Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, Yesu ndiye chitsanzo chathu tonse. Iye anali ndi mphamvu, nzeru, ndi masomphenya ochulukirapo kuposa wina aliyense. Koma chodabwitsa n’chakuti utumiki wake unali wodzichepetsa, wodzipereka, wachikondi, komanso wopatsa chiyembekezo kwa ena.
Ziweruzo zake zinali zolimbikitsa komanso zotsutsa maganizo athu, koma nthawi yomweyo zinkatonthoza ndi kutitsutsa kuti tisinthe makhalidwe athu. M’mabuku a Uthenga Wabwino muli nkhani zambiri zosonyeza utsogoleri wa Yesu kwa anthu ndi ophunzira ake.
Inu mtsogoleri amene mukuwerenga mawu awa, ndikufuna ndikuuzeni kuti chitsanzo chabwino kwambiri chimene mungatsatire ndi Yesu. Lolani Iye akuphunzitseni njira zake, atsogolere mapazi anu, ndipo mudzasiya chizindikiro chabwino m'miyoyo ya anthu amene akuzungulirani.
Njira ya Yesu ndiyo yabwino koposa. Choncho, tisiyeni tidzichepetse, titsatire mapazi a Mphunzitsi wa aphunzitsi, munthu wanzeru woposa onse amene anakhalapo padziko lapansi. Iye ndi wokonzeka kukutsogolerani kuti mupite patsogolo pa chilichonse chimene mungachite.
Mwa Iye, timapeza utsogoleri wabwino, dongosolo, nzeru, mgwirizano, mphamvu, ndi masomphenya. Mulungu akudalitseni.
Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.
Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma aliyense amene akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu;
Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna anzeru, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makumi;
Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;
Chotero munthu atiyese ife, monga atumiki a Khristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu.
Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.
Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.
Chifukwa chake, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake.
Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Khristu Yesu, ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanachiyese cholanda kukhala wofana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m'mafanizidwe a anthu;
Pakuti ndithu, Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la kwa anthu ambiri.
Kunyada kutsogolera kuonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kuphunthwa. Kufatsa mtima ndi osauka kuposa kugawana zofunkha ndi onyada.
Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake? Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu achabe.
Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.
Koma Yesu anawaitana, nati, Mudziwa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye ao, ndipo akulu ao amachita ufumu pa iwo. Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma aliyense amene akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo aliyense amene akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu: monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.
Koma wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu. Ndipo aliyense amene akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.
Koma mwa inu sikutero ai; koma aliyense amene afuna kukhala wamkulu mwa inu adzakhala mtumiki wanu; ndipo aliyense amene afuna kukhala woyamba mwa inu adzakhala kapolo wa onse. Pakuti ndithu, Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la kwa anthu ambiri.
Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkulu mwa inu, akhale ngati wamng'ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira. Pakuti wamkulu ndani, iye wakuseama pachakudya kapena wakutumikirapo? Si ndiye wakuseama pachakudya kodi? Koma Ine ndili pakati pa inu monga ngati wotumikira.
Pamenepo, atatha Iye kusambitsa mapazi ao, ndi kutenga malaya ake, anaseamanso, nati kwa iwo, Nanga chimene ndakuchitirani inu, muchizindikira kodi? Inu munditcha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene. Chifukwa chake, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake. Pakuti ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite.
kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira achite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi changu; iye wakuchita chifundo, achite ndi kukondwa mtima.
Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.
Koma inu ndinu thupi la Khristu, ndi ziwalo, yense pa yekha. Ndipotu Mulungu anaika ena mu Mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu.
Si kuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.
Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu;
musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini; pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine. munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.
chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai; podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo.
Koma, abale, tikupemphani, dziwani iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu; ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha.
Mauwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang'anira, aifuna ntchito yabwino. Koma iwonso ayamba ayesedwe; pamenepo atumikire, akakhala opanda chifukwa. Momwemonso akazi akhale olemekezeka, osadierekeza, odzisunga, okhulupirika m'zonse. Atumiki akhale mwamuna wa mkazi mmodzi, akuweruza bwino ana ao, ndi iwo a m'nyumba yao ya iwo okha. Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukulu m'chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu. Izi ndikulembera ndi kuyembekeza kudza kwa iwe posachedwa, koma ngati ndichedwa, kuti udziwe kuyenedwa kwake pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi. Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero. Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa; wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba chuma; woweruza bwino nyumba yake ya iye yekha, wakukhala nao ana ake omvera iye ndi kulemekezeka konse. Koma ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanji Mpingo wa Mulungu? Asakhale wophunza, kuti podzitukumula ungamgwere mlandu wa mdierekezi. Kuyeneranso kuti iwo akunja adzakhoza kumchitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa mdierekezi.
Akulu akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akuchititsa m'mau ndi m'chiphunzitso.
Chifukwa cha ichi ndinakusiya iwe mu Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akulu m'midzi yonse, monga ndinakulamulira; ngati wina ali wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nao ana okhulupirira, wosasakaza zake, kapena wosakana kumvera mau. Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati wachiwawa, wopanda ndeu, wosati wa chisiriro chonyansa; komatu wokonda kuchereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa; wogwira mau okhulupirika monga mwa chiphunzitso, kuti akakhoze kuchenjeza m'chiphunzitso cholamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye.
Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.
Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mnzanu ndi mboni ya zowawa za Khristu, ndinenso wolawana nao ulemerero udzavumbulutsikawo: Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu. Kwa Iye kukhale mphamvu kunthawi za nthawi. Amen. Mwa Silivano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwachidule, ndi kudandaulira, ndi kuchita umboni, kuti chisomo choona cha Mulungu ndi ichi; m'chimenechi muimemo. Iye wa ku Babiloni wosankhidwa pamodzi nanu akukupatsani moni; ateronso Marko mwana wanga. Mupatsane moni ndi kupsompsonana kwa chikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse muli mwa Khristu. Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo. Ndipo pakuonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota.
Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.
Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kuchidikha.
Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ake; chifukwa mu Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera mu Yerusalemu.
Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mzinda wokhazikika pamwamba paphiri sungathe kubisika. Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo. Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.
Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwe; chifukwa inakhazikika pathanthwepo. Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.
Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.
Ndiponso ndinena kwa inu kuti ngati awiri a inu avomerezana pansi pano chinthu chilichonse akachipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawachitira. Ndipo pamene Yesu anaitana kamwana, anakaimitsa pakati pao, Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.
Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi. Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake. ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
Ndipo kunali masiku awa, Iye anatuluka nanka kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu. Ndipo kutacha, anaitana ophunzira ake; nasankha mwa iwo khumi ndi awiri, amene anawatchanso dzina lao atumwi:
Ine ndiye Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira Ine, monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa.
Chifukwa chake, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi. Koma ife tidzalimbika m'kupemphera, ndi kutumikira mau.
Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako. ndipo zitatha izi anawapatsa oweruza kufikira Samuele mneneriyo. Ndipo kuyambira pamenepo anapempha mfumu; ndipo Mulungu anawapatsa Saulo mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, zaka makumi anai. Ndipo m'mene atamchotsa iye, anawautsira Davide akhale mfumu yao; amenenso anamchitira umboni, nati, Ndapeza Davide, mwana wa Yese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse. Wochokera mu mbeu yake Mulungu, monga mwa lonjezano, anautsira Israele Mpulumutsi, Yesu; Yohane atalalikiratu, asanafike Iye, ubatizo wa kulapa kwa anthu onse a Israele. Ndipo pakukwaniritsa njira yake Yohane, ananena, Muyesa kuti ine ndine yani? Ine sindine Iye. Koma taonani, akudza wina wonditsata ine, amene sindiyenera kummasulira nsapato za pa mapazi ake. Amuna, abale, ana a mbadwa ya Abrahamu, ndi iwo mwa inu akuopa Mulungu, kwa ife atumidwa mau a chipulumutso ichi. Pakuti iwo akukhala mu Yerusalemu, ndi akulu ao, popeza sanamzindikire Iye, ngakhale mau a aneneri owerengedwa masabata onse, anawakwaniritsa pakumtsutsa. Ndipo ngakhale sanapeze chifukwa cha kumphera, anapempha Pilato kuti aphedwe. Ndipo atatsiriza zonse zolembedwa za Iye, anamtsitsa kumtengo, namuika m'manda. Pamenepo, m'mene adasala chakudya ndi kupemphera ndi kuika manja pa iwo, anawatumiza amuke.
Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha.
Pakuti ndilakalaka kuonana ndinu, kuti ndikagawire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike; ndiko, kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse awiri, chanu ndi changa.
Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzake.
Chotero munthu atiyese ife, monga atumiki a Khristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu. Tili opusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tili ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka. Kufikira nthawi yomwe ino timva njala, timva ludzu, tili amaliseche, tikhomedwa, tilibe pokhazikika; ndipo tigwiritsa ntchito, ndi kuchita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira; ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano. Sindilembera izi kukuchititsani manyazi, koma kuchenjeza inu monga ana anga okondedwa. Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Khristu Yesu ine ndinabala inu mwa Uthenga Wabwino. Chifukwa chake ndikupemphani, khalani akutsanza ine. Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Khristu, monga ndiphunzitsa ponsepo mu Mipingo yonse. Koma ena adzitukumula, monga ngati sindinalinkudza kwa inu. Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi. Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.
Chifukwa chake tili atumiki m'malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m'malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.
Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.
Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani; ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse; pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi. Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse chakuonetsa chili kuunika. Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe. Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa. Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani. Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu, ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu; ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.
Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino;
amene timlalikira ife, ndi kuchenjeza munthu aliyense ndi kuphunzitsa munthu aliyense mu nzeru zonse, kuti tionetsere munthu aliyense wamphumphu mwa Khristu;
monga mudziwa kuti tinachitira yense wa inu pa yekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha, ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kuchita umboni, kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wake wa Iye yekha, ndi ulemerero.
Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti mubwevuke kwa mbale yense wakuyenda dwakedwake, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.
Lamulo ili ndipereka kwa iwe, mwana wanga Timoteo, kuti, monga mwa zonenera zidakutsogolera iwe kale, ulimbane nayo nkhondo yabwino;
Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso. Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.
m'zonse udzionetsere wekha chitsanzo cha ntchito zabwino; m'chiphunzitso chako uonetsere chosavunda, ulemekezeko, mau olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana achite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife.
kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.
Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;
Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Khristu anamva zowawa m'malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake;
Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.
Umo tizindikira chikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.
Mbadwo wina udzalemekezera ntchito zanu mbadwo unzake, ndipo udzalalikira zamphamvu zanu. Ndidzalingalira ulemerero waukulu wa ulemu wanu, ndi ntchito zanu zodabwitsa.
ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.
Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza. Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mau ako, ndipo ndi mau ako omwe udzatsutsidwa.
Koma iye amene sanachidziwe, ndipo anazichita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang'ono. Ndipo kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.
Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi mu Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona; nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa. Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa. Koma wookayo ndi wothirirayo ali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha. Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu.
amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano; si la chilembo, koma la mzimu; pakuti chilembo chipha, koma mzimu uchititsa moyo.
kuchokera mwa Iye thupi lonse, lolukidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi.
Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira;
Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima. Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.
Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.
Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino;
Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mau a Mulungu; ndipo poyang'anira chitsiriziro cha mayendedwe ao mutsanze chikhulupiriro chao.
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.