Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Timoteyo 2:2 - Buku Lopatulika

2 chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Muziŵapempherera mafumu ndi onse amene ali ndi ulamuliro, kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, tizitamanda Mulungu pa zonse ndi kumadzilemekeza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mupempherere mafumu ndi onse aulamuliro, kuti tikhale moyo wamtendere ndi bata, woopa Mulungu ndi oyera mtima.

Onani mutuwo Koperani




1 Timoteyo 2:2
22 Mawu Ofanana  

Ine ndine wa awo amene ali amtendere ndi okhulupirika mu Israele; inu mulikufuna kuononga mzinda ndi mai wa mu Israele; mudzamezeranji cholowa cha Yehova?


kuti apereke nsembe zonunkhira bwino kwa Mulungu wa Kumwamba, napempherere moyo wa mfumu ndi wa ana ake.


Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.


Patsani mfumu maweruzo anu, Mulungu, ndi mwana wa mfumu chilungamo chanu.


Mwananga, opa Yehova ndi mfumu yomwe, osadudukira anthu osinthasintha.


Nimufune mtendere wa mzinda umene ndinakutengerani am'nsinga, nimuwapempherere kwa Yehova; pakuti mwa mtendere wake inunso mudzakhala ndi mtendere.


Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.


Ndipo onani, mu Yerusalemu munali munthu, dzina lake Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israele; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.


Ndipo anati, Kornelio kenturiyoyo, munthu wolungama ndi wakuopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umchitira umboni, anachenjezedwa ndi mngelo woyera kuti atumize nakuitaneni mumuke kunyumba yake, ndi kumvetsa mau anu.


M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbumtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.


Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.


Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.


ndi kuti muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuuzani;


Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa