Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 33:3 - Buku Lopatulika

3 Mumuimbire Iye nyimbo yatsopano; muimbe mwaluso kumveketsa mau.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Mumuimbire Iye nyimbo yatsopano; muimbe mwaluso kumveketsa mau.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Muimbireni nyimbo yatsopano, kodolani nsambozo mwaluso ndi kufuula mosangalala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Muyimbireni nyimbo yatsopano; imbani mwaluso, ndipo fuwulani mwachimwemwe.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 33:3
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ndi Aisraele onse anasewera pamaso pa Mulungu ndi mphamvu yao yonse; ndi nyimbo, ndi azeze, ndi zisakasa, ndi malingaka, ndi nsanje, ndi malipenga.


Ndi Kenaniya mkulu wa Alevi anayang'anira kusenzako; anawalangiza za kusenza, pakuti anali waluso.


Ndipo chiwerengo chao, pamodzi ndi abale ao ophunzitsidwa aimbire Yehova, onse anthetemya, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu.


Ndipo amunawo anachita ntchitoyi mokhulupirika; ndi oikidwa awayang'anire ndiwo Yahati ndi Obadiya, Alevi, a ana a Merari; ndi Zekariya ndi Mesulamu, a ana a Akohati, kuifulumiza; ndi Alevi ena aliyense waluso la zoimbira.


Ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano, Mulungu; pa chisakasa cha zingwe khumi ndidzaimbira zakukulemekezani.


Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake.


Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.


Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika; wosasamala odzikuza, ndi opatukira kubodza.


Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; muimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi.


Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; popeza anachita zodabwitsa: Dzanja lake lamanja, mkono wake woyera, zinamchitira chipulumutso.


Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse zili m'menemo, zisumbu ndi okhala mommo.


ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu;


Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.


ndipo aimba ngati nyimbo yatsopano kumpando wachifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinai, ndi akulu; ndipo palibe munthu anakhoza kuphunzira nyimboyi, koma zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, ogulidwa kuchokera kudziko.


Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa