Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 33:1 - Buku Lopatulika

1 Fuulani mokondwera mwa Yehova, inu olungama mtima, oongoka mtima ayenera kulemekeza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Fuulani mokondwera mwa Yehova, inu olungama mtima, oongoka mtima ayenera kulemekeza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Kondwerani mwa Chauta, inu anthu ake. Zoonadi ochita zolungama azitamanda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Imbirani Yehova mokondwera Inu olungama, nʼkoyenera kuti owongoka mtima azitamanda Iyeyo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 33:1
12 Mawu Ofanana  

M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso:


Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino; muimbire zolemekeza dzina lake; pakuti nkokondweretsa kutero.


Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma; pakuti chikondweretsa ichi, chilemekezo chiyenera.


Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima; ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.


Kondwerani mwa Yehova, olungama inu; ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake.


Nsembe ya oipa inyansa Yehova; koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.


monga kwalembedwa, Palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi;


Pakuti monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi ambiri anayesedwa ochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa mmodzi ambiri adzayesedwa olungama.


Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa