Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


110 Mau a m'Baibulo Okhudza Atsogoleri Auzimu

110 Mau a m'Baibulo Okhudza Atsogoleri Auzimu

Mwina mukumva nkhani za atsogoleri amphamvu ndi odzozedwa m'Baibulo, koma chochititsa chidwi kwambiri ndi mtima wawo wowongoka komanso wodzichepetsa. Mulungu sakuona kuchuluka kwa ntchito zomwe timachita m'dzina lake, koma mtima wathu womwe timachitira zimenezo. Masiku ano, Mulungu akufuna atsogoleri okhulupirika, osunga mawu ake, ndi owopa kumupsetsa mtima chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa ife.

Ngakhale Mulungu ankadziwa kuti tidzalakwitsa, Iye anatipatsa madalitso chifukwa cha ntchito zathu ndi kumvera kwathu. Anatisankha chifukwa cha mitima yathu yoyera. Mu mipingo yathu ndi m'nyumba mwathu, muli atsogoleri achikhristu ambiri oyenera kulimbikitsidwa ndi kupempherera.

Apa pansi pali mavesi a m'Baibulo oti muwalemekeze chifukwa cha utumiki wawo wabwino. [mwina apa ndi pomati muyike mavesiwo]




Yesaya 52:7

Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5

Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:2

ndipo madalitso awa onse adzakugwerani, ndi kukupezani, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:30

Iyeyo ayenera kukula koma ine ndichepe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 6:24-26

Yehova akudalitse iwe, nakusunge; Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo; Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 27:16-17

Yehova, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, aike munthu pa khamulo, wakutuluka pamaso pao, ndi kulowa pamaso pao, wakuwatulutsa ndi kuwalowetsa; kuti khamu la Yehova lisakhale ngati nkhosa zopanda mbusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 20:26

Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma aliyense amene akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 5:4

Ndipo palibe munthu adzitengera ulemuwo mwini wake, komatu iye amene aitanidwa ndi Mulungu, monga momwenso Aroni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zefaniya 3:17

Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 1:13

Dzifunireni amuna anzeru, ndi ozindikira bwino, ndi odziwika mwa mafuko anu, ndipo ndidzawaika akhale akulu anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:33

Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:72

Potero anawaweta monga mwa mtima wake wangwiro; nawatsogolera ndi luso la manja ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:12

Kuchita mphulupulu kunyansa mafumu; pakuti mpando wao wakhazikika ndi chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:14

Popanda upo wanzeru anthu amagwa; koma pochuluka aphungu pali chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 6:3

Chifukwa chake, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 18:21

Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna anzeru, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makumi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:2

Pochuluka olungama anthu akondwa; koma polamulira woipa anthu ausa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:6-7

Ndipo mau awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 17:18-20

Ndipo kudzali, pakukhala iye pa mpando wachifumu wa ufumu wake, adzilemberere chofanana cha chilamulo ichi m'buku, achitenge pa ichi chili pamaso pa ansembe Alevi; ndipo azikhala nacho, nawerengemo masiku onse a moyo wake; kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake, kusunga mau onse a chilamulo ichi ndi malemba awa, kuwachita; Akapeza pakati panu, m'mudzi wanu wina umene anakupatsani Yehova Mulungu wanu, wamwamuna kapena wamkazi wakuchita chili choipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kulakwira chipangano chake, kuti mtima wake usadzikuze pa abale ake, ndi kuti asapatukire lamulolo, kulamanja kapena kulamanzere; kuti achuluke masiku ake, mu ufumu wake, iye ndi ana ake pakati pa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:15

Njira ya chitsiru njolungama pamaso pakepake; koma wanzeru amamvera uphungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:9

Mtima wa munthu ulingalira njira yake; koma Yehova ayendetsa mapazi ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:28

Chifundo ndi ntheradi zisunga mfumu; chifundo chichirikiza mpando wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:11

Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:14-16

Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mzinda wokhazikika pamwamba paphiri sungathe kubisika. Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo. Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 20:26-28

Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma aliyense amene akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo aliyense amene akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu: monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:11-12

Koma wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu. Ndipo aliyense amene akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 10:43-45

Koma mwa inu sikutero ai; koma aliyense amene afuna kukhala wamkulu mwa inu adzakhala mtumiki wanu; ndipo aliyense amene afuna kukhala woyamba mwa inu adzakhala kapolo wa onse. Pakuti ndithu, Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la kwa anthu ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:40

Wophunzira saposa mphunzitsi wake; koma yense, m'mene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:42-43

Ndipo Ambuye anati, Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adzamuika kapitao wa pa banja lake, kuwapatsa iwo phoso lao pa nthawi yake? Wodala kapoloyo amene mbuye wake pakufika, adzampeza alikuchita chotero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 13:12-15

Pamenepo, atatha Iye kusambitsa mapazi ao, ndi kutenga malaya ake, anaseamanso, nati kwa iwo, Nanga chimene ndakuchitirani inu, muchizindikira kodi? Inu munditcha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene. Chifukwa chake, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake. Pakuti ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:8

kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira achite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi changu; iye wakuchita chifundo, achite ndi kukondwa mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:14

Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:1-2

Chotero munthu atiyese ife, monga atumiki a Khristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu. Tili opusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tili ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka. Kufikira nthawi yomwe ino timva njala, timva ludzu, tili amaliseche, tikhomedwa, tilibe pokhazikika; ndipo tigwiritsa ntchito, ndi kuchita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira; ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano. Sindilembera izi kukuchititsani manyazi, koma kuchenjeza inu monga ana anga okondedwa. Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Khristu Yesu ine ndinabala inu mwa Uthenga Wabwino. Chifukwa chake ndikupemphani, khalani akutsanza ine. Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Khristu, monga ndiphunzitsa ponsepo mu Mipingo yonse. Koma ena adzitukumula, monga ngati sindinalinkudza kwa inu. Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi. Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 11:1

Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:20

Chifukwa chake tili atumiki m'malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m'malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 1:10

Pakuti kodi ndikopa anthu tsopano, kapena Mulungu? Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Ndikadakhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala kapolo wa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:11-12

Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:27-28

Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino; osaopa adani m'kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chionongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:12-14

Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:12-13

Koma, abale, tikupemphani, dziwani iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu; ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 3:1-7

Mauwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang'anira, aifuna ntchito yabwino. Koma iwonso ayamba ayesedwe; pamenepo atumikire, akakhala opanda chifukwa. Momwemonso akazi akhale olemekezeka, osadierekeza, odzisunga, okhulupirika m'zonse. Atumiki akhale mwamuna wa mkazi mmodzi, akuweruza bwino ana ao, ndi iwo a m'nyumba yao ya iwo okha. Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukulu m'chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu. Izi ndikulembera ndi kuyembekeza kudza kwa iwe posachedwa, koma ngati ndichedwa, kuti udziwe kuyenedwa kwake pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi. Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero. Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa; wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba chuma; woweruza bwino nyumba yake ya iye yekha, wakukhala nao ana ake omvera iye ndi kulemekezeka konse. Koma ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanji Mpingo wa Mulungu? Asakhale wophunza, kuti podzitukumula ungamgwere mlandu wa mdierekezi. Kuyeneranso kuti iwo akunja adzakhoza kumchitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa mdierekezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:17

Akulu akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akuchititsa m'mau ndi m'chiphunzitso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:2

Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:7

Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mau a Mulungu; ndipo poyang'anira chitsiriziro cha mayendedwe ao mutsanze chikhulupiriro chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:17

Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:1

Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziwa kuti tidzalangika koposa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:1-4

Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mnzanu ndi mboni ya zowawa za Khristu, ndinenso wolawana nao ulemerero udzavumbulutsikawo: Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu. Kwa Iye kukhale mphamvu kunthawi za nthawi. Amen. Mwa Silivano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwachidule, ndi kudandaulira, ndi kuchita umboni, kuti chisomo choona cha Mulungu ndi ichi; m'chimenechi muimemo. Iye wa ku Babiloni wosankhidwa pamodzi nanu akukupatsani moni; ateronso Marko mwana wanga. Mupatsane moni ndi kupsompsonana kwa chikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse muli mwa Khristu. Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo. Ndipo pakuonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:66

Mundiphunzitse chisiyanitso ndi nzeru; pakuti ndinakhulupirira malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 143:10

Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kuchidikha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:3

Pereka zochita zako kwa Yehova, ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:1

Wopanduka afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:6

Pakuti udzaponya nkhondo yako ndi upo, ndi kupulumuka pochuluka aphungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:3

Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ake; chifukwa mu Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera mu Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:1

Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:36

Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:1

Ndipo pamene Iye anadziitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuitulutsa, ndi yakuchiza nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:18

Taona mnyamata wanga, amene ndinamsankha, wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; pa Iye ndidzaika Mzimu wanga, ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa akunja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:19-20

Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake. ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:18

Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 6:3-4

Chifukwa chake, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi. Koma ife tidzalimbika m'kupemphera, ndi kutumikira mau.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 20:28

Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:11-12

Pakuti ndilakalaka kuonana ndinu, kuti ndikagawire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike; ndiko, kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse awiri, chanu ndi changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:3

Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:5-9

Ndipo Apolo nchiyani, ndi Paulo nchiyani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anampatsa. Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa. Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa. Koma wookayo ndi wothirirayo ali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha. Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:27-28

Koma inu ndinu thupi la Khristu, ndi ziwalo, yense pa yekha. Ndipotu Mulungu anaika ena mu Mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:24

Si kuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:1

Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:15-16

koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu; kuchokera mwa Iye thupi lonse, lolukidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:3-4

musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini; pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine. munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:28-29

amene timlalikira ife, ndi kuchenjeza munthu aliyense ndi kuphunzitsa munthu aliyense mu nzeru zonse, kuti tionetsere munthu aliyense wamphumphu mwa Khristu; kuchita ichi ndidzivutitsa ndi kuyesetsa monga mwa machitidwe ake akuchita mwa ine ndi mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 2:7-8

Komatu tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga m'mene mlezi afukata ana ake a iye yekha; kotero ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:18

Lamulo ili ndipereka kwa iwe, mwana wanga Timoteo, kuti, monga mwa zonenera zidakutsogolera iwe kale, ulimbane nayo nkhondo yabwino;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:12-16

Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m'mau, m'mayendedwe, m'chikondi, m'chikhulupiriro, m'kuyera mtima. Kufikira ndidza ine, usamalire kuwerenga, kuchenjeza, kulangiza. Usanyalapse mphatsoyo ili mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa chinenero, pamodzi ndi kuika kwa manja a akulu. Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse. Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 1:5-9

Chifukwa cha ichi ndinakusiya iwe mu Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akulu m'midzi yonse, monga ndinakulamulira; ngati wina ali wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nao ana okhulupirira, wosasakaza zake, kapena wosakana kumvera mau. Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati wachiwawa, wopanda ndeu, wosati wa chisiriro chonyansa; komatu wokonda kuchereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa; wogwira mau okhulupirika monga mwa chiphunzitso, kuti akakhoze kuchenjeza m'chiphunzitso cholamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:1-2

Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa chiyero chake. Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo. Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka; ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m'njira, koma chichiritsidwe. Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye: ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao; kuti pangakhale wachigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wake wobadwa nao mtanda umodzi wa chakudya. Pakuti mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeze malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi. Pakuti simunayandikire phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe, ndi mau a lipenga, ndi manenedwe a mau, manenedwe amene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau; Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:2

Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:5

Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:7

koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 32:8

Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:23-24

Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu; ndipo akondwera nayo njira yake. Angakhale akagwa, satayikiratu, pakuti Yehova agwira dzanja lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:3

Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:12

Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu; ndipo mzimu wakulola undigwirizize.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:11

Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m'choonadi chanu, muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:22

Kodi oganizira zoipa sasochera? Koma akuganizira zabwino adzalandira chifundo ndi ntheradi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:12

Mkulu akamvera chinyengo, atumiki ake onse ali oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:20-21

Ndipo ngakhale Ambuye adzakupatsani inu chakudya cha nsautso, ndi madzi a chipsinjo, koma aphunzitsi ako sadzabisikanso, koma maso ako adzaona aphunzitsi ako; ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 48:17

Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israele, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m'njira yoyenera iwe kupitamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:16

Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:19-20

Ndiponso ndinena kwa inu kuti ngati awiri a inu avomerezana pansi pano chinthu chilichonse akachipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawachitira. Ndipo pamene Yesu anaitana kamwana, anakaimitsa pakati pao, Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:20

ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:16

Iye wakumvera inu, andimvera Ine; ndipo iye wakukana inu, andikana Ine; ndipo iye wakukana Ine amkana Iye amene anandituma Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:16

Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:6-8

Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa chisomo chipatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa chikhulupiriro; kapena yakutumikira, tidzipereke ku utumiki uwu; kapena iye wakuphunzitsa, kukuphunzitsako; kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira achite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi changu; iye wakuchita chifundo, achite ndi kukondwa mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:12-13

Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonso Khristu. Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:5

Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Yesu Khristu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu, chifukwa cha Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:3-5

Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse; ndi kukhala nacho inu chilimbano chomwechi mudachiona mwa ine, nimukumva tsopano chili mwa ine. nthawi zonse m'pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndichita pembedzerolo ndi kukondwera, chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 4:5

Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthawi ingatayike.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 1:3

ndi kukumbukira kosalekeza ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi chikondi chochitachita, ndi chipiriro cha chiyembekezo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:11-12

Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso. Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:7

m'zonse udzionetsere wekha chitsanzo cha ntchito zabwino; m'chiphunzitso chako uonetsere chosavunda, ulemekezeko,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:10

pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:5

Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:27

Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:5

Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:11

Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:19

Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga, Wamuyaya, Wapamwamba! Ndikukutamandani chifukwa ndinu Wolungama, Woyera, woyenera kutamandidwa ndi kupembedzedwa konse. Atate, ndikupemphani kuti mulimbitse atsogoleri, dalitsani miyoyo yawo aliyense pa nthawi yovuta ino kuti akhale ndi nzeru zakumwamba popanga chisankho chilichonse ndi kutsogolera onse omwe ali pafupi nawo. Ndikupempha kuti chofunika kwambiri pa miyoyo yawo chikhale kusonyeza chikondi ndi kutumikira anzawo, osafuna zabwino zawo okha, koma za ena. Mzimu Woyera, awathandizeni kuti nthawi zonse akhale ndi mtima wodzichepetsa komanso wodzipereka kwa akuluakulu awo a muutumiki, kuti akhale olimba mtima, okonzeka kumenya nkhondo, kugonjetsa zovuta, ndi kumenyana nkhondo. Atate, chilichonse chomwe achita, achite ndi mtima wonse ngati akuchitira Inu, osati anthu, chifukwa ndinu amene mumathokoza. Ambuye, ndikulengeza utsogoleri wodzala ndi inu ndipo mawu anu akhale ochuluka m'mitima yawo, kuti amvetsetse kuti utsogoleri siudindo kapena maudindo apamwamba, koma ndi utumiki ndi kudzipereka kwa anthu. Monga mwanenera m'mawu anu: "Pakati panu sizikhala choncho, koma aliyense amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu adzakhala mtumiki wanu." Ndikupempha kuti muteteze miyoyo ya atsogoleri aliyense ndi mabanja awo ku ziwembu zonse za mdani. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa