti mtima wanga upendekere ku zoipa, ndisadzipereke ku ntchito zoipa pamodzi ndi anthu ochita zoipa, ndisadye nawo maphwando ao.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 6:14

Musamagwirizana ndi anthu akunja, monga ngati kuti iwo ndi inu mumafanana. Nanga kulungama kungagwirizane bwanji ndi kusalungama? Kapena kuŵala kungayanjane bwanji ndi mdima?

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:13

Pakuti ngati m'moyo mwanu mutsata khalidwelo, mudzafa. Koma ngati ndi chithandizo cha Mzimu Woyera mupha zilakolako zanu zathupi, mudzakhala ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 16:6

Chifukwa cha kudzipereka ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake. Chifukwa choopa Chauta munthu amalewa zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 12:1

Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 15:3

Inu mwayera kale chifukwa cha mau amene ndakuuzani.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:25

Tsono lekani kunama. Aliyense azilankhula zoona zokhazokha ndi mkhristu mnzake, pakuti tonse pamodzi mogwirizana ndife ziwalo za thupi la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:13-14

“Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri.

Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 2:10

Inu ndinu mboni, Mulungu yemwe ndi mboninso, kuti mkhalidwe wathu pakati pa inu okhulupirira unali wangwiro, wolungama, ndi wopanda cholakwa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 1:15

Koma monga Iye amene adakuitanani ali woyera mtima, inunso khalani oyera mtima m'makhalidwe anu onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 10:9

Munthu woyenda mwaungwiro, amayenda mosatekeseka. Koma woyenda njira zoipa, adzadziŵika.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:9

Chikondi chizikhala chopanda chiphamaso. Muzidana ndi zoipa, nkumaika mtima pa kuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wakumwamba, moyo wanga wonse ukukwezetsa ndi kudalitsa dzina lanu, ndinu mlengi wa moyo wanga, zonse zomwe ndili nazo ndi chifukwa cha chisomo chanu chomwe chikuwonekera pa ine tsiku lililonse. Chikondi chanu ndi chachikulu kwambiri kotero kuti ngakhale kuipa kwanga simuleka kundionetsa chifundo chanu. Munandikonda ndipo munatumiza Mwana wanu Yesu kuti ndikhale woyera mwa magazi ake amtengo wapatali. Chifukwa chake pakali pano ndikubwera kwa Yesu, ndikuvomereza machimo anga pamaso panu. Pali zinthu zambiri mwa ine zomwe zayipitsa moyo wanga ndi maganizo anga. Ndikupemphani munditsuke ndi magazi anu ndi kundiyera chifukwa ndikufuna kukhala moyera. Sindikufuna kukukhumudwitsani Ambuye. Mundifufuze, konzani zolinga zanga, kuti chinthu chofunika kwambiri pa moyo wanga mukhale inu, kuti pasakhale chilichonse chomwe ndingadzitamandire nacho kupatula kukhala nanu. Moyo wanga uli m'manja mwanu, mundipange monga momwe mukufunira, mundikwaniritse mu chiyero chanu ndi kuopa kwanu kuti ndikhale molungama pamaso panu, ndi mtima woyera. M'dzina la Yesu, Ameni.