Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


104 Mau a Mulungu Okhudza Kuvina ndi Kulambira

104 Mau a Mulungu Okhudza Kuvina ndi Kulambira

Kale lomwe, kuvina sikunali kololedwa m’malo olambirira monga masikono, m’makachisi, m’masunagoge, komanso sikunali mbali ya kulambira kwa mpingo woyamba. Koma masiku ano, ndimaona kuti kuvina ndi njira yotamandira Mulungu, kufotokoza ndi thupi langa zimene nthawi zina sindingathe kufotokoza ndi mawu.

Kuvina ndi njira yolemekezera Wapamwamba, kusonyeza chisangalalo changa, ndi kukondwerera zipambano zimene amandipatsa tsiku ndi tsiku. Ndikukumbukira kuti koyamba kuvina kutchulidwa m’Baibulo kunali pamene Aisiraeli anaoloka Nyanja Yofiira.

M’buku la Ekisodo 15:20-21, timawerenga mmene Miriamu, mlongo wake wa Aroni, anatengera chimbale ndipo akazi anzake anamutsatira ndi zimbale ndi mavina, akuimbira Yehova chifukwa cha ukulu wake ndi chifukwa chogonjetsa ankhondo a Aigupto panyanja. Chochititsa chidwi n’chakuti chikondwererochi chinachitikira panja, kusonyeza kuti Mulungu amafuna kuti tikondwerere ndi chisangalalo, kulumpha, ndi chimwemwe pazonse zimene atichitira, tikukhala m’ufulu wathunthu.




2 Samueli 6:14

Ndipo Davide anavina ndi mphamvu yake yonse pamaso pa Yehova; Davide nadzimangirira efodi wabafuta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 15:20

Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 15:29

Ndipo polowa likasa la chipangano la Yehova m'mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo anasuzumira pazenera, nao mfumu Davide alikutumphatumpha ndi kusewera; ndipo anampeputsa mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 149:3

Alemekeze dzina lake ndi kuthira mang'ombe; amuimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 150:4

Mlemekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang'ombe: Mlemekezeni ndi zoimbira za zingwe ndi chitoliro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:11

Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera; munandivula chiguduli changa, ndipo munandiveka chikondwero,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 6:5

Ndipo Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anasewera pamaso pa Yehova, ndi zoimbira za mitundumitundu za mlombwa, ndi azeze, ndi zisakasa ndi malingaka, ndi maseche, ndi nsanje.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 18:6

Ndipo kunali pakudza iwo, pamene Davide anabwera atapha Afilistiwo, anthu aakazi anatuluka m'mizinda yonse ya Israele, ndi kuimba ndi kuvina, kuti akakomane ndi mfumu Saulo, ndi malingaka, ndi chimwemwe, ndi zoimbira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 31:13

Ndipo namwali adzasangalala m'masewero, ndi anyamata ndi nkhalamba pamodzi; pakuti ndidzasandutsa kulira kwao kukhale kukondwera, ndipo ndidzatonthoza mitima yao, ndi kuwasangalatsa iwo asiye chisoni chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 11:34

Pofika Yefita ku Mizipa kunyumba yake, taonani, mwana wake wamkazi anatuluka kudzakomana naye ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe; ndipo iyeyu anali mwana wake mmodzi yekha, analibe mwana wina wamwamuna kapena wamkazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 33:1

Fuulani mokondwera mwa Yehova, inu olungama mtima, oongoka mtima ayenera kulemekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 89:16

Akondwera m'dzina lanu tsiku lonse; ndipo akwezeka m'chilungamo chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 31:4

Ndidzamangitsanso mudzi wako, ndipo udzamangidwa, iwe namwali wa Israele; udzakometsedwanso ndi mangaka, ndipo udzatulukira masewero a iwo akukondwerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 8:10

Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 47:1

Ombani m'manja, mitundu yonse ya anthu; fuulirani kwa Mulungu ndi liu la kuimbitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 6:16

Ndipo kunali pamene likasa la Yehova linafika m'mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikuvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 16:29

Mchitireni Yehova ulemerero wa dzina lake; bwerani nacho chopereka, ndipo fikani pamaso pake; lambirani Yehova m'chiyero chokometsetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 25:1

Ndipo Davide ndi akazembe a gulu la nkhondo anapatulira utumikiwo ena a ana a Asafu, ndi a Hemani, ndi a Yedutuni, anenere ndi azeze, ndi zisakasa, ndi nsanje; ndi chiwerengo cha antchito monga mwa kutumikira kwao ndicho:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:1

Ndidzayamika Yehova ndi mtima wanga wonse; ndidzawerengera zodabwitsa zanu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:3

Koma Inu ndinu woyera, wakukhala m'malemekezo a Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 24:7-8

Weramutsani mitu yanu, zipata inu; ndipo kwezekani inu, zitseko zosatha, kuti Mfumu ya ulemerero ilowe. Mfumu imene ya ulemerero ndani? Yehova wamphamvu ndi wolimba, Yehova wolimba kunkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:15

Ambuye, tsegulani pa milomo yanga; ndipo pakamwa panga padzalalikira ulemekezo wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 63:4

Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga; ndidzakweza manja anga m'dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:24-25

Anapenya mayendedwe anu, Mulungu, mayendedwe a Mulungu wanga, mfumu yanga, m'malo oyera. Oimbira anatsogolera, oimba zoimba anatsata m'mbuyo, pakatipo anamwali oimba mangaka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 95:6

Tiyeni, tipembedze tiwerame; tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 100:1-2

Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi. Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: Idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:1

Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 104:33

Ndidzaimbira Yehova m'moyo mwanga: ndidzaimbira Mulungu wanga zomlemekeza pokhala ndilipo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 105:1-2

Yamikani Yehova, itanirani pa dzina lake; bukitsani mwa mitundu ya anthu zochita Iye. ndipo anachiimikira Yakobo, chikhale malemba, chikhale chipangano chosatha kwa Israele. Ndi kunena kuti, Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani, gawo la cholowa chako; pokhala iwo anthu owerengeka, inde, anthu pang'ono, ndi alendo m'mwemo; nayendayenda kuchokera mtundu wina kufikira mtundu wina, kuchokera ufumu wina kufikira anthu ena. Sanalola munthu awasautse; ndipo anadzudzula mafumu chifukwa cha iwowa. Ndi kuti, Musamakhudza odzozedwa anga, musamachitira choipa aneneri anga. Ndipo anaitana njala igwere dziko; anathyola mchirikizo wonse wa mkate. Anawatsogozeratu munthu; anamgulitsa Yosefe akhale kapolo: Anapweteka miyendo yake ndi matangadza; anamgoneka mu unyolo; kufikira nyengo yakuchitika maneno ake; mau a Yehova anamuyesa. Muimbireni, muimbireni zomlemekeza; fotokozerani zodabwitsa zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:22

Ndipo apereke nsembe zachiyamiko, nafotokozere ntchito zake ndi kufuula mokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 108:1-3

Wakhazikika mtima wanga, Mulungu; ndidzaimba, inde ndidzaimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga. Adzandifikitsa ndani m'mzinda wa m'linga? Adzanditsogolera ndani ku Edomu? Si ndinu Mulungu, amene mwatitaya osatuluka nao magulu athu? Tithandizeni mumsauko; pakuti chipulumutso cha munthu ndi chabe. Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima: Ndipo Iye adzapondereza otisautsa. Galamukani, chisakasa ndi zeze; ndidzauka ndekha mamawa. Ndidzakuyamikani mwa mitundu ya anthu, Yehova: ndipo ndidzaimba zakukulemekezani mwa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 138:1

Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 149:1-2

Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake. Akondwere Israele mwa Iye amene anamlenga; ana a Ziyoni asekere mwa mfumu yao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 150:1-6

Aleluya. Lemekezani Mulungu m'malo ake oyera; mlemekezeni m'thambo la mphamvu yake. Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba; mlemekezeni monga mwa ukulu wake waunjinji. Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga; mlemekezeni ndi chisakasa ndi zeze. Mlemekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang'ombe: Mlemekezeni ndi zoimbira za zingwe ndi chitoliro. Mlemekezeni ndi nsanje zomveka: Mlemekezeni ndi nsanje zoliritsa. Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Aleluya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 12:4-5

Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa. Muimbire Yehova; pakuti wachita zaulemerero; chidziwike ichi m'dziko lonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:3

ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:23

Ndipo kudzakhala kuti kuyambira pa mwezi wokhala kufikira ku unzake, ndi kuyambira pa Sabata lina kufikira kulinzake, anthu onse adzafika kudzapembedzera pamaso pa Ine, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:17

Ndi kuti, Tinakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simunavine; tinabuma maliro, ndipo inu simunalire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:30

Ndipo pamene anaimba nyimbo, anatuluka kunka kuphiri la Azitona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:46-47

Ndipo Maria anati, Moyo wanga ulemekeza Ambuye, ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:22

Odala inu, pamene anthu adzada inu, nadzapatula inu, nadzatonza inu, nadzalitaya dzina lanu monga loipa, chifukwa cha Mwana wa Munthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 4:23-24

Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m'choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake. Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira Iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:46-47

Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi mu Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona; nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:25

Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1

Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:15

Kuli chiyani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi chidziwitso changa; ndidzaimba ndi mzimu, koma ndidzaimbanso ndi chidziwitso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 2:14

Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:15

Ayamikike Mulungu chifukwa cha mphatso yakeyake yosatheka kuneneka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:19

ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:4

Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:16

Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:16

Kondwerani nthawi zonse;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:15

Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:13

Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Aimbire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:1

Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kumlemekeza kwake kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 42:4

Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, pakuti ndinkapita ndi unyinji wa anthu, ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu, ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika, ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 47:6

Imbirani Mulungu, imbirani; imbirani mfumu yathu, imbirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:3

Koma olungama akondwere; atumphe ndi chimwemwe pamaso pa Mulungu; ndipo asekere nacho chikondwerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:23

Milomo yanga idzafuula mokondwera poimbira Inu nyimbo; inde, moyo wanga umene munaombola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:65

Pamenepo Ambuye anauka ngati wam'tulo; ngati chiphona chakuchita nthungululu ndi vinyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 92:1-3

Nkokoma kuyamika Yehova, ndi kuimbira nyimbo dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu. Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati; anandidzoza mafuta atsopano. Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira, m'makutu mwanga ndamva chokhumba ine pa iwo akuchita zoipa akundiukira. Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni. Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova, adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu. Atakalamba adzapatsanso zipatso; adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri, kulalikira kuti Yehova ngwolunjika; Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama. Kuonetsera chifundo chanu mamawa, ndi chikhulupiriko chanu usiku uliwonse. Pa choimbira cha zingwe khumi ndi pachisakasa; pazeze ndi kulira kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 100:4

Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:2

Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:15-16

M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso: Dzanja lamanja la Yehova likwezeka, Dzanja lamanja la Yehova lichita mwamphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 136:1

Yamikani Yehova pakuti ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 149:6-9

Nyimbo zakukweza Mulungu zikhale pakamwa pao, ndi lupanga lakuthwa konsekonse m'dzanja lao; kubwezera chilango akunja, ndi kulanga mitundu ya anthu; kumanga mafumu ao ndi maunyolo, ndi omveka ao ndi majerejede achitsulo, kuwachitira chiweruzo cholembedwacho. Ulemu wa okondedwa ake onse ndi uwu. Aleluya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 150:6

Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Aleluya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 3:4

mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka; mphindi yakulira ndi mphindi yakuvina;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:29

Inu mudzakhala ndi nyimbo, monga usiku, podya phwando lopatulika; ndi mtima wokondwa, monga pomuka wina ndi chitoliro, kufikira kuphiri la Yehova, kuthanthwe la Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:10

Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 6:6-8

Ndidzafika kwa Yehova ndi chinai, ndi kuwerama kwa Mulungu Wam'mwamba? Kodi ndifike kwa Iye ndi nsembe zopsereza, ndi anaang'ombe a chaka chimodzi? Kodi Yehova adzakondwera nazo nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndipereke mwana wanga woyamba chifukwa cha kulakwa kwanga, chipatso cha thupi langa chifukwa cha kuchimwa kwa moyo wanga? Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:15

Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:9

Ndipo onani, Yesu anakomana nao, nanena, Tikuoneni. Ndipo iwo anadza, namgwira Iye mapazi ake, namgwadira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:21

Nthawi yomweyo Iye anakondwera ndi Mzimu Woyera, nati, Ndikuvomerezani Inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda; indedi, Atate, pakuti kotero kudakondweretsa pamaso panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 15:10

Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:24

Kufikira tsopano simunapemphe kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:8

Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda; ndipo analowa pamodzi nao mu Kachisi, nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:10

Ndiponso anena, Kondwani, amitundu inu, pamodzi ndi anthu ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:31

Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 11:23-26

Pakuti ine ndinalandira kwa Ambuye, chimenenso ndinapereka kwa inu, kuti Ambuye Yesu usiku uja anaperekedwa, anatenga mkate; ndipo m'mene adayamika, ananyema, nati, Ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa. Koteronso chikho, chitatha chakudya, ndi kuti, Chikho ichi ndi pangano latsopano m'mwazi wanga; chitani ichi, nthawi zonse mukamwa, chikhale chikumbukiro changa. Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:13-14

Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo. Pakuti mau amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:20

Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:10

kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 1:6

Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m'mene mudalandira mauwo m'chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:7

Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:28-29

Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha. Pakuti Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:3

chimene tidachiona, ndipo tidachimva, tikulalikirani inunso, kuti inunso mukayanjane pamodzi ndi ife; ndipo chiyanjano chathu chilinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wake Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 14:3

ndipo aimba ngati nyimbo yatsopano kumpando wachifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinai, ndi akulu; ndipo palibe munthu anakhoza kuphunzira nyimboyi, koma zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, ogulidwa kuchokera kudziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 19:1-3

Zitatha izi ndinamva ngati mau aakulu a khamu lalikulu mu Mwamba, lili kunena, Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu; Ndipo ndinagwa pa mapazi ake kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero. Ndipo ndinaona mutatseguka mu Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama. Ndipo maso ake ali lawi la moto, ndi pamutu pake pali nduwira zachifumu zambiri; ndipo ali nalo dzina lolembedwa, wosalidziwa wina yense koma Iye yekha. Ndipo avala chovala chowazidwa mwazi; ndipo atchedwa dzina lake, Mau a Mulungu. Ndipo magulu a nkhondo okhala mu Mwamba anamtsata Iye, okwera pa akavalo oyera, ovala bafuta woyera woti mbuu. Ndipo m'kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo: ndipo aponda Iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse. Ndipo ali nalo pa chovala chake ndi pa ntchafu yake dzina lolembedwa, MFUMU YA MAFUMU, NDI MBUYE WA AMBUYE. Ndipo ndinaona mngelo alikuima m'dzuwa; ndipo anafuula ndi mau aakulu akunena ndi mbalame zonse zakuuluka pakati pa mlengalenga: Idzani kuno, sonkhanani kuphwando la Mulungu wamkulu, kuti mudzadye nyama ya mafumu, ndi nyama ya akapitao, ndi nyama ya anthu amphamvu, ndi nyama ya akavalo, ndi ya iwo akukwerapo, ndi nyama ya anthu onse, mfulu ndi akapolo, ndi aang'ono ndi aakulu. Ndipo ndinaona chilombocho, ndi mafumu a dziko, ndi magulu a nkhondo ao, osonkhanidwa kuchita nkhondo pa Iye wakukwera pa kavalo, ndi gulu la nkhondo lake. pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo. Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulufure: ndipo otsalawa anaphedwa ndi lupanga la Iye wakukwera pa kavalo, ndilo lotuluka m'kamwa mwake; ndipo mbalame zonse zinakhuta ndi nyama zao. Ndipo anatinso, Aleluya. Ndipo utsi wake ukwera kunthawi za nthawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:1-2

Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake. Ndizo zifunika koposa golide, inde, golide wambiri woyengetsa; zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake. Ndiponso kapolo wanu achenjezedwa nazo, m'kuzisunga izo muli mphotho yaikulu. Adziwitsa zolowereza zake ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika. Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine. Pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu. Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga. Usana ndi usana uchulukitsa mau, ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 29:2

Perekani kwa Yehova ulemerero wa dzina lake, gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:3

Bukitsani pamodzi ndine ukulu wa Yehova, ndipo tikweze dzina lake pamodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:4

Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 42:1

Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 63:5

Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona; ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakufuula mokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 89:15

Odala anthu odziwa liu la lipenga; ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 108:3

Ndidzakuyamikani mwa mitundu ya anthu, Yehova: ndipo ndidzaimba zakukulemekezani mwa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 116:17

Ndidzapereka kwa Inu nsembe yachiyamiko, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 35:10

ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate Woyera, ndikupempha kuti mulimbitse utumiki uliwonse wa kuvina, kuti kukhalapo kwa Mzimu Woyera wanu kubweretse tsopano ndi mphamvu zatsopano pa moyo wa mtsogoleri aliyense ndi magulu a ovinila. Pakadali pano ndikufuna kukuthokozani chifukwa njira imodzi yomwe ndakhala nayo mwayi wakupembedzani ndi kudzera mu kuvina. Ndimapempha kuti mundithandize kwambiri kukulemeketzani osati kokha kudzera mu utumiki wanga, komanso ndi moyo wanga wonse, ndikusunga ubwenzi wolimba ndi inu momwe kuvina kwanga kumakondweretsa pamaso panu. Mundidziwitse kuti sitepe iliyonse ndiyenera kuitenga ndi dongosolo, ulemu ndi kudzichepetsa kwa mtima, osati kudzitamandira, kupikisana kapena kusangalatsa ena, koma kuwonetsa chikondi, chisomo ndi chifundo chanu m'moyo wanga. M'dzina la Yesu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa