1 Timoteyo 2 - Buku LopatulikaPemphero la kwa anthu onse 1 Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse; 2 chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse. 3 Pakuti ichi nchokoma ndi cholandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu; 4 amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi. 5 Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Khristu Yesu, 6 amene anadzipereka yekha chiombolo m'malo mwa onse; umboni m'nyengo zake; 7 umene anandiika ine mlaliki wake ndi mtumwi (ndinena zoona, wosanama ine), mphunzitsi wa amitundu m'chikhulupiriro ndi choonadi. 8 Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani. Zoyenera akazi 9 Momwemonso, akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golide kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali; 10 komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino. 11 Mkazi aphunzire akhale wachete m'kumvera konse. 12 Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale chete. 13 Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Heva; 14 ndipo Adamu sananyengedwe, koma mkaziyo ponyengedwa analowa m'kulakwa; 15 koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m'chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi