Yesaya 2:3 - Buku Lopatulika3 Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ake; chifukwa mu Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera mu Yerusalemu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ake; chifukwa m'Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera m'Yerusalemu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Anthu a mitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda m'njira zakezo.” Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Anthu ambiri adzabwera ndikunena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.” Malangizo adzachokera ku Ziyoni, mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu. Onani mutuwo |
Ndipo iwo adzatenga abale anu onse mwa amitundu onse akhale nsembe ya kwa Yehova; adzabwera nao pa akavalo, ndi m'magaleta, ndi m'machila, ndi pa nyuru, ndi pa ngamira, kudza kuphiri langa lopatulika ku Yerusalemu, ati Yehova, monga ana a Israele abwera nazo nsembe zao m'chotengera chokonzeka kunyumba ya Yehova.