Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Tito 1:7 - Buku Lopatulika

7 Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati wachiwawa, wopanda ndeu, wosati wa chisiriro chonyansa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati wachiwawa, wopanda ndeu, wosati wa chisiriro chonyansa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Woyang'anira mpingo azikhala wosapalamula konse, chifukwa ali ngati kapitao m'banja la Mulungu. Asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena chidakwa, kapena wandeu, kapenanso wokonda kudya phindu la ndalama.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Popeza mkulu wa mpingo amayendetsa ntchito za banja la Mulungu, ayenera kukhala wopanda cholakwa, asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena womwa zoledzeretsa, kapena wandewu, kapena wopeza phindu mwachinyengo.

Onani mutuwo Koperani




Tito 1:7
23 Mawu Ofanana  

Mtima wangawe, usalowe mu chiungwe chao; ulemerero wanga, usadziphatike pa msonkhano yao; chifukwa m'kukwiya kwao anapha munthu. M'kufuna kwao anapundula ng'ombe.


Wokangaza kukwiya adzachita utsiru; ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa.


Munthu wozaza aputa makani; koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.


Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mzinda.


Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m'chifuwa cha zitsiru.


Koma iwonso adzandima ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi chakumwa chaukali, iwo amezedwa ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, adzandima popenya, naphunthwa poweruza.


Kungakhale kumwa vinyo, wansembe asamwe polowa kubwalo la m'katimo.


Usamamwa vinyo, kapena choledzeretsa, iwe ndi ana ako omwe, m'mene mulowa m'chihema chokomanako, kuti mungafe; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu;


Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang'anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake?


Ndipo Ambuye anati, Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adzamuika kapitao wa pa banja lake, kuwapatsa iwo phoso lao pa nthawi yake?


Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu,


Paulo ndi Timoteo, akapolo a Yesu Khristu, kwa oyera mtima onse mwa Khristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang'anira ndi atumiki:


Chifukwa cha ichi ndinakusiya iwe mu Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akulu m'midzi yonse, monga ndinakulamulira;


Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma;


monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;


Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;


koma makamaka iwo akutsata za thupi, m'chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemerero;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa