Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, kutamanda Mulungu kumatanthauza kuvomereza zabwino zonse zimene Mulungu watichitira. Timamuyamika chifukwa cha mphamvu zake zopambana zonse ndipo nthawi zonse timakweza dzina lake.
Ngati tili mu utumiki wotamanda Mulungu, tiyenera kukhala pa ubwenzi ndi Mzimu Woyera nthawi zonse. Chifukwa kudzera mu ubwenzi ndi Iye, timadziwa bwino Mulungu m'miyoyo yathu. Timam'tamanda chifukwa cha zimene tazidziwa tokha, osati zimene tamva kwa ena. Umu ndi momwe timatamanditsira Mulungu Wamuyaya ndikutsogolera anthu kuti amulemekeze ndi kumukweza.
Mwayi wotamanda Mulungu si wa aliyense. Choncho, ndikofunikira kusunga mitima yathu yoyera ndi kupita pamaso pa Mulungu opanda chilema. Tisachite chilichonse chomwe chingatichititse manyazi. Tiyenera kuyamikira mwayi wotumikira Mulungu ndi kumupatsa ulemerero nthawi zonse. Tiyenera kulola kuti nyimbo zatsopano zotamanda Yesu zizituluka m'kamwa mwathu.
Komanso, tiyenera kukumbukira kuti monga atumiki, tiyenera kutetezerana ndikudikirirana kuti mdani asatiipitse. Tiyenera kuyang'ana pa zinthu zoyera, zabwino, ndi zolungama. Monga thupi limodzi, cholinga chathu chikhale choti dzina la Mulungu litamandike pakati pa anthu amoyo.
Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.
Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu, zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye.
Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake.
Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.
kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.
Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.
Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe, kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu; ndidzakulemekezani kosalekeza.
Ndidzayamika Yehova ndi mtima wanga wonse; ndidzawerengera zodabwitsa zanu zonse. ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu; pakuti, Inu Yehova, simunawasiye iwo akufuna Inu. Imbirani zoyamika Yehova, wokhala ku Ziyoni; lalikirani mwa anthu ntchito zake. Pakuti Iye wofuna chamwazi awakumbukira; saiwala kulira kwa ozunzika. Ndichitireni chifundo, Yehova; penyani kuzunzika kwanga kumene andichitira ondidawo, inu wondinyamula kundichotsa kuzipata za imfa. Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse; pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni, ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu. Amitundu anagwa m'mbuna imene anaikumba, lakodwa phazi lao muukonde anautchera. Anadziwika Yehova, anachita kuweruza, woipayo anakodwa ndi ntchito ya manja ake. Oipawo adzabwerera kumanda, inde amitundu onse akuiwala Mulungu. Pakuti sadzaiwalika nthawi zonse waumphawi, kapena chiyembekezo cha ozunzika sichidzaonongeka kosatha. Ukani, Yehova, asalimbike munthu; amitundu aweruzidwe pankhope panu. Ndidzakondwerera ndi kusekera mwa Inu; ndidzaimbira dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu.
Ndidzayamika Yehova monga mwa chilungamo chake; ndipo ndidzaimbira Yehova Wam'mwambamwamba.
muja nyenyezi za m'mawa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe?
Ndidzaitanira Yehova, woyenera kutamandika, ndipo adzandipulumutsa ine kwa adani anga.
Ndipo tatuma pamodzi naye mbaleyo, amene kusimba kwake mu Uthenga Wabwino kuli mu Mipingo yonse;
ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, ndiye mkulu wakuyamba mayamiko, popemphera; ndi Bakibukiya wotsatana naye mwa abale ake, ndi Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.
Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyele, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petahiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu kunthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa chilemekezo ndi chiyamiko chonse.
Namanga guwa la nsembe la Yehova, napherapo nsembe zamtendere ndi zoyamika, nalamulira Yuda atumikire Yehova Mulungu wa Israele.
Onsewa anawalangiza ndi atate wao aimbe m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, zisakasa ndi azeze; atumikire nazo m'nyumba ya Mulungu; ndipo Asafu, Yedutuni, ndi Hemani, anawalangiza ndi mfumu.
Ndipo anatumikira ndi kuimba pakhomo pa Kachisi wa chihema chokomanako mpaka Solomoni adamanga nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, naimirira mu utumiki wao monga mwa malongosoledwe ao.
Ndipo popereka linga la Yerusalemu anafunafuna Alevi m'malo mwao monse, kubwera nao ku Yerusalemu, kuti achite kuperekaku mokondwera, ndi mayamiko, ndi kuimbira, ndi nsanje, zisakasa, ndi azeze.
Ndi Alevi ndiwo Yesuwa, Binuyi, Kadimiyele, Serebiya, Yuda, ndi Mataniya; iye ndi abale ake amatsogolera mayamiko.
Pakuti m'masiku a Davide ndi Asafu kalelo kunali mkulu wa oimbira, ndi wa nyimbo zolemekeza ndi zoyamikira Mulungu.
ndi zikwi zinai odikira; ndi zikwi zinai analemekeza Yehova ndi zoimbira zimene ndinazipanga, anati Davide, kuti alemekeze nazo.
Ndipo poyamba iwo kuimba, ndi kulemekeza Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amowabu, ndi a m'phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha.
Pamenepo Hezekiya anayankha, nati, Tsopano mwadzipatulira kwa Yehova, senderani, bwerani nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika kunyumba ya Yehova. Ndi msonkhano unabwera nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika, ndi onse a mtima wofuna mwini anabwera nazo nsembe zopsereza.
napenya, ndi kuona mfumu inaima pa nsanamira yake polowera; ndi atsogoleri, ndi malipenga, anali kwa mfumu; ndi anthu onse a m'dziko anakondwera, naomba amalipenga; oimbira omwe analiko ndi zoimbirazo, nalangiza poimbira cholemekeza. Pamenepo Ataliya anang'amba zovala zake, nati, Chiwembu, chiwembu.
Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kumlemekeza kwake kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza. Misona ya mkango isowa nimva njala, koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino. Idzani ananu ndimvereni ine, ndidzakulangizani zakumuopa Yehova. Munthu wokhumba moyo ndani, wokonda masiku, kuti aone zabwino? Uletse lilime lako lisatchule zoipa, ndipo milomo yako isalankhule chinyengo. Futuka pazoipa, nuchite zabwino, funa mtendere ndi kuulondola. Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwao. Nkhope ya Yehova itsutsana nao akuchita zoipa, kudula chikumbukiro chao padziko lapansi. Iwowo anaitana, ndipo Yehova anawamva, nawalanditsa kumasautso ao onse. Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi. Masautso a wolungama mtima achuluka, koma Yehova amlanditsa mwa onsewa. Moyo wanga udzatamanda Yehova; ofatsa adzakumva nadzakondwera. Iye asunga mafupa ake onse; silinathyoke limodzi lonse. Mphulupulu idzamupha woipa; ndipo adzawatsutsa kumlandu iwo akudana naye wolungama. Yehova aombola moyo wa anyamata ake, ndipo sadzawatsutsa kumlandu onse akukhulupirira Iye. Bukitsani pamodzi ndine ukulu wa Yehova, ndipo tikweze dzina lake pamodzi.
Ombani m'manja, mitundu yonse ya anthu; fuulirani kwa Mulungu ndi liu la kuimbitsa. Pakuti Yehova Wam'mwambamwamba ndiye woopsa; ndiye mfumu yaikulu padziko lonse lapansi.
Naimirira ansembe mu udikiro wao; ndi Alevi omwe ndi zoimbira za Yehova, adazipanga Davide mfumu kuyamika nazo Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire, polemekeza Davide mwa utumiki wao; ndi ansembe anaomba malipenga pamaso pao, nakhala chilili Israele yense.
Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.
Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.
Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani. Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga; ndidzakweza manja anga m'dzina lanu.
Mu Ziyoni akulemekezani Inu mwachete, Mulungu, adzakuchitirani Inu chowindachi. Mukhutitsa nthaka yake yolima; mufafaniza nthumbira zake; muiolowetsa ndi mvumbi; mudalitsa mmera wake. Muveka chakachi ndi ukoma wanu; ndipo mabande anu akukha zakucha. Akukha pa mabusa a m'chipululu; ndipo mapiri azingika nacho chimwemwe. Podyetsa mpodzaza ndi zoweta; ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu; zifuula mokondwera, inde ziimbira. Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.
Imbirani Mulungu, liimbireni nyimbo dzina lake; undirani mseu Iye woberekekayo kuchidikha; dzina lake ndiye Yehova; ndipo tumphani ndi chimwemwe pamaso pake.
Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu. Ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.
Tikuyamikani Inu, Mulungu; tiyamika, pakuti dzina lanu lili pafupi; afotokozera zodabwitsa zanu.
Potero ife anthu anu ndi nkhosa zapabusa panu tidzakuyamikani kosatha; tidzafotokozera chilemekezo chanu ku mibadwomibadwo.
Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse.
Tiyeni tiimbire Yehova mokondwera; tifuule kwa thanthwe la chipulumutso chathu. Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni, ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, ndipo sadziwa njira zanga. Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga. Tidze nacho chiyamiko pamaso pake, timfuulire Iye mokondwera ndi nyimbo.
Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; muimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi. Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu; dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke; adzaweruza mitundu ya anthu molunjika. Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi; nyanja ibume mwa kudzala kwake. Munda ukondwerere ndi zonse zili m'mwemo; pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzafuula mokondwera. Pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndi mitundu ya anthu ndi choonadi. Muimbireni Yehova, lemekezani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; popeza anachita zodabwitsa: Dzanja lake lamanja, mkono wake woyera, zinamchitira chipulumutso. Yehova anawadziwitsira chipulumutso chake; anaonetsera chilungamo chake pamaso pa amitundu. Anakumbukira chifundo chake ndi chikhulupiriko chake kunyumba ya Israele; malekezero onse a dziko lapansi anaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi. Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: Idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera. Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake ndi nkhosa zapabusa pake. Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake. Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.
Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera. Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu. Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye. Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi. Koma munthu, masiku ake akunga udzu; aphuka monga duwa lakuthengo. Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe: Ndi malo ake salidziwanso. Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana; kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita. Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo. Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi:
Ndidzaimbira Yehova m'moyo mwanga: ndidzaimbira Mulungu wanga zomlemekeza pokhala ndilipo.
Yamikani Yehova, itanirani pa dzina lake; bukitsani mwa mitundu ya anthu zochita Iye. ndipo anachiimikira Yakobo, chikhale malemba, chikhale chipangano chosatha kwa Israele. Ndi kunena kuti, Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani, gawo la cholowa chako; pokhala iwo anthu owerengeka, inde, anthu pang'ono, ndi alendo m'mwemo; nayendayenda kuchokera mtundu wina kufikira mtundu wina, kuchokera ufumu wina kufikira anthu ena. Sanalola munthu awasautse; ndipo anadzudzula mafumu chifukwa cha iwowa. Ndi kuti, Musamakhudza odzozedwa anga, musamachitira choipa aneneri anga. Ndipo anaitana njala igwere dziko; anathyola mchirikizo wonse wa mkate. Anawatsogozeratu munthu; anamgulitsa Yosefe akhale kapolo: Anapweteka miyendo yake ndi matangadza; anamgoneka mu unyolo; kufikira nyengo yakuchitika maneno ake; mau a Yehova anamuyesa. Muimbireni, muimbireni zomlemekeza; fotokozerani zodabwitsa zake zonse. Mfumuyo anatuma munthu nammasula; woweruza mitundu ya anthu anamtsegulira. Anamuika akhale woyang'anira nyumba yake, ndi woweruza wa pa zake zonse: Amange nduna zake iye mwini, alangize akulu ake adziwe nzeru. Pamenepo Israele analowa mu Ejipito; ndi Yakobo anakhala mlendo m'dziko la Hamu. Ndipo anachulukitsatu mtundu wa anthu ake, nawapatsa mphamvu yoposa owasautsa. Anasanduliza mitima yao, kuti adane nao anthu ake, kuti achite monyenga ndi atumiki ake. Anatuma Mose mtumiki wake, ndi Aroni amene adamsankha. Anaika pakati pao zizindikiro zake, ndi zodabwitsa m'dziko la Hamu. Anatumiza mdima ndipo kunada; ndipo sanapikisane nao mau ake. Anasanduliza madzi ao akhale mwazi, naphanso nsomba zao. Mudzitamandire ndi dzina lake loyera: mitima yao ya iwo ofunsira Yehova ikondwere.
Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu! Pakuti akhutitsa mtima wolakalaka, nadzaza mtima wanjala ndi zabwino.
Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.
Aleluya; Lemekezani, inu atumiki a Yehova; lemekezani dzina la Yehova. Lodala dzina la Yehova Kuyambira tsopano kufikira kosatha. Chitulukire dzuwa kufikira kulowa kwake lilemekezedwe dzina la Yehova.
Akufa salemekeza Yehova, kapena aliyense wakutsikira kuli chete: Koma ife tidzalemekeza Yehova kuyambira tsopano kufikira nthawi yonse. Aleluya.
Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha. Amitundu onse adandizinga, zedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. Adandizinga, inde, adandizinga: Indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. Adandizinga ngati njuchi; anazima ngati moto waminga; indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. Kundikankha anandikankha ndikadagwa; koma Yehova anandithandiza. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndipo anakhala chipulumutso changa. M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso: Dzanja lamanja la Yehova likwezeka, Dzanja lamanja la Yehova lichita mwamphamvu. Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo, ndipo ndidzafotokozera ntchito za Yehova. Kulanga anandilangadi Yehova: koma sanandipereke kuimfa ai. Nditsegulireni zipata za chilungamo; ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova. Anene tsono Israele, kuti chifundo chake nchosatha.
Aleluya; Lemekezani dzina la Yehova! Lemekezani inu atumiki a Yehova. Ndiye amene anapanda amitundu ambiri, napha mafumu amphamvu; Sihoni mfumu ya Aamori, ndi Ogi mfumu ya Basani, ndi maufumu onse a Kanani: Ndipo anapereka dziko lao likhale cholowa, cholowa cha kwa Israele anthu ake. Dzina lanu, Yehova, likhala kosatha; chikumbukiro chanu, Yehova, kufikira mibadwomibadwo. Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake, koma adzaleka atumiki ake. Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golide, ntchito ya manja a anthu. Pakamwa ali napo koma osalankhula; maso ali nao, koma osapenya; makutu ali nao, koma osamva; inde, pakamwa pao palibe mpweya. Akuwapanga adzafanana nao; inde, onse akuwakhulupirira. A nyumba ya Israele inu, lemekezani Yehova: A nyumba ya Aroni inu, lemekezani Yehova: Inu akuimirira m'nyumba ya Yehova, m'mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu. A nyumba ya Levi inu, lemekezani Yehova: Inu akuopa Yehova, lemekezani Yehova. Alemekezedwe Yehova kuchokera mu Ziyoni, amene akhala mu Yerusalemu. Aleluya. Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino; muimbire zolemekeza dzina lake; pakuti nkokondweretsa kutero.
Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu. Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera, ndi kuyamika dzina lanu, chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu; popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.
Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi. Ntchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova; ndi okondedwa anu adzakulemekezani. Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu, adzalankhulira mphamvu yanu. Kudziwitsa ana a anthu zamphamvu zake, ndi ulemerero waukulu wa ufumu wake. Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya, ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonseyonse. Yehova agwiriziza onse akugwa, naongoletsa onse owerama. Maso a onse ayembekeza Inu; ndipo muwapatsa chakudya chao m'nyengo zao. Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chao. Yehova ali wolungama m'njira zake zonse, ndi wachifundo m'ntchito zake zonse. Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi. Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa. Masiku onse ndidzakuyamikani; ndi kulemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi. Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawaononga. Pakamwa panga padzanena chilemekezo cha Yehova; ndi zinthu zonse zilemekeze dzina lake loyera kunthawi za nthawi. Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ndi ukulu wake ngwosasanthulika.
Aleluya; Ulemekeze Yehova, moyo wanga. Yehova adzachita ufumu kosatha, Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwomibadwo. Aleluya. Ndidzalemekeza Yehova m'moyo mwanga; ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.
Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma; pakuti chikondweretsa ichi, chilemekezo chiyenera.
Aleluya. Lemekezani Yehova kochokera kumwamba; mlemekezeni m'misanje. Nyama zakuthengo ndi zoweta zonse; zokwawa, ndi mbalame zakuuluka. Mafumu a padziko ndi mitundu yonse ya anthu; zinduna ndi oweruza onse a padziko. Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana. Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba padziko lapansi ndi thambo. Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake, chilemekezo cha okondedwa ake onse; ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye. Aleluya. Mlemekezeni, angelo ake onse; mlemekezeni, makamu ake onse. Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi; mlemekezeni, nyenyezi zonse zounikira. Mlemekezeni, m'mwambamwamba, ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo. Alemekeze dzina la Yehova; popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.
Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake. Akondwere Israele mwa Iye amene anamlenga; ana a Ziyoni asekere mwa mfumu yao. Alemekeze dzina lake ndi kuthira mang'ombe; amuimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze.
Aleluya. Lemekezani Mulungu m'malo ake oyera; mlemekezeni m'thambo la mphamvu yake. Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba; mlemekezeni monga mwa ukulu wake waunjinji. Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga; mlemekezeni ndi chisakasa ndi zeze. Mlemekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang'ombe: Mlemekezeni ndi zoimbira za zingwe ndi chitoliro. Mlemekezeni ndi nsanje zomveka: Mlemekezeni ndi nsanje zoliritsa. Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Aleluya.
Tsiku lomwelo udzati, Ndikuyamikani inu Yehova; pakuti ngakhale munandikwiyira, mkwiyo wanu wachoka, ndipo mutonthoza mtima wanga. Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.
Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, chifukwa mwachita zinthu zodabwitsa, ngakhale zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m'zoonadi.
ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.
nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenge kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?
Ndipo Maria anati, Moyo wanga ulemekeza Ambuye, ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,
Ndipo pakuyandikira Iye tsono potsetsereka pake paphiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau aakulu, chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu anaziona; nanena, Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m'dzina la Ambuye; mtendere mu Mwamba, ndi ulemerero mu Mwambamwamba. Ndipo Afarisi ena a m'khamu la anthu anati kwa Iye, Mphunzitsi, dzudzulani ophunzira anu. Ndipo anathamanga, natsogola, nakwera mumkuyu kukamuona Iye; pakuti anati apite njira yomweyi. Ndipo anayankha nati, Ndinena ndi inu, ngati awa khala chete miyala idzafuula.
nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.
Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva;
Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.
Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.
ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu; ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino. ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu;
Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.
Kondwerani nthawi zonse; Pempherani kosaleka; M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.
Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake. Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.
Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;
Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, ndipo zinalengedwa.
Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.
Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha. Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.
Zitatha izi ndinamva ngati mau aakulu a khamu lalikulu mu Mwamba, lili kunena, Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu; Ndipo ndinagwa pa mapazi ake kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero. Ndipo ndinaona mutatseguka mu Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama. Ndipo maso ake ali lawi la moto, ndi pamutu pake pali nduwira zachifumu zambiri; ndipo ali nalo dzina lolembedwa, wosalidziwa wina yense koma Iye yekha. Ndipo avala chovala chowazidwa mwazi; ndipo atchedwa dzina lake, Mau a Mulungu. Ndipo magulu a nkhondo okhala mu Mwamba anamtsata Iye, okwera pa akavalo oyera, ovala bafuta woyera woti mbuu. Ndipo m'kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo: ndipo aponda Iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse. Ndipo ali nalo pa chovala chake ndi pa ntchafu yake dzina lolembedwa, MFUMU YA MAFUMU, NDI MBUYE WA AMBUYE. Ndipo ndinaona mngelo alikuima m'dzuwa; ndipo anafuula ndi mau aakulu akunena ndi mbalame zonse zakuuluka pakati pa mlengalenga: Idzani kuno, sonkhanani kuphwando la Mulungu wamkulu, kuti mudzadye nyama ya mafumu, ndi nyama ya akapitao, ndi nyama ya anthu amphamvu, ndi nyama ya akavalo, ndi ya iwo akukwerapo, ndi nyama ya anthu onse, mfulu ndi akapolo, ndi aang'ono ndi aakulu. Ndipo ndinaona chilombocho, ndi mafumu a dziko, ndi magulu a nkhondo ao, osonkhanidwa kuchita nkhondo pa Iye wakukwera pa kavalo, ndi gulu la nkhondo lake. pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo. Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulufure: ndipo otsalawa anaphedwa ndi lupanga la Iye wakukwera pa kavalo, ndilo lotuluka m'kamwa mwake; ndipo mbalame zonse zinakhuta ndi nyama zao. Ndipo anatinso, Aleluya. Ndipo utsi wake ukwera kunthawi za nthawi.
Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.
Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.
Zowindira Inu Mulungu, zili pa ine, ndidzakuchitirani zoyamika. Pakuti mwalanditsa moyo wanga kuimfa, simunatero nao mapazi anga kuti ndingagwe? Kuti ndiyende pamaso pa Mulungu m'kuunika kwa amoyo.
Fuulirani kwa Mulungu, dziko lonse lapansi. Pakuti munatiyesera, Mulungu, munatiyenga monga ayenga siliva. Munapita nafe kuukonde; munatisenza chothodwetsa pamsana pathu. Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu; tinapyola moto ndi madzi; koma munatifikitsa potitsitsimutsa. Ndidzalowa m'nyumba yanu ndi nsembe zopsereza, ndidzakuchitirani zowinda zanga, zimene inazitchula milomo yanga, ndinazinena pakamwa panga posautsika ine. Ndidzakufukizirani nsembe zopsereza zonona, pamodzi ndi chofukiza cha mphongo za nkhosa; ndidzakonza ng'ombe pamodzi ndi mbuzi. Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu, ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga. Ndinamfuulira Iye pakamwa panga, ndipo ndinamkuza ndi lilime langa. Ndikadasekera zopanda pake m'mtima mwanga, Ambuye sakadamvera. Koma Mulungu anamvadi; anamvera mau a pemphero langa. Imbirani ulemerero wa dzina lake; pomlemekeza mumchitire ulemerero.
Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe, kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu; ndidzakulemekezani kosalekeza. Ndikhala chodabwitsa kwa ambiri; koma Inu ndinu pothawira panga polimba. M'kamwa mwanga mudzadzala lemekezo lanu, ndi ulemu wanu tsiku lonse.
Ntchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova; ndi okondedwa anu adzakulemekezani. Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu, adzalankhulira mphamvu yanu. Kudziwitsa ana a anthu zamphamvu zake, ndi ulemerero waukulu wa ufumu wake.
Ndidzalemekeza Yehova m'moyo mwanga; ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.
Yerusalemu, lemekezani Yehova; Ziyoni, lemekezani Mulungu wanu. Popeza analimbitsa mipiringidzo ya zitseko zanu: Anadalitsa ana anu m'kati mwanu.
Yehova ndiye wondipulumutsa ine; Chifukwa chake tidzaimba nyimbo zanga, ndi zoimba zazingwe Masiku onse a moyo wathu m'nyumba ya Yehova.
Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.
Ndipo dzidzidzi panali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena, Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.
Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala ophunzira anga.
Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka! Pakuti anadziwitsa ndani mtima wake wa Ambuye? Kapena anakhala phungu wake ndani? Ndipo anayamba ndani kumpatsa Iye, ndipo adzambwezeranso? Chifukwa zinthu zonse zichokera kwa Iye, zichitika mwa Iye, ndi kufikira kwa Iye. Kwa Iyeyo ukhale ulemerero kunthawi zonse. Amen.
koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nao cholowa cha oyera mtima m'kuunika;
akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.
Milomo yanga itulutse chilemekezo; popeza mundiphunzitsa malemba anu. Lilime langa liimbire mau anu; pakuti malamulo anu onse ndiwo olungama.
Mafumu onse a padziko lapansi adzakuyamikani, Yehova, popeza adamva mau a pakamwa panu. Ndipo adzaimbira njira za Yehova; pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.
Pakamwa panga padzanena chilemekezo cha Yehova; ndi zinthu zonse zilemekeze dzina lake loyera kunthawi za nthawi.
Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele; chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo. Ndipo Iye anatikwezera ife nyanga ya chipulumutso, mwa fuko la Davide mwana wake.
Ndipo pakuyandikira Iye tsono potsetsereka pake paphiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau aakulu, chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu anaziona;