Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 33:2 - Buku Lopatulika

2 Yamikani Yehova ndi zeze; muimbireni ndi chisakasa cha zingwe khumi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Yamikani Yehova ndi zeze; muimbireni ndi chisakasa cha zingwe khumi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tamandani Chauta ndi pangwe. Muimbireni nyimbo ndi zeze wa nsambo khumi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mutamandeni Yehova ndi pangwe; muyimbireni Iye nyimbo pa zeze wa zingwe khumi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 33:2
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anasewera pamaso pa Yehova, ndi zoimbira za mitundumitundu za mlombwa, ndi azeze, ndi zisakasa ndi malingaka, ndi maseche, ndi nsanje.


Ndipo Davide ananena ndi mkulu wa Alevi kuti aike abale ao oimbawo ndi zoimbira, zisakasa, ndi azeze, ndi nsanje, azimveketse ndi kukweza mau ao ndi chimwemwe.


Momwemo Aisraele onse anakwera nalo likasa la chipangano la Yehova ndi kufuula, ndi kumveka kwa lipenga, ndi mphalasa, ndi nsanje zomveketsa, ndi zisakasa, ndi azeze.


A Yedutuni, ana a Yedutuni: Gedaliya, ndi Zeri, ndi Yesaya, Hasabiya, ndi Matitiya, asanu ndi mmodzi; mwa chilangizo cha atate wao Yedutuni, ndiye wakunenera ndi kuyamika ndi kulemekeza Yehova ndi zeze.


Onsewa anawalangiza ndi atate wao aimbe m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, zisakasa ndi azeze; atumikire nazo m'nyumba ya Mulungu; ndipo Asafu, Yedutuni, ndi Hemani, anawalangiza ndi mfumu.


Ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano, Mulungu; pa chisakasa cha zingwe khumi ndidzaimbira zakukulemekezani.


Alemekeze dzina lake ndi kuthira mang'ombe; amuimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze.


Ndiponso ndidzakuyamikani ndi chisakasa, kubukitsa choonadi chanu, Mulungu wanga; ndidzakuimbirani nyimbo ndi zeze, ndinu Woyerayo wa Israele.


Pa choimbira cha zingwe khumi ndi pachisakasa; pazeze ndi kulira kwake.


Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kuchita kwanu, ndidzafuula mokondwera pa ntchito ya manja anu.


Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.


Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndi ngati mau a bingu lalikulu; ndipo mau amene ndinawamva anakhala ngati a azeze akuimba azeze ao;


Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse zili nao azeze, ndi mbale zagolide zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa