Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

124 Mau a m'Baibulo a Tsiku la Abusa

Abale ndi alongo, ndikufuna ndikuuzeni za abusa athu. Ntchito yawo yotsogolera anthu a Mulungu ndi yaikulu kwambiri. Amafunika kukhala chitsanzo chabwino kuti ife tionetse Mulungu mwa iwo.

Kutsogolera mpingo ndi mwayi waukulu wochokera kwa Mulungu. Ngakhale nthawi zina sitizindikira khama lawo, Mulungu akuona zonse ndipo ali ndi mphoto yaikulu kwa iwo kumwamba.

Tisaiwale kuti abusa athu nawonso ndi ana a Mulungu. Ndi anthu, amalakwitsa, ndipo ali ndi maganizo ngati ife. Mawu olimbikitsa ndi oyamikira amawasangalatsa kwambiri.

Tiyeni tipempherere abusa athu, kuti Mulungu awasamalire ndi kuwatsogolera nthawi zonse. Tiwalemekeze ndi kuwathandiza m’njira iliyonse yomwe tingathe, kuti adziwe kuti tikuwayamikira.


1 Atesalonika 5:12-13

Koma, abale, tikupemphani, dziwani iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu;

ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 52:7

Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:12

Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 21:17

Ananena naye kachitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro anamva chisoni kuti anati kwa iye kachitatu, Kodi undikonda Ine? Ndipo anati kwa iye, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu ananena naye, Dyetsa nkhosa zanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 20:28

Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha.

Mutu    |  Mabaibulo
3 Yohane 1:2

Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera.

Mutu    |  Mabaibulo
Numeri 6:24-26

Yehova akudalitse iwe, nakusunge;

Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo;

Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 25:21

Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 3:15

ndipo ndidzakupatsani inu abusa monga mwa mtima wanga, adzakudyetsani inu nzeru ndi luntha.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:7

Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mau a Mulungu; ndipo poyang'anira chitsiriziro cha mayendedwe ao mutsanze chikhulupiriro chao.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 2:15

Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 5:17

Akulu akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akuchititsa m'mau ndi m'chiphunzitso.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:11

Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 1:8

Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idamveka padziko lonse lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 23:1

Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 1:2-3

Tiyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu nonse, ndi kukumbukira inu m'mapemphero athu;

ndi kukumbukira kosalekeza ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi chikondi chochitachita, ndi chipiriro cha chiyembekezo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu;

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 3:2

Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 22:14

Pakuti oitanidwa ndiwo ambiri, koma osankhidwa ndiwo owerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 3:14

Ndipo anaika khumi ndi awiri, kuti akhale ndi Iye, ndi kuti akawatume kulalikira,

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 6:34

Ndipo anatuluka Iye, naona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 21:16

Ananena nayenso kachiwiri, Simoni mwana wa Yona, ukonda Ine kodi? Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Weta nkhosa zanga.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:2

Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 10:1

Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wosalowa m'khola la nkhosa pakhomo, koma akwerera kwina, iyeyu ndiye wakuba ndi wolanda.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 10:15

monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 27:23

Udziwitsitse zoweta zako zili bwanji, samalira magulu ako;

Mutu    |  Mabaibulo
Tito 1:7

Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati wachiwawa, wopanda ndeu, wosati wa chisiriro chonyansa;

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 3:15

koma mumpatulikitse Ambuye Khristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha;

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:2-4

Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;

osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.

Ndipo pakuonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 78:70-72

Ndipo anasankha Davide mtumiki wake, namtenga kumakola a nkhosa.

Anamtenga kuja anatsata zoyamwitsa, awete Yakobo, anthu ake, ndi Israele, cholowa chake.

Potero anawaweta monga mwa mtima wake wangwiro; nawatsogolera ndi luso la manja ake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:11

Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:22

Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 3:13

Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukulu m'chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 34:2-4

Wobadwa ndi munthu iwe, Nenera motsutsa abusa a Israele; nenera, nuti nao abusawo, Atero Ambuye Yehova, Tsoka abusa a Israele odzidyetsa okha; kodi abusa sayenera kudyetsa nkhosa?

Chifukwa chake atero nao Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzaweruza pakati pa zoweta zonenepa, ndi zoweta zoonda.

Popeza mukankha ndi nthiti ndi phewa, nimugunda zodwala zonse ndi nyanga zanu, mpaka mwazibalalitsa kubwalo,

chifukwa chake ndidzapulumutsa gulu langa lisakhalenso chakudya; ndipo ndidzaweruza pakati pa zoweta ndi zoweta.

Ndipo ndidzaziutsira mbusa mmodzi; iye adzazidyetsa, ndiye mtumiki wanga Davide, iye adzazidyetsa, nadzakhala mbusa wao.

Ndipo Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wao, ndi mtumiki wanga Davide kalonga pakati pao; Ine Yehova ndanena.

Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'chipululu, ndi kugona kunkhalango.

Pakuti ndidzaika izi ndi midzi yozungulira chitunda changa, zikhale mdalitso; ndipo ndidzavumbitsa mivumbi m'nyengo yake, padzakhala mivumbi ya madalitso.

Ndi mitengo yakuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m'dziko mwao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lao, ndi kuwalanditsa m'manja mwa iwo akuwatumikiritsa.

Ndipo sadzakhalanso chakudya cha amitundu, ndi chilombo chakuthengo sichidzawadyanso; koma adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa.

Ndipo ndidzawautsira mbeu yomveka, ndipo sadzachotsedwanso ndi njala m'dzikomo, kapena kusenzanso manyazi a amitundu.

Mukudya mafuta, muvala ubweya, mukupha zonenepa; koma simudyetsa nkhosa.

Ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wao ndili nao, ndi kuti iwo, nyumba ya Israele, ndiwo anthu anga, ati Ambuye Yehova.

Ndipo inu nkhosa zanga, nkhosa zapabusa panga, ndinu anthu, ndi Ine ndine Mulungu wanu, ati Ambuye Yehova.

Zofooka simunazilimbitse; yodwala simunaichiritse, yothyoka simunailukire chika, yopirikitsidwa simunaibweze, yotayika simunaifune; koma munazilamulira mwamphamvu ndi moopsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 34:11-12

Pakuti atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzapwaira nkhosa zanga ndi kuzifunafuna.

Monga mbusa afunafuna nkhosa zake tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zake zobalalika, momwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 34:16

Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopirikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndikulimbitsa yodwalayo; koma yonenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 9:36

Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 10:6

koma makamaka mupite kunkhosa zosokera za banja la Israele.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 18:12-14

Nanga muyesa bwanji? Ngati munthu ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo ikasokera imodzi ya izo, kodi saleka zija makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai, napita kumapiri, kukafuna yosokerayo?

Ndimo akaipeza, indedi ndinena kwa inu, akondwera nayo koposa ndi makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai zosasokera.

Chomwecho sichili chifuniro cha Atate wanu wa Kumwamba kuti mmodzi wa ang'ono awa atayike.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 20:26-28

Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma aliyense amene akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu;

ndipo aliyense amene akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu:

monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 25:35-40

pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine;

wamaliseche Ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndinali m'nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine.

Pomwepo olungama adzamyankha Iye kuti, Ambuye, tinakuonani Inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? Kapena waludzu, ndi kukumwetsani?

Ndipo tinaona Inu liti mlendo, ndi kukucherezani? Kapena wamaliseche, ndi kukuvekani?

Ndipo tinakuonani Inu liti wodwala, kapena m'nyumba yandende, ndipo tinadza kwa Inu?

koma anzeruwo anatenga mafuta m'nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao.

Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 28:19-20

Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:

Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake.

ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 16:15

Ndipo ananena nao, Mukani kudziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 12:42

Ndipo Ambuye anati, Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adzamuika kapitao wa pa banja lake, kuwapatsa iwo phoso lao pa nthawi yake?

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 15:4-7

Munthu ndani wa inu ali nazo nkhosa makumikhumi, ndipo pakutayika imodzi ya izo, sasiya nanga m'chipululu zinazo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai, nalondola yotayikayo kufikira aipeza?

Ndipo pamene adaipeza, aisenza pa mapewa ake wokondwera.

Ndipo pakufika kunyumba kwake amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena nao, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza nkhosa yanga yotayikayo.

Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe Kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 10:11

Ine ndine Mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 10:14-15

Ine ndiye Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira Ine,

monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 21:15-17

Ndipo pamene atafisula Yesu ananena kwa Simoni Petro, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa? Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Dyetsa anaankhosa anga.

Ananena nayenso kachiwiri, Simoni mwana wa Yona, ukonda Ine kodi? Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Weta nkhosa zanga.

Ananena naye kachitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro anamva chisoni kuti anati kwa iye kachitatu, Kodi undikonda Ine? Ndipo anati kwa iye, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu ananena naye, Dyetsa nkhosa zanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:6-8

Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa chisomo chipatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa chikhulupiriro;

kapena yakutumikira, tidzipereke ku utumiki uwu; kapena iye wakuphunzitsa, kukuphunzitsako;

kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira achite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi changu; iye wakuchita chifundo, achite ndi kukondwa mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 4:1-2

Chotero munthu atiyese ife, monga atumiki a Khristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu.

Tili opusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tili ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.

Kufikira nthawi yomwe ino timva njala, timva ludzu, tili amaliseche, tikhomedwa, tilibe pokhazikika;

ndipo tigwiritsa ntchito, ndi kuchita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira;

ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano.

Sindilembera izi kukuchititsani manyazi, koma kuchenjeza inu monga ana anga okondedwa.

Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Khristu Yesu ine ndinabala inu mwa Uthenga Wabwino.

Chifukwa chake ndikupemphani, khalani akutsanza ine.

Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Khristu, monga ndiphunzitsa ponsepo mu Mipingo yonse.

Koma ena adzitukumula, monga ngati sindinalinkudza kwa inu.

Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi.

Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 12:28

Ndipotu Mulungu anaika ena mu Mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 1:24

Si kuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:2

Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:11-12

Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;

kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:3-5

Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse;

ndi kukhala nacho inu chilimbano chomwechi mudachiona mwa ine, nimukumva tsopano chili mwa ine.

nthawi zonse m'pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndichita pembedzerolo ndi kukondwera,

chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 1:28

amene timlalikira ife, ndi kuchenjeza munthu aliyense ndi kuphunzitsa munthu aliyense mu nzeru zonse, kuti tionetsere munthu aliyense wamphumphu mwa Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 3:1-7

Mauwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang'anira, aifuna ntchito yabwino.

Koma iwonso ayamba ayesedwe; pamenepo atumikire, akakhala opanda chifukwa.

Momwemonso akazi akhale olemekezeka, osadierekeza, odzisunga, okhulupirika m'zonse.

Atumiki akhale mwamuna wa mkazi mmodzi, akuweruza bwino ana ao, ndi iwo a m'nyumba yao ya iwo okha.

Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukulu m'chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.

Izi ndikulembera ndi kuyembekeza kudza kwa iwe posachedwa, koma ngati ndichedwa,

kuti udziwe kuyenedwa kwake pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi.

Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.

Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;

wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba chuma;

woweruza bwino nyumba yake ya iye yekha, wakukhala nao ana ake omvera iye ndi kulemekezeka konse.

Koma ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanji Mpingo wa Mulungu?

Asakhale wophunza, kuti podzitukumula ungamgwere mlandu wa mdierekezi.

Kuyeneranso kuti iwo akunja adzakhoza kumchitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa mdierekezi.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 4:2

lalikira mau; chita nao pa nthawi yake, popanda nthawi yake; tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.

Mutu    |  Mabaibulo
Tito 1:5-9

Chifukwa cha ichi ndinakusiya iwe mu Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akulu m'midzi yonse, monga ndinakulamulira;

ngati wina ali wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nao ana okhulupirira, wosasakaza zake, kapena wosakana kumvera mau.

Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati wachiwawa, wopanda ndeu, wosati wa chisiriro chonyansa;

komatu wokonda kuchereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa;

wogwira mau okhulupirika monga mwa chiphunzitso, kuti akakhoze kuchenjeza m'chiphunzitso cholamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:17

Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 2:25

Pakuti munalikusochera ngati nkhosa; koma tsopano mwabwera kwa Mbusa ndi Woyang'anira wa moyo wanu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:1-4

Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mnzanu ndi mboni ya zowawa za Khristu, ndinenso wolawana nao ulemerero udzavumbulutsikawo:

Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.

Kwa Iye kukhale mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.

Mwa Silivano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwachidule, ndi kudandaulira, ndi kuchita umboni, kuti chisomo choona cha Mulungu ndi ichi; m'chimenechi muimemo.

Iye wa ku Babiloni wosankhidwa pamodzi nanu akukupatsani moni; ateronso Marko mwana wanga.

Mupatsane moni ndi kupsompsonana kwa chikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse muli mwa Khristu.

Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;

osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.

Ndipo pakuonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:105

Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:4-5

Mbadwo wina udzalemekezera ntchito zanu mbadwo unzake, ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.

Ndidzalingalira ulemerero waukulu wa ulemu wanu, ndi ntchito zanu zodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 147:3

Achiritsa osweka mtima, namanga mabala ao.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 1:5

kuti wanzeru amve, naonjezere kuphunzira; ndi kuti wozindikira afikire kuuphungu;

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 11:14

Popanda upo wanzeru anthu amagwa; koma pochuluka aphungu pali chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 12:15

Njira ya chitsiru njolungama pamaso pakepake; koma wanzeru amamvera uphungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 18:1

Wopanduka afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 20:18

Uphungu utsimikiza zolingalira, ponya nkhondo utapanga upo.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 27:23-27

Udziwitsitse zoweta zako zili bwanji, samalira magulu ako;

pakuti chuma sichili chosatha; kodi korona alipobe mpaka mibadwomibadwo.

Amatuta udzu, msipu uoneka, atchera masamba a kumapiri.

Anaankhosa akuveka, atonde aombolera munda;

mkaka wa mbuzi udzakukwanira kudya; ndi a pa banja lako ndi adzakazi ako.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 61:1-2

Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;

Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.

Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zake, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse.

ndikalalikire chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro;

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:14-16

Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mzinda wokhazikika pamwamba paphiri sungathe kubisika.

Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo.

Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:15-20

Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa.

Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula?

Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa.

Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma.

Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto.

Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.

Inde chomwecho pa zipatso zao mudzawazindikira iwo.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 9:37-38

Pomwepo ananena kwa ophunzira ake, Zotuta zichulukadi koma antchito ali owerengeka.

Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 12:18

Taona mnyamata wanga, amene ndinamsankha, wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; pa Iye ndidzaika Mzimu wanga, ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa akunja.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 6:40

Wophunzira saposa mphunzitsi wake; koma yense, m'mene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 10:3-4

Iyeyu, wapakhomo amtsegulira ndi nkhosa zimva mau ake; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina ao, nazitsogolera kunja.

Ine ndi Atate ndife amodzi.

Ayuda anatolanso miyala kuti amponye Iye.

Yesu anayankha iwo, Ndakuonetsani inu ntchito zabwino zambiri za kwa Atate; chifukwa cha ntchito yiti ya izo mundiponya miyala?

Ayuda anamyankha Iye, Chifukwa cha ntchito yabwino sitikuponyani miyala, koma chifukwa cha mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu.

Yesu anayankha iwo, Kodi sikulembedwa m'chilamulo chanu, Ndinati Ine, Muli milungu?

Ngati anawatcha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo cholemba sichingathe kuthyoka),

kodi inu munena za Iye, amene Atate anampatula namtuma kudziko lapansi, Uchita mwano; chifukwa ndinati, Ndili Mwana wa Mulungu?

Ngati sindichita ntchito za Atate wanga, musakhulupirira Ine.

Koma ngati ndichita, mungakhale simukhulupirira Ine, khulupirirani ntchitozo; kuti mukadziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndi Ine mwa Atate.

Anafunanso kumgwira Iye; ndipo anapulumuka m'dzanja lao.

Pamene adatulutsa zonse nkhosa zimtsata iye; chifukwa zidziwa mau ake.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 2:42

Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 6:3

Chifukwa chake, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 1:11-12

Pakuti ndilakalaka kuonana ndinu, kuti ndikagawire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike;

ndiko, kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse awiri, chanu ndi changa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 3:5-9

Ndipo Apolo nchiyani, ndi Paulo nchiyani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anampatsa.

Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa.

Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa.

Koma wookayo ndi wothirirayo ali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha.

Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 4:5

Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 5:20

Chifukwa chake tili atumiki m'malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m'malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 1:10

Pakuti kodi ndikopa anthu tsopano, kapena Mulungu? Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Ndikadakhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala kapolo wa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:15-16

koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu;

kuchokera mwa Iye thupi lonse, lolukidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 2:3-4

musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;

pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine.

munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:16

Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 2:11-12

monga mudziwa kuti tinachitira yense wa inu pa yekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha,

ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kuchita umboni, kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wake wa Iye yekha, ndi ulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Atesalonika 3:1

Chotsalira, abale, mutipempherere, kuti mau a Ambuye athamange, nalemekezedwe, monganso kwanu;

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 1:18

Lamulo ili ndipereka kwa iwe, mwana wanga Timoteo, kuti, monga mwa zonenera zidakutsogolera iwe kale, ulimbane nayo nkhondo yabwino;

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 2:7

umene anandiika ine mlaliki wake ndi mtumwi (ndinena zoona, wosanama ine), mphunzitsi wa amitundu m'chikhulupiriro ndi choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo
Tito 2:7-8

m'zonse udzionetsere wekha chitsanzo cha ntchito zabwino; m'chiphunzitso chako uonetsere chosavunda, ulemekezeko,

mau olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana achite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 10:24-25

ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,

osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:5

Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:19

Tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 25:4-5

Mundidziwitse njira zanu, Yehova; Mundiphunzitse mayendedwe anu.

Munditsogolere m'choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:10

Misona ya mkango isowa nimva njala, koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 71:17-18

Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga; ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwitsa zanu.

Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:11

Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:5-6

Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako;

umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 4:7-9

Nzeru ipambana, tatenga nzeru; m'kutenga kwako konseko utenge luntha.

Uilemekeze, ndipo idzakukweza; idzakutengera ulemu pamene uifungatira.

Idzaika chisada cha chisomo pamutu pako; idzakupatsa korona wokongola.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 30:20-21

Ndipo ngakhale Ambuye adzakupatsani inu chakudya cha nsautso, ndi madzi a chipsinjo, koma aphunzitsi ako sadzabisikanso, koma maso ako adzaona aphunzitsi ako;

ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:29

Iye alimbitsa olefuka, naonjezera mphamvu iye ameme alibe mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 10:8

Chiritsani akudwala, ukitsani akufa, konzani akhate, tulutsani ziwanda: munalandira kwaulere, patsani kwaulere.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 18:19-20

Ndiponso ndinena kwa inu kuti ngati awiri a inu avomerezana pansi pano chinthu chilichonse akachipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawachitira.

Ndipo pamene Yesu anaitana kamwana, anakaimitsa pakati pao,

Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 10:1

Zitapita izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiriawiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 15:12

Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:3

Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 12:12-13

Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonso Khristu.

Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 9:8

Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:13-14

Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.

Pakuti mau amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 2:10

Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:27

Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino;

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 4:5-6

Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthawi ingatayike.

Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 3:12

koma Ambuye akukulitseni inu, nakuchulukitseni m'chikondano wina kwa mnzake ndi kwa anthu onse, monganso ife titero kwa inu;

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 1:7

Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:1-2

Chikondi cha pa abale chikhalebe.

Tili nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira chihema alibe ulamuliro wa kudyako.

Pakuti matupi a nyama zija, mwazi wa izo umatengedwa, ndi mkulu wa ansembe kulowa m'malo opatulidwa, chifukwa cha zoipa, amatenthedwa kunja kwa tsasa.

Mwa ichi Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa Iye yekha, adamva chowawa kunja kwa chipata.

Chifukwa chake titulukire kwa Iye kunja kwa tsasa osenza tonzo lake.

Pakuti pano tilibe mzinda wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo.

Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.

Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.

Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.

Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m'zonse, pofuna kukhala nao makhalidwe abwino.

Ndipo ndikudandaulirani koposa kuchita ichi, kuti kubwera kwanga kwa inu kufulumidwe.

Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 3:1

Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziwa kuti tidzalangika koposa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:5

Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:12

Inu ndinu wodala Yehova; ndiphunzitseni malemba anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:50

Chitonthozo changa m'kuzunzika kwanga ndi ichi; pakuti mau anu anandipatsa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 133:1

Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 3:16

Umo tizindikira chikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse! Ndikubwera kwa Inu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, Inu nokha ndinu Woyenera kutamandidwa ndi kulambiridwa kwakukulu. Ndikukupemphani chifukwa cha m'busa wanga, kuti mafuta a Mzimu Woyera akhale pa moyo wake ndipo tsiku lililonse mulimbitse utumiki umene mwamupatsa. Mudzaze ndi nzeru kuti akhale woyang'anira bwino ndi kuphunzitsa mpingo wanu molingana ndi mawu anu. Dalitsani moyo wake ndi wa banja lake. Muthandizeni kukhalabe mu mgwirizano wa mtendere kuti nthawi zonse azitsatira khalidwe labwino, akusonyeza umboni ndi chikondi cha Khristu. Mawu anu amati: "Koma mkulu ayenera kukhala wosalakidwa, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodziletsa, wanzeru, waulemu, wokonda alendo, wolangiza bwino." Muthandizeni tsiku lililonse kukhala ndi moyo wopemphera ndi kuyanjana nanu kotero kuti chofunika kwambiri pa moyo wake chikhale kukhalapo kwa Mzimu Woyera wanu. Ndikukupemphani kuti muunikire nkhope yanu pa iye, kuti chisomo chanu ndi chiyanjo chanu zikhalebe pa moyo wake. Muzikonzanso mphamvu zake kuti athe kukumana ndi zovuta ndi mavuto kaya muutumiki, zachuma kapena za m'banja. Mulimbitse kuti apulumuke mu mayesero ndi ziyeso m'dzina la Yesu. Ameni.