2 Samueli 6:16 - Buku Lopatulika16 Ndipo kunali pamene likasa la Yehova linafika m'mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikuvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Ndipo kunali pamene likasa la Yehova linafika m'mudzi wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikuvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Pamene Bokosi lachipangano linkaloŵa mu mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo adasuzumira pa windo, naona mfumu Davide akulumphalumpha ndi kuvina molemekeza Chauta. Pamenepo mkaziyo adayamba kunyoza Davide mumtima mwake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Bokosi la Yehova likulowa mu Mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli ankaona ali pa zenera. Ndipo ataona Mfumu Davide ikulumpha ndi kuvina pamaso pa Yehova, ankamunyogodola mu mtima mwake. Onani mutuwo |