Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 10:1 - Buku Lopatulika

1 Zitapita izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiriawiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Zitapita izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiriawiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pambuyo pake Ambuye adasankha anthu 72, naŵatuma aŵiriaŵiri kuti atsogole kupita ku mudzi uliwonse ndi ku malo aliwonse kumene Iye ankati apiteko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Zitatha izi Ambuye anasankha enanso 72 ndi kuwatumiza awiriawiri patsogolo pake ku mzinda uliwonse ndi kumalo kumene Iye anatsala pangʼono kupitako.

Onani mutuwo Koperani




Luka 10:1
14 Mawu Ofanana  

Ndipo pamaso pao panaima amuna makumi asanu ndi awiri a akulu a nyumba ya Israele, ndi pakati pao panaima Yazaniya mwana wa Safani, munthu aliyense ndi mbale yake ya zofukiza m'dzanja lake; ndi fungo lake la mtambo wa zonunkhira linakwera.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Undisonkhanitsire amuna makumi asanu ndi awiri mwa akulu a Israele, amene uwadziwa kuti ndiwo akulu a anthu, ndi akapitao ao; nubwere nao ku chihema chokomanako, kuti aimeko pamodzi ndi iwe.


Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.


Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu; pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake.


Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.


Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ake, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?


natumiza amithenga patsogolo pake; ndipo ananka, nalowa m'mudzi wa Asamariya, kukamkonzera Iye malo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa