Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 6:15 - Buku Lopatulika

15 Chomwecho Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anakwera nalo likasa la Yehova, ndi chimwemwe ndi kulira kwa malipenga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Chomwecho Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anakwera nalo likasa la Yehova, ndi chimwemwe ndi kulira kwa malipenga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Choncho iye pamodzi ndi Aisraele onse adabwera ndi Bokosi lachipangano akufuula ndi kuliza mbetete.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 pamene iyeyo pamodzi ndi Aisraeli onse ankabwera ndi Bokosi la Yehova, akufuwula ndi kuyimba malipenga.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 6:15
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anavina ndi mphamvu yake yonse pamaso pa Yehova; Davide nadzimangirira efodi wabafuta.


Ndipo kunali pamene likasa la Yehova linafika m'mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikuvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwake.


Ndipo Davide ananena ndi mkulu wa Alevi kuti aike abale ao oimbawo ndi zoimbira, zisakasa, ndi azeze, ndi nsanje, azimveketse ndi kukweza mau ao ndi chimwemwe.


Momwemo Davide, ndi akuluakulu a Israele, ndi atsogoleri a zikwi, anamuka kukwera nalo likasa la chipangano la Yehova, kuchokera kunyumba ya Obededomu mokondwera.


Momwemo Aisraele onse anakwera nalo likasa la chipangano la Yehova ndi kufuula, ndi kumveka kwa lipenga, ndi mphalasa, ndi nsanje zomveketsa, ndi zisakasa, ndi azeze.


Ndidzawaveka adani ake ndi manyazi; koma pa iyeyu korona wake adzamveka.


Okondedwa ake atumphe mokondwera mu ulemu: Afuule mokondwera pamakama pao.


Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga; mlemekezeni ndi chisakasa ndi zeze.


Ombani m'manja, mitundu yonse ya anthu; fuulirani kwa Mulungu ndi liu la kuimbitsa.


Kalongayo tsono, polowa iwo alowe pakati pao, ndipo potuluka iwo atulukire pamodzi.


koma ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa