Masalimo 133 - Buku LopatulikaChikondano cha abale ndi chokoma Nyimbo yokwerera; ya Davide. 1 Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi! 2 Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake. 3 Ngati mame a ku Heremoni, akutsikira pa mapiri a Ziyoni. Pakuti pamenepo Yehova analamulira dalitsolo, ndilo moyo womka muyaya. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi