Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Timoteyo 2:9 - Buku Lopatulika

9 Momwemonso, akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golide kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Momwemonso, akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golide kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndikufunanso kuti akazi azivala mwaulemu, mwanzeru ndi moyenera. Inde adzikongoletse, komatu osati ndi tsitsi lochita kukonza monyanyira, kapena ndi zokongoletsa zagolide, kapena mikanda yamtengowapatali, kapena zovala zamtengowapatali.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ndikufunanso kuti amayi azivala mwaulemu, modzilemekeza ndi moyenera. Adzikongoletse koma osati ndi tsitsi loluka mowonjeza muyeso kapena zokongoletsa zagolide kapena mikanda yamtengowapatali kapena ndi zovala zamtengowapatali.

Onani mutuwo Koperani




1 Timoteyo 2:9
20 Mawu Ofanana  

Ndipo mnyamatayo anatulutsa zokometsera zasiliva ndi zagolide, ndi zovala, nampatsa Rebeka: ndipo anapatsa za mtengo wapatali kwa mlongo wake ndi amake.


Ndipo pofika Yehu ku Yezireele, Yezebele anamva, nadzikometsera m'maso, naluka tsitsi lake, nasuzumira pazenera.


Ndipo kunali tsiku lachitatu, Estere anavala zovala zake zachifumu, nakaimirira m'bwalo la m'kati la nyumba ya mfumu, popenyana pa nyumba ya mfumu; ndi mfumu inakhala pa mpando wake wachifumu m'nyumba yachifumu, pandunji polowera m'nyumba.


Popeza Yehova akondwera nao anthu ake; adzakometsa ofatsa ndi chipulumutso.


Adzipangira zimbwi zamawangamawanga; navala bafuta ndi guta wofiirira.


Avala mphamvu ndi ulemu; nangoseka nthawi ya m'tsogolo.


Ndipo taona, mkaziyo anamchingamira, atavala zadama wochenjera mtima,


Komanso Yehova ati, Chifukwa kuti ana aakazi a Ziyoni angodzikuza atakweza makosi ao, ndi maso ao adama nayenda nanyang'ama poyenda pao naliza zigwinjiri za mapazi ao;


Ndipo iwo adzamanga mabwinja akale, nadzamanga pa miunda yakale, nadzakonzanso mizinda yopasuka, mabwinja a mibadwo yambiri.


Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zake, kapena mkwatibwi zovala zake? Koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka.


Nanga iwe, udzachita chiyani pamene udzafunkhidwa? Ngakhale udziveka ndi zofiira, ngakhale udziveka ndi zokometsera zagolide, ngakhale udzikuzira maso ako ndi kupaka, udzikometsera pachabe; mabwenzi adzakunyoza adzafuna moyo wako.


Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Onani, akuvala zofewa ali m'nyumba zamafumu.


komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa