Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Timoteyo 3:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Woyang'anira Mpingo azikhala munthu wopanda chokayikitsa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, akhale wodzigwira, wa maganizo anzeru, waulemu, wosamala bwino alendo, ndi wotha kuphunzitsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Tsono woyangʼanira ayenera kukhala munthu wopanda chotsutsika nacho, mwamuna wa mkazi mmodzi yekha, woganiza bwino, wodziretsa, waulemu, wosamala bwino alendo, wodziwa kuphunzitsa.

Onani mutuwo Koperani




1 Timoteyo 3:2
20 Mawu Ofanana  

Alonda ake ali akhungu, iwo onse ali opanda nzeru; iwo onse ali agalu achete, osatha kuuwa; kungolota, kugona pansi, kukonda kugona tulo.


Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.


Ndipo panali Anna, mneneri wamkazi, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wake, kuyambira pa unamwali wake,


Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo.


kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,


Atumiki akhale mwamuna wa mkazi mmodzi, akuweruza bwino ana ao, ndi iwo a m'nyumba yao ya iwo okha.


Momwemonso atumiki akhale olemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, osati a chisiriro chonyansa;


a kuletsa ukwati, osiyitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira choonadi azilandire ndi chiyamiko.


wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.


Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.


Asawerengedwe wamasiye ngati sanafikire zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wa mwamuna mmodzi,


Ndipo kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndeu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziwa kuphunzitsa, woleza,


okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama m'chikhulupiriro, m'chikondi, m'chipiriro.


Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziwa.


pakuti takhala ife olandirana ndi Khristu, ngatitu tigwiritsa chiyambi cha kutama kwathu kuchigwira kufikira chitsiriziro;


Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;


mucherezane wina ndi mnzake, osadandaula:


Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa