Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 68:3 - Buku Lopatulika

3 Koma olungama akondwere; atumphe ndi chimwemwe pamaso pa Mulungu; ndipo asekere nacho chikondwerero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Koma olungama akondwere; atumphe ndi chimwemwe pamaso pa Mulungu; ndipo asekere nacho chikondwerero.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Koma anthu anu Mulungu, akondwere, asangalale pamaso panu, inde, asekere ndi chimwemwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Koma olungama asangalale ndi kukondwera pamaso pa Mulungu; iwo akondwere ndi kusangalala.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 68:3
16 Mawu Ofanana  

Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu; adzakondwera kwakukulu m'chipulumutso chanu!


Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima; ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.


Pakuti oipa adzatayika, ndipo adani ake a Yehova adzanga mafuta a anaankhosa; adzanyeka, monga utsi adzakanganuka.


Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.


Wolungama adzakondwera pakuona kubwezera chilango, adzasamba mapazi ake m'mwazi wa woipa.


Wolungama adzakondwera mwa Yehova, nadzakhulupirira Iye; ndipo oongoka mtima onse adzalemekeza.


Ndinati kwa odzitamandira, musamachita zodzitamandira; ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga;


Kondwerani mwa Yehova, olungama inu; ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake.


Ndipo mudzakondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi ali m'midzi mwanu, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu.


Kondwerani nthawi zonse;


amene mungakhale simunamuone mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero:


Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.


Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa Iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wake wadzikonzera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa